Chichewa

    Translation: nya-khaledibrahimbe

    Author: Khaled Ibrahim Betala

    Wotsegula

    Surah 1

    [1] “M’dzina la Allah Wachifundo chambiri, Wachisoni chosatha

    [2] “Kutamandidwa konse ndi kwa Allah Mbuye wa zolengedwa zonse

    [3] Wachifundo chambiri, Wachisoni chosatha

    [4] “Mwini tsiku la chiweruziro

    [5] “Inu Nokha tikukupembedzani, ndiponso Inu Nokha tikukupemphani chithandizo

    [6] “Tiongolereni kunjira yoongoka

    [7] “Njira ya omwe mudawapatsa chisomo; osati ya amene adakwiyiridwa (ndi Inu) osatinso ya omwe adasokera

    Ng'ombe

    Surah 2

    [1] “Alif-Lâm-Mîm

    [2] “Ili ndi Buku lopanda chipeneko mkati mwake, ndichiongoko cha (anthu) oopa Allah

    [3] “Omwe amakhulupirira zosaoneka ndi maso (monga Munda wamtendere, Moto, Angelo ndi zina zotere zomwe Allah ndi Mtumiki (s.a.w) adazifotokoza, amapemphera Swala moyenera, ndiponso amapereka m’zimene tawapatsa

    [4] “Ndi amene akukhulupirira zomwe zidavumbulutsidwa kwa iwe, ndi zomwe zidavumbulutsidwa kale iwe usadadze, nakhulupiriranso motsimikiza kuti lilipo tsiku lachimaliziro

    [5] “Iwowo (omwe ali ndi chikhalidwe chotere), ali pachiongoko chochokera kwa Mbuye wawo (Allah), ndipo iwowo ndi omwe ali opambana (pokapeza ulemelero wapamwamba ku Minda ya mtendere)

    [6] “Ndithu amene sadakhulupirire, nchimodzimodzi kwa iwo uwachenjeze kapena usawachenjeze sangakhulupirire

    [7] “(Ali ngati kuti) Allah wawadinda chidindo chotseka mitima yawo ndi makutu awo (kotero kuti kuunika kwa chikhulupiliro sikungalowemo), ndipo m’maso mwawo muli chophimba (sangathe kuona zozizwitsa za Allah); choncho iwo adzalandira chilango chachikulu

    [8] “Pakati pa anthu alipo (anthu achinyengo) amene akunena: “Takhulupirira mwa Allah ndi tsiku lachimaliziro,” pomwe iwo sali okhulupirira

    [9] “Akufuna kunyenga Allah ndi amene akhulupirira, ndipo sanyenga aliyense koma okha, ndipo iwo sazindikira (kuti akudzinyenga okha)

    [10] “M’mitima mwawo muli matenda; ndipo Allah wawaonjezera matenda. Choncho iwo adzalandira chilango chopweteka chifukwa cha bodza lawo

    [11] “Ndipo akauzidwa kuti: “Musaononge padziko,” amayankha kuti: “Ife ndife okonza.”

    [12] “Dziwani kuti, ndithudi, iwo ndiwo ali oononga (pa dziko); koma sakuzindikira

    [13] “Ndipo akauzidwa kuti, “Khulupirirani monga momwe anthu ena akhulupirira,” amayankha kuti: “Kodi tikhulupirire monga momwe zakhulupirira zitsiru?” Dziwani kuti, ndithudi, iwo ndi omwe ali zitsiru, koma sakudziwa

    [14] “Ndipo akakumana ndi amene akhulupirira, amanena: “Takhulupirira.” Koma akakhala pa okha ndi asatana awo, amati: “Ndithudi ife tili pamodzi nanu. Timangowachita chipongwe basi.”

    [15] “Allah adzawalipira chipongwe chawocho, ndipo akuwalekelera akungoyumbayumba (kugwira njakata) m’kusokera kwawo

    [16] “Oterewo ndiomwe asinthanitsa chiongoko ndi kusokera, koma malonda awo sadawapindulire chilichonse, tero sadali oongoka

    [17] “Fanizo lawo lili ngati (munthu wa paulendo wafungatiridwa ndi mdima) yemwe wayatsa moto; ndipo pamene udaunika zomwe zidali m’mphepete mwake, Allah nkuwachotsera kuunika kwawoko nawasiya mu mdima osatha kuona

    [18] “(Nakhala ngati) agonthi, abubu, akhungu; ndipo sangabwelerenso (ku chiwongoko)

    [19] “Kapena (fanizo lawonso) lili ngati chimvula chochokera ku mitambo m’kati mwake muukhala mdima, mphenzi ndi kung’anima, naika zala zawo m’makutu mwawo chifukwa chamkokomo ndikuopa imfa (pomwe kutero sikungawathandize chilichonse). Ndipo Allah akudziwa bwinobwino za osakhulupirira

    [20] “Kung’anima kukuyandikira kutsomphola maso awo; nthawi iliyonse kukawaunikira, nkuyenda m’menemo (mkuunikamo). Koma kukawachitira mdima, nkuyima. ndipo Allah akadafuna akadawachotsera kumva kwawo ndi kuona kwawo. Ndithudi, Allah Ngokhoza chilichonse

    [21] “E inu anthu! pembedzani Mbuye wanu Yemwe adakulengani inu ndi omwe adalipo kale, kuti mukhale oopa (Allah)

    [22] “(Allah) Yemwe adakupangirani nthaka kukhala ngati mphasa, ndi thambo kukhala ngati denga; ndipo adatsitsa madzi kuchokera ku mitambo natulutsa ndi madziwo zipatso zosiyanasiyana kuti zikhale chakudya chanu. Choncho Allah musampangire anzake uku inu mukudziwa (kuti alibe wothandizana naye)

    [23] “Ndipo ngati muli m’chikaiko ndi zomwe tamvumbulutsira kapolo wathu (kuti sizinachokere kwa Ife,) tabweretsani sura imodzi yolingana ndi Quraniyi (m’kayankhulidwe ka nzeru ndi kayalidwe ka malamulo ake). Ndipo itanani athandizi anu (kuti akuthandizeni) osakhala Allah; ngati inu mukunena zoona (kuti Qur’an njopekedwa)

    [24] “Choncho ngati simutha (kubweretsa sura imodzi yonga ya m’Qurani) ndiye kuti simudzatha. Choncho opani Moto omwe nkhuni zake ndi anthu ndi miyala umene wakonzedwera kwa osakhulupirira

    [25] “Ndipo auze nkhani yabwino amene akhulupirira nachita ntchito zabwino (molungama) kuti ndithu adzalandira minda ya mtendere momwe mitsinje ikuyenda pansi pake (ndi patsogolo pake). Nthawi iliyonse kumeneko akapatsidwa zipatso ngati chakudya, adzakhala akunena: “Izi ndizomwe tidapatsidwa kale,” (chifukwa chakuti) adzapatsidwa zipatso zofanana (m’maonekedwe ake ndi zimene adapatsidwapo kale. Koma makomedwe ake ngosiyana). Ndiponso akalandira m’menemo akazi oyeretsedwa (kuuve wamtundu uliwonse); ndipo iwo adzakhala m’menemo nthawi yaitali

    [26] “Ndithu Allah sachita manyazi kupereka fanizo la udzudzu ndi choposerapo (pa udzudzuwo). Koma amene akhulupirira akuzindikira kuti (fanizolo) ndiloona ndi lochokera kwa Mbuye wawo. Koma amene sadakhulupirire, akunena: “Kodi Allah akufunanji pa fanizo lotereli?” (Allah) amawalekelera ambiri kusokera ndi fanizo lotere, komanso amawaongola ambiri ndi fanizonso lotere. Komatu sawalekelera kusokera nalo kupatula okhawo opandukira chilamulo (Chake)

    [27] “Omwe akuswa chipangano cha Allah pambuyo pochimanga (kuti adzachikwaniritsa; ndi kutsatira malamulo a Allah), ndiponso amadula (chibale) chomwe Allah adalamula kuti chilumikizidwe, naononga pa dziko (poyambitsa nkhondo ndi ziwawa); iwo ndiamene ali otayika

    [28] “Kodi mungamkane chotani Allah chikhalirecho inu mudali akufa ndipo adakupatsani moyo (nakuikani pa dziko lapansi)? Kenako adzakupatsani imfa (ikakwana nthawi yanu yofera). Kenako adzakuukitsani (ndikukutulutsani m’manda). Ndipo kenako mudzabwezedwa kwa Iye (kuti mukaweruzidwe pa zomwe mudali kuchita)

    [29] “Iye ndi Yemwe adakulengerani zonse za m’dziko lapansi, kenako adalunjika ku thambo nakonza thambo zisanu ndi ziwiri. Iye Ngodziwa chinthu chilichonse

    [30] “Akumbutse (anthu ako nkhani iyi) panthawi yomwe Mbuye wako anati kwa Angelo: “Ine ndikufuna kuika m’dziko lapansi wondiimilira.” (Angelo) adati: “Kodi muika m’menemo amene azidzaonongamo ndi kukhetsa mwazi, pomwe ife tikukulemekezani ndi kukutamandani mokuyeretsani?” (Allah) adati: “Ndithudi, Ine ndikudziwa zimene simukuzidziwa.”

    [31] “Ndipo (Allah) adaphunzitsa Adam mayina a (zinthu) zonse; nazibweretsa (zinthuzo) pamaso pa Angelo, naati (kwa Angelo): “Ndiuzeni mayina a zinthu izi ngati mukunena zoona (kuti inu ndinu ozindikira zinthu).”

    [32] “(Angelo) adati: “Kuyeretsedwa Nkwanu! Ife tilibe kuzindikira kupatula chimene mwatiphunzitsa. Ndithudi, Inu Ngodziwa kwambiri, Anzeru zakuya.”

    [33] “(Allah) adanena: “E iwe Adam!: Auze mayina ake (azinthuzo).” Ndipo pamene adawauza mayina ake, (Iye) adati: “Kodi Sindinakuuzeni kuti Ine ndikudziwa zobisika zakumwamba ndi pansi, ndiponso ndikudziwa zimene mukuonetsera poyera ndi zimene mukubisa?”

    [34] “Ndipo (akumbutse anthu ako nkhani iyi) parnene tidawauza Angelo: “Mgwadireni Adam.” Onse adamugwadira kupatula Iblisi (Satana); anakana nadzitukumula. Tero adali m’modzi mwa osakhulupirira

    [35] “Ndipo tidati: “E iwe Adam! Khala iwe ndi mkazi wako m’mundamo (mu Edeni); idyani m’menemo motakasuka paliponse pamene mwafuna; koma musauyandikire Mtengo uwu kuopera kuti mungakhale mwa odzichitira okha zoipa.”

    [36] “Koma Satana (Iblisi yemwe uja) adawalakwitsa onse awiriwo (nanyoza lamulo la Allah ndikudya mtengo woletsedwawo), nawatulutsa (mu Mtendere) momwe adaalimo. Ndipo tidawauza: “Tsikani (mukakhale pa dziko lapansi) pakati panu pali chidani. Tsopano pokhala panu ndi pa dziko lapansi, ndipo mukapeza chisangalalo pamenepo kwakanthawi.”

    [37] “Ndipo Adam adalandira mawu kuchokera kwa Mbuye wake, (napempha chikhululuko cha Allah kupyolera m’mawuwo), ndipo (Mbuye wake) adavomera kulapa kwake. Ndithudi, Iyeyo Ngolandira kwambiri kulapa, Wachisoni chosatha

    [38] “Tidati: “Tsikani m’menemo nonsenu. Ngati chitakufikani chiongoko chochokera kwa Ine, choncho amene adzatsate chiongoko Changacho, pa iwo sipadzakhala mantha. Ndiponso iwo sadzadandaula.”

    [39] ““Koma amene sanakhulupirire natsutsa mawu athu, iwowo ndiwo anthu a ku Moto. M’menemo akakhalamo nthawi yaitali.”

    [40] “E inu ana a Israyeli! kumbukirani chisomo Changa chomwe ndidakudalitsani nacho, ndipo kwaniritsani pangano Langa Nanenso ndikwaniritsi pangano lanu. Ndipo Ine Ndekha ndiopeni

    [41] “Ndipo khulupirirani zimene ndavumbulutsa, zomwe zikuchitira umboni zimene muli nazo, ndipo musakhale oyamba kuzikana; ndipo musagulitse mawu Anga ndi (zinthu za) mtengo wochepa. Ndipo Ine Ndekha ndiopeni

    [42] “Ndipo musasakanize choona ndi chonama; ndi kubisa choona uku mukudziwa

    [43] “Ndipo pempherani Swala moyenera ndikupereka chopereka (Zakaat), ndipo weramani pamodzi ndi owerama

    [44] “Kodi mukulamula anthu kuchita zabwino ndi kudziiwala inu eni pomwe inu mukuwerenga Buku? Kodi simuzindikira

    [45] “Ndipo dzithandizeni (pa zinthu zanu) popirira ndi popemphera Swala. Ndithudi, Swala yo ndiyolemera kupatula kwa odzichepetsa (kwa Allah)

    [46] “Omwe akutsimikiza kuti adzakumana ndi Mbuye wawo, ndi kuti adzabwerera kwa Iye

    [47] “E inu ana a Israyeli! Kumbukirani chisomo Changa chomwe ndidakudalitsani nacho. Ndithudi, Ine ndinakuchitirani ubwino kuposa zolengedwa zonse (pa nthawiyo)

    [48] “Choncho opani tsiku lomwe munthu aliyense sadzathandiza mnzake ndi chilichonse, ndipo sikudzavomerezedwa kwa iye (munthuyo) dandaulo lililonse, ndiponso silidzalandiridwa dipo kwa iye; ndipo iwo sadzapulumutsidwa

    [49] “Ndipo (kumbukirani) pamene tidakupulumutsani kwa anthu a Farawo, omwe amakuzunzani ndi chilango choipa; adali kuzinga (kupha) ana anu achimuna ndikuwasiya moyo achikazi. Ndipo m’zimenezo mudali mayeso aakulu ochokera kwa Mbuye wanu

    [50] “Ndipo (kumbukiraninso) pamene tidailekanitsa nyanja chifukwa cha inu (kuti muoloke pa mchenga wouma), potero tidakupulumutsani ndi kuwamiza anthu a Farawo (pamodzi ndi iye mwini) uku inu mukuona; (chomwe chidali chizizwa choonekera)

    [51] “(Kumbukiraninso) pamene tidamulonjeza Mûsa masiku makumi anayi (kuti tidzampatsa buku la Taurat patapita masiku makumi anayi pambuyo pa kupulumuka kwanu ndi kuonongeka kwa Farawo); kenako inu mudapembedza thole (mwana wa ng’ombe) pambuyo pake, (iye kulibe, atapita ku chipangano cha Mbuye wake). Ndipo inu muli ochita zoipa

    [52] “Kenako tidakukhululukirani pambuyo pa zimenezo, kuti muthokoze (mtendere wa Allah)

    [53] “Ndipo (kumbukiraninso) pamene Mûsa tidampatsa buku lolekanitsa choonadi ndi chonama kuti inu muongoke (polilingalira ndi kutsatira malamulo ake)

    [54] “Ndipo (kumbukiraninso) pamene Mûsa adanena kwa anthu ake kuti “E inu anthu anga! Ndithudi, inu mwadzichitira nokha zoipa pompembedza thole (mwana wa ng’ombe). Choncho lapani kwa Mlengi wanu, ndipo iphanani nokha (amene ali abwino aphe oipa). Kutero ndi bwino kwa inu pamaso pa Mlengi wanu.” Choncho (Allah) wavomera kulapa kwanu. Ndithudi, Iye Ngovomera kulapa mochuluka, Wachisoni chosatha

    [55] “Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi) pamene Mudati: “E iwe Mûsa!; Sitingakukhulupirire iwe mpaka timuone Allah masomphenya.” Ndipo nkokomo wa moto udakugwirani uku inu mukuona

    [56] “Kenako tidakuukitsani ku imfa pambuyo pakufa kwanu, kuti muyamike

    [57] “Ndipo tidakuphimbani ndi mthunzi wa mitambo (pamene mudali kuoloka chipululu cha mchenga), ndipo tidakutsitsirani Mana (zakumwa zotsekemera ngati uchi) ndi Salwa (zinziri), ndi kukuuzani: “Idyani zinthu zabwino izi zimene takupatsani.” Komatu sadatichitire Ife choipa koma adali kudzichitira okha zoipa

    [58] “Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi) pamene tidati: “Lowani m’mudzi uwu, ndikudya m’menemo motakasuka paliponse pamene mwafuna; ndipo lowerani pachipata chake uku mutawerama (kusonyeza kuthokoza Allah) ndipo nenani: “E Mbuye wathu! Tikhululukireni machimo athu.” “Tikukhululukirani machimo anu ndipo tiwaonjezera (mphoto yaikulu) ochita zabwino.”

    [59] “Koma anthu oipa adasintha (lamulo la Allah, nanena) mawu ena osati amene adawuzidwa. Tero, anthu oipawo tidawatsitsira mliri wochokera kumwamba, chifukwa chakutuluka kwawo m’chilamulo cha Allah

    [60] “Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi) pamene Mûsa adapemphera anthu ake madzi kwa Allah (atagwidwa ndi ludzu loopsa m’chipululu), tidati: “Menya mwala ndi ndodo yakoyo.” (Atamenya), anatulukadi m’menemo akasupe khumi ndi awiri. Potero fuko lililonse lidadziwa malo awo omwera. (Izi zidachitika kuti asakangane). Choncho idyani, ndiponso imwani mu zopatsa za Allah (popanda inu kuzivutikira), ndipo musasimbwe pa dziko uku mukuononga

    [61] “Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi) pamene mudati: “E iwe Mûsa! Sitingathe kupirira ndi chakudya chamtundu umodzi (chomwe ndi Mana ndi Salwa); choncho tipemphere kwa Mbuye wako kuti atitulutsire (atipatse) ife zimene nthaka imameretsa, monga masamba, nkhaka, adyo, nyemba za mtundu wa chana ndi anyezi.” Iye adati: “Kodi mukufuna kusinthitsa chonyozeka ndi chabwino? Pitani m’midzi, ndipo kumeneko mukapeza zimene mwapemphazi.” Potero adapatsidwa kunyozeka ndi kusauka; nabwerera ndi mkwiyo wa Allah. Zimenezo n’chifukwa chakuti iwo sadali okhulupirira zisonyezo za Allah, ndikuti adali kupha aneneri a Allah popanda chifukwa. Zidali tero chifukwa cha kunyoza kwawo, ndipo adali olumpha malire

    [62] “Ndithu amene akhulupirira (aneneri akale), ndi Ayuda, ndi Akhirisitu ndi Asabayi*; aliyense wa iwo amene akhulupirire Allah (tsopano, monga momwe akunenera Mneneri Muhammad (s.a.w) nakhulupiriranso za tsiku lachimaliziro, uku akuchita ntchito zabwino, akalandira mphoto yawo kwa Mbuye wawo. Pa iwo sipadzakhala mantha, ndiponso sadzadandaula

    [63] “Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi, inu Ayuda) pamene tidalandira chipangano chanu (kuti mudzagwiritsa ntchito zomwe zili m’buku la Taurat), ndipo tidakweza pamwamba panu phiri (la Sinai; tidati kwa inu): “Gwirani mwamphamvu chimene takupatsani, ndipo kumbukirani zili m’menemo (pozigwiritsa ntchito. Ndiponso musazinyozere) kuti mukhale oopa Allah.”

    [64] “Koma pambuyo pazimenezo mudatembenuka ndikunyoza. Pakadapanda ubwino wa Allah ndi chifundo chake pa inu, mukadakhala mwa otayika (oonongeka pa dziko lapansi)

    [65] “Ndithudi mudawadziwa (anthu) amene adapyola malire mwa inu pakuswa kupatulika kwa tsiku la Sabata (m’mene tidawalangira chifukwa chosodza nsomba pa tsiku loletsedwa). Ndipo tidati kwa iwo: “Khalani anyani onyozeka.”

    [66] “Ndipo tidakuchita kukhala anyaniko, chilango chochenjeza amene adalipo pa nthawiyo ndi akudza pambuyo pawo, ndiponso phunziro kwa oopa Allah

    [67] “(Kumbukiraninso nkhani iyi, inu Ayuda) pamene Mûsa adauza anthu ake: “Ndithudi, Allah akukulamulani kuti muzinge ng’ombe.” Iwo adati: “Kodi ukutichitira zachipongwe?” Iye adati: “(Sichoncho), ndikudzitchinjiriza ndi Allah kukhala mwa anthu aumbuli.”

    [68] “Iwo adati: “Tipemphere kwa Mbuye wako kuti atifotokozere bwino za ng’ombeyo.” Iye adati: “Ndithudi Iye akunena kuti ng’ombeyo simkota kapena mthanthi, koma yapakatikati pa zimenezi. Tero chitani zimene mukulamulidwa.”

    [69] “Iwo adatinso: “Tipemphere kwa Mbuye wako kuti atilongosolere maonekedwe ake.” (Mûsa) adati: “Iye akuti ng’ombeyo ikhale yachikasu kwambiri, yowakondweretsa oiwona.”

    [70] “Iwo adatinso: “Tipemphere kwa Mbuye wako kuti atilongosolere mmene kakhalidwe kake kalili. Ndithudi, ng’ombe zimene wafotokozazo n’zofanana kwa ife. Ndipo ndithudi, Allah akafuna tikhala oongoka.”

    [71] “Adati: “Ndithudi Iye akuti, imeneyo ndi n’gombe yosaigwiritsa ntchito yolima m’nthaka, ndiponso yosathilira mbewu; yabwinobwino yopanda banga.” Iwo adati: “Tsopano wabweretsa (mawu a) choonadi.” Choncho adaizinga, koma padatsala pang’ono kuti asachite (lamulolo)

    [72] “Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi) pamene mudapha munthu, kenako mudakangana ndi kukankhirana za munthuyo, (ena ankati uje ndiye wapha, pomwe ena ankati koma uje ndiye wapha). Ndipo Allah atulutsira poyera zimene mudali kubisa

    [73] “Choncho tidati: “Mmenyeni (wakufayo) ndi gawo la nyamayo. (Potero auka ndikunena za amene adamupha).” Momwemo Allah adzawaukitsa akufa (m’manda monga adamuukitsira wakufayo pamaso panu), ndipo akukusonyezani zizindikiro Zake kuti mukhale ndi nzeru

    [74] “Koma mitima yanu idauma pa mbuyo pa zimenezo; (nkukhala gwa!) ngati mwala kapena kuposerapo. Ndithudi pali miyala ina yomwe ikutuluka mkati mwake mitsinje; ndipo pali ina imene imang’ambika nkutuluka madzi mkati mwake; ndipo pali ina imene imagudubuzika chifukwa cha kuopa Allah. (Koma inu Ayuda simulalikika ngakhale mpang’ono pomwe). Ndipo Allah sali wonyalanyaza zimene mukuchita

    [75] ۞ Kodi (inu Asilamu) mukuyembekezera kuti angakukhulupirireni (Ayudawo) pomwe ena a iwo ankamvera mawu a Allah, kenako nkuwasintha pambuyo powazindikira bwinobwino, uku akudziwa

    [76] “Ndipo akakumana ndi amene akhulupirira, amanena: Takhulupirira (kuti uyu, Muhammad (s.a.w) ndi mneneri woona, ndipo watchulidwa m’mabuku athu).” Koma akakhala kwaokha kuseli, amati: “Mukuwauza iwo (Asilamu) zimene Allah anakufotokozerani (m’buku la Taurat) kuti adzakhale ndi mtsutso pa inu kwa Mbuye wanu? Kodi mulibe nzeru

    [77] ““Kodi sadziwa kuti Allah akudziwa zomwe akubisa ndi zomwe akuonetsera poyera? (Kwa Allah palibe chobisika)

    [78] “Ndipo mwa iwo (Ayudawo) zilipo mbuli zosadziwa kuwerenga buku (la Allah), koma ziyembekezero zabodza basi, ndipo iwo alibe china koma kungoganizira

    [79] “Chilango cha ukali chili pa amene akulemba buku ndi manja awo, kenako nanena: “Ili lachokera kwa Allah,” (akunena bodzalo) kuti apeze zinthu za mtengo wochepa (za m’dziko lapansi); choncho kuonongeka kuli pa iwo chifukwa cha zomwe manja awo alemba, ndiponso kuonongeka n’kwawo chifukwa cha zomwe akupeza

    [80] “Ndipo akunena: “Sudzatikhudza Moto kupatula masiku owerengeka basi.”Auze: “Kodi mudapangana naye Allah, kuti potero sadzaswa lonjezo Lake, kapena mukungomunenera Allah zimene simukuzidziwa?”

    [81] “Sichoncho! Koma amene wachita choipa, nam’zungulira machimo akeo, otero ndi anthu a ku Moto. M’menemo adzakhala nthawi yaitali

    [82] “Ndipo amene akhulupirira nachita zabwino, iwowo ndiwo anthu a ku Munda wamtendere. M’menemo adzakhala nthawi yaitali

    [83] “Ndipo (akumbutse nkhani iyinso) pamene tidalandira pangano lamphamvu la ana a Israyeli kuti: Musapembedze aliyense koma Allah; ndipo muwachitire zabwino makolo anu ndi achibale anu, ndi amasiye, ndi masikini (osoŵedwa); ndipo nenani kwa anthu mwaubwino; ndipo pempherani Swala moyenera ndi kupereka Zakaat, kenako mudatembenuka monyozera kupatula ochepa mwa inu, ndipo inu ndinu onyozera

    [84] “Ndipo kumbukirani pamene tidalandira pangano lanu kuti simukhetsa mwazi wanu, ndikutinso simudzatulutsana nokha m’nyumba zanu, ndipo inu munavomereza zimenezi, ndipo inu mukuikira umboni zimenezi (koma simudatsate malamulowo)

    [85] “Tsono inu nomwe ndi amene mukuphana ndikuwatulutsa ena a inu m’nyumba zawo; mukuthandiza adani anu powachitira (abale anu masautso) mwauchimo ndi molumpha malire. Koma akakudzerani akaidi ogwidwa ku nkhondo, mukuwaombola, pomwe nkoletsedwa kwa inu kuwatulutsa. Kodi mukukhulupirira mbali ina ya buku, mbali ina nkuikana? Choncho palibe mphoto kwa ochita izi mwa inu koma kuyaluka pamoyo wa pa dziko lapansi; ndipo tsiku la chiweruziro adzalowetsedwa ku chilango chokhwima kwambiri. Ndipo Allah sali wonyalanyaza zimene mukuchita

    [86] “ Iwowo ndi amene asinthanitsa moyo wa dziko lapansi ndi moyo ulinkudza choncho sadzawachepetsera chilango, ndiponso sadzapulumutsidwa

    [87] “Ndithudi Mûsa tidampatsa buku (la Taurat) ndipo tidatsatiza pambuyo pake atumiki (ena). Ndipo Isa (Yesu) mwana wa Mariya tidampatsa zizizwa zoonekera, ndi kumulimbikitsa ndi Mzimu Woyera (Gabrieli). Nthawi iliyonse akakudzerani mtumiki ndi chomwe mitima yanu siikonda, mumadzikweza. Ena mudawatsutsa ndipo ena mudawapha

    [88] “(Iwo) adati: “Mitima yathu yakutidwa, (potero tikulephera kumvetsa ulaliki wako, iwe Muhammad (s.a.w).’’ Iwo ngabodza pa zimene akunenazi. Koma Allah wawatembelera chifukwa cha kusakhulupirira kwawo). Tero n’zochepa zimene akuzikhulupirira

    [89] “Ndipo pamene buku lidawadzera (m’nyengo ya mtumiki Muhammad {s.a.w}) lochokera kwa Allah, loikira umboni zomwe zili pamodzi ndi iwo (adalikana), pomwe kale (lisadadze bukulo) adali kupempha chithandizo (kupyolera kwa mtumiki wolonjezedwa) chogonjetsera amene sadakhulupirire. Koma pamene chidawadzera chimene adachidziwa, (Qur’an) adachikana. Choncho matembelero a Allah ali pa osakhulupirira

    [90] “N’choipa zedi chimene asinthanitsira (chisangalalo cha tsiku lachimaliziro cha) mitima yawo pa kukana kwao zimene Allah adavumbulutsa, chifukwa cha njiru basi kuti Allah watsitsira chifundo chake amene wamfuna mwa akapolo Ake (amene sali Myuda). Potero adabwerera ndi mkwiyo wa Allah kuonjezera pa mkwiyo wakale. Ndipo osakhulupirira adzakhala ndi chilango chosambula

    [91] “Ndipo akauzidwa (Ayuda): “Khulupirirani zimene Allah wavumbulutsa (kwa mtumiki Muhammad {s.a.w}).” Amanena: “Tikukhulupirira zimene zidavumbulitsidwa kwa ife,” ndipo amazikana zomwe sizili zimenezo ngakhale izo zili zoona, zomwe zikutsimikizira pa zimene ali nazo pamodzi. Nena: “Nanga bwanji mudapha aneneri a Allah kalelo ngati muli okhulupiriradi?”

    [92] “Ndipo adakudzerani Mûsa ndi zisonyezo zoonekera, koma pambuyo pake mudapembedza thole (mwana wa ng’ombe), ndipo potero mudali anthu ochita zoipa kwabasi

    [93] “Ndipo (kumbukirani nkhani iyi, inu ana a Israyeli) pamene tidalandira kwa inu pangano lamphamvu, ndipo tidakukwezerani phiri pamwamba panu (uku tikuti): “Gwiritsani mwamphamvu (malamulo) amene takupatsani, ndipo mverani.” (Iwo) adati: “Tamva (mawu anu), koma tanyozera.” Ndipo adamwetsedwa m’mitima mwawo kukonda kupembedza thole (mwana wang’ombe) chifukwa cha kusakhulupirira kwawo. Nena: “N’choipa zedi chimene chikhulupiliro chanu chikukulamulirani ngati inu mulidi okhulupirira.”

    [94] “Auze (Ayudawo): “Ngati nyumba yomaliza kwa Allah njanu nokha, osati anthu ena (monga momwe mukunenera), ilakalakeni imfa ngati mukunenadi zoona.”

    [95] “Koma sadzailakalaka (imfa) ngakhale pang’ono, chifukwa cha zomwe manja awo adatsogoza (chifukwa cha machimo omwe adadzichitira). Ndipo Allah akudziwa bwino za anthu oipa

    [96] “Ndipo muwapeza (Ayuda) kuti ngokondetsetsa kukhala ndi moyo wautali kuposa anthu ena, kuposanso anthu amene akuphatikiza (Allah ndi mafano). Aliyense wa iwo amafuna atapatsidwa moyo wokwana zaka chikwi chimodzi. Pomwe kupatsidwa kwake moyo wautali sikungamuike kutali ndi chilango. Ndipo Allah akuona zonse zimene akuchita

    [97] “Nena: “Amene akhale mdani wa Gaburieli (chifukwa chobweretsa chivumbulutso kwa Muhammad {s.a.w}, iyeyo ndi mdani wa Allah). Ndithudi, iye waivumbulutsa Qur’an mumtima mwako mwachilolezo cha Allah. Kudzatsimikidzira zomwe zidali patsogolo pake, ndiponso ndi chiongoko ndi nkhani yabwino kwa okhulupirira

    [98] “Amene ali mdani wa Allah, angelo Ake, atumiki Ake, Gaburieli ndi Mikayeli, ndithu Allah ndi mdani wa osakhulupirira

    [99] “Ndithu tavumbulutsa kwa iwe zisonyezo zoonekera. Ndipo palibe wozikana koma okhawo opandukira chilamulo cha Allah

    [100] “Kodi sizili tero kuti panthawi iliyonse akupangana pangano lamphamvu, ena aiwo akulitaya? Koma ambiri aiwo sakhulupirira

    [101] “Ndipo pamene (Ayuda) adawadzera Mtumiki wochokera kwa Allah uku akutsimikidzira chomwe iwo ali nacho, gulu lina mwa omwe adapatsidwa buku adataya buku la Allah kumbuyo kwa misana yawo ngati kuti sakulidziwa

    [102] “Ndipo adatsatira njira za afiti zomwe asatana adali kuwafotokozera m’nthawi ya ufumu wa Sulaiman. Ndipo Sulaiman sadamkane Allah (sadali mfiti), koma asatana ndi amene adamkana, naphunzitsa anthu ufiti (umene adaudziwa kuyambira kale); natsatiranso (njira za ufiti) zimene zinatsitsidwa kwa Angelo awiri Haruta ndi Maruta (ku midzi ya) ku Babulo. Koma Angelowo sadaphunzitse aliyense pokhapokha atamuuza kuti: “Ife ndife mayeso (ofuna kuona kugonjera kwanu malamulo a Allah); choncho musamkane (Allah).” Komabe ankaphunzira kwa iwo njira zolekanitsira pakati pa munthu ndi mkazi wake, (ndi zina zotero). Ndipo sadavutitse aliyense ndi zimenezo koma mwachilolezo cha Allah. Ndipo akuphunzira zomwe zingawavutitse pomwe sizingawathandize. Ndithudi, akudziwa kuti yemwe wausankha (ufitiwo) sadzakhala ndi gawo lililonse (la zinthu zabwino) tsiku lachimaliziro. Ndithudi, nchoipitsitsa chimene adzisankhira okha akadakhala akudziwa

    [103] “Ndipo iwo akadakhulupirira nadzitchinjiriza (ku zoletsedwa), ndithudi, mphoto yochokera kwa Allah ikadakhala yabwino kwa iwo, akadadziwa

    [104] “E inu amene mwakhulupirira! Musam’nenere (Mneneri liwu lakuti) “raina” (ndicholinga chomunenera kuti iye ndi mbutuma), koma mnenereni (liwu lakuti) “utiyang’anire,” ndipo mverani malamulo. Kwa osakhulupirira kuli chilango chopweteka

    [105] “Amene sadakhulupirire mwa anthu a mabuku (Ayuda ndi Akhirisitu) ndi omphatikiza Allah (Arabu), safuna kuti chabwino chilichonse chochokera kwa Mbuye wanu chitsitsidwe kwa inu (Asilamu). Koma Allah amamsankhira chifundo Chake amene wamfuna. Ndipo Allah ndi Mwini ubwino ochuluka

    [106] “Ayah (ndime) iliyonse yomwe tikuifafaniza kapena kuiiwalitsa (mu mtima wako) tikubweretsa yabwino kuposa iyo, kapena yofanana nayo. Kodi sukudziwa kuti Allah Ngokhoza chinthu chilichonse

    [107] “Kodi siudziwa kuti ufumu wakumwamba ndi pansi ngwa Allah? Ndipo inu kupatula Iye Allah mulibe mtetezi ngakhale mthandizi

    [108] “Kodi mukufuna kumfunsa Mtumiki wanu (inu Asilamu) monga momwe Mûsa adafunsidwira kale (mafunso achipongwe)? Ndipo amene angasinthitse chikhulupiliro ndi kusakhulupirira, ndithudi wasokera njira yolingana (yopanda majiga)

    [109] “Ambiri mwa amene anapatsidwa mabuku, akufuna kukubwezani (kukutembenuzani) kuti mukhale osakhulupirira pambuyo pa chikhulupiliro chanu, chifukwa chadumbo lomwe lili m’mitima mwawo (lomwe lawapeza) pambuyo powaonekera choonadi poyera. Choncho akhululukireni ndi kuwasiya kufikira Allah adzabweretse lamulo Lake*; ndithudi Allah Ngokhoza chilichonse

    [110] “Ndipo pempherani Swala moyenera ndiponso perekani Zakaat. Ndipo chilichonse chabwino chimene mukudzitsogozera mukachipeza kwa Allah. Ndithudi, Allah akuona zonse zimene mukuchita

    [111] “Eti akunena: “Palibe amene adzalowe ku Munda wamtendere koma amene ali Myuda Kapena Mkhirisitu.” Zimenezo nzokhumba zawo chabe. Nena: “Bweretsani umboni wanu ngati mukunena zoona.”

    [112] “Ayi, koma amene nkhope yake yagonjera kwa Allah uku akuchita zabwino (kwa anthu anzawo) iye ndi amene adzapeza mphoto yake kwa Mbuye wake. Ndipo pa iwo sipadzakhala mantha, ndiponso iwo sadzadandaula

    [113] “Ndipo Ayuda akumanena: “Akhrisitu alibe chilichonse (chotsamira pa chipembedzo chawo);” naonso Akhrisitu akumanena: “Ayuda alibe chilichonse (chotsamira pa chipembedzo chawo),” pomwe onsewa akuwerenga buku (lomwe adawavumbulutsira popanda kutsatira zili m’bukulo). Momwemonso akunena amene sali odziwa (Arabu opembedza mafano) monga zonena zawo (Ayuda). Allah adzaweruza pakati pawo tsiku la chimaliziro pa zomwe adali kusiyana

    [114] “Kodi alipo woipitsitsa woposa amene akutsekereza (anthu kulowa) m’misikiti ya Allah kuti lisatchulidwe m’menemo dzina Lake nalimbika kuiononga (misikitiyo)? - Kotero kuti sikunali koyenera kwa iwo kulowa mmenemo koma mwa mantha. Kuyaluka kwa pa dziko lapansi nkwawo ndipo tsiku lachimaliziro iwo adzapeza chilango chachikulu

    [115] “Ndipo kuvuma ndi kuzambwe nkwa Allah; ndipo pamalo paliponse pamene mwatembenukira, (pomwe Allah wakulamulirani kuti mutembenukire), pamenepo mupezapo chiyanjo cha Allah. Ndithudi Allah Ngokwanira ponseponse, Wodziwa chilichonse

    [116] “Ndipo (osakhulupirira) akumanena: “Allah wadzipangira mwana.” (Allah) wapatukana ndi zimenezo. Koma (zolengedwa) zonse za kumwamba ndi pansi Nzake. Zonse zikumumvera Iye

    [117] “(Iye ndi) Mlengi wa thambo ndi nthaka popanda chofanizira. Ndipo akafuna chinthu kuti chichitike amangoti: “Chitika,” ndipo chimachitikadi

    [118] “Ndipo aja osadziwa akunena: “Bwanji Allah sakutiyankhula ife? Kapena kutibwerera chizindikiro (chizizwa)?” Mofanana ndi zoyankhula zawozo adanenanso amene adalipo kale. Mitima yawo yalingana. Ndithu Ife tazifotokoza zizindikiro momveka kwa anthu otsimikiza (m’chikhulupiliro)

    [119] “Ndithudi, Ife takutumiza (iwe Mtumiki {s.a.w}) ndi choonadi kuti ukhale wouza nkhani zabwino ndi wochenjeza. Ndipo siudzafunsidwa za anthu a ku Moto

    [120] “Ndipo Ayuda ndi Akhrisitu sangakondwere nawe pokhapokha utatsatira chipembedzo chawo. Nena: “Ndithudi, chiongoko cha Allah ndichomwe chili chiongoko chenicheni.” Ngati utsata zilakolako zawo pambuyo pa zomwe zakudzera, monga kuzindikira (kwenikweni), sudzapeza mtetezi aliyense ngakhale mthandizi kwa Allah

    [121] “Anthu omwe tidawapatsa buku naliwerenga kuwerenga koyenera (kopanda kusintha mawu ake ndi matanthauzo ake), iwo ndi amene akulikhulupirira (bukuli la Qur’an). Koma amene angalikane iwowa ndi omwe ali oonongeka

    [122] “E inu ana a Israyeli! Kumbukirani chisomo changa chomwe ndidakudalitsani nacho. Ndithudi, ndidakuchitirani zabwino kuposa zolengedwa zonse (panthawi imeneyo)

    [123] “Ndipo opani tsiku lomwe munthu aliyense sadzathandiza munthu mnzake ndi chilichonse, ndipo dipo silidzalandiridwa, ngakhale dandaulo lililonse silidzamthandiza, ndiponso iwo sadzapulumutsidwa

    [124] “Ndipo kumbukirani pamene Ibrahim Mbuye wake (Allah) adamuyesa iye mayeso ndi malamulo ambiri; ndipo iye adakwaniritsa. Adamuuza: “Ndithudi, Ine ndichita iwe kukhala mtsogoleri wa anthu.” (Ibrahim adayankha kuti): “Kodi ndi ana anga omwe?” Adati: “(Inde; koma) lonjezo langa silingawafike ochita zoipa.”

    [125] “Ndipo (kumbukiraninso nkhani iyi) pamene tidapanga nyumba (ya Al-Kaaba) kuti pakhale pamalo pobwererapo anthu (poyendera anthu) ndikukhalanso malo achitetezo. Ndipo pachiteni kukhala popemphelera Swala pamalo pomwe Ibrahim adali kuimilira (pomamga nyumbayo). Ndipo tidalamula Ibrahim ndi Ismail kuti: “Ayeretsereni nyumba Yanga oizungulira (pochita twawaf) ndi amene akuchita m’bindikiro, owerama ndi kulambira (kuswali mmememo)

    [126] “Ndipo (kumbukirani nkhani iyi) pamene Ibrahim adanena: “E Mbuye wanga! Uchiteni mzinda uwu (wa Makka) kukhala wa chitetezo, ndipo zipatseni nzika zake zipatso, amene akukhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro mwa iwo. Allah adati: “Nayenso wosakhulupirira ndinkondweretsa pang’ono; kenako ndidzamkankhira ku chilango cha Moto. Taonani kunyansa malo obwerera

    [127] “Ndipo (kumbukiraninso) pamene Ibrahim ndi Ismail ankakhazikitsa maziko a nyumba (uku akupempha kwa Allah): “E Mbuye wathu! Tilandireni (ntchito yathuyi), ndithudi, Inu ndinu Akumva; Odziwa.”

    [128] ““E Mbuye wathu! Tichiteni Kukhalala Asilamu (ogonjera Inu), pamodzinso ndi ana athu muwachite kukhala fuko la Chisilamu (logonjera Inu). Ndipo tidziwitseni (njira) za mapemphero athu; ndipo landirani kulapa kwathu, ndithudi, Inu Ndinu Wolandira kulapa mochuluka; Wachisoni chosatha.”

    [129] ““E Mbuye wathu! Atumizireni mtumiki wochokera mwa iwo, kuti awawerengere Ayah (ndime) zanu ndikuwaphunzitsa buku (Lanu) ndi nzeru ndikuti awayeretse. Ndithudi Inu Ndinu Amphamvu zoposa, Anzeru zakuya.”

    [130] “Kodi ndani anganyozere chipembedzo cha Ibrahim posakhala yemwe mtima wake uli wopusa? Ndithudi, tidamsankha (Ibrahim) pa dziko lapansi; ndipo iye tsiku lachimaliziro adzakhala m’modzi wa anthu abwino.”

    [131] “(Kumbukiraninso) pamene Mbuye wake adamuuza kuti: “Khala Msilamu (gonjera).” (Iye) adati: “Ndili Msilamu (ndagonjera) kwa Mbuye wa zolengedwa zonse.”

    [132] “Ndipo Ibrahim adalangizanso ana ake za zimenezi, chonchonso Ya’qub (adalangizanso ana ake kuti): “E inu ana anga! Ndithudi, Allah wakusankhirani chipembedzo; choncho musafe pokhapokha muli Asilamu (ogonjera Mulungu).”

    [133] “Kapena inu (Ayuda ndi Akhrisitu) mudalipo pamene Ya’qub idamdzera imfa, pamene adati kwa ana ake: “Kodi pambuyo panga mudzapembedza yani?” Iwo adayankha nati: “Tidzapembedza Mulungu wako, Mulungu wa makolo ako; Ibrahim, Ismail ndi Ishâq; Mulungu mmodzi basi. Ndipo ife kwa Iye tili Asilamu (ogonjera).”

    [134] “Umenewo ndi mbadwo wa anthu umene udamka kale. Udzapeza zimene udachita, ndipo inunso mudzapeza zimene mudachita. Ndipo inu simudzafunsidwa zimene iwo ankachita

    [135] “Ndipo (Ayuda ndi Akhrisitu) adati (kwa Asilamu): “Khalani Ayuda kapena Akhrisitu mukhala oongoka.” Nena: “Koma (tikutsata) chipembedzo cha Ibrahim yemwe adaleka zipembedzo zopotoka, ndipo sadali mwa ophatikiza (Allah ndi mafano).”

    [136] “Nenani (inu Asilamu kuwauza Ayuda ndi Akhrisitu); “Takhulupirira Allah ndi zimene zidavumbulutsidwa kwa ife, ndi zimene zidavumbulutsidwa kwa Ibrahim, Ismail, Ishâq, Ya’qub ndi zidzukulu (zake) ndi zimene adapatsidwa Mûsa, Isa (Yesu), ndiponso zimene adapatsidwa aneneri (ena) kuchokera kwa Mbuye wawo. Sitilekanitsa pakati pa mmodzi wa iwo (koma onse tikuwakhulupirira). Ndipo ife kwa Iye tili Asilamu (ogonjera).”

    [137] “Choncho ngati akhulupirira (Ayuda ndi Akhrisitu) monga mmene mwakhulupirira inu, ndiye kuti awongoka. Koma ngati akutembenuka (posakhulupirira) ndiye kuti iwo ali m’kutsutsana. Choncho Allah akuteteza ku zoipa zawo, ndipo Iye Ngwakumva; Wodziwa

    [138] “(Tsatirani) chiongoko cha Allah (Chisilamu). Kodi ndi ndani amene ali ndi chiongoko chabwino kuposa Allah? Ndipo ife Iye Yekha timupembedza

    [139] “Nena (iwe Muhammad {s.a.w} kwa Ayuda ndi Akhrisitu): “Ha! Mukutsutsana nafe za Allah (ponena kuti bwanji wapereka uneneri kumbali ya ife), pomwe Iye ndi Mbuye wathu ndiponso Mbuye wanu? (Pamene mudali olungama adakupatsani uneneri, ndipo pamene mudakhota adakulandani natipatsa ife). Ife tili ndi zochita zathu; inunso muli ndi zochita zanu, ndipo ife tikudzipereka kwathunthu kwa Iye (Allah).”

    [140] “Kapena (inu Ayuda) mukunena kuti Ibrahim, Ismail Ishâq, Yaqub ndi zidzukulu anali Ayuda kapena Akhrisitu? Nena: “Kodi inu ndi odziwa kwambiri kapena Allah?” Kodi ndani woipitsitsa koposa yemwe wabisa umboni omwe ali nao ochokera kwa Allah! Komatu Allah sali wonyalanyaza pa zimene mukuchita

    [141] “Umenewo ndi mbadwo wa anthu umene udamka kale. Udzapeza zimene udachita, ndipo inunso mudzapeza zimene mudachita. Ndipo inu simudzafunsidwa zimene iwo ankachita

    [142] ۞ Posachedwapa mbutuma za anthu zikhala zikunena: “Nchiyani chimene chawatembenuza ku chibula (mbali yoyang’ana popemphera) chawo chomwe akhala akulunjika nkhope zawo.” Nena: “Kuvuma ndi kuzambwe ndi kwa Allah amamuongolera amene wamfuna kunjira yolunjika.”

    [143] “Choncho takusankhani (inu Asilamu) kukhala mpingo wabwino (wapakatikati) kuti mukhale mboni pa anthu ndi kuti Mtumiki (s.a.w) akhale mboni pa inu. Ndipo chibula (choyang’ana mbali ya ku Yerusalemu) chomwe udali nacho sitidachichite koma kuti timdziwitse (adziwike kwa anthu) amene akutsata Mtumiki (s.a.w), ndi yemwe akutembenukira m’mbuyo. Ndipo ndithudi, chidali chinthu chovuta kupatula kwa omwe Allah wawaongola. Ndipo nkosayenera kwa Allah kusokoneza Swala zanu, pakuti Allah Ngoleza kwabasi kwa anthu, Ngwachifundo chambiri

    [144] “Ndithudi, taona kutembenukatembenuka kwa nkhope yako (kuyang’ana) kumwamba. Choncho tikutembenuzira ku chibula chimene ukuchifunacho. Tero tembenuzira nkhope yako kumbali ya Msikiti Wopatulika (Al-Kaaba). Ndipo paliponse pamene mulipo yang’anitsani nkhope zanu kumene kuli (msikitiwo). Ndithudi amene adapatsidwa buku akudziwitsitsa kuti chimenecho nchoonadi chochokera kwa Mbuye wawo. Ndipo Allah siwonyalanyaza zimene akuchita. (Koma chilichonse chikulembedwa m’kaundula)

    [145] “Ndipo awo adapatsidwa buku ngakhale utabwera ndi chisonyezo cha mtundu uliwonse satsata chibula chako, ngakhalenso iwe sutsata chibula chawo. Ndipo ena a iwo sali otsatira chibula cha ena (Akhrisitu satsata chibula cha Ayuda, ndipo Ayuda satsata chibula cha Akhrisitu). Ngati utsatira zofuna zawo, pambuyo pakuti kwakudzera kudziwa ndiye kuti ukhala mwa ochita zoipa

    [146] “Aja amene tidawapatsa buku akumuzindikira (Mtumiki Muhammad {s.a.w}) monga momwe amawazindikilira ana awo. Koma ena mwa iwo akubisa choonadi uku akudziwa

    [147] “(Kuyang’ana ku Al-Kaaba popemphera Swala ndicho) choonadi chomwe chachokera kwa Mbuye wako, choncho usakhale mmodzi mwa openekera

    [148] “Ndipo (mpingo) uliwonse udali ndi chibula chimene udali kuchilunjika. Choncho pikisanani pochita zabwino. Paliponse pamene mungakhale Allah adzakubweretsani nonsenu pamodzi (pa tsiku la chimaliziro). Ndithudi, Allah Ngokhoza chinthu chilichonse

    [149] “Ndipo paliponse pomwe wapita tembenuzira nkhope yako kumbali ya Msikiti Wopatulika (panthawi yopemphera). Chimenecho nchoonadi chochokera kwa Mbuye wako. Ndipo Allah sali wonyalanyaza zimene mukuchita

    [150] “Paliponse pamene wapita (iwe Mtumiki {s.a.w}) tembenuzira nkhope yako kumbali ya Msikiti Wopatulika. Ndipo paliponse pamene (inu Asilamu) muli tembenuzirani nkhope zanu kumbali yake (ya Msikitio) kuti anthu asakhale ndi mtsutso pa inu, kupatula amene adzichitira zoipa mwa iwo. Tero musawaope, koma opani Ine, ndipo ndikwaniritsa chisomo Changa pa inu kuti muongoke

    [151] “Monganso tamtumizira Mtumiki (s.a.w) kwa inu wochokera mwa inu kuti akuwerengereni Ayah (ndime) Zathu, ndikukuyeretsani (kuuve wopembedza mafano) ndi kukuphunzitsani buku ndi nzeru, ndikukuphunzitsani zimene simunali kuzidziwa

    [152] “Choncho ndikumbukireni (pondithokoza pa mtendere umene ndakupatsaniwu). Nanenso ndikukumbukirani (pokulipirani mphoto yaikulu). Ndipo ndiyamikeni; musandikane

    [153] “E inu amene mwakhulupirira! Dzithandizeni (pa zinthu zanu) popirira, ndi popemphera Swala. Ndithudi, Allah ali pamodzi ndi opirira

    [154] “Ndipo musanene za amene aphedwa pa njira ya Allah kuti: “Ngakufa.” Iyayi ngamoyo, koma inu simuzindikira

    [155] “Ndipo ndithu tikuyesani ndi chinachake monga mantha, njala, kuchepa kwa chuma, kutaika kwa miyoyo ndi kuonongeka kwa mbeu. Tero auze nkhani yabwino opirira

    [156] “Omwe vuto lililonse likawapeza amati: “Ndithudi, ife nga Allah, ndipo ndithu kwa Iye tidzabwerera.”

    [157] “Otero ndi amene pa iwo pali madalitso ochokera kwa Mbuye wawo ndi chifundo. Ndiponso iwo ndi amene ali oongoka

    [158] “Ndithudi, Safaa ndi Marwa ndizizindikiro zolemekezera chipembedzo cha Allah. Choncho, amene akukachita mapemphero a Hajj ku nyumbayo, kapena kuchita Umrah, sikulakwa kwa iye kuzungulira pamenepo (pakati pamapiri amenewo). Ndipo amene achite chabwino modzipereka (adzalipidwa). Ndithudi Allah Ngothokoza; Ngodziwa

    [159] “Ndithudi, amene akubisa zimene tavumbulutsa zomwe ndi zisonyezo zoonekera poyera, ndi chiongoko pambuyo pozifotokoza mwatsatanetsatane kwa anthu m’Buku, Allah akuwatembelera iwo. Ndiponso akuwatembelera otembelera

    [160] “Kupatula amene alapa ndi kukonza (zolakwika) nachilongosola (choonadicho kwa anthu), iwowo ndi amene ndiwalandira kulapa kwao. Ndipo ine Ngolandira kulapa kwambiri, Ngwachisoni chosatha

    [161] “Ndithudi, arnene sadakhulupirire, namwalira ali osakhulupirira, pa iwo pali matembelero a Allah, angelo ndi anthu onse

    [162] “M’menemo (m’chilango cha matembelero) adzakhalamo nthawi yaitali. Ndipo chilango sichidzapeputsidwa kwa iwo, ndipo sadzapatsidwa nthawi (yopumula)

    [163] “Ndipo mulungu wanu ndi Mulungu mmodzi basi. Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Ngwachifundo chambiri, Ngwachisoni chosatha

    [164] “Ndithudi, m’kulenga kwa thambo ndi nthaka, ndi kusinthana kwa usiku ndi usana, ndi (kuyenda kwa) zombo zikulu-zikulu zomwe zikuyenda pa nyanja (zitasenza zinthu) zothandiza anthu, ndi madzi amene Allah wawatsitsa kuchokera ku mitambo, naukitsira nawo nthaka pambuyo pokhala youma, nawanditsa m’menemo mtundu uliwonse wa nyama (chifukwa cha madziwo), ndi m’kusinthanasinthana kwa mphepo, ndi mitambo yomwe yalamulidwa kuyenda pakati pa thambo ndi nthaka; ndithudi, (m’mzimenezo) muli zisonyezo kwa anthu anzeru, (kuti Allah alipo)

    [165] “Pali ena mwa anthu amene akudzipangira milungu naifanizira ndi Allah. Amaikonda monga momwe akadamkondera Allah. Koma (Asilamu) amene akhulupirira amamkonda Allah koposa. Ndipo akadaona amene adzichitira zoipa pamene azikachiona chilango (akadazindikira kuti) ndithu mphamvu zonse nza Allah, ndipo ndithu Allah Ngolanga mwaukali

    [166] “(Akumbutse) nthawi imene otsatidwa adzawakana amene adali kuwatsata uku atachiona chilango. Ndipo mgwirizano pakati pawo udzaduka

    [167] “Ndipo otsatirawo adzati: “Kukadakhala kotheka kwa ife kubwerera (ku moyo wa pa dziko) tikadawakana monga iwo atikanira.” Umo ndi momwe Allah adzikawaonetsera zochita zawo kukhala madandaulo awo. Ndipo iwo sadzatulukanso ku Moto

    [168] “E, inu anthu! Idyani zabwino zimene zili m’nthaka zomwe zili zololedwa; ndipo musatsate mapazi a satana. Iye kwa inu ndi mdani woonekeratu

    [169] “Ndithu iye amangokulamulani kuchita zoipa ndi zauve, ndikuti mumnamizire Allah pomunenera zimene simukuzidziwa

    [170] “Ndipo kukanenedwa kwa iwo (kuti): “Tsatirani zimene Allah wavumbulutsa;” akunena: “Koma tikutsatira zimene tidawapeza nazo atate athu.” Kodi ngakhale kuti atate awo sadali kuzindikira chilichonse ndiponso sadali oongoka (awatsatirabe)

    [171] “Ndipo fanizo la amene sadakhulupirire (omwe akulalikidwa mawu a Allah, ndi makani awo) lili ngati (mbusa) yemwe akukuwira ziweto zake ndi kuzikalipira pomwe izo sizimva tanthauzo la mawu oitanawo, koma kuitana (chabe) ndi kufuula. (Iwo) ndi agonthi, abubu ndi akhungu. Tero iwo sangazindikire

    [172] “E inu amene mwakhulupirira! Idyani zinthu zabwino zimene takupatsani, ndipo yamikani Allah ngatidi inu mukumpembedza Iye yekha

    [173] “Iye akukuletsani (kudya) nyama yofa yokha, liwende, nyama yankhumba ndi nyama yodulidwa poikuwira mayina a mafano kusiya Allah. Koma amene wasimidwa (nadya) popanda kuchikhumba choletsedwacho ndi mosapyoza muyeso palibe tchimo kwa iye. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni zedi

    [174] “Ndithudi, amene akubisa zomwe Allah adavumbulutsa m’buku (la Baibulo) m’malo mwake nasankha zinthu zamtengo wochepa, iwo sadya china mmimba mwawo koma moto basi; ndipo Allah sadzawayankhula tsiku lachimaliziro (mwachifundo koma mokwiya); ndipo sadzawayeretsa. Ndipo iwo adzapeza chilango chopweteka

    [175] “Iwo ndi amene asinthanitsa kusokera ndi chiongoko, ndiponso chilango ndi chikhululuko. Kodi ndichiyani chikuwachititsa kukhala opirira ndi Moto

    [176] “Zimenezo nchifukwa chakuti Allah adavumbulutsa buku Lake mwa choonadi (ndipo iwo adalikana). Koma amene asemphana pa zabukuli ali mu nkangano wonkera nawo kutali kusiya choonadi

    [177] “Ubwino suli potembenuzira nkhope zanu mbali yakuvuma ndi kuzambwe (popemphera Swala); koma ubwino weniweni ndi (wa omwe) akukhulupirira Allah, tsiku lachimaliziro, angelo, buku ndi aneneri; napereka chuma - uku eni akuchifunabe - kwa achibale ndi amasiye, ndi masikini ndi a paulendo (omwe alibe choyendera), ndi opempha, ndi kuombolera akapolo; napemphera Swala, napereka chopereka (Zakaat); ndi okwaniritsa malonjezo awo akalonjeza, ndi opirira ndi umphawi ndi matenda ndi panthawi yankhondo. Iwowo ndi amene atsimikiza (Chisilamu chawo). Ndiponso iwowo ndi omwe ali oopa Allah

    [178] “E inu amene mwakhulupirira! Kwalamulidwa kwa inu Qiswas (kubwezerana) molingana kwa ophedwa; mfulu kwa mfulu, kapolo kwa kapolo, mkazi kwa mkazi. Koma amene wakhululukidwa ndi m’bale wakeyo pa chinthu Chilichonse, atsatire ndi kulonjelera dipolo mwaubwino. (Nayenso wolipa) apereke kwa iye mwa ubwino. Kumeneko ndikufewetsa kumene kwachokera kwa Mbuye wanu, ndiponso chifundo. Ndipo amene alumphe malire pambuyo pa izi, iye adzapeza chilango chopweteka

    [179] “Mu Qiswas (kubwezerana kofanana) muli kusunga moyo kwa inu, E, inu eni nzeru! Kuti mudzitchinjirize (ku mchitidwe ophana)

    [180] “Kwalamulidwa kwa inu kuti mmodzi wanu imfa ikamuyandikira, ngati asiya chuma, apereke malangizo (pa zachumacho) kwa makolo ake awiri ndi achibale ake, mwa ubwino. Ichi nchilamulo kwa oopa Allah

    [181] “Ndipo amene asinthe malangizowo pambuyo pakuwamva; uchimo wake uli pa amene akusinthawo. Ndithudi, Allah Ngwakumva; Ngodziwa

    [182] “Ndipo amene waopa kuti wopereka wasiya angapendekere kumbali yokhota kapena ku uchimo, nalinganiza pakati pawo, palibe tchimo kwa iye. Ndithudi, Allah ngokhululuka zedi, Ngwachifundo chambiri

    [183] “E inu amene mwakhulupirira! Kwalamulidwa kwa inu kusala (m’mwezi wa Ramadan) monga momwe kudalamulidwira kwa anthu akale, inu musadabwere kuti muope Allah (popewa zoletsedwa)

    [184] “(Kusalaku nkwa) masiku owerengeka. Koma amene akhale odwala mwa inu kapena akhale paulendo, (namasula masiku ena), akwaniritse chiwerengerocho m’masiku ena. Ndipo kwa amene sangathe kusala apereke dipo lodyetsa masikini. Ndipo amene achite zabwino mwa chifuniro chake, kutero ndibwino kwa iye. Ndipo kusala (pamene kukulolezedwa kumasula) ndibwino kwa inu, ngati muli odziwadi (kufunika kwa kusala)

    [185] “(Mwezi mwalamulidwa kusalawu ndi) mwezi wa Ramadan womwe mkati mwake Qur’an idavumbulutsidwa kuti ikhale chiongoko kwa anthu ndi zizindikiro zoonekera poyera za chiongoko. Ndikutinso ikhale cholekanitsa (pakati pa choonadi ndi bodza). Ndipo mwa inu amene akhalepo (pa mudzi) m’mweziwu, asale. Koma amene ali wodwala, kapena ali pa ulendo, akwaniritse chiwerengero m’masiku ena (cha masiku amene sadasale). Allah akukufunirani zopepuka ndipo samakufunirani zovuta, ndiponso (akufuna) kuti mukwaniritse chiwerengerocho ndi kumlemekeza Allah chifukwa chakuti wakutsogolerani, ndikutinso mukhale othokoza

    [186] “Ndipo akapolo anga akakufunsa za ine, (auze kuti) Ine ndili pafupi nawo. Ndimayankha zopempha za wopempha pamene akundipempha. Choncho iwo ayankhe kuitana kwanga ndipo andikhulupirire kuti aongoke

    [187] “Kwaloledwa kwa inu mu usiku wosala kukumana ndi akazi anu. Iwo ali ngati chovala chanu, inunso muli ngati chovala chawo. Allah wadziwa kuti mudali kudzichitira chinyengo nokha. Choncho walandira kulapa kwanu ndipo wakukhululukirani. Tsopano khudzanani nawo ndipo funani chimene Allah wakulamulirani, ndipo idyani ndi kumwa mpaka udziwike bwinobwino kwa inu ulusi woyera kuchokera ku ulusi wakuda kum’bandakucha (kufikira mudziwe kuti kucha kwalowa, usiku watha). Kenako kwaniritsani kusala mpaka dzuwa litalowa. Ndipo musakhudzane nawo (akazi anu) pamene inu mukuchita mbindikiro m’misikiti. Amenewo ndi malire a Allah; choncho musaayandikire. Motere ndimo Allah akulongosolera mwatsatanetsatane zisonyezo zake kwa anthu kuti akhale oopa Allah (potsatira malamulo ake ndi kusiya zoletsedwa)

    [188] “Ndipo musadye chuma chanu pakati panu mwachinyengo pochipereka kwa oweruza (m’njira ya ziphuphu) ndi cholinga choti mudye gawo la chuma cha anthu mwa uchimo uku inu mukudziwa

    [189] “Akukufunsa za miyezi nena: “Imeneyi ndi miyeso ya nthawi yozindikilira anthu zinthu zawo ndi nthawi ya Hajj.” Ndipo Siubwino kulowera m’nyumba zanu mbali ya kumbuyo kwake, koma ubwino ndiwayemwe akuopa Allah. Ndipo lowerani m’nyumba podzera m’makomo ake. Opani Allah kuti inu mupambane

    [190] “Ndipo menyanani nao nkhondo pa njira ya Allah (modziteteza) amene akukuthirani nkhondo. Koma musalumphe malire (powamenya amene sadakuputeni), ndithu Allah sakonda olumpha malire

    [191] “Ndipo athireni nkhondo (amene akukuthirani nkhondo popanda chifukwa) paliponse pamene mwawapeza; ndipo atulutseni paliponse pamene adakutulutsani; chifukwa kusokoneza anthu pa chipembedzo chawo nkoipitsitsa kuposa kupha. Koma musamenyane nawo pafupi ndi Msikiti Wopatulika pokhapokha atayamba ndiwo kukumenyani pamenepo. Chomwecho ngati atamenyana nanu pamenepo inunso amenyeni. Motero ndi momwe ilili mphoto ya osakhulupirira

    [192] “Koma ngati asiya, ndithudi Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha

    [193] “Ndipo menyanani nao kufikira pasakhale masautso (ochokera kwa iwo powasautsa asilamu popanda chifukwa). Ndipo chipembedzo chikhale cha Allah (osati kupembedza anthu). Koma ngati asiya, pasakhale mtopola kupatula kwa okhawo amene ali ochita zoipa

    [194] “Mwezi wopatulika kwa mwezi wopatulika; ndipo zinthu zopatulika paikidwa kubwezerana. Ndipo amene wakuchitirani mtopola, inunso mchitireni mtopola molingana ndi momwe wakuchitirani mtopola, ndipo opani Allah (musapyoze kuposa momwe wakuchitirani). Ndipo dziwani kuti Allah ali pamodzi ndi oopa

    [195] “Ndipo perekani chuma chanu pa njira ya Allah, ndiponso musadziponye ku chionongeko ndi manja anu; chitani zabwino. Ndithudi, Allah amakonda ochita zabwino

    [196] “Ndipo kwaniritsani Hajj ndi Umrah chifukwa chofuna kukondweretsa Allah. (Izi zili mkutsimikiza kulowa m’mapemphero a Hajj). Ndipo ngati mutatsekerezedwa (kukwaniritsa mapempherowo), choncho zingani nyama zimene zili zosavuta kuzipeza (monga mbuzi), ndipo musamete mitu yanu kufikira nsembeyo ifike pamalo pake pozingirapo (pomwe ndi pamalo pamene mwatsekerezedwapo). Ndipo amene mwa inu ali odwala kapena ali ndi zovutitsa ku mutu kwake, (nachita zomwe zidali zoletsedwa monga kumeta) apereke dipo la kusala kapena kupereka sadaka (chopereka chaulere), kapena kuzinga chinyama. Ndipo ngati muli pa mtendere, choncho amene angadzisangalatse pochita Umrah kenako nkuchita Hajj, azinge nyama imene ili yosavuta kupezeka (monga mbuzi). Ndipo Amene sadapeze, asale masiku atatu konko ku hajjiko ndipo asalenso masiku asanu ndi awiri mutabwerera (kwanu). Amenewo ndi masiku khumi okwanira. Lamuloli ndi la yemwe banja lake silili pafupi ndi Msikiti Wopatulika. Ndipo opani Allah, dziwani kuti Allah Ngwaukali polanga

    [197] “(Mapemphero a) Hajj ali ndi miyezi yodziwika, (yomwe ndi: Shawwal, Dhul Qa’da ndi Dhul Hijjah). Amene watsimikiza kuchita Hajj m’miyezi imeneyo, asachite ndi kuyankhula zauve, ndiponso asapandukire malamulo (pochita zoletsedwa uku iye ali m’mapemphero a Hajj), ndiponso asakangane ali m’Hajjimo. Ndipo chabwino chilichonse chimene mungachite, Allah achidziwa. Ndipo dzikonzereni kamba wa paulendo, ndithu kamba wabwino (wadziko lapansi) ndi amene angakupewetseni kupemphapempha, (koma kamba wabwino wa tsiku lachimaliziro ndiko kuopa Allah). Choncho ndiopeni inu eni nzeru

    [198] “Sikulakwa kwa inu kufunafuna zabwino kwa Mbuye wanu (pogulitsa zinthu zanu uku muli m’mapemphero a Hajj, kapena kugula). Ndipo mukabwerera kuchokera ku Arafat, tamandani Allah pamalo otchedwa Masha’r Harâm (Muzdalifa). Ndipo mkumbukireni monga momwe adakutsogolerani, chikhalirecho kale mudali mwa osokera

    [199] “Kenako yendani limodzi kuchokera pamalo pamene akuchokerapo anthu onse (pomwe ndi pa Arafat), ndipo pemphani chikhululuko kwa Allah. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha

    [200] “Ndipo mukamaliza mapemphero anu (tsiku la Idi komwe ndikuponya sangalawe, kuzinga nyama za nsembe, kumeta ndi kuzungulira Ka’aba (Tawaful Ifâda), mtamandeni Allah monga momwe mudali kutamandira makolo anu kapena mtamandeni koposa. Ndipo alipo ena mwa anthu amene akunena (kuti): “E Mbuye wathu! Tipatseni padziko lapansi.” Ndipo iwo alibe gawo lililonse pa tsiku lachimaliziro

    [201] “Ndipo alipo ena mwa iwo omwe akunena kuti: “E Mbuye wathu! tipatseni zabwino pa dziko lapansi komanso pa tsiku lachimaliziro mudzatipatsenso zabwino, ndi kutitchinjiriza ku chilango cha Moto.”

    [202] “Iwo ali ndi gawo la zimene adachita; ndipo Allah Ngwachangu pakuwerengera

    [203] “Ndipo mtamandeni Allah m’masiku owerengeka. Koma amene wachita changu pa masiku awiri okha (nabwerera kwawo) palibe tchimo pa iye. Ndipo amene wachedwerapo palibenso tchimo pa iye kwa amene akuopa Allah. Choncho opani Allah, ndipo dziwani kuti kwa Iye nkumene mudzasonkhanitsidwa

    [204] “Ndipo mwa anthu alipo amene zoyankhula zake zikukondweretsa (iwe) pano pa dziko la pansi, (koma tsiku lachimaliziro kuipa kwake kudzadziwika). Ndipo iye akutsimikizira Allah kuti akhale mboni pa zomwe zili mu mtima mwake pomwe iye ndi wa makani kwambiri

    [205] “Koma akachoka (kwa iwe) akuyenda pa dziko (uku ndi uku) ncholinga chofuna kuyipitsapo ndi kuononga zomera ndi miyoyo. Komatu Allah sakonda kuononga

    [206] “Ndipo akauzidwa kuti: “Opa Allah”, Akugwidwa ndi mwano womupititsa ku machimo, choncho Jahannam ikukwana kwa iye (kuwuchotsa mwano wakewo). Taonani kuipa kwa malo wokakhazikikamo

    [207] “Ndipo pali wina mwa anthu amene akugulitsa mzimu wake chifukwa chofuna chiyanjo cha Allah; ndipo Allah Ngodekha kwa akapolo ake

    [208] “E inu amene mwakhulupirira! Lowani m’Chisilamu chonse ndipo musatsatire mapazi a satana. Ndithu iye ndi mdani wanu woonekera poyera

    [209] “Ndipo ngati mutaterezuka (kuchimwa) pambuyo pokudzerani zisonyezo (za Allah) zoonekera poyera, dziwani kuti Allah Ngwamphamvu zoposa; Ngwanzeru zakuya

    [210] “Kodi pali china chimene akuyembekeza posakhala kuwadzera Allah m’mithunzi ya mitambo ndi (kuwadzera) angelo; nkuweruzidwa chilamulo (chakuonongeka kwawo)? Komatu zinthu zonse zimabwezedwa kwa Allah

    [211] “Afunse ana a Israyeli kuti ndizizindikiro zingati zopenyeka zomwe tidawapatsa? Komatu amene angasinthe chisomo cha Allah pambuyo pomudzera, (Allah adzamulanga), ndithudi, Allah ngolanga mwaukali

    [212] “Moyo wa pa dziko lapansi wakometsedwa kwa amene sadakhulupirire, ndipo amawachitira chipongwe amene akhulupirira. Koma amene aopa Allah adzakhala pamwamba pawo tsiku la chiweruziro, ndipo Allah amapatsa amene wamfuna popanda chiwerengero

    [213] “Anthu onse adali a chipembedzo chimodzi (cha Chisilamu panthawi ya Adam kufikira Nuh kenako adayamba kupatukana), ndipo Allah adatumiza aneneri onena nkhani zabwino ndi ochenjeza; ndipo pamodzi nawo adavumbulutsa mabuku achoonadi kuti aweruzire pakati pa anthu pa zimene adasemphana. Ndipo sadasemphane pa zimenezo koma aja amene adapatsidwa mabukuwo pambuyo powadzera zizindikiro zoonekera poyera, chifukwa chakuchitirana dumbo pakati pawo. Koma Allah adawaongolera amene adakhulupirira kuchoonadi cha zomwe adasempaniranazo, mwachifuniro chake. Ndipo Allah amamutsogolera ku njira yolunjika amene wamfuna

    [214] “Kodi mukuganiza kuti mukalowa ku Munda wamtendere pomwe sanakudzereni masautso olingana (ndi omwe) adawapeza amene adamuka kale inu musanabadwe? Kusauka ndi matenda zidawakhudza, ndipo adanjenjemeretsedwa koopsa kufikira mtumiki pamodzi ndi amene adakhulupirira naye adati: “Chipulumutso cha Allah chibwera liti?” Dziwani kuti ndithu chipulumutso cha Allah chili pafupi

    [215] “Akukufunsa kuti apereke chiyani? Nena: “Chuma chilichonse chimene mungachipereke, (chiperekeni) kwa makolo awiri, achibale, kwa ana amasiye, kwa osauka, ndi kwa apaulendo. Ndipo chabwino chilichonse chimene mungachite, ndithudi, Allah akuchidziwa. “

    [216] “Kwalamulidwa kwa inu kumenya nkhondo (yotetezera chipembedzo cha Allah ) pomwe iyo (nkhondoyo) njodedwa ndi inu. Komatu mwina mungachide chinthu pomwe icho chili chahwino kwa inu. Mwinanso mungakonde chinthu pomwe icho chili choipa kwa inu. Koma Allah ndiyemwe akudziwa, ndipo inu simudziwa

    [217] “Akukufunsa za (lamulo la) kumenya nkhondo m’miyezi yopatulika. nena: “Kumenya nkhondo m’miyeziyo ndi tchimo lalikulu. Komatu kuwatsekereza anthu ku njira ya Allah, ndi kumkana Allah, (ndi kuletsa anthu) ku Msikiti Wopatulikawo, ndi kutulutsa anthu m’menemo nditchimo loposa kwa Allah. Ndipo kutsekereza anthu kuchipembedzo chawo nzoipa kwabasi kuposa kupha. Ndipo sasiya kumenyana nanu kufikira akuchotseni m’chipembedzo chanu ngati angathe. Ndipo mwa inu amene atuluke m’chipembedzo chake, kenako namwalira uku ali osakhulipirira, iwo ndi omwe ntchito zawo zaonongeka pa dziko lapansi mpaka tsiku lachimaliziro. Ndipo iwo ndi anthu a ku Moto. M’menemo adzakhalamo nthawi yaitali

    [218] “Ndithudi, amene akhulupirira, ndi amene asamuka namenya nkhondo pa njira ya Allah, iwo ndi amene akuyembekezera chifundo cha Allah. Ndipo Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha

    [219] “Akukufunsa za mowa ndi njuga. Nena: “M’zimenezo muli (masautso ndi) uchimo waukulu, ndi zina zothandiza kwa anthu. Koma uchimo wake ngwaukulu zedi kuposa zothandiza zake.” Ndipo akukufunsa kuti aperekenji: Auze: “Chimene chapyolerapo (pa zofuna zanu).” Umo ndi momwe Allah akukufotokozerani ma Ayah (malamulo) kuti mulingalire

    [220] “Za m’dziko lapansi ndi (zinthu) za tsiku lachimaliziro. Ndipo akukufunsa za ana amasiye, nena: “Kuwachitira zabwino ndiwo ubwino; ngati mutasakanikirana nawo, (ndibwinonso). Iwo ndi abale anu; ndipo Allah akumdziwa woononga ndi wochita zabwino. Ndipo Allah akadafuna, akadakukhwimitsirani malamulo. Ndithudi, Allah Ngwamphamvu zoposa; Ngwanzeru zakuya.”

    [221] “Ndipo musakwatire akazi opembedza mafano mpaka atakhulupirira. Ndithudi, mdzakazi wokhulupirira (Allah) ngwabwino kuposa mfulu ya chikazi yopembedza mafano, ngakhale itakukondweretsani. (Ndipo ana anu aakazi a Chisilamu) musawakwatitse kwa amuna osakhulupirira, mpaka akhulupirire. Ndipo kapolo wokhulupirira (Allah) ngwabwino kuposa mfulu yopembedza mafano, ngakhale ikukukondweretsani. Iwowo akuitanira ku Moto. Koma Allah akuitanira ku Munda wamtendere ndi ku chikhululuko mwa lamulo lake. Ndipo Iye akulongosola mwatsatanetsatane ndime za mawu ake kwa anthu, kuti athe kukumbukira

    [222] “Ndipo (iwo) akukufunsa za kukhala malo amodzi ndi azimayi panthawi imene akusamba, auze (kuti): “Zimenezo ndizovulaza (ndiponso ndiuve). Choncho apatukireni akazi m’nthawi ya matenda akumwezi, ndipo musawayandikire mpaka ayere. Ngati atayera, kumananaoni kupyolera m’njira yomwe Allah wakulamulani. Ndithu Allah amakonda olapa, ndiponso amakonda odziyeretsa. ”

    [223] “Akazi anu ali ngati minda yanu; choncho idzereni minda yanu mmene mungafunire; koma dzitsogozereni zabwino nokha, ndipo opani Allah, ndipo dziwaninso kuti mudzakumana naye. Ndipo auze nkhani yabwino amene akhulupirira

    [224] “Ndipo kulumbilira kwanu dzina la Allah musakuchite kukhala chokuletsani kuchita zinthu zabwino (za m’Chisilamu) ndi kuopa Allah, ndi kuyanjanitsa pakati pa anthu. Ndipo Allah Ngwakumva, Ngodziwa

    [225] “Allah sangakulangeni pa kulumbira kwanu kopanda pake, koma adzakulangani chifukwa cha malumbiro anu amene mitima yanu yatsimikiza mwa mphamvu. Ndipo Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngoleza

    [226] “Kwa omwe akulumbilira kuti adzipatula kwa akazi awo, (nyengo yawo) ayembekezere miyezi inayi. Koma ngati atabwerera (nakhala pamodzi ndi akazi awo), ndithudi Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni zedi

    [227] “Ndipo ngati atatsimikiza kulekana, ndithudi Allah Ngwakumva, Ngodziwa

    [228] “Ndipo akazi osiidwa (asakwatiwe) ayembekezere mpaka kuyeretsedwa kutatu kukwanire. Ndipo nkosafunika kwa iwo kubisa chimene Allah walenga m’mimba zawo, ngati akukhulupiriradi Allah ndi tsiku lachimaliziro. Ndipo amuna awo ali ndi udindo wowayenereza kuwabwerera m’nthawi imeneyi ngati akufuna kuchita chimvano. Nawonso azimayi ali ndi zofunika kuchitiridwa (ndi amuna awo) monga m’mene ziliri kwa azimayiwo kuchitira amuna awo mwachilamulo cha Shariya. Koma amuna ali ndi udindo okulirapo kuposa iwo. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa; Ngwanzeru zakuya

    [229] “Twalaq (mawu achilekaniro cha ukwati omwe akupereka mwayi kwa mwamuna kubwereranso kwa mkazi wake), ndi omwe anenedwa kawiri. Kenako amkhazike (mkaziyo) mwa ubwino (ngati afuna kubwererana naye) kapena alekane mwa ubwino (ngati atafunadi kumleka. Ndipo sangathe kubwererana naye ngati atamunenera kachitatu mawu achilekano pokhapokha atakwatiwa kaye ndi mwamuna wina ndi kusiidwa ndi mwamunayo). Ndipo sizili zololedwa kwa inu kuti mutenge (kulanda) chilichonse chimene mudawapatsa (akazi anu) pokhapokha (onse awiri) ngati akuopa kuti satha kusunga malire a Allah (malamulo a Allah). Ngati muopa kuti sasunga malire a Allah, ndiye kuti pamenepo pakhala popanda tchimo kwa iwo (mwamuna woyamba ndi mkaziyu) kulandira (kapena kupereka) chodziombolera mkazi. Awa ndiwo malire a Allah; choncho musawalumphe. Ndipo amene alumphe malire a Allah (powaswa), iwowo ndiwo anthu ochita zoipa

    [230] “Tero ngati atamuleka (ndi kunena katatu mawu achilekaniro, choncho mkazi ameneyo) ngosaloledwa kwa iye pambuyo pakutero, kufikira akwatiwe ndi mwamuna wina. (Ngati mwamuna winayo atamusiya), palibe kulakwa kwa awiriwo kubwererana ngati akuona kuti adzasunga malire a Allah. Ndipo awa ndi malire a Allah omwe akuwalongosola kwa anthu odziwa

    [231] “Ndipo pamene musiya akazi powanenera mawu achilekaniro, niiyandikira kukwana nyengo ya edda yawo (chiyembekezero chawo), abwelereni mwa ubwino; kapena lekananaoni mwa ubwino, ndipo musawabwelere mowavutitsa kuti mupyole malire a Allah (poswa malamulo ake). Ndipo amene achite zimenezo ndiye kuti wadzichitira yekha zoipa. Ndipo ndime za mawu a Allah musazichitire chibwana. Ndipo kumbukirani mtendere wa Allah umene uli pa inu; makamaka chisomo chokuvumbulutsirani buku (la Qur’an) ndi kudziwitsidwa nzeru zomwe akukulangizani nazo. Ndipo opani Allah, ndithudi dziwani kuti Allah Ngodziwa chirichonse

    [232] “Ndipo akazi mukawanenera mawu achilekaniro (oyamba ndi achiwiri), iwo nakwaniritsa chiyembekezero chawo, choncho (inu abale amkazi), musawaletse kukwatiwanso ndi amuna awo (kubwererana) ngati pali chimvano pakati pawo mwa ubwino. Zimenezo akulangizidwa nazo mwa inu yemwe akukhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro. Zimenezo nzabwino kwa inu, ndiponso zoyeretsa. Ndipo Allah akudziwa, pomwe inu simudziwa

    [233] “Ndipo akazi omwe angobereka kumene ayamwitse ana awo zaka ziwiri zathunthu kwa yemwe akufuna kukwaniritsa kuyamwitsa. Ndiudindo wa abambo kuwapezera chakudya chawo ndi chovala chawo (ana awo ndi ) amayiwo, motsatira malamulo a Shariya. Ndipo mzimu wa munthu aliyense sukakamizidwa, koma m’mene ungathere. Ndipo mayi wa mwanayo asazunzidwe chifukwa cha mwana wakeyo. Nayenso bambo wa mwanayo asazunzike chifukwa cha mwana wakeyo. Ndipo lamuloli lilinso chimodzimodzi pa mlowam’malo (ngati bambo atamwalira). Ndipo onse awiri ngati atafuna kumletsa kuyamwa, mogwirizana pakati pa awiriwo, ndi mokambirana palibe kulakwa pa iwo awiriwo. Ndipo ngati mutafuna kuwapezera ana anu akazi ena owayamwitsa (omwe si amayi awo), palibe uchimo mwa inu ngati mwapereka chimene udalonjeza kuwapatsa (oyamwitsawo) mwa ubwino. Ndipo opani Allah; dziwaninso kuti Allah akuona zonse zimene mukuchita

    [234] Ndipo mwa inu amene amwalira nasiya akazi, choncho (akaziwo) ayembekezere (asakwatiwe) miyezi inayi ndi masiku khumi. Ndipo akakwanitsa nyengo ya chiyembekezero chawo cha edda, sitchimo kwa inu pazimene akaziwo adzichitira okha (monga kudzikongoletsa ndi kudziwonetsa kwa ofunsira ukwati); motsatira malamulo a Shariya. Ndipo Allah Ngodziwa zonse zimene mukuchita

    [235] “Ndipo sitchimo kwa inu kupereka mawu okuluwika ofunsira ukwati kwa akaziwo (pamene chiyembekezero cha edda yawo chisanathe. Ndiponso palibe uchimo) kapena kubisa mu mtima mwanu, kuwakwatira (chiyembekezo chawo chikadzatha). Allah wadziwa kuti mukhala mukuwakumbukira akaziwo. Koma musawalonjeze mobisa (kuti: “Ikatha edda ndidzakukwatira).” Koma nenani mawu abwino. Ndipo musatsimikize kumanga ukwati mpaka nyengo yolembedwayo ikwanire. Ndipo dziwani kuti Allah akudziwa zomwe zili m’mitima mwanu. Tero muopeni (Allah), dziwaninso kuti Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngoleza

    [236] “Palibe tchimo pa inu mutawapatsa akazi mawu achilekaniro pomwe simudakhudzane nawo; pomwenso simudawadziwitse gawo la chiwongo chawo; koma asangalatseni (powapatsa chilekaniro). Wopeza bwino apereke malinga ndikupeza bwino kwake; wochepekedwa apereke malingana ndikuchepekedwa kwake. Chilekaniro chosangalatsacho chikhale molingana ndi malamulo a Shariya, ndipo ndilamulo kwa ochita zabwino

    [237] “Ndipo ngati mwalekana nawo (akaziwo) musanakhudzane nawo mutawadziwitsa gawo la chiwongo chawo, apatseni theka la chimene mudagwirizana kuwapatsa pokhapokha ngati akaziwo atakana okha (theka la chiwongocho), kapena (mwamuna) uja yemwe kumangitsa kwa ukwati kuli m’manja mwake amusiire (chiwongo chonsecho mkaziyo). Ndipo ngati mutasiirana (zimenezo) zingakuyandikitseni kumbali yoopa Allah. Ndipo musaiwale kuchitirana zabwino pakati panu (ngakhale kuti mukulekana). Ndithudi Allah akuona zonse zimene mukuchita

    [238] “Sungani mokwanira Swala makamaka Swala yapakatikati; ndipo imilirani modzichepetsa kwa Allah

    [239] “Ndipo ngati muli ndi mantha (kupemphera mwalamulo pamene mukumenyana ndi adani anu), pempherani uku mukuyenda, kapena mutakwera chokwera. Ndipo mukakhala pachitetezo mkumbukireni Allah (pempherani) monga momwe wakuphunzitsirani zomwe simudali kuzidziwa

    [240] “Ndipo mwa inu amene amwalira nasiya akazi awo, alangize (amlowam’malo awo, monga makolo ndi achibale) za akazi awo kuti awapatse zodyera m’nyengo ya chaka chimodzi popanda kutulutsidwa (m’nyumba zomwe ankakhala ndi amuna awo). Koma ngati akaziwo atuluka (okha), palibe kulakwa pa inu pa zimene adzichitira okha zomwe nzogwirizana ndi chilamulo cha Shariya. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa; Ngwanzeru zakuya

    [241] “Ndipo akazi osiidwa ukwati, apatsidwe chilekaniro chowasangalatsa m’chilamulo cha Shariya. Ili ndi lamulo kwa amene akuopa Allah

    [242] “Umu ndi momwe Allah akukulongosolerani ma Ayah ake (ndime zake) kuti inu mukhale ndi nzeru

    [243] “Kodi sudamve (nkhani za) amene adatuluka m’nyumba zawo ali zikwizikwi kuopa imfa? Ndipo Allah adawauza: “Mwalirani,” (ndipo adamwalira chabe popanda chifukwa chilichonse). Kenako Adawaukitsa (kuti adziwe kuti imfa njosathawika). Ndithudi, Allah Ndimwini kuchita zabwino pa anthu, koma anthu ambiri sathokoza

    [244] “Ndipo menyani nkhondo panjira ya Allah, ndipo dziwani kuti Allah Ngwakumva, Ngodziwa chilichonse

    [245] “Kodi ndani angamkongoze Allah ngongole yabwino (yochokera m’chuma chake powapatsa amphawi ndi kupereka pa njira ya Allah) kuti amuonjezere zoonjezera zambiri? Ndipo Allah ndi yemwe amafumbata ndi kutambasula, ndipo kwa Iye nkumene mudzabwezedwa

    [246] “Kodi sudamve nkhani ya akuluakulu a ana a Israyeli pambuyo pa Mûsa? Adanena kwa mneneri wawo: “Tidzozere mfumu kuti timenye nkhondo pa njira ya Allah.” Iye (mneneri wawoyo) adati: “Mwinatu simungamenye nkhondoyo ngati kutalamulidwa kwa inu. (Iwo) adati: “Nchotani kuti tisamenye nkhondo pa njira ya Allah pomwe tatulutsidwa m’nyumba zathu pamodzi ndi ana athu?” Koma pamene adalamulidwa kumenya nkhondoyo, adatembenuka, kupatula ochepa mwa iwo. Ndipo Allah akudziwa bwinobwino za anthu ochita zoipa

    [247] “Ndipo mneneri wawoyo adawauza: “Allah wakusankhirani Taluti kukhala mfumu. (Iwo ) adati: “Nchotani kuti iye akhale ndi ufumu pa ife pomwe ife ngoyenera kupeza ufumu kuposa iye, ndipo sadapatsidwe chuma chambiri?” (Iye) adati: “Ndithu Allah wamusankha pa inu, ndipo wamuonjezera kukhala ndi nzeru zopambana ndi kukhala ndi thupi (lamphamvu). Ndipo Allah amampatsa ufumu wake amene wamfuna. Ndipo Allah ndi Mwini zopereka zambiri, Ngodziwa.”

    [248] “Ndipo mneneri wawo adawauza (kuti): “Ndithu chizindikiro cha ufumu wake, ndikukudzerani bokosi lomwe mkati mwake muli mpumulo wa miyoyo yanu wochokera kwa Mbuye wanu, ndi zotsalira zomwe adazisiya anthu a Mûsa ndi anthu a Harun, atanyamula angelo. Ndithu m’zimenezo muli chisonyezo kwa inu (chosonyeza kuyenera kwa ufumu wake pa inu) ngati mulidi okhulupirira.”

    [249] “Choncho, Taluti pamene adapita ndi magulu (ake) a nkhondo, adati: “Allah akuyesani mayeso ndi mtsinje (womwe mukumane nawo panjira komwe mukupitako). Choncho amene akamwe mmenemo sali nane. Koma amene sakamwa adzakhala pamodzi nane kupatula amene watunga ndi dzanja lake (ndikumwa; iyeyo ndiye kuti sadalakwe). Koma (iwo) adamwa m’menemo kupatula ochepa mwa iwo. Choncho pamene adaoloka iye pamodzi ndi aja omwe adakhulupirira limodzi naye, (iwo) adati: “Lero sitingamuthe Jaluti ndi magulu ake a nkhondo.” Omwe adali ndi chitsimikizo chokumana ndi Allah adati: “Kodi ndimagulu angati ochepa amene adagonjetsa magulu ambiri mwa chilolezo cha Allah! Ndipo Allah Ali pamodzi ndi opirira

    [250] “Ndipo pamene adapita kukalimbana ndi Jaluti (mfumu ya adaniwo), pamodzi ndi magulu ake a nkhondo (anthu a Taluti) adati: “E Mbuye wathu! Titsanulireni chipiliro, ndipo limbikitsani mapazi athu: Tithangateni kwa anthu osakhulupirira.”

    [251] “Choncho, adawagonjetsa mwa chilolezo cha Allah. Ndipo Daud adapha Jaluti; ndipo Allah adampatsa ufumu ndi uneneri, namphunzitsanso zimene adafuna. Allah akadapanda kuwakankha anthu ena kupyolera mwa ena ndiye kuti dziko likadaonongeka. Koma Allah ndi mwini kuchita zabwino pa zolengedwa zonse

    [252] “Awa ndi ma Ayah (ndime) a Allah; tikuwawerenga kwa iwe (Mtumiki s.a.w) mwachoonadi. Ndithudi, iwe ndiwe mmodzi mwa atumiki

    [253] “۞ Amenewo ndi aneneri tidawapatsa ulemelero mosiyanitsa pakati pawo, ena kuposa ena. Mwa iwo alipo amene Allah adawalankhula; ndipo ena adawakwezera kwambiri maulemelero awo. Naye Isa (Yesu) mwana wa Mariya tidampatsa zisonyezo zooneka, ndi kumlimbikitsa ndi Mzimu Woyera (rnngelo Gabriel). Allah akadafuna skadamenyana amene adalipo pambuyo pawo, (pa atumikiwo) pambuyo powadzera zizindikiro zooneka, koma adasiyana. Choncho mwa iwo alipo amene adakhulupirira, ndipo ena mwa iwo sadakhulupirire. Ndipo Allah akadafuna, sakadamenyana; koma Allah amachita zimene akufuna

    [254] “E inu amene mwakhulupirira! Perekani mwa zimene takupatsani lisanadze tsiku lomwe lilibe kugula (chilichonse chokupulumutsani) ngakhale ubwenzi ngakhalenso dandaulo. Ndipo osakhulupirira ndiwo anthu oipa

    [255] Allah palibe wopembedzedwa wina koma Iye, Wamoyo wamuyaya, Woimira ndi Woteteza chilichonse. Kusinza sikumgwira ngakhale tulo. Zonse za kumwamba ndi za pansi nza Iye. Kodi ndani angathe kuombola kwa Iye popanda chilolezo chake? Akudziwa za patsogolo ndi zomwe zili pambuyo pawo ndipo zolengedwazo sizidziwa chilichonse pa zomwe zili m’kudziwa Kwake kupatula chimene wafuna. Mpando wake wachifumu wakwanira kumwamba ndi pansi ndipo sizimamvuta kuzisunga zimenezo. Ndipo Iye (Yekha) Njemwe ali Wapamwambamwamba, Ngwamkulu kwabasi, (Ngolemekezeka kwambiri)

    [256] “Palibe kukakamiza (munthu kulowa) m’chipembedzo; kulungama kwaonekera poyera kusiyana ndi kusalungama. Choncho amene akumkana satana nakhulupirira Allah, ndiye kuti wagwira chigwiliro cholimba, chomwe sichisweka. Ndipo Allah Ngwakumva; Ngodziwa

    [257] “Allah ndi Mtetezi wa amene akhulupirira, amawatulutsa kumdima ndikuwalowetsa mkuunika, koma amene sadakhulupirire, atetezi awo ndi asatana. Amawatulutsa m’kuunika ndi kuwalowetsa mu mdima; iwo ndi anthu a ku Moto. M’menemo adzakhalamo nthawi yaitali

    [258] “Kodi sudamve za yemwe adatsutsana ndi Ibrahim pa za Mbuye wake (Allah)? (Ankanyada) pachifukwa chakuti Allah adampatsa ufumu. Ibrahim adati: “Mbuye wanga ndi yemwe amapereka moyo ndi imfa.” Iye adati: “Inenso ndimapereka moyo ndi imfa.” Ibrahim Adati: “Ndithu Allah amatulutsa dzuwa ku vuma, choncho iwe ulitulutse ku zambwe.” Ndipo uja wosakhulupirira adangoti kakasi, (kusowa chonena). Ndipo Allah satsogolera anthu ochita zoipa

    [259] “Kapena ngati fanizo la uja amene adadutsa pafupi ndi mudzi umene madenga ndi zipupa zake zidaphwasuka (udaferatu) adati: “Kodi Allah adzaukitsa chotani mudzi uwu pambuyo pakufa kwake?” Ndipo Allah adampatsa imfa kwa nthawi yokwana zaka zana limodzi , kenako adamuukitsa namufunsa: “Kodi wakhala nyengo yaitali bwanji?” Adati: “Ndakhala nthawi yatsiku limodzi, kapena theka latsiku.” (Allah) adati: “Korna wakhala zaka zana limodzi, ndipo ona chakudya chako ndi zakumwa zako, sizinaonongeke (sizinavunde). Ndipo yang’ana bulu wako (ali mafupa okhaokha oyoyoka); ndi kuti ukhale chisonyezo kwa anthu, (nchifukwa chake takuukitsa ku imfa). Ndipo yang’ana mafupa (a bulu wako) momwe tingawaukitsire, kenako nkumaaveka minofu.” Choncho pamene zidazindikirika (kwa iye, woukitsidwayo), adati: “Ndikudziwa kuti Allah Ngokhoza chilichonse.”

    [260] “Ndipo (kumbukira) pamene Ibrahim adati: “E Mbuye wanga!, Ndionetseni mmene mudzaaukitsire akufa.” (Allah) adati: “Kodi sunakhulupirirebe?” Adati: “Iyayi, (ndikukhulupirira), koma (ndikufuna kuona zimenezo) kuti mtima wanga ukhazikike.” (Allah) adati: “Choncho katenge mbalame zinayi; uzisonkhanitse kwa iwe (mpaka uyizindikire mbalame iliyonse mmene ilili, ndipo kenako uziduledule zonsezo zidutswazidutswa ndikuzisakaniza ndi kuzigawa mzigawo zinayi). Ndipo paphiri lililonse ukaikepo gawo limodzi la zimenezo, ndipo kenako uziitane. Zikudzera zikuthamanga. Ndipo dziwa kuti Allah ndi Mwini mphamvu zoposa, Ngwanzem zakuya.”

    [261] “Fanizo la amene akupereka chuma chawo pa njira ya Allah lili ngati fanizo la njere imodzi yomwe yatulutsa ngala zisanu ndi ziwiri. Ndipo ngala iliyonse nkukhalamo njere zana limodzi. Ndipo Allah amamuonjezera amene wamfuna (kuposera pamenepa). Ndipo Allah alinazo zambiri, Ngodziwa

    [262] “(Anthu) amene akupereka chuma chawo pa njira ya Allah napanda kutsatiza pa zomwe aperekazo kukumba, ndiponso masautso, iwo ali ndi mphoto kwa Mbuye wawo ndipo pa iwo sipadzakhala mantha; ndiponso sadzadandaula

    [263] “Mawu abwino, ndi kukhululukira (amene wakulakwira) nzabwino zedi kuposa sadaka yotsatizidwa ndi masautso. Ndipo Allah ndiyemwe ali Wolemera kwambiri ndiponso Woleza (kwa zolengedwa Zake)

    [264] “E inu amene mwakhulupirira! Musaononge sadaka zanu pokumba ndiponso popereka masautso, monga yemwe akupereka chuma chake modzionetsera kwa anthu, ndipo sakhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro. Choncho fanizo lake lili ngati thanthwe lomwe pamwamba pake pali dothi. Kenako nkulifikira chimvula (nkuchotsa dothi lonse lija), nkulisiya lopanda kanthu. Tero sadzatha kupeza chilichonse pazimene adachita. Ndipo Allah satsogolera anthu osakhulupirira

    [265] “Ndipo fanizo la anthu amene akupereka chuma chawo chifukwa chofuna chiyanjo cha Allah ndi kulimbikitsa mitima yawo (pa chipembedzo cha Allah) lili ngati fanizo la munda umene uli pachitunda, chiufikira chimvula tero nubweretsa zinthu zake dzochuluka moonjeza kawiri (kuposera pachikhalidwe chake). Ndipo ngati chimvula sichidaudzere, ndiye kuti yamawawa (nkuukwanira mundawo). Ndipo Allah akuona zonse zimene mukuchita

    [266] “Kodi mmodzi wa inu angakonde kukhala ndi munda wa mitengo ya kanjedza ndi mphesa womwe pansi pake mitsinje ikuyenda, iye mmenemo napeza dzinthu dzamitundumitundu, numpeza ukalamba uku ali ndi ana ofooka; ndipo kamvuluvulu wa moto naugwera (mundawo), nupseleratu (angazikonde zimenezi)? Umo ndimomwe Allah akukulongosolerani ma Ayah (ndime za mawu Ake) kuti muganizire

    [267] “E inu amene mwakhulupirira! Perekani zabwino zochokera m’zimene mwapeza ndi zimene takutulutsirani m’nthaka, ndipo musalinge kupereka choipa chomwe inu simukadachilandira (ngati akanakupatsani) pokhapokha mochitsinzinira. (Nanga Allah ndiye alandire choipacho)? Ndipo dziwani kuti Allah Ngolemera (ndiponso) Ngotamandidwa

    [268] “Satana amakuopsezani ndi umphawi ndi kukulamulirani kuchita zoipa (monga umbombo), pomwe Allah akukulonjezani chikhululuko kuchokera kwa Iye ndi ubwino (waukulu ngati mupereka); ndipo Allah ali nazo zambiri, Ngodziwa

    [269] “Amapatsa nzeru (zothandiza) amene wamfuna; ndipo amene wapatsidwa nzeru, ndithudi, wapatsidwa zabwino zambiri. Ndipo (zoterezi) sakumbukira koma eni nzeru okha

    [270] “Ndipo chilichonse chomwe mungapereke kapena naziri (lonjezo) iliyonse yomwe mwalonjeza Allah, ndithudi, Allah akudziwa zonsezi. Ndipo anthu ochita zoipa sadzakhala ndi athandizi

    [271] “Ngati mupereka sadaka moonetsera, ndibwino; ngati mungaipereke mobisa, ndikuipereka kwa osauka, umenewo ndiubwino woposa kwa inu. Ndipo akufafanizirani zoipa zanu (ngati mutero). Ndipo Allah akudziwa zonse zimene mukuchita

    [272] “Siudindo wako kuwaongola, koma Allah amamuongola amene wamfuna, (udindo wako nkulalikira kokha). Ndipo chuma chilichonse chimene mungachipereke, (phindu lake) lili pa inu eni, ndipo musapereke pokhapokha pofunafuna chikondi cha Allah. Ndipo chuma chilichonse chimene mungachipereke adzakubwezerani mokwanira (mphoto yake), ndipo simudzaponderezedwa

    [273] “(Sadakazo ziperekedwe) kwa amphawi amene atsekerezedwa pa njira ya Allah, amene sangathe kuyenda pa dziko (kukachita ntchito yopezera zofunika pamoyo wawo). Amene sadziwa za chikhalidwe chawo, amawaganizira kuti ngolemera chifukwa chakudziletsa kwawo (kupemphapempha). Ungawazindikire (kuti ngosowedwa) ndi zizindikiro zawo. Sapempha anthu mwaliuma. Ndipo chabwino chilichonse chimene mukupereka, ndithudi, Allah ali Wodziwa za icho

    [274] “Amene akupereka chuma chawo usiku ndi usana, mobisa ndi moonekera, ali ndi malipiro awo kwa Mbuye wawo; ndipo pa iwo sipadzakhala mantha, ndiponso sadzadandaula

    [275] “Amene akudya riba (chuma cha katapira) sadzauka (m’manda) koma monga momwe amaimira munthu okhudzidwa ndi ziwanda, mwamisala. (Ndipo) izi nchifukwa chakuti amanena: “Malonda ngolingana ndi katapira,” pomwe Allah waloleza malonda ndipo waletsa katapira. Ndipo amene wamufika ulaliki wochokera kwa Mbuye wake (woletsa katapira) nasiya, choncho chomwe chidapita nchake. Ndipo chiweruzo chake chili kwa Allah (akaona chochita naye). Koma amene abwerera (kuchita malonda a katapira), amenewo ndiwo anthu a ku Moto, mmenemo adzakhalamo nthawi yaitali

    [276] “Allah amachotsa madalitso pa (chuma cha) katapira ndipo amaika madalitso pa chaulere. Ndipo Allah sakonda aliyense wosakhulupirira, wamachimo ambiri

    [277] “Ndithudi, amene akhulupirira, nachita zabwino, napemphera Swala moyenera ndi kupereka chopereka (Zakaat), iwo akapeza malipiro awo kwa Mbuye wawo. Ndipo pa iwo sipadzakhala mantha ndiponso sadzadandaula

    [278] “E inu amene mwakhulupirira! Opani Allah, ndipo siyani zimene zatsalira m’katapira, ngati inu mulidi okhulupirira

    [279] “Ngati simuchita (zimenezo), dziwani kuti mukulimbana ndi Allah ndi Mtumiki Wake. Ndipo ngati mulapa, maziko a chuma chanu ndi anu. Musapondereze, ndiponso musaponderezedwe

    [280] “Ndipo ngati wokongola ali ndi mavuto, choncho (wokongoza) amdikire mpaka apeze bwino. Koma ngati inu (okongoza mungakhululuke pakusiya kuitanitsa ngongole) muisintha kuti ikhale sadaka, ndibwino kwa inu ngati mukudziwa (zimenezo)

    [281] “Ndipo liopeni tsiku lomwe inu mudzabwezedwa kwa Allah. Ndipo kenako munthu aliyense adzalipidwa mokwanira pa zonse zimene adachita (ndi manja ake), ndipo iwo sadzaponderezedwa

    [282] “E inu amene mwakhulupirira! Mukamakongozana ngongole kwa nyengo yodziwika ilembeni. Ndipo mlembi pakati panu alembe mwachilungamo; ndipo mlembi asakane kulemba monga momwe Allah wamphunzitsira; choncho alembe. Ndipo alakatule (mawu olembedwawo ndi wokongolayo) yemwe ngongole ili pa iye. Nayenso aope Allah, Mbuye wake, ndipo asapungule chilichonse m’menemo (m’ngongole). Ndipo ngati wokongola ndiozelezeka kapena wofooka, kapena iye mwini sangathe kulembetsa (momveka), choncho amulembetsere myang’aniri (wakili) wake (yemwe akuyang’anira zinthu zake) mwachilungamo. Ndipo funiraponi mboni ziwiri zochokera mwa anthu anu aamuna (asilamu). Koma ngati amuna awiri palibe, choncho apezeke mwamuna mmodzi ndi akazi awiri (kuti aikire umboniwo), amene mumavomereza kukhala mboni kuti ngati mmodzi mwa iwo (akazi awiriwo) angaiwale mmodzi wawo akumbutse winayo. Ndipo mboni zisakane zikaitanidwa. Ndiponso musanyozere kulemba (ngongoleyo) yaing’ono kapena yaikulu mpaka nyengo yake. Zimenezo (kulembako) ndibwino kwa Allah, ndipo ncholungama zedi kumbali yaumboni, ndiponso nchothandiza kuti musakhale ndi chipeneko. Koma akakhala malonda omwe ali pompo omwe mukupatsana pakati panu (tsintho) sikulakwa kwa inu kusawalemba. Koma funani mboni pamene mukugulitsana. Komatu asavutitsidwe mlembi ndiponso mboni. Ngati mutachita zimenezo (zoletsedwazo) kumeneko ndiko kutuluka (m’chilamulo cha Mulungu wanu), ndipo opani Allah, Allah akukuphunzitsani. Ndipo Allah Ngodziwa chilichonse

    [283] “Ndipo ngati muli pa ulendo, ndipo simudapeze mlembi, choncho (wokongoza) apatsidwe chikole (pinyolo) m’manja mwake. Ngati wina wasungitsa mmodzi wa inu chinthu (pomudalira wokhulupirika) choncho amene wayesedwa wokhulupirikayo abweze chinthucho kwa mwini wake, ndipo aope Allah, Mbuye wake. Ndipo musabise umboni (ngakhale uli wokuipirani). Ndipo amene abise ndiye kuti mu mtima mwake mwalowa uchimo; ndipo Allah akudziwa zonse zimene mukuchita

    [284] “Zonse zakumwamba ndi zapansi nza Allah. Kaya muonetsera poyera zomwe zili m’mitima mwanu kapena kuzibisa, Allah adzakuchitirani nazo chiwerengero. Kenako adzakhululukira amene wamfuna (atalapa). Ndipo adzamlanga amene wamfuna (akapanda kulapa). Ndipo Allah Ngokhoza chilichonse

    [285] “Mtumiki wakhulupirira zimene zavumbulutsidwa kwa iye kuchokera kwa Mbuye wake. Naonso asilamu (akhulupirira). Onse akhulupirira Allah, angelo Ake, mabuku Ake ndi atumiki Ake. (Iwo pamodzi ndi Mtumiki wawoyo akunena kuti): “Sitingalekanitse aliyense pakati pa atumiki Ake, (onse tikuwakhulupirira).” Ndipo akunena: “Tamva ndiponso tamvera, (choncho tikukupemphani) chikhululuko chanu. E Mbuye wathu! Ndipo kwa Inu nkobwerera.”

    [286] “Allah sakakamiza mzimu uliwonse koma chimene chili cholingana ndi kukhoza kwake. (Ndipo phindu la) zimene mzimuwo udapeza ndilake ndiponso kuluza kwa zomwe udapeza nkwake. (Asilamuwo amanena) “E Mbuye wathu! Musatilange tikaiwala kapena tikalakwitsa, E Mbuye wathu! Musatisenzetse mtolo (wamalamulo) monga munawasenzetsera amene adalipo patsogolo pathu. E Mbuye wathu! Musatisenzetse chimene sitingachithe. Tifafanizireni machimo athu, tikhululukireni zolakwa zathu, ndiponso tichitireni chifundo. Inu Ndinu Mtetezi wathu. Choncho tithangateni ku anthu osakhulupirira.”

    Banja la Imran

    Surah 3

    [1] “Alif-Lâm-Mîm

    [2] “Allah (ndimmodzi), palibe winanso wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye Yekha, Wamoyo wamuyaya, Woimira ndi kuteteza chilichonse

    [3] “Wakuvumbulutsira buku mwachoonadi, lomwe likutsimikizira zomwe zidalipo patsogolo pake. Ndipo adavumbulutsa Taurat ndi Injil

    [4] “Kale, kuti (mabukuwo) akhale chotsogolera anthu. Ndipo adavumbulutsa (Qur’an) yolekanitsa pakati pa choonadi ndi chonama * Ndithudi, aja amene sadakhulupirire zizindikiro za Allah, adzakhala ndi chilango chaukali. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa, Wobwezera (chilango mwaukali)

    [5] “Ndithudi, kwa Allah sikungabisike chilichonse cha pansi ngakhale cha kumwamba

    [6] “Iye ndi Yemwe amakulinganizani muli m’mimba mmaonekedwe anu mmene akufunira. Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye; Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya

    [7] “Iye ndi Yemwe wakuvumbulutsira buku (ili la Qur’an), lomwe mkati mwake muli ndime zomveka zomwe ndimaziko a bukuli. Ndipo zilipo zina zokuluwika. Koma amene m’mitima mwawo muli kusokera, akutsata zomwe zili zokuluwika ndi cholinga chofuna kusokoneza anthu, ndi kufuna kudziwa tanthauzo lake lenileni. Palibe amene akudziwa tanthauzo lake lenileni koma Allah basi. Koma amene azama pa maphunziro, amanena: “Tawakhulupirira (ma Ayah amenewa). Onse ngochokera kwa Mbuye wathu.” Ndipo palibe angakumbukire koma eni nzeru basi

    [8] “(Anzeruwo amanena): “ E Mbuye wathu! Musaikhotetse mitima yathu pambuyo potiongola. Tipatseni chifundo chochokera kwa Inu. Ndithudi, Inu Ndinu wopatsa kwambiri

    [9] “E Mbuye wathu! Inu ndinu Wosonkhanitsa anthu patsiku lopanda chikaiko, ndithudi, Allah saswa lonjezo

    [10] “Ndithu amene sadakhulupirire, chuma chawo sichidzawathandiza chilichonse ngakhalenso ana awo, ku chilango cha Allah. Ndipo iwo ndi nkhuni za ku Moto

    [11] “(Khalidwe la awa osakhulupiira, amumbadwo wako iwe mneneri Muhammad {s.a.w}, liri) ngati khalidwe la anthu a Farawo ndi amene adalipo pambuyo pawo. (Iwo) adatsutsa zisonyezo Zathu. Choncho, Allah adawakhaulitsa chifukwa cha machimo awo. Ndipo Allah Ngolanga mwaukali

    [12] “Auze amene sadakhulupirire: “Posachedwapa mugonjetsedwa ndi kusonkhanitsidwa ndi kuponyedwa ku Moto. Taonani kuipa kwa malo wokakhazikikamo!”

    [13] ““Ndithudi, padapezeka chisonyezo chachikulu kwa inu m’magulu awiri omwe adakumana (tsiku la nkhondo ya Badri), pomwe gulu limodzi limamenya (nkhondo) pa njira ya Allah, pamene linalo lokanira, (ndipo gululo) linkawaona (Asilamu) kukhala ochuluka kawiri kuposa ilo, poona ndi maso awo. Ndipo Allah amamlimbikitsira mphamvu ndi chipulumutso chake amene wamfuna. Ndithudi, m’zimenezo muli malingaliro (akulu) kwa eni kupenyetsetsa mwanzeru.”

    [14] “Kwakometsedwa kwa anthu kukonda zilakolako (za moyo wawo) monga akazi, ana, milumilu ya chuma cha golide ndi siliva, ndi mahachi oyang’aniridwa bwino, ziweto ndi mbewu. Izo ndi zosangalatsa za moyo wa dziko lapansi (zomwe sizili kanthu). Koma kwa Allah ndiko kuli mabwelero abwino

    [15] “Nena: “Kodi ndikuuzeni zomwe zili zabwino kuposa zimenezo? Kwa omwe ali olungama, akapeza kwa Mbuye wawo Minda yomwe pansi pake (ndi patsogolo pake) mitsinje ikuyenda; adzakhala mmenemo nthawi yaitali ndikulandira akazi oyeretsedwa ndi chiyanjo chochokera kwa Allah. Ndipo Allah akuona akapolo ake onse

    [16] “Omwe akunena: “Mbuye wathu! Ndithudi, ife takhulupirira. Choncho tikhululukireni machimo athu ndi kutipewetsa ku chilango cha Moto.”

    [17] “Opirira, onena zoona, omvera, opereka chaulere ndi opempha chikhululuko nthawi yam‘bandakucha

    [18] “Allah (Mwini) akuikira umboni kuti: “Palibe wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye basi.” Ndipo akuikiranso umboni (zomwezi) angelo ndi eni nzeru (kuti Iye) Ngokhazikitsa chilungamo. Palibe wina wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye. Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya

    [19] “Ndithudi, chipembedzo (choona) kwa Allah ndi Chisilamu. Ndipo amene adapatsidwa buku (Ayuda ndi Akhrisitu) sadatsutsane koma pambuyo powabwerera kuzindikira. (Adatsutsana) chifukwa cha dumbo lomwe lidali pakati pawo. Ndipo amene akukana zisonyezo za Allah, (Allah akamulanga pa tsiku la chiweruziro). Ndithu Allah Ngwachangu powerengera

    [20] “Ngati (osakhulupirira) atsutsana nawe, nena: “Ndayang’anitsa nkhope yanga kwa Allah (ndadzipereka kwa Iye) pamodzi ndi amene anditsata.” Ndipo nena kwa onse adapatsidwa buku (Ayuda Ndi Akhrisitu) ndi osadziwa kulemba ndi kuwerenga (Arabu): “Kodi mwagonjera (kwa Allah)?” Ngati agonjera ndiye kuti aongoka. Koma ngati atembenukira kumbali, udindo wako ndikufikitsa uthenga basi. Ndipo Allah akuona akapolo Ake onse

    [21] “Ndithudi, amene akutsutsa zizindikiro za Allah ndi kupha aneneri popanda choonadi, ndikuphanso anthu omwe akulamula (kuchita) zolungama, auze nkhani ya chilango chopweteka

    [22] “Iwowo ndi omwe zochita zawo zaonongeka pa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro. Ndipo iwo sadzapeza athandizi

    [23] “Kodi sukuwaona omwe apatsidwa gawo la buku (la Allah)? Akuitanidwa ku buku la Allah kuti liwaweruze pakati pawo; kenako gulu lina la iwo likutembenukira kumbali iwo ali onyoza

    [24] “Zimenezo (kusalabadira malamulo a Allah) nchifukwa chakuti amanena: “Sudzatikhudza Moto koma masiku ochepa basi.” Ndipo zawanyenga pa chipembedzo chawo zomwe adali kupeka (kuti adzakhululukidwa kapena kulangidwa masiku ochepa okha)

    [25] “Kodi zidzakhala zotani pamene tidzawasonkhanitsa tsiku lopanda chikaiko? Ndipo mzimu uliwonse udzalipidwa mokwanira pa zomwe udachita. Ndipo iwo sadzaponderezedwa

    [26] “Nena “E Mbuye wanga! Mwini ufumu wonse. Mumapereka ufumu kwa yemwe mwamfuna. Ndipo mumachotsa ufumu kwa yemwe mwamfuna. Mumapereka ulemelero kwa yemwe mwamfuna, ndipo mumamsambula yemwenso mwamfuna. Ubwino wonse uli m’manja Mwanu. Ndithudi, Inu ndinu Wokhonza chilichonse.”

    [27] “(Inu) mumalowetsa usiku mu usana (ndikukhala usana wautali monga m’nyengo yotentha). Ndipo mumalowetsa usana mu usiku (nkukhala usiku wautali monga m’nyengo yachisanu). Mumatulutsa cha moyo m’chakufa; ndipo mumatulutsa chakufa m’chamoyo. Ndipo mumapatsa rizq (chakudya) amene mwamfuna mopanda chiwerengero.”

    [28] “Asilamu asapale ubwenzi osakhulupirira kusiya Asilamu anzawo. Amene achite zimenezo, sadzakhala ndi chilichonse pachipembedzo cha Allah, kupatula (kupalana nawo ubwenzi mwachiphamaso) chifukwa cha kudzitchinjiriza kwa iwo. Ndipo Allah Iye Mwini akukuchenjezani (za chilango Chake). Ndipo kobwerera ndi kwa Allah (basi)

    [29] “Nena: “Ngati mubisa zomwe zili m’zifuwa zanu, kapena kuzionetsa (poyera), Allah akuzidziwa. Iye akudziwa zonse zakumwamba ndi zapansi. Ndipo Allah Ngokhoza chilichonse.”

    [30] “Tsiku lomwe mzimu uliwonse udzapeza zabwino zomwe udachita zitabweretsedwa, ndiponso zoipa zomwe udachita; udzalakalaka kuti pakadakhala ntunda wautali pakati pa machimo ake ndi iye. Ndipo Allah Mwini akukuchenjezani za chilango Chake. Ndipo Allah Ngoleza kwa akapolo Ake

    [31] “Nena: (Iwe Mtumiki) “Ngati inu mukumkonda Allah, tsatani ine; Allah akukondani ndikukukhululukirani machimo anu. Ndipo Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha.”

    [32] “Nena: “Mvereni Allah ndi Mtumiki (wake).” Koma ngati akana, (Allah awakhaulitsa). Ndithudi, Allah sakonda anthu osakhulupirira

    [33] “Ndithudi Allah adasankha Adam ndi Nuh ndi banja la Ibrahim ndi banja la Imran pa zolengedwa zonse

    [34] “Ana ena kuchokera mwa ena pakati pawo. Ndipo Allah Ngwakumva, Ngodziwa

    [35] “(Kumbukirani) pamene adanena mkazi wa Imran (mayi wa Mariya), m’mapemphero ake): “Mbuye wanga! Ndapereka kwa Inu chimene chili m’mimba mwanga monga “waqf” (wotumikira m’kachisi Wanu). Tero landirani ichi kwa ine. Ndithudi, Inu ndinu Akumva, Wodziwa.”

    [36] “Choncho pamene adam’bala adati: “Mbuye wanga! Ndabala wamkazi!” Ndipo Allah akudziwa kwambiri chimene wabereka - “Ndipo wamwamuna (yemwe ndimayembekezera kubala) sali ngati wamkazi (amene ndamubala. Sangathe kutumikira moyenera mkachisi Wanu). Ndipo ine ndamutcha Mariya (wotumikira Allah). Ndipo ndikupempha Chitetezo Chanu pa iye ndi ana ake kwa satana wothamangitsidwayo.”

    [37] “Choncho Mbuye wake adamulandira, kulandira kwabwino; namkulitsa, kukulitsa kwabwino. Adampatsa Zakariya kuti amulere. Nthawi iliyonse Zakariya akamulowera mchipinda mwake (mwa Mariya) m’kachisimo, amampeza ali ndi chakudya. Amati: “Iwe Mariya! Ukuzipeza kuti izi?” (Iye) amati: “Izi zikuchokera kwa Allah. Ndipo Allah amampatsa yemwe wamfuna popanda chiyembekezo (mwini wakeyo).”

    [38] “Pompo Zakariya adapempha Mbuye wake nati: “Mbuye wanga! Ndipatseni kuchokera kwa Inu mwana wabwino. Ndithudi, Inu ndinu Akumva pempho!”

    [39] “Mwadzidzidzi, mngelo adamuitana uku iye ataimilira akupemphera mchipinda cha m’kachisi: “Allah akukuuza nkhani yabwino (yakuti ubereka mwana; dzina lake) Yahya yemwe adzakhala wotsimikizira (mneneri yemwe adzabadwa) ndi liwu lochokera kwa Allah, (yemwe ndi mneneri Isa (Yesu) amene adzakhalanso wolemekezeka ndi wolungama ndi mneneri wa mwa anthu abwino.”

    [40] “(Zakariya) adati: “Mbuye wanga! Ndidzakhala bwanji ndi mwana pomwe ukalamba wandifikira, nayenso mkazi wanga ndichumba.” (Mngelo adati): “Ndimomwemo; Allah amachita chimene wafuna.”

    [41] “(Iye) adati: “Mbuye wanga! Ndipatseni chizindikiro!” Adati: “Chizindikiro chako ndikuti sudzatha kuyankhula ndi anthu mpaka masiku atatu koma momangolozera (ndi chala) basi. Ndipo tamanda Mbuye wako, kutamanda kwambiri ndiponso umlemekeze (popemphera) madzulo ndi m’mawa.”

    [42] “Ndipo (kumbukira) pamene angelo adati: “E Iwe Mariya! Ndithudi, Allah wakusankha, wakuyeretsa ndipo wakulemekeza, mwa akazi onse amitundu ya anthu.”

    [43] ““E iwe Mariya, dzichepetse kwa Mbuye wako ndi kumlambira powerama pamodzi ndi owerama.”

    [44] “Izi ndizina mwa nkhani zobisika zomwe tikukuvumbulutsira. Sudali nawo pamene amaponya zolembera zawo (m’madzi m’njira ya mayere) kuti aone ndani mwa iwo alere Mariya. Komanso sudali nawo pamene adali kutsutsana

    [45] “(Kumbukira) pamene angelo adati: “E iwe Mariya! Ndithu Allah akukuuza nkhani yabwino (kuti ubereka mwana popanda mwamuna koma kupyolera mu) liwu lochokera kwa Iye (Allah, lakuti: “Bereka,” ndipo nkubereka popanda kupezana ndi mwamuna). Dzina lake ndi Mesiya Isa (Yesu) mwana wa Mariya, adzakhala wolemekezeka pa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro; ndiponso ndi mmodzi wa oyandikitsidwa kwa Allah

    [46] “Iye adzayankhula ndi anthu ali mchikuta ndi kuukulu (wake). Ndipo adzakhala mmodzi wa anthu abwino.”

    [47] “(Mariya) adati: “Mbuye wanga! Ndingakhale ndi mwana bwanji pomwe sadandikhudze munthu aliyense (wamwamuna)?” (Mngelo) adati: “Ndi momwemo. Allah amalenga chimene wafuna. Akafuna chinthu amanena kwa icho: ‘Chitika,’ ndipo chimachitikadi.”

    [48] ““Ndipo Allah adzamphunzitsa kulemba, nzeru, Taurat ndi Injili.”

    [49] ““Ndipo (adzamchita kukhala) mneneri kwa ana a Israyeli (adzakhala akuwauza kuti): “Ine ndakudzerani ndi zizindikiro kuchokera kwa Mbuye wanu kuti ndikuumbireni dongo ngati chithunzi chambalame, nkuuzira m’menemo nkukhaladi mbalame mwa chilolezo cha Allah. Ndipo ndichiritsa osapenya chibadwire, ndiwamaangamaanga (chinawa), ndi kuukitsa akufa mwa chilolezo cha Allah. Ndipo ndikuuzani zomwe mudye ndi zimene musunge m’nyumba zanu. Ndithudi, m’zimenezi muli zizindikiro kwa inu ngati mulidi okhulupirira.”

    [50] ““Ndipo (ndikhala) wotsimikizira zomwe zidalipo patsogolo panga (rn’buku la) Taurat. Ndipo ndadza kuti ndikulolezeni zina mwa zomwe zidaletsedwa kwa inu. Ndipo ndakudzerani ndi zizindikiro kuchokera kwa Mbuye wanu (zotsimikizira uthenga wanga). Choncho, opani Allah ndi kundimvera (ine).”

    [51] ““Ndithu Allah ndiye Mbuye wanga ndiponso Mbuye wanu; choncho mupembedzeni. Iyi ndiyo njira yoongoka.”

    [52] “Koma pamene Isa (Yesu) adazindikira mwa iwo kusakhulupirira adati: “Ndani akhale athandizi anga kwa Allah (popitiriza kufalitsa Chipembedzo Chake)?” Ophunzira ake adati: “Ife ndife athandizi a Allah (pofalitsa Chipembedzo Chake). Takhulupirira Allah; ndipo ikira umboni kuti ife ndithu ndi odzipereka kwa Allah (Asilamu).”

    [53] ““Mbuye wathu! Tazikhulupirira zimene mwavumbulutsa, ndipo tamtsata Mtumikiyo. Choncho tilembeni pamodzi ndi oikira umboniwo.”

    [54] “Ndipo (Ayuda) adakonza chiwembu (chofuna kupha Isa (Yesu), koma Allah adachiwononga chiwembu chawocho. Allah Ngokhoza bwino zedi poononga ziwembu za anthu a chiwembu

    [55] “(Kumbukirani) pamene Allah adati: “Iwe Isa (Yesu)! Ine ndikukwaniritsira nyengo yako yokhala ndi moyo (Ayuda sachita kanthu kwa iwe). Ndipo ndikunyamulira kwa Ine ndiponso ndikuyeretsa kwa anthu osakhulupirira (omwe ndi adani ako). Ndipo amene akutsata (iwe) ndiwasankha kukhala apamwamba pa amene sadakhulupirire kufikira tsiku lachimaliziro. Kenako kobwerera kwanu nkwa Ine, ndipo ndidzaweruza pakati panu pa zomwe mudali kusiyana

    [56] “Tsono amene sadakhulupirire, ndiwakhaulitsa ndi chilango chaukali pa dziko lapansi ndi tsiku lachimaliziro, ndipo sadzapeza athandizi

    [57] “Koma amene akhulupirira nachita zabwino, (Allah) adzawalipira malipiro awo (mokwanira). Ndipo Allah sakonda anthu ochita zoipa

    [58] “Izi tikukuwerengera iwezi ndi zivumbulutso ndi ulaliki waluntha

    [59] “Ndithudi, fanizo la Isa (Yesu) kwa Allah lili ngati fanizo la Adam; adamulenga ndi dothi namuuza kuti: “Khala munthu.” Ndipo adakhaladi

    [60] “(Ichi ndi) choona chochokera kwa Mbuye wako; choncho usakhale mwa okaikira

    [61] “Tsopano amene akutsutsana nawe (iwe Mtumiki s.a.w) pa ichi pambuyo pokudzera kuzindikira, auze: “Bwerani tiitane ana athu ndi ana anu, akazi athu ndi akazi anu, ife ndi inu; kenako modzichepetsa tipemphe tembelero la Allah kuti likhale pa amene ali abodza (mwa ife).”

    [62] “Ndithu iyi ndinkhani yoona; ndipo palibe woyenera kupembedzedwa mwa choonadi koma Allah. Ndithudi, Iye Allah Ngwamphamvu Zoposa, Ngwanzeru Zakuya

    [63] “Ngati atembenuka (monyoza, Allah awalanga); ndithudi Allah Ngodziwa za oononga

    [64] “Nena: “Inu eni buku (la Allah, Ayuda ndi Akhrisitu!) Idzani ku liwu lolingana pakati pathu ndi inu (lakuti) tisapembedze aliyense koma Allah (Mmodzi Yekha), ndiponso tisamphatikize ndi chilichonse ndipo ena mwa ife asawasandutse anzawo kukhala milungu m’malo mwa Allah.” Ngati atembenuka ndi kunyoza, nenani: “Ikirani umboni kuti ife ndife Asilamu (ogonjera malamulo a Allah).”

    [65] “E inu amene mwapatsidwa buku! Bwanji mukutsutsana za Ibrahim pomwe Taurat ndi Injili sizidavumbulutsidwe koma pambuyo pake. Kodi simuzindikira

    [66] “Taonani! Inu mudatsutsana pa zomwe mudazidziwa, nanga bwanji mukutsutsana pa zomwe simuzidziwa? Allah ndi Yemwe akudziwa. Pomwe inu simudziwa

    [67] “Ibrahim sadali Myuda ndipo sadali Mkhrisitu, koma adali wolungama Msilamu (wodzipereka); ndipo sadali mwa ophatikiza (Allah ndi zinthu zina)

    [68] “Ndithu anthu omwe ali oyenera kudzilumikiza ndi Ibrahim ndi amene adamutsata (m’nyengo yake) ndi Mtumiki uyu (Muhammad {s.a.w}) ndi amene amkhulupirira (Mtumikiyu). Ndipo Allah ndi Mtetezi wa okhulupirira

    [69] “Gulu lina la anthu amene adapatsidwa buku likufuna kukusokeretsani; ndipo sasokeretsa aliyense koma iwo wokha, pomwe (iwo eni) sakuzindikira

    [70] “E inu amene mwapatsidwa buku! Bwanji mukuzikana zizindikiro za Allah (Qur’an) pomwe mukudziwa

    [71] “E inu amene mwapatsidwa buku! Bwanji mukusakaniza choona ndi chabodza, ndipo mukubisa choona uku mukudziwa

    [72] “Ndipo gulu lina la amene adapatsidwa buku lidati (kwa anzawo): “Khulupirirani chomwe chavumbulutsidwa kwa Asilamu kumayambiliro kwa usana, ndipo chikaneni kumalekezero kwake (kwa usana) mwina angabwelere (kusiya Chisilamu)

    [73] “Ndipo musakhulupirire aliyense kupatula yekhayo yemwe watsata chipembedzo chanu. (Allah adauza Mtumiki {s.a.w}), nena: “Ndithudi, chiongoko chenicheni ndi chiongoko cha Allah basi.” (Amene adapatsidwa buku Adanena kwa anzawo: “Musakhulupirire) kuti angapatsidwe aliyense zofanana ndi zomwe mwapatsidwa inu (Ayuda ndi Akhrisitu), kapena kuti angakutsutseni kwa Mbuye wanu.” (Allah adati kwa mtumiki{s.a.w}), nena: “Ndithu zabwino zonse zili m’manja mwa Allah; amazipereka kwa yemwe wamfuna. Allah ndi Mataya, Ngodziwa.”

    [74] “Amamsankhira chifundo Chake amene wamfuna. Ndipo Allah ndi Mwini ubwino wawukulu

    [75] “Ndipo mwa iwo muli anthu ena oti ukawasungitsa milumilu ya chuma, akubwezera. Ndipo mwa iwo muli ena oti ukawasungitsa “dinar” (ndalama imodzi) sangakubwezere pokhapokha upitirize kwa iye kuimilira (kulonjelera). Izi nchifukwa chakuti amanena: “Palibe njira pa ife (yotidzudzulira) chifukwa chozibera mbulizi.” Koma akumnamizira Allah uku iwo akudziwa

    [76] “Sichoncho (monga momwe akunenera)! Koma amene akukwaniritsa lonjezo lake napewa machimo (ndiyemwe ayenera kukhala wokondedwa kwa Allah). Ndithudi, Allah amakonda opewa machimo

    [77] “Ndithu anthu amene akusinthanitsa chipangano cha Allah ndi malumbiliro awo, (ndi zinthu za) mtengo wochepa, iwo alibe gawo labwino pa tsiku lachimaliziro. Ndipo Allah sadzawayankhula (ndi mawu abwino); ndipo sadzawayang’ana (ndi diso la chifundo) pa tsiku lachimaliziro. Ndiponso sadzawayeretsa (kumachimo awo); ndipo iwo adzapeza chilango chopweteka

    [78] “Ndipo ndithu mwa iwo muli gulu lomwe likukhotetsa malirime awo (powerenga) buku kuti muwaganizire (mawu awowo) kuti ndi a m’buku la Allah); pomwe si a m’buku (la Allah). Ndipo akunena: “Izi zachokera kwa Allah.” Pomwe zimenezo sizinachokere kwa Allah; ndipo akumnamizira Allah uku akudziwa

    [79] “Sikoyenera kwa munthu yemwe Allah wampatsa buku ndi chiweruzo ndi uneneri, kenako nanena kwa anthu: “Khalani opembedza ine, mmalo mwa Allah.” Koma (awauze): “Khalani opembedza Allah, anzeru, aluntha chifukwa choti mukuphunzitsa buku ndi chifukwanso cha zomwe mukaphunzira.”

    [80] “Ndipo sangakulamulireni kuwasandutsa angelo ndi aneneri kukhala milungu. Kodi angakulamulireni kusakhulupirira pambuyo poti muli Asilamu (ogonjera)

    [81] “Ndipo (kumbukirani) pamene Allah adatenga lonjezo kwa aneneri, (n’kuwauza): “Ndikakupatsani buku ndi nzeru, nakudzerani Mtumiki wotsimikizira zomwe zili pamodzi ndi inu, mudzamkhulupirire ndi kumthangata.” (Allah) adatinso: “Kodi mwavomereza ndi kulandira pa zimenezi pangano langali?” (Iwo) adati: “Tavomereza.” (Iye) adati: “Tsono chitirani umboni, ine ndili pamodzi nanu mwa oikira umboni.”

    [82] “Ndipo amene adzatembenuke pambuyo pa lonjezoli, (Allah adzawalanga chifukwa chakuti) iwo ngopandukiradi chilamulo cha Allah

    [83] “Kodi akufuna chipembedzo chomwe si cha Allah pomwe chinthu chilichonse chili kumwamba ndi pansi chikugonjera Iye, mofuna kapena mosafuna? Ndipo onse adzabwezedwa kwa Iye

    [84] “Nena: “Takhulupirira Allah ndi zomwe zavumbulutsidwa pa ife, ndi zomwe zidavumbulutsidwa kwa Ibrahim, ndi Ismail, Ishâq ndi Yaqub ndi zidzukulu (zake), ndi zimene adapatsidwa Mûsa ndi Isa (Yesu), ndi aneneri (ena) zochokera kwa Mbuye wawo. Sitisiyanitsa aliyense pakati pawo, ndipo ife kwa Iye ndi Asilamu (odzipereka kwathunthu).”

    [85] “Ndipo amene angafune chipembedzo chosakhala Chisilamu, sichidzalandiridwa kwa iye. Ndipo iye tsiku lachimaliziro adzakhala mmodzi mwa (anthu) otaika

    [86] “Kodi Allah angawaongole bwanji anthu omwe atuluka m’chikhulupiliro pambuyo pakukhulupirira natsimikiza kuti Mtumiki (uyu Muhammad{s.a.w}) ngoona, nkuwafikiranso zisonyezo zoonekera? Koma Allah saongola anthu ochita zoipa

    [87] “Ndithu mphoto yawo ndiyakuti pa iwo pali matembelero a Allah, a angelo ndi anthu onse

    [88] “M’menemo adzakhala nthawi yaitali; ndipo sichidzapeputsidwa chilango kwa iwo, ndiponso sadzapatsidwa danga

    [89] “Kupatula anthu amene alapa, pambuyo pa zimenezo nachita zabwino. ndithudi, Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha

    [90] “Ndithudi, amene atuluka m’chikhulupiliro pambuyo pokhulupirira, kenako naonjezera kusakhulupirira, kulapa kwawo sikudzavomerezedwa konse. Ndipo iwo ndiosekera

    [91] “Ndithudi amene sadakhulupirire, nkumwalira pamene ali osakhulupirira, sikudzalandiridwa kwa aliyense wa iwo ngakhale atapereka dipo la golide lodzadza dziko lonse. Iwo ndi omwe adzalandire chilango chopweteka, ndipo sadzakhala ndi athandizi

    [92] “۞ Simudzapeza ubwino (weniweni) kufikira mutapereka m’zimene mukuzikonda. Ndipo chilichonse chimene mupereka, ndithudi, Allah akuchidziwa

    [93] “Zakudya zonse zidali zololedwa kwa ana a Israyeli kupatula chimene adadziretsa Israyeli mwini wake Taurat isadavumbulutsidwe. Nena: “Bwerani ndi Tauratiyo ndipo iwerengeni ngati mukunena zoona.”

    [94] “Choncho aliyense amene adzapekera bodza Allah pambuyo pa izi iwo ndiwochita zoipa

    [95] “Nena: “Allah wanena zoona. Choncho tsatirani chipembedzo cha Ibrahim yemwe adali wolungama; sadali mwa ophatikiza Allah ndi mafano.”

    [96] “Ndithudi, nyumba yoyamba yomwe idakhazikitsidwa chifukwa cha anthu (kuti azipempheramo) ndiyomwe ili pa Bakka (ku Makka); yodalitsidwa ndiponso ndichiongolo kwa anthu onse

    [97] “M’menemo muli zizindikiro zoonekera (zozindikiritsa kupatulika kwake ndi ukale wake); ndi pamalo pomwe Ibrahim adali kuimilira; ndipo amene akulowamo amakhala m’chitetezo; ndipo Allah walamula anthu kuti akachite Hajj ku nyumbayo amene angathe kukonzekera ulendo wonka kumeneko. Ndipo yemwe angakane, (osapitako pomwe ali nazo zomuyenereza), ndithudi, Allah Ngwachikwanekwane pa zolengedwa Zake

    [98] “Nena: “E inu amene mudapatsidwa buku! chifukwa chiyani mukuzikana zizindikiro za Allah pomwe Allah ndi Mboni wa zonse zimene mukuchita?”

    [99] “Nena: “ E inu amene mudapatsidwa buku! Chifukwa chani mukutsekereza anthu amene akhulupirira kuyenda pa njira ya Allah? Mukufuna kuti ikhote pomwe inu ndinu mboni (kuti ndi njira ya Allah yopanda choipa)? Komatu Allah sanyalanyaza zomwe mukuchita.”

    [100] “E inu amene mwakhulupirira! Ngati muwamvera ena mwa amene apatsidwa buku, akubwezani kuti mukhale osakhulupirira pambuyo pa chikhulupiliro chanu

    [101] “Kodi mukukanira bwanji pomwe ndime za Allah zikuwerengedwa kwa inu, pomwenso Mtumiki Wake ali pamodzi nanu? Ndipo amene agwiritse mwa Allah (bwinobwino), ndithudi iye wawongoleredwa kunjira yoongoka

    [102] “E inu amene mwakhulupirira! Opani Allah; kuopa kwenikweni. Ndipo musafe pokhapokha mutakhala Asilamu (ogonjera)

    [103] “Ndipo gwiritsani chingwe (chipembedzo) cha Allah nonsenu, ndipo musagawikane. Kumbukirani mtendere wa Allah womwe uli pa inu; pamene mudali odana ndipo Iye adalunzanitsa pakati pa mitima yanu, tero mwa mtendere Wake mudakhala abale; ndipo mudali m’mphepete mwa dzenje la moto (wa Jahanama), ndipo Iye adakupulumutsanimo. Umo ndi momwe Allah akukufotokozerani ma Ayah Ake (ndime Zake) kuti muongoke

    [104] “Ndipo mwa inu lipezeke gulu la anthu oitanira ku zabwino (Chisilamu) ndipo alamule (kuchita) zabwino ndikuletsa zoipa. Iwo ndiwo opambana

    [105] “Ndipo musakhale monga aja amene adagawikana nasiyana pambuyo powadzera zisonyezo zoonekera poyera (zowaletsa kutero). Ndipo iwo adzakhala ndichilango chachikulu

    [106] “Patsikulo nkhope zina zidzakhala zowala pomwe nkhope zina zidzakhala zakuda. Tsono amene nkhope zawo zidzakhala zakuda, (adzauzidwa): “Kodi mudakana ( Allah) pambuyo pa chikhulupiliro chanu? Choncho, lawani chilango (chopweteka) chifukwa cha zomwe mudali kuzikana.”

    [107] “Tsono (anthu odala) omwe nkhope zawo zidzawale, adzakhala m’chifundo cha Allah. Iwo mmenemo adzakhala nthawi yaitali

    [108] “Awo ndi ma Ayah (ndime) a Allah; tikukuwerengera mwa choonadi. Ndipo Allah safuna kupondereza zolengedwa (Zake)

    [109] “Chilichonse cha kumwamba ndipansi ncha Allah. ndipo zinthu zonse zidzabwezedwa kwa Allah

    [110] “Inu (Asilamu) ndinu gulu labwino limene lasankhidwa kwa anthu. Mukulamula (kuchita) zabwino ndi kuletsa zoipa, ndipo mukukhulupirira mwa Allah. Ndipo aja adapatsidwa buku akadakhulupirira monga momwe (adawalamulira) kukadakhala kwabwino kwa iwo. (Koma) mwa iwo alipo okhulupirira pomwe ambiri mwa iwo ngopandukira (chilamulo cha Allah)

    [111] “Sangakuvutitseni (adani anuwo, makamaka Ayuda) koma ndi timasautso (tochepa); ngati (atayesera) kukuthirani nkhondo, akufulatirani (kuthawa); ndipo kenako sangapulumutsidwe

    [112] “Adindidwa chidindo chakunyozeka paliponse pamene angapezeke kupatula (akagwira) chingwe (cha chipembedzo) cha Allah, kapena chingwe cha anthu (pothandizidwa ndi anthu ena. Koma paokha sangakhale ndi nyonga). Abwerera ndi mkwiyo wa Allah; ndipo chidindo chaumphawi chadindidwa pa iwo. Izi nchifukwa chakuti iwo sadali kukhulupirira mawu a Allah, ndipo amapha aneneri popanda choonadi. Izi nchifukwa chakutinso adanyoza ndi kulumpha malire

    [113] “Iwo amene adapatsidwa buku sali ofanana. Mwa iwo muli anthu olungama omwe akuwerenga ma Ayah (ndime) a Allah nthawi za usiku uku akumulambira

    [114] “Amakhulupirira Allah ndi lsiku lomaliza; ndipo amalamulira (kuchita) zabwino ndikuletsa zoipa; ndipo amachita changu pa zinthu zabwino. Ndipo iwo ndi omwe ali mwa anthu abwino

    [115] “Ndipo chabwino chilichonse chimene angachite sadzakanidwa nacho, (koma adzawalipira malipiro abwino). Ndipo Allah Ngodziwa za amene akuopa Iye

    [116] “Ndithudi, amene sakhulupirira, chuma chawo ngakhale ana awo, sizidzawathandiza chilichonse kwa Allah. Ndipo iwo ndi anthu a ku Moto basi; adzakhala mmenemo nthawi yaitali

    [117] “Fanizo la chimene akupereka mwaulere pa moyo uwu wa dziko lapansi, chili ngati mphepo yomwe mkati mwake muli chisanu chaukali, chagwera pa munda wa anthu omwe adadzichitira okha zoipa, n’kuuonongeratu. Si Allah amene adawachitira zoipa, koma iwo okha adadzichitira zoipa

    [118] “E inu amene mwakhulupirira! Musawachite omwe sali mwa inu kukhala abwenzi; owauza chinsinsi, iwo sasiya kukuchitirani choipa. Amakonda zimene zikukuvutitsani. Chidani chawo (pa inu) chaonekera m’milomo yawo. Ndipo zimene zikubisa zifuwa zawo, nzazikulu zedi. Ndithudi, takufotokozerani zizindikiro zonse ngati inu muli anthu ozindikira

    [119] “Ha! Inu ndinu amene muwakonda (adani anu) pomwe iwo sakukondani ngakhale inu mukukhulupirira mabuku onse! Akakumana nanu amanena (mwachiphamaso): “Takhulupirira.” Koma akakhala kwa okha, amakulumirani nsonga za zala chifukwa chaukali. Nena: “Mwalirani ndiukali wanuwo ndithudi, Allah akudziwa za m’zifuwa (mwanu).”

    [120] “Ngati chabwino chikakufikirani, amaipidwa nacho; koma choipa chikakugwerani amachikondwelera. Koma ngati inu mupirira ndi kuopa Allah, ndale zawo sizingakuvutitseni chilichonse. Ndithu Allah akudziwa bwino zonse zimene iwo akuchita

    [121] “(Kumbukira) pamene unachoka m’mawa kusiya banja lako kuti uwakonzere Asilamu malo omenyanira (nkhondo). Ndipo Allah Ngwakumva, Ngodziwa

    [122] “(Kumbukira) pamene magulu awiri mwa inu anafunitsitsa kuti athawe (chifukwa cha mantha monga momwe adathawira achinyengo). Koma Allah adali Mtetezi wa magulu awiriwo. (Choncho adawasunga kuti asathawe). Ndipo okhulupirira ayadzamire kwa Allah Yekha basi

    [123] “Allah adakupulumutsani pa (nkhondo) ya Badri pomwe inu munali ofooka (chifukwa chakuchepa ndi kusakhala ndi zida zokwanira). Choncho opani Allah kuti mumthokoze (nthawi zonse pa zomwe akukuchitirani)

    [124] “(Kumbukira) pamene umauza okhulupirira: “Kodi sizikukukwanirani pokuonjezerani Mbuye wanu zikwi zitatu za angelo otsitsidwa

    [125] “Inde, ngati mupirira ndi kudziteteza ku machimo, ndipo (adani anu) nakudzerani mwachangu chawo chimenechi, pamenepo Mbuye wanu adzakuonjezerani ndi zikwi zisanu za angelo odziwa kumenya nkhondo.”

    [126] “Ndipo Allah sadachite izi (potumiza angelo) koma kuti ukhale uthenga wabwino kwa inu ndi kuti pakutero mitima yanu ikhazikike ndi zimenezo. Ndipo chithandizo sichichokera (kwa wina aliyense) koma kwa Allah basi, Wamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya

    [127] “(Kuchita izi) nkuti adule gawo la osakhulupirira (kuti ena a iwo aphedwe) kapena awasambule ndi kuti abwelere ali olephera

    [128] “Iwe ulibe chako pa izi. Mwina (Allah) angalandire kulapa kwawo kapena kuwalanga pakuti ndithu iwo ndi anthu oipa

    [129] “Zonse zakumwamba ndi zapansi nza Allah; amamkhululukira amene wamfuna, ndikumulanga amene wamfuna. Komatu Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha

    [130] “E inu amene mwakhulupirira! Musadye Riba (chuma cha katapira), kumangoonjezeraonjezera. Ndipo opani Allah kuti mupambane

    [131] “Ndipo opani Moto umene wakonzedwa kwa (anthu) osakhulupirira

    [132] “Ndipo mverani Allah ndi Mtumiki kuti mumveredwe chisoni

    [133] “Ndipo chimkereni mwachangu chikhululuko cha Mbuye wanu (kupyolera m’zochita zanu zabwino), ndi Munda (Wake) umene Kutambasuka kwake (mulifupi) kuli ngati kumwamba ndi pansi, (womwe) wakonzedwa kuti ukhale wa oopa Allah

    [134] “Omwe amapereka (zopereka zawo mwaulere) pamene akupeza bwino ngakhale pamene akuvutika; amenenso amabisa ukali wawo ndi okhululukira anthu. Ndipo Allah amakonda ochita zabwino

    [135] “Ndi amene amati akachita uve (wamachimo), kapena kudzichitira okha zoipa, amakumbukira Allah nampempha chikhululuko pa machimo awo. Kodi ndindani angakhululuke machimo kupatula Allah; ndipo napanda kupitiriza machimo omwe achita uku akudziwa

    [136] “Iwowo mphoto yawo ndi chikhululuko chochokera kwa Mbuye wawo, ndi minda yoyenda mitsinje pansi pake (ndi patsogolo pake), momwe akakhalamo nthawi yaitali. Taonani kukoma malipiro a ochita zabwino

    [137] “Zidapita njira za zilango zambiri zosiyanasiyana zomwe adapatsidwa amene adalipo patsogolo panu. Tero tayendani pa dziko ndi kuona momwe adalili mapeto a anthu otsutsa

    [138] “Uku ndi kulengeza poyera kwa anthu (onse); komanso chiongoko ndi ulaliki kwa (anthu) oopa Allah

    [139] “Ndipo musafooke (pomenya nkhondo), ndiponso musadandaule (ndi mavuto amene akupezani) pakuti ndinu apamwamba, ngati mulidi okhulupirira

    [140] “Ngati mwavulazidwa, naonso anthuwo avulazidwanso molingana. Ndipo amenewo ndimasiku, timawapatsa anthu mosinthanasinthana. (Ichi chachitika) kuti Allah aonetse poyera amene akhulupirira (moona; choncho sadathawe konse); ndi kuti awachite ena mwa inu kukhala Shuhadaa (ofera pankhondo yoyera). Komatu Allah sakonda anthu ochita zoipa

    [141] “(Izi) nkuti Allah awayeretse amene akhulupirira ndikuwathetseratu osakhulupirira

    [142] “Kodi mukuganiza kuti mukalowa ku Munda wamtendere pomwe Allah asadawaonetsere poyera amene amenyera chipembedzo cha Allah mwa inu ndi kuwaonetseranso poyera opirira (pa nkhondo ya Allah)

    [143] “Ndithudi, mudali kuilakalaka imfa musanakumane nayo. Ndithudi tsopano mwaiona (ndikuphedwa kwa abale anu) inu mukupenya

    [144] “Muhammad (s.a.w) sali chinthu china koma Mtumiki chabe. Patsogolo pake adamuka atumiki ambiri. Kodi ngati atamwalira kapena kuphedwa, mungabwelerenso m’mbuyo? Ndipo amene abwelere m’mbuyo mwake savutitsa Allah ndi chilichonse; koma Allah adzalipira othokoza

    [145] “Munthu aliyense sangafe pokhapokha mwa chilolezo cha Allah, (ndi kukwanira) nthawi yake yolembedwa. Ndipo amene akufuna mphoto ya pa dziko la pansi, timpatsa pompo; ndipo amene akufuna Mphoto ya tsiku lachimaliziro tidzampatsa konko. Ndipo, tidzawalipira (zabwino) othokoza

    [146] “Ndi Aneneri angati adamenyana (ndi adani) pamodzi ndi anthu olungama ambiri, komatu sadataye mtima pa mavuto omwe adawagwera pa njira ya Allah; sadafooke ndipo sadagonjere (adani awo), ndipo Allah amakonda opirira

    [147] “(Anthu olungamawa) kunena kwawo sikudali kwina koma ankati: “Mbuye wathu! Tikhululukireni machimo athu ndi kupyola malire kwathu m’zinthu zathu. Ndipo limbikitsani mapazi athu (panjira Yanu) ndipo tithandizeni ku anthu osakhulupirira.”

    [148] “Choncho Allah adawapatsa mphoto ya pa dziko lapansi ndi mphoto yabwino ya tsiku lachimaliziro. Allah amakonda ochita zabwino

    [149] “E inu amene mwakhulupirira! Ngati muwamvere amene sadakhulupirire, akubwezerani kumbuyo kwanu (kumachitidwe achikunja) tero mudzakhala otaika

    [150] “Komatu Allah ndiye Mbuye wanu. Iye Ngwabwino kwabasi kuposa athandizi (ena onse)

    [151] “Tiponya mantha m’mitima mwa amene sadakhulupirire chifukwa chakumphatikiza Allah (ndi mafano) omwe Allah sadatsitsire umboni (wosonyeza umulungu wawo) ndipo malo awo adzakhala ku Moto. Taonani kuipitsitsa malo a anthu ochita zoipa

    [152] “Ndithudi, Allah adakutsimikizirani lonjezo lake (lakuti muwagonjetsa adani). Choncho mudali kuwapha mwachilolezo Chake kufikira pamene mudafooka ndikuyamba kukangana za lamulolo, tero mudalinyozera pambuyo pokuonetsani zimene mumazikonda; (pamenepo mpomwe adasiya kukuthangatani). Alipo ena mwa inu amene akukonda dziko lapansi (zamdziko), ndipo alipo ena mwa inu amene akukonda tsiku lachimaliziro. Kenako (Allah) adakuchotsani pa iwo (adakusiitsani kuwamenya osakhulupirirawo) kuti akuyeseni mayeso. Koma Iye tsopano wakukhululukirani. Ndipo Allah ndi mwini kuchita zabwino pa okhulupirira

    [153] “Kumbukirani pamene mudali kuthawa mwa liwiro popanda kumvera aliyense; pomwe Mtumiki adali kukuitanani, ali pambuyo panu. Ndipo (Allah) Adakupatsani madandaulo pa madandaulo. (Motero wakukhululukirani) kuti musadandaule pa zomwe zakudutsani, ngakhalenso (pa masautso) omwe akupezani. Ndipo Allah Ngodziwa zonse zimene muchita

    [154] “Kenako pambuyo pa kudandaula, adakutsitsirani mpumulo - tulo tomwe tidaphimba gulu lina mwa inu. Padali gulu lina lomwe maganizo awo adawatangwanitsa namuganizira Allah ndizoganizira zopanda choonadi, zoganizira zaumbuli; ankati: “Ha! Kodi tili ndi chiyani ife pa chinthu ichi?” Nena: “Zinthu zonse nza Allah.” Akubisa m’mitima mwawo zomwe sakuzionetsa kwa iwe. Akunena: “Tidakakhala ndi chilichonse pa chinthu ichi, sitikadaphedwa apa.” Nena: “Ngakhale mukadakhala m’nyumba zanu, ndithudi kwa iwo amene imfa idalembedwa (kuti amwalire) akadapita kumalo omwalilirawo, koma Allah (adachita izi) kuti awonetse poyera zomwe zili m’zifuwa zanu. Ndikuyeretsa zomwe zili m’mitima mwanu. Ndipo Allah Ngodziwa za mzifuwa.”

    [155] “Ndithudi, mwa inu amene adabwerera m’mbuyo (kuthawa) tsiku lomwe magulu awiri a nkhondo adakumana (pa nkhondo ya Uhudi; gulu la osakhulupirira ndi gulu lankhondo la Asilamu), satana ndiyemwe adawaterezetsa chifukwa cha zina (zolakwa) zomwe adachita; ndipo Allah (tsopano) wawakhululukira. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngoleza koposa

    [156] “E inu amene mwakhulupirira! Musakhale ngati amene sadakhulupirire, nanena za anzawo pamene akuyenda pa dziko kapena pomwe akumenyana nkhondo (ndikufera konko): “Akadakhala ndi ife sakadafa, ndiponso sakadaphedwa.” Allah (adawathira maganizo amenewa) kuti azipange zimenezo kukhala zodandaulitsa m’mitima mwawo. Komatu Allah ndi amene amapereka moyo ndi imfa. Ndipo Allah akuona zonse zomwe mukuchita

    [157] “Ndipo ngati mwaphedwa pa njira ya Allah, kapena kufa, (palibe chotaika kwa inu) pakuti chikhululuko ndi chisoni zochokera kwa Allah nzabwino kuposa zomwe akuzisonkhanitsa (pa moyo wa pa dziko lapansi)

    [158] “Ndipo ngati mumwalira kapena kuphedwa (n’chimodzimodzi), ndithudi nonsenu mudzasonkhanitsidwa kwa Allah

    [159] “Chifukwa cha chifundo chochokera kwa Allah, uli woleza mtima kwa iwo, (iwe Mtumiki Muhammad {s.a.w}). Ndipo ukadakhala waukali, wouma mtima, ndithudi, akadakuthawa pamaso pako. Choncho akhululukire ndi kuwapemphera chikhululuko (kwa Allah); ndipo chita nawo upo pa zinthu. Ndipo ngati watsimikiza, tsamira kwa Allah (basi, ndi kuchita chimene watsimikiza kuchichita). Ndithudi, Allah amakonda oyadzamira Kwake (odalira Iye)

    [160] “Ngati Allah akupulumutsani, palibe amene angathe kukugonjetsani. Ndipo ngati akulekani, ndaninso angakupulumutseni pambuyo pake. Choncho, okhulupirira ayadzamire kwa Allah basi

    [161] “Nkosatheka kwa Mtumiki kuchita chinyengo. Ndipo amene achite chinyengo adzadza pa tsiku lachimaliziro ndi zomwe adazichitira chinyengo. Kenako munthu aliyense adzalipidwa mokwanira pa zomwe adachita. Ndipo sadzaponderezedwa

    [162] “Kodi amene akutsata chokondweretsa Allah angalingane ndi yemwe wabwerera ndi mkwiyo wochokera kwa Allah, ndipo Jahannam nkukhala malo ake? Taonani kuipa kumalo obwerera

    [163] “Iwo ali ndi maulemelero (osiyanasiyana) kwa Allah. Ndipo Allah akuona zonse zomwe akuchita

    [164] “Ndithudi, Allah adawachitira ubwino waukulu okhulupirira powatumizira Mtumiki wochokera mwa iwo yemwe akuwawerengera ma Ayah ake (ndime zake) ndikuwayeretsa ndikuwaphunzitsa buku ndi (mawu a) nzeru. Ndithudi, kale adali mkusokera koonekera

    [165] “Pamene sautso lidakupezani lomwe inu mudawathira nalo (adani anu) lochulukirapo kawiri, mudanena: “Lachokera kuti (sautso) ili?” Nena: “Ilo lachokera kwa inu eni (chifukwa cha kunyoza lamulo lomwe adakuuzani). Ndithudi, Allah Ngokhoza chilichonse.”

    [166] “Ndipo sautso lomwe lidakupezani tsiku lomwe adakumana magulu awiri ankhondo, lidali mwa chilolezo cha Allah ndikutinso awaonetsere poyera okhulupirira

    [167] “Ndi kuwadziwitsa amene adachita uchiphamaso. Iwo adauzidwa: “Bwerani, menyani (nkhondo) pa njira ya Allah kapena mwatsekereze (adani kwa ife).” Adati: “Tikadadziwa kuti pali kumenyana, ndithudi, tikadakutsatani (koma kumeneko kuli kuphedwa kokhakokha basi).” Iwo tsiku limenelo adali pafupi ndikusakhulupirira kuposa chikhulupiliro (ngakhale kuti masiku onse amasonyeza Chisilamu mwa chiphamaso). Akunena ndi milomo yawo zomwe sizili m’mitima mwawo. Koma Allah akudziwa bwinobwino (zonse) zomwe akubisa

    [168] “Iwo ndi amene adanena za abale awo pomwe iwo adakhala osapita ku nkhondo: “Akadatimvera, sibwenzi ataphedwa.” Nena: “Dzichotsereni imfa nokha, (kuti musafe) ngati mukunenadi zoona.”

    [169] “Ndipo musawaganizire omwe adaphedwa pa njira ya Allah kuti ndi akufa, koma iwo ngamoyo, akudyetsedwa kwa Mbuye wawo

    [170] “Akukondwera pa zimene wawapatsa Allah kuchokera m’zabwino Zake. Ndipo akufunira mafuno abwino amene sadakumane nawo omwe ali pambuyo pawo, (omwe alipobe pa dziko lapansi) ponena kuti pa iwo sipadzakhala mantha kapena kudandaula

    [171] “Akukondwelera chisomo ndi ubwino zochokera kwa Allah, ndi kuti Allah sasokoneza malipiro a okhulupirira

    [172] “(Awa ndi) amene adavomera Allah ndi Mtumiki pambuyo povulazidwa; kwa amene achita zabwino mwa iwo ndi kuopa Allah, adzakhala ndi malipiro aakulu

    [173] “Omwenso adauzidwa ndi anthu (olembedwa ganyu ndi Akafiri aku Makka) kuti: “Anthu Akusonkhanirani. Choncho aopeni.” Koma (zonenazo) zidawaonjezera chikhulupiliro (Asilamu). Ndipo adati: “Allah akutikwanira, ndipo Iye ndi Mtetezi wabwino koposa.”

    [174] “Choncho adabwerera ndi chisomo ndi ubwino zochokera kwa Allah. Sichidawakhudze choipa chilichonse; adatsatira zokondweretsa Allah. Ndipo Allah ndimwini ubwino waukulu

    [175] “Ndithudi uyo (anakuopsezani) ndi satana yemwe amaopseza anzake. Choncho musawaope, ndiopeni Ine ngati inu mulidi okhulupirira

    [176] “Ndipo asakudandaulitse omwe akuthamangira kuchita zinthu zachikunja. Ndithu iwo sangapereke sautso lililonse kwa Allah. Allah akufuna kuti asawaikire gawo lililonse la (zabwino) tsiku lachimaliziro, ndipo pa iwo padzakhala chilango chachikulu

    [177] “Ndithudi, amene asinthanitsa kusakhulupirira ndi chikhulupiliro, sangathe kumvutitsa Allah ndi chilichonse. Ndipo pa iwo padzakhala chilango chopweteka

    [178] “Ndipo amene sadakhulupirire asaganize kuti nthawi yaitali imene tikuwapatsayi njabwino kwa iwo. Ndithudi, tikuwapatsa nthawiyi kuti aonjezere kuchita uchimo. Ndipo pa iwo padzakhala chilango chosambula

    [179] “Nkosatheka kwa Allah kusiya okhulupirira momwe mulilimu, mpaka atalekanitsa (pakati pawo) oipa ndi abwino. Ndipo nkosatheka kwa Allah kukudziwitsani zinthu zamseri, koma Allah amasankha mwa atumiki ake amene wamfuna (nkumdziwitsa zina mwa zimenezo). Choncho khulupirirani Allah ndi atumiki ake. Ndipo ngati mukhulupirira ndi kuopa (Allah), pa inu padzakhala malipiro aakulu

    [180] “Ndipo asaganize amene akuchitira umbombo zimene Allah wawapatsa kuchokera m’zabwino Zake kuti kutero ndibwino kwa iwo, koma kutero nkoipa kwa iwo. Adzanjatidwa magoli pa zomwe adazichitira umbombo pa tsiku lachimaliziro. Ndipo um’lowam’malo wa zakumwamba ndi pansi ngwa Allah. Ndipo Allah akudziwa zonse zimene mukuchita

    [181] “Ndithu Allah wamva liwu (lonyogodola) la omwe (Ayuda) anena kuti: “Allah ngosauka, ndipo ife ndife olemera.” Tazilemba zimene anena, ndipo (talembanso) kupha kwawo aneneri popanda choonadi. Ndipo tidzawauza (tsiku la chiweruziro): “Lawani chilango cha Moto owotcha.”

    [182] ““Izi nchifukwa cha zomwe manja anu adatsogoza. Ndithudi, Allah sali opondereza akapolo Ake.”

    [183] “Amene anenanso: “Allah Adatilamula ife kuti tisakhulupirire mtumiki aliyense mpaka atabwera ndi nsembe yopserezedwa ndi moto.” Nena: “Adakudzerani atumiki ndisanadze ndi zisonyezo zooneka ndi chimene mukunenachi. Nanga bwanji mudawapha, ngati mukunenadi zoona?”

    [184] Ndipo ngati akutsutsa iwe (Mtumiki Muhammad (s.a.w}, sichachilendo) adatsutsidwanso atumiki patsogolo pako omwe adadza ndi zisonyezo zoonekera ndi mabuku anzeru, ndi mabukunso ounika

    [185] “Munthu aliyense adzalawa imfa. Ndithudi, mudzalipidwa malipiro anu mokwanira tsiku lachimaliziro. Ndipo amene adzatalikitsidwe ndi Moto nalowetsedwa ku Munda wamtendere, ndiye kuti wapambana, (kupambana kwakukulu), ndipo moyo wapadziko lapansi sulikanthu koma ndichisangalalo chonyenga basi

    [186] “Ndithu mudzayesedwa m’chuma chanu ndi miyoyo yanu; ndipo mudzamva masautso ambiri kuchokera kwa omwe adapatsidwa mabuku kale ndiponso kuchokera kwa omwe akuphatikiza Allah ndi zinthu zina (Arab), koma ngati mupirira ndi kudzisunga ku zomwe mwaletsedwa ndi Allah, (ndiye kuti mwachita chinthu chabwino kwambiri) pakuti zinthu izi (ndi zinthu zazikulu) zofunika munthu kuikirapo mtima

    [187] “Ndipo (akumbutse) pamene Allah adamanga chipangano ndi amene adapatsidwa buku (ndi kuwauza) kuti ndithudi mudzalifotokoze mwatsatanetsatane (bukulo) kwa anthu, ndipo musadzalibise. Koma Adaliponya kumbuyo kwa misana yawo naligulitsa ndi mtengo wochepa. Taonani kuipa chimene adagula (chimene adasankha)

    [188] “Musaganize kuti amene akukondwera ndi zinthu (zoipa) zomwe achita nakonda kutamandidwa ndi zomwe sadachite, musawaganizire kuti akapulumuka. (Koma kuti) pa iwo padzakhala chilango chopweteka

    [189] “Ndipo ufumu wa kumwamba ndi pansi ngwa Allah; ndipo Allah Ngokhoza chilichonse

    [190] “Ndithudi, m’kulenga kwa kumwamba ndi dziko lapansi ndi kusinthana kwa usiku ndi usana, muli zisonyezo kwa eni nzeru

    [191] “Omwe amakumbukira Allah, ali chiimire, ali chikhalire, ndi ali chigonere chamnthiti mwawo; namalingalira kalengedwe ka thambo ndi nthaka (mmene Allah adazilengera, uku akuti): “E Mbuye wathu! simunalenge izi mwachabe. Ulemelero Ngwanu. Tichinjirizeni ku chilango cha Moto.”

    [192] ““E Mbuye wathu! Ndithudi, yemwe mudzamulowetse ku Moto ndiye kuti mwamuyalutsa, ndipo sipadzakhala athandizi kwa ochita zoipa.”

    [193] ““E Mbuye wathu! Ndithudi, ife tamva woitana akuitanira ku chikhulupiliro kuti: ‘Khulupirirani Mbuye wanu,’ ndipo takhulupirira. E Mbuye wathu! Tikhululukireni machimo athu ndi kutifafanizira zoipa zathu, ndipo mutenge mizimu yathu tili pamodzi ndi anthu abwino.”

    [194] ““E, Mbuye wathu! Tipatseni zimene mudatilonjeza kupyolera mwa atumiki anu ndipo musadzatisambule tsiku lachimaliziro. Ndithudi, inu simuswa lonjezo.”

    [195] “Choncho Mbuye wawo adawavomereza (zopempha zawo ponena kuti): “Ndithudi, ine sindidzasokoneza (khama la) ntchito yabwino kwa ochita ntchito mwa inu, kaya atakhala mwamuna kapena mkazi, (pakuti) inu ndinu amodzi. Choncho amene asamuka (kumidzi yawo mwachifuniro chawo), naapirikitsidwa m’midzi yawo navutitsidwa pa njira Yanga, namenya nkhondo ndikuphedwa, ndithudi, ndiwafafanizira zolakwa zawo. Ndipo ndidzawalowetsa m’Minda yomwe pansi pake (ndi patsogolo pake) mitsinje ikuyenda. Amenewo ndimalipiro ochokera kwa Allah, ndipo kwa Allah kuli malipiro abwino.”

    [196] “Ndithu kusakunyenge kuyendayenda pa dziko kwa amene sadakhulupirire

    [197] “Ndichisangalalo chochepa; kenako malo awo ndi kumoto wa Jahannam. Taonani kuipa kwa malo wokakhazikikamo

    [198] “Koma amene aopa Mbuye wawo (potsatira zolamulidwa ndi kuleka zoletsedwa) adzapeza Minda yamtendere momwe mitsinje ikuyenda pansi (ndi patsogolo pake). Adzakhala m’menemo nthawi yaitali, ndi phwando lochokera kwa Allah. Ndipo zomwe zili kwa Allah nzabwino kwa anthu abwino (kuposa zosangalatsa za dziko lapansi)

    [199] “Ndithudi mwa amene adapatsidwa buku, alipo amene akukhulupirira Allah ndi zimene zavumbulutsidwa kwa inu, ndi zimene zidavumbulutsidwa kwa iwo, uku akudzichepetsa kwa Allah; sagulitsa ndime za Allah ndi mtengo wochepa (wa pa dziko lapansi). Iwo adzalandira malipiro awo kwa Mbuye wawo. Ndithudi, Allah Ngwachangu pakuwerengera

    [200] “E inu amene mwakhulupirira! Pirirani, ndipo agonjetseni adani anu ndikupirirako; ndipo tetezani malire anu ndipo muopeni Allah kuti mukhale opambana

    Akazi

    Surah 4

    [1] “E inu anthu! Opani Mbuye wanu yemwe adakulengani kuchokera mwa munthu mmodzi (Adam) ndipo adalenga mmenemo mkazi wake (Hawa), ndipo adafalitsa amuna ndi akazi ambiri kuchokera mwa awiriwo. Ndipo opani Allah yemwe kupyolera mwa Iye mumapemphana. Ndipo (sungani) chibale. Ndithudi Allah Ndimyang’aniri pa inu (akuona chilichonse chimene muchita)

    [2] “Ndipo apatseni ana amasiye chuma chawo; musasinthanitse choipa ndi chabwino. Ndipo musadye chuma chawo pochiphatikiza ndi chuma chanu. Ndithudi, (zonsezo) ndiuchimo waukulu

    [3] “Ngati mwaopa kuti simungachite chilungamo pa amasiye (opaninso kusawachitira chilungamo akazi pamitala), choncho kwatirani amene mukuwafuna mwa akazi; awiri, kapena atatu, kapena anayi (basi). Koma ngati mukuopa kuti simungathe kuchita chilungamo, (kwatirani) mmodzi basi kapena amene manja anu akumanja adapeza (mdzakazi). Kutero kudzakuchititsani kuti musapendekere (kumbali yosalungama)

    [4] “Ndipo akazi apatseni chiwongo chawo monga mphatso. Koma (akazi anuwo) ngati atakupatsani mokoma mtima chilichonse (m’chiwongocho), idyani mokondwa ndi mothandizika nacho

    [5] “Ozerezeka musawapatse chuma chanu chomwe Allah wachichita kukhala cholimbitsa matupi anu ndi moyo wanu. Koma adyetseni nacho ndikuwaveka nacho ndikuwauza mawu abwino (monga kuti: Mukadzakula ndikukhala olungama, tidzakupatsani chuma chanu)

    [6] “Ayeseni amasiye (akayandikira kukula nsinkhu kuti muone kuti atha kuchita ntchito yabwino ndi chuma chawo mukawapatsa), kufikira atafika nthawi yokwatira/kukwatiwa. Ndipo ngati mutawaona kuti ali ndi nzeru zabwino, apatseni chuma chawo. Musachidye mosasamala ndi mwachangu poopa kuti angakule. Ndipo amene ali opeza bwino adziletse (kulandira mphoto yolelera ana amasiyewo). Koma amene ali wosauka adye mwa ubwino (osati moononga). Ndipo pamene mukuwapatsa chuma chawo, funani mboni (zoonelera kuperekedwa kwa chumacho). Ndipo Allah ali Wokwana kukhala Muwelengeri (ndi Woyang’anira)

    [7] “Amuna m’chuma chimene makolo ndi achibale asiya ali ndi gawo. Naonso akazi ali ndigawo m’chuma chimene asiya makolo ndi achibale (chapafupi), ngakhale chitakhala chochepa kapena chochuluka ndigawo logawidwa (ndi Allah)

    [8] “Ndipo panthawi yogawa, ngati angabwere achibale, amasiye ndi osauka (omwe alibe gawo pa chumacho), apatseniko kanthu ndi kunena nawo mawu abwino

    [9] “Ndipo (wowasiirawo) aope (kusachita chilungamo), kuti naonso ngati atasiya ana awo ofooka pambuyo, akadawaopera (kuchenjeleredwa). Choncho aope Allah ndipo anene mawu olingana (kwa ana amasiyewo)

    [10] “Ndithu amene akudya churna cha ana amasiye mopondereza, akudya ndi kuthira moto m’mimba zawo. Ndipo adzalowa ku Moto woyaka

    [11] “Allah akukulamulani za ana anu achimuna apate gawo lolingana ndi gawo la akazi awiri. Ngati akaziwo ali (opitilira) awiri, ndiye kuti adzalandira zigawo ziwiri mwa zigawo zitatu (/3) za (chumacho) chimene wasiya (womwalira), ngati mwana wamkazi ndi mmodzi, apatsidwe gawo limodzi mwa magawo awiri (1/2), naonso makolo ake awiri aliyense wa iwo alandile gawo limodzi mwa magawo asanu ndi limodzi (1/6) achuma chosiidwacho, ngati (womwalirayo) wasiya mwana (kapena mdzukulu). Koma ngati sadasiye mwana, ndipo makolo ake awiri ndiwo awasiira, ndiye kuti mayi wake alandire gawo limodzi mwamagawo atatu (1/3) achumacho, (ndipo bambo alandire 2/3). Ngati wakufayo wasiya abale, ndiye kuti mayi wake apeza gawo limodzi mwa magawo asanu ndi limodzi (1/6) achumacho. (Kugawa chumaku kuchitike) atachotsapo chimene iye adalamulira kuti adzachipereke kwakutikwakuti, kapena kulipira ngongole (zake). Atate anu ndi ana anu, simudziwa inu kuti ndani mwa iwo amene ali ndi chithandizo chapafupi kwa inu. Amenewa ndi malamulo omwe akhazikitsidwa ndi Allah. Ndithudi, Allah ngodziwa kwambiri, Ngwanzeru zakuya

    [12] “Inunso mupata gawo limodzi mwa magawo awiri (/2) achuma chimene akazi anu asiya ngati alibe mwana (kapena mdzukulu), ngati asiya mwana ndiye kuti inu mupata gawo limodzi m’magawo anayi (1/4) achuma chosiidwacho mutachotsapo zomwe adalamula kuti zipite kwakutikwakuti kapena ngongole zake, naonso akazi anu apata gawo limodzi m’magawo anayi (1/4) pa chuma chomwe mwasiya, ngati mulibe mwana (ndi mdzukulu). Koma ngati mwasiya mwana (ndi mdzukulu), (akaziwo) apata gawo limodzi m’magawo asanu ndi atatu (1/8) pa chuma chomwe mwasiya mutachotsapo chomwe mudanena kuti chipite kwakutikwakuti kapena kulipira ngongole (zanu). Ngati mwamuna kapena mkazi alowedwa m’malo pachuma pomwe alibe mwana (ndi mdzukulu) ngakhale makolo awiri, koma ali naye m’bale wake (wakuchikazi) kapena mlongo wake (wakuchikazinso) aliyense wa iwo apata gawo limodzi m’magawo asanu ndi limodzi (1/6). Ndipo ngati ali ochulukirapo, ndiye kuti agawirana gawo limodzi m’magawo atatu (1/3) a chumacho pambuyo pochotsapo chomwe chidanenedwa kuti chipita kwakutikwakuti kapena kulipira ngongole, popanda kupereka mavuto. Awa ndi malamulo ofunika omwe achokera kwa Allah. Ndipo Allah Ngodziwa kwambiri (pokhazikitsa malamulo); Woleza (pa akapolo Ake)

    [13] “Amenewo ndiwo malire a Allah; (musawalumphe). Ndipo amene angamvere Allah ndi Mtumiki Wake adzamulowetsa m’Minda yomwe pansi (ndi patsogolo pake) mitsinje ikuyenda. Adzakhala m’menemo nthawi yaitali. Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu

    [14] “Koma amene anganyoze Allah ndi Mtumiki Wake, ndi kulumpha malire ake, (Allah) adzamulowetsa ku Moto; nadzakhala m’menemo nthawi yaitali. Ndipo adzapeza chilango chosambula

    [15] “Ndipo omwe achite cha uve (chigololo) mwa akazi anu, afunireni mboni zinayi za mwa inu zoikira umboni pa iwo. Ngati ataikira umboni (kuti achitadi cha uvecho), atsekereni m’nyumba kufikira imfa idzawapeze, kapena Allah adzawaikire njira ina (monga kuphedwa)

    [16] “Ndipo amuna awiri mwa inu amene akuchita zauve (monga kuchitana ukwati amuna okhaokha ‘matanyula’), akhaulitseni (powalanga). Tsono ngati atalapa ndikukonza bwino (mkhalidwe wawowo) asiyeni. Ndithudi, Allah Ngolandira kulapa, ndiponso Ngwachisoni chambiri

    [17] “Ndithudi kulapa kovomerezeka ndi Allah nkwa omwe amachita zoipa mwa umbuli kenako nkulapa mwachangu. Amenewo ndiomwe Allah amawalandira kulapa kwawo. Ndipo Allah Ngodziwa kwambiri Ngwanzeru zakuya

    [18] “Kulapa sikungalandiridwe pa omwe akuchita zoipa mpaka imfa kumfikira m’modzi wa iwo (pamenepo) nkunena: “Ndithudi ine ndikulapa tsopano.” Ngakhalenso pa omwe akufa ali osakhulupirira. Iwo tawakonzera chilango chopweteka

    [19] “E inu amene mwakhulupirira! Sikovomerezedwa kwa inu kuwalowa chokolo akazi mowakakamiza. Ndipo musawaletse (kukwatiwa ndi amuna ena) ndi cholinga choti muwalande zina mwa zomwe mudawapatsa, (nkosaloledwa kutero) kupatula ngati atachita choipa choonekera. Ndipo khalani nawo mwa ubwino. Ngati mutawada (musalekane nawo), mwina mungade chinthu chomwe Allah waika zabwino zambiri mkati mwake

    [20] “Ndipo ngati mufuna kusintha mkazi wina m’malo mwa wina (pokwatira wina kusiya wakale) pomwe mmodzi wa iwo (woyambayo) mudampatsa milumilu ya chuma, musatenge (kulanda) chilichonse. Kodi mungachitenge mwa chinyengo ndi uchimo woonekera

    [21] “Kodi mungachitenge bwanji pomwe mudalowana wina ndi mnzake, ndipo (akazi) adalandira kwa inu chipangano cholimba

    [22] “Ndipo musakwatire akazi amene adakwatiwapo ndi atate anu, kupatula zomwe zidapita, (musabwerezenso kuzichita). Ndithudi, chinthu ichi nchauve ndipo nchodedwa ndiponso ndinjira yoipa

    [23] “Kwaletsedwa kwa inu kukwatira amayi anu, ana anu, alongo anu, azakhali anu, amayi anu aang’ono kapena aakulu, ana achikazi am’bale wanu, ana achikazi a mlongo wanu, amayi anu amene adakuyamwitsani, alongo anu oberekedwa ndi amene adakuyamwitsanipo. Mayi a akazi anu, ana achikazi owapeza amene mukuwasunga woberekedwa ndi akazi anu omwe mwalowana nawo. Koma ngati simudalowane nawo, nkosaletsedwa kwa inu kukwatira ana awowo; ndi akazi a ana amuna omwe ngochokera kumisana yanu. Ndiponso nkoletsedwa kwa inu kukwatira mophatikiza mkazi ndi mchemwali wake obadwa naye, kupatula zomwe zidapita. Ndithudi Allah Ngokhululuka kwambiri Ngwachisoni zedi

    [24] “۞ Ndiponso (nkoletsedwa kwa inu kukwatira) akazi okwatiwa kupatula chimene manja anu akumanja apeza (mdzakazi). Ili ndi lamulo la Allah lomwe lili pa inu. Ndipo kwalolezedwa kwa inu (kukwatira akazi) omwe sali m’gulu ili. Afunefuneni ndi chuma chanu m’njira ya ukwati, osati chiwerewere. Choncho, amene mwawakwatira mwa iwo nkusangalala nawo, apatseni chiwongo chawo chomwe chakakamizidwa. Palibe kuipa kwa inu (kupereka) chomwe mwagwirizana m’malo mwa chomwe chidatchulidwa. Ndithudi, Allah Ngodziwa, Ngwanzeru zakuya (pokhazikitsa malamulo Ake)

    [25] “Ndipo amene sangathe mwa inu kupeza chuma chokwatilira mkazi amene ali mfulu wokhulupirira, (akwatireni adzakazi) achisungwana okhulupirira, mwa omwe manja anu akumanja apeza, Allah akudziwa kwambiri chikhulupiliro chanu. Ndinu amodzi kuchokera kwa wina ndi mnzake (nonsenu ndinu ana a Adam). Akwatireni ndi chilolezo cha mabwana awo, ndipo apatseni chiwongo chawo mwachilamulo. (Akwatireni) omwe ali akazi odzisunga, osati achiwerewere kapena ochita zibwenzi. Ndipo akakwatiwa, kenako nkuchita chauve, chilango chawo nditheka lachilango cha mfulu. Kumeneko (kukwatira akapoloko) ndilamulo kwa yemwe mwa inu akuopa kuti angachite chiwerewere. Koma ngati mutapirira (posiya kukwatira akapolo) ndibwino kwa inu kutero. Ndipo Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha

    [26] “Allah akufuna kukufotokozerani ndi kukutsogolerani kunjira za omwe adalipo patsogolo panu; ndiponso akufuna kulandira kulapa kwanu. Ndipo Allah Ngodziwa kwambiri, Ngwanzeru zakuya

    [27] “Ndiponso Allah akufuna kulandira kulapa kwanu. Koma amene akutsata zilakolako zawo akufuna mupotoke; kupotoka kwakukulu

    [28] “Allah akufuna kukupeputsirani, pakuti munthu adalengedwa wofooka (alibe mphamvu za thupi ngakhale zolimbana ndi zilakolako za moyo)

    [29] “E inu amene mwakhulupirira! Musadye chuma chanu mwachinyengo koma m’njira yamalonda ndi moyanjana pakati panu. Ndipo musadziphe nokha (ngakhale kupha anzanu). Ndithudi, Allah ali Wachisoni pa inu

    [30] “Ndipo amene achite izi molumpha malire ndi mopanda chilungamo, iyeyo tidzamulowetsa kumoto. Ndipo zimenezo nzopepuka kwa Allah

    [31] “Ngati mudzitalikitsa kumachimo akuluakulu omwe mukuletsedwa, ndiye kuti tikufafanizirani zolakwa zanu (zing’onozing’ono) ndipo tidzakulowetsani malo aulemu

    [32] “Ndipo musazilakelake (mwadumbo) zomwe Allah wawadalitsa nazo ena mwa inu. Amuna ali ndi gawo (lokwanira) la zomwe apeza. Nawonso akazi ali ndi gawo (lokwanira) la zomwe apeza. Ndipo mpempheni Allah zabwino zake. Ndithudi, Allah Ngodziwa chilichonse

    [33] “Ndipo anthu tawaikira alowa mmalo pa zomwe asiya makolo awiri ndi achibale. Ndipo amene mudagwirizana nawo chipangano, apatseni gawo lawo. Ndithudi, Allah Ndimboni pa chilichonse

    [34] “Amuna ndiayang’aniri pa akazi chifukwa choti Allah watukula ena pa ulemelero pamwamba pa ena, chifukwa cha chuma chawo chimene apereka. Choncho, akazi abwino ndi omwe ali omvera, odzisunga ngakhale amuna awo palibe pakuti Allah wawalamula kudzisunga. Ndipo akazi omwe mukuopa mnyozo wawo, achenjezeni; ndipo kenako achokereni pamphasa, (apo ayi), akwapuleni (kukwapula kosavulaza), koma ngati akukumverani, musawafunire njira yowavutitsira. Ndithu Allah ndi yemwe ali Wapamwamba, Wamkulu (kuposa inu nonse)

    [35] “Ndipo (inu aweruzi) ngati muopa mkangano pakati pawo (pa mwamuna ndi mkazi wake), tumizani nkhoswe ya kuchimuna ndi nkhoswe ya kuchikazi. Ngati iwo atafuna kuyanjanitsa, Allah awapatsa mphamvu zoyanjanitsira pakati pawo (okanganawo). Allah Ngodziwa nkhani zobisika, ndiponso Ngodziwa nkhani zoonekera

    [36] “Ndipo mpembedzeni Allah, ndipo musamphatikize ndi chilichonse; ndipo achitireni zabwino makolo awiri, ndi achibale, ndi ana amasiye ndi masikini ndi mnansi woyandikana naye nyumba, ndi wapadera wogundizana naye nyumba, ndi mnzako wokhala naye limodzi, ndi wapaulendo yemwe alibe choyendera, ndi omwe manja anu akumanja apeza (adzakazi). Ndithudi, Allah sakonda wodzitukumula ndi wodzitama

    [37] “Omwe amachita umbombo ndi kulamula anthu kuchita umbombo ndi kubisa zabwino zomwe Allah wawapatsa. Komatu osakhulupirira tawakonzera chilango choyalutsa

    [38] “Ndi omwe akupereka chuma chawo modzionetsera kwa anthu ndipo sakhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro. Ndiponso yemwe satana angakhale bwenzi lake, ndithudi ali ndi bwenzi loipa

    [39] “Kodi pakadakhala vuto lanji kwa iwo ngati akadakhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro napereka zina mwa zomwe Allah wawapatsa? Ndipo Allah ali Wodziwa bwino za iwo

    [40] “Ndithudi, Allah sachitira (anthu) zosalungama ngakhale kanthu kolemera ngati kanyelere; ngati kanthuko kali kabwino amakachulukitsa ndi kupereka malipiro aakulu kuchokera kwa Iye

    [41] “Nanga zidzakhala bwanji tikadzabweretsa mboni pa m’badwo uliwonse ndikukubweretsa iwe (Mneneri Muhammad{s.a.w}) kuti ukhale mboni pa m’badwo uwu

    [42] “Tsiku limenelo aja omwe sadakhulupirire namunyoza Mtumiki, adzakhumba kuti nthaka ikadafafanizidwa pa iwo (akwiliridwe, asaukitsidwe). Ndipo sadzatha kum’bisira Allah nkhani iliyonse (m’zomwe adachita m’moyo wa pa dziko)

    [43] “E inu amene mwakhulupirira! Musayandikire Swala uku muli oledzera, mpaka mudziwe chimene mukunena; ngakhalenso pamene muli ndi janaba (musapemphere kufikira mutasamba) kupatula amene ali pa ulendo (achite Tayammam). Ndipo ngati muli odwala, kapena muli pa ulendo, kapena m’modzi wanu wadza kuchokera kuchimbudzi, kapena mwakhudza akazi (m’njira ya ukwati) ndipo simunapeze madzi (osamba) chitani Tayammam ndi dothi labwino; lipakeni kunkhope kwanu ndi m’mikono mwanu. Ndithudi, Allah Ngofafaniza machimo, Ngokhululuka kwambiri

    [44] “Kodi sukuwaona omwe adapatsidwa gawo la (nzeru zozindikira) buku (la Allah, omwe ndi Ayuda ndi Akhrisitu), akudzisankhira kusokera ndiponso akufuna mutasokera kusiya njira (yabwino)

    [45] “Ndipo Allah akudziwa bwinobwino za adani anu. Ndipo Allah akukwanira kukhala Mtetezi. Allah akukwananso kukhala Mthandizi

    [46] “Mwa Ayuda alipo omwe amasintha mawu kuwachotsa m’malo mwake. Ndipo amanena (chabe ndi milomo yawo): “Tamva;” (pomwe mitima yawo ikunena): “Tanyoza.” (Ndipo akunena kuuza Mtumiki): “Imva koma wosamveredwa (ndipo pakati pakuyankhula kwawo amanena mawu akuti) ‘Raaina’ (ncholinga chomnenera kuti iye ndimbutuma), mokhotetsa malilime awo (mu zoyankhula zawo kuti akhale ngati akumunenera zabwino pomwe akumtembelera) ndi cholinga chotukwana chipembedzo (cha Chisilamu). Akadakhala kuti iwo adanena: “Tamva ndipo tamvera; ndipo imva, utiyang’anire,” (mmalo mwa kunena kwawo kwakuti: ‘Raaina’), zikadakhala zabwino ndizolingana kwa iwo. Koma Allah adawatembelera chifukwa cha kusakhulupirira kwawo. Sakhulupirira koma pang’ono basi

    [47] “E inu amene mwapatsidwa buku! Zikhulupirireni zomwe tavumbulutsa zikutsimikizira zomwe muli nazo tisanazisinthe nkhope zanu ndi kuzitembenuzira kumbuyo kwake, kapena tisanawatembelere monga momwe tidawatembelera omwe sadalemekeze kupatulika kwa tsiku la Sabata. Ndipo lamulo la Allah ndilochitikadi

    [48] “Ndithudi Allah sangakukhululuke kuphatikizidwa (ndi chinachake), koma amakhululuka (machimo ena) osati amenewa kwa amene wamfuna. Ndipo amene angamphatikize Allah, ndithudi, wadzipekera uchimo waukulu

    [49] “Kodi sukuwaona omwe akudziyeretsa okha? Koma Allah amamuyeretsa amene wamufuna (pomulimbikitsa kuchita zabwino). Ndipo sadzaponderezedwa ngakhale ndi kachinthu kochepa konga kaulusi kokhala mkati mwakhokho la tende

    [50] “Taona, momwe akumpekera Allah bodza! Ndipo izi zikukwana kukhala tchimo loonekera

    [51] “Kodi sukuwaona omwe apatsidwa gawo la nzeru zozindikira buku (la Allah)? Amakhulupirira mafano ndi asatana, ndipo akumati kwa amene sadakhulupirire: “Awa ali panjira yoongoka kwabasi kuposa okhulupirira (Asilamu).”

    [52] “Iwo ndi omwe Allah wawatembelera. Ndipo amene Allah wamtembelera, simungathe kumpezera wompulumutsa

    [53] “Kodi ali ndi gawo la ufumu (wa Allah? Nchifukwa ninji akunyasidwa munthu wina akaninkhidwa utumiki)? Zikadatero ndiye kuti sakadawapatsa anthu ngakhale kochepa kwambiri monga khokho la tende

    [54] “Kodi akuchitira anthu dumbo pa zomwe Allah wawapatsa ndi ufulu wake? Choncho tidalipatsa banja la Ibrahim buku ndi nzeru. Ndipo tidawapatsa ufumu waukulu

    [55] “Choncho alipo ena mwa iwo amene anazikhulupirira izi, ndiponso alipo ena mwa iwo omwe adziika nazo kutali. Ndipo Jahannam ikukwanira kukhala Moto waukali wowatentha

    [56] “Ndithu amene sadakhulupirire zizindikiro Zathu, tidzawalowetsa ku Moto. Nthawi iliyonse yomwe makungu awo adzikapselera tidzidzawasinthira makungu ena kuti adzapitirize kulawa chilango. Ndithudi, Allah Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya

    [57] “Ndipo amene akhulupirira ndi kuchita zabwino, Tidzawalowetsa m’minda momwe mitsinje ikuyenda pansi (ndi patsogolo) pake. Adzakhala mmenemo muyaya. Ndipo iwo adzapeza mmenemo akazi oyeretsedwa (ku uve wamtundu uliwonse) ndi kuwalowetsa ku mithunzi yabwino kwambiri

    [58] “Ndithudi, Allah akukulamulani kubweza kwa eni zomwe mwakhulupirika nazo. Ndipo pamene mukuweruza pakati pa anthu, weruzani mwachilungamo. Ndithu malangizo amene Allah akukulangizani, ngabwino kwambiri. Ndithudi, Allah Ngwakumva, Ngoona

    [59] “E inu amene mwakhulupirira! Mumvereni Allah ndiponso mumvereni Mtumiki, ndi omwe ali ndi udindo pa inu. Ngati Mutatsutsana pa chinthu chilichonse, chibwezeni kwa Allah ndi Mtumiki Wake, ngatidi mukukhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro, kutero ndibwino; ndipo zotere zili ndi zotsatira zabwino

    [60] “Kodi sukuwaona omwe akungonena chabe kuti akhulupirira zomwe zavumbulutsidwa kwa iwe ndi zomwe zidavumbulutsidwa patsogolo pako, pomwe iwo akufuna kuti akaweruzidwe ndi maweruzo osagwirizana ndi Shariya, pomwenso alamulidwa kukana njira zotere? Koma satana akufuna kuwasokeretsa, kusokera kwakutali

    [61] “Ndipo akauzidwa: “Idzani ku zomwe Allah wavumbulutsa, ndiponso (idzani) kwa Mtumiki.” Uwaona achinyengo akudziika kutali kwabasi ndi iwe

    [62] “Kodi zingakhale bwanji litawabwerera vuto chifukwa cha zomwe manja awo adatsogoza? Kenako nkukudzera (iwe Mtumiki) uku akulumbira: “Tikulumbira Allah; sitinafune china chilichonse koma zabwino zokha ndi chimvano.”

    [63] “Iwo ndi omwe Allah akudziwa zomwe zili m’mitima mwawo. Choncho dzipatule kwa iwo, ndipo alangize ndi kuwauza mawu ogwira mtima

    [64] “Ndipo sitidamtumize mtumiki aliyense koma kuti azimveredwa mwa lamulo la Allah. Ngati akadakudzera pamene adadzichitira okha zoipa, (chifukwa chokafuna chiweruzo cha satana) napempha chikhululuko kwa Allah (naye) Mtumiki nkuwapempheranso chikhululuko, ndithudi, akadampeza Allah ali Wolandira kulapa kwawo ali Wachisoni chosatha

    [65] “Ndikulumbira (m’choonadi cha) Mbuye wako, iwo sangakhale okhulupirira moona pokhapokha akuyese muweruzi wawo pa zomwe akukangana pakati pawo. Kenako asaone vuto m’mitima yawo pa zomwe waweruza, ndipo adzipereke kwathunthu (pogonjera chiweruzo chako)

    [66] “Ndipo ngati tikadawalamula kuti: “Dzipheni nokha,” kapena: “Tulukani m’nyumba zanu; (mupite kunkhondo kapena musamuke),” sakadachita zimenezo kupatula ochepa mwa iwo. Koma akadachita zomwe auzidwa, zikadakhala zabwino kwa iwo. Ndipo zikadawalimbikitsa kwambiri (Chisilamu chawo)

    [67] “Ndipo zikadatero, tikadawapatsa malipiro aakulu ochokera kwa Ife

    [68] “Ndiponso tikadawatsogolera ku njira yoongoka (yokawafikitsa ku Munda wamtendere)

    [69] “Ndipo amene angamvere Allah ndi Mtumiki wake, iwowo ndi omwe adzakhale pamodzi ndi omwe Allah adawadalitsa, kuyambira aneneri, olungama, mashahidi (asilamu ofela ku nkhondo) ndi anthu abwino. Taonani ubwino wokhala nawo pamodzi iwowo

    [70] “Umenewo ndiubwino wochokera kwa Allah. Ndipo Allah Ngodziwa mokwanira

    [71] “E inu amene mwakhulupirira! Khalani ochenjera (ndi adani anu; musanyengedwe nawo). Pitani (kunkhondo) gulu limodzilimodzi, kapena pitaniko nonsenu pamodzi (monga momwe Mtumiki angakulangizireni)

    [72] “Ndipo ndithu alipo ena mwa inu otsalira m’mbuyo sapita ku nkhondo, (ndiponso amaletsa anzawo). Ngati vuto litakupezani, (yense wa iwo) amanena: “Allah wandichitira chisomo posakhala m’gulu lawo kumeneko.”

    [73] “Koma ngati utakupezani ubwino wochokera kwa Allah (monga kupeza chuma chambiri chosiidwa ndi adani, kapena kupambana kumene) amanena ngati kuti padalibe chikondi pakati panu ndi pakati pake: “Kalanga ine! Ndikadakhala nawo pamodzi pa nkhondo imeneyi, (ndiye kuti) ndikadapambana; kupambana kwakukulu.”

    [74] “Choncho, amenye nkhondo pa njira ya Allah omwe akugulitsa moyo (wawo) wadziko lapansi ndi tsiku lachimaliziro. Ndipo amene angamenye nkhondo pa njira ya Allah, kenako ndikuphedwa kapena kupambana tidzampatsa malipiro aakulu

    [75] “Mwatani inu osamenyana pa njira ya Allah, ndi (kuwapulumutsa) omwe ali ofooka, aamuna ndi aakazi ndi ana, omwe akunena: “Mbuye wathu! Titulutseni m’mudzi uwu omwe anthu ake ndiopondereza; ndipo tipatseni mtetezi wochokera kwa Inu; ndiponso tipatseni mthandizi wochokera kwa Inu.”

    [76] “Amene akhulupirira, akumenya nkhondo pa njira ya Allah. Koma amene sadakhulupirire, akumenya nkhondo panjira ya satana. Choncho menyanani ndi abwenzi a satana. Ndithudi, ndale za satana nzofooka

    [77] “Kodi sukuwaona omwe adauzidwa kuti: “Aletseni manja anu (kumenyana ndi osakhulupirira mpaka lidze lamulo lakumenyana)? Koma tsono pempherani Swala ndikupereka chopereka basi. Koma pamene adalamulidwa kumenyana, pompo gulu lina la iwo lidaopa anthu (osakhulupirira) ngati likuopa Allah kapena kuposerapo. Ndipo adati: “Mbuye Wathu! chifukwa ninji mwatilamula kumenyana? Ha! Mukadatichedwetsa kufikira nyengo yochepa, (zikadakhala bwino).” Nena: “Chisangalalo cha m’dziko n’chochepa. Koma tsiku lachimaliziro ndilabwino kwambiri kwa amene akuopa (Allah). Ndipo simudzaponderezedwa ngakhale pa chinthu chaching’ono monga ulusi wakhokho la tende!”

    [78] “Paliponse pamene mungakhale imfa ikupezani ngakhale mutakhala m’malinga olimba, ndipo ngati ubwino utawafika (opembedza mafano ndi achiphamaso) amati: “Ubwinowu, ukuchokera kwa Allah.” Koma choipa chikawafikira, amati: “Ichi chachitika chifukwa cha iwe (Muhammad).” Nena: “Zonse zachokera kwa Allah.” Kodi ngotani anthu awa, sangathe kuzindikira nkhani

    [79] “Chabwino chimene chakufikira (iwe munthu) ndiye kuti chachokera kwa Allah. Koma choipa chimene chakufikira ndiye kuti chachokera kwa iwe mwini (chifukwa cha zochita zako zoipa). Ndipo takutumiza (iwe Muhammad) kwa anthu kukhala Mtumiki. Ndipo Allah ndimboni yokwana

    [80] “Yemwe angamvere Mtumiki ndiye kuti wamvera Allah, (chifukwa chakuti zonse zomwe iye akulamula nzotumidwa ndi Allah). Ndipo amene atembenukire kutali (kunyoza iwe, ndiye kuti zoipa zili pa iye mwini). Sitidakutumize iweyo kukhala muyang’anili pa iwo

    [81] “Amati: “Tikumvera.” Koma akachoka kwa iwe, gulu lina la iwo limapangana usiku zosagwirizana ndi zomwe ukunena (pamaso pawo). Koma Allah akulemba zonse zomwe akupangana. Choncho apatukire ndipo yadzamira kwa Allah. Ndipo Allah wakwanira kukhala Mtetezi

    [82] “Kodi bwanji sakuilingalira Qur’an? Ndipo ikadakhala kuti siikuchokera kwa Allah, ndithudi, mmenemo akadapeza kusiyana kwambiri

    [83] “Ndipo chikawadzera chinthu chilichonse chokhuza chitetezo kapena mantha, amachifalitsa. Koma akadachibwezera kwa Mtumiki ndi kwa omwe ali ndi udindo pa iwo, akadachidziwa omwe amafufuzafufuza zinthu mwa iwo (kuti kodi nzoyenera kuzifalitsa kapena ayi). Pakadapanda ubwino wa Allah ndi chifundo chake pa inu, ndithudi, mukadamtsatira satana kupatula ochepa

    [84] “Choncho menya nkhondo pa njira ya Allah, suukukakamizidwa (za anthu ena) koma iwe mwini, ndipo akhwirizire Asilamu. Ndithu Allah angatsekereze mtopola wa omwe sadakhulupirire. Ndipo Allah Ngwaukali kwambiri pomenya nkhondo ndiponso Wolanga kwabasi

    [85] “Amene angampemphere (mnzake) pempho labwino (lothandizira pa zabwino) adzapeza gawo mmenemo. Ndipo amene angampemphelere pemphero loipa, adzapeza gawo m’zoipazo. Ndipo Allah Ngodziwa chilichonse

    [86] “Ndipo pamene mwalonjeredwa; kulonjeredwa kwamtundu uliwonse (Salam) vomerani ndi malonje abwino oposa amenewo, kapena bwezani ofanana nawo. Ndithudi, Allah Ngowerengera chinthu chilichonse

    [87] “Allah! Palibe wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye basi. Ndithudi, adzakusonkhanitsani tsiku la chiweruziro lopanda chikaiko mwa ilo. Kodi ndani ali onena zoona kuposa Allah

    [88] “Kodi mwatani inu pokhala magulu awiri pa nkhani ya achiphamaso (achinyengo) pomwe Allah wawatembenuza chifukwa cha (zoipa) zomwe achita? Kodi mukufuna kuti mumuongole amene Allah wamlekelera kusokera? Ndipo amene Allah wamulekelera kusokera, simungathe kumpezera njira (yomuikira ku chilungamo)

    [89] “Ndipo akufuna kuti mukadakhala osakhulupirira monga momwe iwo sadakhulupirire tero kuti mukhale ofanana. Musawachite kukhala abwenzi mpaka asamukire panjira ya Allah. Koma ngati anyoza, agwireni ndi kuwapha paliponse mwawapeza (monga momwe akukuchitirani inu). Ndipo musamuyese mtetezi ngakhale mthandizi aliyense wa iwo

    [90] “Kupatula omwe akugwirizana ndi anthu amene pali pangano pakati panu ndi iwo, kapena omwe akudza kwa inu uku zifuwa zawo zili zobanika kumenyana nanu, kapena kumenyana ndi anthu awo. (Oterewo musamenyane nawo). Ngati Allah akadafuna, akadawapatsa mphamvu yokugonjetserani, choncho akadakumenyani. Ngati atakupewani, osamenyana nanu ndipo nkukupatsani mtendere, ndiye kuti Allah sadakupangireni njira pa iwo (yakuti mumenyane nawo)

    [91] “Muzawapeza ena omwe akufuna kupeza chitetezo kwa inu ndi kupeza chitetezo kwa anthu awo. Nthawi iliyonse akabwezedwa ku ukafiri (ndi anzawo osakhulupirira), amagweramo mwamtheradi (nkuyamba kumenyananso ndi inu), ngati sadzipatula kwa inu ndipo osakupatsani mtendere ndi kutsekereza manja awo, agwireni ndi kuwapha paliponse pamene mwawapeza (monga momwe iwo akuchitira kwa inu) ndipo takupangirani chisonyezo choonekera pa iwo

    [92] “Ndipo sikoyenera kwa wokhulupirira kupha wokhulupilila (mnzake mwadala) pokhapokha mwangozi. Ndipo yemwe wapha wokhulupilila mwangozi, apereke ufulu kwa kapolo wa Chisilamu ndi dipo lomwe alipereke kwa ofedwawo pokhapokha akakana okha (amulowa mmalo a womwalilayo), monga m’njira ya sadaka. Ngati wophedwayo ndi mnansi wa adani anu pomwe ali wokhulupilila, perekani ufulu kwa kapolo wa Chisilamu, (palibenso dipo lina). Ngati wophedwayo ndi mmodzi wa anthu omwe pakati panu ndi iwo pali chipangano (chosamenyana nkhondo), ndiye kuti amulowammalo ake apatsidwe dipo; apatsidwenso ufulu kapolo wa Chisilamu. Ndipo ngati sadapeze (zoterozo), asale miyezi iwiri yotsatana. Iyo ndiyo njira yolapira (pa uchimo wotere) yochokera kwa Allah. Ndipo Allah Ngodziwa Ngwanzeru zakuya

    [93] “Ndipo amene angaphe wokhulupilila mwadala, mphoto yake ndi Jahannam; mmenemo adzakhala nthawi yaitali. Ndipo Allah amkwiira ndi kumtembelera ndi kumkonzera chilango chachikulu

    [94] “E inu amene mwakhulupirira! Mukayenda pa njira ya Allah, musachite chinthu pokhapokha mutaonetsetsa bwino. Ndipo musanene kwa amene akukulonjerani Salamu (kuti): “Sindiwe wokhulupirira,” (nkumupha). Mukufuna zinthu zamdziko lapansi komatu kwa Allah kuli zopeza zambiri. Umo ndi momwe inunso mudalili kale; koma Allah adakuchitirani chifundo (choncho mudalowa m’Chisilamu. Penyetsetsani bwinobwino). Ndithu Allah Ngodziwa bwinobwino nkhani zonse zimene muchita

    [95] “Sangafanane okhulupirira omwe akukhala osapita kunkhondo pomwe sali ovutika, ndi amene akumenya nkhondo yoyera pa njira ya Allah ndi chuma chawo ndi miyoyo yawo. Allah wawatukula pa ubwino ndi pa nyota amene akuchita Jihâd ndi chuma chawo ndi miyoyo yawo kuposa okhala. Koma onsewo Allah wawalonjeza zabwino. Koma wawapambanitsa ochita Jihâd malipiro aakulu kuposa ongokhala

    [96] “Adzapata nyota zazikulu zochokera kwa Iye ndi chikhululuko ndi chisoni. Ndipo Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni zedi

    [97] “Ndithudi amene angelo atenga miyoyo yawo, ali odzichitira okha zoipa (posasamuka ku Makka), adzawauza kuti: “Mudachitanji (pachipembedzo chanu?)” Iwo adzati: “Tidali ofooka ndi oponderezedwa padziko; (choncho sitidathe kuchita mapemphero athu).” (Angelo) adzati: “Kodi dziko la Allah silidali lotambasuka kotero kuti inu nkusamukira kwina m’menemo?” Iwowo malo awo ndi Jahannam. Taonani kuipa kwa malo obwerera

    [98] “Kupatula omwe adali ofooka kwenikweni amuna, akazi ndi ana omwe sangathe kuchita ndale yamtundu uliwonse, ndipo sangathe kulondola njira (yonkera ku Madina)

    [99] “Choncho iwo ndithudi Allah angawafafanizire machimo, pakuti Allah Ngofafaniza machimo, Wokhululuka

    [100] “Ndipo amene angasamuke pa njira ya Allah (chifukwa cha chipembedzo chake,) apeza malo ambiri m’dzikomo othawira ndikupeza bwino. Ndipo amene angatuluke m’nyumba mwake kuti asamuke chifukwa cha Allah ndi Mtumiki Wake, kenako nkumpeza imfa (m’njira), ndithu malipiro ake atsimikizika kwa Allah. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha

    [101] “Ndipo ngati mukuyenda pa dziko, sikulakwa kwa inu kufupikitsa Swala ngati mukuopa kuti angakusokonezeni omwe sadakhulupirire. Ndithudi, osakhulupirira ndi adani anu oonekera

    [102] “Ndipo ngati uli pamodzi (ndi Asilamu pankhondo) ndikuwatsogolera Swala, ndiye kuti gulu limodzi la iwo liimilire pamodzi ndi iwe ndikupemphera uku atagwirizira zida zawo. Ndipo akamaliza kulambira kwawo, apite kumbuyo kwanu (kuti akulondereni) ndipo lidze gulu lina lomwe silidapemphere, lipemphere nawe pamodzi; nawonso achenjere ndikugwirizira zida zawo (nkupemphera), chifukwa chakuti omwe sadakhulupirire akufuna kuti mutanyalanyaza zida zanu ndi katundu wanu angokuukirani nthawi imodzi. Koma sikulakwa kwa inu mutaika pansi zida zanu chifukwa chakuvutitsidwa ndi mvula kapena ngati mukudwala. Koma chenjeranaoni. Ndithudi Allah wawakonzera chilango choyalutsa osakhulupirira

    [103] “Mukamaliza Swala, pitirizani kumkumbukira Allah muli chiimire, chikhalire kapena mutagona chammbali. Ngati mutapeza chitetezo (chifukwa chakuti nkhondo palibe), pempherani Swala zanu mwa chilamulo. Ndithudi, Swala ndilamulo lokhala ndi nthawi kwa okhulupirira

    [104] “Ndipo musachite ulesi kutsata anthu (omwe ndi adani), ngati mukumva kupweteka, iwonso akumva kupweteka monga momwe inu mukumvera kupweteka. Koma inu mukuyembekezera kwa Allah chomwe iwo sakuyembekezera. Ndipotu Allah Ngodziwa, Ngwanzeru

    [105] “Ndithudi, takuvumbulutsira buku mwa choonadi kuti uweruzire pakati pa anthu, monga momwe Allah wakuphunzitsira. Ndipo usakhale mtetezi wa achinyengo

    [106] “Ndipo mpemphe chikhululuko Allah. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha

    [107] “Ndipo usawaikile kumbuyo omwe akudzichitira okha chinyengo. Allah sakonda yemwe ali wachinyengo, wamachimo

    [108] “Akudzibisa kwa anthu (pochita za machimo) koma sakuzibisa kwa Allah pomwe Iye adali nawo pamodzi pamene adali kupangana usiku mawu osakondweretsa. Allah akudziwa bwinobwino zimene akuchita

    [109] “Taonani! Inu ndi amene mwaayikira kumbuyo pa moyo wa pa dziko lapansi. Kodi ndani amene adzatsutsana ndi Allah pa iwo tsiku lachimaliziro, kapena ndani adzakhale mtetezi wawo

    [110] “Ndipo amene angachite choipa (povutitsa ena), kapena kudzichitira yekha zoipa, kenako nkupempha chikhululuko kwa Allah, adzampeza Allah ali Wokhululuka kwabasi, Wachisoni chosatha

    [111] “Ndipo amene angachite tchimo, ndiye kuti akudzichitira yekha. Allah Ngodziwa, Ngwanzeru zakuya

    [112] “Ndipo amene angachite cholakwa (chaching’ono) kapena tchimo (lalikulu) kenako nkumponyera nalo yemwe sadalakwe (momunamizira), ndithudi wasenza bodza lamkunkhuniza ndi uchimo woonekera

    [113] “Ndipo pakadapanda ubwino wa Allah ndi chisoni chake pa iwe, ndithudi, gulu limodzi la iwo likadalinga kukusokeretsa. Ndipo iwo palibe yemwe akadamsokeretsa koma iwo okha basi. Ndipo sangathe kukuvutitsa ndi chilichonse. Ndipo Allah wakuvumbulutsira buku, kudzanso luntha. Ndipo wakuphunzitsa zomwe sudali kuzidziwa. Ndipo ubwino wa Allah umene uli pa iwe ngwaukulu zedi

    [114] “Palibe ubwino m’zambiri zimene akunong’onezana kupatula amene akulamulira ena kupereka sadaka, kapena kuchita zabwino, kapenanso kuyanjanitsa pakati pa anthu (pakunong’onezana mawu). Amene angachite zimenezi, chifukwa chofuna chiyanjo cha Allah, tidzampatsa malipiro aakulu

    [115] “Ndipo amene anyoza Mtumiki pambuyo pomuonekera chiongoko, nkutsata njira yosakhala ya okhulupirira, timtembenuzira kumene watembenukira mwini wakeko. Ndipo tidzamulowetsa ku Jahannam. Taonani kuipa malo ofikira

    [116] “Ndithudi, Allah sakhululuka (uchimo) womphatikiza ndi chinthu china, (pochiyesa kuti ndi mnzake wa Allah). Koma Iye amakhululukira machimo ena omwe sali amenewo kwa yemwe wamfuna. Ndipo yemwe angamphatikize Allah (ndi milungu yabodza), ndithudi, wasokera kusokera konka nako kutali (ndi njira yachoonadi)

    [117] “Sapembedza Allah koma mafano achikazi, ndiponso sapembedza china koma satana wonyoza (wamachimo)

    [118] “(Yemwe) Allah adamtembelera. Ndipo iye (satana) adati (kwa Allah): “Ndithudi, ndikadzipezera gawo lodziwika mwa akapolo anu.”

    [119] ““Ndipo ndikawasokeretsa ndi kuwapatsa ziyembekezo (zabodza) ndithu ndikawalamula kuti azikadula makutu a ziweto, ndipo ndikawalamulanso kuti azikasintha chilengedwe cha Allah.” Ndipo amene angamulole satana kukhala mtetezi wake kusiya Allah, ndiye kuti wataika koonekera

    [120] “(Satana) akuwalonjeza ndikuwapatsa chiyembekezo (pa zinthu zomwe sizingachitike). Ndithudi, satana sawalonjeza china koma chinyengo basi

    [121] “Iwowo malo awo ndi ku Jahannam ndipo sadzapeza pothawira kutuluka mmenemo

    [122] “Ndipo omwe akhulupirira ndi kumachita zabwino, tidzawalowetsa ku Minda yomwe pansi (ndi patsogolo) pake mitsinje ikuyenda. Adzakhala m’menemo muyaya. Ili ndilonjezo loona la Allah. Kodi ndani woona ponena kuposa Allah

    [123] “(Kulowa ku Munda wamtendere) sikuli pa kukhumba kwanu ngakhalenso pa kukhumba kwa anthu a buku (Ayuda ndi Akhrisitu). Amene angachite choipa, adzalipidwa (nacho), ndipo sadzapeza mtetezi ngakhale mpulumutsi kupatula Allah

    [124] “Ndipo amene angachite ntchito zabwino, mwamuna kapena mkazi, pomwe iye ali wokhulupirira, iwo ndiamene adzalowa ku Munda wamtendere. Ndipo sadzaponderezedwa pa chilichonse, ngakhale chochepetsetsa kwambiri ngati kamphako ka nthangala ya tende

    [125] “Kodi ndani yemwe ali ndi chipembedzo chabwino choposa yemwe walunjika nkhope yake kwa Allah, iye ali wochita zabwino ndipo akutsata njira ya Ibrahim woona pa chikhulupiliro. Ndipo Allah adasankha Ibrahim kukhala bwenzi

    [126] “Ndipo zonse za kumwamba ndi pansi nza Allah; ndipo Allah ndi amene wazungulira chinthu chilichonse kuchidziwa

    [127] “Ndipo akukufunsa zomwe zikukhudza azimayi nena: “Allah akukuuzani nkhani za iwo ndi zomwe zikuwerengedwa kwa inu m’buku (ili) za akazi amasiye omwe simukuwapatsa (chiwongo chawo) chomwe chidalamulidwa kwa iwo, komabe mukufuna kuwakwatira, ndi za ana omwe ali ofooka ndi oponderezedwa; ndipo (akukuuzani) kuti limbikirani kuwayang’anira ana amasiye mwachilungamo. Ndipo chabwino chilichonse chimene muchita, Allah akuchidziwa

    [128] “Ndipo ngati mkazi ataona kwa mwamuna wake nkhanza ndi kumusala, palibe kulakwa pa iwo kuyanjana pakati pawo mwachimvano. Ndipo chimvano ndichabwino. (Munthu aliyense amaumilira chimene afuna) chifukwa chakuti mitima ya anthu imaumilira umbombo. Koma ngati muchita zabwino ndi kuopa Allah, ndithudi, Allah Ngodziwa nkhani zanu zonse zomwe muchita

    [129] “Ndipo inu simungathe kuchita chilungamo (chenicheni) pakati pa akazi ngakhale mutayesetsa chotani. Koma musapendekere (mbali imodzi); kupendekera kwathunthu kotero kuti nkumusiya (yemwe simukumfunayo) ngati kuti wapachikidwa (osadziwika kuti ngokwatiwa kapena ayi). Ndipo ngati mutayanjana ndi kuopa Allah (zingakhale bwino). Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni zedi

    [130] “Koma ngati atalekana, Allah angalemeretse aliyense wa iwo kuchokera m’zabwino zake zochuluka ndipo Allah ali nazo zambiri, Ngwanzeru zakuya

    [131] “Zonse za kumwamba ndi pansi nza Allah. Ndithudi, tidawalangiza omwe adapatsidwa buku patsogolo panu ndi inunso kuti muopeni Allah. Koma ngati mungakane, ndithudi, zonse za kumwamba ndi pansi nza Allah. Ndipo Allah Ngokhupuka kwabasi Wotamandidwa

    [132] “Zonse za kumwamba ndi pansi nza Allah; ndipo Allah akukwana kukhala Mtetezi (kwa anthu Ake)

    [133] “Ngati atafuna, akuchotsani, inu anthu, ndi kubweretsa ena. Ndipo Allah ali Wokhoza pazimenezo

    [134] “Amene afuna mphoto ya dziko lapansi, (afunefune kwa Allah). Kwa Allah ndikumene kuli mphoto ya pa dziko lapansi ndi ya tsiku lachimaliziro. Ndipo Allah Ngwakumva, Ngopenya

    [135] “E inu amene mwakhulupirira! Khalani oimiritsa chilungamo, opereka umboni chifukwa cha Allah; ngakhale kuti ubwere ndi masautso kwa inu, kapena kwa makolo anu, kapena kwa abale anu, ngakhale ali olemera kapena osauka, (musayang’ane zimenezo). Allah ndiye woyenera kuyang’ana za awiriwo. Choncho musatsate zilakolako ndi kusiya chilungamo. Ngati mukhotetsa (umboni), kapena kupewa (kupereka umboni) ndithudi nkhani zonse zomwe mukuchita Allah akuzidziwa

    [136] “E inu amene mwakhulupirira! Khulupirirani Allah ndi Mtumiki Wake, ndi buku lomwe analivumbulutsa pa Mtumiki Wake, ndi mabuku omwe adawavumbulutsa kale. Ndipo amene akane Allah, angelo Ake, mabuku Ake, atumiki Ake ndi tsiku lachimaliziro, ndiye kuti wasokera; kusokera konkera nako kutali

    [137] “Ndithudi, amene adakhulupirira, kenako nkusakhulupirira, nadzakhulupiriranso, kenako nkusakhulupiriranso, naonjezera kusakhulupirira, Allah sadzawakhululukira, ndipo sadzawawongolera m’njira (yabwino)

    [138] “Auze achiphamaso kuti adzapeza chilango chowawa

    [139] “Omwe amaachita osakhulupirira kukhala abwenzi awo kusiya Asilamu. Kodi akufuna kupeza ulemelero kwa iwo? Ndithudi ulemelero wonse ngwa Allah; (suli m’manja mwa anthu)

    [140] “Ndithudi Iye wakuvumbulutsirani m’buku (ili) kuti mukamva ma Ayah (ndime) a Allah akukanidwa ndi kuchitiridwa chipongwe, musakhale pamodzi nawo mpaka alowe m’zokamba zina. (Ngati mutakhala nawo) ndiye kuti mukhala chimodzimodzi ndi iwo. Ndithudi, Allah adzawasonkhanitsa achiphamaso ndi osakhulupirira onse m’moto wa Jahannam

    [141] “(A chiphamaso) omwe akukuyembekezerani (kuti mavuto akugwereni), ngati mutapeza kupambana kochokera kwa Allah, amakuuzani: “Kodi sitidali nanu limodzi?” Koma ngati osakhulupirira atapeza gawo (lopambana), amanena (kwa osakhulupirira): “Kodi Sitidayandikire kukugonjetsani pamene tidali m’gulu lankhondo la okhulupirira koma timakutsekerezani kwa okhulupirira?” Koma Allah adzaweruza pakati panu tsiku la chiweruziro. Ndipo Allah sangawaikire njira osakhulupirira pa okhulupirira (kuti awagonjetse kotheratu)

    [142] “Ndithu achiphamaso akufuna kunyenga Allah koma Iye awalanga (chifukwa cha chinyengo chawocho). Ndipo akaimilira kupemphera Swala, amaimilira mwaulesi ndikungoonetsa anthu (kuti akupemphera). Ndipo satchula Allah koma pang’ono pokha

    [143] “Akungoyendayenda pakati pa awa ndi awa (pakati pa Asilamu ndi osakhulupirira). Iwo sali mbali iyi kapena mbali inayo. Ndipo amene Allah wamlekelera kuti asokere sungampezere njira yolungama

    [144] “E inu amene mwakhulupirira! Musawachite osakhulupirira kukhala abwenzi anu kusiya okhulupirira (Asilamu), kodi mukufuna kuti Allah akhale ndi umboni woonekera pa inu (kuti ndinu oyipa)

    [145] “Ndithu achiphamaso adzakhala pansi penipeni pa Moto; ndipo sudzampeza mthandizi woimira iwo

    [146] “Kupatula amene alapa (pambuyo pa uchiphamaso wawo); nakonza (makhalidwe awo) nadziphatika kwa Allah; namuyeretseranso Allah chipembedzo chawo. Choncho iwo ali pamodzi ndi okhulupirira. Ndipo Allah adzapatsa okhulupirira malipiro akulu

    [147] “Allah sangakulangeni ngati mumthokoze ndi kumkhulupirira. Ndithudi, Allah Ngolandira kuthokoza kwanu, ndiponso Ngodziwa

    [148] “۞ Allah sakonda kutulutsa mawu ofalitsa kuipa (kwa anthu) kupatula yekhayo wachitiridwa zoipa. Ndipo Allah Ngwakumva, Ngodziwa

    [149] “Ngati mungaonetse chabwino, kapena kuchibisa, kapena kukhululukira zoipa, (zoterozo ndizo zofunika), ndithu Allah Ngokhululuka ndiponso Ngokhoza

    [150] “Ndithudi amene sakhulupirira Allah ndi atumiki Ake, ndikumafuna kulekanitsa pakati pa Allah ndi atumiki Ake, ndikumanena kuti: “Ena tikuwakhulupirira, koma ena tikuwakana,” ndikumafunanso kukhonza njira yapakati pa zimenezo

    [151] “Iwowo ndiosakhulupirira enieni. Ndipo osakhulupirira tawakonzera chilango choyalutsa

    [152] “Tsopano amene akhulupirira Allah ndi atumiki Ake, napanda kulekanitsa pakati pa aliyense wa iwo (koma nkuwakhulupirira onse), iwo adzawapatsa malipiro awo. Ndipo Allah Ngokhululuka kwambiri, Wachisoni chosatha

    [153] “Anthu amene adapatsidwa buku (Ayuda) akukupempha (iwe Mtumiki) kuti uwatsitsire buku kuchokera kumwamba. Ndithudi, adampemphanso Mûsa zazikulu kuposa zimenezi pomwe adati: “Tiwonetse Allah poyera.” Choncho udawagwira moto wamphenzi chifukwa cha kuipitsa kwao (motowo udachotsa miyoyo yawo chifukwa cha kusakhulupirira kwawo. Zitatero Allah adawapatsa moyo kachiwiri). Kenako iwo adapanga thole (mwana wang’ombe monga mulungu wawo) pambuyo powafikira chisonyezo choonekera. Koma tidawakhululukira zimenezo, ndipo tidampatsa Mûsa chisonyezo choonekera poyera

    [154] “Ndipo tidatukula phiri la Al-Tur pamwamba pawo (Ayudawo) polandira pangano lawo; tidati kwa iwo: “Lowani pachipata (cha dziko ili la Sham) mutawerama.” Tidatinso kwa iwo: “Musalumphe malire pa nkhani ya Sabata.” Ndipo tidalandira kwa iwo pangano lokhwima

    [155] “Choncho (tidawalanga) chifukwa chakuswa mapangano awo, ndi kukana kwawo zisonyezo za Allah, ndi kupha kwawo aneneri popanda choonadi, ndi kunena kwawo kwakuti: “Mitima yathu yakutidwa (siingathe kuzindikira zomwe ukunena iwe Muhammad {s.a.w}).” (Ai, Siinakutidwe ndi chilichonse), koma Allah waidinda zidindo chifukwa cha kusakhulupirira kwawo; tero sakhulupirira koma pang’ono pokha

    [156] “Chifukwanso cha kusakhulupirira kwawo ndi kumnamizira kwawo Mariya bodza lalikulu (kuti wabala Isa (Yesu) m’njira ya chiwerewere

    [157] “Ndikuyankhula kwawo (kwakuti): “Ife tamupha Mesiya Isa (Yesu) mwana wa Mariya, Mtumiki wa Allah; pomwe sadamuphe ndipo sadampachike pa mtanda. Koma adasokonezedwa (ndi munthu wina namuganizira kuti ndi Isa (Yesu). Ndithudi, amene akutsutsana pankhaniyi (Ayuda ndi Akhrisitu) ali m’chikaiko pa iyo; alibe kudziwa kotsimikizika, koma akungotsatira zongoganizira. Ndipo, sadamuphe mosimikiza (kuti ndi iye)

    [158] “Koma Allah adamkweza kwa Iye ndipo Allah Ndimwini mphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya

    [159] “Palibe aliyense mwa anthu omwe adapatsidwa buku (Ayuda ndi Akhrisitu) koma kuti azamkhulupirira iye (Yesu kuti sadali mulungu) imfa yake (Yesuyo) isadadze (izi zizachitika pamene Yesuyo azabwerenso padziko lapansi kumapeto kwa dziko). Nayenso (Yesu) pa siku la chiweruziro adzaikira umboni pa iwo (kuti iye adali chabe kapolo wa Allah)

    [160] “Chifukwa chakuchita kwawo zoipa, awo Ayuda, tidaletsa kwa iwo zinthu zabwino (zakudya) zomwe zidali zovomerezeka kwa iwo; ndiponso chifukwa cha kutsekereza kwawo anthu ambiri kuyenda panjira ya Allah

    [161] “Ndi kudya kwawo riba (katapira) pomwe adaletsedwa kuti asadye; ndiponso chifukwa chakudya kwawo chuma cha anthu mwachinyengo. Ndipo osakhulupirira mwa iwo tawakonzera chilango chopweteka

    [162] “Koma mwa iwo amene azama pa maphunziro, ndi okhulupirira (onsewo) akukhulupirira zimene zavumbulutsidwa kwa iwe ndi zimene zidavumbulutsidwa patsogolo pako. Ndipo omwe akupitiriza kupemphera Swala, ndi kupereka Zakaati, ndi kukhulupirira Allah komanso tsiku lachimaliziro, iwo tidzawapatsa malipiro aakulu

    [163] “Ndithudi, takuvumbulutsira (chivumbulutso) monga momwe tidamuvumbulutsira Nuh (Nowa) ndi aneneri amene anadza pambuyo pake. Ndipo tidamuvumbulutsiranso Ibrahim, Ismail, Ishâq, Ya’qub ndi mbumba yake. Ndipo (tidamuvumbulutsiranso) Isa (Yesu), Ayyub (Yobu), Yunus (Yona), Haarun (Aroni) ndi Sulaiman, ndipo Daud tidampatsa Zabur (Masalimo)

    [164] “Ndipo (tidavumbulutsanso chivumbulutso) kwa atumiki omwe takusimbira kale nkhani zawo komanso kwa atumiki ena omwe sitinakusimbire (nkhani zawo); ndipo Allah adayankhula ndi Mûsa mwachindunji

    [165] “(Iwo ndi) atumiki omwe adauza nkhani zabwino (kwa anthu abwino) ndi kuwachenjeza (oipa) kuti anthu asadzakhale ndi mtsutso pa Allah pambuyo pa (kudza kwa) atumikiwa. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya

    [166] “Koma Allah akuikira umboni zimene wakuvumbulutsira kuti (nzoona), adavumbulutsa mwanzeru Zake. Nawonso angelo akuikira umboni. Ndipo Allah akukwana kukhala mboni

    [167] “Ndithu amene sadakhulupirire, nawatsekereza (anthu) kuyenda pa njira ya Allah, ndithudi asokera; kusokera kwakukulu

    [168] “Ndithudi, amene sadakhulupirire, namachita zoipa, sali Allah owakhululukira iwowo ndi kuwaongolera njira

    [169] “Kupatula njira yomka ku Jahannam, mmenemo akakhala muyaya. Ndipo zimenezo nzopepuka kwa Allah

    [170] “E inu anthu! Ndithu Mtumiki wakudzerani ndi choonadi chochokera kwa Mbuye wanu. Choncho khulupirirani; ndi bwino kwa inu kutero. Koma ngati mukana, (dziwani kuti) zonse zakumwamba ndi zapansi nza Allah. Ndipo Allah Ngodziwa kwambiri Ngwanzeru zakuya

    [171] “E inu anthu a buku! Musamalumphe malire pa chipembedzo chanu. Ndipo musamamnenere Allah koma zowona (zokhazokha). Ndithu Mesiya Isa (Yesu) mwana wa Mariya, ndi mtumiki wa Allah (ndiponso ndi munthu wolengedwa) ndi liwu Lake lomwe adaliyika mwa Mariya ndiponso (ali) ndi mzimu (moyo) wochokera kwa Iye (Allah, monga mizimu ina yonse imachokera kwa Iye). Choncho Khulupirirani Allah ndi atumiki Ake. Musamanene: “Utatu wa Mulungu;” siyani, (zikhululupiliro za utatu wa Mulungu), kutero ndibwino kwa inu. Ndithudi, Allah ndi Mulungu m’modzi (basi). Ulemelero wake ngotukuka kutali ndi kukhala ndi mwana. Nzake zonse za kumwamba ndi pansi. Ndipo Allah ndiMtetezi Wokwanira

    [172] “Mesiya (Mneneri Isa {Yesu}) sangaone kunyozeka kukhala kapolo wa Allah, ngakhalenso angelo oyandikitsidwa (kwa Allah). Ndipo amene angaone kunyozeka pa ukapolo wake kwa Allah nadzitukumula, onse adzawasonkhanitsa kwa Iye (ndipo kenako nkuwalonga kung’anjo ya Moto)

    [173] “Koma amene adamkhulupirira (Yesuyo) ndi kuchita zabwino adzawapatsa malipiro ao mokwanira ndi kuwaonjezera mu zabwino Zake. Koma amene adaona kunyozeka (pokhala kapolo wa Allah) nadzitukumula, adzawalanga chilango chowawa; ndipo sadzapeza bwenzi ngakhale mtetezi kupatula Allah

    [174] “E inu anthu! Ndithudi, wakudzerani umboni wochokera kwa Mbuye wanu. Ndipo takuvumbulutsirani kuunika koonekera poyera

    [175] “Tsono amene akhulupirira Allah ndi kudziphatika kwa Iye, iwo adzawalowetsa ku chifundo ndi kuzabwino zochokera kwa Iye, ndikuwatsogolera kwa Iye njira yoongoka

    [176] “Akukufunsa (iwe Mneneri, za malamulo a chuma cha munthu yemwe wafa osasiya mwana kapena kholo). Nena: “Allah akukulamulani pa zayemwe sadasiye mwana ndi kholo (kuti) ngati munthu atamwalira pomwe alibe mwana, koma ali ndi mlongo wake (wa bambo amodzi), choncho (mlongo wakeyo) alandire theka (½) la zomwe wasiya (womwalirayo). Nayenso angalandire chuma (chamlongo wake) ngati alibe mwana. Ndipo ngati iwo ali (alongo) awiri, ndiye kuti adzalandira magawo awiri mmagawo atatu (/3) a zomwe wasiya. Ndipo ngati ali abale (angapo) amuna ndi akazi, ndiye kuti mwamuna aliyense alandire gawo lolingana ndi la akazi awiri. Umo ndi momwe Allah akukufotokozerani (malamulo Ake) mwatsatanetsatane kuti musasokere. Ndipo Allah Ngodziwa chilichonse

    Gome lokhala ndi chakudya

    Surah 5

    [1] “E inu amene mwakhulupirira! Kwaniritsani mapangano onse (omwe ali pakati panu ndi anthu anzanu). Kwalolezedwa kwa inu (kudya nyama ya) ziweto (monga ngamira, ng’ombe ndi mbuzi), kupatula chomwe mukuuzidwa (kuti ncholetsedwa). Koma nkosaloledwa kwa inu kuchita ulenje mutalowa m’mapemphero a Hajj, (kapena muli m’nthaka yopatulika ya ku Makka). Ndithudi, Allah akulamula chimene wafuna

    [2] “E inu amene mwakhulupirira! Musanyozere kupatulika kwa zizindikiro za Allah (pochiyesa chosapatulika chomwe Allah wachichita kukhala chopatulika; monga kutuluka m’mapemphero a Hajj usadakwaniritse), kapenanso (kunyozera) kupatulika kwa mwezi wopatulika (poyambitsa nkhondo mmenemo), kapena (kupatulika kwa nyama zomwe zatumizidwa ku Makka monga) nsembe, kapena (kuchotsa kupatulika kwa) makoza (omwe nyamazo zimavekedwa monga chizindikiro chosonyeza kuti ndinsembe ya ku Makka), kapena (kupatulika kwa) omwe akulinga kupita kunyumba yopatulika (ku Makka), (omwe akupita kumeneko) ndi cholinga chofunafuna ubwino wa Mbuye wawo ndi chiyanjo Chake. Ndipo ngati mutatuluka m’mapemphero anu a Hajj mukhoza kuchita ulenje (ngati mutafuna); ndipo kusakuchititseni kuwada anthu chifukwa chakuti adakutsekerezani kufika ku Msikiti Wopatulika (wa ku Makka) kuti mulumphe malire (pobwezera mtopola umene adakuchitirani). Koma thandizanani pa zabwino ndikuopa (Allah); musathandizane pa machimo ndi pa chidani. Ndipo muopeni Allah. Ndithu Allah Ngwaukali pokhaulitsa

    [3] “Kwaletsedwa kwa inu (kudya) chakufa chokha, liwende, nyama ya nkhumba, chomwe chazingidwa m’dzina osati la Allah, chomwe chafa ndi kubanika, chomwe chafa ndi kumenyedwa, ndi chimene chafa pakugwa kuchokera pamwamba, chimene chafa polasidwa ndi nyanga (yachinzake), chomwe chafa pakujiwa ndi chilombo (cha m’thengo) kupatula chomwe mwachipeza chili rnoyobe nkuchizinga ndi chimene chazingidwa paguwa la mafano; ndiponso (nkoletsedwa kwa inu) kufuna kudziwa zobisika pochita maula. Zonsezi ndi uchimo. Lero amene sadakhulupirire ataya mtima (za kugonjetsa) chipembedzo chanu. Choncho musawaope, koma opani Ine. Lero ndakukwaniritsirani chipembedzo chanu ndipo ndakwaniritsa pa inu chisomo changa. Ndakusankhirani Chisilamu kukhala chipembedzo chanu. Koma amene wasimidwa chifukwa chanjala, popanda kupendekera kumachimo, (nkudya zoletsedwazi, palibe kanthu). Ndithu Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha

    [4] “Akukufunsa (Asilamu) chomwe chaloledwa kwa iwo (kudya). Nena: “Chaloledwa kwa inu chilichonse chabwino. Ndi (chimene chagwidwa ndi) nyama kapena mbalame zaukali zomwe mwaziphunzitsa kusaka. Muziphunzitse zimene Allah wakuphunzitsani. Choncho idyani chimene zakugwilirani, ndipo chitchulireni dzina la Allah pochikhwirizira. Ndipo opani Allah. Ndithudi Allah Ngwachangu pakuwerengera

    [5] “Lero mwaloledwa zonse zabwino ndi chakudya cha omwe adapatsidwa buku nchololedwa kwa inu, ndiponso chakudya chanu nchololedwa kwa iwo, ndipo (mukuloledwa kuwakwatira) akazi abwino a mwa okhulupirira ndi akazi abwino a mwa omwe adapatsidwa ma buku kale, ngati mwawapatsa chiwongo chawo m’njira yomanga nawo ukwati, osati mochita nao chiwerewere, osatinso mochita nao zibwenzi. Ndipo amene akane kukhulupirira, ndiye kuti yaonongeka ntchito yake; ndipo iye tsiku lachimaliziro adzakhala mwa oluza (otaiyika)

    [6] ““E inu amene mwakhulupirira! Pamene mwaimilira kuti mukaswali, sambitsani nkhope zanu, ndi manja anu mpaka mmagongono; ndipo pakani madzi pa mitu panu ndi kusambitsa mapazi anu mpaka mu akakolo. Ngati muli ndi janaba dziyeretseni (sambani thupi lonse); ndipo ngati muli odwala kapena muli paulendo, kapena mmodzi wanu wachokera kokadzithandiza kapenanso mwakhalira limodzi ndi mkazi, ndiye simudapeze madzi, chitani Tayammamu ndi dothi labwino ndipo pakani ku nkhope zanu ndi mmanja mwanu. Allah sakufuna kukuvutitsani, koma akufuna kukuyeretsani ndi kukwaniritsa chisomo chake pa inu kuti muthokoze

    [7] “Ndipo kumbukirani chisomo cha Allah pa inu ndi pangano lake lomwe mudapangana Naye, pamene mudati: “Tamva, ndipo tamvera.” Muopeni Allah. Ndithudi Allah Ngodziwa za m’mitima

    [8] “E inu amene mwakhulupirira! Khalani olungama kwa Allah, opereka umboni mwachilungamo, ndipo chidani cha anthu pa inu chisakuchititseni kuti musachite chilungamo. Chitani chilungamo; kutero kumakuyandikitsani ku “taquwa” (kuopa Allah). Ndipo opani Allah. Ndithudi, Allah Ngodziwa nkhani zonse za (zinthu) zomwe muchita

    [9] “Allah walonjeza omwe akhulupirira ndi kuchita zabwino kuti adzapeza chikhululuko ndi malipiro aakulu

    [10] “Ndipo amene sadakhulupirire, natsutsa zizindikiro Zathu, iwo ndi anthu a ku Moto

    [11] “E inu amene mwakhulupirira! Kumbukirani mtendere wa Allah omwe uli pa inu, pamene anthu ena adatsimikiza kukutambasulirani manja awo (pofuna kuchita nanu nkhondo) koma (Allah) adawatsekereza manja awo kukufikani inu. Choncho opani Allah. Ndipo kwa Allah Yekha, ayadzamire okhulupirira

    [12] “Ndipo ndithudi, Allah adamanga pangano ndi ana a Israyeli, ndipo tidawaikira Akuluakulu khumi ndi awiri mwa iwo. Ndipo Allah adati: “Ndithudi Ine ndili pamodzi ndi inu, ngati mupemphera Swala ndikupereka chopereka, ndikukhulupirira atumiki Anga, ndi kuwalemekeza ndi kumkongoza Allah Ngongole yabwino, ndithudi ndikufafanizirani zoipa zanu, ndikudzakulowetsani m’Minda yomwe pansi (ndi patsogolo) pake pakuyenda mitsinje. Koma amene akane mwa inu pambuyo pa (chipangano) ichi, ndithu wasochera njira yowongoka.”

    [13] “Choncho chifukwa chakuswa pangano lawo, tidawatembelera; ndipo tidaumitsa mitima yawo. Ankasintha mawu (a Allah omwe adali m’mabuku a Taurat ndi Injili) kuwachotsa m’malo mwake ndipo adasiya kukwaniritsa gawo lalikulu la zomwe adakumbutsidwa. Ndipo ukhala ukuona (iwe Mtumiki {s.a.w}) chinyengo mwa ambiri a iwo, kupatula ochepa a iwo. Choncho akhululukire ndi kuwaleka. Ndithudi, Allah amakonda ochita zabwino

    [14] “Naonso aja amene akuti: “Ife ndife Akhrisitu,” tidalandira pangano lawo koma adasiya gawo lalikulu la zomwe adakumbutsidwa. Tero tidabzala pakati pawo chidani ndi kusakondana mpaka tsiku lachimaliziro. Ndipo Allah adzawawuza zimene adali kuchita

    [15] “E inu anthu a buku! Ndithudi wakufikani Mtumiki Wathu yemwe akukufotokozerani poyera zambiri zomwe munkabisa za m’buku. Koma akusiya zambiri (posazilongosola). Ndithudi kwakudzerani kuunika kochokera kwa Allah ndi buku lomwe likufotokoza mwatchutchutchu (chinthu chilichonse)

    [16] “Ndi bukulo Allah akuwatsogolera kunjira zamtendere amene akutsata chiyanjano chake ndikuwatulutsa mu m’dima ndi kuwaika m’kuunika mwa lamulo Lake, ndi kuwatsogolera kunjira yoongoka

    [17] “Ndithudi, amukana (Allah) amene akunena kuti Mulungu ndiye Mesiya Mwana wa Mariya. Nena: “Ndani akadatha kuletsa chilichonse kwa Allah ngati Iye akadafuna kuononga Mesiya mwana wa Mariya ndi mayi wakeyo, ndi onse omwe ali m’dziko lapansi? Ndipo ufumu wa kumwamba ndi pansi ndi zapakati pake ngwa Allah. Amalenga chimene wafuna. Ndipo Allah Ngokhoza chilichonse.”

    [18] “Ndipo Ayuda ndi Akhrisitu akunena: “Ife ndife ana a Mulungu ndiponso okondeka ake.” Nena: (Iwe Mtumiki) “Nchifukwa ninji Allah amakukhaulitsani kamba ka machimo anu? Koma inu ndinu anthu chabe mwa omwe adawalenga. Amamkhululukira amene wamfuna; ndipo amamulanga amene wamfuna. Ufumu wa kumwamba ndi pansi ndi za pakati pake ngwa Allah. Ndipo kwa Iye nkobwerera.”

    [19] “E inu anthu a buku! Ndithudi, wakudzerani Mtumiki Wathu yemwe akukufotokozerani inu, pa nthawi yopanda atumiki, kuti musadzanene kuti: “Sadadze kwa ife wonena nkhani zabwino ndiwochenjeza.” Choncho wakudzeranidi wonena nkhani zabwino ndi wochenjeza. Ndipo Allah Ngokhoza chilichonse

    [20] “(Ndipo kumbukirani) pamene Mûsa adauza anthu ake: “Inu anthu anga! Kumbukirani mtendere wa Allah umene uli pa inu, pamene adawachita ena mwa inu kukhala aneneri; ndipo adakuchitani kukhala mafumu (pambuyo poti mudali onyozeka m’dziko la Iguputo m’manja mwa Farawo). Ndipo wakupatsani zomwe sadampatsepo aliyense mwa zolengedwa.”

    [21] ““Inu anthu anga. Lowani m’dziko loyeretsedwalo limene Allah adakulemberani, ndipo musabwelere m’mbuyo kuti mungasanduke otaika.”

    [22] “(Iwo) adati: “Iwe Mûsa, ndithudi mmenemo muli anthu amphamvu. Ndipo ife sitikalowamo kufikira atatulukamo okha. Choncho ngati atatulukamo, pamenepo ndiye tikalowa.”

    [23] “Anthu awiri mwa amene ankaopa Allah, omwe awiriwo Allah adawapatsa chisomo, adati (kwa anzawo): “Alowereni pa chipata (cha dzikolo). Ngati mukalowamo ndithudi, inu mukapambana. Ndipo kwa Allah Yekha yadzamirani ngati inu mulidi okhulupirira.”

    [24] “(Iwo) adati: “Iwe Mûsa, ife sitikalowamo mpang’ono pomwe, pomwe iwo ali momwemo. Choncho pita iwe ndi Mbuye wako, ukamenyane nawo; ife tikhala pompano.”

    [25] “(Mûsa) adati: “E Mbuye wanga! Ndithudi, ine ndilibe nyonga (yokakamizira aliyense kutsatira lamulo Lanu) koma pa ine ndekha ndi pa m’bale wanga. Choncho tisiyanitseni ndi anthu awa opandukira chilamulo.”

    [26] “Allah adati: “Choncho laletsedwa dzikolo kwa iwo kulilowa kwa zaka makumi anayi. Akhala akuyendayenda pa dziko. Tero, usawadandaulire anthu opandukira chilamulo.”

    [27] “Ndipo awerengere nkhani mwachoonadi ya ana awiri a Adam, pamene adapereka nsembe. Ndipo idalandiridwa ya mmodzi wawo, koma ya winayo siidalandiridwe. (Amene nsembe yake siidalandiridwe) adati (kwa mnzake): “Ndithudi ndikupha.” Mnzakeyo adati: “Ndithudi, Allah amalandira nsembe ya amene akuopa (Allah).”

    [28] ““Ngati utambasula dzanja lako pa ine kuti undiphe, ine sinditambasula dzanja langa pa iwe kuti ndikuphe. Ndithudi, ine ndikuopa Allah Mbuye wa zolengedwa.”

    [29] ““Ine ndikufuna kuti usenze machimo anga pamodzi ndi machimo ako, choncho ukakhale m’gulu la anthu a ku Moto. Ndipo awo ndio malipiro a anthu ochita zoipa.”

    [30] “Choncho mtima wake udamkometsera kupha m’bale wake, ndipo adamuphadi. Tero adali wotaika

    [31] “Pamenepo Allah adatumiza khwangwala yemwe amafukula pansi kuti amusonyeze mmene angakwililire mtembo wa m’bale wake. (Wopha mnzake) adati: “Kalanga ine! Ndalephera kuti ndifanane ndi khwangwala uyu, kuti ndikwilire mtembo wa m’bale wanga.” Choncho adali mmodzi mwa odzinena

    [32] “Pachifukwa chazimenezo, tidawalamula ana a Israyeli kuti amene wapha munthu popanda iye (wophedwayo) kupha munthu, kapena kuchita chisokonezo pa dziko, ali ngati wapha anthu onse. Ndipo amene wamuleka munthu ali ndi moyo, ali ngati awapatsa moyo anthu onse. Ndithudi, atumiki Athu adawadzera iwo ndi zisonyezo zoonekera. Koma ndithu ambiri a iwo, pambuyo pa zimenezo, adapitirizabe kuononga pa dziko

    [33] “Ndithu mphoto ya amene akulimbana ndi Allah ndi Mtumiki Wake (pochita zomwe waletsa) ndi kudzetsa chionongeko pa dziko, aphedwe kapena apachikidwe pa mtanda, kapena adulidwe manja awo ndi miyendo yawo mosemphanitsa (dzanja lakumanja ndi phazi lakumanzere, ndipo dzanja lakumanzere ndi phazi lakumanja); kapena apirikitsidwe mdzikomo. Uku ndikuyaluka kwawo pa dziko lapansi. Ndipo iwo pa tsiku lachimaliziro adzalandira chilango chachikulu

    [34] “Kupatula amene alapa musanawagwire. Ndipo dziwani kuti Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha

    [35] “E inu amene mwakhulupirira! Muopeni Allah ndipo funafunani njira zokufikitsani kwa Iye. Menyani nkhondo pa njira yake kuti mupambane

    [36] “Ndithudi, aja amene sadakhulupirire, akadakhala ndi zonse za m’dziko ndi zina zonga izo kuti azipereke monga dipo kuti apulumuke kuchilango cha tsiku lachimaliziro (Qiyâma) sizikadavomerezedwa kwa iwo. Ndipo iwo adzapeza chilango chopweteka

    [37] “Adzafuna (mwanjira iliyonse) kuti atuluke ku Moto, koma sadzatulukamo. Ndipo adzakhala ndi chilango chamuyaya

    [38] “Ndipo wakuba wamwamuna ndi wakuba wamkazi, aduleni manja awo; kukhala mphoto ya zomwe achita ndi chilango chochokera kwa Allah. Allah Ngwanyonga zoposa, Ngwanzeru zakuya

    [39] “Koma amene walapa pambuyo pakuchita kwake zoipa, namachita zabwino, Allah alandira kulapa kwake. Ndithudi, Allah Ngokhululuka kwabasi Ngwachisoni chosatha

    [40] “Kodi sukudziwa kuti Allah Ngwake ufumu wa kumwamba ndi pansi? amamulanga yemwe wamfuna (akalakwa), ndipo amamukhululukira amene wamfuna. Ndipo Allah Ngokhoza chilichonse

    [41] “E iwe Mtumiki! Asakudandaulitse amene akuchita changu kukana Allah mwa omwe akunena ndi pakamwa pawo chabe: “Takhulupirira,” pomwe mitima yawo siikukhulupirira. Namonso mwa Ayuda, alipo amene amamvetsera (zimene ukunena) kuti azikanena bodza, amamvetsera mmalo mwa anthu ena amene sadadze kwa iwe (omwe ndi akuluakulu awo), amasintha mawu (a m’buku la Taurat) m’malo mwake, omwenso amanena (kuuza otsatira awo kuti): “Ngati mukapatsidwe (ndi Muhammad {s.a.w}) izi (takuuzanizi), kalandireni, koma ngati musakapatsidwe zimenezi kachenjereni.” Ndipo munthu yemwe Allah akufuna kuti amuyese mayeso sungathe kumpezera chilichonse kwa Allah. Iwowo ndiomwe Allah sadafune kuyeretsa mitima yawo. Apeza kuyaluka pa dziko lapansi. Ndipo tsiku lachimaliziro adzapeza chilango chachikulu

    [42] “Okonda kumvetsera zabodza; osaopa pakudya (zinthu) zoletsedwa (zaharamu). Choncho akakudzera aweruze pakati pawo, kapena uwapatukire. Ndipo ngati uwapatukira, palibe chomwe angakuvutitse nacho. Ngati uweruza pakati pawo weruza mwachilungamo. Ndithudi, Allah amakonda olungama

    [43] “Kodi angakuyese muweruzi chotani pomwe iwo alinayo Taurat momwe muli chiweruzo cha Allah. Pambuyo powaweruza akutembenuka (monyoza)! Ndipo iwo sali okhulupirira

    [44] “Ndithudi, tidaivumbulutsa Taurat yokhala ndi chiongoko ndi kuunika; aneneri (a Allah) omwe adagonjera (Allah), adali kulamulira nayo Ayuda, ndiponso Arabbaniyyuna (aphunzitsi a malamulo) ndi Ahabaru (Ansembe) omwe adapemphedwa kusunga buku la Allah ndipo iwo adali mboni pa ilo, choncho (inu Asilamu) musaope anthu, koma opani Ine. Ndipo musasinthanitse Ayah (ndime) zanga ndi (zinthu za) mtengo wochepa. Ndipo amene sakuweruza ndi chimene Allah wavumbulutsa, iwowo ndiwo osakhulupirira (okana Allah)

    [45] “Ndipo m’menemo (m’buku la Taurat) tidawalamula kuti: “Munthu aphedwe chifukwa chopha mnzake, ndi kuti diso kwa diso, mphuno kwa mphuno; khutu kwa khutu; dzino kwa dzino, ndiponso kubwezerana mabala.” Koma amene wakhululuka ndiye kuti dipo likhala kwa iye. Ndipo amene saweruza ndi chimene Allah wavumbulutsa iwowo ndiwo anthu ochita zoipa

    [46] “Ndipo tidatsatiza pa mapazi a aneneriwo, Isa (Yesu) mwana wa Mariya kudzatsimikizira zomwe zidali patsogolo pake m’buku la Taurat. Ndipo tidampatsa Injili yomwe m’kati mwake muli chiongoko ndi kuunika; ndikutsimikizira zomwe zidali patsogolo pake za m’buku la Taurat. Ndipo ndi chiongoko ndi ulaliki wabwino kwa oopa (Allah)

    [47] “Anthu abuku la Injili alamulire potsatira zimene Allah adavumbulutsa mmenemo. Ndipo amene asiya kulamulira ndi zomwe Allah wavumbulutsa iwo ndiwo opandukira malamulo (a Allah)

    [48] “Ndipo takuvumbulutsira buku mwa choonadi, lomwe likuikira umboni mabuku omwe adalipo patsogolo pake, ndi kuwateteza, (monga ponena kuti: “Lamulo ili ndiloona; ili iyayi.”) Choncho weruza pakati pawo ndi zomwe Allah wavumbulutsa, ndipo usatsate zofuna zawo kusiya choona chomwe chakufika. Ndipo m’badwo uliwonse mwa inu tidaupangira shariya (malamulo) yake ndi njira yake. Allah akadafuna, akadakuikani kukhala mpingo umodzi (wotsata chilamulo chofanana). Koma akufuna kukuyesani pa zomwe wakupatsani. Choncho pikisanani pa zinthu zabwino. Inu nonse kobwerera kwanu nkwa Allah. Naye adzakuuzani (nonsenu) mu zomwe mudali kusiyana

    [49] “Weruza pakati pawo ndi chimene Allah wavumbulutsa, ndipo usatsate zofuna zawo, koma chenjera nawo kuti angakusokoneze nkusiya zina mwa zimene Allah wavumbulutsa kwa iwe. Ndipo ngati anyozera dziwa kuti Allah afuna kuwapatsa chilango cha ena mwa machimo awo. Ndithudi, anthu ambiri ngopandukira (malamulo a Allah)

    [50] “Kodi iwo akufuna chiweruzo cha nthawi yaumbuli (chamasiku aumbuli, Chisilamu chisanadze)? Kodi ndani ali wabwino poweruza kuposa Allah kwa anthu otsimikiza (kuti Allah alipo)

    [51] “E inu amene mwakhulupirira! Ayuda ndi Akhrisitu musawapale ubwenzi (nkumawauza chinsinsi chanu). Iwo pakati pawo ndi abwenzi ndi atetezi kwa wina ndi mnzake. Amene awapale ubwenzi mwa inu, ndiye kuti iye ndi m’modzi wa iwo. Ndithudi, Allah satsogolera anthu ochita zoipa

    [52] “Uwaona omwe m’mitima mwawo muli matenda (a chinyengo) akuthamangira kwa iwo (Ayuda) uku akuti: “Tikuopa lingatigwere tsoka (ngati Asilamuwa atagwa m’tsoka), koma posachedwapa Allah abweretsa lamulo logonjetsa (midzi), kapena chinthu china chochokera kwa Iye (monga kuwaulula achinyengo zomwe akubisa m’mitima mwawo). Choncho adzasanduka odzinena chifukwa cha zomwe adabisa m’mitima mwawo

    [53] “Ndipo amene adakhulupirira nayamba kunena (chitaululika chinyengo cha achinyengowo): “Kodi awa si omwe adali kulumbilira dzina la Allah m’kulumbilira kwawo kwamphamvu kuti iwo ali pamodzi ndi inu?” Zochita zawo zaonongeka. Tero akhala otaika

    [54] “E inu amene mwakhulupirira! Amene mwa inu asiye chipembedzo chake, ndiye kuti posachedwapa Allah abweretsa anthu omwe awakonda, nawonso amkonda; odzichepetsa kwa okhulupirira (anzawo); amphamvu kwa osakhulupirira; omenyera nkhondo chipembedzo cha Allah, saopa kudzudzula kwa odzudzula. Umenewu ndi ubwino wa Allah; amaupereka kwa amene wamfuna. Ndipo Allah ndi Mataya; Ngodziwa kwambiri

    [55] “Ndithu mtetezi wanu ndi Allah ndi Mtumiki wake ndi omwe akhulupirira omwe akupemphera Swala ndi kupereka Zakaat uku ali odzichepetsa

    [56] “Ndipo amene achite Allah ndi Mtumiki Wake, ndi omwe akhulupirira kukhala atetezi ake, (ndithu iwo ndi a chipani cha Allah). Ndithu chipani cha Allah ndicho chopambana

    [57] “E inu amene mwakhulupirira! Musapalane nawo ubwenzi omwe akuchichitira chipongwe ndi masewera Chipembedzo chanu mwa omwe apatsidwa mabuku patsogolo panu, ndiponso mwa osakhulupirira, ndipo opani Allah ngati inu mulidi okhulupirira

    [58] “Mukaitanira kokapemphera Swala (mukachita azana) akuichitira chipongwe ndi masewera; ndithudi zimenezo nchifukwa chakuti iwo ndianthu opanda nzeru

    [59] “Nena: “E inu anthu a buku! Kodi mukuona cholakwika kwa ife kaamba kakuti takhulupirira Allah ndi zomwe zavumbulutsidwa kwa ife ndi zomwenso zidavumbulutsidwa kale? Ndithudi, ambiri mwa inu ndi opandukira chilamulo (cha Allah).”

    [60] “Nena: “Kodi ndikuuzeni za uja amene ali ndi malipiro oipa kwa Allah kuposa izi? Ndiomwe Allah wawatembelera ndi kuwakwiira ndi kuwasandutsa ena kukhala anyani ndi nkhumba, ndi opembeza satana. Awo ndiwo okhala ndi malo oipa, ndiponso osokera njira yowongoka.”

    [61] “Ndipo (achinyengo) akakudzerani, akunena: “Takhulupirira,” pamene alowa kwa inu ali osakhulupirira ndipo atulukanso ali osakhulupirira. Koma Allah Ngodziwa kwambiri zomwe akhala akubisa

    [62] “Uwaona ambiri a iwo akuthamangira machimo ndi mtopola ndi kudya zoletsedwa. Ndithudi, zimene akhala akuchitazo ndizoipa zedi

    [63] “Bwanji odziwa za malamulo ndi akuluakulu a chipembedzo sadawaletse zoyankhula za uchimo ndi kudya kwawo zinthu zoletsedwa? Ndithudi, zomwe akhala akuchitazo ndi zoipa zedi

    [64] “Ndipo Ayuda adati: “Dzanja la Allah lafumbatika (sitikupeza chuma ngati kale). (Koma sichoncho); manja awo ndiwo afumbatika (posachita zabwino ndi kuchenjelera anthu). Ndipo atembeleredwa chifukwa cha zomwe anena. Koma manja ake (Allah) ngotambasuka. Amapatsa mmene wafunira. Ndithudi, zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako, ziwaonjezera ambiri a iwo (Ayuda) kulumpha malire ndi kusakhulupirira. Ndipo taika chidani ndi kusakondana pakati pawo mpaka tsiku la chimariziro. Nthawi iliyonse akayatsa moto wa nkhondo, Allah amauzimitsa. Ndipo amayesetsa kudzetsa chisokonezo pa dziko, (koma Allah sawathandiza). Ndipo Allah sakonda owononga

    [65] “Ndipo kukadakhala kuti awa anthu a buku adakhulupirira ndi kumuopa Allah, tikadawafafanizira zolakwa zawo, ndi kuwalowetsa m’minda ya mtendere

    [66] “Akadakhala kuti iwo adaigwiritsa ntchito Taurat ndi Injili, ndi zomwe zidavumbulutsidwa kwa iwo kuchokera kwa Mbuye wawo (monga Qurani), ndithudi akanadya za kumwamba ndi za pansi pa myendo yawo. Mwa iwo alipo amene akutsatira njira yabwino. Komanso ambiri mwa iwo nzoipa zedi zomwe akuchita

    [67] “E iwe Mtumiki! Fikitsa (kwa anthu) zomwe zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako. Ngati suchita, ndiye kuti sudafikitse uthenga Wake. Ndipo Allah akuteteza kwa anthu; (usaope aliyense). Ndithudi, Allah satsogolera anthu osakhulupirira

    [68] “Nena: “E inu anthu a buku! Simuli kanthu (pa chipembedzo chanu) mpaka muimilire (kutsatira malamulo) a Taurat ndi Injili ndi zomwe zavumbulutsidwa kwa inu kuchokera kwa Mbuye wanu, ziwaonjezera kulakwa ndi kusakhulupirira ambiri a iwo zomwe zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako, choncho usadandaule za anthu osakhulupirira

    [69] “Ndithudi, amene akhulupirira ndi amene ali m’chipembedzo cha Chiyuda, ndi Asabayi, ndi Akhrisitu, - amene akhulupirire Allah ndi tsiku lachimaliziro, (monga momwe akulangizira Mtumiki Muhammad {s.a.w}) nachita zabwino, - palibe mantha kwa iwo ndiponso sadzadandaula

    [70] “Ndithudi, tidalandira pangano kwa ana a Israyeli (kuti adzamvera Allah) ndipo tidawatumizira atumiki. Nthawi iliyonse akawadzera mtumiki ndi chomwe mitima yawo siinkafuna, adawatsutsa ena (mwa atumikiwo), ndipo ena ankawapha kumene

    [71] “Ndipo ankaganiza kuti sipapezeka chilango; tero adali akhungu ndi agonthi. Kenako Allah adawalandira kulapa kwawo (pamene adalapa). Komabe ambiri a iwo adali akhungu, ndi ogontha. Ndipo Allah akuona zimene akuchita

    [72] “Ndithudi am’kana Allah amene anena kuti, Mulungu ndiye Isa (Yesu) mwana wa Mariya.” Pomwe Mesiya adati: “Inu ana a Israyeli! Pembedzani Allah Yemwe ndi Mbuye wanga ndiponso Mbuye wanu.” Ndithudi, amene aphatikize Allah ndi chinthu china, ndithudi Allah waletsa kwa iye kukalowa ku Munda wamtendere, ndipo malo ake ndi ku Moto. Ndipo anthu ochita zoipa sadzakhala ndi athandizi

    [73] “Ndithudi, am’kana Allah amene amanena kuti “Ndithu Allah ndi mmodzi mwa (milungu) itatu,” pomwe palibe mulungu wina koma Mulungu Mmodzi yekha. Ngati sasiya zomwe akunenazo, ndithudi, mwa iwo amene sadakhulupirire chiwakhudza chilango chopweteka

    [74] “Kodi salapa kwa Allah ndi kumpempha chikhululuko? Komatu Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha

    [75] “Mesiya mwana wa Mariya sali chilichonse koma ndi Mtumiki wa Allah chabe. Ndithudi, atumiki ambiri adapita kale patsogolo pake. Nayenso mayi wake ndi mkazi wachoonadi, onse awiri adali kudya chakudya, (ndipo chotsatira chake amapita kokadzithandiza. Nanga ndi milungu yotani yopita kukadzithandiza?) Taona momwe tikufotokozera kwa iwo zizindikiro. Taonanso mmene akutembenuziridwa (kusiya choonadi)

    [76] “Nena: “Kodi mukupembedza chimene sichingakupatseni vuto ngakhale chabwino, kusiya Allah? Pomwe Allah ndiye Wakumva, Wodziwa.”

    [77] “Nena: “E inu anthu a buku! Musapyole malire pa chipembedzo chanu popanda choonadi ndipo musatsatire zofuna za anthu omwe adasokera kale, nawasokeretsanso ambiri, ndi kusokera kunjira yowongoka (yolungama).”

    [78] “Adatembeleredwa amene sadakhulupirire nwa ana a Israyeli kupyolera m’lirime la Daud ndi Isa (Yesu) mwana wa Mariya. Zimenezo nchifukwa chakuti adanyoza ndipo adali opyola malire

    [79] “Sadali kuletsana choipa chomwe adali kuchichita. Taona kuipitsitsa zomwe adali kuchita

    [80] “Uwaona ambiri a iwo akupalana ubwenzi ndi omwe sadakhulupirire Allah, (opembedza mafano ndi cholinga chomenya nkhondo chipembedzo cha Chisilamu). Nzoipa kwambiri zomwe adadzitsogozera okha. Tero Allah adawakwiira ndipo m’masautso adzakhalamo nthawi yaitali

    [81] “Ndipo akadamkhulupirira Allah (moyenera) ndi mneneriyo (Muhammad {s.a.w}) ndi zomwe zidavumbulutsidwa kwa iye sakadawachita abwenzi. Koma ambiri a iwo ngopandukira chilamulo cha Allah

    [82] “۞ Ndithudi, uwapeza anthu amene ali oyipitsitsa pa chidani ndi anthu okhulupirira (Asilamu) ndi Ayuda komanso opembedza mafano. Ndipo uwapeza oyandikira ubwenzi ndi okhulupirira (Asilamu) ndi awo akunena kuti: “Ife ndi Akhrisitu.” Zimenezo n’chifukwa chakuti mwa iwo alipo ophunzira ndi oopa Allah, ndi chifukwanso chakuti iwo (Akhirisitu) sadzitukumula

    [83] “Ndipo akamva zomwe zavumbulutsidwa kwa Mtumiki, uona maso awo akugwetsa misozi chifukwa cha choonadi chomwe achizindikira. Akunena: “Mbuye wathu! Takhulupirira; choncho tilembeni pamodzi ndi oikira umboni (choonadi).”

    [84] “(Atadzudzulidwa polowa m’Chisilamu iwo adati): “Chifukwa ninji tisamkhulupirire Allah ndi choonadi chomwe chatifika, pomwe tikuyembekezera Mbuye wathu kukatilowetsa (ku Munda wamtendere) pamodzi ndi anthu abwino?”

    [85] “Choncho Allah adzawalipira, pa zomwe adanena, Minda yomwe pansi (ndi patsogolo) pake mitsinje ikuyenda. M’menemo adzakhalamo nthawi yaitali. Imeneyo ndiyo mphoto ya ochita zabwino

    [86] “Ndipo amene sadakhulipirire, nkutsutsa zizindikiro zathu, iwowo ndiwo anthu a ku Moto

    [87] “E inu amene mwakhulupirira! Musazichite zabwino zomwe Allah wakulolezani kukhala zoletsedwa. Ndipo musalumphe malire, ndithudi Allah sakonda anthu olumpha malire

    [88] “Idyani zabwino zomwe Allah wakupatsani zomwe zili zololedwa. Ndipo opani Allah yemwe inu mukumkhulupirira

    [89] “Allah sangakulangeni chifukwa chakulumbira kwanu kopanda pake. Koma akulangani kamba ka malumbiro omwe mwalumbira motsimikiza. Choncho dipo lake ndikuwadyetsa osauka khumi ndi chakudya cha mlingo wapakatikati chomwe mumawadyetsa anthu anu; kapena kuwaveka, kapena kumpatsa ufulu kapolo. Koma amene sangapeze zimenezo, asale masiku atatu. Ili ndi dipo la kulumbira kwanu pamene mukulumbira. Ndipo sungani malumbilo anu, (musaswe chomwe mudalumbilira). Motero ndi momwe Allah akukufotokozerani zizindikiro Zake kuti muthokoze

    [90] “E inu amene mwakhulupirira! Ndithudi, mowa (kutchova) njuga, kupembedza mafano ndi kuombeza maula, (zonsezi) ndi uve, mwa ntchito za satana. Choncho zipeweni kuti mupambane

    [91] “Ndithudi, satana akufuna kudzetsa chidani ndi kusakondana pakati panu kudzera m’mowa ndi njuga, ndikuti akutsekerezeni kukumbukira Allah ndi kupemphera Swala. Kodi inu simusiya

    [92] “Mverani Allah, ndipo mverani Mtumiki ndipo chenjerani (musanyoze malamulo a Allah). Ngati munyoza, dziwani kuti udindo wa Mtumiki Wathu ndikufikitsa uthenga woonekera basi

    [93] “Palibe tchimo kwa amene akhulupirira ndi kuchita zabwino pazomwe adadya (zisadaletsedwe) ngati akupitiriza kuopa ndikukhulupirira ndikuchita zabwino; kenako nkuopanso (ataletsedwa zina) ndikukhulupirira; (atalamulidwa zinanso) nkuopanso ndikuchita zabwino. Ndipo Allah, amakonda ochita zabwino

    [94] “E inu amene mwakhulupirira! Ndithu Allah akuyesani ndi nyama zina zozichita ulenje, zomwe manja anu ndi mikondo yanu ingazifikire, kuti Allah amuwonetsere poyera amene akumuopa mwanseri. Ndipo amene alumphe malire (posaka nyamayo ndi kupha) pambuyo pa zomwe mwauzidwazo, adzapeza chilango chopweteka

    [95] “E inu amene mwakhulupirira! Musaphe nyama ya mtchire pomwe inu muli m’mapemphero a Hajj kapena Umrah. Ndipo mwa inu amene angaphe mwadala nyama ya mtchireyo, dipo (lake likhale kuzinga) yofanana ndi yomwe waphayo, mu mtundu wa nyama zowetedwa, (monga mmene) angaweruzire olungama awiri a mwa inu, kukhala nsembe yoperekedwa ku Ka’aba (kuti ikazingidwe kumeneko ndi kuwagawira osauka); kapena alipe dipo la chakudya kudyetsa masikini; kapena m’malo mwake asale kuti alawe kupweteka kwa chinthu chakecho. Ndipo Allah afafaniza zomwe zidapita kale. Koma amene achitenso, Allah amukhaulitsa ndi chilango chochokera kwa Iye. Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa, Wokhaulitsa koopsa

    [96] “Nkololezedwa kwa inu kusaka nyama za m’nyanja ndi chakudya chake (chomwe chapezeka m’nyanjamo chitafa chokha). Chimenecho ndi kamba wanu (inu amene simuli pa ulendo) ndiponso a pa ulendo. Kwaletsedwa kwa inu kusaka za pamtunda pomwe muli m’mapemphero a Hajj kapena Umrah. Opani Allah Yemwe kwa Iye mudzasonkhanitsidwa

    [97] “Allah wapanga Ka’aba kukhala nyumba yopatulika, ndikukhala pamalo popezera zosowa za anthu. Ndipo adapanganso miyezi (inayi) yopatulika, ndi kupereka nyama zansembe ku Makka zovekedwa makoza monga zisonyezo (kusonyeza kuti zikupita ku Makka). Zonsezi nkuti mudziwe kuti Allah akudziwa za kumwamba ndi pansi, ndikuti Allah Ngodziwa chilichonse

    [98] “Dziwani kuti ndithudi, Allah Ngolanga mwaukali. Ndikutinso Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha

    [99] “Pa mtumiki palibe china koma kufikitsa chabe (uthenga). Ndipo Allah akudziwa zimene mukuzionetsera poyera ndi zimene mukuzibisa

    [100] “Nena (kwa aliyense kuti): “Zoipa ndi zabwino sizingafanane ngakhale kutakusangalatsa kuchuluka kwa zoipazo; choncho opani Allah, E! Inu eni nzeru kuti mupambane.”

    [101] “E inu amene mwakhulupirira! Musamafunse za zinthu zomwe zitasonyezedwa kwa inu zikuipirani. Ndipo ngati muzifunsa pomwe Qur’an ikuvumbulutsidwa, zionetsedwa kwa inu. Allah wakhululuka zimenezo. Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngoleza

    [102] “Anthu amene adalipo kale inu musanadze, adazifunsapo zotere. Ndipo pachifukwa chimenecho adasanduka osakhulupirira

    [103] “Allah sadaike (kuletsedwa kwamtundu uliwonse) pa nyama yotchedwa Bahira*, ngakhale Saiba**, ngakhale Wasila***, ngakhalenso Hami****. Koma amene sadakhulupirire akumpekera Allah bodza. Ndipo ambiri a iwo sagwiritsa ntchito nzeru zawo

    [104] “Ndipo akauzidwa: “Tadzani kuchilamulo cha zomwe Allah wavumbulutsa ndi (zomwe akunena) Mtumiki.” Akunena: “Tikukwaniritsidwa ndi zomwe tidawapeza nazo makolo athu.” Kodi ngakhale kuti makolo awowo sadali kudziwa chinthu chilichonse ndipo sadali oongoka, (awatsatirabe)

    [105] “E inu amene mwakhulupirira! Dziganizireni nokha. Ndipo amene asokera sangakupatseni mavuto ngati inu mutalungama. Nonsenu kobwerera kwanu nkwa Allah basi. Choncho adzakuuzani zimene mudali kuchita

    [106] “E inu amene mwakhulupirira! Pamene chamfikira mmodzi wa inu chisonyezo cha imfa, ndipo akufuna kusiya chilawo (wasiya) funani mboni ponena mawuwo. Aikire umboni awiri olungama mwa inu (Asilamu) kapena apadera ngati muli pa ulendo, ndipo zisonyezo za imfa zitaonekera. Ngati mutazikaikira zitsekerezeni (kuti zisachoke) mboni ziwiri pambuyo pa Swala (yomwe amasonkhana anthu ambiri), ndipo zilumbilire m’dzina la Allah kunena (kuti): “Sitikusinthanitsa malumbirowa ndi china chake ngakhale chitakhala chothandiza kwa ife kapena mmodzi mwa abale athu. Sitikubisa umboni umene Allah watilamula kuti tiupereke moona. Ife ngati titabisa umboni (kapena kuyankhula chonama), ndithudi tikhala mwa anthu ochimwa.”

    [107] “Koma ngati kutaoneka kuti mboni ziwiri zija zanama pa umboni wawo, kapena zabisa chinthu, apo awiri achibale a wakufayo aimiire m’malo mwa mboni ziwirizo, (pambuyo pa Swala kuti aulule za bodza lawo). Choncho alumbilire m’dzina la Allah kuti: “Ndithu kulumbira kwathu nkoyenera kuvomerezedwa kuposa kulumbira kwawo; ndipo sitinapyole malire (mukulumbira kwathu). Ndipo sitikuzipekera mbonizo bodza. Ndithudi, ngati ife titachita zotere, ndiye kuti tikhala mwa ochita zoipa, (oyenera kulandira chilango cha Allah).”

    [108] “Chilamulochi ndi njira yapafupi kuti mboni zikwaniritse umboni wawo mnjira yoyenera, (ndikuti zisamalire kulumbira Allah kwawo); kapena kuopa kuyaluka bodza lawo likaonekera poyera, pambuyo polumbira enawo (izi zili polumbira amlowa mmalo pokana umboni wawo). Ndipo opani Allah (mkulumbira kwanu ndi kukhulupirika kwanu), ndipo mverani malamulo Ake. Allah satsogolera anthu opandukira chilamulo Chake

    [109] “(Kumbukirani) tsiku lomwe Allah adzasonkhanitsa, atumiki ndikuwafunsa kuti: “Kodi mudayankhidwa chiyani?” Iwo adzati: “Ife sitidziwa. Ndithudi, Inuyo ndiye Wodziwa zamseri.”

    [110] “Kumbukiraninso pamene Allah adzati: “Iwe Isa (Yesu) mwana wa Mariya! Kumbuka chisomo Changa pa iwe ndi pa mayi wako, pamene ndinakuthandiza ndi mzimu woyera (Gabriel), (kotero kuti) udalankhula kwa anthu (mawu omveka) pamene udali mchikuta ndiponso pamene udali wamkulu. Ndipo (kumbuka) pamene ndidakuphunzitsa kulemba, nzeru; (ndinakuzindikiritsanso buku la) Taurat ndi Injili. (Kumbukanso) pamene udaumba dongo chithunzi chambalame mwa lamulo Langa. Utatero udauziramo ndipo zidasanduka mbalame mwa lamulo Langa. Ndipamene udali kuchiza akhungu ndi achinawa, mwa lamulo Langa. Ndipamene unkawatulutsa (m’manda) ena mwa akufa mwa lamulo Langa. Ndipamene ndinawatsekereza ana a Israyeli kwa iwe (kuti asakuzunze) pamene udawadzera ndi zisonyezo zooneka, ndipo aja mwa iwo omwe sadakhulupirire, adati: “Ichi sichina, koma ndi matsenga owonekera.”

    [111] “Ndipo (kumbukira) pamene ndidawaululira ophunzira ako kuti: “Ndikhulupirireni Ine ndi Mtumiki Wanga (uyu Isa {Yesu}).” Iwo adati: “Takhulupirira; ndipo khalani mboni kuti ife ndife Asilamu (ogonjera mwa Inu).”

    [112] “(Kumbukira) pamene ophunzira ako adati: “E iwe Isa (Yesu) mwana wa Mariya: Kodi Mbuye wako angathe kutitsitsira chakudya kuchokera kumwamba?” (Isa {Yesu}) adati: “Opani Allah, ngati inu mulidi okhulupirira. (Musamangopempha zozizwitsa).”

    [113] “(Iwo) adati: “Tikufuna kudya chimenecho, ndikuti mitima yathu ikhazikike, ndikutinso tidziwe kuti watiuza choona; tero kuti tikhale oikira umboni pa chimenecho.”

    [114] “Isa (Yesu) mwana wa Mariya adati: “Inu Allah Mbuye wathu! Titsitsireni chakudya kuchokera kumwamba kuti chikhale chikondwelero cha oyambilira ndi omalizira mwa ife, komanso chikhale chisonyezo chochokera kwa Inu; choncho tipatseni ndithu inu ndinu Abwino popatsa kuposa opatsa.”

    [115] “Allah adati: “Ndithu Ine ndikuchitsitsa kwa inu. Koma amene adzatsutse mwa inu pambuyo pa ichi, ndithu Ine ndidzamulanga ndi chilango chomwe sindidamulangepo nacho aliyense mwa zolengedwa.”

    [116] “Ndipo (kumbukirani) pamene Allah adzanena: “Iwe Isa (Yesu) mwana wa Mariya: Kodi iwe udauza anthu kuti: ‘Ndiyeseni ine ndi mayi wanga monga milungu iwiri m’malo mwa Allah?” (Mneneri Isa {Yesu}) adzaati: “Ulemelero ukhale pa Inu. Sikoyenera kwa ine kunena zomwe sizili zoyenera (kwa ine mawu amenewa ngabodza). Ngati ndikadanena, ndiye kuti mukadadziwa. Inu mukudziwa zomwe zili mu mtima mwanga, pomwe ine sindidziwa zomwe zili mwa Inu. Ndithudi, Inu ndinu Wodziwa zamseri.”

    [117] ““Sindinawauze chilichonse kupatula chimene mudandilamula kuti: ‘Pembedzani Allah, Mbuye wanga ndiponso Mbuye wanu.’ Ndipo ndinali mboni kwa iwo pamene ndidali nawo. Koma pamene mudanditenga, Inu ndiye mudali Muyang’aniri pa iwo; ndipo Inu ndinu Mboni ya chilichonse.”

    [118] ““Ngati muwalanga, ndithudi iwo ndi akapolo anu. Ndipo mukawakhululukira, ndithudi, Inu ndinu Mwini mphamvu zoposa, Wanzeru zakuya.”

    [119] “Allah adzati: “Ili ndi tsiku lomwe olankhula zoona kudzawathandiza kuona kwawo. Iwo adzalandira Minda yomwe pansi (ndi patsogolo) pake mitsinje ikuyenda. M’menemo adzakhala muyaya. Allah adzawayanja; naonso adzamuyanja. Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu

    [120] “Allah Yekha ndiye Mwini ufumu wa kumwamba ndi pansi, ndi zam’menemo. Ndipo Iye Ngokhoza chilichonse

    Ziweto

    Surah 6

    [1] “Kuyamikidwa konse kwabwino nkwa Allah, Yemwe adalenga thambo ndi nthaka, napanga mdima ndi kuunika pamwamba pa izi, kenako amene sadakhulupirire akumfanizira Mbuye wawo ndi milungu yabodza

    [2] “Iye ndi Yemwe adakulengani ndi dongo, kenako adaika nthawi (yothera cholengedwa chilichonse), ndi nthawi ina yodziwika kwa Iye (yomwe njoukitsira zolengedwa ku imfa). Ndipo pa izi inu (osakhulupirira) mukukaikira

    [3] “Ndipo Iye ndi Allah (Wopembedzedwa) kumwamba ndi pansi. Akudziwa za mkati mwanu ndi zakunja kwanu, ndipo akudziwa zimene mukupeza (kuchokera mzochitachita zanu, zabwino kapena zoipa)

    [4] “Ndipo palibe pamene chikuwadzera chisonyezo chilichonse mwa zisonyezo za Mbuye wawo koma akuzitembenukira kumbali

    [5] “Ndithudi, atsutsa choonadi (Qur’an) pamene chawadzera. Posachedwapa ziwafika nkhani (za zilango) zimene adali kuzichitira chipongwe

    [6] “Kodi saona kuti ndi mibadwo ingati tidaiononga patsogolo pawo? Tidawapatsa mphamvu yopezera za m’dziko zomwe sitidakupatseni inu. Ndipo tidawavumbwitsira mvula yopitiriza (mwa ubwino choncho, adasangalala kopambana). Ndipo tidaipanga mitsinje kuyenda pansi pawo (pansi pa mitengo yawo ndi nyumba zawo). Kenako tidawaononga chifukwa cha machimo awo, ndipo pambuyo pawo tidalenga mibadwo ina

    [7] “Ndipo ngati tikadakutsitsira malemba (olembedwa) m’mapepala, (monga momwe adakufunsira), nkuwakhudza ndi manja awo, amene sadakhulupirire akadati: “Ichi sichina koma ndi matsenga owoneka.”

    [8] “Ndipo amanena: “Bwanji iye osamtsitsira mngelo (kuti aziikira umboni kwa anthu za uneneri wake)?” Tikadakutsitsira mngelo (nkusakhulupirira), ndithu chiweruzo cha kuonongeka kwawo chikadakwaniritsidwa. Ndipo sakadapatsidwanso mpata

    [9] “Ndipo tikadampanga iyeyo kukhala mngelo, tikadamsandutsa kukhala munthu (chifukwa iwo sangathe kumuona mngelo), ndipo tikadati asakanikirane nawo monga momwe eni amasakanikirana (kotero kuti sakadamdziwa kuti mngelo ndi uyu)

    [10] “Ndithudi, adachitidwa chipongwe atumiki patsogolo pako; koma (mapeto ake) aja mwa iwo omwe adachita chipongwe zidawazinga zomwe adali kuzichitira chipongwe

    [11] “Nena: “Yendani pa dziko, kenako tayang’anani momwe adalili mapeto a otsutsa.”

    [12] “Nena (mowafunsa): “Nzayani zomwe zili kumwamba ndi pansi?” Nena kwa iwo (ngati sakuyankha): “Nza Allah.” Iye wadzikakamiza kuwachitira chifundo (anthu Ake). (Pachifukwa chimenechi amawapatsa nthawi osawalanga mwachangu). Ndithudi adzakusonkhanitsani tsiku la Qiyâma lopanda chikaiko. Amene adzitaya okha, sakhulupirira (za tsikulo)

    [13] “Nza Iye (Allah) zonse zili mu nthawi ya usiku ndi usana. Iye Ngwakumva, Ngodziwa

    [14] “Nena: “Ndidzipangire mtetezi wanga kusiya Allah, Mlengi wa thambo ndi nthaka? Iye Njemwe amadyetsa ndipo sadyetsedwa.” Nena: “Ndalamulidwa kukhala woyamba mwa olowa m’Chisilamu.” Ndipo (ndauzidwa kuti): “Usakhale mwa ophatikiza (Allah ndi mafano)”

    [15] “Nena (kwa iwo): “Ine ndikuopa chilango cha tsiku lalikulu ngati ndinyoza Mbuye wanga.”

    [16] “Yemwe adzapewetsedwe ku chilangocho tsiku limenelo, ndiye kuti wamchitira chifundo; kumeneko nkupambana kowonekera

    [17] “Ngati Allah atakukhudza ndi mazunzo, palibe aliyense angathe kukuchotsera, koma Iye basi; ndipo ngati atakukhudza ndi zabwino (palibe amene angakutsekereze ku zabwinozo). Iye ali ndi mphamvu pa chilichonse

    [18] “Iye ndi Mgonjetsi pa anthu ake (onse); Iye Ngwanzeru zakuya, Wodziwa nkhani zonse

    [19] “Nena: “Kodi nchinthu chanji chomwe umboni wake uli waukulu koposa?” Nena (ngati sakuyankha): “Ndi (umboni wa) Allah basi. (Iye) ndi Mboni pakati pa ine ndi inu. Ndipo Qur’an iyi yavumbulutsidwa kwa ine kuti ndikuchenjezeni nayo ndi amene yawafika (pali ponse pamene ali). Kodi inu mukutsimikiza ndi kuikira umboni kuti pali milungu ina pamodzi ndi Allah?” Nenanso: “Koma ine sindikuikira umboni.” Nenanso: “Iye ndi Mulungu Mmodzi Yekha. Ndithudi, ine ndili kutali ndi zomwe mukumphatikiza nazo.”

    [20] “Omwe tidawapatsa buku akumzindikira (Muhammad {s.a.w} bwinobwino) monga momwe akuwazindikilira ana awo. Koma omwe adziononga okha, iwo sangakhulupirire

    [21] “Kodi ndani woipitsitsa zedi woposa yemwe akum’pekera Allah bodza. Kapena kutsutsa zizindikiro Zake? Ndithudi, oipa sangapambane

    [22] “Ndipo (akumbutse) tsiku lomwe tidzawasonkhanitsa onse pamodzi; kenako tidzati kwa omwe adali kuphatikiza (Allah ndi mafano): “Ali kuti aphatikizi anu aja omwe munkati ngothandizana ndi Allah?”

    [23] “Ndipo dandaulo lawo silidzakhala lina koma kunena: “Tikulumbilira Allah Mbuye wathu, sitidali ophatikiza (mafano ndi Allah).” (Uku kudzakhala kuyesera kumunamiza Allah)

    [24] “Taona momwe akudzinamizira okha ndipo zidzawasokonekera zomwe adali kuzipeka (ponena kuti izo ndi milungu zidzawapulumutsa kwa Allah)

    [25] “Alipo ena mwa iwo omwe akukumvetsera (ukamawerenga Qur’an), ndipo taika zitsekero pa mitima yawo kuti asazindikire (chifukwa cha machimo awo omwe akhala akuchita), ndi m’makutu mwawo kulemera kwa ugonthi; ndipo akaona chozizwitsa chilichonse, sakuchikhulupirira, kufikira akakudzera kudzakangana nawe, awo amene sadakhulupirire akuti: “Izi (zimene utilankhulazi), sikanthu koma ndi nkhani zopeka za anthu akale.”

    [26] “Ndipo iwo akuletsa (anthu kutsatira) izi, ndipo (eniwo) akudzitalikitsa nazo. Palibe wina akumuononga koma iwo okha, ndipo sakudziwa

    [27] “Ndipo ukadaona (tsiku la Qiyâma) pamene adzawaimitsa pa Moto nkuyamba kunena: “Ha! Tikadabwezedwa (ku dziko lapansi) ndipo sitikadatsutsanso zizindikiro za Mbuye wathu; ndipo tikadakhala mwa okhulupirira.”

    [28] “(Sichoncho) koma zawaonekera poyera zomwe adali kubisa kale. Ndipo akadabwezedwa akadabwerezanso kuchita zimene adaletsedwa. Ndithudi iwo ngabodza basi

    [29] “Akumanena: “Palibe moyo wina koma moyo wathu wa pa dziko lapansi basi. Ndipo ife sitidzaukitsidwanso m’manda.”

    [30] “Ndipo ukadaona (tsiku la chiweruziro) pamene azikaimitsidwa pamaso pa Mbuye wawo nauzidwa: “Kodi ichi sichoona?” (Iwo) nati: “Inde nchoona, tikulumbira Mbuye wathu.” (Allah) adzati: “Lawani chilango chifukwa cha kusakhulupirira kwanu (aneneri a Allah).”

    [31] “Ndithudi, ataika ndi kuonongeka amene akutsutsa zokumana ndi Allah, mpaka mwadzidzidzi nthawi ya Qiyama itawafikira, adzati: “Ho! Masautso pa ife chifukwa chakusalabadira kwathu za zimenezi, uku iwo atasenza mitolo ya machimo kumisana kwao. Taonani kuipa kwa zomwe akusenza

    [32] “Ndipo moyo wadziko lapansi sikanthu, koma ndi masewera ndi chibwana. Koma nyumba yomaliza ndiyabwino koposa, (siyofanana ndi chisangalalo cha pa dziko lapansi) kwa omwe akuopa Allah. Bwanji simuzindikira

    [33] “Ndithu tikudziwa kuti zikukudandaulitsa zomwe akukunenera (pokunyoza ndi kukuyesa wabodza. Ndithu iwo sakukutsutsa iwe; koma oipawa akutsutsa zizindikiro za Allah)

    [34] “Ndithudi, atumiki onse adatsutsidwa iwe usadadze. Koma adapirira ku zomwe adatsutsidwa, ndipo adazunzidwa kufikira pamene chipulumutso Chathu chidawafika. Palibe wosintha mawu a Allah. Ndithu zakufika nkhani za atumiki (momwe muli malingaliro ndi maphunziro ambiri)

    [35] “Ndipo ngati nkovuta kwa iwe kudzipatula kwawoku (ndi zomwe wadza nazozi pomwe iwo akukuumiriza kuti uwabweretsere chozizwitsa, nawe nkumafuna; zikadatero, pomwe Ine sindikufuna), choncho ngati uli wokhoza kufunafuna njira ya pansi penipeni m’nthaka (kukafuna zozizwitsazo), kapena (ungathe kupeza) makwelero nkukwera kumwamba nkubwera ndi chozizwitsa (chimene akufuna, chita). Allah Akadafuna akadawasonkhanitsa onse ku chiwongoko. Choncho, usakhale mwa osazindikira zinthu

    [36] “Ndithudi amene akuvomereza, ngomwe akumva (ndipo anthu awa amene safuna kumvera chilichonse ndi akufa ngakhale ali moyo). Ndipo akufa Allah adzawaukitsa (m’manda mwawo) kenako adzabwezedwa kwa Iye

    [37] “Ndipo akumanena: “Bwanji sichinatsitsidwe chozizwitsa kwa iye kuchokera kwa Mbuye wake?” Nena: “Ndithudi, Allah Ngokhoza kutsitsa chozizwitsa koma ambiri a iwo sadziwa (zomwe Allah afuna).”

    [38] “Ndipo palibe nyama ili yonse pa nthaka, ngakhale mbalame yowuluka ndi mapiko ake awiri koma ndi magulu a zolengedwa ngati inu (zomwe Allah adazilenga). Sitinasiye chinthu chilichonse kapena kuchinyozera chilichonse m’buku (chomwe nchofunika koma tachifotokoza). Ndipo tero kwa Mbuye wawo adzasonkhanitsidwa

    [39] “Ndipo amene atsutsa zizindikiro Zathu, ndiagonthi ndiponso abubu, ali mu m’dima (wa umbuli). Amene Allah wamfuna amamlekelera kusokera. Ndipo amene wamfuna amamuika pa njira yolunjika (yomwe ndi njira ya Chisilamu)

    [40] “Nena: “Tandiuzani ngati mazunzo a Allah atakufikani (pompano pa dziko lapansi), kapena kukufikani nthawi (ya chilango cha tsiku lachimaliziro) kodi mudzaitana yemwe sali Allah (kuti akupulumutseni) ngati inu muli owona.”

    [41] ““Koma Iye yekha ndi Yemwe mudzampempha, ndipo Iye adzakuchotserani zomwe mukumpempha (kuti akuchotsereni) ngati atafuna. Ndipo mudzaiwala zomwe mudali kuziphatikiza (ndi Allah).”

    [42] “Ndithu tidawatumiza (atumiki) ku mibadwo yomwe idalipo iwe usadadze. Ndipo tidaikhaulitsa (mibadwoyo) ndi mazunzo ndi masautso kuti iyo idzichepetse (pambuyo podzikuza)

    [43] “Pamene masautso adawafika kuchokera kwa Ife, bwanji sadaphunzire kudzichepetsa? Koma mitima yawo idali youma, ndipo satana adawakometsera machimo omwe iwo adali kuchita

    [44] “Ndipo pamene adanyozera zimene ankakumbutsidwa tidawatsekulira makomo a chinthu chilichonse (chimene adali kuchifuna) kufikira pamene adasangalala ndi zomwe adapatsidwa, tidawagwira mwadzidzidzi; pompo adataya mtima

    [45] “Choncho mizu ya anthu oipa idadulidwa. Ndipo kuyamikidwa konse kwabwino nkwa Allah, Mbuye wa zolengedwa

    [46] “Nena: “Tandiuzani, ngati Allah atakuchotserani kumva kwanu ndi kupenya kwanu, nadinda chidindo m’mitima yanu (kuti asalowemo mawu amalangizo a mtundu uliwonse), kodi ndi mulungu uti, kupatula Allah, amene angakubwezereninso (zimenezi)?” Taona momwe tikufotokozera mwatsatanetsatane zizindikiro kenako iwo akunyozera

    [47] “Nena: “Tandiuzani, ngati masautso a Allah atakufikani mwadzidzidzi kapena moonekera, kodi angaonongeke ndi ena osati anthu ochita zoipa?”

    [48] “Ndipo sititumiza atumiki koma kuti akhale ouza nkhani zabwino ndi ochenjeza. Choncho amene akhulupirira nakonza zinthu, pa iwo sipadzakhala mantha ndiponso sadzadandaula

    [49] “Ndipo amene atsutsa zizindikiro zathu, chilango chidzawakhudza chifukwa chakupandukira kwawo chilamulo

    [50] “Nena: “Ine sindikukuuzani kuti ndili nazo nkhokwe za Allah kapena kuti ndikudziwa zamseri, ndiponso sindikukuuzani kuti ine ndine mngelo. Ine sinditsata china koma zomwe zikuvumbulutsidwa kwa ine.” Nena: “Kodi wakhungu ndi wopenya angafanane? Bwanji simukuganizira?”

    [51] “Achenjeze ndi Qur’an iyi omwe akuopa kuti adzasonkhanitsidwa kwa Mbuye wawo pomwe ali opanda mtetezi ngakhale muomboli aliyense kupatula Iye, kuti iwo aope (Allah)

    [52] “Ndipo usawathamangitse omwe akupembedza Mbuye wawo m’mawa ndi madzulo pofuna chiyanjo Chake. Chiwerengero chawo sichili pa iwe ngakhale pang’ono, ndipo chiwerengero chako sichili pa iwo ngakhale pang’ono kotero kuti nkwathamangitsa. (Ngati uwapirikitsa) ukhala m’gulu la anthu ochita zoipa

    [53] “Ndipo momwemo tawasankha ena (osauka) kukhala mayeso a ena (olemera) kuti (osauka) anene: “Kodi awa ndi omwe Allah wawasankhira ubwino mwa ife (ndikutisiya ife?)” Kodi Allah sali Wodziwa zedi amene akumthokoza

    [54] “Ndipo (iwe Mneneri) akakudzera (awo osauka) amene akhulupirira zizindikiro zathu (atalakwa pang’ono), auze: “Mtendere ukhale pa inu. Mbuye wanu wadzikakamiza kukhala Wachifundo, kuti mwa inu amene achite choipa mwaumbuli, koma pambuyo pake nkulapa, nachita zabwino, Allah amkhululukira; Iye Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha.”

    [55] “Mmenemo ndi momwe tikufotokozera zizindikiro mwatsatanetsatane (kuti choonadi chioneke) ndi kuti njira ya oipa idziwike bwinobwino

    [56] “Nena: “Ndithu ine ndaletsedwa kupembedza amene mukuwapembedza kusiya Allah.” Nena: “Sinditsata zilakolako zanu; ndikadatero ndikadasokera ndipo sindikadakhala mwa owongoka.”

    [57] “Nena: “Ndithu ine ndili ndi umboni wowoneka wochokera kwa Mbuye wanga (wotsimikizira zomwe ndikunenazi), koma inu mwautsutsa. Ndilibe (chilango) chimene mukuchifulumizitsacho. Palibe kulamula koma nkwa Allah. Amakamba zoona zokhazokha; Iye Ngwabwino mwa oweruza (onse).”

    [58] “Nena: “Ndikadakhala nacho chimene mukuchifulumizitsacho, ndiye kuti chinthucho chikadachitika pakati pa ine ndi inu (ndikadakuonongani koma ndilibe nyonga). Ndipo Allah akuwadziwa bwino anthu ochita zoipa.”

    [59] “Ndipo Iye (Allah) ali nawo Makiyi a zobisika palibe akuwadziwa koma Iye basi. Ndipo akudziwa za pamtunda ndi za panyanja. Ndipo palibe tsamba limene limagwa koma amalidziwa. Ndipo (siigwa) njere mu mdima wa m’nthaka (koma iye akudziwa). Ndipo (sichigwa) chachiwisi ngakhale chouma, koma chili m’buku loonetsa chilichonse

    [60] “Iye ndiyemwe amakupatsani imfa (yatulo) nthawi yausiku, ndipo amadziwa zimene mwachita masana, kenako amakudzutsani mmenemo kuti ikwane nthawi yanu yoikidwa (yofera); kenako kwa Iye ndiko kobwerera kwanu, nadzakuuzani zimene munkachita

    [61] “Iye ndi M’gonjesi pa akapolo Ake ndipo amakutumizirani (angelo) osunga, (olemba zochita zanu); kufikira mmodzi wanu imfa ikamdzera, angelo athuwo amampatsa imfa, ndipo iwo sanyozera (ntchito yawo)

    [62] “Kenako adzabwezedwa kwa Allah, Mbuye wawo Woona. Dziwani kuti kuweruza Nkwake. Iye Ngwachangu powerengera kuposa owerengera (onse)

    [63] “Nena: “Kodi ndani amakupulumutsani m’masautso a pamtunda ndi panyanja?” Mumampempha modzichepetsa ndi motsitsa mawu (kuti): “Ngati atipulumutsa m’mazunzo awa, ndithudi tidzakhala mwa othokoza.”

    [64] “Nena: “Allah ndi Yemwe amakupulumutsani ku zimenezo ndi ku masautso a mtundu uliwonse. Kenako inu mukumphatikiza ndi mafano

    [65] “Nena: “Iye Ngokhoza kukutumizirani chilango kuchokera pamwamba panu kapena pansi pa miyendo yanu, kapena kudzetsa chisokonezo nkukhala magulumagulu (osamvana), ndipo (akhoza) kuwalawitsa ena a inu chilango cha mtopola wa ena.” Taona momwe tikufotokozera zizindikiro kuti iwo azindikire

    [66] “Koma anthu ako aitsutsa iyo (Qur’an) pomwe ili yoona. Nena: “Ine sindili muyang’anili pa inu.”

    [67] “Nkhani iliyonse (yomwe yatchulidwa apa) ili ndi nthawi yake yodziwika (yofikira). Ndipo posachedwapa mudziwa (izi)

    [68] “Ndipo (iwe Msilamu weniweni) ukawaona omwe akuchita chipongwe ndi Ayah Zathu, apatuke mpaka anene nkhani ina. Ndipo ngati satana atakuiwalitsa, (nkukhala nawo pomwe iwo akukambirana zotere), choncho, pambuyo pokumbukira usakhale pamodzi ndi anthu ochita zoipa

    [69] “Palibe chilichonse chimene chingawapeze oopa Allah chochokera m’chiwerengero cha oipawo, koma chofunika kwa iwo (oopa Allah) ndikuwakumbutsa (oipawo) kuti aope (aleke zomwe akunenazo)

    [70] “Asiye amene achita chipembedzo chawo kukhala masewera ndi chibwana. Ndipo wawanyenga moyo wadziko lapansi. Choncho, akumbutse ndi Qur’aniyo (kuti achenjere), kuti ungaonongedwe mtima uliwonse (ndi kuikidwa m’ndende) kupyolera mu zomwe udapata. Ndipo sukhala ndi mtetezi ngakhale muomboli posakhala Allah, ngakhale utayesera kupereka dipo lamtundu uliwonse silingavomerezedwe (kwa mzimuwo). Awo ndi omwe aonongeka ndi kunjatidwa chifukwa cha zomwe adapeza. Iwo adzakhala ndi chakumwa cha madzi a moto owira kwambiri, ndi chilango chopweteka chifukwa cha kusakhulupirira kwawo (Allah)

    [71] “Nena: “Kodi tipembedze omwe sali Allah, omwe sangatipatse phindu (ngati titawapembedza), ndiponso sangathe kutivutitsa (tikasiya kuwapembedza), ndetibwezedwe m’mbuyo pambuyo potitsogolera Allah? Tikhale chimodzimodzi aja omwe satana adawasokeretsa, nkukhala achewuchewu pa dziko? Ali nawo anzawo omwe akuwaitanira ku chiongoko (kuti) ‘Bwerani kwathu, (koma samva. Sitingakhale monga anthu otere).” Nena: “Utsogozi weniweni ngwa Allah, ndipo talamulidwa kuti tigonjere Mbuye wa zolengedwa zonse.”

    [72] “Ndikuti: “Pempherani Swala, ndipo muopeni Iye, Yemwe kwa Iye mudzasonkhanitsidwa.”

    [73] “Iye ndiye adalenga thambo ndi nthaka mwa choonadi. Ndipo panthawi imene akunena (kuchiuza chinthu): “Chitika,” ndipo chimachitikadi. Mawu ake ndioona. Ndipo ufumu udzakhala Wakewake tsiku limene Lipenga lidzaimbidwa. Ngodziwa zamseri ndi zooneka. Iye Ngwanzeru zakuya, Wodziwa nkhani zonse

    [74] “Ndipo (kumbukirani) pamene Ibrahim adauza bambo ake, Azara: “Kodi mukupanga mafano kukhala milungu? Ndithu ine ndikukuonani inu ndi anthu anu kuti muli m’kusokera koonekera.”

    [75] “Ndipo momwemo tidamuonetsa Ibrahim ufumu wa kumwamba ndi pansi (kuti ngwa Allah) kuti akhale m’modzi mwa otsimikiza

    [76] “Ndipo pamene kunam’dera adaona nyenyezi. Adati (mwadaladala kuti abutse nzeru za opembedza mafano): “(Nyenyezi) iyi ndiye mbuye wanga.” Pamene idalowa, adati: “Sindikonda (milungu) yomalowa, (yomasowa, yakutha).”

    [77] “Pamene adaona mwezi ukutuluka, adati: “Uyu ndiye mbuye wanga.” Koma pamene udalowa, adati: “Ngati Mbuye wanga sandiongolera, ndithudi, ndikhala m’gulu la anthu osokera.”

    [78] “Pamene adaona dzuwa likutuluka, adati: “Uyu ndiye mbuye wanga; uyu ngwamkulu kwabasi.” Koma pamene lidalowa, adati: “E inu anthu anga! Ine ndili kutali ndi zomwe mukumphatikiza nazo (Allah)

    [79] “Ndithu ine ndalungamitsa nkhope yanga kwa Yemwe adalenga thambo ndi nthaka, ndapendekera kwa Iye Yekha. Ndipo ine sindili mwa om’phatikiza (Allah ndi mafano)

    [80] “Ndipo anthu ake adakangana naye (pomuuza kuti: “Bwanji ukusiya chipembedzo chamakolo ako; uona malaulo”). (Iye) adati: “Kodi Mukukangana nane pa za Allah pomwe Iye wanditsogolera? Ndipo Sindingaope zimene mukumphatikiza Naye, kupatula Mbuye wanga akafuna chinthu, (apo chiyenera kuchitika). Mbuye wanga akudziwa chinthu chilichonse bwinobwino. Bwanji simulalikika?”

    [81] ““Ndipo ndingaope chotani zomwe mwaziphatikiza (ndi Allah) pomwe inu simuopa kuti mukumphatikiza Allah (ndi mafano) omwe Allah sadawatsitsire pa inu umboni (kuti muziwapembedza). Choncho ndi gulu liti m’magulu awa awiri (langa kapena lanu) loyenera koposa kupeza chitetezo? Ngati inu mudziwa (zinthu).”

    [82] “(Palibe chikaiko kwa) amene adakhulupirira ndipo sadasakanize chikhulupiliro chawo ndi kupondereza (shirk), iwowo ali nacho chitetezo. Ndiponso iwo ndi omwe ali oongoka

    [83] “Ndipo izi ndi zizindikiro Zathu (mitsutso Yathu), zomwe tidampatsa Ibrahim pa anthu ake. Timamtukulira ulemelero amene tamfuna. Ndithu Mbuye wako Ngwanzeru zakuya, Ngodziwa kwambiri

    [84] “Ndipo tidampatsa (Ibrahim mwana wotchedwa) Ishaq ndi (mdzukulu wotchedwa) Ya’qub. Onse tidawaongola. Nayenso Nuh tidamuongola kale (asadadze Mneneri Ibrahim). Ndipo kuchokera m’mbumba yake (Nuh, tidamuongola) Daud, Sulaiman, Ayubu, Yûsuf, Mûsa, ndi Harun. Ndipo umo ndi momwe timawalipirira ochita zabwino

    [85] “Tidamutsogoleranso Zakariya, Yahya, Isa (Yesu) ndi Iliyasa. Onse adali mwa anthu abwino

    [86] “Ndi Ismail, Eliya, Yunus (Yona) ndi Luti (Loti). Onsewa tidawapatsa ubwino pa zolengedwa zonse

    [87] “(Ndiponso tidawatsogolera) ena mwa atate awo, ana awo ndi abale awo. Ndipo tidawasankha ndi kuwaongolera ku njira yolunjika

    [88] “Ichi ndi chiongoko cha Allah. Ndi icho akuongolera yemwe wamfuna mwa akapolo Ake. Akadakhala kuti (aneneriwo) adamphatikiza (Allah ndi zina) zikadawaonongekera zimene ankachita

    [89] “Iwo ndi omwe tidawapatsa mabuku, chiweruzo, ndi uneneri. Choncho ngati awa (osakhulupirira) azikane izi, basi, tazipereka kale kwa anthu omwe sangazikane

    [90] “Iwo ndi omwe Allah adawaongola choncho, tsatira chiongoko chawo. Nena: “Sindikukupemphani malipiro pa izi (zomwe ndikukuphunzitsanizi, koma ndikungotumikira Allah). Ichi sichina koma ndi ulaliki kwa zolengedwa (majini ndi anthu).”

    [91] “Koma (Ayuda) sadamulemekeze Allah monga momwe zikufunikira pomulemekeza pomwe adati: “Allah Sadavumbulutsepo chilichonse kwa munthu aliyense.” (Adanena izi pamene mtumiki adawauza kuti Qur’an ndi buku lomwe Allah wavumbulutsa). Nena: “Kodi ndani adavumbulutsa buku lomwe lidadza ndi Mûsa? Lomwe lidali kuunika ndi chiwongoko kwa anthu, lomwe mwalipanga kukhala magawo-magawo; zimene mwafuna kuonetsa kwa anthu mukuzionetsa. Koma zambiri mukubisa (zomwe sizigwirizana ndi zofuna zanu). Ndipo mwaphunzitsidwa (ndi iyi Qur’an) zomwe simudali kuzidziwa, inu ngakhale makolo anu. Nena: “Allah (ndi Yemwe wavumbulutsa iyi Qur’an ndi mabuku ena.”) Kenako asiye azingosewera m’kubwebweta kwawo (kopanda pake)

    [92] “Ndipo ili ndibuku limene talivumbulutsa lamadalitso ochuluka; lotsimikizira zomwe zidalitsogolera. Ndikuti uchenjeze manthu wa mizinda (Makka) ndi amene ali m’mphepete mwake. Ndipo amene akukhulupirira tsiku lachimaliziro, akulikhulupirira (bukuli). Ndipo iwo Swala zawo akuzisunga bwino

    [93] “Kodi ndani woipitsitsa koposa yemwe wampekera bodza Allah kapena wonena: “Kwavumbulutsidwa kwa ine,” pomwe sikunavumbulutsidwe kwa iye chilichonse; ndi yemwe akunena: ‘“Ndivumbulutsa monga chimene Allah wavumbulutsa.” Ukadawaona anthu ochita zoipa akuthatha ndi imfa, nawo angelo atatambasula manja awo (powamenya uku akuwauza): “Tulutsani moyo wanu; lero mulipidwa chilango chonyozetsa chifukwa cha zomwe mudali kunenera Allah popanda choonadi, ndi kudzitukumula kwanu pa zizindikiro zake.” (Ukadaona zoopsa kwabasi)

    [94] “Ndipo (tsiku la Qiyâma tidzakuuzani): “Ndithudi, mwatidzera mmodzimmodzi (payekhapayekha popanda chuma ndi ana kuti zikupulumutseni), monga mmene tidakulengerani pachiyambi. Ndipo mwasiya kumbuyo kwanu zonse zomwe tidakupatsani. Ndipo sitikuona pamodzi nanu apulumutsi anu aja, amene munkati ngothandizana (ndi Allah; ndi kuti iwo ndi apulumutsi anu). Ndithudi mgwirizano omwe udali pakati panu waduka. Ndipo zakusokonekerani zimene munkaziganizira (kuti ndi milungu).”

    [95] “Ndithu Allah ndi Yemwe amang’amba njere ndi mbewu ya zipatso (kuti zimere). Amatulutsa chamoyo m’chakufa. Ndiponso Ngotulutsa chakufa m’chamoyo. Ameneyu ndi Allah, nanga mukutembenuzidwa chotani

    [96] “Iye ndi Yemwe ali Wotsekula m’bandakucha, ndipo amaupanga usiku kukhala wabata (nthawi yopumula) ndi dzuwa ndi mwezi kukhala zowerengera masiku ndi zaka (kalendala). Ichi nchikonzero cha Wamphamvu zoposa, Wodziwa kwambiri

    [97] “Iye ndi amene anakupangirani nyenyezi kuti mulondole njira kudzera mwa izo mu m’dima wa pamtunda ndi panyanja. Ndithu talongosola mokwanira zizindikiro (zathu) kwa anthu odziwa

    [98] “Ndipo Iye ndi yemwe adakulengani kuchokera mu mzimu umodzi. (Kwa inu) alipo malo okhalapo (dziko lapansi kapena m’mimba mwa mayi) ndiponso posungirapo (mmanda kapena munsana mwa bambo). Ndithu tafotokoza zizindikiro (Zathu) kwa anthu ozindikira

    [99] “Iye ndi Yemwe amavumbwitsa mvula kuchokera kumwamba. Ndi madzi a mvulayo timameretsa mmera wa chinthu chilichonse. Ndipo m’menemo tikuphukitsa masamba obiriwira, tikutulutsa mmenemo njere zosanjikana; ndiponso m’kanjedza m’mikoko mwake mumatuluka maphava ogoweka (ndizipatso). Ndipo amakumeretserani minda ya mphesa, mzitona ndi makomamanga, ofanana ndi osafanana. Tapenyani zipatso zake pamene zikupatsa ndi kupsa kwake. Ndithu m’zimenezo muli zizindikiro kwa anthu okhulupirira

    [100] “Ndipo (pamwamba pa izi) anthu ampangira Allah ziwanda kukhala athandizi (Ake), pomwe Iye ndi Yemwe adazilenga. Ndipo akumnamizira kuti ali ndi ana aamuna ndi aakazi popanda kudziwa. Ali kutali Wolemekezekayo, ndipo watukuka kuzimene akusimbazo

    [101] “Iye ndiye Mlengi wathambo ndi nthaka, zingatheke bwanji kukhala ndi mwana pomwe Iye alibe mkazi? Ndipo ndi Yemwe adalenga chinthu chilichonse. Ndiponso Iye Ngodziwa zedi chinthu chilichonse

    [102] “Ameneyu ndi Allah, Mbuye wanu; palibe wina woti nkumpembedza mwa choonadi koma Iye. Mlengi wa chinthu chilichonse. Choncho, mpembedzeni. Iye ndi Muyang’aniri wa chinthu chilichonse

    [103] “Maso samufika (kuti nkumuona); koma Iye amawafika maso (amawaona pamodzi ndi eni masowo). Iye Ngodziwa zobisika kwambiri, Ngodziwa zoonekera

    [104] “(Nena iwe Mtumiki): “Ndithu umboni otsimikizika wakufikani kuchokera kwa Mbuye wanu, choncho amene atsekule maso ake nkuyang’ana ndiye kuti (zotsatira zake zabwino) zili pa iye mwini. Ndipo amene atseke maso ake zili pa iye mwini (zotsatira zake zoipa). Ndipo ine sindili muyang’anili wanu.”

    [105] “Motero tikulongosola mwatsatanetsatane zizindikiro, (kuti azindikire). Ndikuti anene: “Wachita kuphunzira (izi, si Allah amene wakuuza.” Ndipo tazibwerezabwereza chonchi) kuti tilongosole ndi kufotokoza momveka kwa anthu odziwa

    [106] “Tsata zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako. Palibe wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye. Ndipo apewe opembedza mafano

    [107] “Ndipo Allah akadafuna sakadamphatikiza (ndi mafano), ndipo sitidakuike pa iwo kukhala muyang’aniri wawo. Ndipo iwe suli muyimiliri wawo

    [108] “Ndipo usawatukwane amene akupembedza (mafano) kusiya Allah, kuopera kuti angamtukwane Allah mwamwano popanda kuzindikira. Motero taukometsera m’badwo ulionse ntchito zake. Potsiriza adzabwerera kwa Mbuye wawo, choncho, Iye adzawauza zonse zomwe adali kuchita

    [109] “Ndipo (akafiri) adalumbira Allah ndi malumbiro awo amphamvu kuti ngati chitawadzera chozizwitsa ndithu adzachikhulupirira. Nena: “Zozizwitsa zili kwa Allah (sizili mmanja mwanga). Kodi nchinthu chanji chingakudziwitseni (inu Asilamu) kuti (ngakhale) chitaza (chozizwitsacho) iwo sangakhulupirire?”

    [110] “Ndipo titembenuza mitima yawo ndi maso awo (kotero kuti sangathe kuchikhulupirira ngakhale atachiona chozizwitsacho) monga momwe sadaikhulupirire (Qur’an) poyamba ndipo tiwasiya akuyumbayumba m’machimo awo

    [111] “۞ Ndipo ngati tikadawatumizira angelo (kuti adzaikire umboni za uneneri wako), ndipo akufa nkuwayankhula, (naonso nkuvomereza kuti izi nzoona; kuonjezera apo) nkuwasonkhanitsira chinthu chilichonse pamaso pawo, sakadakhulupirira pokhapokha Allah akadafuna koma ambiri a iwo sazindikira

    [112] “Ndipo nchomwechi tidamuikira adani mneneri aliyense (omwe) ndi asatana a mu anthu ndi asatana a m’ziwanda, (omwe) amadziwitsana wina ndi mnzake mawu okometsa ncholinga chonyenga. Ndipo Mbuye wako akadafuna, sakadatha kuchita zimenezi choncho asiye ndi zimene akupeka

    [113] “Ndi kuti ipendekere ku mawu amenewo mitima ya anthu osakhulupirira tsiku la chimaliziro, ndi kuyanjana nawo (mawuo) ndikutinso apeze (machimo) omwe amawapeza

    [114] “(Nena:) “Kodi ndifune woweruza wina kusiya Allah, pomwe Iye ndi Yemwe adavumbulutsa buku kwa inu lofotokoza chilichonse?” Ndipo omwe tidawapatsa buku akudziwa kuti (Qur’an) yavumbulutsidwa ndi Mbuye wako mwachoonadi. Choncho, usakhale mwa okaikira

    [115] “Ndipo mawu a Mbuye wako akwanira moona ndi mwachilungamo. Palibe amene angathe kusintha mawu Ake. Iye Ngwakumva, Ngodziwa

    [116] “Ngati umvera ambiri amene ali pa dziko lapansi, akusokeretsa pa njira ya Allah. Satsatira koma zakungoganizira. Ndipo sali chilichonse koma akungonama

    [117] “Ndithu Mbuye wako ndi Yemwe akudziwa bwino amene asokera ku njira Yake, ndiponso Iye akudziwa bwino za oongoka

    [118] “Choncho, idyani (nyama) zomwe dzina la Allah latchulidwapo (pozizinga osati zofa zokha), ngati inu mukhulupiriradi Ayah (zizindikiro) Zake

    [119] “Mungasiirenji kudya (nyama) imene poizinga dzina la Allah latchulidwapo, pomwe wakufotokozerani momveka chomwe wachiletsa kwa inu, kupatula (mukadya choletsedwacho) mosimidwa ndi kukakamizidwa (chifukwa cha njala)? Koma ndithu ambiri akusokeretsa (ena) mwa zifuniro zawo popanda kudziwa. Ndithu Mbuye wako ndi Yemwe akudziwa bwino za olumpha malire

    [120] “Siyani machimo oonekera ndi obisika. Ndithu amene achita machimo adzalipidwa chifukwa cha zomwe adali kuchita (zoipa)

    [121] “Ndipo musadye (nyama) imene yazingidwa popanda kutchula dzina la Allah. Kutero ndikuchimwa. Ndithudi, asatana amanong’onezera abwenzi awo kuti akangane ndi inu (m’zinthu zonga zimenezi). Ngati muwamvera, ndiye kuti mukhala opembedza mafano

    [122] “Kodi yemwe adali wakufa, kenako nkumuukitsa ndi kumpangira kuunika; choncho ndi kuunikako nkumayenda kwa anthu, kodi angafanane ndi yemwe chikhalidwe chake chili mu mdima (wa umbuli) ndipo sakutha kutuluka m’menemo? Motero zakometsedwa kwa osakhulupirira (zoipa) zomwe akhala akuchita

    [123] “Chomwechonso tidaika mmudzi uli wonse akuluakulu owonongamo kuti azichitamo ndale (zoletsa anthu kuyenda pa njira ya Allah). Ndipo ndale zawo sizipweteka aliyense koma iwo eni, koma sazindikira

    [124] “Ndipo chizindikiro chikawadzera, amati: “Sitikhulupirira, mpaka tipatsidwe monga zomwe atumiki a Allah adapatsidwa.” Allah ndiamene akudziwa pamalo pomwe akuika uneneri Wake, (sikuti angapatsidwe munthu aliyense). Posachedwa kunyozeka kochokera kwa Allah ndi chilango choopsa ziwafika amene achita zoipa chifukwa cha ndale zawo zomwe akhala akuchita

    [125] “Choncho, amene Allah akufuna kumuongola, amamtsekula chifuwa chake kuti Chisilamu chilowemo, ndipo yemwe Allah akufuna kumulekelera kusokera amachichita chifuwa chake kukhala chobanika, chovutika kwambiri (kutsata Chisilamu) ngati kuti akukwera kumwamba. Umo ndi momwe Allah akuwaunjikira uve anthu omwe sakukhulupirira

    [126] “Ndipo iyi (chipembedzo cha Chisilamu) ndi njira ya Allah yoongoka. Ndithu tazifotokoza zizindikiro momveka kwa anthu okumbukira

    [127] “(Anthu abwino) adzapeza Nyumba yamtendere kwa Mbuye wawo. Iye ndi Mtetezi wawo, chifukwa cha zomwe adali kuchita

    [128] “Ndipo (akumbutse) tsiku limene adzawasonkhanitsa onse (nkuwauza): “E inu khamu la ziwanda! Ndithudi, mudatenga okutsatirani ambiri mwa anthu (powasokoneza).” Ndipo abwenzi awo mwa anthu adzati: “Mbuye wathu! Tidali kupindulitsana pakati pathu, ndipo tsopano taifikira nyengo yathu imene mudatiikira.” (Allah) adzati: “Malo anu ndi ku Moto. Mukakhala m’mmenemo nthawi yaitali, pokhapokha Allah akafuna.” Ndithu Mbuye wako Ngwanzeru zakuya, Ngodziwa kwambiri

    [129] “Chomwechi timaika chimvano pakati pawochita zoipa chifukwa cha machimo omwe adali kupeza (kuchokera m’zochita zawo zoipa)

    [130] “(Tsiku la Qiyâma adzafunsidwa): “E inu magulu a ziwanda ndi anthu! Kodi sadakudzereni atumiki ochokera mwa inu, amene amakufotokozerani zizindikiro zanga, nakuchenjezani zokumana ndi tsiku lanu ili?” Adzati: “Tadziikira umboni tokha.” Ndipo moyo wa dziko lapansi udawanyenga. Ndipo adzaziikira okha umboni kuti iwo adali osakhulupirira

    [131] “Zimenezi nchifukwa choti Mbuye wako sali woononga midzi mwachinyengo pomwe eni ake ali oiwala. (Koma ankawatumizira aneneri kuti awachenjeze ndi kuwakumbutsa)

    [132] “Ndipo onse adzakhala ndi nyota (za ulemelero) kuchokera m’zochita zawo. Ndipo Mbuye wako sali wamphwayi pa zimene akuchita

    [133] “Ndipo Mbuye wako Ngokwanira (Wolemera), Mwini chifundo. Ngati afuna angakuchotseni ndi kuwaika m’malo mwanu amene wawafuna monga momwe adakulengerani kuchokera m’mbumba ya anthu ena

    [134] “Ndithu (palibe chikaiko) zomwe mukulonjezedwa zifika. Ndipo simungathe kuzilepheretsa

    [135] “Nena: “E inu anthu anga! Chitani zanu (zimene mufuna) momwe mungathere. Nanenso ndichita zanga. Choncho mudzaziwa kuti ndani mapeto ake adzakhale ndi malo abwino. Ndithudi, sangapambane anthu ochita zoipa.”

    [136] “Ampangira Allah (amugawira) gawo m’zomera ndi ziweto zimene (Allah) adalenga. Akunena: “Gawo ili ndi la Allah.” Mkuyankhula kwawo kwachabe: “Ndipo gawo ili ndi la aja omwe tikuwaphatikiza ndi Allah.” Choncho zomwe alinga kuwapatsa aphatikizi awo, sizingafike kwa Allah. Ndipo zimene zili za Allah, ndizomwe zingafike kwa aphatikizi awo (mafano awo). Kwaipitsitsa kuweruza kwaoku

    [137] “Momwemo milungu yawo imawakometsera ambiri mwa ophatikiza Allah ndi mafano kupha ana awo (monga nsembe ya mafanowo) kuti awaononge ndikuwabweretsera chisokonezo pa chipembedzo chawo. Ndipo ngati Allah akadafuna, sakadachita zimenezo. Choncho asiye ndi izo zomwe akupeka

    [138] “Iwo akuti: “Ziweto izi ndi mbewu izi, nzoletsedwa; palibe angazidye koma amene tawafuna (kuti adye),” zonsezi mkuyankhula kwawo kwachabe. Ndipo (amanenanso): “Ziweto izi, misana yake njoletsedwa (kukwerapo).” Ndipo pa ziweto zina satchula dzina la Allah pozizinga; kungompekera bodza Iye. Ndipo posachedwa adzawalipira pa zomwe adali kupeka

    [139] “Ndipo amanenanso: “Zimene zili m’mimba mwa ziweto izi, ndi za amuna okha; ndipo nzoletsedwa kwa akazi athu.” Koma ngati chili chibudu, onse adali kugawana (amuna ndi akazi). Ndithudi, adzawalipira ndi zonena zawozo. Ndithu Iye (Allah), Ngwanzeru zakuya, Wodziwa kwambiri

    [140] “Ndithu adaluza amene adapha ana awo mwa umbuli popanda kudziwa, ndi kuletsa (chakudya) chimene Allah awapatsa, pakungompekera bodza Allah. Ndithu adasokera ndipo sadali oongoka

    [141] “Ndipo Iye (Allah) ndi amene adapanga minda (ya mitengo) yothaza ndi yosathaza; ndipo (adapanga) mitengo yakanjedza ndi mmera wazipatso zosiyanasiyana makomedwe ake ndipo adapanganso mzitona ndi makomamanga, zofanana (mmaonekedwe) ndi zosiyana (mmakomemedwe). Idyani zipatso zake pamene zikupatsa. Ndipo perekani chopereka chake tsiku lokolola (powapatsa masikini ndi ogundizana nawo nyumba). Ndipo musaziononge pakudya mopyoza muyeso. Ndithu Iye (Allah) sakonda opyoza muyeso

    [142] “Ndipo m’gulu la nyama, (Allah adalenga) zonyamulira katundu ndi zopangira choyala (bweya bwake). Idyani zimene Allah wakupatsani ndipo musatsate mapazi a satana (ndi abwenzi ake pozichita halali kapena haramu zomwe Allah sadalamule. Satana sakufunirani zabwino); ndithu iye ndi mdani wanu woonekera

    [143] “(Adakulengerani) mitundu isanu ndi itatu ya nyama (pophatikiza zazimuna ndi zazikazi); nkhosa (adalenga) ziwiri (yaimuna ndi yaikazi); mbuzi (adalenga) ziwiri (yaimuna ndi yaikazi). Nena: “Kodi Iye adakuletsani zazimuna zonse ziwiri, (mbuzi ndi nkhosa) kapena zazikazi ziwiri, (nkhosa ndi mbuzi), kapena zomwe zili m’mimba mwa zazikazi ziwirizo? Ndiuzeni mwa nzeru ngati mukunenazi nzoona (kuti Allah adatero)

    [144] “Ndipo (adalenganso) ngamira ziwiri, (yaikazi ndi yaimuna). Ng’ombe (adalenganso) ziwiri, (yaimuna ndi yaikazi). Nena: “Kodi (Iye) adakuletsani zazimuna zonse ziwiri (ngamira ndi ng’ombe), kapena zazikazi zonse ziwiri (ngamira ndi ng’ombe), kapena zomwe zili m’mimba mwa zazikazi ziwirizo? Kodi mudali mboni pamene Allah ankakulamulani izi? Kodi ndi ndani woipitsitsa kuposa amene akupekera bodza Allah kuti asokeretse anthu popanda kudziwa (malamulo a Allah)? Ndithu Allah saongola anthu ochita zoipa

    [145] “Nena: “Sindikupeza m’zimene zavumbulutsidwa kwa ine choletsedwa (kudya) kwa yemwe akufuna kudya. Pokhapokha chikakhala chakufa chokha, kapena liwende lomwe limachucha, kapena nyama ya nkhumba; chifukwa chakuti zonsezi ndi uve (ndiponso kudya zotere) ndiko kutuluka m’chilamulo cha Allah. Kapena (nyama) yozingidwa popanda kutchulapo dzina la Allah. Koma amene wasimidwa (nkudya zoterezi) popanda kukonda kapena kupyoza Malire, ndithu Mbuye wako Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha. (Wotere amamkhululukira)”

    [146] “(Izi ndi zomwe takuletsani). Naonso Ayuda tidawaletsa kudya nyama iliyonse yokhala ndi zikhadabu, ndipo ng’ombe ndi mbuzi tidawaletsa kudya mafuta ake kupatula mafuta omwe misana yake yasenza, kapena okhala m’matumbo, kapena omwe asakanikirana ndi mafupa. Tidawalipira izi chifukwa cha machimo awo. Ndithu Ife ndioona (pa zomwe tikunenazi)

    [147] “Ngati akukutsutsa (pa zimene zavumbulutsidwa), auze (mowachenjeza): “Mbuye wanu (Yemwe ngofunika kum’khulupirira ndi kutsatira malamulo ake) Ngwachifundo chambiri (kwa yemwe akumumvera, ndi yemwe akumunyoza pano pa dziko lapansi). Komatu chilango chake sichibwezedwa kwa anthu oipa.”

    [148] “Amene akuphatikiza (Allah ndi mafano) anena: “Ngati Allah akadafuna, sitikadam’phatikiza, ife ngakhale makolo athu. Ndipo sitikadaletsa chilichonse. (Choncho, izi zomwe tikuchita, Allah akuziyanja). Momwemonso adatsutsa omwe adalipo patsogolo pawo kufikira adalawa chilango chathu. Nena: “Kodi muli nako kudziwa (kokutsimikizirani zimenezi), koti mungatitulutsire (umboni wake wotsimikizira kuti Allah adakulamulani zimenezi)? Inu simutsatira china, koma zongoganizira basi. Ndipo Simukunena china koma zabodza basi.”

    [149] “Nena: “Allah ndi Yemwe ali ndi umboni wokwanira. Choncho akadafuna, akadakuongolani nonsenu.”

    [150] “Nena: “Tabweretsani mboni zanuzo zomwe zingapereke umboni kuti Allah adaletsa izi.” Choncho ngati zitapereka umboni, (mboni zawozo) usaikire nawo umboni pamodzi ndi iwo. Ndipo usatsate zofuna za omwe atsutsa zizindikiro zathu ndi amene sakhulupirira tsiku lachimaliziro; omwenso akufanizira Mbuye wawo ndi milungu yabodza

    [151] “Nena: “Idzani kuno, ndikuwerengereni zomwe Mbuye wanu wakuletsani. Musamphatikize ndi chilichonse, ndipo achitireni zabwino makolo anu; musaphe ana anu chifukwa chakuopa umphawi; ife tikupatsani rizq inu pamodzi ndi iwo; musayandikire zoyipa, zoonekera ndi zobisika; ndipo musaphe munthu yemwe Allah adaletsa (kumupha) kupatula ikapezeka njira yoyenereza (kumupha). Akukulangizani izi kuti muziike mu nzeru zanu.”

    [152] ““Ndipo musachiyandikire chuma cha mwana wamasiye, koma m’njira yabwino (monga kuchichulukitsa ndi malonda) mpaka afike pansinkhu wokwanira. Ndipo kwaniritsani mwachilungamo miyeso ya mbale ndi masikelo; sitikakamiza munthu koma chimene angathe; ndipo pamene mukunena, (popereka umboni), nenani mwachilungamo ngakhale (umboniwo) uli wokhudza achibale. Ndipo kwaniritsani lonjezo la Allah. Izi ndi zomwe akukulangizani kuti mukumbukire.”

    [153] “(Auze kuti): “Ndithu iyi ndi njira yanga yoongoka. Choncho itsateni. Ndipo musatsate njira zina zambiri kuopera kuti zingakulekanitseni ndi njira Yake, (Allah) wakulangizani izi kuti mudziteteze kuzoipa.”

    [154] “Ndipo Mûsa tidampatsa buku (kukhala) lokwaniritsa (chisomo) kwa yemwe wachita zabwino, lofotokoza chinthu chilichonse, chiongoko ndi chifundo, kuti iwo akhulupirire za kukumana ndi Mbuye wawo

    [155] “Ndipo iyi (Qur’an) ndi buku lodalitsika lomwe talivumbulutsa (kwa inu), choncho, litsateni ndi kuopa (Allah) kuti muchitiridwe chifundo

    [156] “Kuti musadzanene (tsiku la Qiyâma) kuti: “Mabuku adavumbulutsidwa pa magulu awiri omwe adalipo patsogolo pathu, (Ayuda ndi Akhrisitu); ndipo ife sitidadziwe chilichonse pa zomwe adali kuwerenga ndi kuphunzira.”

    [157] “Kapena kuti musadzati: “Likadavumbulutsidwa buku kwa ife, ndithudi, tikadakhala oongoka kuposa iwo.” Choncho, chakudzerani chizindikiro kuchokera kwa Mbuye wanu, ndi chiongoko ndi mtendere. Kodi ndani woipitsitsa kwambiri kuposa amene watsutsa zizindikiro za Allah ndi kutembenukira kutali Nazo? Tidzawalipira amene akutembenukira kutali ndi zizindikiro zathu, chilango choipa, chifukwa cha kudziika kwawo kutali

    [158] “Kodi chilipo chimene akudikira kuposa kuwadzera angelo (kudzawachotsa miyoyo yawo?) Kapena kudza Mbuye wako (tsiku la Qiyâma kuzaweruza)? Kapena kudza zina mwa zizindikiro za Mbuye wako (zomwe adati zidzadza)? Tsiku lakudza zina mwa zizindikiro za Mbuye wako, munthu (wosakhulupirira) chikhulupiliro chake (panthawiyo) sichidzamthandiza, yemwe sadakhulupirirepo kale, kapena (msilamu) yemwe sanapindule nacho chikhulupiliro chake. Nena: “Dikirani. Nafenso tikudikira.”

    [159] “Ndithudi, anthu amene achigawa Chipembedzo chawo, nakhala Mipingomipingo, iwe Siuli nawo pachilichonse. Ndithu zotsatira zawo zili kwa Allah, (ndi yemwe adzawalanga. Ndipo panthawi yowalanga) adzawauza zomwe adali kuchita

    [160] “Amene wachita chabwino alipidwa zabwino khumi zofanana ndi icho. Ndipo amene wachita choipa sadzalipidwa koma chonga icho (popanda kuonjezera). Ndipo iwo sadzaponderezedwa

    [161] “Nena: “Ndithudi, ine Mbuye wanga wandiongolera ku njira yoongoka, kuchipembedzo cholingana, chomwe ndi chipembedzo cha Ibrahim, yemwe adali wolungama. Sadali mwa ophatikiza (Allah ndi mafano)

    [162] “Nena: “Ndithudi, Swala yanga, mapemphero anga onse, moyo wanga, ndi imfa yanga, (zonse) nza Allah, Mbuye wa zolengedwa zonse.”

    [163] ““Alibe wothandizana naye. Izi ndi zomwe ndalamulidwa, ndipo ine ndine woyamba mwa Asilamu (ogonjera Allah).”

    [164] “Nena: “Kodi ndifune mbuye wina kusiya Allah, pomwe Iye ndi Mbuye wa chinthu chilichonse? Ndipo mzimu uliwonse siuchita choipa koma ukudzichitira wokha. Mzimu wosenza machimo siudzasenza machimo a mzimu wina. Kenako kobwerera kwanu (nonse) ndi kwa Mbuye wanu, (Allah), ndipo adzakuuzani zomwe mudali kusiyana.”

    [165] “Ndipo Iye ndi Yemwe wakuchitani kukhala am’lowam’malo pa dziko (kulowa m’malo mwa anzanu omwe adaonongeka). Ndipo wawatukula pa ulemelero (ndi pa chuma) ena a inu pamwamba pa ena kuti akuyeseni pa zomwe wakupatsani. (Amene apatsidwa chuma ndi ulemelero athandize amene sadapatsidwe. Ndipo amene sadapatsidwe apirire asalande chinthu chamwini). Ndithudi, Mbuye wako Ngwachangu pokhaulitsa. Ndiponso Iye Ngokhululuka kwabasi Ngwachisoni chosatha

    Malo Otalika

    Surah 7

    [1] “Alif-Lâm-Mîm-Sad

    [2] “(Iyi Qur’an ndi) buku (lopatulika) lomwe lavumbulutsidwa kwa iwe. Choncho chifuwa chako chisabanike ndi ilo (poopa kufikitsa mawu ake kwa anthu kuti angakuyese wabodza;) kuti uwachenjeze nalo (otsutsa) ndi kuti likhale chikumbutso kwa okhulupirira (kuti aonjezere chikhulupiliro chawo)

    [3] “Tsatirani zomwe zavumbulutsidwa kwa inu kuchokera kwa Mbuye wanu, ndipo musawatsatire omwe sali Allah powayesa atetezi (anu). Ndizochepa zimene mumazikumbukira

    [4] “Ndimidzi yambiri imene tidaiononga ndipo chilango Chathu chidaidzera nthawi ya usiku, kapena usana iwo atagona tulo tamasana (akupumula monga momwe zinawachitikira anthu a Loti ndi anthu a Shuaib)

    [5] “Ndipo sikunali kulira kwawo pamene chinawafika chilango chathu koma kunena (ndi kuvomereza): “Ndithudi, ife tinali ochita zoipa.” (Koma kuvomereza kwawoko sikunawapindulire kanthu)

    [6] “Mtheradi tidzawafunsa (anthu) amene anatumiziridwa (atumiki), naonso atumikiwo tidzawafunsa

    [7] “Tsono tidzawauza mozindikira bwino-bwino (chilichonse chimene ankachita). Ndipo sitidali kutali (nawo pamene ankachita zochita zawo)

    [8] “Ndipo sikero (yoyezera zochita za anthu) tsiku limenelo idzakhala yoona (yopanda chinyengo). Choncho, amene idzalemere miyeso yake (ya zabwino), iwowo ndiwo opambana

    [9] “Ndipo amene idzapepuke miyeso yawo (ya zinthu zawo zabwino), iwo ndi amene ataya pachabe moyo wawo chifukwa cha kuzichitira zosalungama zizindikiro Zathu

    [10] “Ndithudi tinakupatsani mphamvu yokhalira pa dziko, ndipo takupangirani m’menemo zinthu zofunika pa moyo wanu. Koma kuyamika kwanu mpang’ono

    [11] “Ndithudi, tinakulengani, kenako tidakukonzani (pokupatsani ziwalo) ndi kunena kwa angelo kuti: “Mgwadireni Adam.” Ndipo adamgwadira kupatula Iblis, sadali mwa ogwada

    [12] “(Allah) adati: “Nchiyani chakuletsa kumgwadira pamene ndakulamula?” (Satana) anati: “Ine ndine wabwino kuposa iye. Ine munandilenga ndi moto koma iye mudamulenga ndi dongo.”

    [13] “(Allah) adati: “Choncho, choka m’menemo ndi kutsikira pansi. Sikofunika kwa iwe kudzitama m’menemo. Tuluka, ndithu iwe ndiwe mmodzi wa onyozeka.”

    [14] “(Satana) adati: “Ndipatseni nthawi mpaka tsiku limene adzaukitsidwa (akapolo anu ku imfa).”

    [15] “(Allah) adati: “Ndithudi iwe ndi mmodzi wa opatsidwa nthawi.”

    [16] “Iye (chifukwa cha njiru yake yoopsa pa Adam) adati: “Tsono chifukwa chakuti mwandichita ine kukhala wopotoka, ndidzawakhalira (akapolo Anu ndi kuwabisalira) pa njira Yanu yoongoka (ndi cholinga chowasokeretsa).”

    [17] “Kenako ndidzawadzera (mbali ya) kutsogolo kwawo, m’mbuyo mwawo, kumbali yakumanja kwawo ndi kumanzere kwawo, mwakuti simudzapeza ambiri a iwo oyamika

    [18] “(Allah) adati: “Tuluka m’menemo, uli wonyozeka ndi wothamangitsidwa. Amene adzakutsata iwe mwa iwo, ndithudi, (ndikamponya ku Moto). Ndipo ndikaidzadzitsa Jahannam ndi inu nonse.”

    [19] “(Kenako Allah adanena kwa Adam) “E iwe Adam! Khala ndi mkazi wako m’Munda wamtendere (sangalalani ndi zomwe zili m’menemo), idyani paliponse pamene mwafuna. Koma mtego uwu musawuyandikire kuopera kuti mungakhale m’gulu la odzichitira okha zoipa.”

    [20] “Choncho satana adawanong’oneza (zoipa) kuti awaonetsere zomwe zidabisika kwa iwo za maliseche awo. Ndipo (satana) adati: “Mbuye wanu sadakuletseni mtengo uwu, koma pachifukwa chakuti mungasanduke angelo awiri, kapena kuti mungakhale okhala nthawi yaitali.”

    [21] “Ndipo adawalumbilira onse awiri kuti: “Ndithudi, ine ndine mmodzi mwa olangiza (ndikukufunirani zabwino).”

    [22] “Tero adawakopa mwachinyengo. Ndipo pamene adalawa zipatso za mtengowo umaliseche wawo udaoneka kwa iwo nayamba kudziphatika masamba (a mitengo) a m’mundamo. Ndipo Mbuye wawo adawaitana (mowadzudzula) nati: “Kodi sindinakuletseni mtengowu ndi kukuuzani kuti satana ndi mdani wanu woonekeratu?”

    [23] “Iwo (Adam ndi mkazi wake) adati (modzichepetsa): “E Mbuye wathu! Tadzichitira tokha zoipa, ngati simutikhululukira ndi kuchita nafe chifundo ndiye kuti tikhala mwa otaika.”

    [24] “(Allah) adati: “Tsikani pansi uku pali chidani pakati panu. Ndipo padziko lapansi ndipokhala panu ndi kusangalala kwanu mpaka m’nthawi yoikidwayo.”

    [25] “(Allah) adatinso: “Muzikakhala moyo pamenepo, ndipo muzikafa pamenepo; ndipo momwemo mudzatulutsidwa (mutauka kwa akufa).”

    [26] “E inu ana a Adam! Ndithu tatsitsa kwa inu chovala chobisa umaliseche wanu ndi chodzikongoletsera nacho. Koma chovala choopa nacho Allah (pakudziyeretsa ku zoletsedwa) chimenecho ndicho chabwino koposa. Zimenezo ndi zizindikiro za (chisomo cha) Allah kuti iwo akumbukire

    [27] “E inu ana a Adam! Satana asakusokonezeni monga momwe adawatulutsira makolo anu m’Munda wamtendere ndi kuwavula onse awiri chovala chawo kuti awasonyeze umaliseche wawo. Ndithu iye ndi mtundu wake akukuonani pomwe inu simukuwaona. Ndithu asatana tawachita kukhala abwenzi a osakhulupirira

    [28] “Ndipo (osakhulupirira) akachita chauve amanena: “(Ichi) tidawapeza nacho makolo athu (akuchichita), ndiponso Allah watilamula chimenechi.” Nena: “Ndithu Allah salamula zonyansa. Kodi mukumunenera Allah zomwe simukuzidziwa?”

    [29] “Nena: “Mbuye wanga walamula chilungamo; ndiponso (wandiuza kuti ndikuuzeni kuti) lungamitsani nkhope zanu (kwa Iye) m’nthawi ya Swala iliyonse, ndipo mpembedzeni Iye Yekha momuyeretsera chipembedzo monga Iye adakulengani pachiyambi, momwemonso mudzabwerera kwa Iye.”

    [30] “Gulu lina waliongola, pomwe gulu lina patsimikizika pa ilo kusokera chifukwa chakuti iwo adasankha asatana kukhala atetezi (awo) kusiya Allah; ndipo akuganiza kuti iwo ngoongoka

    [31] “E inu ana a Adam! Tengani (valani) zovala zanu zabwino pamene mukukapemphera Swala iliyonse ndipo idyani ndi kumwa; koma musapyoze muyeso. Iye (Allah) sakonda opyoza muyeso (oononga)

    [32] “Nena: “Ndani waletsa zokongoletsa za Allah (zovala), zomwe Iye (Allah) adawatulutsira akapolo Ake ndi zakudya zabwino?” Nena: “Zinthu zimenezo nzololedwa kwa amene akhulupirira (Asilamu) pamoyo wa pa dziko lapansi. (Zidzakhala) zawozawo tsiku la chimaliziro. M’menemo ndi momwe tikulongosolera Ayah (Zathu) kwa anthu ozindikira.”

    [33] “Nena (kwa iwo): “Ndithu Mbuye wanga waletsa zinthu zauve zoonekera ndi zobisika, ndi machimo, ndi kuwukira (atsogoleri) popanda choonadi, ndi kumphatikiza Allah ndi chomwe sadachitsitsire umboni (wakuti chiphatikizidwe ndi Iye); ndiponso (waletsa) kumunenera Allah zimene simukuzidziwa.”

    [34] “M’badwo ulionse uli ndi nthawi yakeyake (yofera). Ndipo nthawi yawo ikadza sangaichedwetse ngakhale ola limodzi, ndiponso sangaifulumizitse

    [35] “E inu ana a Adam! Akakudzerani Atumiki ochokera mwa inu namakuuzani zivumbulutso Zanga, (avomereni), choncho omwe adzitchinjiriza ku zoletsedwa ndi kuchita zabwino, sipadzakhala mantha pa iwo ndiponso sadzadandaula

    [36] “Ndipo amene atsutsa zivumbulutso zathu nadzitukumula nazo, awo ndi anthu a ku Moto, adzakhala mmenemo nthawi yaitali

    [37] “Kodi ndani woipitsitsa koposa munthu wopekera bodza Allah kapena wotsutsa zivumbulutso Zake? Iwo gawo (lachakudya chimene) adawalembera liwafika (pano pa dziko lapansi ngakhale kuti ngosakhulupirira mwa Allah). Kufikira pomwe adzawadzera atumiki Athu (angelo kudzatenga miyoyo yawo), nawapatsadi imfa uku akunena: “Kodi zili kuti zija munkazipembedza kusiya Allah?” Adzati: “Zatisowa.” Ndipo adzadzichitira okha umboni kuti iwo adali okana (Allah)

    [38] “(Allah) adzati (pa tsiku la chiweruziro): “Lowani ku Moto pamodzi ndi mibadwo imene idamuka kale (inu musanabwere) yochokera m’ziwanda ndi mu anthu. M’badwo uliwonse pamene uzikalowa, udzatembelera unzake, kufikira pamene onse adzasonkhana m’menemo. Adzanena apambuyo kwa oyambilira awo: “Mbuye wathu! Awa, adatisokeretsa. Apatseni chilango cha Moto chochuluka.” (Allah) adzanena: “Aliyense mwa inu akhala ndi chilango chochuluka; koma izi inu simukudziwa.”

    [39] “Ndipo oyamba awo adzati kwa otsiriza awo: “Inunso mudalibe ubwino woposa ife; choncho, lawani chilango cha zomwe mudapeza (m’zochitachita zanu).”

    [40] “Ndithudi, amene akutsutsa zivumbulutso Zathu nadzitukumula nazo (pakukana kuzitsata), sadzatsekulidwa kwa iwo makomo a kumwamba, ndipo sadzalowa ku Munda wamtendere mpaka ngamira idzalowe pa bowo la singano. Umo ndimomwe timawalipirira anthu ochimwa

    [41] “Moto wa Jahannam ndi mphasa yawo; ndipo pamwamba pawo adzakhala ndi (chofunda cha Moto) chowaphimba. Umo ndimomwe Tikuwalipirira anthu osalungama

    [42] “Ndipo amene akhulupirira ndikumachita zabwino, sitikakamiza munthu aliyense koma chimene angachithe, awo ndiwo anthu a ku Munda wamtendere. M’menemo iwo akakhala nthawi yaitali

    [43] “Ndipo tidzachotsa kusakondana (komwe kudali) m’mitima mwawo; (adzakhala okondana ngakhale pa dziko lapansi adali odana), uku pansi ndi patsogolo pawo mitsinje ikuyenda; ndipo adzanena (m’kuthokoza kwawo): “Kuyamikidwa konse nkwa Allah, Yemwe adatitsogolera ku ichi (chomwe chatidzetsera mtendere). Sitikadaongoka pakadapanda Allah kutiongola. Atumiki a Mbuye wathu adadza ndi choonadi.” Ndipo adzaitanidwa (ndi kuuzidwa kuti): “Uwu ndi Munda wamtendere umene mwapatsidwa chifukwa cha zomwe mudali kuchita.”

    [44] “Anthu a ku Munda wamtendere adzaitana anthu aku Moto (adzanena kuti): “Ndithudi ife tapeza zimene Mbuye wathu adatilonjeza kuti nzoona. Kodi nanunso mwapeza zomwe Mbuye wanu adakulonjezani kuti nzoona?” (Anthu a ku Moto) adzanena: “Inde.” Choncho wolengeza pakati pawo adzalengeza kuti: “Matembelero a Allah ali pa anthu ochita zoipa.”

    [45] ““Omwe ankaletsa anthu kuyenda pa njira ya Allah nafuna kuikhotetsa njirayo (kuti ioneke yokhota pamaso pa anthu), omwenso sadakhulupirire za tsiku lachimaliziro.”

    [46] “Ndipo pakati pawo (pa anthu a ku Munda wamtendere ndi a ku Moto) padzakhala chotchinga. Ndipo pamwamba pachikweza padzakhala anthu ena (ofanana ntchito zawo zabwino ndi zoyipa) omwe akazindikira onse (a ku Jannah ndi ku Moto), ndi zizindikiro zawo. Ndipo akawaitana anthu a ku Jannah (kuti): “Salaamun Alayikum (mtendere ukhale pa inu).” Koma asanailowe uku ali ndi chikhulupiliro (kuti ailowa)

    [47] “Ndipo maso awo akakatembenuzidwa (kuyang’ana) ku mbali ya anthu a ku Moto, adzanena: “Mbuye wathu musatiike pamodzi ndi anthu ochita zoipa. (Tikhululukireni zolakwa zathu. Tilowetseni ku Jannah).”

    [48] “Ndipo anthu aja apachikweza adzawaitana anthu (a ku Moto), adzawadziwa ndi zizindikiro zawo, nati: “Sikudakuthandizeni kuchuluka kwanu kuja, ngakhale zija mudali kudzitama nazo.”

    [49] ““Kodi awa siaja munkawalumbilira kuti Allah sangawaninkhe chifundo? (Taonani tsopano, auzidwa kuti): “Lowani ku Jannah. Palibe mantha pa inu, ndiponso simudandaula.”

    [50] “Naonso anthu a ku Moto adzaitana a ku Jannah (ndikuwauza kuti): “Tatipungulirani madzi kapena chinthu chimene Allah wakupatsani.” (Anthu a ku Jannah) adzanena kuti:“Ndithu Allah waletsa kupereka zonse ziwirizo kwa osakhulupirira.”

    [51] “Omwe adachita chipembedzo chawo kukhala zinthu zopanda pake ndiponso masewero; ndipo udawanyenga moyo wa m’dziko. Choncho, lero Ifenso tiwaiwala (tiwaleka ku Moto) monga momwe adakuiwalira kukumana ndi tsiku lawo ili, ndi chifukwa chakukana kwawo zivumbulutso Zathu

    [52] “Ndithudi, tawabweretsera buku lomwe talifotokoza mwanzeru, lomwe ndichiongoko ndi chifundo kwa anthu okhulupirira

    [53] “Kodi chiliponso chomwe akudikilira osati zotsatira zake (za bukulo)? Ndipo tsiku lakudza zotsatira zake, adzanena amene kale sadalilabadire: “Ha! Atumiki a Mbuye wathu adadzadi ndi choonadi (tsopano tikuvomereza). Kodi tingakhale nawo ife aomboli oti atiombole (kwa Mbuye wathu), kapena tingabwezedwe kuti tikachite (zabwino) osati zija tinkachita?” Zoonadi adziononga okha, ndipo zawasowa zabodza zomwe adali kupeka

    [54] “Ndithudi, Mbuye wanu ndi Allah Yemwe adalenga thambo ndi nthaka m’masiku asanu ndi limodzi. Kenako adakhazikika pa Arsh (Mpando Wake wachifumu). Amauchita usiku kuti uvindikire usana, zimatsatana mwamsangamsanga. Ndipo dzuwa ndi mwezi ndi nyenyezi nzofewetsedwa, (zikuyenda mogonjera) ndi Lamulo Lake. Dziwani kuti kulenga ndi kulamula Nkwake. Ndithudi, watukuka Allah Mbuye Wazolengedwa (zonse)

    [55] “Mpempheni Mbuye wanu modzichepetsa ndi mwakachetechete. Ndithu Iye sakonda opyola malire

    [56] “Ndipo musaononge pa dziko pambuyo popakonza. Mpempheni (Allah) mwamantha ndi mwakhumbo. Ndithu chifundo cha Allah chili pafupi kwa (anthu Ake ) ochita zabwino

    [57] “Ndipo Iye ndi Yemwe amatumiza mphepo kuti ikhale nkhani yosangalatsa patsogolo pa chifundo Chake (mvula), kufikira mphepoyo itasenza mitambo yolemera yomwe tikuitumiza ku dziko lakufa. Ndipo kupyolera mwa iyo tikutsitsa madzi ndipo ndimadzio tikutulutsa mitundu yonse ya zipatso. Momwemo ndimo tidzawaukitsira akufa. (Zonsezi) nkuti inu mukumbukire

    [58] “Ndipo m’nthaka yabwino umatuluka mmera wake (mwachangu) mwachilolezo cha Mbuye wake. Ndipo nthaka yomwe ili yoipa siitulutsa (mmera wake) koma movutikira. M’menemo ndi momwe Tikuchifotokozera chivumbulutso momveka kwa anthu oyamika

    [59] “Ndithudi, tidamtumiza Nuh kwa anthu ake. (Iye) adati: “E inu anthu anga! Pembedzani Allah. Inu mulibe mulungu wina koma Iye. Ndithu ine ndikukuoperani chilango cha tsiku lalikulu.”

    [60] “Akuluakulu a mwa anthu ake adati: “Ndithu ife tikukuona kuti uli m’kusokera koonekera (potiletsa izi zomwe tidawapeza nazo makolo athu).”

    [61] “(Iye) adati: “E anthu anga! Palibe kusokera mwa ine. Koma ine ndine Mtumiki wochokera kwa Mbuye wa zolengedwa!”

    [62] ““Ndikufikitsa kwa inu uthenga wa Mbuye wanga. Ndiponso ndikukulangizani; ndipo ndikudziwa zochokera kwa Allah zomwe inu simukuzidziwa.”

    [63] ““Kodi mukudabwa kukudzerani ulaliki wochokera kwa Mbuye wanu kudzera mwa munthu wa mwa inu, (yemwe wadza) kuti akuchenjezeni ndi kuti muope (Allah), ndikutinso muchitiridwe chifundo?”

    [64] “Koma adamtsutsa. Choncho, tidampulumutsa iye ndi amene adali naye pamodzi m’chombo. Ndipo tidawamiza aja adatsutsa zizindikiro Zathu. Ndithudi, iwo adali anthu akhungu

    [65] “Ndipo kwa Âdi (tidaatumizira) m’bale wawo Hûd. Adati: “E inu Anthu anga! Mpembedzeni Allah. Mulibe mulungu wina koma Iye basi. Kodi simungaope?”

    [66] “Akuluakulu a mwa anthu ake omwe sadakhulupirire adanena: “Ife tili kukuona kuti uli mu uchidzete, ndipo ife tikukuganizira kuti ndiwe m’modzi wa a bodza.”

    [67] “(Iye) adati: “E inu anthu anga! Palibe uchidzete mwa ine. Koma ine ndine Mtumiki wochokera kwa Mbuye wa zolengedwa.”

    [68] ““Ndikufikitsa kwa inu uthenga wa Mbuye wanga. Ndipo ine ndine mlangizi wanu (wokufunirani zabwino), wokhulupirika.”

    [69] ““Kodi mukudabwa pokudzerani ulaliki kuchokera kwa Mbuye wanu kupyolera mwa munthu wochokera mwa inu kuti akuchenjezeni? Kumbukirani (mtendere wa Allah) pamene adakuikani kukhala amlowam’malo pambuyo pa anthu a Nuh, ndipo akuonjezerani m’kalengedwe kukhala a misinkhu itali-itali ndi amphamvu. Kumbukiraninso mtendere wa Allah (pothokoza) kuti mupambane.”

    [70] “Iwo adati: “Kodi watidzera kuti timpembedze Allah Yekha ndikusiya zomwe ankapembedza makolo athu? Tibweretsere chimene ukutilonjezacho ngati uli mmodzi mwa onena zoona.”

    [71] “(Iye) adati: “Palibe chikaiko, chilango ndi mkwiyo wochokera kwa Mbuye wanu zakugwerani. Kodi mukukangana nane pa za maina (a mafano) omwe mudawatcha inu ndi makolo anu, pomwe Allah sadatsitse umboni uliwonse pa milungu yanu yabodzayo? Choncho, dikirani. Inenso ndili pamodzi nanu mwa odikira.”

    [72] “Choncho tidampulumutsa pamodzi ndi amene adali naye mwa chifundo chathu, ndipo tidadula mizu ya omwe adatsutsa zivumbulutso Zathu. Ndipo sadali okhulupirira

    [73] “Ndipo kwa Asamudu tidamtumiza m’bale wawo Swaleh. Adati: “E inu anthu anga! Gwadirani Allah; inu mulibe mulungu wina koma Iye basi. Chizindikiro chochokera kwa Mbuye wanu chadza kwa inu. Iyi ndi ngamira ya Allah monga chisonyezo chanu (chizizwa chanu), choncho, isiyeni izidya m’dziko la Allah, ndipo musaikhudze ndi choipa kuopera kuti chingakugwereni chilango chowawa kwambiri.”

    [74] ““Ndipo kumbukirani pamene (Allah) adakupangani kukhala amlowammalo pambuyo pa mtundu wa Âdi. Ndipo adakukhazikani pa dziko (mwa ubwino). Mukudzimangira nyumba zikuluzikulu mchigwa, ndiponso kusema ndi kuboola mapiri kukhala nyumba. Choncho kumbukirani mtendere wa Allah, ndipo musaononge pa dziko pofalitsa chisokonezo.”

    [75] “Adanena akuluakulu omwe adali odzitukumula mwa anthu ake kuuza omwe adaponderezedwa kwa amene adakhulupirira mwa iwo: “Kodi muli ndi chitsimikizo kuti Swalih ngotumizidwa ndi Mbuye Wake (wapatsidwa utumiki)?” (Iwo) Adati: “Ndithu ife tikukhulupirira zomwe watumidwa nazo (kuzifikitsa kwa ife).”

    [76] “Omwe adadzitukumula adati: “Ndithu ife tikuzikana zomwe mwazikhulupirirazo.”

    [77] “Choncho adaipha (adaizinga) ngamira ndi kunyoza lamulo la Mbuye wawo, nati: “E iwe Swaleh! Tibweletsere (chilango) chimene wakhala ukutilonjeza ngati ulidi mmodzi wa otumidwa.”

    [78] “Choncho, chivomerezi chidawagwira mwadzidzidzi, adapezeka ali akufa chigwadire m’nyumba zawo

    [79] “Tero, Swalih adawasiya (nkupita kwina kwake) uku akunena: “E anthu anga! Ndidafikitsadi uthenga wa Mbuye wanga kwa inu. Ndipo Ndidakuchenjezani ndi kukulangizani. Koma inu simufuna alangizi.”

    [80] “Nayenso Luti (tidamtuma, ndipo kumbuka) pamene adati kwa anthu ake: “Kodi mukuchita chonyansa chomwe sadakutsogolereni aliyense kuchichita mwa anthu akale m’zolengedwa zonse?”

    [81] ““Ndithu inu mukuwadzera amuna mwa chilakolako kusiya akazi! Ndithudi, inu ndinu anthu olumpha malire.”

    [82] “Kuyankha kwa anthu ake sikudali kwa mtundu wina koma kuti: “Apirikitseni m’mudzi wanu. Ndithu iwowo ndi anthu odziyeretsa. (Choncho akhaliranji m’mudzi wa uve? Akakhale ndi anzawo ochita zaukhondo).”

    [83] “Koma tidampulumutsa iye ndi banja lake, kupatula mkazi wake; adali m’gulu la otsalira m’mbuyo (adaonongeka)

    [84] “Ndipo tidatsakamula pa iwo chimvula (cha miyala). Choncho, taona mmene adaliri mapeto a anthu oipa

    [85] “Nakonso kwa anthu aku Madiyan, (tidamtumiza) m’bale wawo Shuaib. Adati: “E inu anthu Anga! Gwadirani Allah. Mulibe mulungu wina koma Iye basi. Umboni owonekera wadza kuchokera kwa Mbuye wanu. Choncho pimani miyeso (yanu ya mbale) ndi masikelo mwachilungamo. Musawachepetsere anthu zinthu zawo; ndipo musaononge pa dziko pamhuyo polikonza. Kutero ndi kwabwino kwa inu ngati muli okhulupiriradi.”

    [86] ““Ndipo musamawakhalire anthu pa njira iliyonse mowabisalira ndi kumawaopseza, ndi kuwatsekereza kuyenda pa njira ya Allah amene amkhulupirira Iye, ndi kufuna kuikhotetsa njirayo (kuti anthu asaitsate). Ndipo kumbukirani pamene mudali ochepa nakuchulukitsani. Ndipo onani momwe adalili mapeto a owononga.”

    [87] ““Ndipo ngati pali gulu la anthu mwa inu amene akhulupirira uthenga umene ndatumidwa nawo, ndi gulu la anthu limene silidakhulupirire, pirirani mpaka Allah aweruze pakati pathu. Iye Ngwabwino poweruza kuposa oweruza.”

    [88] “۞ Akuluakulu omwe adadzikuza mwa anthu ake, adanena: “Tikupirikitsa, iwe Shuaib m’mudzi mwathu muno ndi amene akhulupirira pamodzi nawe, pokhapokha mutabwerera ku chipembedzo chathu.” (Iye) adati: “Kodi ngakhale kuti tikuchida?”

    [89] ““Ngati titabwerera m’chipembedzo chanu pambuyo potipulumutsa Allah m’menemo, ndiye kuti tampekera Allah bodza. Sikungatheke kwa ife kubwerera m’chipembedzo chimenecho pokhapokha atafuna Allah, Mbuye wathu. Mbuye wathu Ngodziwa zonse. Ndipo kwa Allah Yekha ndiko tayadzamira. Mbuye wathu! Weruzani mwa choonadi pakati pathu ndi pakati pa anthu athu. Inu Ngabwino poweruza kuposa oweruza.”

    [90] “Ndipo akuluakulu mwa anthu ake omwe sadakhulupirire adati: “Ngati mutsatira Shuaib ndithudi pamenepo ndiye kuti mukhala otayika.”

    [91] “Choncho chivomerezi chidawaononga mwadzidzidzi motero adapezeka akufa chigwadire mnyumba zawo

    [92] “Amene adamutsutsa Shuaib adakhala ngati sadakhalepo m’mudzimo. Amene adamutsutsa Shuaib ndi omwe adali otayika

    [93] “(Pamene nthawi yakuonongeka kwawo idayandikira, Shuaib adatuluka m’mudzimo pamodzi ndi aja adakhulupirira) nawasiya oipawo (kunka kutali) uku akunena: “E inu anthu anga! Ndinafikitsadi uthenga wa Mbuye wanga ndipo ndinakuchenjezani ndiye nchotani ndidandaule za anthu okanira.”

    [94] “Ndipo palibe pamene tidamtuma mneneri aliyense m’mudzi uliwonse (nkumukana) koma tinkawalanga eni mudziwo ndi masautso ndi mavuto kuti afatse (ndi kulambira Allah; koma ayi adakanika)

    [95] “Kenako tinasintha pamalo pa choipa pobweretsapo chabwino, (tidawachotsera masautso ndi mavuto ngakhale sadali okhulupirira) mpaka anachuluka, ndi kuchulukanso chuma chawo; anayamba kunena kuti: “Masautso ndi mavuto adawakhudzaponso makolo athu. (Zoterezi sizachilendo kwa ife).” Choncho tidawaononga mwadzidzidzi asakudziwa

    [96] “Chikhala kuti eni midziwo adakhulupirira naopa (Allah pamene aneneri adawadzera), tikadawatsekulira madalitso ochokera kumwamba ndi pansi. Koma adatsutsa (aneneri) ndipo tidawaononga chifukwa cha zoipa zomwe ankachita

    [97] “Kodi anthu a m’mizinda (iyo momwe muli anthu oipa) ali ndi chitetezo cholimba kuti chilango chathu sichingawadzere usiku iwo ali mtulo

    [98] “Kapena anthu a m’mizindayo ali ndi chitetezo cholimba kuti chilango Chathu sichingawafike masana uku iwo akusewera

    [99] “Kodi akudziika pa chitetezo ku chilango cha Allah? Sangadziike pa chitetezo ku chilango cha Allah kupatula anthu otayika basi

    [100] “Kodi sadadziwe awa omwe alandira dziko molowa mmalo pambuyo pa eni dzikolo (anthu akale) kuti tikadafuna tikadawaika m’masautso chifukwa cha machimo awo ndi kuwadinda mitima yawo kotero iwo sakadamva (kanthu)

    [101] “Iyo ndi midzi (ikuluikulu) yomwe tikukusimbira iwe zina mwa nkhani zake. Ndithudi, adawadzera atumiki awo ndi zizindikiro (zoonekera poyera zosonyeza kuti iwo ndi atumiki a Allah). Koma sadali oti nkukhulupirira pa zomwe adazitsutsapo kale. Umo ndi mmene Allah amadindira ndi kuitseka mitima ya osakhulupirira (kotero kuti sangathandizike ndi malangizo a mtundu uliwonse)

    [102] “Ndipo ambiri a iwo sitidawapeze akukwaniritsa lonjezo lililonse koma tidawapeza ambiri a iwo ali opandukira (chilamulo cha Allah)

    [103] “Kenako pambuyo pawo (aneneriwo) tidamtumiza Mûsa pamodzi ndi zizindikiro Zathu kwa Farawo ndi nduna zake, koma adazikana (zizindikirozo). Choncho taona momwe adalili mathero aoononga

    [104] “Ndipo Mûsa adati: “E iwe Farawo! Ndithu ine ndine mthenga wochokera kwa Mbuye wa zolengedwa zonse.”

    [105] ““Ndikofunika kwa ine kuti ndisamnenere Allah chilichonse koma choonadi basi. Ndithu ndakudzerani ndi chizindikiro choonekera kuchokera kwa Mbuye wanu. Choncho, aleke ndinke nawo ana a Israyeli.”

    [106] “(Farawo) adati: “Ngati wadza ndi chizindikiro, bwera nacho (tichione), ngati iwe ulidi mmodzi wa onena zoona.”

    [107] “Choncho adaponya ndodo yake pansi. Mwadzidzidzi, idasanduka njoka yooneka

    [108] “Ndipo adatulutsa dzanja lake pompo lidakhala loyera, lowala kwa oliona

    [109] “Nduna za mwa anthu a Farawo zidati: “Ndithu uyu ndi wamatsenga wodziwa (kwambiri zamatsenga).”

    [110] ““Akufuna kukusamutsani mdziko mwanu. Nanga mukulangiza zotani?”

    [111] “(Iwo) adati (kwa Farawo): “Muleke pang’ono iye ndi m’bale wakeyu (usawaphe); ndipo tumiza osonkhanitsa m’mizinda kuti akusonkhanitsire (amatsenga onse akuluakulu).”

    [112] ““Kuti akubweretsere wamatsenga aliyense wodziwa kwambiri.”

    [113] “Amatsenga adadza kwa Farawo; nati: “Kodi ife tipeza malipiro ngati titapambana?”

    [114] “(Farawo) adati: “Inde, ndipo mudzakhala mwa oyandikitsidwa (mudzakhala nduna zanga).”

    [115] “(Amatsenga) adati: “E iwe Mûsa! Kodi uyamba kuponya ndiwe (matsenga ako pamaso pa anthu), kapena ife tikhale oyambilira kuponya?”

    [116] “Mûsa adati: “Ponyani.” Choncho pamene adaponya adalodza maso a anthu ndikuwaopseza. Ndipo adadza ndi matsenga aakulu zedi

    [117] “Ndipo tidamzindikiritsa Mûsa ndi chivumbulutso (kuti): “Ponya ndodo yako.” Pompo iyo idameza zamatsengazo

    [118] “Choncho, choonadi chidatsimikizika, ndipo zidapita pachabe zomwe ankachita

    [119] “Choncho adagonjetsedwa pamenepo, nakhala onyozeka

    [120] “Ndipo amatsenga adadzigwetsa uku akulambira (Allah)

    [121] “Adati: “Takhulupirira Mbuye wa zolengedwa zonse.”

    [122] ““Mbuye wa Mûsa Ndi Harun.”

    [123] “Farawo adati: “Mwamkhulupirira chotani iye ndisanakupatseni chilolezo? Ndithu iyi ndi ndale yomwe mwaichita mu mzindamu (inu ndi Mûsa) kuti muwatulutsemo eni mzindawo. Koma posachedwa mudziwa (chimene ndikuchiteni).”

    [124] ““Ndithudi, nditseteka manja anu ndi miyendo yanu mosinthanitsa; (kudula dzanja lakudzanjadzanja ndi mwendo wa kumanzere, kapena dzanja la kumanzere ndi mwendo wakudzanjadzanja). Kenako ndikupachikani nonsenu.”

    [125] “(Iwo) adati: “Ndithu ife kwa Mbuye wathu ngobwerera.”

    [126] ““Komatu palibe choipa chimene waona mwa ife kupatula kuti takhulupirira zizindikiro za Mbuye wathu pamene zatidzera. E Mbuye wathu! Titsanulireni chipiliro, ndipo tipatseni imfa uku tili Asilamu (ogonjera Inu).”

    [127] “Ndipo nduna za mwa anthu a Farawo zidati (kwa Farawo): “Kodi umuleka Mûsa ndi anthu ake kuti abwere ndi chisokonezo m’dziko, ndi kuti akusiye iwe ndi milungu yako (yomwe adatilangiza makolo athu kuti tipembedze pamodzi ndi iwe)? (Farawo) Adati: “Tipha ana awo achimuna ndikuwasiya amoyo (ana awo) achikazi. Ndithudi ife pa iwo tili ndi mphamvu zowagonjetsera.”

    [128] “Mûsa adauza anthu ake: “Pemphani chithandizo kwa Allah, ndipo pirirani. Ndithu dzikoli ndi la Allah; amalipereka kwa amene wamfuna mwa akapolo Ake. Ndipo mapeto abwino nga anthu olungama.”

    [129] “(Iwo) adati: “Takhala tikuzunzidwa usanatidzere ndiponso (tsopano) pamene watidzera.” (Mûsa) adati: “Mwina Mbuye wanu amuononga mdani wanu ndipo akuchitani kukhala alowammalo m’dzikoli, ndi kuti aone mmene mungachitire.”

    [130] “Ndithu tidawakhaulitsa anthu a Farawo ndi chilala, ndi kuchepekedwa zokolola; kuti mwina angakumbukire

    [131] “(Adali chonchi): Ubwino ukawadzera, amati: “Ubwinowu nchifukwa cha zochita zathu zabwino.” Ndipo choipa chikawadzera, amakankhira kwa Mûsa ndi amene adali naye. (Amati iye ndiye wadzetsa tsokalo chifukwa choisambula milungu yawo). Dziwani kuti tsoka lawo limachokera kwa Allah (chifukwa cha zochita zawo zoipa). Koma ambiri a iwo sazindikira

    [132] “Ndipo adati (kwa Mûsa): “Chisonyezo chilichonse chimene ungatibweretsere kuti utilodze nacho (siupindula kanthu). Ifetu sitikukhulupirira.”

    [133] “Choncho, tidawatumizira chigumula, (mliri wa) dzombe, nsabwe, achule ndi magazi monga zizindikiro zosiyanasiyana. Koma adadzikuza; ndipo adali anthu oipa

    [134] “Pamene chilango chidawakhudza, amati: “E iwe Mûsa! Tipemphere kwa Mbuye wako pa zomwe adakulonjeza. Ngati utichotsera chilangochi, ndithudi tikukhulupirira, ndipo tiwatumiza pamodzi nawe ana a Israyeli (kuti unke nawo kumene ukufuna).”

    [135] “Koma pamene tidawachotsera chilangocho kufikira nthawi yawo yomwe iwo amayenera kuifika, pompo iwo adaswa lonjezo

    [136] “Choncho, tidawabwezera chilango ndikuwamiza m’nyanja chifukwa chakuti iwo adatsutsa zizindikiro Zathu, ndipo sadali ozilabadira

    [137] “Ndipo anthu omwe adali kuponderezedwa tidawachita kukhala amlowammalo a kuvuma kwa dziko ndi kuzambwe kwake, lomwe tidaikamo madalitso (ambiri). Ndipo mawu abwino a Mbuye wako adakwaniritsidwa kwa ana a Israyeli chifukwa cha kupirira kwawo (pa zomwe adakumana nazo). Ndipo tidazigumula ndi kuziononga zomwe Farawo ndi anthu ake ankapanga ndi zomwe ankamanga

    [138] “Ndipo tidawaolotsa ana a Israyeli pa nyanja (ndi kupulumuka ku masautso a Farawo), nadza kwa anthu omwe adali kupembedza mafano awo. (Iwo) adati: “E iwe Mûsa! Nafenso tipangire mulungu (wamafano) monga milungu yomwe ali nayo iwo.” (Mneneri Mûsa) adati: “Ndithudi, inu ndinu anthu osazindikira.”

    [139] ““Ndithudi awa aonongedwa m’zomwe ali nazozi, ndiponso ndizachabe zomwe akhala akuchita.”

    [140] “Adati: “Kodi ndikufunireni mulungu wina kusiya Allah chikhalirecho Iye wakuchitirani zabwino zoposa pa zolengedwa zonse?”

    [141] “Ndipo kumbukirani pamene tidakupulumutsani (m’manja) mwa anthu a Farawo omwe adali kukuzunzani ndi chilango choyipa ndipo anali kupha ana anu aamuna ndi kusiya ana anu aakazi. Pa ichi padali mayeso aakulu ochokera kwa Mbuye wanu

    [142] “Ndipo tidamlonjeza Mûsa masiku makumi atatu (kuti achite mapemphero kuti kenako timpatse Taurat). Ndipo tidawakwaniritsa ndi masiku khumi; chomwecho lidakwanira pangano la Mbuye wake (lopita kukampatsa Tauratiyo) m’masiku makumi anayi. Ndipo Mûsa adati kwa m’bale wake Harun: “Lowa m’malo mwanga pa (kuwatsogolera) anthu angawa. Ndipo konza; usatsate njira ya oononga.”

    [143] “Pamene Mûsa adafika kumalo achipangano Chathucho, ndipo Mbuye wake namulankhula, (Mûsa) adati: “Mbuye wanga! Dzionetseni kwa ine kuti ndikuoneni.” Allah adati: “Sungathe kundiona; koma yang’ana phirilo (lomwe lili patsogolo pako). Ngati likhazikika pamalo pake (popanda kusweka), ukhoza kundiona.” Choncho Mbuye wake pamene adadzionetsa kwa phirilo, adalichita kukhala loswekasweka ndipo Mussa adagwa ndi kukomoka. Pamene adatsitsimuka adati: “(Ha! Ndikutsimikizadi kuti) Inu ndinu Wolemekezeka. Ndalapa kwa Inu, ndipo ndine woyamba mwa okhulupirira (izi).”

    [144] “(Allah) adati: “E iwe Mûsa! Ndithu Ine ndakusankha iwe mwa anthu onse, (kukusankhira) uthenga Wanga ndi kuyankhulana Nane. Choncho landira chimene ndakupatsa, ndipo khala m’modzi wa anthu othokoza.”

    [145] “Ndipo tidamlembera m’mapale (m’masileti) maphunziro aulaliki wa mtundu uliwonse wofotokoza chinthu chilichonse: “Choncho, atenge mwa mphamvu ndi kuwalamulira anthu ako kuti awagwire mwa ubwino wake. Posachedwapa ndidzakusonyezani midzi ya oipa oswa malamulo athu (momwe idaonongekera. Ndipo ndikulowetsani inu m’menemo).”

    [146] “Ndiwatembenuzira kuzilingalira zizindikiro Zanga awo omwe akudzitukumula pa dziko popanda choonadi, ndipo akaona chizindikiro chilichonse sachikhulupirira, ndipo akaona njira yolungama sakuiyesa njira (sakuitsata), koma akaona njira yosokera akuiyetsa njira (akuitsata). Zimenezo nchifukwa chakuti iwo adatsutsa zizindikiro Zathu ndipo anali osazilabadira

    [147] “Ndipo awo amene atsutsa zizindikiro Zathu ndi nkumano wa tsiku lachimaliziro, zochita zawo zaonongeka. Kodi adzalipidwa china kuposa zomwe adali kuchita

    [148] “Ndipo pambuyo pake (popita kukalandira Taurat), anthu a Mûsa adaumba (fano la) thole (mwana wa ng’ombe) kuchokera mu zodzikongoletsera zawo (zibangiri zawo za siliva ndi golide); yemwe adali ndi thupi ndi kumatuluka mawu (koma wopanda moyo). Kodi sakuona kuti ilo (fano lawolo) silikuwalankhula ndiponso silikuwaongolera njira (yabwino?) Koma adalipanga basi (kuti likhale mulungu wawo wa fano) potero adali kudzichitira okha zoipa

    [149] “Pamene adazindikira kulakwa kwawo, (anadandaula kwambiri) naona kuti iwo asokera, anati: “Ngati Mbuye wathu satimvera chisoni ndi kutikhululukira, ndithudi, tikhala mwa otaika (oonongeka).”

    [150] “Ndipo pamene Mûsa adabwerera kwa anthu ake ali wokwiya, wodandaula (pomva zomwe zidachitikazo), adati: “Umlowam’malo wanu womwe mudandichitira pambuyo panga, ngoipa zedi. Kodi mudalifulumilira lamulo la Mbuye wanu; (mudachita zanuzanu musanadziwe chimene angakulamulireni Mulungu wanu)? Ndipo adawaponya pansi mapalewo (momwe mudalembedwa malamulo a chipembedzo chake). Nagwira mutu wa M’bale wake nkuukokera kwa iye. (kufuna kummenya chifukwa cha mkwiyo umene adali nawo. M’bale wakeyo) adati: “E iwe mwana wa mayi anga! Ndithu anthu (awa) adandiyesa wofooka, potero (sadamvere malangizo anga). Adatsala pang’ono kundipha. Choncho usawakondweretse adani (ndi chilango chako) pa ine, ndipo usandiike pamodzi ndi anthu oipa.”

    [151] “(Mûsa) adati: “Mbuye wanga! Ndikhululukireni ine ndi m’bale wanga ndipo tilowetseni m’chifundo Chanu. Inu Ndinu Achifundo kuposa achifundo onse.”

    [152] “Ndithu omwe adapanga (fano la ) Thole uwafika mkwiyo wa Mbuye wawo ndi kunyozeka pa moyo wa dziko lapansi. M’menemo ndi momwe timawalipirira anthu opeka (zinthu za chipembedzo)

    [153] “Ndipo omwe adachita zoipa, kenako nkulapa pambuyo pake nakhulupirira ndithu Mbuye wako pambuyo pakulapako, Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni

    [154] “Pamene mkwiyo wa Mûsa udatotobwa, adatola mapale aja omwe m’malembo mwake mudali chiongoko ndi chifundo kwa omwe amaopa Mbuye wawo

    [155] “Ndipo Mûsa adasankha anthu ake makumi asanu ndi awiri (omwe adali amakhalidwe abwino) kuti akafike kumalo a chipangano chathu (chimene tidamuuza kuti akabwere nawo pa phiripo kuti akapemphe chikhululuko pa machimo awo omwe adachitidwa ndi anzawo oipa). Ndipo pamene chivomerezi chachikulu chidawafika (adatsala pang’ono kufa). (Mûsa) adati: “Mbuye wanga! Ngati mukadafuna mukadawaononga iwo ndi ine kale (pamaso pa anzawo onse kuti adzionere okha kuti amwalira ndi mphamvu za Allah, osati pakuwapha ine). Kodi mutiononga chifukwa cha zochita za mbuli zathu? Izi sichina koma ndi mayesero anu. Kupyolera m’mayeserowo mumamlekelera kusokera amene mwamfuna, ndi kumtsogolera amene mwamfuna. Inu ndiye Mtetezi wathu; choncho, tikhululukireni ndi kutimvera chifundo. Inu ndinu Abwino mwa okhululuka onse.”

    [156] ““Ndipo tilembereni zabwino pa dziko lino lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro, ndithudi tibwerera kwa inu!” (Allah) adati: “Chilango changa ndichifikitsa kwa yemwe ndamfuna (mwa anthu oipa); ndipo chifundo Changa chakwanira pa chilichonse (pa abwino ndi oipa). Choncho ndiwalembera (kuti mtendere umenewu udzakhale wawowawo pa tsiku lachimaliziro) amene akupewa (zoletsedwa) ndi kumapereka Zakaat, ndi kumakhulupirira zizindikiro Zathu;”

    [157] ““Omwe akutsata Mtumiki, mneneri wosatha kuwerenga ndi kulemba (ngakhale ali choncho, akuphunzitsa zophunzitsa zodabwitsa); yemwe akumpeza atalembedwa kwa iwo m’buku la Taurat ndi Injili. Akuwalamula zabwino ndi kuwaletsa zoipa, ndi kuwaloleza zabwino ndi kuwaletsa zodetsedwa (zoipa); ndi kuwatula mitolo yawo ndi magoli omwe adali pa iwo (malamulo ovuta kuwatsata). Choncho, amene amkhulupirira (Muhammad {s.a.w}) ndi kumamlemekeza ndi kumuthangata, natsata kuunika (Quran) komwe kudavumbulutsidwa pamodzi ndi iye, iwo ndiwo opambana.”

    [158] “Nena: “E inu anthu! Ndithu ine ndine Mtumiki wa Allah kwa inu nonse. (Allah) Yemwe ali nawo ufumu wa kumwamba ndi pansi. Palibe wopembedzedwa mwa choonadi koma Iye. Amapatsa moyo ndi imfa. Choncho, khulupirirani mwa Allah ndi Mtumiki Wake yemwe ndi Mneneri wosadziwa kulemba ndi kuwerenga, yemwe akukhulupirira Allah ndi mawu Ake. Ndipo mtsatireni kuti muongoke.”

    [159] “Ndipo mwa anthu a Mûsa, mudali gulu lomwe linkatsogolera anzawo ku choonadi. Ndipo ndi choonadicho ankachita chilungamo

    [160] “Ndipo tidawagawa iwo m’mafuko khumi ndi awiri (osiyanasiyana) monga mitundu ikuluikulu. Ndipo tidamuvumbulutsira Mûsa pamene anthu ake adampempha madzi, kuti: “Menya mwala ndi ndodo yakoyo.” Ndipo mudatuluka akasupe khumi ndi awiri mwakuti fuko lililonse lidadziwa malo ake omwera. Ndipo tidawaphimba ndi mthunzi wa mtambo, ndi kuwatumizira mana ndi salwa (mbalame). (Tidawauza): “Idyani zinthu zabwinozi zomwe takupatsani.” Komatu sadatichitire choipa (pamene adachita zamphulupulu), koma adadzichitira okha zoipa

    [161] “Ndipo pamene adauzidwa: “Khalani mu Mzinda uwu (Yerusalemu), ndipo idyani m’menemo paliponse pamene mwafuna, ndipo nenani (polowa mu mzindamo uku mutawerama): “Tifafanizireni machimo athu, (E Inu Mbuye wathu)!” Ndipo lowerani pa chipata (chake) modzichepetsa; tikukhululukirani zolakwa zanu ndipo tiwaonjezera zabwino ochita zabwino

    [162] “Koma aja amene adadzichitira okha zoipa, mwa iwo adasintha mawu ena kusiya omwe adauzidwa; choncho, tidawatumizira chilango chochokera kumwamba chifukwa chodzichitira okha zoipa

    [163] “Tawafunsani nkhani ya mudzi umene udali m’mphepete mwa nyanja; (anthu am’mudziwo) pamene adali kuswa (lamulo la) tsiku la Sabata (lomwe adauzidwa kuti pa tsikuli asamachite usodzi wa nsomba, koma m’malo mwake azichita mapemphero okha). Nsomba zawo zinkawadzera yandayanda patsiku la Sabata, koma patsiku lomwe silidali la Sabata sizidali kuwabwerera (yandayanda). Motero tidawayesa mayeso chifukwa chakuchimwa kwawo

    [164] “Ndipo (akumbutse ) pamene gulu lina mwa iwo linkanena (kwa omwe amachenjeza amene adaswa kupatulika kwa tsiku la Sabata pamene adati): “Pali phindu lanji kuwachenjeza anthu omwe Allah awawononga kapena kuwalanga ndi chilango chaukali pompano pa dziko lapansi)? (Iwo) adati: “Kuti tidzakhale ndi chidandaulo kwa Mbuye wathu (ponena kuti tidawachenjeza koma sadatimvere) ndi kutinso mwina angaope (Allah nasiya kuswa lamulo Lake).”

    [165] “Choncho, pamene sanalabadire zimene anauzidwa ndi kuchenjezedwa, tinawapulumutsa (anthu) omwe amaletsa zoipa, ndipo tidawakhaulitsa amene ankadzichitira okha zoipa ndi chilango choipa kwambiri chifukwa chakupandukila (kwawo) malamulo

    [166] “Pamene anadzikweza pakusasiya zimene analetsedwazo tidawauza: “Khalani anyani, oyaluka (paliponse).”

    [167] “Ndipo (akumbutse) pamene Mbuye wako analengeza (kuti) ndithu adzawatumizira iwo (Ayuda) anthu mpaka tsiku la Qiyâma, omwe adzawazunza ndi mazunzo oipa. Ndithu Mbuye wako ngofulumira kulanga, ndipo ndithu palibe chikaiko, Iye Ngokhululuka kwambiri, Ngwachifundo chambiri

    [168] “Ndipo tidawalekanitsa pakati pawo (Ayuda), ndi kuwabalalitsa pa dziko lonse kukhala mafuko osiyanasiyana. Ena mwa iwo abwino (olungama) ndipo ena sali choncho (oipa). Tinawayesa mayeso a zabwino ndi zoipa kuti abwelere (koma ayi, sanabwelere)

    [169] “Choncho, anawatsatira pambuyo (anthu abwinowo), otsatira atsopano omwe analandira buku (la Allah nalowa mmalo mwa iwo koma popanda kulitsata ndi kulilingalira). Ankatenga zinthu zoletsedwa za pa dziko lapansi uku akunena: “Tidzakhululukidwa, (Allah adzatikhululukira).” Ngati zina zonga izo zitawapeza, amazitenganso. Kodi silidatengedwe pangano kwa iwo la m’buku kuti sadzamunenera Allah bodza koma zoona zokhazokha? (Nanga akuneneranji kuti Allah adzawakhululukira pomwe akupitiriza machimo)? Pomwe iwo aphunzira zomwe zili mmenemo. Komatu nyumba ya chimaliziro idzawakhalira bwino amene akuopa (Allah). Nanga bwanji simukuzindikira

    [170] “Ndipo amene akugwirisitsa buku (la Allah potsata zophunzitsa zake) ndi kumapemphera Swala, (tidzawalipira zabwino). Ndithu Ife sitipititsa pachabe malipiro a ochita zabwino

    [171] “Ndipo(akumbutse) pamene tidalizula phiri ndikulinyamula pamwamba pawo monga denga (kapena mtambo umene wawavindikira) natsimikiza kuti liwagwera, (tidawauza): “Landirani, mwamphamvu malamulo amene takupatsani, ndipo kumbukirani zomwe zili m’menemo (pozitsata ndi kuzichita); kuti inu muope.”

    [172] “Ndipo (kumbukirani) pamene Mbuye wako adawatulutsa ana a Adam m’misana ya atate awo ndi kuwachititsa umboni okha (powauza kuti): “Kodi Ine sindine Mbuye wanu?” Iwo adati: “Inde tikuikira umboni (kuti Inuyo ndiye Mbuye wathu).” (Allah adawauza kuti): “Kuopera kuti mungadzanene tsiku louka kwa akufa: “Ife sitidali kuzindikira chipanganochi.”

    [173] “Kapena mungadzati: “Makolo athu ndi amene adapembedza mafano kale, ndipo ife tidali ana odza pambuyo pawo (choncho tidawatsatira pazimene ankachita). Kodi nanga mutiononga chifukwa cha zomwe adachita oipa?”

    [174] “M’menemo ndi momwe tikulongosolera mokwanira zivumbulutso kuti mwina iwo angabwelere (kwa Allah)

    [175] “Ndipo alakatulire nkhani za yemwe tidampatsa zizindikiro zathu nadzichotsa m’menemo (m’zizindikiromo), ndipo satana anamtsata, choncho adali m’gulu la osokera

    [176] “Ndipo tikadafuna tikadamtukula nazo (ulemelero wake). Koma iye adapendekera ku za mdziko natsatira zilakolako zake. Fanizo lake lili ngati galu. Ngati utamkalipira amathawa uku akutulutsa lirime lake kunja. Ngakhale utamsiya amatulutsabe kunja lirime lake. Umo ndi momwe liliri fanizo la anthu otsutsa zizindikiro Zathu. Choncho asimbire nkhani izi kuti angalingalire

    [177] “Taonani kuipa fanizo la anthu omwe atsutsa zizindikiro Zathu ndi kudzichitira okha zoipa

    [178] “Amene Allah wamuongola ndiye woongoka. Ndipo amene wamulekelera kusokera (chifukwa chakusatsatira kwake malangizo a Allah), iwo ndiwo otaika (oonongeka)

    [179] “Ndithudi, ziwanda zambiri ndi anthu tidawalengera kukalowa ku (Moto wa) Jahannam. Mitima ali nayo koma sazindikira nayo kanthu; ndipo maso ali nawo koma sapenyera nawo (zodabwitsa za Allah); ndipo makutu ali nawo koma samvera nawo (zowapindulitsa). Iwo ali ngati ziweto, kapena iwo ndi osokera zedi kuposa Ziweto. Iwo ndi osalabadira

    [180] “Ndipo Allah ali nawo maina abwino. Choncho, muitaneni ndi mainawo. Alekeni amene akupotoza maina Ake posachedwapa alipidwa zomwe akhala akuchita

    [181] “Ndipo mwa amene tidawalenga, alipo anthu oongolera (anzawo) ku choonadi. Ndipo kupyolera mchoonadicho akuchita chilungamo

    [182] “Ndipo amene atsutsa zivumbulutso zathu, tiwalekelera pang’onopang’ono, kenako nkuwakhaulitsa kuchokera momwe iwo sakudziwa

    [183] “Ndipo ndiwapatsa kanthawi. Ndithu kukhaulitsa kwanga nkokhwima

    [184] “Kodi sadalingalire kuti munthu wawoyo (mneneri Muhammad {s.a.w}) alibe misala? Iye sali koma mchenjezi woonekera poyera

    [185] “Kodi saona ufumu wa kumwamba ndi pansi, ndi zinthu zomwe Allah adalenga? Mwina mwake nthawi yawo yofera yayandikira. (Nanga adzalingalira liti zolengedwa za Allah)? Kodi ndi nkhani iti pambuyo pa iyi (Qur’an) imene adzaikhulupirira

    [186] “Amene Allah wamulekelera kusokera, alibe muongoli. Ndipo Allah akuwasiya akuyumbayumba m’kusokera kwawo

    [187] “Akukufunsa za nthawi (ya Qiyâma) kuti idzakhalako liti? Nena: “Kudziwika kwa nthawi yake kuli kwa Mbuye wanga. palibe amene angaionetse poyera nthawi yake koma Iye. Nkovuta kwambiri kumwamba ndi pansi (kuizindikira nthawi yake). Siidzakudzerani koma mwadzidzidzi.” Akukufunsa ngati kuti iwe ukudziwa bwino za nthawiyo. Nena: “Kudziwika kwa nthawi yake kuli kwa Allah. Koma anthu ambiri sadziwa.”

    [188] “Nena: “Ine ndekha ndilibe mphamvu yodzibweretsera chabwino kapena kudzichotsera choipa, koma chimene Allah wafuna. Ndikadakhala kuti ndikudziwa za mseri, ndikadadzichulukitsira zabwino, ndipo choipa sichikadandikhudza. Ine sindili chilichonse koma mchenjezi ndi wouza anthu okhulupirira nkhani zabwino.”

    [189] “Iye ndi Yemwe adakulengani kuchokera mwa munthu mmodzi, napanga mwa iye mkazi wake kuti adzikhala naye. Pamene adamkumbatira, adakhala ndi pakati popepuka nayenda napo (mosalemedwa). Koma pamene (pakatipo) padalemera (patangotsala pang’ono kuti abereke) anampempha Allah, Mbuye wawo (kuti): “Ngati mutipatsa mwana wabwino, ndithu tidzakhala mwa othokoza kwambiri.”

    [190] “Choncho, pamene adawapatsa mwana wabwino (yemwe adapempha) adamchitira Allah anzake (mafano) pa chimene adawapatsacho. Koma Allah watukuka kuzimene akumphatikiza nazozo

    [191] “Kodi akumphatikiza (Allah) ndi zinthu zomwe sizilenga chilichonse pomwe izo zikulengedwa

    [192] “Ndipo sizingathe kuwathandiza ngakhale kudzithandiza zokha (podzibweretsera zabwino ndi kudzichotsera zoipa)

    [193] “Ngati (milungu yamafanoyo) mutaiitanira ku chiongoko, siingakutsatireni (chifukwa chakuti siimva kapena kuzindikira chilichonse). Nchimodzimodzi kwa inu kuiitana kapena kukhala chete (palibe chimene ingadziwe)

    [194] “Ndithu amene mukuwapembedza kusiya Allah, ndi akapolo monga inu. (Koma inu muposa iwo). Choncho aitaneni ndipo akuyankheni ngati inu mulidi owona (pa zimene mukunenazi)

    [195] “Kodi iwo ali nayo miyendo yoyendera? Kapena ali nawo manja ogwilira. Kapena ali nawo maso openyera? Kapena ali nawo makutu omvelera? Nena: “Aitaneni aphatikizi anuwo, ndipo kenako ndichitireni chiwembu ndipo musandipatse nthawi.”

    [196] ““Ndithu Mtetezi wanga ndi Allah, Yemwe wavumbulutsa buku (ili lopatulika). Ndipo Iye amawateteza ochita zabwino.”

    [197] ““Ndipo omwe mukuwapembedza kusiya Iye (Allah,) sangathe kukupulumutsani ndiponso sangathe kudzipulumutsa okha.”

    [198] “Ngati mutawaitanira ku chiwongoko, sangamve; koma uwaona akukuyang’ana koma pomwe iwo sakuona

    [199] “Khala ndi khalidwe lokhululuka, lamula zabwino ndipo dzipatule ku mbuli

    [200] “Ndipo ngati manong’onong’o a satana atakuvutitsa, dzitchinjirize ndi Allah. Ndithu Iye Ngwakumva, Ngodziwa

    [201] “Ndithu amene akuopa (Allah), udyerekezi wa satana ukawakhudza amakumbukira (Allah), nkuona (njira yotulukira muudyerekezi wakewo)

    [202] “Koma anzawo (omwe ali oipa) amawalimbikitsa m’machimo, ndipo kenako saleka (kupitiriza machimowo)

    [203] “Ngati siudawabweretsere chozizwitsa, akunena: “Bwanji wosachibweretsa pa iwe wekha? Nena: “Ndithudi ndikutsatira zimene zikuvumbulitsidwa kwa ine kuchokera kwa Mbuye wanga. (Sindichita chinthu mwa ine ndekha). Iyi (Qur’an) ndi umboni (waukulu pa zoyankhula zanga) kuchokera kwa Mbuye wanu. (Izo) ndi chiongoko ndi chifundo kwa anthu okhulupirira.”

    [204] “Ndipo Qur’an ikamawerengedwa, mvetserani (mwatcheru) ndi kukhala chete, kuti muchitiridwe chifundo

    [205] “Ndipo mtchule Mbuye wako mu mtima mwako modzichepetsa, mwa mantha ndi mosakweza mawu m’mawa ndi madzulo; ndipo usakhale mwa osalabadila (malamulo a Allah)

    [206] “Ndithu amene ali kwa Mbuye wako, (angelo), sadzitukumula posiya kumpembedza (Mbuye wawo, koma iwo) amam’lemekeza ndi kumlambira

    Zofunkha

    Surah 8

    [1] “Akukufunsa za chuma cholandidwa pa nkhondo (mmene chingagawidwire). Nena: “Chuma cholanda pa nkhondo ndi cha Allah ndi Mtumiki (ndiamene ali olamula kagawidwe kake); choncho, muopeni Allah ndipo yanjanani mwachibale pakati panu. Mverani Allah ndi Mtumiki Wake, ngati mulidi okhulupirira.”

    [2] “Ndithu okhulupirira, enieni ndi amene akuti Allah akatchulidwa mitima yawo imadzadzidwa ndi mantha; pamenenso Ayah Zake zikuwerengedwa kwa iwo zimawaonjezera chikhulupiliro, ndipo amayadzamira kwa Mbuye wawo Yekha basi; (sakhulupirira nyanga ndi mizimu ya anthu akufa)

    [3] “Amene amaimilira kupemphera napereka chimene tawapatsa, (pa njira ya Allah, ndikuthandiza ovutika)

    [4] “Awa (okhala ndi makhalidwe otere) ndi amene ali okhulupirira mwachoonadi. Iwo adzapeza ulemelero (wapamwamba) kwa Mbuye wawo, ndi chikhululuko ndi zopatsidwa zaulemu

    [5] “Monga mmene Mbuye wako adakulamulira kutuluka m’nyumba yako (kupita ku Badr kukachita nkhondo ndi osakhulupirira) mwachoonadi, ndithu gulu lina la okhulipirira silidafune (kuchoka kukakumana ndi adani)

    [6] “Akutsutsana nawe (pa chinthu) choona pambuyo pakuti chaonekera poyera. (Kukuwaipira kukumana ndi adani) ngati kuti akubusidwa kunka ku imfa akuona

    [7] “(Kumbukirani, E inu okhulupirira!) Pamene Allah anakulonjezani gulu limodzi mwa magulu awiri kuti likhale lanu (kuti mumenyane nalo). Koma inu mukufuna lopanda mphamvu kuti likhale lanu (kuti ndilo mumenyane nalo). Koma Allah akufuna kuchitsimikiza choonadi ndi mawu Ake ndi kudula mizu ya osakhulupirira, (pomenyana ndi gulu lamphamvulo, omwe ndi ankhondo a Chikuraishi)

    [8] “Kuti achitsimikizire choonadi ndi kulichotsa bodza; ngakhale zikuwaipira anthu oipa

    [9] “(Kumbukirani) pamene mudali kupempha Mbuye wanu chithandizo, ndipo anakuyankhani kuti: “Ndithudi, Ine ndikuthandizani ndi chikwi cha angelo otsatizana potsika, (omenya nkhondo).”

    [10] “Ndipo Allah sadachite ichi koma kuti chikhale nkhani yabwino (yosangalatsa), ndi kuti mitima yanu ikhazikike ndi chimenecho. Ndipo palibe chipulumutso (chothandiza) koma chimene chachokera kwa Allah. Ndithu Allah Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya

    [11] “(Kumbukirani) pamene anakugonetsani tulo tomwe tidali mtendere wochokera kwa Iye, ndipo anavumbwitsa mvula pa inu yochokera ku mitambo kuti akuyeretseni nayo (matupi anu) ndikukuchotserani manong’onong’o a satana, ndi kuipatsa mphamvu mitima yanu ndiponso ndi kulimbikitsa mapazi anu (pamchenga)

    [12] “(Kumbukira) pamene Mbuye wako anawauza angelo kuti: “Ine ndili pamodzi nanu (pokulimbikitsani ndi chithandizo Changa). Alimbikitseni amene akhulupirira, ndipo ndidzathira mantha mmitima mwa amene sadakhulupirire. Choncho amenyeni mmwamba mwa makosi awo, ndi kuwadula nsonga za zala zawo (zimene akugwilira zida)

    [13] “Izi ndi chifukwa chakuti iwo anatsutsana ndi Allah ndi Mtumiki wake (iwo podziika mbali ina kusiya komwe kudali Allah). Amene anatsutsana ndi Allah ndi Mtumiki Wake, ndithu Allah ndi wolanga kwambiri (amalanga ndi chilango choopsa)

    [14] “Chimenecho ndi chilango (cha Allah E inu Maquraish)! Choncho chilaweni. Ndithu osakhulupirira adzapeza chilango cha Moto

    [15] “E inu amene mwakhulupirira! Pamene mukumana nawo (pa nkhondo) amene sadakhulupirire alikudza kwa inu mwa unyinji musawatembenuzire misana kuthawa

    [16] “Ndipo amene adzawatembenuzire msana kuthawa pa tsikulo - osati kutembenuka (kwa ndale) kofuna kumenyana kapena kukalowa m’gulu (la Asilamu ena) - ndiye kuti adziitanira mkwiyo wochokera kwa Allah; ndipo malo ake ndi ku Jahannam, kumeneko ndi ku malo koipa kubwererapo

    [17] “Inu simudawaphe (ndi mphamvu zanu) koma Allah ndi Yemwe anawapha; siudawagende pamene udagenda koma Allah ndi amene anawagenda (pofikitsa mchenga m’maso mwawo, wachita zimenezi) kuti awachitire zabwino Asilamu powapatsa dalitso labwino lochokera kwa Iye. Ndithu Allah Ngwakumva, Ngodziwa

    [18] “Izi akuchitirani (pakalipano), ndithudi Allah afooketsa ndale za osakhulupirira

    [19] “Ngati mwakhala mukufuna chiweruzo (pogwilira nsalu yovindikira Ka’aba kuti mupambane pa nkhondo), chiweruzo chakudzerani (chokomera Asilamu). Ndipo ngati musiya (kuwazunza okhulupirira kapena kusiya kunyoza Allah) chikhala chinthu chabwino kwa inu. Koma ngati mubwereza (kuwaputa) nafenso tidzabwereza (kukulangani). Gulu lanu lankhondo silikuthandizani kanthu ngakhale lichuluke chotani. Ndipo Allah ali pamodzi ndi okhulupirira

    [20] “E inu amene mwakhulupirira! Mverani Allah ndi Mtumiki Wake, ndipo musamtembenukire kumbali pamene inu mukumva

    [21] “Ndipo musakhale monga aja achinyengo omwe akunena: “Tamva (choonadi ndipo tachisunga),” pomwe iwo sakumva (kumva kochigonjera)

    [22] “Ndithu nyama zoipitsitsa pamaso pa Allah ndi agonthi, abubu amene alibe nzeru, (omwe ndi aphatikizi ndi anthu achinyengo)

    [23] “Ndipo Allah akadadziwa mwa iwo (ndi kudziwa kwake kopanda chiyambi); kuti muli ubwino (pakuwamveretsa Qur’an ndi kuwazindikiritsa) akadawamveretsa. (Koma chikhalidwe chawo chili cha mtundu umenewo) ndipo ngakhale akadawamveretsa (Qur’an ndikuwazindikiritsa) akadatembenuka m’mbuyo uku akunyoza (chifukwa cha kugonjera zilakolako zawo)

    [24] “E inu amene mwakhulupirira muvomereni Allah (pa zimene akukulamulani) ndiponso muvomereni Mtumiki Wake pamene akukuitanirani ku chimene chingakupatseni moyo (wabwino wa pa dziko lapansi ndi tsiku lachimaliziro). Ndipo dziwani kuti Allah amatchinga pakati pa munthu ndi mtima wake (amautembenula mmene akufunira). Ndipo dziwani kuti kwa Iye mudzasonkhanitsidwa

    [25] “Ndipo muope mazunzo (a Allah a pano pa dziko lapansi) omwe sangagwere okhawo amene adzichitira zoipa mwa inu (koma adzawagweranso amene akusiya kuletsa zoipa) ndipo dziwani kuti Allah Ngolanga kwambiri

    [26] “Ndipo kumbukirani (inu Asilamu) pamene mudali owerengeka, ochepa, onyozeka m’dziko. Mumakhala moopa anthu kuti angakufwambeni, koma anakupatsani pamalo pabwino pokhala, nakulimbikitsani ndi chipulumutso Chake, nakuninkhani zinthu zabwino kuti muyamike (Allah)

    [27] “E inu amene mwakhulupirira! Musachitire Allah ndi Mtumiki (Wake) chinyengo (pa kutsata zimene mwaletsedwa). Ndipo musazichitire chinyengo zimene mwakhulupirika nazo uku mukudziwa (kuti kutero ndikulakwa)

    [28] “Ndipo dziwani kuti chuma chanu ndi ana anu ndimayesero (oyesedwa ndi Allah kuti aone mmene mungagwiritsire nazo ntchito). Ndi kuti kwa Allah kuli malipiro aakulu

    [29] “E inu amene mwakhulupirira! Ngati muopa Allah, adzakupatsani chilekanitso (cholekanitsa pakati pa choonadi ndi chachabe), ndiponso akufafanizirani zoipa zanu ndi kukukhululukirani. Ndipo Allah ndi Mwini ubwino waukulu

    [30] “Ndipo (kumbukira) pamene omwe sadakhulupirire amakuchitira chiwembu kuti akunjate, kapena akuphe, kapena akutulutse (m’dziko lawo la Makka mwachipongwe). Ndipo amachita chiwembu, naye Allah anawononga chiwembu chawocho. Ndipo Allah ndiwokhoza koposa poononga ziwembu (za anthu oipa)

    [31] “Ndipo (Aquraish) zikawerengedwa Ayah (ndime) Zathu kwa iwo amanena: “Tidazimva (izi kale). Tikadafuna tikadanena zonga izi. Izi sikanthu koma ndinthano za anthu akale.”

    [32] “Ndipo (kumbukira) pamene adati: “E Inu Allah! Ngati ichi (chimene wadza nacho Muhammad {s.a.w}) chili choonadi chochokera kwa Inu, tivumbwitsireni mvula ya miyala yochokera kumwamba, kapena mutibweretsere chilango chowawa kwambiri.”

    [33] “Koma Allah sangawalange pomwe iwe uli nawo. Ndipo Allah sakadawalanga pomwe (ena mwa iwo) akupempha chikhululuko

    [34] “(Kodi iwo Aquraish) ali ndi chinthu chanji (chabwino chimene) chingamuletse Allah kuwalanga? Pomwe iwo akuwatsekereza anthu kulowa mu Msikiti Wopatulika. Iwo sanayenere kukhala ouyang’anira (Msikitiwo). Palibe angauyang’anire koma olungama, koma anthu ambiri sadziwa

    [35] “Ndipo mapemphero awo pa nyumba yopatulikayo sadali kanthu, koma kuyimba miluzi ndi kuomba m’manja. Choncho (adzauzidwa): “Lawani chilango chifukwa chakusakhulupirira kwanu.”

    [36] “Ndithu osakhulupirira akupereka chuma chawo (pa nkhondo yolimbana ndi Asilamu) ndi cholinga choti awatsekeleze anthu kuyenda pa njira ya Allah. Choncho adzapitiriza kupereka chumacho kenako chidzakhala chowadandaulitsa, ndipo adzagonjetsedwa. Ndipo omwe sanakhulupirire adzasonkhanitsidwa ku Jahannam

    [37] “Kuti Allah alekanitse oipa ndi abwino, ndi kuti awayike ena mwa oipawo pamwamba pa anzawo, potero nkuwaunjika oipawo mulu umodzi, kenako nawaponya ku Jahannam. Iwowa ndi anthu otaika

    [38] “Nena kwa osakhulupirira kuti: “Ngati asiya (zochita zawo zoipa), adzakhululukidwa zimene zidatsogola. Koma ngati abwereza (kuwazunza Asilamu, tiwalanga) ndithudi njira ya Allah yomwe idachitika kwa anthu akale inadutsa (powalanga akasiya kutsata malamulo a Allah)

    [39] “Ndipo menyanani nawo osakhulupirira kufikira shirik itatha ndipo chipembedzo chonse chikhale cha Allah. Ndipo ngati asiya, ndithu Allah Ngoona zomwe akuchita

    [40] “Koma ngati apitiriza kunyoza kwawo, dziwani kuti Allah ndi Mtetezi wanu, Mtetezi wokoma mtima koposa, ndi Mthandizi wabwino

    [41] “۞ Ndipo dziwani kuti chilichonse chimene mwapeza monga chuma cholanda ku nkhondo, gawo limodzi mwa magawo asanu ndi cha Allah ndi Mtumiki, ndi a chibale (a Mtumiki), amasiye, masikini ndi munthu wa pa ulendo (amene asowedwa choyendera pa ulendo. Tsatilani malamulowa) ngatidi mwakhulupirira Allah ndi chimene tachivumbulutsa kwa kapolo Wathu pa tsiku lachilekanitso (lolekanitsa pakati pa choona ndi chabodza), tsiku limene magulu awiri adakumana (tsiku la nkhondo ya Badr, gulu la nkhondo la Asilamu ndi gulu la nkhondo la osakhulupirira). Ndipo Allah Ngokhoza kuchita chilichonse

    [42] “(Kumbukirani) pamene mudali mbali ya chigwa yoyandikira (mzinda wa Madina) pomwe iwo (ankhondo a Chikuraishi) adali mbali ya kutali ya tsidya lina (la chigwacho) pomwe aulendo amalonda adali cha kumunsi kwanu. Ngati mukadapangana nthawi yokumanirana (kuti mukumane nthawi yakutiyakuti), mukadasiyana posunga chipangano (chifukwa cha kuopa kuchuluka kwa adani anuwo). Koma (mwakumana mosayembekezera ndi ankhondo a adaniwo) kuti Allah akwaniritse chinthu chomwe nchofunika kuti chichitike, kuti awonongeke amene waonongeka (posankha kusakhulupirira) ndi umboni woonekera (umene adaukana kuutsata), ndi kuti akhale ndi moyo amene wakhala ndi moyo (amene watsata njira ya Chisilamu) ndi umboninso woonekera. Ndithudi Allah Ngwakumva zonse, Ngodziwa kwambiri

    [43] “(Kumbukira) pamene Allah adakuonetsa iwo ku maloto kwako kuti ngochepa (pachiwerengero chawo potero udalimba mtima za kukumana nawo), akanakuonetsa iwo kuti ngambiri pa chiwerengero chawo; inu (Asilamu) mukadalephera (mukanataya mtima) ndipo mukanakangana pa chinthucho. (Ena akanafuna kumenyana nawo pamene ena akanakana), koma Allah anakutetezani (ku zimenezo). Ndithu Iye Ngodziwa kwambiri za m’mitima

    [44] “Ndipo (kumbukirani) pamene anakuonetsani iwo m’maso mwanu, pamene munakumana nawo kuti iwo ndi ochepa, (owerengeka, kuti mukhale ndi chidwi chomenyana nawo), ndiponso anakuchepetsani kwambiri m’maso mwawo (kuti iwo aone kuti nkosafunika kukonzekera kwambiri chifukwa chakuchepa kwa omenyana nawowo), kuti Allah akwaniritse chimene adalamula kuchitika. Kwa Allah Yekha ndiko kobwerera zinthu zonse

    [45] “E inu amene mwakhulupirira! Pamene mukumana ndi gulu (la osakhulupirira) mulimbe mtima, ndipo tamandani Allah kwambiri kuti mupambane

    [46] “Ndipo mumvereni Allah ndi Mtumiki Wake, musakangane (kuopera kuti) mungakhale olephera (ndi kutaya mtima), ndikuchoka mphamvu zanu. Koma pitirizani kupirira. Ndithudi, Allah ali pamodzi ndi anthu opirira

    [47] “Ndipo musakhale ngati anthu amene anatuluka m’nyumba zawo modzikweza ndi modzionetsera kwa anthu, ndikuwasekereza anthu kuyenda pa njira ya Allah. Koma Allah ndi Wodziwa kwambiri zimene akuchita

    [48] “Ndipo (kumbukira) pamene satana adawakometsera zochita zawo zoipa (aja osakhulupirira) nati: “Lero palibe aliyense mwa anthu amene angakugonjetseni, ndipo ine ndine mtetezi wanu.” Koma pamene magulu awiri ankhondo anaonana (anakumana pamaso ndi pamaso) satana anabwerera pambuyo (kuthawa) nati: “Ine ndikudzipatula mwa inu. Ndithu ine ndikuona zimene inu simukuziona. Ndithu ine ndikuopa Allah.” Ndipo Allah Ngwaukali polanga

    [49] “(Kumbukirani) pamene achiphamaso ndi amene ali ndi matenda m’mitima mwawo amanena: “Anthu awa chipembedzo chawo (cha Chisilamu) chawanyenga.” Komatu amene akuyadzamira kwa Allah ndithudi Allah Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya

    [50] “Ndipo ukadaona angelo pamene akuchotsa miyoyo ya anthu amene sadakhulupirire (pa imfa yawo) uku akumenya kunkhope zawo ndi kumisana yawo (uku akunena): “Lawani chilango cha Moto woocha. (Ukadaziona zoopsa kwabasi).”

    [51] ““Izo ndi chifukwa cha (machimo) amene manja anu anawatsogoza, ndipo Allah sali opondereza akapolo (Ake).”

    [52] “(Khalidwe lawo awa lili ) ngati khalidwe la anthu a Farawo ndi omwe adalipo patsogolo pawo. Anazikana zizindikiro za Allah, choncho Allah anawalanga chifukwa cha machimo awo. Ndithudi Allah Ngwamphamvu, Wolanga moopsa

    [53] “Izo, (posawadzera miliri yotere) nchifukwa chakuti Allah sasintha chisomo (Chake) chimene wachipereka kwa anthu mpaka anthuwo asinthe okha zomwe zili m’mitima mwawo, (posiya kuthokoza Allah nayamba kuyenda m’njira zolakwira Allah). Ndithu Allah Ngwakumva Ngodziwa chilichonse

    [54] “(Khalidwe lawo lili) ngati khalidwe la anthu a Farawo ndi omwe adalipo patsogolo pawo. Adatsutsa zizindikiro za Mbuye wawo. Choncho, tidawaononga chifukwa cha machimo awo, ndipo tidawamiza anthu a Farawo. Ndipo onse adali ochita zoipa

    [55] “Ndithu nyama zoipitsitsa kwa Allah ndi amene sakhulupirira. (amamkana Allah ngakhale choonadi akuchidziwa bwinobwino), choncho iwo sakhulupirira

    [56] “Omwe unapangana nawo chipangano kenako naaswa chipangano chawo panthawi iliyonse (imene mwapangana), ndiponso iwo saopa Allah

    [57] “Choncho, ngati uwapeza ku nkhondo, (menyana nawo), uwabalalitse (kuti likhale phunziro kwa) amene ali pambuyo pawo kuti iwo azindikire

    [58] “Ngati uopa kusakhulupirika kwa anthu (omwe unapangana nawo chipangano), atayire (chipangano chawocho), mwachilungamo; ndithu Allah sakonda (anthu) osakhulupirika

    [59] “Ndipo (anthu) amene sadakhulupirire asaganize kuti ampitilira (Allah kotero kuti sachita kanthu ndi iwo), iwo sangamulepheretse Allah (chimene akufuna kuchita pa iwo)

    [60] “Ndipo akonzekereni mmene mungathere ndi mphamvu zanu (zonse zomenyera nkhondo), ndiponso poikiratu mahatchi odikira nkhondo kuti muwaopseze nazo adani a Allah ndi adani anu (amene mukuwadziwa) ndiponso (ndi) ena omwe (inu) simukuwadziwa. Koma Allah akuwadziwa. Ndipo chilichonse mungapereke pa njira ya Allah chidzalipidwa kwa inu modzadza ndipo simuzaponderezedwa

    [61] “Ndipo ngati (awo adani) apendekera kumbali yokhalirana mwa mtendere, nawenso pendekera (ku mbaliyo) ukatero yadzamira kwa Allah. Ndithudi Iye Ngwakumva, Ngodziwa

    [62] “Ngati afuna kukunyenga pa chimvanochi, ndithudi, Allah akukwanira kwa iwe (kukuteteza). Iye ndi Yemwe anakuthangata ndi chipulumutso chake ndi okhulupirira

    [63] “Ndipo (Allah) analuzanitsa pakati pa mitima yawo (poika chikondi pakati pawo). Ngati ukanapereka zonse za m’dziko lapansi (ncholinga choti uwaluzanitse mitima yawo mwa iwe wekha) sukadatha kuluzanitsa pakati pa mitima yawo. Koma Allah adaluzanitsa pakati pawo. Ndithu Iye Ngwamphamvu zoposa Ngwanzeru zakuya

    [64] “E iwe Mneneri! Allah akukwanira kwa iwe kukuteteza pamodzi ndi amene akutsata (iwe) mwa okhulupirira

    [65] “E iwe Mneneri! Alimbikitse okhulupirira kupita ku nkhondo. Ngati mwa inu muli anthu makumi awiri olimba mtima (ndiye kuti) adzawagonjetsa mazana awiri (a mwa anthu osakhulupirira). Ngati mwa inu muli anthu zana limodzi (olimba mtima ndiye kuti) adzagonjetsa chikwi chimodzi (1,000) cha anthu omwe sadakhulupirire, chifukwa chakuti iwo ndi anthu osazindikira

    [66] “Tsopano Allah wakupeputsirani (lamulo lovutali), ndipo wadziwa kuti muli kufooka mwa inu. Choncho ngati mwa inu muli anthu zana limodzi olimba mtima adzagonjetsa mazana awiri. Ngati alipo mwa inu chikwi chimodzi, adzagonjetsa zikwi ziwiri, mwachilolezo cha Allah. Allah ali pamodzi ndi opirira

    [67] “Sichoyenera kwa Mneneri kukhala ndi akayidi mpaka amenye nkhondo (kwambiri) ndi kugonjetseratu maiko molimba (ndi pamene atha kukhala ndi akayidi). Mukufuna zinthu za m’dziko pomwe Allah akufuna (mupeze mphoto ya) tsiku lachimaliziro! Ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa Ngwanzeru zakuya

    [68] “Pakadapanda lamulo la Allah limene linatsogolera kale (lokulolezani chuma chopeza ku nkhondo), chilango chachikulu chikanakugwerani, chifukwa cha zimene munatenga (ku-nkhondo ya Badri)

    [69] “Tsopano idyani chuma chimene mwalanda pa nkhondo (chomwe chili) chololedwa, chabwino, ndipo pitirizani kuopa Allah. Ndithu Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha

    [70] “E iwe Mneneri! Uza akaidi a pankhondo amene ali m’manja mwanu kuti ngati Allah aona chabwino chilichonse m’mitima mwanu, adzakupatsani zoposa zimene mwalandidwa ndipo adzakukhululukirani; Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha

    [71] “Ngati akufuna kukuchitirani chinyengo (chinyengo chawo sichiphula kanthu pa iwe), ndithu anamuchitirapo kale Allah chinyengo (chifukwa cha kusakhulupirira kwawo). Choncho anakupatsa mphamvu zowagonjetsera iwo. Ndipo Allah Ngodziwa, Ngwanzeru zakuya

    [72] “Ndithu anthu amene anakhulupirira nasamuka kwawo ndi kumenyana pa njira ya Allah ndi chuma chawo ndi moyo wawo; ndiponso amene anawalandira (iwo) ndi kuwapatsa malo ndi kuwathandiza, awa ndiabale otchinjirizana wina ndi mnzake. Ndipo anthu amene akhulupirira koma nasiya kusamuka (kudza ku Madina), palibe udindo pa inu wa kuwateteza kufikira nawonso atasamuka (kudza ku Madina). Ngati atakupemphani chithandizo cha chipembedzo athandizeni, kupatula (akaputana ndi anthu) amene pakati panu ndi iwo pali chipangano, (pamenepo musawathandize pomenyana ndi osakhulupirirawo omwe muli nawo chipangano). Ndipo Allah Ngowoona zomwe muchita

    [73] “Ndipo (anthu) amene sadakhulupirire (Allah) amatetezana okha ndi kukhala abwenzi pakati pawo. Ngati nanunso simuchita izi, padzakhala chisokonezo m’dziko ndi chionongeko chachikulu

    [74] “Amene akhulupirira nasamuka, namenya nkhondo panjira ya Allah (pamodzi nanu), ndiponso amene anawalandira (osamukawo), nawapatsa malo ndi kuwathandiza, iwo ndi omwe ali okhulupirira mwa choonadi. Iwo adzapeza chikhululuko ndi zopatsidwa za ulemu

    [75] “Ndipo aja akhulupirira pambuyo (pa Amuhajirina ndi Answari), nawonso nasamukira (ku Madina kukakhala pamodzi ndi Mtumiki ndi Asilamu anzawo), namenyanso nkhondo pamodzi nanu, iwo ndi amene ali mwa inu. Koma achibale chakubadwana, ndiamene ali oyenera (kulowerana mmalo pa chuma) ena ndi ena, mmene zilili) m’buku la Allah. Ndithudi, Allah Ngodziwa chilichonse

    Kulapa

    Surah 9

    [1] “Uku ndikudzipatula kochokera kwa Allah ndi Mtumiki wake ku (mapangano) amene mudapangana nawo (kenako nkuswa mapangano awowo) a m’gulu la Amushirikina

    [2] “(Auze Amushirikina kuti): Yendani pa dziko miyezi inayi basi. (Pambuyo pake sipadzakhala chitetezo pakati pawo ndi ife). Ndipo dziwani kuti inu simungathe kumpambana Allah. Ndipo Allah Ngosambula osakhulupirira

    [3] “Ndipo uku ndi kulengeza kochokera kwa Allah ndi Mtumiki Wake kwa Anthu pa tsiku la Hajj yaikulu kuti ndithu Allah ndi Mtumiki Wake adzichotsa mmapangano a Amushirikina (omwe ali achinyengo). Choncho, ngati mulapa ndibwino kwa inu; ndipo ngati mutembenuka ndi kunyoza, dziwani kuti inu simungamulepheretse Allah. Ndipo auze za chilango chowawa amene sadakhulupirire

    [4] “Kupatula ena amene mudapangana nawo mapangano mwa Amushirikina, (omwe adasunga mapangano awo), kenako sadapungule chilichonse ndipo sadathandize aliyense pa inu, akwaniritseni mapangano awo mpaka m’nyengo yawo. Ndithu Allah akukonda amene akumuopa (ndi kusunga mapangano)

    [5] “Ndipo miyezi yopatulika ikatha (yomwe njoletsedwa kuchitamo nkhondo), apheni Amushirikina paliponse pamene mwawapeza (menyanani nawo), ndipo agwireni (monga momwe iwo akukuchitirani). Ndipo azungulireni ndi kuwakhalira pa njira zonse. Koma akalapa nayamba kupemphera Swala, ndikupereka chopereka (Zakaat), ilekeni njira yawoyo (asiyeni). Ndithu Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha

    [6] “Ndipo ngati mmodzi wa Amushirikina Atakupempha chitetezo (kuti amvere mawu a Allah), mtetezeni kuti amve mawu a Allah. Kenako (ngati sadakhutitsidwe nawo), mpititseni kumalo kwake mwamtendere (ngati safuna kulowa m’Chisilamu). Izi nchifukwa chakuti iwo ndi anthu osadziwa

    [7] “Chingakhalepo bwanji chipangano pakati pa Amushirikina (oswa mapangano nthawi ndi nthawi) ndi Allah ndi Mthenga Wake, kupatula okhawo amene mudapangana nawo mapangano pa Msikiti Wopatulika? (Amene adakwaniritsa mapangano awo). Ngati iwo akupitiriza kulungama (posunga mapanganowo) kwa inu, nanunso pitirizani kulungama kwa iwo. Ndithu Allah akukonda amene akumuopa

    [8] “(Kodi inu ndiye osunga malonjezo?) Bwanji? Pomwe iwo akakhala ndi mphamvu pa inu sakusungirani chibale kapena pangano? Amakusangalatsani ndi pakamwa pawo pomwe mitima yawo ikukana (kukukondani). Ndipo ambiri a iwo ngoukira malamulo (a Allah)

    [9] “Asinthanitsa Ayah za Allah (ndi zinthu za dziko lapansi) ndi mtengo wochepa, ndipo atsekereza (anthu) kunjira Yake. Ndithu nzoipa kwabasi zomwe iwo akhala akuchita

    [10] “Sasunga chibale pa okhulupirira ngakhale pangano. Awo ndiwo opyola malire

    [11] “Koma ngati alapa nayamba kupemphera Swala ndikupereka chopereka (Zakaat), ndiye kuti ndi abale anu pa chipembedzo. Ndipo tikuzifotokoza Ayah zi (mwabwino) kwa anthu odziwa

    [12] “Ndipo ngati aswa malumbiro awo pambuyo pomanga chipangano chawo, ndi kuyamba kutukwana chipembedzo chanu, menyanani nawo atsogoleri a kusakhulupirira. Ndithu iwo alibe mapangano, (sasunga mapangano. Menyanani nawo) kuti iwo aleke (machitidwe awo oipa)

    [13] “Kodi nchotani kuti musamenyane nawo anthu omwe aswa malonjezo awo, natsimikiza kumtulutsa (kumpirikitsa mu mzinda wa Makka, kapena kumupha) Mtumiki? Iwo ndi amene adayamba kukuputani pachiyambi, nanga mukuwaopa chotani? Allah ndiye wofunika kumuopa, ngati inu mulidi okhulupirira

    [14] “Menyanani nao; Allah awalanga kupyolera m’manja anu, ndipo awasambula ndi kukupulumutsani kwa iwo ndi kuchiritsa kuwawidwa (komwe kudali) m’mitima mwa anthu okhulupirira (chifukwa cha masautso omwe adawapeza kwa iwo)

    [15] “Ndi kuchotsa mkwiyo wa m’mitima mwawo (Asilamu). Ndi kuti Allah Alandire kulapa kwa amene wamfuna. Ndipo Allah Ngodziwa, Ngwanzeru zakuya

    [16] “Kodi mukuganiza kuti mungosiidwa chabe Allah asanawaonetsere poyera amene amenyera chipembedzo mwa inu ndi amene sachita ubwenzi (ndi wina wake) kupatula Allah ndi Mtumiki wake ndi okhulupirira? Ndipo Allah Ngodziwa zonse zimene muchita

    [17] “Nkosayenera kwa Amushirikina kukhala (ndi udindo) woyang’anira Misikiti ya Allah pomwe iwo akudzichitira okha umboni kuti ngosakhulupirira. Awo (ndi omwe) zochita zawo zabwino zapita pachabe. Ndipo iwo ku Moto adzakhala nthawi yaitali

    [18] “Ndithu oyang’anira Misikiti ya Allah ndi kuiyendera ndi amene akhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro, ndi kumapemphera Swala ndi kupereka chopereka (Zakaat) ndipo saopa aliyense koma Allah yekha. Choncho, iwowo ndi amene akuyembekezeka kukhala mwa oongoka

    [19] “Kodi kumwetsa madzi (anthu) ochita Hajj ndi kusunga Msikiti Wopatulika mukukuyesa kuti nkofanana ndi yemwe wakhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro, ndi kumenya nkhondo pa njira Ya Allah? Sangakhale ofanana kwa Allah. Ndipo Allah saongola anthu ochita zolakwa

    [20] “Amene akhulupirira, ndi kusamuka, ndi kumenya nkhondo pa njira ya Allah ndi chuma chawo ndi matupi awo, ali ndi ulemelero waukulu kwa Allah. Iwowo ndiwo opambana

    [21] “Mbuye wawo akuwauza nkhani yabwino ya chifundo chochokera kwa Iye, ndi chiyanjo (Chake) ndi Minda yomwe mkati mwake adzapezamo mtendere wamuyaya

    [22] “Adzakhala m’menemo muyaya. Ndithu Allah ali nawo malipiro aakulu zedi

    [23] “E inu amene mwakhulupirira! Musawachite makolo anu ndi abale anu kukhala atetezi anu ngati (iwo) akukonda kusakhulupirira m’malo mokhulupirira. Ndipo mwa inu amene ati awasankhe kukhala atetezi, otero ndiwo adzichitira okha zoipa

    [24] “Nena: “Ngati makolo anu, ana anu, abale anu, akazi anu, ndi anansi anu ndi chuma chimene mwachipata, ndi malonda anu amene mukuopa kuti angaonongeke, ndi nyumba zanu zimene mukuzikonda, (ngati zinthuzi zili) zokondeka kwamhiri kwa inu kuposa Allah ndi Mtumiki Wake ndi kuchita Jihâd pa njira Yake, choncho dikirani kufikira Allah adzabwera ndi lamulo Lake (lokukhaulitsani). Ndipo Allah satsogolera anthu otuluka m’chilamulo (Chake)

    [25] “Ndithu Allah wakhala akukupulumutsani (kwa adani anu) m’malo ambiri omenyanira nkhondo, ndi pa tsiku la Hunaini, pamene kudakunyengani kuchuluka kwanu. Koma sikudakuthandizeni chilichonse. Ndipo dziko lidakupanani ngakhale kuti lidali lotambasuka ndipo kenako mudatembenukira kumbuyo (kuthawa)

    [26] “Kenaka Allah adatsitsa mpumulo Wake kwa Mtumiki Wake ndi kwa okhulupirira. Ndipo adatsitsa asilikali ankhondo (angelo) omwe simudawaone. Ndipo adawakhaulitsa osakhulupirira. Imeneyo ndiyo mphoto ya osakhulupirira

    [27] “Ndipo pambuyo pa izi, Allah alandira kulapa kwa amene wamfuna (mwa osakhulupirira powalowetsa m’Chisilamu). Ndipo Allah Ngokhululuka Ngwachisoni chosatha

    [28] “E inu amene mwakhulupirira! Ndithu opembedza mafano ndi nyansi, choncho, asayandikire Msikiti Wopatulika chikatha chaka chaochi. Ngati mukuopa umphawi, posachedwa Allah Akulemeretsani ndi zabwino Zake akafuna. Ndithu Allah Ngodziwa zonse, Ngwanzeru zakuya

    [29] “Menyanani ndi omwe sakhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro, omwenso sakusiya zoletsedwa zomwe Allah ndi Mtumiki Wake waletsa; omwenso satsatira chipembedzo choona mwa amene adapatsidwa mabuku. (Menyanani nawo) kufikira apereke msonkho ndi manja awo uku ali odzichepetsa

    [30] “Ndipo Ayuda akunena kuti Uzairi ndimwana wa Mulungu, naonso Akhrisitu akunena kuti Mesiya (Isa {Yesu}) ndimwana wa Mulungu. Awa ndi mawu amene akunena ndi pakamwa pawo (popanda umboni wochokera kwa Allah); akutsanzira zonena za omwe sadakhulupirire kale. Allah awaononge; kodi iwo akusokera chotani (kusiya choonadi)

    [31] “Awachita ophunzira a za chipembedzo chawo ndi ansembe awo kukhala milungu kusiya Allah (powatsata pa zimene akuwalamula popanda umboni wa Allah). (Amsandutsanso) Mesiya (Isa {Yesu}) mwana wa Mariya (kukhala mulungu); chikhalirecho sadalamulidwe china koma kupembedza Mulungu Mmodzi. Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye, wapatukana ndi zimene akumphatikiza nazozo

    [32] “Akufuna kuzimitsa kuunika kwa Allah (Chisilamu) ndi pakamwa pawo; ndipo Allah sadzalola koma kukwaniritsa kuunika kwake ngakhale kuti osakhulupirira zikuwanyansa

    [33] “Iye ndi Yemwe adatuma Mtumiki Wake ndi ulangizi ndiponso chipembedzo choona kuti achiwonetsere pa zipembedzo zonse, ngakhale atanyansidwa nazo Amushirikina

    [34] “E inu amene mwakhulupirira! Ndithu ambiri ophunzira a za chipembedzo cha Chiyuda ndi cha Chikhristu, akudya chuma cha anthu mwachinyengo ndi kusekeleza anthu ku njira ya Allah. Ndipo amene akusonkhanitsa golide ndi siliva popanda kuzipereka pa njira ya Allah, auze nkhani ya chilango chowawa

    [35] “Pa tsiku lomwe (chuma chawo) chidzatenthedwa ku moto wa Jahannam, ndipo ndi chumacho zidzatenthedwa nkhope zawo, nthiti zawo ndi misana yawo (ali kuwuzidwa kuti): “Izi ndi zija zomwe mudadzisungira nokha. Choncho lawani (chilango) cha zomwe mudali kuzisunga

    [36] “Ndithu chiwerengero cha miyezi kwa Allah (pa chaka), ndi miyezi khumi ndi iwiri m’chilamulo cha Allah kuyambira tsiku lomwe adalenga thambo ndi nthaka. M’menemo muli miyezi inayi yopatulika. Ichi ndicho chipembedzo cha Allah cholunjika, choncho musadzichitire nokha zoipa m’menemo. Ndipo menyanani ndi Amshrikina nonse pamodzi monga momwe akumenyana nanu onse pamodzi. Ndipo dziwani kuti Allah ali pamodzi ndi oopa

    [37] “Ndithu kutalikitsa ndi kuchedwetsa (mwezi wopatulika kuti usafike mwamsanga), kumaonjezera kusakhulupirira (mwa Allah), zoterozo akusokerezedwa nazo amene sadakhulupirire. Chaka china amauyesa wosapatulika pomwe chaka china amauyesa wopatulika ndi cholinga chokwaniritsa chiwerengero cholingana ndi miyezi yomwe Allah adaipatula kukhala yopatulika. Choncho, chimene Allah adaletsa, amachiyesa chololedwa. Zakometsedwa kwa iwo zochita zawo zoipa. Ndipo Allah sawatsogolera anthu osakhulupirira

    [38] “E inu amene mwakhulupirira! Mwatani; mukauzidwa (kuti): “Pitani mukachite Jihâd pa njira ya Allah,” mukudziremetsa pa nthaka (polemedwa ndi kutulukako)? Kodi mwasangalatsidwa ndi moyo wa pa dziko lapansi kuposa moyo wa tsiku lachimaliziro? Koma zosangalatsa za m’moyo wa dziko lapansi poyerekeza ndi (moyo wa) tsiku lachimaliziro, ndi zochepa kwambiri

    [39] “Ngati simupita (ku nkhondoko), (Allah) akulangani ndi chilango chowawa, ndipo abweretsa anthu ena m’malo mwa inu; ndipo simungamuvutitse ndi chilichonse (ngati musiya kupita kukamenyera chipembedzo Chake). Ndipo Allah Ngokhoza chilichonse

    [40] “Ngati simumthandiza (Mtumuki Muhammad {s.a.w} palibe kanthu), ndithu Allah adamthandiza pamene adamtulutsa aja amene sadakhulupirire. Pamene adali awiriwiri kuphanga, pamene ankanena kwa mnzake: “Usadandaule. Ndithu Allah ali nafe pamodzi.” Ndipo Allah adatsitsa mpumulo Wake pa iye, ndipo adaamthangata ndi asilikali a nkhondo omwe simudawaone. Ndipo mawu a amene sadakhulupirire adawachita kukhala apansi ndipo mawu a Allah ndiwo apamwamba. Ndipo Allah Ngopambana, Ngwanzeru zakuya

    [41] “Pitani (mukamenyane) muli opepukidwa ndi olemedwa; ndipo menyerani njira ya Allah nchuma chanu ndi inu nomwe. Zimenezi nzabwino kwa inu ngati muli anthu odziwa

    [42] “Ukadakhala ulendo wokafuna za m’dziko zopepuka kuzipeza, ndi ulendo wofupika, ndithu akadakutsata (achiphamaso). Koma ulendo wamavutowu wakhala wautali kwa iwo. Ndipo iwo alumbilira Allah (ponena kuti): “Kukadakhala kotheka kwa ife, tikadapita nanu.” (Pa mawu awa), akudziononga okha. Ndipo Allah akudziwa kuti iwo Ngabodza

    [43] Allah wakukhululukira. Bwanji wawaloleza kutsalira? (Ukadayembekeza) kufikira adziwike kwa iwe amene akunena zoona, ndikuti uwadziwe abodza

    [44] “Sangakupemphe chilolezo (chotsala ku nkhondo) amene akhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro kuti asapite kukamenyera (chipembedzo cha Allah) ndi chuma chawo ndi Matupi awo. Ndipo Allah akuwadziwa amene akumuopa

    [45] “Ndithu amakupempha chilolezo aja amene sakhulupirira Allah ndi tsiku la chimaliziro, ndipo mitima yawo yakaikira, ndipo iwo, chifukwa cha kukaika kwawo akungotekeseka

    [46] “Akadafunadi kuti atuluke (kupita ku nkhondo) akadakonzekera zokonzekera za ku nkhondo; koma Allah sadafune kuti iwo apiteko; choncho adawatsekereza, ndipo kudanenedwa: “Khalani pamodzi ndi Otsalira.”

    [47] “Ngati akadatuluka nanu pamodzi, sakadakuonjezerani chilichonse koma chisokonezo ndi kuyenda mwa ukazitape pakati panu ndicholinga chokufunirani chisokonezo, ndipo mwa inu alipo akuwamvelera, ndipo Allah Ngodziwa za oipa

    [48] “Ndithudi, akhala akukufunirani chisokonezo kuyambira kale, akusanthulirasanthulira zinthu (n’cholinga choti athane nawe) kufikira choonadi chadza ndi kuonekera poyera lamulo la Allah (lowakhaulitsa Ayuda) iwo asakufuna

    [49] “Ndipo mwa iwo pali yemwe akuti: “Ndiloreni ine (kuti nditsale ku nkhondo) ndipo musandiponye m’mayeso (kuopa kuti ndingalakwe ndikaona akazi akumeneko).” Dziwani kuti iwo agwera kale m’mayesero. Ndipo, ndithu Jahannam ikawazinga mbali zonse osakhulupirira

    [50] “Chikakupeza chabwino, (iwe Mtumiki Muhammad (s.a.w) ndi okutsatira) zimawanyansa, ndipo vuto likakupeza amanena: “Tidalingalira zinthu zathu kale. (Nchifukwa chake mavuto atizemba).” Ndipo amatembenuka nkupita uku akukondwa

    [51] “Nena: “Palibe chomwe chitipeze koma chimene Allah watilembera. Iye ndi Mbuye wathu.” Choncho, Asilamu ayadzamire kwa Allah Yekha

    [52] “Nena: “Kodi chilipo chimene mukuyembekezera mwa ife posakhala chimodzi mwa zinthu ziwiri zabwino, (kupambana pa nkhondo ndi kupeza zotolatola zake, kapena kufa ndikukalowa ku Munda wamtendere)? Ndipo nafe tikukuyembekezerani kuti Allah akupatsani chilango chochokera kwa Iye, kapena kupyolera m’manja mwathu. Choncho bayembekezerani; nafenso tikuyembekezera nanu limodzi.”

    [53] “Nena (kwa achiphamaso): “Perekani (chuma chanu) mwa chifuniro kapena mosafuna sichizalandiridwa kwa inu. Ndithu inu ndinu anthu otuluka m’chilamulo cha Allah.”

    [54] “Palibe chomwe chidaletsa kulandiridwa kwa zopereka zawo koma chifukwa chakuti iwo sadakhulupirire Allah ndi Mtumiki Wake; ndiponso sapita kopemphera koma mwaulesi; ndipo sapereka chopereka koma monyinyirika

    [55] “Ndipo chisakudolole chuma chawo kapena ana awo. Ndithu Allah akufuna kuwalanga nazo pa moyo wa pa dziko lapansi, ndi kuti mitima yawo ichoke ali osakhulupirira

    [56] “Ndipo akulumbira (m’dzina la) Allah kuti iwo ali pamodzi ndi inu; pomwe iwo sali pamodzi nanu koma ndithu iwo ndi anthu amantha

    [57] “Ngati akadapeza linga lothawiramo pena mapanga kapena pamalo pena polowa (ndithu) akadathawira kumeneko mwa liwiro

    [58] “Ndipo alipo ena mwa iwo (achiphamaso) amene akukunyogodola mkugawa kwako sadaka. Akapatsidwa kanthu m’menemo amakondwera koma akapanda kupatsidwa akukwiya nawe

    [59] “Ndipo ngati iwo akadakondwera ndi chimene Allah ndi Mtumiki Wake wawapatsa, nanena: “Allah watikwanira. Posachedwapa Allah ndi Mtumiki Wake atipatsa zabwino Zake. Ndithu ife tikufunitsitsa kwa Allah.” (Ndiye kuti Allah akadawapatsa zambiri)

    [60] “Ndithu sadaka (za Zakaati) ndi za mafukara, masikini, ogwira ntchito yosonkhetsa sadakazo, owalimbitsa mitima yawo (pa Chisilamu amene alowa kumene), kuombolera akapolo (kuti akhale afulu), kuthandizira amene ali m’ngongole; kuzipereka pa njira ya Allah; ndi kuwapatsa a paulendo (omwe alibe choyendera). Ili ndi lamulo lochokera kwa Allah, ndipo Allah Ngodziwa kwabasi, Ngwanzeru zakuya

    [61] “Ndipo alipo ena mwa iwo amene akuzunza Mneneri ponena kuti: “Uyu ndi khutu (lomvetsera nkhani iliyonse popanda kuiganizira).” Nena: “Ndi khutu labwino kwa inu.” (Mwini khutulo) amakhulupirira Allah, amakhulupirira (zonena) za okhulupirira, ndipo (iye) ndichifundo kwa amene akhulupirira mwa inu. Ndipo amene akuvutitsa Mtumiki wa Allah adzakhala ndi chilango chopweteka

    [62] “Akulumbira kwa inu potchula dzina la Allah kuti akukondweretseni (chikhalirecho akunyoza Allah ndi Mtumiki Wake), pomwe Allah ndi Mtumiki Wake ndiye wofunika kuti amkondweretse ngati iwo ngokhulupiriradi (mwachoonadi)

    [63] “Kodi sadziwa kuti amene akulimbana ndi Allah ndi Mtumiki Wake, adzapeza moto wa Jahannam ndi kukhalamo nthawi yaitali? Kumeneko ndikuyaluka kwakukulu

    [64] “Achiphamaso akuopa kuwatsikira Sura yomwe ingawafotokozere (zachinyengo chawo) chomwe chili m’mitima mwawo. Nena: “Chitani zachipongwe. Ndithu Allah atulutsira poyera zomwe mukuziopazo (kuti Asilamu asazidziwe).”

    [65] “Ndipo utawafunsa (chifukwa ninji chipembedzo akuchichitira chipongwe)? Anena: “Ife timangosereula ndi kusewera basi (palibe china).” Nena: “Mumachitira Allah ndi Ayah (ndime) Zake ndi Mtumiki Wake zachipongwe?”

    [66] “Musapereke madandaulo (abodza), ndithu mwaonetsera ukafiri wanu poyera, pambuyo pa kukhulupirira kwanu (kwabodza). Ngati gulu lina mwa inu tilikhululukira (litalapa), gulu lina tililanga chifukwa cha kupitiriza kulakwa kwawo

    [67] “Achiphamaso aamuna ndi achiphamaso aakazi onse khalidwe lawo ndi limodzi. Amalamulira zoipa ndikuletsa zabwino, ndipo amafumbata manja awo (sathandiza pa zabwino). Amuiwala Allah (ponyozera malamulo Ake). Iyenso wawaiwala (powanyozera). Ndithu achiphamaso ngotuluka mchilamulo (cha Allah)

    [68] “Allah walonjeza achiphamaso aamuna ndi achiphamaso aakazi ndi akafiri moto wa Jahannam, akakhala m’menemo nthawi yaitali. Umenewo ukukwanira kwa iwo (kuwalanga). Ndipo Allah wawatembelera, ndipo iwo adzapeza chilango cha nthawi zonse

    [69] “(Inu osakhulupirira) ndinu ofanana ndi amene adalipo patsogolo panu. (Tikuonongani monga tidawaonongera iwo; koma) iwo adali ndi nyonga zambiri kuposa inu; adalinso ndi chuma chambiri ndi ana ambiri kuposa inu. Choncho, adasangalalira gawo lawo, inunso mukusangalalira gawo lanu monga momwe adasangalalira gawo lawo omwe adalipo patsogolo panu, ndipo mwamira m’zoipa monga momwe adamilira iwo. Awo ndi amene zochita zawo zidapita pachabe padziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro. Awo ndi omwe ali otaika (oluza)

    [70] “Kodi siidawadzere nkhani ya amene adalipo patsogolo pawo anthu a Nuh, Âdi ndi Samudu; anthu a Ibrahim ndi anthu a ku Madiyan ndi (anthu) a m’midzi imene idatembenuzidwa kumwamba kukhala pansi, pansi kukhala kumwamba? Atumiki awo adawadzera ndi zisonyezo zoonekera (koma adakana kuwatsata. Choncho, Allah adawaononga). Allah sadawachitire choipa, koma ankadzichitira okha zoipa

    [71] “Okhulupirira aamuna ndi okhulupirira aakazi, ndiabwenzi omvana pakati pawo. Amalamula zabwino ndikuletsa zoipa ndipo amapemphera Swala ndi kupereka chopereka (zakaat), ndipo amamvera Allah ndi Mtumiki Wake. Awo ndi omwe Allah adzawachitira chifundo. Ndithu Allah Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya

    [72] “Allah waalonjeza okhulupirira aamuna ndi okhulupirira aakazi Minda yomwe pansi (ndi patsogolo) pake mitsinje ikuyenda, adzakhala m’menemo nthawi yaitali. Ndi mokhala mwabwino m’Minda ya Edeni. Ndipo chiyanjo chochokera kwa Allah ndichachikulu (omwe ndi mtendere waukulu kwambiri kuposa zonse). Kumeneko ndiko kupambana zedi

    [73] “E iwe Mneneri! Limbana ndi osakhulupirira ndi achiphamaso ndipo uwaumire mtima. Mbuto yawo ndi ku Jahannam. Taonani kuipa kwa malo obwerera

    [74] “(Achiphamaso pambuyo pomunenera Allah ndi Mtumiki Wake mawu oipa), akulumbira potchula dzina la Allah (kuti) sadanene (zonyoza), pomwe adanenadi mawu aukafiri, ndipo akana chikhulupiliro pambuyo posonyeza Chisilamu chawo (chabodza); ndipo adatsimikiza (kuchita) zomwe sadathe kuzifika. Komatu sadaone choipa (m’kudza kwa Chisilamu), koma kuti Allah ndi Mtumiki Wake adawalemeretsa ndi zabwino zake. Choncho Ngati alapa, zikhala zabwino kwa iwo. Ndipo ngati anyoza, Allah awalanga ndi chilango chowawa pa moyo wa pa dziko lapansi ndi patsiku lachimaliziro. Ndipo sadzakhala ndi mtetezi ngakhale aliyense wowapulumutsa pa dziko

    [75] “Pakati pawo alipo amene adalonjeza Allah kuti, “Ngati atipatsa zabwino zake (chuma) tidzapereka sadaka ndi kukhala m’gulu la ochita zabwino.”

    [76] “Koma pamene adawapatsa zabwino Zakezo, adazichitira umbombo nanyoza, natembenukira kutali (ndi Allah)

    [77] “Choncho, chotsatira chake adawaika chinyengo m’mitima mwawo kufikira tsiku lokumana naye (Allah), chifukwa cha kuphwanya kwawo zomwe adamulonjeza Allah. Ndiponso chifukwa cha zabodza zomwe ankanena

    [78] “Kodi sadziwa kuti Allah akudziwa zobisika zawo ndi manong’onong’o awo ndikuti Allah Ngodziwa zinthu zamseri

    [79] “Amene akuwanyogodola okhulupirira opereka sadaka yambiri, ndiponso (amene akunyoza) amene sapeza (chopereka) koma chinthu chochepa; ndikumawachitira chipongwe, Allah adzawalipira chipongwe chawocho. Iwo adzapeza chilango chopweteka

    [80] “(E iwe Mtumiki!) Uwapemphere chikhululuko (achiphamaso) kapena usawapemphere, (zonsezo nchimodzimodzi). Ngakhale utawapemphera chikhululuko chochuluka kwabasi mokwanira makumi asanu ndi awiri Allah sangawakhululukire. Zimenezo nchifukwa chakuti iwo amkana Allah ndi Mtumiki Wake. Ndipo Allah satsogolera anthu ophwanya malamulo (Ake)

    [81] “Akondwa amene adasiidwa m’mbuyo (osapita kunkhondo) chifukwa chakukhala kwawo m’mbuyo polekana ndi Mtumiki wa Allah, nakuda kumenyana pa njira ya Allah ndi chuma chawo ndi miyoyo yawo, nati (kwa anzawo): “Musapite (ku nkhondo) m’nthawi yotenthayi.” Auze: “Moto wa Jahannam ngotentha kwambiri akadakhala akuzindikira.”

    [82] “Choncho, aseke pang’ono (padziko lapansi). Ndipo adzalira kwambiri (patsiku lachimaliziro); (iyo ndi) mphoto ya zomwe adapeza (kuchokera m’zochita zawo zoipa)

    [83] “Ngati Allah akubweza (ku nkhondoko) nkufika kugulu lina la mwa iwo ndipo iwo nkukupempha chilolezo chakutuluka (kupita ku nkhondo zomwe zidzapezeke mtsogolo), nena: “Inu simudzatuluka nane mpaka muyaya, ngakhalenso kumenyana ndi adani pamodzi nane; inu mudakonda kukhala nthawi yoyamba; choncho khalani (nthawi zonse) pamodzi ndi otsalira (pambuyo).”

    [84] “Ndipo usamupemphelere konse aliyense wa iwo yemwe wamwalira, ndipo usaimilire pamanda ake (kumpemphelera); ndithu iwo amukana Allah ndi Mtumiki Wake, ndipo amwalira uku ali opandukira chilamulo (cha Allah)

    [85] “Ndipo chisakudolole chuma chawo kapena ana awo. Ndithu Allah akufuna kuwalanga ndi zimenezo pa dziko lapansi, ndi kuti mizimu yawo ichoke ali osakhulupirira

    [86] “Ndipo Sura ikavumbulutsidwa (yonena kuti): “Mkhulupirireni Allah ndi kumenya nkhondo (chifukwa cha chipembedzo Chake) pamodzi ndi Mtumiki Wake,” opeza bwino mwa iwo akukupempha chilolezo (kuti asapite ku nkhondo), ndipo akuti: “Tisiye tikhale pamodzi ndi okhala (otsalira m’mbuyo).”

    [87] “Akondwera pokhala limodzi ndi otsalira m’mbuyo (akazi ndi ana). Ndipo mitima yawo yadindidwa chidindo (yatsekedwa), choncho iwo sazindikira

    [88] “Koma Mtumiki ndi amene akhulupirira pamodzi ndi iye amenya nkhondo ndi chuma chawo ndi matupi awo. Iwowo ndiwo opeza zabwino, ndiponso iwowo ndiwo opambana

    [89] “Allah wawakonzera minda yoyenda mitsinje pansi (ndi patsogolo) pake; adzakhala m’menemo nthawi yaitali. Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu

    [90] “Ndipo adza eni madandaulo (owona) mwa anthu akumidzi (omwe ndi Asilamu) kuti awapatse chilolezo (chosapita ku nkhondo). Koma adakhala (popanda kupempha chilolezo kwa Mtumiki) amene amunamiza Allah ndi Mtumiki Wake. (Amenewa ndi achiphamaso omwe amadzitcha kuti ndi Asilamu pomwe sadali Asilamu). Mwa iwo amene sadakhulupirire Allah chiwapeza chilango chopweteka

    [91] “Palibe tchimo (kusapita kunkhondo) kwa amene ali ofooka (pachilengedwe chawo), ngakhale kwa odwala, ngakhale kwa omwe sapeza chothandiza (pa ulendo ngakhale chosiira akubanja lawo) ngati iwo ali ndi cholinga chabwino pa Allah ndi Mtumiki Wake. Palibe njira (yowadzudzulira) amene akuchita zabwino. Ndipo Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni zedi

    [92] “Ndiponso (palibe tchimo) kwa amene akukudzera kuti uwatenge (kupita ku nkhondo) iwe uunena: “Ndilibe choti ndikunyamulireni,” nabwerera maso awo akutuluka misozi chifukwa cha kudandaula posapeza zimene zingawathandize pa ulendowo

    [93] “۞ Ndithu njira (yodzudzulidwa) ili pa arnene akukupempha chilolezo (choti asapite ku nkhondo ndi kusiyanso kupereka chuma chawo) pomwe iwo ngolemera. Akonda kukhala pamodzi ndi otsala m’mbuyo. Ndipo Allah wadinda chidindo (cha mantha) m’mitima mwawo, tero sadziwa (chilichonse chowathandiza)

    [94] “Akudandaulirani madandaulo mukabwerera kwa iwo (ndi kukumana nawo). Nena: “Musapereke madandaulo; sitikukhulupirirani. Allah watifotokozera kale nkhani zanu. Posachedwa Allah ndi Mtumiki Wake aona zochita zanu, kenako muzabwezedwa (pambuyo pa imfa) kwa Wodziwa zamseri ndi zoonekera. Choncho, Iye adzakufotokozerani zimene mudali kuchita.”

    [95] “Mukabwerera kwa iwo, adzalumbira m’dzina la Allah kwa inu kuti muwasiye (musawachite kanthu). Choncho, apatukireni. Ndithu iwo ndiuve ndipo malo awo ndi ku Jahannam. Iyi ndi mphoto ya zomwe adali kupeza (kuchokera m’zochita zawo zoipa)

    [96] “Akulumbira kwa inu kuti muwayanje, choncho ngati muwayanja, ndithu Allah sayanja anthu otuluka m’chilamulo

    [97] “Arabu a kumizi ngoyipitsitsa pa kusakhulupirira ndi uchiphamaso ndiponso ngoyenera kusazindikira malire a zomwe Allah wavumbulutsa kwa Mtumiki Wake. Komatu Allah Ngodziwa kwambiri, Ngwanzeru zakuya

    [98] “Ndipo alipo ena mwa Arabu a kuchimizi omwe amachichita chimene akupereka pa njira ya Allah ngati dipo (laulere lopanda phindu), ndikumadikira kwa inu kuti miliri ikupezeni. Miliri yoipa ili pa iwo; (iwapeza okha). Ndipo Allah Ngwakumva (nkhani iliyonse), Wodziwa (chilichonse)

    [99] “Ndipo alipo ena mwa Arabu a kuchimizi omwe akukhulupirira Allah ndi tsiku lachimaliziro ndipo zomwe akupereka (pa njira ya Allah) amazichita monga chodziyandikitsira nacho kwa Allah, ndi (chowachititsa kuti apeze) mapemphero a Mtumiki. Tamverani! Ndithu zimenezo ndizinthu zowayandikitsa kwa Allah. Allah adzawalowetsa ku Mtendere Wake. Ndithu Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha

    [100] “Ndipo amene adatsogolera poyamba, a m’gulu la Amuhajirina ndi Answari, ndi omwe adawatsatira iwo mwa ubwino, Allah adzakondwa nawo. Naonso adzakondwera Naye (pa zomwe adzapatsidwa ndi Allah). Ndipo wawakonzera minda yomwe mitsinje ikuyenda pansi (ndi pasogolo) pake, adzakhala m’menemo muyaya. Uko ndikupambana kwakukulu

    [101] “Ndipo ena mwa Arabu a kuchimizi omwe akukhala m’mphepete mwanu (m’mphepete mwa mzinda wa Madina) alipo achiphamaso (achinyengo), ndiponso eni mzinda wa Madina aphunzira ukatswiri wachinyengo (kotero kuti) sukuwadziwa, Ife tikuwadziwa. Tiwalanga kawiri (pa dziko lapansi) ndipo kenako adzabwezedwa kuchilango chachikulu (pa tsiku lachimaliziro)

    [102] “Ndipo alipo ena omwe avomereza uchimo wawo (nalapa kwa Allah). Asakaniza zochita zabwino ndi zina zoipa. Ndithu Allah alandira kulapa kwawo. Ndithu Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha

    [103] “Tenga sadaka (Zakaat) m’chuma chawo kuti uwayeretse nayo (kumachimo ndi umbombo) ndi kuti uwatukulire nayo ulemelero wawo kwa Allah; ndipo apemphere (zabwino ndi chiongoko). Ndithu mapemphero ako kwa iwo ndimpumulo. Ndipo Allah Ngwakumva, Wodziwa (chilichonse)

    [104] “Kodi sadziwa kuti Allah ndi Yemwe amalandira kulapa kwa akapolo Ake, ndi kulandira sadaka, ndikuti Allah ndi Mwini kulandira kulapa mochuluka ndiponso Wachisoni chosatha

    [105] “Ndipo auze: “Gwirani ntchito; Allah ndi Mtumiki Wake ndi okhulupirira aona ntchito yanuyo posachedwa. Ndipo (kenako) mudzabwezedwa kwa Wodziwa zamseri ndi zoonekera poyera. Choncho adzakuuzani zonse (zimene) mudali kuchita.”

    [106] “Ndipo aliponso ena amene (adagwa m’machimo omwe) akuyembekezera lamulo la Allah, (kulapa kwawo sikunavomerezekebe), kapena awalanga kapenanso awavomera kulapa kwawo. Ndipo Allah Ngodziwa (khalidwe lawo ndi zomwe zili m’mitima mwawo), Wanzeru zakuya (pa zonse zomwe akuchita kwa anthu Ake popereka mphoto ndi chilango)

    [107] “Ndipo (alipo achiphamaso ena) amene adamanga msikiti ndi cholinga chodzetsa masautso ndi (kulimbikitsa) kusakhulupirira Allah ndi kuwagawa okhulupirira (mu umodzi wawo) ndi kuupanga kukhala msasa wa omwe adamthira nkhondo Allah ndi Mtumiki Wake kale. Ndithu alumbira (ndikunena): “Sitidali ncholinga china (pomanga msikitiwo) koma ubwino.” Koma Allah akuikira umboni kuti iwo ngabodza

    [108] “Usaimilire (ndi kupemphera) m’menemo mpang’ono pomwe. Ndithu msikiti umene udakhazikitsidwa poyamba ncholinga choopa Allah ndiwo wofunika kuti uimilire m’menemo (ndi kupemphera). M’menemo muli anthu okonda kudziyeretsa (matupi ndi mitima yawo); ndipo Allah amakonda odziyeretsa

    [109] “Kodi amene wakhazikitsa maziko a chomanga chake chifukwa choopa Allah ndi kufunafuna chiyanjo (Chake), sindiye wabwino, kapena Yemwe wakhazikitsa maziko a chomanga chake m’mphepete mwa dzenje (lakuya) lomwe dothi lake likugumukira (m’dzenjemo) ndipo nkugwa pamodzi naye m’moto wa Jahannam, (ameneyu ndiye wabwino)? Ndithudi, Allah saongolera anthu ochita zoipa

    [110] “Chomanga chawo chomwe adachimanga sichileka kudzetsa chikaiko ndi kusakhazikika m’mitima mwawo kufikira mitima yawo itaduka (ndi madandaulo kapena imfa). Ndipo Allah Ngodziwa (chilichonse), Ngwanzeru zakuya (m’zochitachita Zake)

    [111] “Ndithu Allah wagula kwa okhulupirira moyo wawo ndi chuma chawo (kuti apereke moyo wawo ndi chuma chawo pomenya nkhondo pa njira ya Allah) kuti iwo alandire Munda wamtendere. Akumenya nkhondo pa njira ya Allah, ndipo akupha ndi kuphedwa. Ili ndi lonjezo loona lokakamizika pa Iye lomwe likupezeka m’buku la Taurati, Injili ndi Qur’an. Kodi ndani wokwaniritsa lonjezo lake kuposa Allah? Choncho kondwerani ndi kugulitsa kwanu komwe mwagulitsana Naye. Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu

    [112] “(Awo amene alonjezedwa kupeza izi, ndi) omwe amalapa (akalakwa); ochita mapemphero (awo m’njira yoyenera); otamanda Allah kwambiri; ochulukitsa kusala (Swaumu kapena oyendayenda padziko ncholinga chochitira zabwino anthu), owerama, ogwetsa nkhope zawo pansi; olamula zabwino; oletsa zoipa ndi osunga malire a Allah (malamulo Ake). Choncho, auze nkhani yabwino awo amene akhulupirira

    [113] “Nkosayenera kwa Mneneri ndi amene akhulupirira kuwapemphera chikhululuko opembedza mafano ngakhale atakhala abale awo, pambuyo poonekera kwa iwo kuti iwowo ndi anthu a ku Moto

    [114] “Ndipo sikudali kupempha chikhululuko kwa Ibrahim kuwapemphera bambo wake koma chifukwa cha lonjezo lomwe adamulonjeza. Koma pamene zidaonekera kwa iye poyera kuti iwo (bambo wake) ndi mdani wa Allah, adadzipatula kwa iwo. Ndithudi, Ibrahim adali wochulukitsa kupempha Allah modzichepetsa, woleza mtima

    [115] “Ndipo Allah sangasokeretse anthu (ndi kupititsa chilango pa iwo) pambuyo powaongolera ku Chisilamu; koma pokhapokha atawonetsa poyera kwa iwo zimene zingafunike kuzipewa. Ndithu Allah Ngodziwa chilichonse

    [116] “Ndithudi, Allah ndi Wake ufumu wakumwamba Ndi pansi. Amapereka moyo ndi imfa. Inu mulibe mtetezi ngakhale mthandizi koma Allah basi

    [117] “Ndithu Allah wafunira zabwino Mtumiki Wake ndi Amuhajirina ndi Answari amene adamtsatira iye (Muhammad {s.a.w}) m’nthawi yamasautso (pokamenyana ndi Aroma pankhondo ya Tabuk), nthawi yomwe mitima ya ena a iwo idatsala pang’ono kupotoka (kutsata machitidwe achikafiri); kenako Allah adawatembenukira ndi chifundo. Ndithu Iye (Allah) kwa iwo Ngodekha, Ngwachisoni chosatha

    [118] “Ndiponso (adawatembenukira mwachifundo) aja atatu amene adawadikiritsa (pakusavomera msanga kulapa kwawo), kufikira pamene dziko lidawapana ngakhale lidali lophanuka, nabanika m’mitima mwawo natsimikiza kuti palibe komuthawira Allah (kwina) koma kwa Iye (Allah polapa). Kenako (Allah) adawatsogolera kulapa kuti alape. Ndithu Allah Ngolandira kulapa, Ngwachisoni chosatha

    [119] “E inu amene mwakhulupirira! Opani Allah, ndipo khalani pamodzi ndi owona (amene akuchitsimikiza Chisilamu chawo ndi zochita zawo, osati kungoyankhula pakamwa pokha)

    [120] “Nkosayenera kwa anthu a mu mzinda wa Madina ndi amene ali m’mphepete mwawo, mwa Arabu a kuchimizi, kutsalira m’mbuyo mwa Mtumiki wa Allah (poleka kutsagana naye ku nkhondo), ndiponso nkosayenera kwa iwo kudzikonda okha kuposa iye (Mtumiki). Zimenezo nchifukwa chakuti iwo silingaapeze ludzu kapena mavuto kapena njala pa njira ya Allah, ndipo sangaponde malo owakwiitsa osakhulupirira, ndipo sangampatse mdani chompatsa chilichonse chopweteka koma kulembedwa kwa iwo pa zimenezo (kuti achita) ntchito yabwino. Ndithu Allah sawononga malipiro a ochita zabwino

    [121] “Ndipo sangapereke chopereka chaching’ono kapena chachikulu, ndipo sangadutse ntunda wachigwa; koma kulembedwa kwa iwo kuti Allah adzawalipira malipiro abwino pa zomwe adali kuchita

    [122] “Nkosafunika kwa okhulupirira kutuluka onse (m’midzi yawo kupita ku Madina ndi kusiya midzi yopanda anthu). Nchifukwa ninji silituluka gulu m’fuko lililonse mwa iwo (ndikupita ku Madina kwa Mtumiki) kukaphunzira bwino za Chipembedzo, ndipo akawachenjeze anthu awo akazabwerera kwa iwo kuti aope

    [123] “E inu amene mwakhulupirira! Menyani nkhondo ndi awo osakhulupirira amene ali pafupi nanu, ndipo apeze kuuma mtima mwa inu. Ndipo dziwani kuti ndithu Allah ali pamodzi ndi oopa (Iye)

    [124] “Ndipo nthawi zonse sura (yatsopano) ikavumbulutsidwa, alipo mwa iwo (achiphamaso) amene akunena: “Ndani mwa inu sura iyi yamuonjezera chikhulupiliro?” Koma amene akhulupirira yawaonjezera chikhulupiliro ndipo iwo akukondwera

    [125] “Koma amene ali ndi matenda m’mitima mwawo, yawaonjezera zoipa pamwamba pa zoipa zomwe adali nazo, ndipo akufa ali osakhulupirira

    [126] “Kodi saona kuti iwo akuyesedwa mayeso chaka chilichonse kamodzi, kapena kawiri, (kapena kochulukirapo)? Koma salapa (kwa Allah) ndiponso iwo sakumbukira

    [127] “Ndipo nthawi iliyonse sura yatsopano ikavumbulutsidwa amayang’anana (iwo achiphamaso kuti athawe, asamvere mawu ake, uku akuuzana pakati pawo): “Kodi alipo amene akukuonani?” Kenako amatembenuka nkuthawa. Tero, Allah waikhotetsa mitima yawo chifukwa chakuti iwo ndi anthu osazindikira

    [128] “Ndithu wakudzerani Mtumiki wochokera mwa inu. Zimamudandaulitsa iye zomwe zikukuvutitsani; iye ngoikira mtima pa inu pokufunirani zabwino; ndipo pa okhulupirira ngodekha ndiponso ngwachisoni

    [129] “Koma ngati (iwo osakhulupirira) apitiriza kunyoza, nena: “Allah wandikwanira (palibe vuto lingapezeke kuchokera kwa inu) palibe woti nkupembedzedwa koma Iye basi. Ndatsamira kwa Iye. Ndipo Iye, ndi Bwana wa Arsh (mpando wachifumu) yaikulu!”

    Yona

    Surah 10

    [1] “Alif-Lam-Ra. Izi ndi Ayah za m’buku lanzeru. (Lokamba zanzeru zokhazokha)

    [2] “Kodi nchodabwitsa kwa anthu kuti tamuvumbulutsira (chivumbulutso) munthu wochokera mwa iwo (yemwe ndi Muhammad {s.a.w}) kuti: “Chenjeza anthu ndipo awuze nkhani yabwino amene akhulupirira kuti iwo adzapeza ulemelero waukulu kwa Mbuye wawo?” Osakhulupirira adati: “Ndithudi uyu ndi wa matsenga (mfiti) wowonekera.’’

    [3] “Ndithu Mbuye wanu ndi Allah Amene adalenga thambo ndi nthaka (ndi zonse za m’menemo) m’masiku asanu ndi limodzi; (masiku omwe palibe yemwe akuwadziwa kutalika kwake koma Iye Yekha), kenako adakhazikika pa Arsh (Mpando Wake wachifumu, kukhazikika kwake akukudziwa ndi Iye Yekha basi). Amayendetsa zinthu (za zolengedwa Zake). Palibe muomboli (woombola wina) koma pambuyo pa chilolezo Chake (Allah). Uyo ndiye Allah Mbuye wanu; choncho mupembedzeni Iye. Kodi simungakumbukire (kuti mafanowo si milungu)

    [4] “Kobwerera kwanu nonsenu ndi kwa Iye. Ili ndilonjezo la Allah loona. Ndithu Iye ndi Yemwe adayamba kulenga (zolengedwa), ndiponso ndi Yemwe adzazibwereza (pambuyo pa imfa) kuti adzawalipire amene adakhulupirira ndi kumachita zabwino mwa chilungamo. Ndipo amene sadakhulupirire, akapeza zakumwa za madzi owira ndi chilango chopweteka chifukwa cha kusakhulupirira kwawo

    [5] “Iye (Allah) ndiYemwe adapanga dzuwa kukhala lowala, ndi mwezi kukhala wounika; ndipo adaukonzera mbuto (masitesheni) kuti mudziwe kuchuluka kwa zaka ndi chiwerengero chake. Allah sadalenge zimenezo koma mwachoonadi (ndi cholinga cha nzeru). Akufotokoza Ayah (Zake) kwa anthu ozindikira

    [6] “Ndithu m’kusinthanasinthana kwa usiku ndi usana, ndi zomwe Allah walenga kumwamba ndi pansi, ndithudi, ndi zisonyezo kwa anthu oopa (Allah)

    [7] “Ndithu amene sayembekeza kukumana Nafe, nakondetsetsa umoyo wapadziko lapansi ndi kukhazikika (mtima) ndi za mmenemo, ndi omwe akunyozera Ayah Zathu

    [8] “Iwowo (onse) malo awo ndi ku Moto chifukwa cha zomwe adazipeza (m’njira zosayenera)

    [9] “Ndithu amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, Mbuye wawo awaongola chifukwa cha chikhulupiliro chawo. Pansi (ndi patsogolo) pawo mitsinje ikuyenda m’Minda yamtendere

    [10] “Mapemphero awo m’menemo adzakhala kunena: “Subuhanaka Lahuma’ Ulemelero ndi Wanu, E Inu Allah!” Ndipo kulonjerana kwawo m’menemo kudzakhala kunena: “Salaam (alayikum’) Mtendere (ukhale pa inu).” Ndipo duwa yawo yomaliza (idzakhala kuyamika ponena kuti) “Alham’du Lillah Rabil a’lamin’. Kuyamikidwa konse nkwa Allah Mbuye wa zolengedwa.”

    [11] “Ndipo Allah akadakhala kuti akuwapatsa anthu zoipa mwachangu (zomwe iwo akuzifulumizitsa) monga mmene amawapatsira mwachangu zabwino (akamupemphamo, ndiye kuti) ikadalamulidwa nthawi yawo (yowaonongera koma Allah amawamvera chisoni), koma amene saopa kukumana Nafe tikuwasiya akuyumbayumba m’zoipa zawo

    [12] “Ndipo vuto likamkhuza munthu amatipempha (m’kakhalidwe kake konse), chogona, chokhala kapena choimilira. Koma tikamchotsera vuto lomwe lidampeza, amayenda ngati sanatipempheko pa vuto Iomwe Iidamkhudza. Momwemo ndimo zakometseredwa kwa opyola malire zomwe ankachita

    [13] “Ndipo ndithu tidaiononga mibadwo yambiri patsogolo panu pamene idachita zoipa. Komatu atumiki awo adawadzera ndi zisonyezo zoonekera, koma sadali oti nkukhulupirira. Umo ndi momwenso tidzawalipire anthu ochita zoipa

    [14] “Kenako takupangani inu (Asilamu) kukhala olowa m’malo mwawo pa dziko pambuyo pawo kuti tione mmene mungachitire (zabwino kapena zoipa)

    [15] “Ndipo Ayah Zathu zomveka bwino zikawerengedwa kwa iwo, akunena amene sayembekezera kukumana ndi Ife: “Bwera ndi Qur’an (yogwirizana ndi zofuna zathu) osati iyi, kapena uyisinthe (pang’ono).” Nena: “Nkosatheka kwa ine kuisintha mwachifuniro changa. Sinditsata koma zimene zikuvumbulutsidwa kwa ine. Ndithu ine ndikuopa chilango cha tsiku lalikulu ngati ndinyoza Mbuye wanga.”

    [16] “Nena: “Allah akadafuna, sindikadakuwerengerani Qur’aniyi ndiponso sakadakudziwitsani Qur’aniyo, ndidakhala pakati panu moyo wanga (zaka zambiri) isadavumbulutsidwe, (simudandimve ndikunena chilichonse cha utumiki). Kodi mulibe nzeru?”

    [17] “Ndani woipitsitsa woposa yemwe akumpekera Allah bodza, ndi yemwe akutsutsa Ayah Zake? Ndithudi, sangapambane wochita zoipa

    [18] “Ndipo iwo akupembedza milungu yina kusiya Allah, yomwe singathe kuwapatsa masautso (ngati atasiya kuipembedza) ndiponso siyingathe kuwapatsa chithandizo (ngati atalimbika kuipembedza) ndipo akunena: “Iwo (mafanowo) ndi aomboli athu kwa Allah.” Nena: “Kodi mukumuuza Allah zomwe sakudziwa kumwamba ndi pansi? Wapatukana Allah Ndipo watukuka kuzimene akum’phatikiza nazo.”

    [19] “Ndipo ndithudi anthu kalero (m’nthawi ya Adam) adali mpingo umodzi (opembedza Allah), koma adasiyana (pambuyo pake). Ndipo pakadapanda liwu lochokera kwa Mbuye wako, lomwe lidatsogola (lakuti adzawalanga tsiku la Qiyâma), ndithu kukadaweruzidwa pakati pawo m’zomwe adali kusiyana

    [20] “Ndipo akunena: “Kukadakhala kuti chinatsitsidwa kwa iye chizindikiro (chotsimikizira uneneri wake) chochokera kwa Mbuye wake (chomwe takhala tikuchipempha nthawi ndi nthawi).” Nena (kwa iwo): “Ndithu kudziwa zobisika nkwa Allah Yekha. Choncho dikirani (chiweruzo cha Allah) inenso pamodzi nanu ndine mmodzi wa odikira.”

    [21] “Ndipo tikawalawitsa anthu mtendere pambuyo pa masautso omwe adawakhudza, pompo iwo amayamba kuzichitira ndale Ayah Zathu. Nena: “Allah ngwachangu kwambiri poononga ndale (zawo).” Ndithu amithenga athu (angelo) akulemba ziwembu zanu (zonse) zimene mukuchita

    [22] “Iye ndi Yemwe amakuyendetsani pa ntunda ndi pa nyanja; kufikira pomwe mumakhala m’zombo; ndipo zimayenda nawo (zombozo) ndi mphepo yabwino, naisangalalira. (Mwadzidzidzi) namondwe nkuzidzera (zombozo) ndipo mafunde nkuwadzera mbali zonse natsimikiza kuti azingidwa (ndi chionongeko); amampempha Allah modzipereka kwa Iye mukupempha kwawo (uku akunena): “Ngati mutipulumutsa pa ichi, tidzakhala m’gulu la oyamika (nthawi zonse)!”

    [23] “Koma akawapulumutsa, pompo akuyamba kudzitukumula ndi kuononga pa dziko popanda chowayenereza (kutero). E inu anthu! Ndithu kuononga kwanu kukubweretserani masautso inu nokha. Ndipo chisangalalo (chake) cha moyo wa dziko lapansi (nchochepa). Kenako kobwerera kwanu ndi kwa Ife, ndipo tidzakuuzani zomwe munkachita

    [24] “Ndithu fanizo la moyo wadziko lapansi lili ngati madzi amvula, tawatsitsa kuchokera ku mitambo nkusakanikirana ndi zomera za m’nthaka zomwe anthu ndi nyama amadya; kufikira nthaka ikakwaniritsa kukongola kwake ndi kudzikometsa ndipo eni (nthaka) nkuganiza kuti iwo ali ndi mphamvu pa nthakayo (pokolola zomwe zili pamenepo). Mwadzidzidzi nkuzidzera lamulo Lathu (za pa nthakazo), usiku kapena masana, nkuzichita kukhala ngati zokololedwa ngati kuti sizidalipo dzulo (lake). Motere tikufotokoza Ayah kwa anthu olingalira

    [25] “Ndipo Allah akuitanira (anthu Ake) ku Nyumba yamtendere. Ndipo amamuongolera kunjira yolungama amene wamfuna (ngati ali wotheka kuongoka)

    [26] “Ndipo omwe achita zabwino, adzapata (malipiro) abwino ndi zoonjezera. Ndipo fumbi silikavindikira nkhope zawo. Ndiponso kunyozeka sikukawapeza. Iwowo ndiwo anthu a ku Munda wamtendere; mmenemo akakhala nthawi yaitali

    [27] “Ndipo amene akolola zoipa (kuchokera m’zochita zawo zoipa) mphoto ya choipa ndiyofanana ndi icho; ndipo kunyozeka kudzawapeza; sadzakhala ndi aliyense wotha kuwateteza ku chilango cha Allah. Nkhope zawo zidzakhala ngati zaphimbidwa ndi zidutswa za usiku wa m’dima, (zidzakhala zakuda kwambiri); awo ndiwo anthu a ku Moto. Iwo mmenemo adzakhala nthawi yaitali

    [28] “Ndipo (akumbutse za) tsiku lomwe tidzawasonkhanitsa onse. Kenako tidzawauza amene ankaphatikiza (Allah ndi mafano kuti): “Imani pompo inu pamodzi ndi aphatikizi anuwo.” Ndipo tidzawasiyanitsa pakati pawo; koma aphatikizi awowo adzati: “Simudali kutipembedza ife (koma mudali kupembedza zilakolako zanu).”

    [29] ““Allah akukwanira kukhala mboni pakati pathu ndi pakati panu. Ndithu ife sitidali kuzindikira za mapemphero anu. (Sitinkazindikira kuti inu mukutipembedza).”

    [30] “Kumeneko munthu aliyense adzadziwa zimene adatsogoza; ndipo adzabwezedwa kwa Allah, Mbuye wawo Woona ndipo zidzawasowa zimene adali kupeka

    [31] “Nena: “Kodi ndani akukupatsani (zopatsa) kuchokera kumwamba (povumbwitsa mvula), ndi pansi (pomeretsa mmera)? Nanga ndani amakupatsani kumva ndi kupenya? Nanga ndani amene akutulutsa chamoyo kuchokera m’chakufa, ndi kutulutsa chakufa kuchokera m’chamoyo? Nanga ndani akukonza zinthu zonse?” Anena: “Ndi Allah.” Choncho, nena: “Kodi bwanji simukumuopa?”

    [32] “Uyo ndi Allah, Mbuye wanu Woona; nanga pali chiyani pambuyo poleka choonadi, sikusokera basi? Kodi nanga mukutembenuzidwa chotani (kusiya choonadi)

    [33] “Momwemo liwu la Mbuye wako latsimikizika kwa amene adatuluka m’chilamulo cha Allah kuti iwo sadzakhulupirira

    [34] “Nena: “Kodi alipo mwa aphatikizi anu (mafano) amene angayambitse kulenga zolengedwa; kenako (zitafa) ndikuzibweza?” Nena: “Allah ndi Yemwe akuyambitsa zolengedwa kenaka ndi kuzibweza (pambuyo poonongeka). Nanga mukunamizidwa chotani (kusiya chikhulupiliro)?”

    [35] “Nena: “Kodi alipo mwa aphatikizi anu (mafano) woongolera kuchoonadi?” Nena: “Allah ndi Yemwe akuongolera ku choonadi. Kodi amene akutsogolera ku choonadi sindiye woyenera kwambiri kutsatidwa kapena (woyenera kutsatidwa ndi) yemwe sakutha kudziongola pokhapokha atawongoledwa ndi wina wake? Nanga mwatani kodi, kodi mukuweruza bwanji?”

    [36] “Ndipo ambiri a iwo satsatira (china) koma zoganizira basi, (osati chomwe afufuza ndikuchizindikira ndi nzeru zawo). Ndithu choganizira sichithandiza ngakhale pang’ono ku choonadi. Ndithu Allah akudziwa zonse zimene akuchita

    [37] “Ndipo sikotheka Qur’an iyi kukhala yopekedwa, yosachokera kwa Allah (monga momwe munenera). Koma (yachokera kwa Allah) kutsimikizira zomwe zidalipo patsogolo pake, ndi kulongosola za buku (lakale). Palibe chikaiko m’menemo (kuti) yachokera kwa Mbuye wa zolengedwa

    [38] “Kapena akunena kuti waipeka? Nena: “Tabwerani ndi sura (imodzi) yofanana ndi iyo, ndipo itanani amene mungathe (kuwaitana kuti akuthandizeni) kupatula Allah, ngati inu mukunena zoona (kuti Qur’aniyi waipeka Muhammad {s.a.w}).”

    [39] “Koma atsutsa zomwe sakuzizindikira (m’mene zilili) ngakhale tanthauzo lake (la kuona kwake kapena kunama kwake) lisanawafike. Momwemonso adatsutsa omwe adalipo patsogolo pawo. Choncho, taona momwe mathero a anthu ochimwa adalili

    [40] “Ndipo mwa iwo pali ena omwe akuikhulupirira (Qur’an), ndipo ena mwa iwo sakuikhulupirira. Ndipo Mbuye wako akuwadziwa bwino oononga

    [41] “Ndipo ngati apitiriza kukutsutsa, nena: “Ine ndili ndi ntchito yanga, inunso muli ndi ntchito yanu. Inu mwatalikirana nazo zimene ndikuchita, inenso ndatalikirana nazo zimene mukuchita!”

    [42] “Ndipo mwa iwo alipo ena amene akumvetsera kwa iwe, (koma osati ndi cholinga choti adziwe). Kodi iwe ungathe kuwamveretsa agonthi, chikhalirecho nzeru alibe

    [43] “Ndipo alipo ena mwa iwo amene akukutong’olera maso (kukuyang’ana monyoza). Kodi iwe ungathe kuwatsogolera akhungu, chikhalirecho sali openya

    [44] “Ndithu Allah sachitira anthu choipa chilichonse. Koma anthu akudzichitira okha zoipa. (Adapatsidwa nzeru, koma sazigwiritsa ntchito)

    [45] “Ndipo (akumbutse za) tsiku lomwe adzawasonkhanitsa (onse) ngati kuti sadakhale (pa dziko lapansi) koma ola limodzi la usana (atathedwa nzeru). Adzazindikirana pakati pawo; (koma aliyense sadzalabadira mnzake). Ndithu aonongeka amene adatsutsa za kukumana ndi Allah ndipo sadali oongoka

    [46] “Ndipo ngati tingakusonyeze (pompano pa dziko lapansi) zina mwa zomwe tikuwalonjeza ndikuwachenjeza nazo, kapena kukubweretsera imfa (usadazione zimenezo), kobwerera kwawo nkwa Ife basi. Kenako Allah ndi mboni pa zomwe akuchita

    [47] “Ndipo fuko lililonse lili ndi Mtumiki ndipo akazabwera Mtumiki wawo (tsiku la chiweruziro), kudzaweruzidwa pakati pawo mwa chilungamo ndipo sadzaponderezedwa

    [48] “Ndipo akunena (osakhulupirira): “Kodi lonjezo ili lidzachitika liti ngati mukunena zoona?”

    [49] “Nena: “Ndilibe mphamvu mwandekha pa (kudzichotsera) vuto ngakhale (kudzibweretsera) thandizo. (Nanga za zimenezo ndingadziweponji)? Koma chimene Allah wafuna (ndi chomwe chimachitika). M’badwo uli wonse uli ndi nthawi yake (yofera). Nthawi yawo (yofera) ikadza sangathe kuichedwetsa ola limodzi ngakhale kuifulumizitsa.”

    [50] “Nena: “Kodi mukuona bwanji, ngati chilango chakecho chitakudzerani usiku kapena usana (mungathe kuthawa)? Nanga bwanji ochimwa akuchifulumizitsa (kuti chidze mwachangu)?”

    [51] (““Kodi chikadza ndipamene mudzachikhulupirire?” Panthawiyo mudzauzidwa): “Kodi tsopano (ndi pamene mukukhulupirira), chikhalirecho mudali kuchifulumizitsa (kale)?”

    [52] “Kenako kudzanenedwa kwa amene adachita zoipa: “Lawani chilango chamuyaya! Kodi mungalipidwe zina osakhala zomwe mudazipata (kuchokera m’zochita zanu zoipa)?”

    [53] “Eti akukufunsa: “Kodi nzoona izo (zimene ukunena)?” Nena: “Inde! Ndikulumbira kwa Mbuye wanga, zimenezo ndi zoona. Ndipo inu simuli olepheretsa (Allah).”

    [54] “Ndipo kukadakhala kuti munthu aliyense amene adachita zoipa, nkukhala nazo zonse zam’dziko akadapereka zonse kuti adziombole nazo (pamene adzaona kuopsa kwa chilango cha tsikulo). Ndipo akadzachiona chilango, adzayesetsa kubisa madandaulo (awo; koma adzaonekera poyera). Ndipo kudzaweruzidwa mwachilungamo pakati pawo, ndipo iwo sadzaponderezedwa

    [55] “Tamverani! Ndithu zonse za kumwamba ndi pansi nza Allah. Tamverani! Ndithu lonjezo la Allah ndi loona, koma ambiri a iwo sadziwa

    [56] “Iye (Allah ndi amene) amapereka moyo ndi imfa. Ndipo kwa Iye (nonsenu) mudzabwezedwa

    [57] “E inu anthu! Ndithu ulaliki wakudzerani kuchokera kwa Mbuye wanu ndi machiritso a matenda omwe ali m’mitima mwanu, ndiponso nchiongoko ndi chifundo kwa okhulupirira

    [58] “Nena: “Chifukwa cha ubwino wa Allah ndi chifundo Chake (mwapeza zimenezi), choncho asangalalire zimenezi.” Izi ndizabwino kwambiri kuposa zimene akusonkhanitsa (m’zinthu za dziko lapansi)

    [59] “Nena: “Kodi mukuona bwanji, rizq lomwe Allah wakutsitsirani? Kenako inu lina mwa ilo mwalichita kukhala loletsedwa (la haramu), ndipo lina mwa ilo kukhala lololedwa (la halali).” Nena: “Kodi Allah adakulolezani (kuchita zimenezo), kapena mukumpekera Allah bodza?”

    [60] “Kodi ali ndi ganizo lotani amene akumpekera Allah bodza pa za tsiku la Qiyâma? Ndithu Allah Ndi mwini ubwino wochuluka kwa anthu. Koma ambiri a iwo sathokoza

    [61] “Ndipo siutanganidwa ndi ntchito iliyonse, ndiponso simuwerenga m’menemo (chinthu chilichonse) cha m’Qur’an ndipo simuchita ntchito ina iliyonse (inu anthu) koma Ife timakhala mboni pa inu pamene mukutanganidwa nayo. Ndipo sichibisika kwa Mbuye wako chinthu chilichonse ngakhale cholemera ngati nyelere, m’nthaka ngakhale kumwamba. Ndipo ngakhale chocheperapo zedi kuposa pamenepo kapena chokulirapo koma chili m’kuku (la Allah) lofotokoza chilichonse

    [62] “Tamverani! Ndithu okondedwa a Allah sadzakhala ndi mantha (pa tsiku la Qiyâma), ndipo sadzadandaula

    [63] “(Amenewo ndi) amene adakhulupirira ndi kumuopa (Allah)

    [64] “Iwo ali ndi zabwino pa moyo wa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro. Palibe kusintha pa mawu a Allah. Uku ndiko kupambana kwakukulu

    [65] “Ndipo (iwe, Mtumiki) zisakudandaulitse zonena zawo (zomwe akukunenera monyoza). Ndithu ulemelero ndi mphamvu zonse nza Allah. Iye Ngwakumva, Ngodziwa

    [66] “Tamverani! Ndithu (zonse) za kumwamba ndi za pansi, nza Allah. Ndipo amene akupembedza zina kusiya Allah, satsatira aphatikizi (a Allah). Akungotsatira zoganizira, ndipo iwo sanena china koma bodza basi

    [67] “Iye (Allah) ndi Yemwe adakupangirani usiku kuti muzipumamo, ndi (adakupangirani) usana kukhala wowala (kuti mupenye). Ndithu m’zimene muli zisonyezo (zosonyeza chifundo cha Allah pa zolengedwa Zake) kwa anthu akumva

    [68] “Akunena: “Allah wadzipangira mwana.” Wapatukana ndi zimenezo! Iye Ngokwanira, (salakalaka mwana ngakhale mthangati aliyense). NdiZake (zonse) za kumwamba ndi za pansi. Inu mulibe umboni pa zimenezi. Kodi mukumnenera Allah zomwe simukuzidziwa

    [69] “Nena: “Ndithu amene akumpekera Allah bodza, sadzapambana.”

    [70] “Ndichisangalalo chochepa basi m’dziko lapansi. Kenako kwa Ife ndiwo mabwelero awo. Kenako tidzawalawitsa chilango chaukali chifukwa cha kusakhulupirira kwawo

    [71] “Ndipo awerengere (molakatula) nkhani za Nuh pamene adanena kwa anthu ake: “E inu anthu anga! Ngati kukhala kwanga pamodzi ndi inu ndi kukumbutsa kwanga Ayah za Allah kukukukulirani, ine ndatsamira kwa Allah (sindisiya ntchito yangayi). Choncho sonkhanitsani zinthu zanu pamodzi ndi milungu yanuyo; (sonkhanani kuti mundichitire choipa, ine sindilabadira chilichonse). Ndipo chinthu chanucho chisabisike kwa inu, (chitani moonekera. Ine sinditekeseka ndi chilichonse). Kenako chitani pa ine (chimene mufuna kuchita) ndipo musandipatse danga

    [72] “Ngati mutembenuka ndikunyoza, (ndikufuna kwanu). Ine sindinakupempheni malipiro. Malipiro anga kulibe kulikonse (kumene ndingalandire) koma kwa Allah, ndipo ndalamulidwa kuti ndikhale mmodzi mwa Asilamu (ogonjera Iye).”

    [73] “Koma adamutsutsa. Choncho tidampulumutsa pamodzi ndi amene adali naye m’chombo. Ndipo tidawasankha iwo kukhala otsala (pa dziko anzawo ataonongeka). Ndipo tidawamiza amene adatsutsa Ayah Zathu. Choncho taona momwe mapeto a ochenjezedwa adalili

    [74] “Pambuyo pake tidawatumiza atumiki (ambiri) kwa anthu awo. Adawadzera ndi zisonyezo zoonekera poyera koma sadali okhulupirira zimene ena adazitsutsa kale, (adatsatira njira zomwezo za anzawo). Umo ndi momwe tikudindira zidindo m’mitima ya anthu opyola malire

    [75] “Kenako pambuyo pawo tidamtuma Mûsa ndi Haarun pamodzi ndi zizindikiro zathu kwa Farawo ndi nduna zake, koma adadzikweza. Tero adali anthu ochita zoipa

    [76] “Ndipo pamene choonadi chidawadzera kuchokera kwa Ife, adanena: “Ndithu awa ndimatsenga oonekera.”

    [77] “Mûsa adati: “Mukutero pa choonadi pamene chakudzerani? Kodi matsenga ali chonchi? Ndipo amatsenga sangapambane (ngakhale zitatani).”

    [78] “(Iwo) adati: “Kodi watidzera kuti utichotse ku zimene tidawapeza nazo makolo athu kuti ukulu ukhale wa inu awiri m’dzikoli? Koma ife sitingakukhulupirireni awirinu.”

    [79] “Ndipo Farawo adati: “Ndibweretsereni wamatsenga aliyense wodziwa kwambiri (zamatsenga).”

    [80] “Ndipo pamene amatsenga adadza, Mûsa adati kwa iwo: “Ponyani zomwe mufuna kuponya (kuti musonyeze ukatswiri wanu kwa anthu).”

    [81] “Pamene adaponya, Mûsa adati: “Zomwe mwabweretsa ndi matsenga. Allah awaononga pompano. Ndithu Allah sakonza ntchito za oononga.”

    [82] ““Ndipo Allah achilimbikitsa choonadi ndi mau Ake, ngakhale oipa anyansidwe nazo.”

    [83] “Sadamkhulupirire Mûsa kupatula achinyamata a mwa anthu ake, chifukwa choopa Farawo ndi nduna zake kuti angawazunze. Ndithu Farawo adali wodzikuza pa dziko, ndithudi, adali m’modzi mwa opyola malire

    [84] “Ndipo Mûsa adati: “E inu anthu anga! Ngati inu mwakhulupirira Allah, choncho tsamirani kwa Iye ngati mulidi Asilamu (owona)

    [85] “Choncho (iwo) adati: “Tayadzamira kwa Allah. E Mbuye wathu! Musatichite kukhala mayetsero kwa anthu oipa.”

    [86] ““Ndipo tipulumutseni mwa chifundo Chanu ku anthu osakhulupirira.”

    [87] “Ndipo tidavumbulutsa kwa Mûsa ndi m’bale wake mawu Athu (oti): “Apangireni nyumba anthu anu mu Eguputo ndipo nyumba zanu zichiteni kukhala misikiti (pakuti simungathe kukhala ndi misikiti yoonekera), ndipo pempherani Swala. Ndipo auze nkhani yabwino okhulupirira (kuti Allah awapatsa zabwino pa moyo wa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro).”

    [88] “Ndipo Mûsa adati: “Mbuye wathu! Inu mwampatsa Farawo ndi nduna zake zodzikometsera, ndi chuma chambirimbiri pa moyo wa pa dziko. Mbuye wathu, (iwo akugwiritsa ntchito zimenezi) kuti asokeretse anthu pa njira Yanu. Mbuye wathu, wonongani chuma chawo ndipo iumitseni mitima yawo popeza sakhulupirira kufikira ataona chilango chowawa.”

    [89] “(Allah) adati: “Pempho lanu lavomerezedwa! Choncho lungamani mwaubwino, ndipo musatsate njira za omwe sadziwa.”

    [90] “Ndipo tidawaolotsa pa nyanja ana a Israyeli. Ndipo Farawo ndi asilikali ake ankhondo adawatsata moipitsa ndi mwamtopola, kufikira pamene kumira kudampeza; (iye) adati: “Ndakhulupirira kuti palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Yemwe ana a Israyeli amkhulupirira. Ndipo ine ndine mmodzi mwa Asilamu (omugonjera monga iwo akumgonjera).”

    [91] “(Angelo adamuuza kuti:) “Tsopano (ndipamene ukukhulupirira), pomwe kale udanyoza ndikukhala mmodzi wa oononga!”

    [92] ““Choncho lero tikupulumutsa (polisunga) thupi lako, kuti ukhale chisonyezo kwa amene akudza m’mbuyo mwako (kuti adziwe kuti sudali mulungu). Koma ndithu anthu ambiri salabadira zisonyezo Zathu.”

    [93] “Ndipo ndithu (pambuyo pake) tidawakonzera mokhala mwabwino ana a Israyeli, ndikuwapatsa zabwino. Sadasiyane kufikira pamene kuzindikira kudawadzera. Ndithu Mbuye wako adzaweruza pakati pawo tsiku la Qiyâma pa zimene adali kutsutsana

    [94] “Ngati uli ndi chipeneko pa zimene takuvumbulutsira, afunse amene akuwerenga mabuku akale (Ayuda ndi Akhrisitu amene alowa m’Chisilamu). Ndithu choonadi chakufika kuchokera kwa Mbuye wako. Choncho usakhale mwa amene akukaikira

    [95] “Ndiponso usakhale mwa omwe akutsutsa zizindikiro za Allah, kuopa kuti ungadzakhale m’gulu la otaika

    [96] “Ndithu aja amene liwu la Mbuye wako latsimikizika pa iwo, sakhulupirira

    [97] “Ndipo ngakhale kuti chisonyezo chamtundu uliwonse chiwadzere (sangakhulupirirebe), mpaka aone chilango chopweteka

    [98] “Kodi udalipo mudzi (ndi umodzi womwe pakati pa midzi mwa yomwe tidaiwononga), umene udalapa ndi kukhulupirira (pambuyo poona chilango kotero kuti) chikhulupiliro chake nkuuthandiza pa nthawi imeneyo, osati kupatula anthu a Yunus okha? Pamene adakhulupirira, tidawachotsera chilango choyalutsa m’moyo wa padziko lapansi, ndipo tidawasangalatsa kufikira nthawi yawo (yofera)

    [99] “Ndipo Mbuye wako akadafuna (kuwakakamiza anthu mwamphamvu kuti akhulupirire), onse ali m’dziko lapansi akadakhulupirira (sipakadatsala ndi mmodzi yemwe. Koma Allah safuna kukakamiza anthu mwamphamvu). Nanga kodi iwe uwakakamiza anthu kuti akhale okhulupirira

    [100] “Ndipo palibe munthu angakhulupirire popanda chilolezo cha Allah. Iye amaachitira ukali amene alibe nzeru (amene sagwiritsa ntchito nzeru zawo)

    [101] “Nena: “Yang’anani nchiyani chikupezeka kumwamba ndi pansi!” Ndipo zisonyezo zonsezi ndi machenjezo onsewa sangawakwanire (ndi kuwapindulira kanthu) anthu osakhulupirira

    [102] “Kodi chiliponso chimene akudikira posakhala (kuwadzera) monga masiku (azilango zomwe zidawapeza) amene adapita kale (iwo asadafike)? Nena: “Dikirani nanenso ndili pamodzi nanu mwa odikira.”

    [103] “Kenako tidzawapulumutsa atumiki Athu ndi amene adakhulupirira. Chotere nkoyenera kwa Ife kuwapulumutsa okhulupirira

    [104] “Nena: “E inu anthu! Ngati inu muli ndi chipeneko pa chipembedzo changa, (dziwani kuti) sindingapembedze zimene mukuzipembedza kusiya Allah; koma ine ndipembedza Allah (Mmodzi yekha) Yemwe amakupatsani imfa (ndi moyo). Ndipo ndalamulidwa kukhala mmodzi wa okhulupirira.”

    [105] ““Ndiponso (ndauzidwa kuti): ‘Lungamitsa nkhope yako kuchipembedzo momuyeretsera Allah mapemphero Ake, ndipo usakhale mmodzi mwa ophatikiza (Allah ndi zinthu zina).’

    [106] “‘Ndipo (kuti), usapembedze chimene sichingakupindulitsire zabwino, kapena kukubweretsera masautso, kusiya Allah. Ngati utero ndiye kuti iwe ndi mmodzi wa oipa.”

    [107] “Ndipo ngati Allah atakukhudza ndi masautso, palibe aliyense owachotsa kupatula Iye. Ngatinso atakufunira zabwino, palibe amene angaubweze ubwino Wake. (Iye) amadza ndi ubwinowo kwa amene wamfuna mwa akapolo Ake. Ndipo Iye Ngokhululuka Ngwachisoni zedi

    [108] “Nena: “E inu anthu! Choonadi chakudzerani kuchokera kwa Mbuye wanu. Choncho amene waongoka, (zabwino zake) zili pa iye mwini. Ndipo amene wasokera, ndithu zotsatira za kusokera zili pa iye mwini. Ndipo ine sindili muyang’aniri pa inu, (udindo wanga ndi kuchenjeza basi).”

    [109] “Ndipo (andiuza kuti): “Tsatira zimene zikuvumbulutsidwa kwa iwe ndipo pirira kufikira Allah adzaweruze. Iye Ngoweruza bwino kuposa aweruzi onse.”

    Hudu

    Surah 11

    [1] “Alif-Lam-Ra. Ili ndi buku lomwe ndime zake zakonzedwa bwino ndipo zafotokozedwa mwatsatanetsatane kuchokera kwa Allah Mwini nzeru zakuya Wodziwa chilichonse

    [2] “(Wachita zimenezi) kuti musampembedze wina wake koma Allah yekha. Ndithudi ine kwa inu ndimchenjezi wochokera kwa Iye ndiponso wokuuzani nkhani zabwino

    [3] “Ndikuti mupemphe chikhululuko kwa Mbuye wanu ndipo mulape kwa Iye. Akupatsani chisangalalo chabwino mpakana m’nthawi yoikidwa. Ndipo adzampatsa (tsiku lachimaliziro) aliyense wochita zabwino ubwino wake. Koma, ngati mupotoka ine kwanga nkukuoperani za chilango cha tsiku lalikulu

    [4] “Kobwerera kwanu nkwa Allah basi. Iye ali ndi mphamvu pa chilichonse

    [5] “Tamverani! Iwo akubisa zimene zili m’mitima yawo kuti amubise Iye (Allah). Mverani! Ndithudi pamene akuzifunda nsalu zawo Iye akudziwa zimene akuzibisa ndi zimene akuzionetsa. Ndithudi Iye ndiwodziwa za mzifuwa

    [6] “۞ Ndipo palibe nyama iliyonse panthaka koma rizq lake lili kwa Allah; ndipo (Iye) akudziwa mbuto yake yamuyaya ndi mbuto yake yakungodutsapo (yomwe ndi pano padziko lapansi). Zonse zili m’buku lofotokoza chilichonse

    [7] “Ndipo Iye ndi Yemwe adalenga thambo ndi nthaka m’masiku asanu ndi limodzi, ndipo Arsh Yake (Mpando Wake wachifumu) idali pa madzi. (Adakulengani) kuti akuyeseni mayeso, ndani mwa inu ali wochita zabwino. Koma ukanena (kwa iwo kuti): “Inu mudzaukitsidwa pambuyo pa imfa,” amene sadakhulupirire akuti: “Izi sikanthu koma ndi matsenga oonekera.”

    [8] “Ndipo ngati titawachedwetsera chilango mpaka m’nthawi yodziwika (ndi kukhazikitsidwa ndi Ife), akunena (mwamwano): “Nchiyani chikumanga chilangocho (kuti chidze)? “Tamverani! Tsiku lomwe chidzawadzera, sichidzachotsedwa kwa iwo ndipo zomwe adali kuzichita mwachibwana zidzawazinga

    [9] “Ndipo munthu tikamulawitsa mtendere wochokera kwa Ife, kenako nkuuchotsa kwa iye, ndithu amakhala wotaya mtima kwambiri ndikukhala wosathokoza

    [10] “Koma ngati titamulawitsa mtendere pambuyo pa masautso omwe adamkhudza, amati: “Masautso andichoka,”(ndipo sakhala wotanganidwa ndi ntchito zabwino zosonyeza kuyamika Allah), ndithudi iye amakhala wosangalala, wodzitukumula

    [11] “Koma amene apirira ndi kumachita ntchito zabwino, iwowo ndiwo adzapeza chikhululuko ndi malipiro aakulu (kwa Allah)

    [12] “Mwina usiya zina mwa zomwe zikuvumbulutsidwa kwa iwe ndikubanika nazo mchifuwa mwako chifukwa chakuti akunena: “Bwanji sizidatsitsidwe kwa iye nkhokwe za chuma kapena bwanji mngelo osadza pamodzi ndi iye?” Koma ndithu iwe ndiwe mchenjezi basi ndipo Allah ndiye muyang’aniri wa chinthu chilichonse

    [13] “Kapena akunena kuti: “Waipeka Qur’an?” Nena: “Tabweretsani sura khumi zopekedwa zomwe zingafanane ndi iyi (Qur’an) ndipo aitaneni amene mungathe (kuwaitana) kupatula Allah. (Adze akuthandizeni kulemba bukulo) ngati mukunena zoona!”

    [14] ““Ngati sakuyankhani, choncho, dziwani kuti yavumbulutsidwa (Qur’aniyo) m’kudziwa kwa Allah, ndikuti kulibe mulungu wina koma Iye. Nanga kodi inu simugonjera (Iye)?”

    [15] “Amene akufuna moyo wa dziko lapansi ndi zokometsera zake, tiwapatsa pompo pa dziko lapansi (malipiro a) zochita zawo mokwanira, ndipo iwo m’menemo sachepetseredwa chilichonse

    [16] “Iwo ndi omwe sadzakhala ndi kanthu tsiku lachimaliziro koma Moto basi. Ndipo zimene adachita m’menemo zidzaonongeka, ndiponso nzopanda phindu zimene ankachita

    [17] “Nanga kodi munthu yemwe ali ndi chisonyezo choonekera chochokera kwa Mbuye wake (kotero kuti m’moyo mwake akuyenda molungama; yemwe ndi mneneri Muhammad {s.a.w}), ndipo Mboni ili naye pamodzi ikumtsata yochokera kwa Iye (Mbuye wake yomwe ndi Qur’an kapena Gaburiel), ndipo patsogolo pake padali buku la Mûsa lomwe lidali chitsanzo chabwino ndi mtendere, (wotereyu angafanane ndi yemwe ali mum’dima wa umbuli yemwenso sadziwa cholinga chakulengedwa kwake?) Awa (amene aongoka) akulikhulupirira (buku ili la Qur’an), ndipo amene ati asalikhulupirire m’magulu (a adani), Moto ndiwo malo awo alonjezo. Choncho, usakhale ndi chipeneko pa ichi; ndithudi ichi ndi choona chochokera kwa Mbuye Wako koma anthu ambiri sakhulupirira

    [18] “Ndipo palibe oipitsitsa kuposa yemwe wapeka bodza pakumnamizira Allah (kuti ali ndi mwana ndi athandizi). Iwo adzabweretsedwa kwa Mbuye wawo (tsiku la Qiyâma) ndipo mboni (zomwe ndi angelo) zidzanena: “Awa ndi omwe adapekera Mbuye wawo bodza. Mverani! Tembelero la Allah lili pa ochita zoipa.”

    [19] “Omwe akutsekereza anthu kutsata njira ya Allah ndi kufuna kuikhotetsa (njirayo). Ndiponso iwo sakhulupirira za tsiku lachimaliziro

    [20] “Iwowa sangathe kumulepheretsa (Allah) m’dziko, ndiponso alibe atetezi pambuyo pa Allah. Chilango chawo chidzaonjezeredwa (chifukwa cha zoipa zawo). Sadali kutha kumva ngakhale kuona (chifukwa cha mkwiyo umene udali m’mitima mwawo wokwiira choonadi)

    [21] “Awa ndi omwe adziononga okha ndipo zomwe adali kuzipeka zidzawataika

    [22] “Zoonadi, iwo ndiotaika kwakukulu pa tsiku lachimaliziro

    [23] “Ndithu amene akhulupirira ndi kumachita zabwino ndi kumadzichepetsa kwa Mbuye wawo, iwowo ndiwo anthu a ku Munda wamtendere. M’menemo adzakhala nthawi yaitali

    [24] “Fanizo la magulu awiriwa (okhulupirira ndi osakhulupirira), lili ngati (munthu) wakhungu ndi gonthi, ndi (munthu) wopenya ndi wakumva. Kodi awiriwa angakhale ofanana (pa chikhalidwe chawo)? Bwanji simukuganiza

    [25] “Ndipo ndithu Ife tidamtuma Nuh (monga Mtumiki) kwa anthu ake (kuti akawauze): “Ine kwa inu ndine mchenjezi owonekera poyera.”

    [26] ““Ndikuti musapembedze aliyense koma Allah basi. Ndithu ine ndikukuoperani chilango cha tsiku lopweteka.”

    [27] “Ndipo pompo akuluakulu mwa omwe sadakhulupirire mwa anthu ake, adati: “Sitikukuona koma ndiwe munthu monga ife, ndipo sitikukuona koma kuti akutsata anthu a pansi pathu ofooka pa nzeru (omwe sadalingalire mozama za iwe). Ndipo sitikukuonani kuti muli ndi ulemelero ndi ubwino wochuluka kuposa ife. Koma tikukuganizirani kuti ndinu onama.”

    [28] “(Iye) adati: “E inu anthu anga! Kodi muona bwanji ngati ndili ndi chisonyezo chowonekera chochokera kwa Mbuye wanga ndipo wandipatsa chifundo chochokera kwa Iye (monga uneneri), ndipo chabisika kwa inu, kodi tingakukakamizeni kuvomereza pomwe simukuchifuna?”

    [29] ““Ndipo E inu anthu anga! Ine sindikukupemphani chuma pa uthengawu. Palibe malipiro anga, koma ali kwa Allah basi. Ndipo ine sindingathamangitse amene akhulupirira (monga momwe mudandipemphera kuti ndiwathamangitse anthu ofooka kuti inu mulowe m’malo mwawo), ndithu iwo adzakumana ndi Mbuye wawo, ndipo ine ndikukuonani monga anthu osazindikira (mbuli).”

    [30] ““Ndipo E inu anthu anga! Ndani angandithandize kwa Allah ngati nditawathamangitsa? Kodi simuganiza?”

    [31] ““Ndipo ine sindikukuuzani kuti ndili ndi nkhokwe za chuma cha Allah kapena kuti ine ndikudziwa zinthu zamseli, ndiponso sindikunena kuti ndine m’ngelo. Ndiponso sindikunena kwa omwe maso anu akuwachepetsa kuti Allah sadzawapatsa chabwino. Allah akudziwa zam’mitima mwawo. (Ngati nditatero) ndiye kuti ine pamenepo ndili m’gulu la oipa.”

    [32] “(Iwo) adati: “E iwe Nuh! Watsutsana nafe, ndipo wachulukitsa kutsutsana nafe. Choncho bweretsa kwa ife chimene ukutilonjezacho, ngati ulidi mwa onena zoona

    [33] “Adati: “Ndithu Allah achibweretsa kwa inu ngati afuna, ndipo inu simungathe kumulepheretsa (chimene wafuna).”

    [34] ““Ndipo kulangiza kwanga sikungakuthandizeni ngati ntafuna kukulangizani, ngati Allah akufuna kukulekelerani kusokera. Iye ndiye Mbuye wanu. Ndipo kwa Iye mudzabwezedwa.”

    [35] “Kapena akunena (osakhulupirira a m’Makka kuti: “Muhammad) waipeka (Qur’an mwa iye yekha)?” Nena: “ngati ndayipeka ndiye kuti machimo ake (akupekawo) ali pa ine. Ndipo ine ndili kutali ndi zoipa zimene mukuchita.”

    [36] “Ndipo tidamuululira Nuh kuti: “(Tsopano) sakhulupirira aliyense mwa anthu ako kupatula okhawo akhulupirira kale. Choncho, usadandaule pa zimene adali kuchita.”

    [37] ““Ndipo khoma chombo moyang’aniridwa ndi Ife, ndi ulangizi wathu (satha kukuchitira choipa), ndipo usandiyankhulitse za iwo amene achita zoipa (kuti ndiwakhululukire). Ndithudi, iwo amizidwa.”

    [38] “Ndipo adayamba kukhoma chombo. Nthawi iliyonse akamdutsa akuluakulu a mwa anthu ake, adali kumchitira chipongwe. Naye ankanena (kuti): “Ngati inu Mukutichitira chipongwe, nafenso tidzakuchitirani chipongwe monga momwe mukutichitira chipongwe.”

    [39] ““Posachedwa mudziwa kuti ndani chimdzere chilango chomuyalutsa ndi kumtsikira chilango chopitilira.”

    [40] “Kufikira pamene lidadza lamulo lathu, madzi naphulika mu uvuni, (chomwe chidali chisonyezo cha Nuh chosonyeza kudza kwa lamulo loona kwa anthu ake) tidamuuza (kuti): “Kweza m’menemo (m’chombo) mtundu uliwonse (wa nyama), ziwiriziwiri, (yaikazi ndi yaimuna), ndi anthu a kubanja lako kupatula omwe chiweruzo (cha Allah) chatsimikizidwa pa iwo (kuti aonongeke), ndipo (atengenso onse) amene akhulupirira.” Komatu ndi ochepa kwambiri amene adakhulupirira pamodzi ndi iye

    [41] “Ndipo (Nuh) adati: “Kwerani m’menemo mwadzina la Allah mkuyenda kwake ndi mkukocheza kwake. Ndithu Mbuye wanga Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni zedi.”

    [42] “Ndipo (chombocho) chidali kuyenda nawo m’mafunde onga mapiri, ndipo Nuh adaitana mwana wake yemwe adali patali (atakana kulowa m’chombo): “Mwana wanga! Kwera pamodzi ndi ife usakhale pamodzi ndi osakhulupirira.”

    [43] “(Iye) adati: “Ndithawira kuphiri likanditeteza ku madziwa.” Nuh adati: “Lero palibe otetezedwa ku lamulo la Allah kupatula yemwe Allah wamchitira chifundo.” Pompo mafunde adatchinga pakati pawo. Choncho adali mgulu la omizidwa

    [44] “Ndipo (pambuyo poonongeka onse ndi zonse zomwe Allah adafuna kuti zionongeke), kudanenedwa: “E iwe nthaka! Meza madzi ako. Ndipo iwe thambo! Amange (madzi ako amvula).” Choncho, madzi adaphwa ndipo lamulo lidakwaniritsidwa (loononga anthu oipa). Ndipo (chombo) chidaima pamwamba pa (phiri lotchedwa) Judi, ndipo kudanenedwa: “Aonongeke onse ochita zoipa.”

    [45] “Ndipo Nuh adafuulira Mbuye wake nati. “E Mbuye wanga! Ndithu mwana wanga ali mgulu la akubanja langa (akuonongedwa). Ndipo ndithu lonjezo lanu ndiloona, ndipo Inu Ndinu Woweruza mwachoonadi kuposa aweruzi onse.”

    [46] “(Allah) adati: “E iwe Nuh! Ndithu iyeyo si (mwana) wa m’banja lako. Iye zochita zake sizili zabwino. Choncho usandipemphe zomwe siukuzidziwa, Ine ndikukulangiza kuti usakhale m’gulu la osazindikira (mbuli).”

    [47] “(Nuh) adati: “E Mbuye wanga! Ndikudziteteza mwa Inu kuti ndisakupempheninso zomwe sindikuzidziwa. Ngati simundikhululukira ndi kundichitira chifundo, ndikhala mwa anthu otaika.”

    [48] “Kudanenedwa: “E iwe Nuh! Tsika (pa nthaka youma) mwamtendere wochokera kwa Ife, ndipo madalitso ambiri akhale pa iwe ndi pa anthu omwe ali nawe; ndipo kudzakhala mibadwo ina (yoipa pambuyo pako) yomwe tidzaisangalatsa, ndipo kenako chidzaikhudza chilango chowawa chochokera kwa Ife.”

    [49] “Izi ndi zina mwa nkhani zobisika zomwe tikukuululira iwe. Siudali kuzidziwa, iwe ngakhale anthu ako, patsogolo pa ichi, (Qur’an isadadze). Choncho, pirira. Ndithu mathero abwino adzakhala kwa anthu oopa Allah

    [50] “Ndipo anthu (amtundu) wa Âdi, tidawatumizira m’bale wawo Hûd. Adati: “E inu anthu anga! Pembedzani Allah! (Siyani kupembedza mafano). Mulibe mulungu wina koma Iye. Inu simuli kanthu koma ndinu opeka bodza (m’kunena kwanu kwakuti mafano ndi anzake a Allah).”

    [51] ““E inu anthu anga! Sindikukupemphani malipiro pa ichi (uthengawu). Palibe Malipiro anga koma ali kwaYemwe adandilenga. Kodi mulibe nzeru?”

    [52] ““Ndipo E inu anthu anga! Pemphani chikhululuko kwa Mbuye wanu, (pa machimo omwe mwakhala mukuchita), kenako lapani kwa Iye. Akutumizirani mitambo yodzetsa mvula yambiri, ndipo akuonjezerani mphamvu pa mphamvu zanu (zomwe muli nazo). Choncho, musatembenuke kukhala oipa.”

    [53] “(Iwo) adati: “E iwe Hûd! Sudatibweretsere chisonyezo chooneka (chosonyeza kuti ndiwe Mneneri), ndipo ife sitisiya (kupembedza) milungu yathu chifukwa cha zoyankhula zakozo. Ndipo ife sitikukhulupirira.”

    [54] ““Sitinena kanthu, koma kuti (mwina) milungu yathu ina yakulodza misala.” (Iye) adati: “Ndithu ine ndikupereka umboni kwa Allah ndipo inunso perekani umboni kuti ine ndili kutali ndi zimene mukumphatikiza nazo (Allah pomazipembedza).”

    [55] ““Kusiya Iye; (milungu yanuyo sindikuiopa ngati ili ndi mphamvu pamodzi ndi inu), tero ndichitireni chiwembu nonsenu, ndipo kenako musandiyembekezere (musandipatse nthawi).”

    [56] ““Ndithu ine ndatsamira kwa Allah, Mbuye wanga yemwenso ali Mbuye wanu. Palibe chinyama chilichonse koma Allah wachigwira tsumba lake (ndikuchiyendetsa mmene akufunira). Ndithudi, Mbuye wanga Ngwachilungamo.”

    [57] ““Ngati munyoza (kulandira chimene ndakuuzani palibe vuto kwa ine); ndithu ndafikitsa kwa inu chimene ndatumidwa. Ndipo Mbuye wanga (awaononga osakhulupirira, ndipo) abweretsa anthu ena m’malo mwanu, ndipo inu simungamusautse konse. Ndithu Mbuye wanga ndi Msungi wa chilichonse.”

    [58] “Ndipo pamene lamulo lathu lidafika (lakuwaononga), tidampulumutsa Hûd ndi amene adakhulupirira pamodzi naye, mwachifundo Chathu, ndipo tidawapulumutsa kuchilango chokhwima

    [59] “Ndipo awa ndi Âdi. Adatsutsa Ayah (ndime) za Mbuye wawo ndi kunyoza atumiki Ake; ndipo adatsata lamulo la yense wodzikweza, wamakani

    [60] “Ndipo adatsatizidwa ndi tembelero pa moyo wapano padziko lapansi ndi tsiku la Qiyâma (tsiku la chiweruziro). Dziwani! Ndithu Âdi adakana Mbuye wawo. Ha! Adaonongeka Âdi, anthu a Hûd

    [61] “Ndipo kwa anthu (a mtundu) wa Samud, (tidatuma) m’bale wawo Swaleh. Adati: “E inu anthu anga! Lambirani Allah. Mulibe mulungu wina koma Iye Yekha. Iye adakuumbani ndi nthaka ndi kukukhazikani m’menemo. Ndipo mpempheni chikhululuko (pa zolakwa zanu), kenako tembenukirani kwa Iye. Ndithu Mbuye wanga ali pafupi (ndi akapolo Ake). Ndipo Ngovomera mapempho (aopempha).”

    [62] “Iwo adati: “E iwe Swaleh! Ndithudi, udali woyembekezeka (kukhala mfumu kwa ife) patsogolo pa izi (usanabwere ndi izi). Ha! Kodi ukutiletsa kulambira zomwe makolo athu adali kulambira? Ndithu ife tili m’chikaiko chokaikira zomwe ukutiitanirazo.”

    [63] “(Iye) adati: “E inu anthu anga! Mukuona bwanji ngati ndili ndi chisonyezo choonekera chochokera kwa Mbuye wanga (chosonyeza kuona kwa zimenezi), nandipatsanso chifundo chochokera kwa Iye. Nanga ndi yani angandipulumutse ku chilango cha Allah ngati nditamunyoza? Choncho, simungandionjezere china chake koma kutaika basi.”

    [64] ““Ndipo E inu anthu anga! Iyi ngamira ya Allah ndi chisonyezo kwa inu. Ilekeni izidya panthaka ya Allah, ndipo musaikhudze ndi choipa kuopa kuti chilango chomwe chili pafupi chingakuonongeni.”

    [65] “Koma adaipha. Choncho (Swaleh) adati: “Sangalalani m’midzi yanuyi pamasiku atatu. (Kenako mulangidwa). Limenelo ndi lonjezo osati labodza.”

    [66] “Choncho pamene lamulo Lathu lidadza (lakuononga midziyo), tidampulumutsa Swalih ndi anthu amene adakhulupirira naye, kukuyaluka kwa tsiku limenelo, mwa chifundo Chathu. Ndithu Mbuye wako ndi Mwini mphamvu, Ngopambana

    [67] “Ndipo amene adadzichitira okha zoipa phokoso lalikulu lidawaononga, tero kudawachera m’nyumba zawo ali lambilambi (atafa)

    [68] “Ngati kuti iwo mudalibemo m’menemo. Mverani! Ndithu Asamudu adamkana Mbuye wawo. Choncho Asamudu adaonongeka

    [69] “Ndipo ndithu atumiki athu (angelo) adadza kwa Ibrahim ndi uthenga wabwino. (Iwo) adati: “Mtendere!” (Iye) adayankha: “Mtendere (ukhale pa inu!)” Ndipo (Ibrahim) sadakhalitse (adafulumira) kudza nayo nyama yootcha ya thole (mwana wa ng’ombe)

    [70] “Koma pamene adaona kuti manja awo sakuwatambasula kuchakudya adawadodoma, nadzadzidwa nawo mantha. (Iwo) Adati: “Usaope; ndithu ife tatumidwa kwa anthu a Luti (kuti tikawaononge ndiponso kukupatsa nkhani yabwino).”

    [71] “Ndipo (m’menemo nkuti) mkazi wake (wa Ibrahim) ali chiimire, ndipo adaseka. Kenaka tidamuuza uthenga wabwino (wakubadwa kwa) Ishaq ndipo pambuyo pa Ishaq, Ya’qub

    [72] “(Iye) adati: “Kalanga ine! Ndibereka pomwe ine ndili nkhalamba, ndiponso uyu mwamuna wanga ndi nkhalamba? Ndithudi, ichi ndi chinthu chododometsa.”

    [73] “(Angelowo) adati: “Ukudabwa ndi lamulo la Allah? Chisomo cha Allah ndi madalitso ake zili pa inu, E inu eni nyumba iyi! Iye Ngoyamikidwa, Mwini ulemelero!”

    [74] “Ndipo pamene Ibrahim mantha adamchokera ndikumufikira uthenga wabwino, adayamba kutidandaulira za anthu a Luti (kuti tisawaononge)

    [75] “Ndithu Ibrahim adali wodekha, wodandaulira Allah komanso wobwerera kwa Iye mwachangu (polapa)

    [76] “(Tidamuuza): “E iwe Ibrahim! Siya ichi. Lamulo la Mbuye wako, ndithu ladza. Ndipo ndithu iwo chiwadzera chilango chosabwezedwa.”

    [77] “Ndipo atumiki athu pamene adafika kwa Luti, iye anadandaula za iwo ndi kubanika nao mu mtima (chifukwa chosowa njira yowatetezera kwa anthu oipa pomwe iye sadadziwe kuti alendowo ndi angelo), nati: “Lino ndi tsiku lovuta.”

    [78] “Ndipo anthu ake adadza akuthamangira kwa iye (ku nyumba kwake kuti adzachite zauve ndi alendowo). Ndipo kalenso ankachita zoipa zokhazokhazi, (Luti) adati: “E anthu anga! Nawa asungwana anga; ngoyenera kwa inu (kuwakwatira, osati amuna anzanu) choncho, opani Allah, ndipo musandiyalutse pamaso pa alendo anga. Kodi mwa inu mulibe munthu woongoka?”

    [79] “(Iwo) adati: “Ndithu ukudziwa bwino kuti tilibe khumbo ndi atsikana ako. Ndipo ndithu iwe ukudziwa bwino chimene tifuna.”

    [80] “(Iye) adati: “Ndikadakhala nayo mphamvu (yomenyana nanu) kapena kotsamira kolimba kwamphamvu (ndikadalimbana nanu kuti musachite zauve ndi alendowa).”

    [81] “(Athengawa) adati: “E iwe Luti! Ife ndi athenga a Mbuye wako. Safika kwa iwe (ndi chilichonse choipa). Ndipo choka pamodzi ndi banja lako m’gawo la usiku, ndipo aliyense wa inu asatembenuke (kuyang’ana m’mbuyo akamva mkokomo wa kudza kwa chilangocho), kupatula mkazi wako; iye chimpeza chimene chiwapeze anthu enawo. Ndithu lonjezo lawo ndi m’mawa. Kodi m’mawa suudayandikire?”

    [82] “Choncho, pamene lidadza lamulo lathu, tidaugadabula (m’zindawo) kumwamba kukhala pansi, pansi kukhala kumwamba, ndipo tidawavumbwitsira mvula ya sangalawe zopangika ndi dongo lotentheka ndi moto, zogwirana kwambiri

    [83] “(Sangalawezo) zokhala ndi zizindikiro kwa Mbuye wako. (Sangalawe iliyonse idali ndi mwini wake); ndipo chilango chimenechi sichili kutali ndi anthu oipa

    [84] “Ndipo, ku Madiyan tidamtuma m’bale wawo Shuaib, iye adati: “E inu anthu anga! Pembedzani Allah; mulibe mulungu wina koma Iye. Ndipo musachepetse mulingo wa mbale ndi wasikelo (powapimira anthu), ine ndikukuonani kuti ndinu opeza bwino, ndipo ndikukuoperani chilango cha tsiku (lalikulu) lomwe lidzakuzingani.”

    [85] ““Ndipo E inu anthu anga! Kwaniritsani mulingo wa mbale ndi wasikelo mwachilungamo, ndipo musawachepetsere anthu zinthu zawo (mwachinyengo). Ndipo musafalitse zoipa pa dziko ndi cholinga chodzetsa chisokonezo.”

    [86] ““Chuma chimene wakusiirani Allah (m’njira yovomerezeka) ndicho chabwino kwa inu ngati muli okhulupirira. Ndipo ine sindine msungi wanu.”

    [87] “Adati: “E iwe Shuaib! Kodi mapemphero ako akukulamula (kuti utilamule) kuti tisiye zimene makolo athu ankapembedza, kapena kuti tisiye kuchita zimene tifuna pachuma chathu? (Adati mwachipongwe) ndithudi, iwe ndiwe wanzeru, ndi wolungama.”

    [88] “(Iye) adati: “E inu anthu anga! Mukuona bwanji ngati ndili ndi umboni wowonekera wochokera kwa Mbuye wanga, ndipo nkundipatsa rizq labwino (lahalali) lochokera kwa Iye, (ndisiye zimenezi ndi kusankha njira yokhota)? Ndipo sindifuna kusiyana nanu pochita chimene ndakuletsani. Sindifuna china, koma kukonza mmene ndingathere; ndipo kupambana kwanga (pazimenezi) kuli kwa Allah. Kwa Iye ndatsamira, ndipo kwa Iye ndikutembenukira.”

    [89] ““Ndipo E inu anthu anga! Kutsutsana nane kusakuchimwitseni kuopera kuti chingakupezeni chonga chimene chidawapeza anthu a Nuh kapena anthu a Hûd kapenanso anthu a Swaleh; ndipo anthu a Luti sali kutali ndi inu.”

    [90] ““Ndipo mpempheni chikhululuko Mbuye wanu ndipo lapani kwa Iye (posiya machimo ndikuchita zabwino). Ndithu Mbuye wanga Ngwachisoni Ngwachikondi chochuluka (kwa anthu Ake).”

    [91] “(Iwo) adati: “E iwe Shuaib! Sitikumvetsa zambiri mwa zomwe ukunena. Ndipo ife tikukuona wofooka mwa ife. Pakadapanda akubanja lako, tikadakugenda ndi miyala. Ndipo ulibe ulemelero pa ife (koma tikusunga ulemu wa anthu akubanja lako).”

    [92] “(Iye) adati: “E inu anthu anga! Kodi anthu akubanja kwanga ndiwo olemekezeka kwambiri kwa inu kuposa Allah? Ndipo mwamuyika Iye (Allah) kukhala kumbuyo kwa misana yanu. Ndithu Mbuye wanga zonse zimene mukuchita akuzidziwa bwinobwino.”

    [93] ““Ndipo E anthu anga! Chitani (zimene mufuna) mmene mungathere; inenso ndichita chimodzimodzi (mmene ndingathere). Posachedwapa mudziwa ndani chimufike chilango chomsambula, ndipo ndani wabodza. Ndipo dikirani inenso ndidikira pamodzi ndi inu.”

    [94] “Ndipo pamene lamulo Lathu lidadza, tidampulumutsa Shuaib pamodzi ndi amene adakhulupirira naye, mwachifundo Chathu. Ndipo amene adachita zoipa, phokoso lidawachotsa moyo, tero kudawachera m’nyumba zawo ali lambilambi (atafa)

    [95] “Ndiye ngati sadakhalemo. Tamverani! Adaonongeka (anthu) a ku Madiyan monga momwe adaonongekera Asamudu

    [96] “Ndipo ndithu tidamtuma Mûsa pamodzi ndi zozizwitsa zathu ndi umboni woonekera

    [97] “Kwa Farawo ndi nduna zake. Koma iwo adatsata lamulo la Farawo, ndipo lamulo la Farawo siloongoka

    [98] “Tsiku la Qiyâma, (Farawo) adzawatsogolera anthu ake ndi kuwafikitsa ku Moto. Ndipo taonani pamalo poipa kufikirapo

    [99] “Iwo adatsatizidwa ndi tembelero pano pa dziko lapansi ndipo pa tsiku la Qiyâma (adzatsatizidwanso). Taonani kuipa mphoto (yawo) yopatsidwa

    [100] “Izi ndi zina mwa nkhani za m’mizinda (zomwe) tikukusimbira. Ina mwa iyo ikadalipobe, ndipo ina idatha

    [101] “Ndipo sitidawachitire choipa (powaononga). Koma adadzichitira okha zoipa (pakusakhulupirira Allah ndi kupembedza mafano ndikuipitsa pa dziko), milungu yawo yomwe ankaipembedza kusiya Allah siidawathandize chilichonse pamene lidadza lamulo la Mbuye wako (la kuwaononga). Ndipo (milunguyo) siidawaonjezere (china chake) koma chionongeko basi

    [102] “Ndipo mmenemo ndi momwe kumakhalira kulanga kwa Mbuye wako pamene alanga anthu a m’mizinda akakhala oipa (pa makhalidwe). Ndithu kulanga kwake (Allah) nkowawa, nkwaukali

    [103] “Ndithu m’zimenezi muli lingaliro kwa yemwe akuopa chilango cha tsiku lachimaliziro. Limenelo ndi tsiku losonkhanitsidwa anthu. Ndipo limenelo ndi tsiku lochitiridwa umboni (ndi zolengedwa zonse)

    [104] “Ndipo sitikulichedwetsa koma m’nthawi yowerengeka (kwa Allah, ngakhale kuti kwa anthu likuoneka kuti lili kutali)

    [105] “Tsiku lakudza (zoopsa zake), sadzayankhula aliyense koma mwachilolezo Chake (Allah). Ena adzakhala oipa, ndipo (ena) adzakhala abwino

    [106] “Tsono amene adzakhala oipa kobwerera kwawo nkumoto. Iwo adzakhala m’menemo akufuula potulutsa mawu ndi kuwabweza (monga kulira kwa bulu)

    [107] “Adzakhala m’menemo nthawi yaitali momwe thambo ndi nthaka zidzakhalire, kupatula Mbuye wako akadzafuna. Ndithu Mbuye wako Ngochita chimene wafuna

    [108] “Tsono amene adzakhale abwino adzakhala m’Munda wamtendere. Adzakhala mmenemo nthawi yaitali momwe thambo ndi nthaka zidzakhalire, kupatula Mbuye wako akadzafuna; zopatsa (za Mbuye wako ndizo zopatsa) zosatha

    [109] “Choncho, usakhale ndi chipeneko pa zimene awa akuzipembedza (kuti ndimilungu yabodza). Sapembedza koma momwe amapembedzera makolo awo kale. Ndipo ndithu Ife tiwapatsa gawo lawo (la chilango) mokwanira popanda kuchepetsa

    [110] “Ndipo ndithu tidampatsa buku Mûsa, koma kusiyana kudabuka mmenemo (pakatanthauzidwe ka bukulo pambuyo pa Mûsa). Pakadapanda mawu a Mbuye wako omwe adatsogola (oti sadzawalanga nthawi isanafike), ndithu kukadaweruzidwa pakati pawo. Ndipo ndithu iwo ali m’kukaika ndi kupeneka (kwakukulu) pa zimenezo

    [111] “Ndipo ndithu Mbuye wako adzawapatsa onsewo mphoto ya zochita zawo mokwanira. Ndithu Iye Ngodziwa (zonse) zimene akuchita

    [112] “Choncho (E iwe Mtumiki!) Pitiriza kulungama monga momwe akulamulira (iwe) pamodzi ndi omwe atembenukira (kwa Allah), ndipo musapyole malire. Ndithu Iye akuona zonse zimene muchita

    [113] “Ndipo musapendekere kwa amene sali olungama kuopa kuti chilango cha Moto chingakukhudzeni; ndipo simudzakhala ndi atetezi kwa Allah, ndipo potero simudzathandizidwa (chilichonse)

    [114] “Ndipo pemphera Swala nsonga ziwiri za usana ndi nthawi za usiku zomwe zili pafupi ndi usana. Ndithu zabwino zimachotsa zoipa. Ichi ndi chikumbutso kwa okumbukira

    [115] “Ndipo pirira (E iwe Mtumiki! Pokwaniritsa malamulo a Mbuye wako)! Ndithu Allah sataya malipiro a ochita zabwino

    [116] “Kodi bwanji sadakhalepo, mu mibadwo ya anthu akale, eni nzeru (omvera akalangizidwa), oletsa kuononga pa dziko kupatula ochepa amene tidawapulumutsa mwa iwo? Ndipo amene adadzichitira okha zoipa adatsata zomwe adasangalatsidwa nazo, choncho, adali ochita zoipa

    [117] “Ndipo Mbuye wako sali woononga midzi mopanda chilungamo pomwe eni ake (midziyo) ali ochita zabwino

    [118] “Ndipo Mbuye wako akadafuna, anthu onse akadawachita kukhala mpingo umodzi. Choncho saleka kukhala osiyana (maganizo)

    [119] “Kupatula omwe Mbuye wako wawachitira chifundo; ndipo chifukwa cha chifundocho, adawalenga (koma okha akusankha zoipa). Ndipo mawu a Mbuye wako akwaniritsidwa (akuti): “Ndithudi, ndizadzadzitsa Jahannam ndi ziwanda ndi anthu onse pamodzi (omwe adali oipa).”

    [120] “Ndipo tikukusimbira zonse mwa nkhani za atumiki zomwe tikukulimbikitsa nazo mtima. Ndipo m’zimenezi choonadi chakufika ndi ulaliki ndiponso chikumbutso kwa okhulupirira

    [121] “Ndipo auze amene sadakhulupirire (kuti): “Chitani mmene mungathere; nafenso tichita (mmene tingathere).”

    [122] ““Ndipo dikirani (chiweruzo cha Allah) nafenso tikudikira.”

    [123] “Zonse zobisika za kumwamba ndi pansi nza Allah ndipo zidzabwezedwa kwa Iye. Choncho, mpembedzeni ndi kutsamira kwa Iye. Ndithu Mbuye wako siwonyalanyaza zimene mukuchita

    Yusufu

    Surah 12

    [1] “Alif-Lâm-Ra. Izi ndi Ayah (ndime) za m’buku lomwe likuonetsera poyera (chilichonse chofunika)

    [2] “Ndithu Ife taivumbulutsa Qur’an ya Charabu kuti inu muzindikire

    [3] “Ife tikukusimbira nkhani zabwino zedi pokuzindikiritsa Qur’an iyi; ndithu udali mmodzi mwa osadziwa zinthu, isanakufike

    [4] “Akumbutse za Yûsuf pamene adauza bambo wake: “E inu bambo wanga! Ndithu ine ndaona kutulo nyenyezi khumi ndi imodzi, dzuwa ndi mwezi, zonsezo ndaziona zikundigwadira.”

    [5] “(Bambo wake) adati: “E iwe mwana wanga! Usawasimbire abale ako maloto ako (kuopa kuti) angakuchitire chiwembu; ndithu satana kwa munthu, ndi mdani woonekera.”

    [6] ““Ndipo momwemo Mbuye wako akusankha komanso akuphunzitsa kumasulira nkhani (za maloto) ndi kukwaniritsa mtendere Wake pa iwe, ndi pa mbumba ya Ya’qub monga momwe adakwaniritsira kwa makolo ako kale, Ibrahim ndi Ishaq. Ndithu Mbuye wako Ngodziwa, Ngwanzeru zakuya.”

    [7] “Ndithu mwa Yûsuf ndi abale ake, muli malingaliro ambiri kwa ofunsa (zinthu kuti adziwe)

    [8] “Kumbuka pamene (abale a Yûsuf) adati: “Ndithu Yûsuf ndi m’bale wake (Binyamini) ngokondeka zedi kwa bambo wathu kuposa ife pomwe ife ndife gulu lamphamvu. Ndithu bambo wathu ali mkusokera koonekera (sadziwa yemwe ali ndi chithandizo chokwanira).”

    [9] ““Mupheni Yûsuf kapena mukamponye ku dziko (lakutali), kuti nkhope ya bambo wanu ikutembenukireni (pakuti nthawi imeneyo Yûsuf sadzakhalapo, yemwe akumkonda kwambiriyo); ndipo pambuyo pake (mutalapa tchimoli) mdzakhala abwino, (kwa Allah).”

    [10] “Adanena wonena mwa iwo: “Musamuphe Yûsuf, koma mponyeni m’chitsime chakuya; adzamtola ena a paulendo ngati inu mwalingadi kutelo.”

    [11] “(Pambuyo pogwirizana paganizo lomuponya m’chitsime chakuya adapita kwa bambo wawo) anati: “E bambo wathu! Kodi bwanji simutikhulupirira pa Yûsuf, pomwe ife timamfunira zabwino?”

    [12] “Mperekeni mawa pamodzi ndi ife (kubusa) kuti akadye mokondwa ndi kusewera; ndithudi, ife tikamsamala.”

    [13] “(Bambo wawo) adati: “Ndithu zikundidandaulitsa zakuti mupite naye; ndikuopa kuti angajiwe ndi mimbulu pomwe inu simukulabadira za iye.”

    [14] “(Iwo) adati: “Ngati mimbulu itamudya pomwe ife ndife gulu lanyonga kwambiri, ndiye kuti tidzakhala otaika.”

    [15] “Ndipo pamene adanka naye ndi kugwirizana pakati pawo kuti amuike mchitsime chakuya, (adamuikadi). Ndipo tidamzindikiritsa iye (Yûsuf): “Ndithu udzawauza chinthu chawochi (chimene akuchitirachi) pomwe iwo sakudziwa.”

    [16] “Ndipo adadza kwa bambo awo madzulo akulira

    [17] “Akunena: “E bambo wathu! Tidapita kokapikisana (kuthamanga), ndipo tidamsiya Yûsuf pomwe padali ziwiya zathu; choncho mimbulu yamudya koma inu simutikhulupirira (pa zimene tikukuuzanizi) ngakhale kuti tikunena zoona.”

    [18] “Ndiponso adabwera ndi mkanjo wake (wa Yûsuf) uli ndi magazi abodza. (Bambo wawo pamene adauona mkanjowo uli wosang’ambika) adati: “Koma mitima yanu yakukometserani chinthu (chomwe mwamchitira mnzanu mwa chifuniro chanu; ndipo chimene ine ndingachite ndi) kupirira kwabwino; ndipo Allah ndi Wopemphedwa chithandizo pa zimene mukunenazi.”

    [19] “Ndipo aulendo adadza (pafupi ndi chitsimecho) ndipo adatuma wotunga madzi wawo, choncho iye adaponya ndowa yake (m’chitsime, ndipo akukoka ndowa ija adaona mwana) nati: “Eee, chisangalalo changa! Aka kamwana kakamuna!” Pomwepo iwo (amene adalipo pa chitsimepo) adam’bisa (kwa a paulendo anzawo) monga katundu wamalonda (yemwe adamgula). Koma Allah ankadziwa zimene adali kuchita (ndipo adanka naye ku Iguputo)

    [20] “Ndipo adamgulitsa pa mtengo wochepa ndi ndalama zapang’ono, zowerengeka (poopa kuti angawadzere eni mwanayo). Ndipo sadalabadire za iye

    [21] “Ndipo uja (amene) adamgula ku Iguputo, adati kwa mkazi wake: “Mkonzere pokhala pabwino (kapolo uyu), mwina angatithandize kapena tingamsandutse kukhala mwana (wathu).” Motero tidamkhazika Yûsuf m’dziko (la Iguputo mwachisangalalo), ndi kuti timphunzitse kumasulira nkhani (maloto). Ndipo Allah Ngopambana pa zinthu Zake (zimene wafuna kuti zichitike); koma anthu ambiri sadziwa

    [22] “Ndipo pamene (Yûsuf) adafika pa nsinkhu wozindikira zinthu, tidampatsa kuweruza ndi nzeru. Umo ndi momwe timawalipirira ochita zabwino

    [23] “Ndipo mkazi uja yemwe m’nyumba mwake mudali iye adamlakalaka (Yûsuf) popanda iye kufuna. Ndipo (mkaziyo) adatseka zitseko nati: “Bwera kuno.” (Yûsuf) adati: “Ndikudzitchinjiriza ndi Allah (kuchita tchimolo). Ndithu iye (mwamuna wako) ndi bwana wanga. Wandikonzera bwino pokhala panga (m’nyumba mwakemu, ndipo sindichita chinyengo chotere). Ndithu achinyengo siziwayendera bwino.”

    [24] “Ndipo (mkaziyo) adaikira mtima pa iye (kuti achite naye kanthu), ndipo naye (Yûsuf) adaikira mtima pa iye (kuti ammenye). Pakadapanda kuona chisonyezo cha Mbuye wake (chakumzindikiritsa kuti asatero, akadammenya. Koma adamthawa). Tidachita izi kuti timchotsere chinthu choipa ndi chauve; ndithudi, iye adali mwa akapolo athu oyeretsedwa

    [25] “Ndipo (onse awiri) adathamangitsana kukhomo (uku Yûsuf akuthawa) ndipo (mkaziyo) adang’amba mkanjo wake chakumbuyo. Ndipo awiriwa adampeza bwana wake (wa mkaziyo yemwe ndimwamuna wake) pakhomo; mkaziyo adati (kwa mwamuna wake mwaugogodi): “Palibe mphoto kwa yemwe akufuna kuchita choipa ndi mkazi wako koma kumponya kundende, kapena kupatsidwa chilango chowawa.”

    [26] “(Yûsuf) adati (podziteteza): “(Mkazi) uyu ndi yemwe wandifuna popanda ine kumufuna.” Ndipo mboni yochokera ku banja la mkaziyo idaikira umboni; (idati): “Ngati mkanjo wake wang’ambidwa cha kutsogolo, ndiye kuti (mkazi uyu) akunena zoona, ndipo iye (Yûsuf) ndi mmodzi mwa onena zabodza.”

    [27] ““Koma ngati mkanjo wake wang’ambidwa chakumbuyo ndiye kuti (mkazi uyu) wanena bodza ndipo iye (Yûsuf) ndi mmodzi mwa onena zoona.”

    [28] “Choncho (mwamuna uja) pamene adaona mkanjo wake (wa Yûsuf) utang’ambidwa chakumbuyo, (adadziwa kuti Yûsuf ndi amene amafuna kugwiliridwa), adati: “Ndithudi, izi ndi ndale zanu akazi. Ndithu ndale zanu ndi zazikulu (iwe mkazi wanga ndi amene udatsimikiza kuchita choipa ndi mnyamatayu).”

    [29] ““Yûsuf! Zisiye izi (usauze aliyense). Ndipo (iwe mkazi) pempha chikhululuko ku tchimo lako. Ndithu iwe ndiwe mmodzi mwa olakwa!”

    [30] “Ndipo akazi a mu mzindamo (ataimva nkhaniyi) anati: “Mkazi wa nduna akulakalaka m’nyamata wake popanda kulakalakidwa ndi iye; ndithu chikondi chamufooketsa zedi; ndithudi, ife tikumuona (mkaziyu kuti) ali m’kusokera koonekera.”

    [31] “Ndipo (mkazi wa nduna) pamene adamva kunyogodola kwawo, adawaitana (kuti adzaone kukongola kwa Yûsuf kuti adziwe kuti yemwe wathedwa nzeru polakalaka Yûsuf ngosayenera kudzudzulidwa). Ndipo adawakonzera phwando ndikupatsa aliyense wa iwo mpeni; kenaka adamuuza (Yûsuf): “Tuluka ndi kubwera pamaso pa iwo.” Choncho pamene (akazi aja) adamuona, adaona kuti nchinthu chachikulu zedi ndipo adadzicheka manja awo (ndi mipeni ija. Sadazindikire kuti akudzicheka chifukwa cha chidwi ndi kukongola kwa Yûsuf), ndipo adati: “Hasha Lillah! (tikudzitchinjiriza kwa Allah) uyu simunthu, uyu sichina koma ndi mngelo wolemekezeka.”

    [32] “(Mkazi wa nduna) adati: “Uyu ndi amene mumandidzudzula naye. Ndithudi ndidamulakalaka pomwe iye samandifuna ndipo anadziteteza. Ndipo ngati sachita chimene ndikumulamula, ndithu amangidwa ndipo ndithu akhala m’gulu la onyozeka!”

    [33] “(Yûsuf) adati: “E Mbuye wanga! Ndende ndi yabwino kwa ine kuposa izi akundiitanira. Ngati simundichotsera ndale zawo ndiye kuti ndiwacheukira ndikukhala mmodzi mwa mbuli.”

    [34] “Ndipo Mbuye wake adamuyankha (pempho lake) ndikumchotsera ndale zawo. Ndithudi, Iye Ngwakumva, Ngodziwa

    [35] “Kenako kudaoneka kwa iwo, (nduna ndi anthu ake) pambuyo poona zizindikiro (zonse zakuyeretsedwa kwa Yûsuf) kuti akamponye kundende kwa nthawi yochepa (pofuna kumusungira ulemu mkazi wa nduna)

    [36] “Ndipo anyamata awiri adalowa m’ndende pamodzi ndi iye. Mmodzi mwa iwo adati (kumuuza Yûsuf): “Ndithu ine ndalota ndikufulula mowa.” Ndipo wina adati: “Ndithu ine ndalota ndikusenza mikate pamutu panga yomwe idali kudyedwa ndi mbalame. Tiuze tanthauzo lake. Ndithu ife tikukuona iwe kuti ndiwe mmodzi wa anthu abwino.”

    [37] “(Yûsuf) adati: “(Kupyolera mu uneneri umene ndapatsidwa ndingathe kukumasulirani maloto anuwa ndi zinthu zina zobisika kwa inu), sichikudzerani chakudya cha mtundu uliwonse choti mungapatsidwe koma ndikhala nditakumasulirani tanthauzo lake chisanakufikeni; (ngati mukufunadi ndikuchitirani zimenezi). Izi ndi zina mwa zomwe Mbuye wanga wandiphunzitsa. Ndithudi, ine ndasiya njira za anthu osakhulupirira Allah ndiponso omwe akukana za tsiku la chimaliziro.”

    [38] ““Ndipo ine ndatsata chipembedzo cha makolo anga Ibrahim, Ishâq ndi Ya’qub; ndipo sikudali koyenera kwa ife kumphatikiza Allah ndi chilichonse. (Ndipo kuzindikira) zimenezi ndi ubwino wa Allah umene uli pa ife ndi anthu ena, koma anthu ambiri sathokoza.”

    [39] ““E inu anzanga awiri a m’ndende! Kodi milungu yambiri yosiyana ndiyo yabwino (kupembedzedwa), kapena Allah Mmodzi Mwini mphamvu (pachilichonse)?”

    [40] ““Simupembedza china kusiya Iye (Allah) koma ndi maina basi amene inu nokha mudawatcha ndi makolo anu, Allah sadatsitse umboni uliwonse pa zimenezo. Palibe lamulo lina koma ndi la Allah basi. Walamula kuti musampembedze aliyense koma Iye basi. Chimenecho ndicho chipembedzo choongoka, koma anthu ambiri sadziwa (monga inu mulili popembedza mafano).”

    [41] ““E inu anzanga awiri a m’ndende! Tsono mmodzi wa inu (abwerera ku ntchito yake) azikamwetsa mowa bwana wake (monga zidalili poyamba); koma winayo aphedwa mopachikidwa, ndipo mbalame zidzadya mmutu wake. Chiweruzo chaweruzidwa kale (kwa Farawo) pa chinthu chomwe mudali kufunsa.”

    [42] “Ndipo (Yûsuf) adauza yemwe adamdziwa kuti apulumuka mwa awiriwo: “Ukandikumbuke ponditchula pamaso pa bwana wako (Farawo; ukamuuze kuti ndamangidwa popanda tchimo).” Koma satana adamuiwalitsa kumkumbutsa bwana wake. Tero (mneneri Yûsuf) adakhala m’ndende zaka zingapo

    [43] “Ndipo (tsiku lina) mfumu (Farawo adalota) nati (kwa nduna zake): “Ndithudi, ine ndalota ng’ombe zisanu ndi ziwiri zonenepa zikudyedwa ndi ng’ombe zisanu ndi ziwiri zowonda ndiponso ndalota ngala zisanu ndi ziwiri zaziwisi ndi zina (zisanu ndi ziwiri) zouma. E inu akuluakulu! Ndimasulireni maloto angawa, ngati inu mumatha kumasulira maloto.”

    [44] “(Iwo) adati: “Amenewa ndi maloto osakanikirana (simaloto omveka)! Ndipo ife sitili odziwa kumasulira maloto amtundu umenewu.”

    [45] “Pamenepo amene adapulumuka mwa awiri aja adanena atakumbukira (pempho la Yûsuf) patapita nyengo (yaitali), adati: “Ine ndikuuzani tanthauzo lake. Choncho nditumeni (kuti ndikakufunireni tanthauzo lake).”

    [46] “(Adanka kundende ndikumpempha Yûsuf chikhululuko chifukwa cha kuiwala kwake. Ndipo adati): “Yûsuf! E iwe woona! Tiuze za ng’ombe zisanu ndi ziwiri zonenepa zikudyedwa ndi zisanu ndi ziwiri zoonda, ndi ngala zisanu ndi ziwiri zaziwisi ndi zina zouma; kuti ine ndibwelere kwa anthu kuti akadziwe.”

    [47] “(Yûsuf) adati: “Mudzalima zaka zisanu ndi ziwiri mondondozana ndi mwakhama ndipo zimene mwakolola zisiyeni m’ngala zake, kupatula zochepa zimene muzidzadya (kuti zam’ngalazo mudzadye mzaka zanjala).”

    [48] ““Kenako pambuyo pake zidzadza zaka zisanu ndi ziwiri za masautso zomwe zidzadya zimene mudasunga m’mbuyo, kupatula zochepa zimene muzidzazisunga (mobisa kuti zidzakhale mbewu.)”

    [49] ““Kenako pambuyo pa izi chidzadza chaka chomwe anthu m’menemo adzapulumutsidwa (ndi Allah), ndipo m’menemo adzafinya (zakumwa).”

    [50] “Ndipo mfumu idati: “M’bweretseni iye kwa ine.” Koma pamene mthenga (wa Mfumu) adamfika (Yûsuf, iye) adati: “Bwerera kwa bwana wako ndipo ukamfunse nkhani ya akazi omwe ankadzicheka manja awo. Ndithu Mbuye wanga akudziwa bwino ndale zawo. (Koma ndikufuna Mfumu kuti idziwe za kuyera kwanga kuti andiyeretsere maganizo ndipo asandiope).”

    [51] “(Mfumu idasonkhanitsa akazi aja ndipo) idati: “Kodi nkhani yanu njotani pamene mudamulakalaka Yûsuf pomwe iye sakufuna?” Adati: “Hasha Lillah! (Tikudzitchinjiriza kwa Allah)! Ife sitidadziwe choipa chilichonse kwa iye. (Tidayesayesa kuti achite nafe choipa koma sadalole).” (Nayenso) mkazi wa nduna adati: “Tsopano choonadi chatsimikizika; ine ndine amene ndidamulakalaka pomwe iye sakufuna. Ndithu iye ndi mmodzi mwa owona.”

    [52] “(Yûsuf adati): “Zimenezo (zofuna kuti afunsidwe chonchi) n’chifukwa chakuti (nduna) idziwe kuti ine sindidaichitire zoipa iyo kulibe, ndi kuti Allah saongolera ndale za anthu achinyengo (kuti zipambane).”

    [53] “۞ “Ndipo ine sindikuyeretsa mtima wanga. Ndithu mtima uliwonse umalamulira kwambiri ku zoipa kupatula umene Mbuye wanga wauchitira chifundo. Ndithudi, Mbuye wanga Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha.”

    [54] “Choncho Mfumu idati: “Mubwere naye kwa ine kuti ine mwini ndimsankhe.” Ndipo pamene adayankhula naye, (Mfumu) idati: “Ndithu iwe lero kwa ife wakhala wolemekezeka, wokhulupirika.”

    [55] “(Yûsuf) adati: “Ndiikeni kukhala muyang’aniri wa nkhokwe za dzinthu zam’dziko lonse. Ndithudi, ine ndine msungi wodziwa.”

    [56] “Ndipo motero tidampatsa ulemelero Yûsuf m’dziko (la Iguputo); amakhala m’menemo paliponse pamene wafuna. Timam’bweretsera chifundo Chathu amene tamfuna, ndipo sitisokoneza malipiro a ochita zabwino

    [57] “Ndithudi malipiro a tsiku la chimaliziro ngabwino zedi kwa amene akhulupirira ndipo adali kumuopa (Allah)

    [58] “Ndipo adadza abale (ake) a Yûsuf (kukafuna chakudya kumeneko pamene ku Kenani kudagwa chilala chadzaoneni) ndikulowa kwa iye, ndipo (iye) adawazindikira pomwe iwo sankamzindikira

    [59] “Ndipo pamene adawakonzera chakudya chawo, adati: “(Ngatimudzabwereranso kachiwiri) mudzabwere ndi m‘bale wanu wa kumbali ya bambo anu, kodi simuona kuti ine ndikukwaniritsa muyeso, ndipo ndine wabwino kwambiri polandira (alendo)?”

    [60] ““Koma ngati simudzandibweretsera iye, simudzakhala ndi mulingo (wachakudya) kwa ine, ndipo musadzandiyandikire.”

    [61] “(Iwo) adati: “Tikayesetsa kuwanyengelera bambo wake za iye (kufikira akatipatse). Ndithu ife tikachita zimenezi.”

    [62] “Ndipo (Yûsuf) adati kwa anyamata ake a ntchito: “Ikani chuma chawo m’mitolo yawo kuti akachizindikire akabwerera ku mawanja awo. (Tachita izi kuti) mwina angabwelerenso (kuno).”

    [63] “Ndipo pamene adabwerera kwa bambo wawo, adati: “E bambo wathu! Tikamanidwa muyeso wa chakudya (pa ulendo wachiwiri pokhapokha titsagane ndi m’bale wathuyu). Choncho mtumizeni m’bale wathu pamodzi ndi ife kuti akatipimire (mlingo wokwana); ndithu ife tikamsunga.”

    [64] “(Ya’qub) adati: “Kodi ndingakukhulupirireni pa iye kuposa momwe ndidakukhulupirirani pa m’bale wake kale (yemwe mudamsokeretsa)? Koma Allah ndi Yemwe ali Wabwino posunga, Ndipo Iye Ngwachifundo zedi kuposa achifundo onse.”

    [65] “Ndipo pamene adatsekula katundu wawo, adapeza chuma chawo chabwezedwa kwa iwo. Adati: “E bambo wathu! Tingafunenso chiyani (kwa munthu waufuluyu)? Ichi chuma chathu chabwezedwa kwa ife; ndipo tikabweretsa chakudya chothandizira mawanja athu; ndipo m’bale wathu tikamsunga; tikapezanso muyeso wangamira imodzi yoonjezera. Umenewu ndi mlingo wochepa (kwa mfumu ya ufuluyo).”

    [66] “(Ya’qub) adati: “Sindingamtumize pamodzi ndi inu pokhapokha mundipatse lonjezo m’dzina la Allah kuti ndithudi mudzambweza kwa ine pokhapokha nonsenu mutazingidwa (ndi zoopsa).” Ndipo pamene adapereka lonjezo lawo, (iye) adati: “Allah ndiye Muyang’aniri (mboni) pa zimene tikunenazi.”

    [67] “Adatinso: “E inu ana anga! Musakalowe (mu Iguputo) pachipata chimodzi koma kaloweni pa zipata zosiyanasiyana. Ndipo sindingakuthandizeni chilichonse kwa Allah. Lamulo ndi la Allah basi; kwa Iye ndiko ndatsamira; ndipo otsamira atsamire kwa Iye.”

    [68] “Ndipo pamene adalowa monga momwe bambo wawo adawalamulira, sikudawathandize chilichonse kwa Allah kupatula khumbo lomwe lidali mu mtima mwa Ya’qub (ndilomwe) adalikwaniritsa, (Ya’qub adali kufuna Yûsuf ndi m’bale wake akumane mwamseri; ndipo adakumanadi). Ndithu iye (Ya’qub) adali wanzeru chifukwa chakuti tidamphunzitsa. Koma anthu ambiri sadziwa

    [69] “Ndipo pamene adalowa kwa Yûsuf (ndikumuona m’bale wake atalowa payekha), adamkumbatira m’bale wakeyo nati: “Ndithu ine ndine m’bale wako; choncho usadandaule pa zimene (abale athu) akhala akuchita.”

    [70] “Ndipo pamene adawakonzera chakudya chawo, adaika chikho chomwera madzi mumtolo wa m’bale wakeyo. Kenako woitana adaitana: “E inu a paulendo! Ndithu inu ndinu akuba.”

    [71] “(Onse abale ake a Yûsuf) pamene adawacheukira, adati: “Kodi mukusowa chiyani?”

    [72] “Adati: “Tikusowa muyeso wa Mfumu; ndipo amene aubweretse, alandira mtolo wangamira yathunthu.” (Ndipo Mneneri Yûsuf adati): “Ndipo ine ndine muimiliri pa zimenezi.”

    [73] “(Iwo) adati: “Tikulumbira Allah! Ndithu inu mukudziwa kuti sitidadze kudzaononga m’dziko, ndiponso sitili akuba.”

    [74] “Adati: “Mphoto (chilango) yake ikhala yotani ngati mukunena bodza?”

    [75] “Adati: “Mphoto yake ndi yemwe (chikhocho) chapezeka mu mtolo wake, iye ndiye mphoto yake. (Agwidwe monga kapolo kwa chaka chimodzi).” Umu ndi momwe timawalipirira anthu achinyengo

    [76] “Ndipo (mneneri Yûsuf) adayamba kufufuza m’mitolo mwawo asanafufuze mu mtolo wa m’bale wake; kenako adachitulutsa mu mtolo wa m’bale wake. Umu ndi momwe tidamlinganizira ndale Yûsuf (kuti ampeze m’bale wake). Mwachilamulo cha mfumu (ya m’dzikolo) sakadamutenga m’bale wake (monga kapolo) koma mmene Allah adafunira (powaonetsa abale ake za chilamulo cha kwawo chomuika mu ukapolo munthu wakuba). Timawakwezera pa ulemelero amene tawafuna. Ndipo pa wodziwa aliyense pali wodziwanso kuposa iye

    [77] “(Iwo) adati: “Ngati waba, m’bale wakenso adabapo kale.” (Uku kudali kumunamizira Yûsuf bodza pomwe iwo sankadziwa kuti yemwe akuyankhula nayeyo ndiye Yûsuf). Koma Yûsuf adabisa (mawu awa) mu mtima mwake, (chifukwa chowamvera chisoni) ndipo sadawaululire. Adati: “Inu muli ndi chikhalidwe choipa ndipo Allah akudziwa zomwe mukunena!”

    [78] “(Iwo) adati: “E inu bwana! Uyu ali ndi bambo wake wokalamba kwambiri; choncho tengani mmodzi wa ife mmalo mwake; ndithudi, ife tikuona kuti inu ndinu mmodzi mwa ochita zabwino.”

    [79] “(Yûsuf) adati: “Ha! tikudzitchinjiriza mwa Allah, sitingagwire wina koma yemwe chuma chathu tachipeza ndi iye, kuopa kuti tingakhale ochita zoipa.”

    [80] “Choncho, pamene adataya mtima za iye, adapita pambali kukanong’onezana. Wamkulu wawo adati: “Kodi simudziwa kuti bambo wanu adatenga lonjezo kuchokera kwa inu m’dzina la Allah (kuti mudzam’bweza iyeyo?) ndiponso kale mudalakwa (pa mapangano anu) pa za Yûsuf. Choncho sindichoka dziko lino kufikira atandilola bambo (kutero) kapena Allah andilamule (zondichotsa kuno pomasulidwa m’bale wangayu); Iye Ngwabwino polamula kuposa olamula.”

    [81] ““Bwererani kwa bambo wanu ndipo mukawauze (kuti): “E bambo wathu! Ndithu mwana wanu waba. Ndipo ife sitidaikire umboni (wakuti wakuba achitidwe ukapolo) koma pa zomwe tidazidziwa (kuti mwa ife mulibe wakuba), ndipo sitidali kudziwa zamseri.”

    [82] ““Ndipo afunseni anthu a m’mudzi momwe tidalimo ndi a pa ulendo omwe tadza nawo, ndipo ndithudi ife tikunena zoona.”

    [83] “(Ya’qub) adati: “Koma mitima yanu yakukometserani chinthu. (Kwanga ndi) kupirira kwabwino kokha basi. Mwina Allah adzandibweretsera onse pamodzi. Ndithudi, Iye Ngodziwa, Ngwanzeru zakuya.”

    [84] “Ndipo adawachokera ndikunena (kuti): “Ha! kudandaula kwanga za Yûsuf!” Ndipo maso ake adayera chifukwa cha kudandaula ndipo iye adadzazidwa ndi chisoni

    [85] “(Iwo) adati: “Tikulumbira Allah! Simusiya kumkumbukira Yûsuf (ndikulira) mpaka mufika podwala, kapena mukhala mwa owonongeka (ndi imfa).”

    [86] “(Iye) adati: “Ndithu ine ndikusuma dandaulo langa ndi kukhumata kwanga kwa Allah, ndipo ndikudziwa kupyolera mwa Allah zomwe simukudziwa.”

    [87] ““E ana anga! Pitani mukafufuzefufuze za Yûsuf ndi m’bale wake, ndipo musataye mtima pa chifundo cha Allah. Ndithu palibe amene amataya mtima za chifundo cha Allah koma anthu osakhulupirira.”

    [88] “(Ndipo adapita ku Iguputo). Choncho pamene adalowa kwa iye (Yûsuf), adati: “E inu olemekezeka! Masautso atikhudza, ife ndi maanja athu; choncho tabwera ndi chuma chopanda pake. Tidzadzireni mlingo (ngakhale chuma chathucho chili chopanda pake), ndipo tithandizeni mwaulere. Ndithu Allah amawalipira othandiza mwaulere.”

    [89] “(Iye) adati: “Kodi mukudziwa zomwe mudamchitira Yûsuf ndi m’bale wake pamene inu mudali mu umbuli?”

    [90] “(Iwo) adati: “Kodi iwe ndiwe Yûsuf?” Adati: “Ine ndine Yûsuf, ndipo uyu ndi m’bale wanga; Allah watichitira zabwino. Ndithu amene aopa Allah ndikumapirira, (Allah amulipira). Ndithu Allah sasokoneza malipiro a ochita zabwino.”

    [91] “(Iwo) adati: “Tikulumbira Allah! Allah wakusankha pa ife, ndipo ife tidalidi olakwa.”

    [92] “(Iye) adati: “Lero palibe kukudzudzulani; Allah akukhulukirani, ndipo Iye Ngwachifundo chochuluka kuposa achifundo.”

    [93] ““Pitani ndi mkanjo wangawu ndipo mukauponye pamaso pa bambo wanga ndipo iwo akapenya. Kenako nonsenu ndi maanja anu onse mudze kwa ine.”

    [94] “Ndipo aulendo pamene adamuka (kubwerera kwawo). Bambo wawo (yemwe adali ku Kenani) adati: “Ndikumva fungo la Yûsuf pakadapanda kuti muli ndi chikhulupiliro choti ndasokonezeka nzeru, (mukadandikhulupirira)”

    [95] “(Iwo) adati: “Tikulumbira Allah! Ndithu muli mkusokera kwanu kwa kale (pokonda Yûsuf kuposa ife).”

    [96] “Choncho pamene adadza wotenga nkhani yabwino, adauponya (mkanjo wa Yûsuf) pankhope pake, ndipo pompo adapenya. Adati: “Kodi sindinakuuzeni kuti ine ndikudziwa kupyolera mwa Allah zomwe inu simukuzidziwa?”

    [97] “(Iwo) adati: “E bambo wathu! Tipemphereni chikhululuko pa machimo athu. Ndithu ife tidali olakwa.”

    [98] “(Iye) adati: “Posachedwapa (ndikamuona Yûsuf) ndikupempherani chikhululuko kwa Mbuye wanga. Ndithu Iye Ngokhululuka zedi, Ngwachisoni chosatha.”

    [99] “Ndipo pamene adalowa kwa Yûsuf, adawakumbatira makolo ake ndikunena: “Lowani mu Iguputo, In-shaa-Allah, (Allah akalola) mwamtendere.”

    [100] “Ndipo (pamene adafika kwa Yûsuf), (iye) adawakweza makolo ake ndikuwaika pa chimpando (chake) chachifumu, ndipo onse adagwa kumlambira (monga mwachizolowezi chawo nthawi imeneyo). Ndipo (Yûsuf) adati: “E inu bambo wanga! Ili ndilo tanthauzo (lenileni) la maloto anga akale. Palibe chipeneko Mbuye wanga wawatsimikiza (malotowo). Ndipo adandichitira zabwino ponditulutsa kundende ndi pokubweretsani inu kuchokera kumidzi (Kenani), pambuyo pokhwirizira (chidani) satana pakati pa ine ndi abale anga. Ndithudi Mbuye wanga amadziwa kwambiri chinsinsi cha zomwe wakonza kuti zichitike. Ndithu Iye Ngodziwa, Ngwanzeru

    [101] “(Kenako adathokoza ndi kupempha Allah kuti): “E Mbuye wanga! Ndithu mwandipatsako ufumu ndi kundiphunzitsako kumasulira nkhani (maloto). E Inu Mlengi wa thambo ndi nthaka! Inu ndiye Mtetezi wanga pa dziko lapansi ndi tsiku la chimaliziro. (Ndipo nthawi ya imfa yanga) mudzandipatse imfa ndili Msilamu ndipo kandikumanitseni ndi ochita zabwino.”

    [102] “Izi ndi zina mwa nkhani zamseri (zomwe) tikukuululira iwe. Ndipo siudali nawo pamodzi pamene adatsimika chochita chawo (uku) akuchita chiwembu (chawo) choipa

    [103] “Ndipo ambiri mwa anthu sakhulupirira ngakhale utalimbika chotani

    [104] “Ndipo sukuwapempha malipiro pa zimenezi. Sichina izi (zimene wadza nazo), koma ndi ulaliki kwa zolengedwa zonse

    [105] “Ndipo ndi zisonyezo zingati (zosonyeza kuti Allah alipo) kumwamba ndi pansi zomwe akuzidutsa pamene iwo sakuzilabadira

    [106] “Ndipo ambiri a iwo sakhulupirira Allah koma momphatikiza

    [107] “Kodi akudziika pachitetezo kuti silingawadzere tsoka lachilango cha Allah, kapena kuti siingawadzere Qiyâma mwadzidzidzi pomwe iwo sakuzindikira

    [108] “Nena: “Iyi ndi njira yanga. Ndikuitanira kwa Allah mwa nzeru zokwanira, ine ndi omwe akunditsata. Ndithu Allah wapatukana (ndi mbiri zopunguka). Ndipo ine sindili mwa ophatikiza (Allah ndi zinthu zina).”

    [109] “Ndipo sitidatume (mtumiki aliyense) patsogolo pako koma adali amuna amene tidawavumbulutsira (chivumbulutso); ochokera mwa anthu a m’mizinda. Kodi sadayende (iwo osakhulupirira) pa dziko nkuona momwe mathero a oipa omwe adalipo patsogolo pawo (momwe adalili)? Ndipo nyumba ya tsiku la chimaliziro njabwino kwa owopa Allah. Kodi mulibe nzeru

    [110] “Mpaka pamene atumiki adataya mtima (za anthu awo) nkuganiza kuti ayesedwa onama, chithandizo chathu chidawadzera, ndipo amene tidawafuna adapulumuka. Koma chilango chathu sichibwezedwa kwa anthu oipa

    [111] “Ndithu m’nkhani zawo izi muli phunziro kwa eni nzeru. (Qur’aniyi) simawu opekedwa, koma (iyi Qur’an) ndi chitsimikizo cha zomwe zidalipo patsogolo pake (m’mabuku ena a Allah), ndi kumasulira kwa tsatanetsatane pa chilichonse ndiponso chiongoko ndi mtendere kwa anthu okhulupirira

    Bingu

    Surah 13

    [1] “Alif-Lâm-Mîm-Râ. Izi ndi Ayah (ndime) za buku ili (lomwe lasonkhanitsa chilichonse chofunika); ndipo chomwe chavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako, nchoonadi; koma anthu ambiri sakhulupirira

    [2] “Allah ndi Yemwe adatukula thambo popanda mizati imene mukuiona; kenako adakhazikika pa Arsh (Mpando Wachifumu Waukulu, kukhazikika koyenera ndi Iye komwe kulibe chofanizira); ndipo adafewetsa dzuwa ndi mwezi (kwa anthu). Chilichonse mwa zimenezi chikupitilira kuyenda mpaka nyengo imene idaikidwa. Iye ndi Yemwe akuyendetsa zinthu; akulongosola Ayah (ndime) kuti mukhale ndi chitsimikizo pa zakukumana ndi Mbuye wanu

    [3] “Ndipo Iye ndi Yemwe adatambasula nthaka ndikuika mapiri ndi mitsinje m’menemo. Ndipo mtundu uliwonse wazipatso adaupanga m’menemo kukhala mitundu iwiri iwiri, (yachimuna ndi yachikazi), amavindikira usiku ndi usana. Ndithu m’zimenezi muli zisonyezo (zazikulu zosonyeza kuti Allah alipo) kwa anthu olingalira

    [4] “Ndipo m’nthaka muli zigawo zogundana, (koma kumeretsa kwake kwa zomera nkosiyanasiyana). Mulinso minda ya mphesa ndi mmera wina ndi kanjedza wokhala ndi nthambi ndi wopanda nthambi; (zonsezi) zikuthiliridwa ndi madzi amodzi ofanana, ndipo tikuzichita zina kukhala zabwino kuposa zina mkakomedwe kake. Ndithu m’zimenezi muli zisonyezo kwa anthu anzeru

    [5] “Ndipo ngati ukudabwa, (basi) chodabwitsa kwambiri ndiko kuyankhula kwawo (koti): “Kodi tikadzakhala dothi, ndi zoona tidzakhala ndi chilengedwe chatsopano? (Allah sangathe zimenezi).” Iwowo ndi amene sadakhulupirire Mbuye wawo. Ndipo kwa iwowo mudzakhala magoli m’makosi mwawo; ndipo iwo ndi anthu a ku Moto, m’menemo adzakhala nthawi yaitali

    [6] “Ndipo akukufulumizitsa kuti ubweretse choipa (chomwe ndi chilango chawo) m’malo mwa chabwino; ndithu chikhalirecho zilango zambiri zidapita kale (zomwe akadayenera kuchenjera nazo)! Koma Mbuye wako ndi mwini chikhululuko kwa anthu pa uchimo wawo. Ndipo ndithu Mbuye wako Ngolanga mwaukali

    [7] “Ndipo osakhulupirira akunena: “Bwanji sichidatsitsidwe kwa iye chozizwitsa chochokera kwa Mbuye wake?” Ndithu iwe ndiwe mchenjezi, ndipo mtundu uliwonse wa anthu uli ndi muongoli (wakewake yemwe ali ndi njira zakezake zoongolera anthuwo, osati kutsata njira za muongoli wina)

    [8] “Allah akudziwa chilichonse chimene mkazi asenza (m’mimba mwake) ndi zimene mimba zikupungula ndi zimene zikuonjezera. Chinthu chilichonse kwa Iye chili ndi mlingo (wake)

    [9] “(Iye ndi Yemwe ali) Wodziwa zamseri ndi zoonekera, Wamkulu, Wapamwambamwamba

    [10] “Ndi chimodzimodzi (kwa Iye Allah) amene akubisa liwu lake mwa inu ndi amene akulikweza ndi yemwe akudzibisa usiku ndi yemwe akuyenda usana, (onse akuwadziwa)

    [11] “(Munthu aliyense) ali nalo gulu (la angelo) patsogolo pake ndi pambuyo pake (omwe) amamulondera (ndi kulemba zomwe akuchita) mwa lamulo la Allah. Ndithudi, Allah sasintha zomwe zilipo kwa anthu mpaka atasintha iwo zomwe zili m’mitima yawo. Ndipo Allah akawafunira anthu chilango, palibe chochitsekereza; ndipo alibe mtetezi m’malo mwake (Allah)

    [12] “Iye ndi Yemwe amakuonetsani kung’anima mokuopyezani (kuphedwa ndi mphezi) ndi mokupatsani chiyembekezo chabwino (chakudza mvula). Ndipo amabweretsa mitambo yolemera (ndi madzi amvula)

    [13] “Ndipo mphezi imalemekeza Allah ndi kumthokoza, naonso angelo (amamlemekeza) momuopa. Ndipo Allah, amatumiza kumenya kwa mphezi ndi kummenya nako amene wamfuna. Ndipo iwo (okanira) akutsutsana pa za Allah (kuti alipo kapena palibe pomwe Iye alipo). Ndipo Iye Ngolanga mwaukali

    [14] “Kwa Iye ndiko kuli (kuvomera) pempho lachoonadi. Ndipo aja amene akupempha mafano kusiya Iye (Allah), sawayankha pa chilichonse koma (chikhalidwe chawo) chili ngati yemwe akutambasulira madzi manja ake awiri kuti afike m’kamwa mwake; koma sangafike. Ndipo mapemphero a osakhulupirira sali kanthu koma ndi otaika basi (opita pachabe)

    [15] “Ndipo amene ali kumwamba ndi pansi amamgwadira Allah mwachifuniro ndi mopanda chifuniro; ndiponso zithunzi zawo (zimamgwadira) m’mawa ndi madzulo

    [16] “Nena: “Ndani Mbuye wa thambo ndi nthaka?” Nena: “Ndi Allah.” Nena: “Mukudzipangira milungu ina kusiya Iye, (milungu) yomwe siingadzibweretsere zabwino kapena kudzichotsera sautso?” Nena: “Kodi angakhale ofanana wakhungu ndi wopenya? Kodi kapena ungafanane mdima ndi kuunika?” Kapena ampangira anzake Allah omwe adalenga zofanana ndi zomwe Allah adalenga kotero kuti zolengedwa (zambali ziwirizo) zikufanana kwa iwo? Nena: “Allah ndiye Mlengi wa chilichonse. Ndipo Iye ndi Mmodzi Wayekha, Wopambana (ndipo chimene Iye wafuna ndi chimene chimachitika)”

    [17] “Adatsitsa madzi, kuchokera ku mitambo, ndipo zigwa zidayendetsa madzi mwa mlingo wake. Ndipo msefukiro wamadzi udatenga thovu lomwe limayandama pamwamba pa madzi. Ndiponso zomwe amazisungunula pa moto chifukwa chofuna zodzikongoletseranazo kapena ziwiya (monga zagolide ndi siliva), mumakhalanso thovu chimodzimodzi. Umo ndi momwe Allah akuperekera fanizo lachoonadi ndi fanizo lachonama. Tsono thovu, limangopita monga zitakataka chabe; koma zimene zimathandiza anthu, zimakhazikika m’nthaka. Umo ndi m’mene Allah akuperekera mafanizo

    [18] “Amene adavomera Mbuye wawo, adzapeza zabwino. Koma amene sadamuvomere, ngakhale akadakhala nazo zonse za m’dziko ndi zina zonga izo pamodzi, ndikuzipereka kuti adziombolere (sizikadavomerezedwa). Ndipo iwo adzakhala ndi chiwerengero choipa. Ndipo malo awo ndi ku Jahannam, taonani kuipa kwa malo okakhazikikamo

    [19] “Kodi amene akudziwa kuti zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako nzoona, angafanane ndi yemwe ali wakhungu? Ndithudi eni nzeru ndi okhawo olingalira

    [20] “(Iwowo ndi) omwe akukwaniritsa lonjezo la Allah, ndipo saswa lonjezo lomangika (pakati pawo ndi anzawo)

    [21] “Ndiponso omwe akulumikiza zomwe Allah walamula kuti zilumikizidwe (monga chibale), pamodzi ndi kuopa Mbuye wawo ndi kuopanso chiwerengero choipa (chomwe chidzawapeza oipa tsiku lachimaliziro tero amayesetsa kuwapatuka machitidwe oipa)

    [22] “Ndi omwenso amapirira chifukwa chofuna chiyanjo cha Mbuye wawo ndi kupemphera Swala ndi kupereka mu zomwe tawapatsa, mobisa ndi moonekera, ndi kuchotsa choipa ndi chabwino (pochita chabwino pa choipacho); iwo ndi omwe adzapeza malipiro (abwino) a ku Nyumba ya tsiku la chimaliziro

    [23] “Minda yamuyaya adzailowa iwo (pamodzi) ndi amene adachita zabwino mwa makolo awo, akazi awo ndi ana awo; ndipo angelo azikalowa kwa iwo khomo lililonse

    [24] “(Uku akunena): “Salaamun Alayikumu (Mtendere uli pa inu) chifukwa chakupirira kwanu (pochita zabwino ndi kusiya zoipa ndi kukhala mwaubwino ndi anzanu)! Taona kukhala bwino zotsatira za Nyumba ya tsiku la chimaliziro.”

    [25] “Koma amene akuswa lonjezo la Allah (ndi malonjezo a anthu anzawo) pambuyo polimanga motsimikiza, ndi kumadula chimene Allah walamula kuti chilumikizidwe, ndi kumaononga padziko, iwowo ndiwo adzapeza tembelero; ndiponso adzapeza Nyumba yoipa

    [26] “Allah amamtambasulira rizq amene wamfuna, ndipo amamfumbatiranso (kumchepetsera arnene wamfuna). Ndipo akusangalalira moyo wa pa dziko lapansi, suli kanthu moyo wapadziko poyerekeza ndi moyo wa pambuyo pa imfa, koma ndi chisangalalo chochepa basi

    [27] “Ndipo amene sadakhulupirire akunena: “Bwanji sichidatsitsidwe kwa iye chozizwitsa kuchokera kwa Mbuye wake?”‘ Nena: “Ndithu Allah amalekelera kusokera amene wamfuna (chifukwa chosafuna kutembenukira kwa Iye Allah); ndipo amamuongolera amene akutembenukira kwa Iye.”

    [28] “(Awa ndi) amene akhulupirira, ndipo mitima yawo ikukhazikika pokumbukira Allah. Dziwani, pokumbukira Allah mitima imakhazikika (imatonthola)

    [29] “Amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, chisangalalo nchawo ndi mabwelero abwino

    [30] “Momwemo takutuma kwa anthu omwe adapita patsogolo pawo anthu ena (ndipo amva nkhani zawo zonse); kuti uwawerengere zimene tikukuvumbulutsira; koma iwo akumkana (Allah) Wachifundo chambiri. Nena: “Iyeyo ndi Mbuye wanga! Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye; ndatsamira kwa Iye, ndipo kobwerera kwanga nkwa Iye basi.”

    [31] “Ndipo ikadakhalapo Qur’an yomwe chifukwa cha iyo mapiri akadayendetsedwa (panthawi yoiwerenga), kapena chifukwa cha iyo, nthaka ikadang’ambidwa, kapena chifukwa cha iyo, akufa akadayankhulitsidwa, (yochititsa zimenezi ikadakhala Qur’an iyi. Koma ntchito ya Qur’an siimeneyo)! Zinthu zonse nza Allah. Kodi sadadziwebe amene akhulupirira, kuti Allah akadafuna akadawaongolera anthu onse (ku Chisilamu; akadawalenga monga angelo opanda zilakolako, koma wawapatsa nzeru ndi zilakolako kuti alimbane ndi ziwirizi; ena apambane ndi kulowa ku Munda wamtendere). Ndipo tsoka silisiya kuwapeza amene sadakhulupirire chifukwa cha zomwe achita, kapena litsika pafupi ndi dziko lawo kufikira lonjezo la Allah lifike (lowachotsa moyo), ndithudi, Allah saswa malonjezo (Ake)

    [32] “Ndipo ndithu adachitidwa chipongwe atumiki akale iwe usanadze koma ndidawalekelera amene sadakhulupirire (sindidawalange mwachangu), ndipo kenako ndidawalanga. Kodi chilango changa chidali chotani

    [33] “Kodi amene akuimilira mzimu uliwonse pa zimene udapeza (kuti adzaulipire, sindiye woyenera kupembedzedwa)? Ndipo ampangira Allah anzake. Nena: “Atchuleni (anzakewo).” Kodi kapena mukumuuza zomwe sakuzidziwa pa dziko, kapena (zomwe mukunenazo) ndimawu chabe (opanda cholinga chilichonse)? Koma amene sadakhulupirire akometsedwa ndi bodza lawoli lamkunkhuniza, ndipo atsekerezedwa kunjira (ya choonadi). Ndipo amene Allah wamulekelera kusokera alibe muongoli (wina womuongolera)

    [34] “Ali nacho chilango m’moyo wa dziko lapansi, koma chilango chapambuyo pa imfa nchokhwima zedi; ndipo sadzakhala ndi mtetezi kwa Allah

    [35] “Fanizo la Munda wamtendere umene alonjezedwa amene akuopa Allah (uli tere:) Pansi (ndi patsogolo) pake ikuyenda mitsinje. Zipatso zake ndi mthunzi wake nzanthawi zonse. Awa ndiwo malekezero a omwe akuopa Allah; koma malekezero a osakhulupirira ndi ku Moto basi

    [36] “Ndipo (ena mwa) omwe tidawapatsa mabuku (Ayuda ndi Akhrisitu), akusangalalira zimene zavumbulutsidwa kwa iwe (ndipo akulowa m’Chisilamu). Koma ena mu unyinji wa osakhulupirira akukana gawo lina la nkhaniyi. Nena: “Ndalamulidwa kupembedza Allah basi; ndi kusamphatikiza (ndi china). Ndikuitanira kwa Iye, ndipo kwa Iye ndiwo mabwelero anga.”

    [37] “Ndipo momwemo taivumbulutsa (iyi Qur’an) m’Chiarabu kuti ikhale chilamulo (cha Allah). Ngati utsata zofuna zawo pambuyo pokufika kuzindikiraku, sudzakhala ndi bwenzi ngakhale mtetezi kwa Allah

    [38] “Ndipo ndithu tidatuma atumiki patsogolo pako iwe usanadze ndipo tidawalola kukhala ndi akazi ndi ana; (sichachilendo iwe kukhala ndi akazi ndi ana). Ndipo nkosatheka kwa mtumiki kudzetsa chozizwitsa koma pokhapokha ndi chilolezo cha Allah. Nyengo iliyonse ili ndi lamulo lake limene Allah adalilemba. (Nyengoyo ikakwana, lamulo limadza)

    [39] “Allah amafafaniza zimene wafuna ndi kulimbikitsa (kuti zisachoke zomwe wafuna), ndipo gwero la malamulo onse lili kwa Iye (Allah)

    [40] “Ndipo ngati tikusonyeza zina mwa (zilango) zimene tawalonjeza, kapena kukupatsa imfa (usanazione zilangozo, ndithu ziwafikabe). Ndithu udindo wako ndi kufikitsa uthenga basi (umene walamulidwa kuufikitsa kwa iwo) ndipo Ife udindo wathu ndi kuwerengera (zochita zawo)

    [41] “Kodi sadaone kuti tikulidzera dziko lawo ndi kulichepetserachepetsera malire ake? Ndipo Allah amalamula (mwachilungamo) palibe wotsutsa lamulo Lake. Ndipo Iye Ngwachangu pakuwerengera

    [42] “Koma amene adalipo kale iwo kulibe, adachita ziwembu; koma kuononga ziwembu zonsezo nkwa Allah basi. (Iye) akudziwa zimene cholengedwa chilichonse chachita. Ndipo osakhulupirira adzadziwa zotsatira zabwino za Nyumba ya tsiku la chimaliziro kuti zidzakhala zayani

    [43] “Ndipo amene sadakhulupirire akuti iwe sindiwe mtumiki. Nena: “Allah akukwanira kukhala mboni pakati panga ndi pakati panu (kuti ine ndine Mtumiki), ndiponso aja omwe ali ndi nzeru ya m’buku.” (Monga ena mwa Ayuda ndi Akhrisitu omwe adalowa Chisilamu)

    Ibrahimu

    Surah 14

    [1] “Alif-Lâm-Ra. (Ili ndi) buku lomwe talivumbulutsa kwa iwe kuti uwatulutse anthu mu mdima ndi kuwaika mkuunika - mwalamulo la Mbuye wawo - uwapititse kunjira ya Mwini mphamvu zoposa, Woyamikidwa

    [2] “Allah, Yemwe ndi Zake zonse zakumwamba ndi pansi. Ndipo kuonongeka ndi chilango chokhwima kudzatsimikizika pa osakhulupirira

    [3] “Amene akukondetsa moyo wadziko lapansi kuposa moyo wa pambuyo pa imfa, ndipo amatsekereza (anthu) ku njira ya Allah ndikufuna kuikhotetsa (pomwe njirayo njosakhota). Iwo ali mkusokera kotalikana kwambiri (ndi choonadi)

    [4] “Ndipo sitidamtume mtumiki aliyense koma ndi chiyankhulo cha anthu ake kuti awafotokozere. Kenako Allah akumsiya kusokera amene wamfuna (chifukwa mwini wake safuna kuongoka). Ndipo amamuongolera yemwe wamfuna, ndipo Iye Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya

    [5] “Ndipo ndithu tidamtumiza Mûsa ndi zozizwitsa Zathu (tidamuuza): “Achotse anthu ako mu mdima (wa umbuli) ndi kuwaika mkuunika (kwa chikhulupiliro) ndipo uwakumbutse masiku a Allah (a masautso).” Ndithu m’zimenezo muli zizindikiro kwa yense wopirira, wothokoza

    [6] “Ndipo (akumbutse anthu ako) pamene Mûsa adauza anthu ake: “Kumbukirani mtendere wa Allah umene uli pa inu pamene adakupulumutsani kwa anthu a Farawo, omwe adakuzunzani ndi chilango choipa. Ankazinga (kupha) ana anu aamuna ndi kuwasiya amoyo ana anu aakazi; ndithu m’zimenezi mudali mayeso aakulu ochokera kwa Mbuye wanu.”

    [7] “Ndipo (kumbukani) pamene Mbuye wanu adalengeza kuti: “Ngati muthokoza, ndikuonjezerani; ndipo ngati simuthokoza (dziwani kuti) chilango changa nchaukali.”

    [8] “Ndipo Mûsa adati (kwa anthu ake): “Ngati inu mukana (pakusiya kuthokoza) pamodzi ndi onse a m’dziko, (Allah salabadira chilichonse pa zimenezo), ndithudi Allah Ngwachikwanekwane; Ngotamandidwa.”

    [9] “Kodi siidakudzereni nkhani ya omwe adalipo patsogolo panu? Anthu a Nuh, Âdi ndi Samudu? Ndi omwe adadza pambuyo pawo? Omwe palibe akuwadziwa kupatula Allah. Atumiki awo adawadzera ndi umboni oonekera. Koma adabwezera manja awo kukamwa kwawo (kusonyeza kutsutsa), ndipo adati: “Ndithu ife tikuzikana zimene mwatumizidwa nazo, ndipo ife tili mchikaiko pa zimene mukuitanira, ndiponso mchipeneko.”

    [10] “Atumiki awo adati: “Kodi mwa Allah, Mlengi wa thambo ndi nthaka muli chikaiko? Iye akukuitanani kuti akukhululukireni machimo anu, ndi kuti (mukakhulupirira) akupatseni nthawi (pokutalikitsirani moyo wanu) kufikira pa nthawi yoyikidwa.” Adati: “Inu sikanthu kena koma ndinu anthu ngati ife. Mungofuna kutitsekereza ku zimene ankazipembedza makolo athu; choncho tibweretsereni umboni woonekera.”

    [11] “Atumiki awo adati kwa iwo: “(Zoonadi), ife ndife anthu ngati inu, koma Allah amamchitira zabwino yemwe wamfuna mwa akapolo ake. Ndipo ife tilibe nyonga zokubweretserani chisonyezo koma mwachilolezo cha Allah. Ndipo kwa Allah yekha atsamire okhulupirira onse.”

    [12] ““Nanga kwa ife kuli chiyani kuti tisatsamire kwa Allah pomwe watisonyeza njira zathu. Ndipo tipirira pa zimene mukutisautsa nazo. Choncho, kwa Allah Yekha atsamire otsamira.”

    [13] “Ndipo amene sadakhulupirire, adanena kwa atumiki awo: “Ndithu tikutulutsani m’dziko lathu, pokhapokha mubwelere m’chipembedzo chathu.” Koma Mbuye wawo (Allah) adawavumbulutsira uthenga (wakuti): “Ndithu tiwaononga ochita zoipa (osakhulupirira).”

    [14] ““Ndipo tikukhazikani (inu) pambuyo pawo m’dzikomo. Apeza zimenezi omwe aopa kuimilira pamaso pa Ine, ndi kuopa chilango Chnga.”

    [15] “Ndipo (atumikio) adapempha chithandizo (kwa Allah), ndipo adaonongeka aliyense wodzikuza, wamakani

    [16] “(Yemwe) kutsogolo kwake Jahannam ikumdikira, ndipo (kumeneko) adzamumwetsa madzi amafinya (otuluka m’matupi a anthu a ku Moto)

    [17] “Adzakhala akumwa koma movutikira ndipo ululu wa imfa udzamdzera mbali zonse koma sadzafa; ndipo kuonjezera apo, pali chilango (china) chaukali

    [18] “Fanizo la amene sadakhulupirire Mbuye wawo, zochita zawo (zabwino zomwe sadzalipidwa nazo chabwino chilichonse chifukwa chakuti sadazichite pofuna kukondweretsa Allah) zili ngati phulusa lomwe likuulutsidwa ndi mphepo ya mkuntho; ndipo sadzatha kupindula chilichonse pa zimene adachita, uko ndikutaika konka nako kutali (ndi choonadi)

    [19] “Kodi siuona kuti Allah adalenga thambo ndi nthaka mwachoonadi? Ndipo atafuna angakuchotseni (nthawi imodzi) ndikubweretsa zolengedwa zina zatsopano

    [20] “Ndipo zimenezo kwa Allah sizovuta

    [21] “Ndipo onse (adzatuluka m’manda mwawo ndiponso) akaonekera kwa Allah (kuti awalipire). Pamenepo ofooka (omwe adasokera chifukwa chotsatira atsogoleri awo) adzanena kwa omwe ankadzikuza: “Ndithu ife tidali kukutsatirani inu; kodi inu simungathe kutichotsera kanthu kochepa m’chilango cha Allah chi?” (Atsogoleri) adzati: “Allah akadationgolera, tikadakuongolerani; (koma tsopano) ndi chimodzimodzi kwa ife titekeseke ndi chilangochi, kapena tipirire nacho; tilibe pothawira.”

    [22] “Ndipo satana adzanena chiweruzo chikadzalamulidwa (oipa kulowa ku Moto, abwino kulowa ku Munda wamtendere): “Ndithu Allah adakulonjezani lonjezo loona (ndipo wakwaniritsa). Nane ndidakulonjezani, koma sindidakukwaniritsireni. Ndidalibe mphamvu pa inu (yokukakamizirani kunditsata) koma ndimangokuitanani basi, ndipo munkandiyankha. Choncho musandidzudzule, koma dzidzudzuleni nokha. Sindingathe kukuthangatani ndiponso inu simungathe kundithangata. Ndithu ine ndidakukana kundiphatikiza kwanu ndi Allah kale. Ndithu ochita zoipa adzapeza chilango chowawa.”

    [23] “Ndipo amene adakhulupirira ndi kuchita zabwino, adzalowetsedwa ku Minda yomwe pansi (ndi patsogolo) pake mitsinje ikuyenda, adzakhala m’menemo nthawi yaitali mwachilolezo cha Mbuye wawo. Kulonjerana kwawo m’menemo kudzakhala: “Mtendere!”

    [24] “Kodi suona momwe Allah waponyera fanizo (la liwu labwino)? Liwu labwino lili ngati mtengo wabwino (umene) mizu yake njolimba, ndipo nthambi zake zanka kumwamba

    [25] “Umapereka zipatso zake nthawi iliyonse mwachifuniro cha Mbuye wake. (Umo ndi momwe liwu labwino lilili, limabwera ndi zabwino). Ndipo Allah amaponyera anthu mafanizo kuti akumbukire

    [26] “Tsono fanizo la liwu loipa, lili ngati mtengo woipa, umene wazulidwa m’nthaka omwe uli osakhazikika

    [27] “Allah amawalimbikitsa amene akhulupirira ndi mawu olimba m’moyo wa dziko lapansi, ndi moyo wapambuyo pa imfa; ndipo Allah amawalekelera kusokera omwe akudzichitira okha zoipa; ndipo Allah amachita zimene wafuna

    [28] “Kodi sudawaone omwe asintha mtendere wa Allah moukana ndikuwafikitsa anthu awo (omwe adawatsata m’zoipa) kunyumba ya chionongeko

    [29] “(Yomwe ndi) Jahannam; adzailowa; taonani kuipa malo okhazikikapo

    [30] “Ndipo ampangira Allah anzake kuti asokeretse (anthu) kunjira Yake! Nena: “Sangalalani pang’ono chabe! Ndithu kobwerera kwanu nkuMoto!”

    [31] “Auze akapolo Anga amene akhulupirira kuti apemphere Swala ndikupereka zina mwa zomwe tawapatsa, mobisa ndi moonekera lisanawafike tsiku lopanda (chithandizo cha) kudziombola ndi (chithandizo cha) ubwenzi

    [32] “Allah ndi Yemwe adalenga thambo ndi nthaka, ndipo adatsitsa madzi ku mitambo, ndi madziwo adatulutsa zipatso kuti zikhale Rizq lanu (chakudya chanu). Ndipo adakufewetserani zombo kuti ziziyenda pa nyanja mwa lamulo Lake; ndiponso adakufewetserani mitsinje

    [33] “Adakufewetseraninso dzuwa ndi mwezi, mopitilira (nthawi zonse). Ndiponso adakufewetserani usiku ndi usana

    [34] “Ndipo wakupatsani mu zonse zomwe mwampempha (ndi zimene simudam’pemphe). Ngati mutayesa kuwerenga madalitso a Allah, simungathe kuwawerenga. Ndithu munthu ngwachinyengo chachikulu, ngosathokoza

    [35] “Ndipo (kumbukani) pamene Ibrahim adanena: “Mbuye wanga! Uchiteni mzinda uwu (wa Makka) kukhala wa mtendere; ndipo ndipatuleni ine ndi ana anga ku machitidwe opembedza mafano.”

    [36] ““Mbuye wanga! Ndithu (mafano) awa asokeretsa anthu ambiri. Choncho amene wanditsata, ndithu iyeyo ali mwa ine (mudzamulipira chabwino monga mwandilonjeza), ndipo amene wandinyoza (mutha kumukhululukira) ndithu Inu Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni.”

    [37] ““Mbuye wanga! Ndithu ine ndaikhazika ina mwa mbumba yanga (mwana wanga Ismail) pachigwa ichi (cha Makka) chopanda zomera pa Nyumba Yanu Yopatulika (Al-Ka’ba); Mbuye wathu (aloleni) kuti akhale opemphera Swala; choncho ichiteni mitima ya anthu kukhala yopendekera kwa iwo (akonde kudzakhala malo amenewo), ndipo apatseni zipatso kuti athokoze.”

    [38] ““Mbuye wathu! Ndithu Inu mukudziwa zimene tikubisa ndi zomwe tikuonetsa poyera. Ndipo palibe chilichonse chobisika kwa Allah, m’dziko kapena kumwamba

    [39] ““Kuyamikidwa konse nkwa Allah Yemwe wandipatsa ine ku ukulu Ismail ndi Ishâq. Ndithu Mbuye wanga Ngwakumva pempho (la kapolo Wake).”

    [40] ““Mbuye wanga! Ndichiteni kukhala wopemphera Swala pamodzi ndi mbumba yanga. Mbuye wathu! Landirani zopempha zanga.”

    [41] ““Mbuye wathu! Ndikhululukireni ine ndi makolo anga ndi amene akhulupirira, (makamaka) patsiku la chiwerengero (Qiyâma)!”

    [42] “Ndipo usaganize kuti Allah waiwala zomwe akuchita oipa. Ndithudi, Iye akuwalekelera chabe mpaka tsiku lomwe maso awo adzatong’oke (chifukwa cha mantha)

    [43] “(Adzakhala) akuyenda mothamanga mitu ili m’mwamba ndipo maso awo osatha kuphethira, ndipo m’mitima mwawo muli mopanda kanthu (mopanda ganizo lililonse chifukwa cha kudzadzidwa ndi mantha)

    [44] “Ndipo achenjeze anthu za tsiku lomwe chilango chidzawadzera; ndipo amene ankadzichitira okha zoipa adzakhala akunena: “Mbuye wathu! Tichedwetseni kanthawi kochepa (tipatseninso mwawi kuti tibwelere pa dziko); tikayankhe kuitana Kwanu ndi kuwatsata atumiki.” (Adzauzidwa): “Kodi simunkalumbira kale kuti inu simudzachoka (pa dziko)?”

    [45] ““Chikhalirecho mudakhala m’malo mommuja mwa omwe adadzichitira okha zoipa; ndipo kudaonekeratu poyera kwa inu mmene tidawachitira (powaononga); ndipo tidakufotokozerani mafanizo (osiyanasiyana koma inu mudatsutsa).”

    [46] “Ndithudi, adachita ziwembu zawo, koma ziwembu zawo zili kwa Allah (akuzidziwa bwinobwino); ndipo ziwembu zawozo angakhale zitatha kuchotsetsa mapiri (sangamchite kanthu Mtumiki Muhammad (s.a.w} popeza Allah wamteteza

    [47] “Choncho usaganize kuti Allah Ngwakuswa lonjezo Lake kwa atumiki Ake. Ndithu Allah ndi mwini mphamvu (salephera chilichonse), Ngobwezera chilango mwaukali

    [48] “(Likumbukireni) tsiku lomwe nthaka iyi idzasinthidwa kukhala nthaka ina (yachilendo), ndi thambonso (lidzakhala lina), ndipo iwo (anthu onse adzatuluka m’manda mwawo) adzaonekera pamaso pa Allah Mmodzi Wamphamvu (zopanda malire)

    [49] “Ndipo oipa udzawaona tsiku limenelo atanjatidwa ndi unyolo

    [50] “Zovala zawo zidzakhala zaphula, ndipo Moto udzavindikira nkhope zawo

    [51] “Kuti Allah aulipire mzimu uliwonse pa zomwe udakolola; ndithu; Allah Ngwachangu pakuwerengera

    [52] “Izi zikukwana kukhala phunziro kwa anthu kuti achenjezedwe nazo, ndi kuti azindikire kuti Iye (Allah) ndi Mulungu Mmodzi basi, ndikuti eni nzeru akumbukire

    Malo a miyala

    Surah 15

    [1] “۞ Alif-Lâm-Râ. Izi ndi Aaya (ndime) za m’buku (lomwe lasonkhanitsa chilichonse chofunika,) ndi Qur’an yomveka bwino

    [2] “Nthawi zambiri omwe sadakhulupirire (pamene adzakhala m’Moto) adzalakalaka kuti akadakhala okhulupirira (pamoyo wa pa dziko lapansi)

    [3] “Asiye azidya (chakudya monga momwe zidyera nyama) ndi kusangalala; ndipo chiyembekezo chiziwatangwanitsa ndi kuwanyenga; posachedwa adziwa (kuti zimene amaziyembekezerazo nzabodza)

    [4] “Ndipo sitidaononge mudzi uliwonse (m’midzi yochita zoipa) koma udali ndi nthawi yake (youwonongera) yodziwika

    [5] “Ndipo palibe mtundu wa anthu umene ungaitsogolere nthawi yake (yofera) kapena kuichedwetsa (itakwana kale)

    [6] “Ndipo (osakhulupirira) akunena (mwachipongwe) “E iwe amene wavumbulutsiridwa ulaliki! Ndithudi ndiwe wamisala.”

    [7] ““Bwanji iwe osatibweretsera angelo (kuti akuchitire umboni) ngati uli mmodzi waonena zoona?”

    [8] “(Allah akuwauza:) “Ife sititsitsa angelo pokhapokha kutatsimikizika (tikawatuma kukapereka chilango kwa anthu). Ndipo pamenepo sangapatsidwe nthawi.”

    [9] “Ndithu Ife ndife omwe tavumbulutsa Qur’an, ndipo ndithudi, tiisunga

    [10] “Ndithudi tidatuma (atumiki) patsogolo pako m’magulu (a anthu) akale, oyamba

    [11] “Ndipo sadali kuwadzera mtumiki aliyense, koma ankamchitira chipongwe

    [12] “Momwemo tikuupititsa (mkhalidwe wachipongwewu) m’mitima mwa oipa

    [13] “Koma saikhulupirira Qur’aniyi chikhalirecho mafanizo a anthu oyamba awadutsa (ndipo aona momwe tidawaonongera)

    [14] “Ndipo tikadawatsekulira (awa osakhulupirira) khomo lakumwamba ndipo nkukhala akukwera m’menemo (ndi kutsika monga momwe amafunira kuti zimenezo zikhale chozizwitsa cha Mtumiki)

    [15] “Akadati: “Ndithu maso athu aledzera; (iyayi) koma ndife anthu olodzedwa (tikuona zomwe sindizo).”

    [16] “Ndithudi, kumwamba tidaikako “Buruji” (njira momwe zikuyendamo nyenyezi) ndipo tidakukongoletsa kwa okuwona

    [17] “Ndipo tidakuteteza kwa satana aliyense wopirikitsidwa (kumwambako akafuna kukamvetsera zimene zikunenedwa kumeneko)

    [18] “Kupatula amene amamvetsera mobera; ndipo pompo chinsakali chamoto choonekera chimamtsata

    [19] “Ndipo nthaka tidaiyala ndi kuikamo mapiri ndipo tameretsa mmera wa chinthu chilichonse m’menemo mwamlingo (wake)

    [20] “Ndipo mmenemo takupangirani zinthu zoyendetsa moyo (wanu zakudya ndi zakumwa ndi zina zotere) ndiponso (tidakupatsani ana ndi ziweto) zomwe inu simungathe kuzidyetsa. (Ife ndife amene tikuzikonzera chakudya chawo, osati inu)

    [21] “Ndipo palibe chinthu chilichonse koma gwero lake likuchokera kwa Ife; ndipo sitichitsitsa koma mwamlingo wodziwika (osati mwachisawawa)

    [22] “Ndipo timazitumiza mphepo zitasenza madzi, ndipo madziwo tikuwatsitsa kuchokera kumitamboyo; kenako tikukumwetsani madziwo (tikukumwetseraninso ziweto zanu, mitengo yanu ndi zina), ndipo inu si amene mukuwasunga (madziwo)

    [23] “Ndipo ndithudi, Ife ndife omwe timapereka moyo, ndi kupereka imfa. Ndiponso Ife ndi Amlowam’malo (a chinthu chilichonse chimene chikusiidwa chopanda mwini)

    [24] “Ndipo ndithu tikuwadziwa mwa inu amene atsogola (amene adafa kale), ndipo ndithu tikuwadziwanso amene atsalira (ali ndi moyobe ndi amene sanabadwe)

    [25] “Ndipo ndithu palibe chikaiko, Mbuye wako ndi Yemwe adzawasonkhanitsa (pambuyo pa imfa kuti adzawaweruze). Iye ndi Wanzeru zakuya, Wodziwa chilichonse

    [26] “Ndipo ndithu tidamlenga munthu ndi dongo louma lolira lochokera ku matope odera, osinthika mtundu

    [27] “Ndipo ziwanda tidazilenga kale ndi moto wamphepo yotentha kwambiri

    [28] “Ndipo (kumbuka) pamene Mbuye wako adauza angelo (kuti): “Ndithu Ine ndilenga munthu ndi dongo louma lolira lochokera ku matope odera osinthika mtundu.”

    [29] ““Choncho ndikamkwaniritsa ndikumuuzira mzimu wolengedwa ndi Ine, muweramireni momulemekeza.’’

    [30] “Choncho angelo onse adamuweramira

    [31] “Kupatula Iblis; adakana kukhala mmodzi mwa owerama

    [32] “Allah adati: “E iwe Iblis! Chifukwa ninji sudakhale pamodzi ndi owerama?”

    [33] “Adati: “Sindingamuweramire munthu yemwe mwam’lenga ndi dongo louma lolira lochokera ku matope odera osinthika mtundu.”

    [34] “(Allah) adati: “Choncho choka m’menemo; ndithu iwe ndiwe wopirikitsidwa (ku chifundo Changa).”

    [35] ““Ndipo ndithu matembelero ali pa iwe mpaka tsiku lamalipiro.”

    [36] “(Iblis) adati: “Mbuye wanga choncho ndipatseni nthawi mpaka tsiku limene adzaukitsidwe kwa akufa.”

    [37] “(Allah) adati: “Ndithu iwe ndi mmodzi mwa opatsidwa nthawi (danga).”

    [38] “Kufikira tsiku la nthawi yodziwika (ikadzafika nthawi imeneyo, udzafa).”

    [39] “(Satana) adati: “Mbuye wanga! Pakuti mwanena kuti ndine wosokera, choncho ndikawakometsera za m’dziko (kufikira kuti akakulakwireni), ndithu ndikawasokeretsa onse.”

    [40] ““Kupatula akapolo anu oyeretsedwa, mwa iwo.”

    [41] “(Allah) adati: “Iyi ndinjira yoongoka yobwerera kwa Ine (ndipo adzandidzera akadzafuna).”

    [42] “Ndithudi akapolo Anga pa iwo sudzakhala ndi mphamvu kupatula okutsata (mwachifuniro chawo) mwa opotoka.”

    [43] “Ndithu Jahannam ndiwo malo awo olonjezedwa kwa onse

    [44] “Ili ndi makomo asanu ndi awiri; khomo lililonse lili ndi gawo logawidwa mwa iwo

    [45] “Ndithudi owopa Allah adzakhala m’minda ndi akasupe (omwe adzakhala patsogolo pawo)

    [46] “(Ndipo tidzawauza) “Lowani m’menemo mwamtendere, mosatekeseka.”

    [47] “Ndipo tidzawachotsera mfundo za chidani zomwe zidali m’mitima mwawo; (adzakhala) mwachibale, (mokondana,) atakhala pa mipando yachifumu atayang’anizana nkhope

    [48] “Mmenemo masautso sakawakhudza, ndiponso sadzatulutsidwamo

    [49] “Auze akapolo anga kuti ndithu Ine ndine Wokhululuka kwambiri, Wachisoni chosatha

    [50] “Ndipo ndithu chilango Changa ndi chilango chopweteka zedi

    [51] “Ndipo auze nkhani ya alendo a (Mneneri) Ibrahim

    [52] “Pamene adalowa kwa iye ndikunena: “Salaman (Mtendere!)” (Iyenso adawayankha: “Mtendere ukhalenso pa inu.” Ndipo Pamene adaona kuti akana chakudya) Adati: “Ndithu ife tikukuopani.”

    [53] “Iwo adati: “Usaope! Ife tikukuuza nkhani yabwino ya (kuti ubala) mwana wanzeru kwambiri.”

    [54] “Iye adati: “Ha! Mukundiuza nkhani iyi pomwe ukalamba wandifikira? Kodi nkhani yabwinoyi mukundiuza mnjira yotani?”

    [55] “Iwo adati: “Takuuza nkhani yabwinoyi mwachoonadi; choncho, usakhale mwa otaya mtima.”

    [56] “Iye adati: “(Ine sinditaya mtima ndi chifundo cha Allah. Ndipo) palibe angataye mtima ndi chifundo cha Allah, koma wosokera basi (yemwe sazindikira ukulu wa Allah).”

    [57] “Iye adati: “Nanga cholinga chanu china nchiyani, E inu otumidwa?”

    [58] “Iwo adati: “Ife tatumidwanso kwa anthu aja oipa (kuti tikawaononge).”

    [59] ““Kupatula akubanja la Luti, ndithu ife tikawapulumutsa onse.”

    [60] ““Koma mkazi wake (wa Luti), tamkonzera kukhala mmodzi wa otsalira pambuyo.”

    [61] “Ndipo pamene atumikiwo adawadzera anthu a Luti (ali mmaonokedwe amunthu)

    [62] “(Luti) adati: “Ndithudi, inu ndi anthu osadziwika (sitikudziwani).”

    [63] “Iwo adati: “Inde, ife takudzera ndi zomwe (iwo) adali kuzikaikira, (zomwe ndi chilango chawo).”

    [64] ““Ndipo tadza kwa iwe ndi (chinthu) choonadicho, ndithu ife ndi owona (pazimene tinenazi).”

    [65] ““Choncho, choka ndi banja lako mkati mwa usiku; ndipo iwe udziwatsata pambuyo pawo; tsono aliyense wa inu asayang’ane kumbuyo (akamva mkokomo wachilango chochokera kumwamba, kuopa kuti angafe), ndipo yendani (mwachangu) kunka komwe mukulamulidwa.”

    [66] “Ndipo tidamudziwitsa iyeyo (Luti) lamulo lathu lakuti ndithu phata lawo anthu (ochimwawo) lidzadulidwa kum’banda kucha

    [67] “Ndipo adadza (kwa Luti) anthu a m’mudziwo akusangalala (poona kuti kwadza alendo okongola kuti achite nawo zadama)

    [68] “(Mneneri Luti) adati: “Ndithu awa ndialendo anga; choncho musandiyalutse (pochita nawo zadama).”

    [69] ““Muopeninso Allah, ndipo musandichititse manyazi (pamaso pawo).”

    [70] “Iwo adati (kwa Mneneri Luti): “Kodi sitidakuletse kulandira anthu (achilendo)?”

    [71] “Iye adati: “Awa (akazi onsewa ali ngati) ana anga. Ngati inu ndinu ochita (chimene chalamulidwa, akwatireni; musachite zauve ndi alendowa).”

    [72] “Ndikulumbira moyo wako, ndithu iwo m’kuledzera kwawo (ndi zoipa) akungoyumbayumba

    [73] “Choncho mkuwe wa chilango udawagwira pamene dzuwa linkatuluka

    [74] “Choncho (midziyo) tidaigadabula kumwamba kukhala pansi, (pansi kukhala kumwamba); ndipo tidawavumbwitsira mvula yamiyala (yotentha) ya moto

    [75] “Ndithudi, (m’nkhani iyi) muli malingaliro (aakulu) kwa anthu olingalira zinthu

    [76] “Ndipo (midzi) iyi (yomwe tidaiwononga chotereyi), ili chikhalire m’njira moyenda anthu (ndipo iwo akuona zizindikiro zake)

    [77] “Ndithudi, mzimenezi muli phunziro (lalikulu) kwa okhulupirira

    [78] “Ndipo ndithu anthu a m’nkhalango (anthu a Mneneri Shuaib) adali ochita zoipa kwabasi

    [79] “Choncho, tidawalanga. Ndipo (maiko) awiriwa ali m’njira zoonekera, (momwe Aquraish amadutsa pa maulendo awo)

    [80] “Ndipo ndithu okhala m’chigwa cha Hijr (Asamuda), Adatsutsa atumiki

    [81] “Tidawapatsa zisonyezo zathu, koma sadazilabadire

    [82] “Iwo adali kujoba nyumba m’mapiri mwamtendere (ankaboola mapiri kuwasandutsa nyumba zawo)

    [83] “Choncho, chiphokoso cha chilango chidawapeza m’mawa

    [84] “Sichidawathandize (chuma) chomwe ankachipeza (ngakhalenso zimene ankazichita)

    [85] “Sitidalenge thambo ndi nthaka ndi (zonse) zapakati pake koma (kulimbikitsa) choonadi. Ndipo palibe chikaiko, Qiyâma idza. Choncho mkhululukire kukhululuka kwabwino (aliyense wokuchitira zoipa)

    [86] “Ndithudi, Mbuye wako, Iye ndi Mlengi wa zonse, Wodziwa kwambiri

    [87] “Ndipo ndithu takupatsa (Ayah izi) zisanu ndi ziwiri zomawerenga kawirikawiri, (Sûrat Al-Fatihah), ndi Qur’an yolemekezeka

    [88] “Usatong’olere maso ako (kuyang’ana) zimene tawasangalatsa nazo mitundumitundu ya mwa iwo (monga chuma cha anthu osakhulupirira). Usawadandaulirenso iwo ndipo tsitsa phiko lako kwa okhululupirira, (uwafungatire)

    [89] “Ndipo nena: “Ndithu ine ndine mchenjezi woonekera (sindikubisa chilichonse kuopera kuti chingakutsikireni chilango).”

    [90] “Monga momwe tidatsitsira (chilango) kwa amene adadzigawa m’magulu

    [91] “Omwe aichita Qur’an kukhala magawomagawo; (zina nkuzikhulupirira, zina nkuzitsutsa)

    [92] “(Allah akudzilumbilira kuti:) Pali Mbuye wako, tidzawafunsa onse (tsiku la Qiyâma)

    [93] “Pazimene ankachita (padziko lapansi)

    [94] “Choncho, lengeza zimene ukulamulidwa, ndipo uwapewe opembedza mafano, (usaope chilichonse kwa iwo)

    [95] “Ndithu Ife tikukwanira kukuteteza ku (zoipa za) achipongwe

    [96] “Omwe akupanga milungu ina ndi kuiphatikiza ndi Allah, posachedwapa adziwa (zotsatira zake)

    [97] “Ndithu Ife tikudziwa kuti chifuwa chako chikubanika ndi zimene akunenazo

    [98] “(Koma pirira), lemekeza Mbuye wako pamodzi ndi kumtamanda (ndi rnbiri Zake zabwino) ndipo khala mwa olambira (Allah)

    [99] “Ndipo mpembedze Mbuye wako mpaka chikufike chitsimikizo (imfa)

    Njuchi

    Surah 16

    [1] “Lamulo la Allah lidzafika, (ndithu) choncho, musalifulumizitse; (ndipo khulupirirani kuti Iye ndi Allah) Woyera Wopatukana ndi mbiri zopunguka, ndipo watukuka ku zomwe akumphatikiza nazo

    [2] “Amatumiza angelo pansi pamodzi ndi chivumbulutso mwa lamulo Lake (Allah), kwa omwe wawafuna mwa akapolo Ake (powauza) kuti: “Achenjezeni (anthu zakuti): ‘Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Ine ndekha, choncho ndiopeni.”

    [3] “Adalenga thambo ndi nthaka mwachoonadi (osati mwakungoseweretsa chabe) ndipo watukuka kuzimene akumphatikiza nazo (ophatikiza Allah ndi mafano)

    [4] “Adalenga munthu kuchokera ku dontho la umuna. Ha! kenaka iye (munthuyo) wakhala wotsutsana naye (Allah) woonekera

    [5] “Ndipo adalenga ziweto (monga ngamira, ng’ombe ndi mbuzi) mwa izo mukupeza zofunda, ndi zothandiza (zina zambiri), ndipo zina mwa izo mumazidya

    [6] “Ndipo mumakondwa ndi kunyadira chifukwa cha kukongola kwa izo mukamabwera nazo (kuchokera kubusa mimba zitakhuta), ndi popita nazo (kubusa zikuyenda mwandawala)

    [7] “Ndipo zimasenza mitolo yanu (yolemera) kukafika nayo ku midzi yakutali komwe simumatha kukafikako popanda kuvutika kwambiri. Ndithu Mbuye wanu Ngodekha kwabasi, Ngwachisoni zedi

    [8] “(Adalenganso) akavalo, nyumbu ndi abulu kuti muzizikwera ndi kutinso zizikhala chokometsera chanu (cholowetsa chisangalalo m’mitima yanu); ndipo adzalenga (zokwera zina) zomwe simukuzidziwa

    [9] “Ndipo ndi udindo wa Allah kusonyeza njira yolungama (yomwe ingakufikitseni ku Munda wamtendere), koma zilipo njira zina zokhota (zomwe sizifikitsa ku choonadi). Ndipo Allah akadafuna, akadakuongolani nonsenu (mwa chifuniro chanu ndi mopanda chifuniro chanu. Koma Iye adakupatsani nzeru kuti musankhe nokha njira imene mufuna)

    [10] “Iye ndi Amene akukutsitsirani madzi kuchokera ku mitambo, madziwo mumamwa (pothetsa ludzu lanu), ndipo ndi madziwo mitengo imamera; mitengo yomwe mumadyetsera ziweto (zanu)

    [11] “Ndi madzi omwewo amakumeretserani mmera, (mitengo ya) mzitona, kanjedza, mphesa, ndi mitundu ina yonse ya zipatso. Ndithu kupezeka kwa zimenezi ndi chisonyezo (chosonyeza mphamvu za Allah) kwa anthu olingalira

    [12] “Ndipo chifukwa cha inu adagonjetsa usiku ndi usana; dzuwa ndi mwezi; (zonse zidalengedwa kuti zibwere ndi zokomera inu). Nazo nyenyezi zidagonjetsedwa mwa lamulo Lake. Ndithu m’zimenezi muli zizindikiro kwa anthu anzeru

    [13] “Ndiponso ndi zimene adakulengerani m’nthaka (zinthu zododornetsa monga nyama, mmera, miyala yamtengo wapatali, zamoyo ndi zopanda moyo), zautoto wosiyanasiyana ndi maonekedwe osiyanasiyana; ndithu m’zimenezo muli zisonyezo kwa anthu olalikika

    [14] “Ndipo Iye ndi Yemwe adagonjetsa nyanja kuti mudye nyama yamatumbi (ya) m’menemo (nsomba) ndikuti mutulutse m’menemo zodzikongoletsera zomwe mumavala; ndipo uona zombo zikuluzikulu zikung’amba (mafunde) m’menemo kuti mufunefune zabwino zake (njira ya malonda), ndi kuti muthokoze (Mbuye wanu Allah)

    [15] “Ndipo adaika panthaka mapiri ataliatali kuti (nthaka) isagwedezeke nanu; ndipo (adaika) mitsinje ndi misewu kuti muongoke (potsata njira yeniyeni ndikukafika komwe mukufuna)

    [16] “Ndipo (adaikanso) zizindikiro zina, ndiponso kupyolera m’nyenyezi, iwo amalondola njira

    [17] “Kodi Yemwe amalenga angalingane ndi omwe salenga? Kodi simungakumbukire (ndikudziwa kulakwa kwanu pomuyerekeza Allah ndi mafano)

    [18] “Ngati mutayesera kuwerengera mtendere wa Allah simungathe kuuwerengera (wonse); ndithudi, Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha

    [19] “Ndipo Allah akuzidziwa zimene mukuzibisa, ndi zomwe mukuwonetsera

    [20] “Ndipo zomwe mukuzipembedza kusiya Allah, sizilenga chilichonse, ndipo izo nzolengedwa

    [21] “Zakufa zopanda moyo; ndipo sizizindikira kuti nliti akufa adzaukitsidwa (m’manda mwawo)

    [22] “Mulungu wanu ndi Mulungu Mmodzi Yekha; koma amene sakhulupirira za tsiku la chimaliziro, mitima yawo ikukana (kukhulupirira umodzi wa Allah), ndipo iwo akudzitukumula

    [23] “Palibe chikaiko, Allah akudziwa zomwe akubisa, ndi zomwe akuzilengeza. Ndithudi, Iye sakonda odzikuza

    [24] “Ndipo (osakhulupirira) akafunsidwa: “Kodi Mbuye wanu watumizanji (kwa Mneneri Muhammad {s.a.w})?” Akunena: “(Sadatumize chilichonse koma) nthano zabodza za anthu akale.”

    [25] “(Motero akuwasokeretsa anthu) kuti akasenze mitolo yawo (ya machimo) yokwanira pa tsiku la Qiyâma, ndiponso gawo lamitolo ya omwe akuwasokeretsa popanda kuzindikira (osokerawo). Tamverani! Ndi yoipa kwabasi mitolo yomwe azikaisenza

    [26] “Adachita ndale omwe adalipo patsogolo pawo; choncho Allah adagumula maziko anyumba zawo. Ndipo madenga adawagwera pamwamba pawo; ndipo chilango chidawadzera kuchokera komwe sadali kukudziwa

    [27] “Kenako tsiku la Qiyâma adzawayalutsa ndi kunena: “Ali kuti omwe mudali kundiphatikiza nawo, omwe chifukwa cha iwo mudali kukangana (ndi Mtumiki)?” Adzanena omwe apatsidwa nzeru: “Ndithu kuyaluka ndi tsoka loipa zili pa osakhulupirira lero.”

    [28] “Omwe angelo akutenga miyoyo yawo atadzichitira okha zoipa (ponyoza Allah). Choncho adzadzipereka (kwa angelowa, kuti atenge miyoyo yawo akunena:) “Sitidali kuchita choipa chilichonse.” (Angelo adzati:) “Zoona, palibe chikaiko, Allah akudziwa kwambiri zomwe munkachita.”

    [29] ““Choncho, lowani makomo a ku Jahannam; mukakhala m’menemo nthawi yaitali.” Taonani kuipitsitsa kwa malo a anthu odzikweza

    [30] “Ndipo kukanenedwa kwa omwe akuopa Allah (kuti): “Kodi nchiyani watumiza Mbuye wanu?” Amati: “Zabwino.” Kwa omwe achita zabwino padziko ili lapansi, awapatsanso zabwino, ndipo Nyumba ya tsiku la chimaliziro njabwino kwambiri, ndipo taonani ubwino wa Nyumba ya oopa (Allah)

    [31] “Minda yamuyaya adzailowa, pansi pake padzakhala pakuyenda mitsinje (ndi patsogolo pake), chokhumba chilichonse akachipeza mmenemo (popanda kuchivutikira); umo ndi momwe Allah amawalipirira omuopa (iye)

    [32] “Amene miyoyo yawo angelo amaitenga iwo ali abwino, uku akuwauza: “Mtendere uli pa inu, lowani ku Munda wamtendere chifukwa cha (zabwino) zija zomwe mudali kuzichita.”

    [33] “Kodi akuyembekezera china, awa osakhulupirira, posakhala kuti angelo awadzere ndikuwaononga; kapena kuti liwadzere lamulo la Mbuye wako (lakuwalanga)? Momwemo ndi m’mene adachitiranso omwe adalipo patsogolo pawo. Koma Allah sadawachitire choipa koma adadzichitira okha choipa

    [34] “Choncho, zoipa za zomwe adachita zidawapeza, ndipo chilango chidawazinga pa zomwe ankazichita mwachipongwe

    [35] “Ndipo aja amapembedza mafano akuti: “Allah akadafuna, sitikadapembedza chilichonse kusiya Iye, ife ngakhale makolo athu; ndiponso palibe chomwe tikadachiyesa choletsedwa popanda lamulo Lake.” Momwemo ndimo adachitiranso aja omwe adalipo patsogolo pawo. Kodi atumiki ali ndi udindo winanso, osati kufikitsa uthenga woonekera (womveka)

    [36] “Ndipo ndithu ku mtundu uliwonse tidatumiza mtumiki (amene amawauza kuti): “Pembedzani Allah, ndi kumpewa (Iblis) woipa.” Choncho alipo ena mwa iwo omwe Allah adawaongola, ndipo alipo ena mwa iwo omwe kusokera kudatsimikizika pa iwo. Choncho yendani pa dziko ndikuyang’ana (kuti) kodi adali bwanji mathero a otsutsa

    [37] “Ngati uwumilira kwambiri kuti uwaongole, komatu Allah saongola yemwe akusokeretsa (ena), ndipo sadzapeza wowathangata

    [38] “Ndipo iwo adalumbilira m’dzina la Allah, kulumbilira kwawo kwamphamvu (kuti) Allah sadzaukitsa amene afa; nchotani (kuti asawaukitse?) Ili ndi lonjezo lokakamizika kwa Iye, (kuwaukitsa ndi kuwalipira); koma anthu ambiri sadziwa

    [39] “(Adzawaukitsa) kuti awafotokozere za zomwe adali kusiyana ndi kuti amene sadakhulupirire adziwe kuti ndithu iwo adali abodza

    [40] “Ndithu liwu Lathu pa chinthu chimene tikuchifuna kuti chichitike ndikuchiuza basi kuti: “Chitika,” ndipo chimachitikadi

    [41] “Ndipo omwe adasamuka chifukwa cha Allah (kusiya midzi yawo) pambuyo poponderezedwa (kumeneko,) ndithu tiwakhazika mwaubwino pa dziko lapansi; ndipo malipiro a tsiku la chimaliziro (omwe akuwayembekezera), ngakulu zedi, akadakhala akudziwa (awa oipa)

    [42] “(Amene adzapeza zimenezi, ndi) omwe adapirira ndi kutsamira kwa Mbuye wawo

    [43] “Ndipo patsogolo pako (aneneri) omwe tidawatuma adalinso amuna, omwe tidawavumbulutsira chivumbulutso. Choncho afunseni eni chikumbumtima (za m’mabuku a Allah akale) ngati inu simukudziwa

    [44] “(Tidabwera) ndi zisonyezo zoonekera pamodzi ndi mabuku; ndipo takuvumbulutsira ulaliki kuti uwafotokozere anthu zomwe zavumbulutsidwa kwa iwo kuti aganizire

    [45] “Kodi adziika pachitetezo, amene akuchita ndale zoipa, kuti Allah sangawakwilire ndi nthaka, kapena chilango kuwadzera kuchokera komwe sadali kukudziwa (sadali kukuyembekezera)

    [46] “Kapena (Allah) kuwalanga mkuyenda kwawo kwa uku ndi uko? Pomwe iwo sangathe kumulepheretsa Allah kuchita chomwe wafuna pa iwo

    [47] “Kapena kuwalanga uku ali ndi mantha oyembekezera chilango (pakulanga m’modzim’modzi kufikira onse atatha)? Ndithu Mbuye wanu Ngodekha Ngwachisoni chosatha

    [48] “Kodi sadaone chinthu chilichonse (molingalira) m’zimene Allah adalenga zomwe zithuzi zake zimazungulira kudzanjadzanja ndi kumanzere, kulambira Allah uku zili zodzichepetsa kwa Iye? (Nanga iwo osakhulupirira akudzikweza chotani pamaso pa Allah)

    [49] “Ndipo zimalambira Allah zonse za kumwamba ndi zapansi, nyama ndi angelo; iwo sadzikuza (pa mapemphero)

    [50] “Amaopa Mbuye wawo Yemwe ali pamwamba pawo; ndipo amachita zokhazo zomwe alamulidwa

    [51] “Ndipo Allah wanena: “Musadzipangire milungu ina iwiri. Ndithudi, Iye ndi Mulungu Mmodzi. Choncho opani Ine ndekha.”

    [52] “Zonse zakumwamba ndi pansi nza Iye, ndipo kumumvera ndi kumugonjera nkwake nthawi zonse. Kodi muopa wina amene sali Allah

    [53] “Ndipo mtendere wonse umene muli nawo udachokera kwa Allah (koma inu simuthokoza), ndipo masautso akakukhudzani Iye ndi amene mumamulilira

    [54] “Koma akakuchotserani masautso, pompo gulu lina la mwa inu limamphatikiza Mbuye wake (ndi mafano)

    [55] “Ncholinga choti akane mtendere umene tawapatsa, choncho sangalalani pang’ono, posachedwapa mudziwa (mapeto a zochita zanu)

    [56] “Ndipo gawo la zomwe tawapatsa akuliikira (milungu yawo yabodza) yomwe siizindikira chilichonse. Tallahi, (ndikulumbira Allah,) ndithudi, mudzafunsidwa pa zimene munkapeka

    [57] “Ndipo (mwaumbuli) akumuikira Allah ana aakazi (ponena kuti adabereka ana aakazi) Subuhana! (Wayera Allah kuzimenezi!) Ndipo iwo (eni) amadzifunira amene amawakonda (omwe ndi ana achimuna)

    [58] “Ndipo mmodzi wawo akauzidwa nkhani ya (kuti wabereka) mwana wamkazi nkhope yake imada, ndipo amadzala ndi madandaulo

    [59] “Amadzibisa kwa anthu chifukwa chankhani yoipa imene wauzidwa (nayamba kulingalira): Kodi akhale naye pamodzi ndikuyaluka (pamaso pa anthu), kapena angomkwilira m’dothi (ali moyo)? Mverani! Ndi choipa kwabasi chiweruzo chawo

    [60] “Kwa awo amene sakhulupirira za tsiku la chimaliziro, ali ndi mbiri yoipa; koma Allah ali ndi mbiri zapamwamba; ndipo Iye Ngwanyonga, Ngwanzeru zakuya

    [61] “Ndipo Allah akadakhala akulanga anthu (mwachangu) pa zolakwa zawo, sakadasiya ngakhale nyama imodzi pamwamba pa nthaka; koma akuwachedwetsera (chilangocho) mpaka panthawi yoikidwa; ndipo ikadzadza nthawi yawoyo, sangathe kuichedwetsa ngakhale ola limodzi; ndiponso sangathe kuifulumizitsa (ngakhale ola limodzi)

    [62] “Ndipo akumuikira Allah zimene (iwo) akuzida (omwe ndi ana aakazi pomati Allah adabala ana aakazi), ndipo malirime awo akunena bodza kuti iwo adzapeza zabwino (kwa Allah); palibe chikaiko, ndithu Moto ndi wawo, ndipo iwo adzasiidwa (mmenemo)

    [63] “Pali Mulungu! Ndithudi tidatumiza (atumiki) kumitundu yomwe idalipo patsogolo pako, koma satana adawakometsera zochita zawo (zoipa ankaziona kuti nzabwino napitiriza kuzichita). Choncho iye (satana) ndi bwenzi wawo lero, (koma pa tsiku la chimaliziro, adzadana naye kwambiri), ndipo iwo adzapata chilango chowawa

    [64] “Ndipo sitidakutumizire buku (ili) koma kuti uwafotokozere zomwe akusiyana pa izo ndi kuti (likhale) chiongoko ndi chifundo kwa anthu okhulupirira

    [65] “Ndipo Allah watsitsa madzi kuchokera ku mitambo, ndipo akuipatsa moyo nthaka ndi madziwo (pomeretsa mbewu) pambuyo poti nthakayo idali yakufa; ndithu m’zimenezo muli chisonyezo (chosonyeza kukhoza kwa Allah) kwa anthu amene amamva

    [66] “Palibe chikaiko, m’ziweto muli phunziro ndi lingaliro kwa inu. Timakumwetsani zomwe zili m’mimba mwa izo, (zomwe zimatuluka) pakati pa ndowe ndi magazi, (omwe ndi) mkaka woyera, wabwino wokoma kwa oumwa

    [67] “Ndipo kuchokera ku zipatso za tende ndi mphesa, mumakonza zakumwa zoledzeretsa (zomwe nzoletsedwa) ndikupezanso rizq labwino (m’zipatsozo); ndithudi m’zimenezo muli lingaliro kwa anthu oganiza mwanzeru

    [68] “Ndipo Mbuye wako adaizindikiritsa njuchi kuti: “Dzikonzere nyumba m’mapiri, m’mitengo, ndi (m’ming’oma) imene (anthu) amakonza.”

    [69] ““Tsono idya zipatso zamtundu uliwonse ndikuyenda m’njira za Mbuye wako zimene wazifewetsa (kuziyenda).” Chimatuluka m’mimba mwake chakumwa cha utoto wosiyanasiyana (uchi), mwa icho muli kuchilitsa kwa anthu (kumatenda ochuluka), ndithu m’zimenezo muli zizindikiro kwa anthu oganiza (zinthu) mwakuya

    [70] “Ndipo Allah adakulengani, kenako akukupatsani imfa (nthawi ya moyo wanu ikatha); ndipo mwa inu alipo ena amene akubwezedwa ku moyo wonyozeka (waukalamba wogwa nkumina) kotero kuti asadziwe kanthu pambuyo pakudziwa (zambiri); ndithudi Allah Ngodziwa kwambiri Wokhoza (chilichonse chimene wafuna kuti chichitike)

    [71] “Ndipo Allah wapereka zopereka Zake mochuluka kwa ena kuposa ena; ndipo amene apatsidwa mochulukawo sangagawire zopatsidwa zawo omwe manja awo adzanjadzanja apeza (akapolo awo) kuti akhale ofanana pa zopatsidwazo, (nanga bwanji inu mukuti Allah ngofanana ndi akapolo Ake pomwe inu simufuna kufanana ndi akapolo anu?) Nanga kodi mtendere wa Allah akuukana

    [72] “Ndiponso Allah adakulengerani akazi a mtundu wanu, ndipo adakupangirani ana ndi zidzukulu kuchokera mwa akazi anuwo; ndipo adakupatsani zinthu zabwinozabwino, kodi akukhulupirira zachabe, ndi kuchikana chisomo cha Allah

    [73] “Ndipo akumusiya Allah ndikupembedza zomwe sizingawapezere zopatsa ngakhale pang’ono, zochokera kumwamba ndi pansi ndipo sizikhoza chilichonse

    [74] “Choncho, musaponyere mafanizo Allah. Ndithudi Allah akudziwa, pomwe inu simudziwa (chinsinsi cha zinthu)

    [75] “Allah akuponya fanizo la (anthu awiri: Wina ndi) kapolo wopatidwa (wokhala pansi pa ulamuliro wa munthu wina); yemwe alibe mphamvu pa chilichonse; ndi (munthu) yemwe tampatsa zabwino zochokera kwa Ife, ndipo iye nkupereka rizqlo mobisa ndi moonekera; kodi angafanane (awiriwa? Nanga bwanji mukufananitsa Allah ndi mafano?) Kuyamikidwa konse nkwa Allah. Koma ambiri aiwo sadziwa (kuyamika Allah)

    [76] “Ndipo Allah waponyanso fanizo la anthu (ena) awiri: Mmodzi ndi bubu (wosatha kuyankhula), alibe mphamvu pa chilichonse; ndipo iye ndi mtolo wolemetsa chabe bwana wake; kulikonse kumene wamulunjikitsa, sabwerako ndi chabwino (chifukwa cha umbutuma wake). Kodi iye angafanane ndi yemwe akulamula mwa chilungamo, yemwenso ali pa njira yolunjika

    [77] “Ndipo chinsinsi cha (za) kumwamba ndi (za) pansi ncha Allah Yekha, (Iye ndiye amene akudziwa zochitika m’menemo, osati wina wake). Ndipo kuchitika kwa Qiyâma kuli ngati kuphetira kwa diso, kapena kufulumilirapo. Ndithudi, Allah Ngokhoza chilichonse

    [78] “Ndipo Allah adakutulutsani m’mimba mwa amayi anu pomwe simudali kudziwa chilichonse; ndipo adakupatsani kumva, kuona ndi mitima kuti muthokoze

    [79] “Kodi saona mbalame mu mlengalenga zikugonjera (Allah)? Palibe amene akuzigwira (kuti zisagwe) koma Allah Yekha. Ndithudi m’zimenezo muli zizindikiro kwa anthu okhulupirira

    [80] “Ndipo Allah adakuikirani nyumba zanu kuti zikhale mokhala (mwanu), ndiponso adakupangirani zikopa za ziweto (kukhala zotheka kuzikonza) kukhala nyumba, zomwe mumaziona kuti nzopepuka kuzitenga panthawi Ya ulendo wanu ndi panthawi ya kukhazikika kwanu (pamalo); ndipo kuchokera ku bweya wake wautaliutali ndi bweya wake wa manyunyu (ung’onoung’ono), ndi tsitsi lake (la ziwetozo,) mumakonza ziwiya (zovala) zosangalatsa, kwa kanthawi

    [81] “Ndipo mwa zina zomwe Allah adapanga, adakupangirani zodzetsa mthunzi; ndipo adakupangirani mokhala kumapiri (monga mapanga akuluakulu). Adakupangiraninso nsalu (zathonje ndi ubweya) zokutetezani ku kutentha (ndi kuzizira), ndiponso (adakupangirani) zovala (za chitsulo) zokutetezani pankhondo zanu. Umo ndi momwe akukukwaniritsirani chisomo Chake kuti mugonjere (Iye)

    [82] “Koma ngati anyoza, basi palibe udindo wina pa iwe koma kufikitsa uthenga womveka (popanda kubisapo kalikonse)

    [83] “Akuchidziwa chisomo cha Allah; koma akuchikana, ndipo ambiri a iwo ngosakhulupirira

    [84] “Ndipo (akumbutse za) tsiku lomwe tidzautsa mboni mu mtundu uliwonse; kenako sikudzaloledwa, kwa amene sadakhulupirire, (kupereka madandaulo) ndipo iwo sadzauzidwa kuti afunefune chiyanjo cha Allah (koma chilango basi)

    [85] “Ndipo amene achita zoipa akadzachiona chilango (ndikuyamba kudandaula ndi kulira), sichidzachepetsedwa kwa iwo (chilangocho), ndipo sadzapatsidwa mwayi wina

    [86] “Ndipo amene ankam’phatikiza Allah akadzawaona aphatikizi awowo adzati: “Mbuye wathu! Awa ndiaphatikizi athu omwe tidali kuwapembedza m’malo mwa Inu.” Ndipo (aphatikiziwo akadzamva mawu awa) adzawaponyera mawu awo (nkunena kuti): “Ndithu inu ndi abodza.”

    [87] “Ndipo tsiku limenelo onse adzadzitula kwa Allah; ndipo zidzawataika zomwe adali kuzipeka

    [88] “Tsono amene sadakhulupirire ndi kumaletsa anthu kunjira ya Allah tidzawaonjezera chilango pamwamba pa chilango chifukwa chakuononga kwawo

    [89] “Ndipo (akumbutse za) tsiku lomwe tidzautsa mboni mu mtundu uliwonse zochokera mwa iwo omwe adzawachitira umboni (pa zomwe zinkachitika ndi iwo); ndipo tidzakubweretsa iwe kukhala mboni pa awa (anthu ako); ndiponso takuvumbulutsira buku ili lomwe likufotokoza za chinthu chilichonse lomwenso ndi chiongoko ndi mtendere ndiponso ndinkhani yosangalatsa kwa ogonjera (Allah)

    [90] “Ndithudi, Allah akulamula (kuchita) chilungamo, ndikuchita zabwino, ndi kupatsa achinansi, ndipo akuletsa zauve ndi zoipa ndi kupyola malire; akukulangizani kuti muzindikire ndi kukumbukira

    [91] “Ndipo kwaniritsani lonjezo (limene mukupereka mdzina) la Allah pamene mulonjeza, ndipo musaswe malonjezowo pambuyo pakuwalimbikitsa; pomwe mwasankha Allah kukhala mboni yanu; ndithu Allah akudziwa (zonse) zimene mukuchita

    [92] “Ndipo musakhale monga mkazi yemwe adakhulula ulusi wake pambuyo pouluka mwamphamvu, mukukuchita kulumbira kwanu pakati panu kukhala kwa chinyengo, chifukwa chakuti gulu la mtundu wina nlochuluka kwambiri kuposa gulu la mtundu wina (powasiya omwe mudalonjezana nawo chifukwa chakuwaona kuchepa, ndi kukagwirizana ndi omwe simudalonjezane nawo chifukwa chakuwaona kuchuluka); ndithu Allah akukuyesani mayeso pa njira yotere; ndipo ndithu pa tsiku la Qiyâma adzakufotokozerani za zomwe mudali kusiyana

    [93] “Ndipo Allah akadafuna, ndithu akadakuchitani kukhala gulu limodzi, (nonsenu mukadamumvera monga momwe adawachitira angelo, koma adakupatsani ufulu kuti muchite chimene mufuna); komatu amamulekelera kusokera amene wamfuna, ndipo amamuongola wamfuna; ndipo, ndithu mudzafunsidwa pa zomwe munkachita

    [94] “Ndipo musakuchite kulumbira kwanu kukhala njira yonyengelerana pakati panu, kuopera kuti mwendo ungatelere (pa njira yolungama nkukagwera ku Moto) pambuyo pokhazikika mwendowo (pa njirapo) ndi kukazilawa zoipa chifukwa chakutsekereza kwanu (anthu) ku njira ya Allah, ndipo nkupeza chilango chachikulu (tsiku lachimaliziro)

    [95] “Ndipo musagulitse mapangano a Allah ndi mtengo wochepa (wa zomwe mukupeza pano pa dziko lapansi). Chimene chili kwa Allah, ndicho chabwino kwa inu ngati mukudziwa

    [96] “Zomwe mulinazo nzakutha ndipo zili kwa Allah ndizo zosatha. Ndithudi Ife tidzawapatsa malipiro (aakulu zedi) amene adapirira oposera zabwino zimene ankachita

    [97] “Amene akuchita zabwino, wamwamuna kapena wamkazi uku ali wokhulupirira timkhazika ndi moyo wabwino (pano pa dziko, ndi tsiku la Qiyâma) tidzawalipira malipiro awo mochuluka kwambiri chifukwa cha zabwino zomwe ankachita

    [98] “Ndipo ukafuna kuwerenga Qur’an dzitchinjirize ndi Allah kwa satana wopirikitsidwa (ponena kuti Awudhu Billahi mina Shaitwani Rajim)

    [99] “Ndithu iye (satana) alibe mphamvu pa amene akhulupirira ndi kutsamira kwa Mbuye wawo

    [100] “Ndithudi mphamvu zake zili pa amene akumusankha (amulola) kukhala bwenzi lawo (mlangizi wawo) ndiponso ndi omwe akumphatikiza iye (ndi Allah)

    [101] “Ndipo tikasintha Ayah (ndime) ndikubwera ndi Ina pamalopo, pomwe Allah akudziwa zimene akuvumbulutsa, akunena: “Ndithu iwe ndiwe wopeka.” Koma ambiri a iwo sadziwa (chilichonse)

    [102] “Nena: “Mzimu woyera (Gabriel) waitsitsa (Qur’an) kuchokera kwa Mbuye wako mwachoonadi kuti awalimbikitse nayo amene akhulupirira ndi kuti ikhale chiongoko ndi nkhani yabwino kwa amene alowa m’Chisilamu (amene agonjera Allah)

    [103] “Ndithu tikudziwa kuti iwo akunena: “Pali munthu amene akumphunzitsa.” (Koma) chiyankhulo cha amene akumganizirayo nchachilendo, ndipo ichi (chiyankhulo cha Qur’an) ndi chiyankhulo cha Chiarabu chomveka

    [104] “Ndithudi amene sakhulupirira Ayah (ndime) za Allah, Allah sawaongolera (kunjira ya choonadi), choncho adzapeza chilango chowawa

    [105] “Ndithudi amene sakhulupirira Ayah (ndime) za Allah ndi amene amapeka bodza (ndi kumalifalitsa kwa anthu) ndipo iwowo ndiwo onama

    [106] “Amene akukana Allah, pambuyo pomukhulupirira, (chilango chachikulu chikumuyembekezera), kupatula yemwe adakakamizidwa, uku mtima wake utakhazikika pa chikhulupiliro; koma amene akutsekulira mtima wake kusakhulupirira, mkwiyo wa Allah uli pa iwo (ndipo anthu otere) adzapata chilango chachikulu

    [107] “Zimenezo nchifukwa chakuti iwo adakonda moyo wa dziko lapansi kwambiri kuposa wa pambuyo pa imfa; ndi kutinso Allah saongola anthu osakhulupirira

    [108] “Iwo ndi omwe Allah adawadinda m’mitima mwawo, m’makutu mwawo, ndi m’maso mwawo (chifukwa cha kusimbwa kwawo). Ndipo iwo ngonyalanyaza (malamulo a Allah) kwambiri

    [109] “Palibe chikaiko chakuti iwo ngotaika kwambiri pa tsiku la chimaliziro

    [110] “Ndithudi kenako Mbuye wako, kwa amene adasamuka pambuyo pakusautsidwa (kufikira adanena zosayenera) komanso nkuchita Jihâd ndikupirira (chifukwa cha chipembedzo), ndithu Mbuye wako pambuyo pa zimenezo, Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosantha

    [111] “(Akumbutse za) tsiku lomwe mzimu uliwonse udzadza ukudziteteza wokha (wosalabadira za mwana wake, mkazi wake ndi abale ake), ndipo mzimu uliwonse udzalipidwa molingana ndi zochita zake zimene unkachita, ndipo iwo sadzachitidwa chinyengo (pochepetsedwa mphoto yawo yoti alandire)

    [112] “Ndipo Allah waponya fanizo lamudzi womwe udakhala mwa mtendere mokhazikika, rizq lake (madalitso) linkaudzera mochuluka kuchokera malo aliwonse; koma (mudziwo) udakana mtendere wa Allah (pakusathokoza); choncho Allah adaulawitsa chovala cha njala ndi mantha chifukwa cha (zoipa) zomwe (anthu ake) adali kuchita

    [113] “Ndipo adawadzera mtumiki wochokera mwa iwo, koma adamtsutsa; choncho chilango chidawafika uku ali odzichitira okha zoipa

    [114] “Choncho idyani zimene Allah wakupatsani zomwe zili zahalali, zabwino; ndipo yamikani mtendere wa Allah ngatidi mukupembedza Iye

    [115] “Ndithu wakuletsani (kudya) zakufa zokha, magazi (liwende), nyama ya nkhumba ndi chimene chazingidwa posatchula dzina la Allah. Koma amene wasimidwa (nadya choletsedwa) mosafuna kapena kupyoza muyeso (Allah amkhululukira), ndithudi Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni

    [116] “Ndipo musanene chifukwa chabodza lomwe malirime anu akunena (kuti) “Ichi nchololedwa; ichi ncholetsedwa; (popanda umboni).” Kuopera kuti mungampekere bodza Allah. Ndithu amene akupekera bodza Allah, sangapambane

    [117] “Ndichisangalalo chochepa (cha m’dziko lapansi chimene chikuwachititsa zimenezo); ndipo iwo adzapata chilango chowawa

    [118] “Ndipo kwa Ayuda tidawaletsa kale zimene takusimbira. Ndipo sitidawachitire chinyengo (pakuwaletsa zimenezo), koma iwo okha adali kudzichitira chinyengo

    [119] “Kenako ndithu Mbuye wako, kwa amene achita zoipa mwaumbuli ndipo nkulapa pambuyo pazimenezo nachita zabwino, ndithudi Mbuye wako pambuyo pa zimenezo Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha

    [120] “Ndithu Ibrahim adali mtsogoleri (chitsanzo chabwino kwa anthu), womvera Allah, wopendekera ku choonadi ndipo sadali mwa omuphatikiza (Allah ndi mafano)

    [121] “(Adali) wothokoza mtendere Wake (Allah); adamsankha ndipo adamuongolera ku njira yolunjika

    [122] “Ndipo tidampatsa zabwino padziko lapansi, ndipo ndithudi, iye pa tsiku la chimaliziro adzakhala m’gulu la anthu abwino

    [123] “Kenako takuvumbulutsira (iwe Muhammad{s.a.w} mawu) akuti: “Tsatira njira (chipembedzo) ya Ibrahim (yemwe adali) wokwanira mkulungama, ndipo sadali mwa omuphatikiza (Allah ndi mafano.)”

    [124] “Ndithudi Sabata idaikidwa kwa amene adatsutsana pa za iyo (Sabatayo); ndithu Mbuye wako adzaweruza pakati pawo tsiku la Qiyâma pa zomwe adali kusiyana

    [125] “Itanira (anthu) ku njira ya Mbuye wako mwanzeru ndi ulaliki wabwino; ndipo tsutsana nawo mkutsutsana kwabwino (osati motukwanana kapena monyozana). Ndithu Mbuye wako Iye Ngodziwa kwambiri za amene asokera ku njira Yake, ndiponso Iye Ngodziwa kwambiri za amene aongoka

    [126] “Ndipo ngati mukubwezera (choipa chimene mwachitiridwa), bwezerani cholingana ndi chimene mwachitiridwacho, koma ngati mutapirira (posiya kubwezera), ndithu kutero ndi ubwino kwa opirira

    [127] “Ndipo pirira. Kupirira kwakoko kusakhale pa china chake koma Allah basi. Ndipo usadandaule chifukwa cha iwo, (iwo akudzisokeretsa okha). Ndipo usakhale wobanika chifukwa cha chiwembu chomwe akuchita

    [128] “Ndithu Allah ali pamodzi ndi amene akumuopa ndi amenenso akuchita zabwino

    Ulendowausiku

    Surah 17

    [1] “۞ Ulemelero ngwa Yemwe adayendetsa kapolo Wake usiku (umodzi) kuchokera mu Msikiti Wopatulika (wa Makka) kupita ku Msikiti wakutali (wa Baitul-Muqaddas), womwe tidazidalitsa zomwe zauzungulira. (Tidampititsa kumeneko) kuti timsonyeze zina mwa zisonyezo Zathu; ndithu Iye (Allah) Ngwakumva, Ngowona ( chilichonse)

    [2] “Ndipo Mûsa tidampatsa buku (la Taurat) tidaliika kukhala chiongoko kwa ana a Israyeli (Allah adawauza): “Musadzipangire atetezi kusiya Ine.”

    [3] “(Ndiponso adawauza kuti: “E inu) Mbumba ya amene tidawanyamula pamodzi ndi Nuh! (Khalani othokoza monga tate wanu.) Ndithu iye adali kapolo wothokoza kwambiri.”

    [4] “Ndipo tidawazindikiritsa ana a Israyeli m’bukulo, kuti: “Ndithu inu muononga pa dziko kawiri, ndipo mudzapyola malire pochita zoipa, kupyola malire kwakukulu

    [5] “Ndipo likadzafika lonjezo (lakupatsidwa chilango chakuononga) koyamba mkuononga kuwiriko, tidzawakhwirizira pa inu anthu athu, eni kumenya nkhondo mwaukali, adzakhala akuzungulira mkatikati mwa nyumba (zanu), ndipo lidali lonjezo lochitika

    [6] “Kenako tidakubwezerani kupambana pa iwo (omwe adakugonjetsani poyamba); ndipo tidakupatsani chuma ndi ana, ndi kukudalitsani kukhala ndi gulu lochuluka

    [7] “(Tidati kwa iwo): “Ngati muchita bwino (pomumvera Allah), ubwino ngwanu (pa dziko lapansi ndi pa tsiku la Chimaliziro); ngati muipitsa (ponyoza Allah), kuipako kuli pa inu nokha. Choncho pamene idadza nthawi ya lonjezo lachilango chomaliza, (tidakutumizirani adani anu) kuti apereke kunyozeka pa nkhope zanu, ndikutinso alowe mu Nsikiti monga adalowera mnthawi yoyamba, ndikuti aononge chilichonse chimene achigonjetsa; kuononga kwakukulu.”

    [8] ““(Koma ngati mudzalungama mzochita zanu), Mbuye wanu adzakuchitirani chifundo; ndipo ngati mudzabwereranso (ku machitidwe anu okhota), tidzabwereranso (kukulangani). Ndipo taikonza Jahannam kukhala ndende ya osakhulupirira.”

    [9] “Ndithu iyi Qur’an ikuongolera ku njira yoongoka ndi kuwasangalatsa okhulupirira omwe akuchita zabwino, kuti ndithu iwo adzalandira malipiro aakulu (pa tsiku la chiweruziro)

    [10] “Ndikutinso omwe sadakhulupirire za tsiku la chimaliziro tawakonzera chilango chowawa

    [11] “Ndipo munthu amafulumira kupempha zoipa monga momwenso amafulumilira kupempha zabwino; ndithu munthu ngwaphuma (mzochita zake)

    [12] “Ndipo tapanga usiku ndi usana (mkusinthana-sinthana kwake) monga zisonyezo ziwiri (zosonyeza umodzi wa Allah ndi mphamvu Zake zoposa); ndipo tidachifafaniza chisonyezo cha usiku (kuti chisakhale ndi kuunika) ndipo chisonyezo cha usana tidachipanga kuti chikhale ndi kuunika; kuti mufunefune ubwino wochokera kwa Mbuye wanu, ndikuti mudziwe chiwerengero cha zaka ndichiwerengero (cha miyezi ndi masiku); ndipo chinthu chilichonse (chofunika pa chipembedzo ndi za m’dziko), tachilongosola bwinobwino, mwatsatanetsatane

    [13] “Ndipo munthu aliyense tammangilira mkhosi mwake zochita zake; ndipo tsiku la Qiyâma tidzamtulutsira kaundula (momwe muli zochita zake), adzampeza wovundukulidwa

    [14] “(Kudzanenedwa kwa iye:) “Werenga kaundula wako (kupyolera m’mphamvu za Allah ngakhale pa dziko lapansi siunkatha kuwerenga); mzimu wako ukwanira lero kudziwerengera.”

    [15] “Amene waongoka (potsatira njira ya choonadi) ndithu wadzipindulira yekha, ndipo amene wapotoka (ku njira ya choonadi) ndithu wadzitaya iye mwini. Ndipo msenzi wosenza machimo sadzasenza mtolo wa machimo a wina. Ndipo Ife siolanga (zolengedwa) kufikira titatumiza mtumiki (kuti azidziwitse choonadi. Zikakana ndipomwe timazilanga)

    [16] “Ndipo tikafuna kuononga mudzi (pamene eni mudziwo akuchita zoipa), timawalamula opeza bwino a m’menemo (kuti asiye zoipa). Koma akapitiriza kuononga kwawo m’menemo, apo ndipo liwu (la kuwaononga) limatsimikizidwa pa iwo ndipo timauononga, kuononga kwakukulu

    [17] “Ndimibadwo ingati imene tidaiononga pambuyo pa Nuh! Ndipo akukwanira Mbuye wako kudziwa bwinobwino ndi kuona bwinobwino uchimo wa akapolo Ake. (Palibe chobisika kwa Iye m’zochitachita za anthu)

    [18] “Amene afuna zachangu (zosangalatsa za m’dziko ndikumaikirapo mtima pa izo), timpatsiratu mwachangu pa dziko lapansi chimene tikufuna kwa amene tafuna (kumpatsa;) koma (tsiku la chimaliziro) tamkonzera Jahannam adzailowa ali wonyozeka, wopirikitsidwa apa ndi apo

    [19] “Ndipo amene afuna tsiku la chimaliziro (mzochita zake) ndikuligwilira ntchito yake yeniyeni uku ali okhulupirira, iwowo khama lawo lidzakhala lolandiridwa

    [20] “Onse awa, (abwino ndi oipa), timawapatsa awa ndi awa mwazopatsa za Mbuye wako; ndipo zopatsa za Mbuye wako sizotsekerezedwa (kuti zisamfike kapolo Wake)

    [21] “Taona (ndi diso lolingalira) m’mene tawasiyanitsira mkupeza bwino, ena nkukhala pamwamba pa anzawo (pa chuma ndi pa moyo wangwiro); ndipo pa tsiku la chimaliziro kusiyana kwawo pa masitepe ndi ulemelero, nkwakukulu kwabasi

    [22] “Usadzipangire mulungu wina ndi kumphatika kwa Allah; kuti ungadzakhale wodzudzulidwa (kwa Allah) ndikusiidwa wopanda m’thandizi

    [23] “Ndipo walamula Mbuye wako kuti musapembedze (wina) koma Iye Yekha, ndi kuti muchitire zabwino makolo (anu). Ngati m’modzi wa iwo afika msinkhu waukalamba uli naye, kapena onse awiri, usawanenere mawu amnyozo, ndiponso usawakalipire koma yankhula nawo ndi mau aulemu

    [24] “Ndipo afungatire ndi phiko lodzichepetsa powachitira chisoni, ndipo nena: “Mbuye wanga achitireni chisoni (makolo anga) monga momwe ankandilelera ku ubwana.”

    [25] “Mbuye wanu akudziwa kwambiri zomwe zili m’maganizo mwanu; ngati muli ofuna kuchita zabwino, (kwa makolo anu Iye akudziwa. Ndipo ngati mutawalakwira, kenako ndikulapa), ndithu Iye ndi Mwini kukhululukira otembenukira kwa Iye

    [26] “Ndipo mnansi wako, masikini ndi wapaulendo (yemwe alibe choyendera) mpatse gawo lake (la chuma chako) ndipo usamwaze (chuma chako) mosakaza

    [27] “Ndithu omwaza chuma mosakaza ndiabale a satana (otsatira satana), ndipo satana ngosathokoza kwa Mbuye wake

    [28] “Ndipo ngati ukuwapewa opempha (pamene ulibe chowapatsa) pamene ukufunafuna chifundo cha Mbuye wako chomwe ukuchiyembekezera, nena kwa iwo mau ofewa (ponena kuti: “Ndikapeza chokupatsani, ndikuninkhani.”)

    [29] “Ndipo mkono wako usaukhalitse ngati kuti wamangidwa kukhosi kwako, ndiponso usautambasule mosayenera, ungadzakhale wodzudzulidwa ndiwosowa

    [30] “Ndithu Mbuye wako amamtambasulira rizq amene wamfuna, ndikulichepetsa (kwa amene wamfuna). Ndithu Iye Ngodziwa bwino; wopenya bwino za akapolo Ake

    [31] “Ndipo musaphe ana anu poopa umphawi. Ife ndi amene tikuwapatsa iwo ndi inu. Ndithu kupha anawo ndi tchimo lalikulu

    [32] “Ndipo musachiyandikire chiwerewere; ndithu (icho) ndi uve (chonyansa chachikulu), ndiponso ndi njira yoipa

    [33] “Ndipo musaphe munthu amene Allah waletsa (kumupha) koma mwachoonadi (poweruza oweruza zakuphedwa ngati utam’gwera mulandu woyenera kuphedwa). Ndipo amene waphedwa mopanda chilungamo, tapereka mphamvu kwa mlowammalo wake (wa wophedwayo atafuna angamuphenso kapena kumsiya ndikulandirapo dipo); koma asapyole malire mukuphako. Ndithu iye ngothandizidwa ndi Shariya

    [34] “Ndipo musachiyandikire chuma cha wamasiye (pochidya mosayenera) koma pokhapokha m’njira yomwe ili yabwino, kufikira atakula, (apo tsono apatsidwe chumacho); ndipo kwaniritsani lonjezo, popeza lonjezo lidzafunsidwa (tsiku la Qiyâma)

    [35] “Ndipo kwaniritsani mlingo pamene mulinga, ndipo yesani ndi sikelo zabwino, zimenezo ndi zabwino (kwa inu) ndiponso mathero (ake) ngabwino

    [36] “Ndipo usazitsate (pongoziyankhulayankhula kapena kuzichita) zomwe sukuzidziwa; ndithu makutu, maso ndi mtima zonsezo zidzafunsidwa

    [37] “Ndipo usayende padziko modzitukumula; ndithu iwe sungang’ambe nthaka ndiponso sungalifikire phiri m’kutalika

    [38] “Zonsezi kuipa kwake nkonyansidwa kwa Mbuye wako

    [39] “Izi ndi zina mwa za nzeru zomwe Mbuye wako wakuvumbulutsira. Usakhale ndi mulungu wina ndi kumphatikiza kwa Allah, kuti ungadzaponyedwe ku Jahannam uli wodzudzulidwa ndi wopirikitsidwa apa ndi apo

    [40] “Kodi Mbuye wanu wakusankhirani ana aamuna, ndipo mwini wadzipangira ana aakazi achingelo? Ndithu inu mukunena liwu lalikulu

    [41] “Ndipo ndithu talongosola lamulo la chinthu chilichonse mwatsatanetsatane m’Qur’an iyi kuti akumbukire, ndipo (oipa) siikuwaonjezera (china) koma kuida ndi kuithawa

    [42] “Nena: “Pakadakhala milungu ina pamodzi ndi Allah, monga momwe akunenera, ikadafuna njira yomufikira (Mbuye) Mwini Arsh (Mpando wa chifumu, ndi kumthira nkhondo).”

    [43] “Wayera ndipo watukuka Allah ku zimene akunenazo; kutukuka kwakukulu (kwabasi)

    [44] “Zonse zakumitambo isanu ndi iwiri ndi nthaka ndi zam’menemo, zikulemekeza Iye; ndipo palibe chilichonse koma chikumlememekeza ndi kumtamanda; koma inu simuzindikira kulemekeza kwawo! Ndithudi Iye (Allah) Ngodekha, Ngokhululuka

    [45] “Ndipo ukamawerenga Qur’an (zikukhala ngati) taika chotchinga chosaonekera pakati pako ndi pakati pa amene sadakhulupirire za tsiku la chimaliziro

    [46] “Ndipo (ngati) taika zitsekelero m’mitima mwawo kuti angaizindikire, ndipo (ngati) mmakutu mwawo muli kulemera kwa ugonthi. Ndiponso ukamtchula m’Qur’an Mbuye wako Yekha, iwo akutembenuka ndi misana yawo moipidwa

    [47] “Ife tikudziwa chifukwa chomwe akuimvetsera (Qur’an), pamene akukumvetsera ndi pamene akunong’onezana awo achinyengo, pamene akunena awo oyipa (kuuza Asilamu kuti): “Inu simutsatira (wina) koma munthu wolodzedwa.”

    [48] “Ona momwe akukufanizira ndi mafanizo abodza. (Nthawi zina akuti ndiwe wolodzedwa, nthawi zina akuti ndiwe mfiti!) Choncho asokera, ndipo sangathe kupeza njira (yeniyeni)

    [49] “Ndipo akunena: “Kodi tikadzakhala mafupa odukaduka, tidzaukitsidwanso kukhala zolengedwa zatsopano?”

    [50] “Nena: “Khalani miyala kapena zitsulo.”

    [51] ““Kapena cholengedwa chilichonse mwa zomwe zikuoneka kuti nzovuta kwambiri m’mitima mwanu (m’maganizo mwanu), (ngakhale mutakhala zimenezo, mudzaukitsidwa).” Pamenepo anena: “Ndani adzatibweza?” Nena: “Yemwe adakulengani pachiyambi.” Pamenepo adzakupukusira mitu yawo ndi kunena: “Zichitika liti zimenezo?” Nena: “Mwina zili pafupi!”

    [52] ““(Zidzakhala) pa tsiku lomwe adzakuitanani (Allah), ndipo inu mudzayankha momuyamikira, ndipo mudzaganizira kuti simudakhale (pa dziko lapansi) koma (kwa) nthawi yochepa.”

    [53] “Ndipo auze akapolo Anga kuti (nthawi zonse) azinena zomwe zili zabwino; chifukwa satana amakhwirizira mikangano pakati pawo; ndithu satana kwa munthu, ndi m’dani woonekera

    [54] “Mbuye wanu akukudziwani bwino. Ngati afuna akuchitirani chisoni (mukatembenukira kwa Iye), ndipo ngati afuna, akulangani (mukapitiriza kumnyoza); ndipo sitidakutumize kuti ukhale muyang’anili wawo

    [55] “Ndipo Mbuye wako akuwadziwa bwino onse ali kumwamba ndi pansi, ndithu tawapatsa ulemelero wambiri aneneri ena kuposa ena. Ndipo Daud tidampatsa Zaburi

    [56] “Nena: “Aitaneni amene mukuwatcha kuti ndi milungu kusiya Iye (Allah) kuti akuchotsereni masautso, sadzatha kukuchotserani vuto lililonse ngakhale kulisintha (kuti likhale chabwino).”

    [57] “Iwo amene akuwapempha (naonso) akufunafuna njira yoziyandikitsira kwa Mbuye wawo (ngakhale) omwe ali pafupi mwa iwo (ndi Allah, monga angelo); naonso akuyembekezera chifundo chake ndi kuopa chilango chake; ndithu chilango cha Mbuye wako, nchoopedwa

    [58] “Ndipo sipadzapezeka mudzi uliwonse koma Ife tidzauphwasula tsiku la Qiyâma lisanadze, kapena tidzaulanga ndi chilango chaukali (ngati uli woyenerana ndi zimenezo). Izi zidalembedwa m’buku

    [59] “Ndipo palibe chimene chikutiletsa kutumiza zizizwa (zomwe akuzipempha) koma kuti anthu akale adazitsutsa. Asamuda tidawapatsa ngamira yaikazi kuti ikhale chizindikiro choonekera (chozizwitsa) koma adaichitira zosayenera; ndipo sititumiza zizizwa ndi cholinga china, koma kuchenjeza

    [60] “Ndipo (kumbuka) pamene tidakuuza kuti ndithu Mbuye wako wawazungulira anthu (mowadziwa bwinobwino;) ndipo sitidawachite maloto omwe tidakuonetsa koma kuti akhale mayeso kwa anthu, (kuti kodi akhulupirira kapena sakhulupirira), ndiponso (kutchula kwa) rntengo wotembeleredwa m’Qur’an (ndimayetseronso kwa iwo;) ndipo tikuwachenjeza, koma (machenjezo athu) sakuwaonjezera china koma kulumpha malire kwakukulu basi

    [61] “Ndipo (akumbutse) pamene tidauza angelo kuti: “Mugwadireni Adam.” Ndipo adamugwadira kupatula Iblis (iye) adati: “Kodi ndimugwadire yemwe mwamlenga ndi dongo?”

    [62] “Adatinso (kwa Allah): “Kodi mukuona uyu amene mwampatsa ulemelero kuposa ine? Ngati mundipatsa nthawi mpaka tsiku la Qiyâma, ndithu ndiononga mbumba yake (yonse) kupatula ochepa basi.”

    [63] “(Allah) adati: “Choka! Amene adzakutsata mwa iwo, ndithu Jahannam ndiyo mphoto yanu mphoto yokwanira.”

    [64] “Ndipo apusitse amene ungawathe mwa iwo ndi liwu lako; ndipo asonkhanitsire gulu lako la nkhondo la okwera akavalo ndi loyenda ndi miyendo; tenga gawo lako pa chuma chawo ndi ana awo; ndipo alonjeze (malonjezo abodza).” Koma satana salonjeza china koma chinyengo basi

    [65] ““Ndithu akapolo Anga, ulibe nyonga pa iwo.” Ndipo Mbuye wako akukwanira kukhala mtetezi (wawo)

    [66] “Mbuye wanu ndi yemwe amakuyendetserani zombo pa nyanja kuti munke mufunafuna ubwino Wake. Ndithu Iye Ngwachisoni kwa inu

    [67] “Ndipo akakupezani masautso pa nyanja, amasowa amene mumakhala mukuwapembedza kupatula Iye (Allah). Koma akakupulumutsirani kumtunda, mukutembenuka ndi kunyoza Allah. Ndithu munthu ndi wokana (mtendere wa Allah sayamika)

    [68] “Kodi mukudziika pa chitetezo ndi chilango cha Allah (mukafika pa ntunda) kuti Allah sangakulowetseni pansi mbali iliyonse ya pa ntunda, kapena sangakutumizireni chigumula chamchenga (kapena miyala) kenako inu simudzapeza mtetezi (wokupulumutsani ku chilangocho)

    [69] “Kapena mwadziika pachitetezo kuti (Allah) sadzakubwezeraninso m’nyanjamo kachiwiri ndipo nkudzakutumizirani chimphepo chaukali ndikukumizani chifukwa cha kusakhulupirira (ndi kusathokoza kwanu,) kenako inu nkusapeza wokutetezani kwa Ife

    [70] “Ndipo ndithu tawalemekeza ana a Adam; ndipo tawapatsa zokwera pa ntunda ndi pa nyanja; tawapatsa zopatsa zabwino kwambiri; ndipo tawapatsa ulemelero kuposa zambiri m’zomwe tidalenga; ulemelero waukulu kwabasi

    [71] “(Akumbutse za) tsiku lomwe tidzaitana anthu onse m’dzina la mneneri wawo; choncho, amene adzapatsidwe akaundula awo ndi dzanja lamanja iwo adzawerenga akaundula awowo (mwachisangalalo), ndipo sadzaponderezedwa ngakhale pa (kachinthu kakang’ono monga) kaulusi ka mkati mwa njere ya kanjeza

    [72] “Ndipo amene ali wakhungu pano (pa dziko lapansi posapenya zizindikiro) adzakhalanso wakhungu pa tsiku la chimaliziro, ndipo adzakhala wosokera kwambiri njira (kumeneko)

    [73] “Ndipo ndithu adatsala pang’ono kukusokoneza pa zimene tavumbulutsa kwa iwe kuti utipekere zina zake m’malo mwa izi; pamenepo, akadakusankha kukhala bwenzi (lawo)

    [74] “Ndipo tikadapanda kukulimbikitsa, ukadapendekera kwa iwo, kupendekera kwa pang’ono

    [75] “Tero ndithu tikadakulawitsa chilango chachikulu cha moyo (wa pa dziko lapansi) ndi chilango chachikulu utafa; kenako siukadapeza mthandizi wokupulumutsa kwa Ife

    [76] “Ndipo padatsala pang’ono kuti akusowetse mtendere m’dziko ili (la Makka) kuti akutulutse m’menemo; koma pambuyo pako sakadakhala (ndi moyo) kupatula (nthawi) yochepa

    [77] “Chimenechi ndi chikhalidwe cha omwe tidawatuma patsogolo pako mwa atumiki Athu, ndipo supeza kusintha pachikhalidwe Chathu

    [78] “Pemphera Swala (za Farazi), dzuwa likapendeka mpaka mu mdima wausiku (zomwe ndi Swala za Dhuhri, Asri, Maghrib ndi Isha), ndipo pempheranso Swala ya Fajir: ndithu Swala ya Fajir amaichitira umboni (angelo)

    [79] “Ndipo pakati pa usiku, dzuka mtulo ndi kupemphera Swala; ilo ndipemphero loonjezera pa iwe, kuti Mbuye wako akakuimike pamalo pa ulemu potamandidwa (ndi zolengedwa zonse pa tsiku la Qiyâma)

    [80] “Ndipo nena (mawu awa pomwe ukupemphera): “Mbuye wanga! Ndilowetseni, kulowetsa kwabwino (paliponse pamene ndikulowa), ndiponso nditulutseni, kutulutsa kwabwino (paliponse pamene ndikutuluka); ndipatseni mphamvu zochokera kwa Inu zondithandiza ndi kugonjetsera adani.”

    [81] “Ndipo nena: “Choonadi chafika, ndipo chachabe chachoka; ndithu chachabe ndichochoka (ngakhale patapita nthawi yaitali).”

    [82] “Ndipo tikuivumbulutsa Qur’an yomwe imachiritsa (matenda a mmitima) ndiponso ndi chifundo kwa okhulupirira. Komabe osalungama siikuwaonjezera (kanthu kena) koma kutayika

    [83] “Ndipo tikampatsa chisomo munthu, (monga moyo wangwiro ndikupeza bwino), amatembenuka (ndikusiya kutikumbukira ndikutipempha), ndipo amadziika kutali (ndi Ife chifukwa chakudzitama ndikudzikuza), koma masautso akamkhudza, (monga matenda ndi umphawi) amataya mtima kwambiri

    [84] “Nena (iwe Mneneri, kwa osakhulupirira a Chikuraishi,): “Aliyense (wa ife ndi inu) akuchita ntchito (zake ndikuyenda panjira yake) ndipo Mbuye wanu Ngodziwa kwambiri za yemwe ali panjira yolondola (potsatira choonadi).”

    [85] “Ndipo akukufunsa (iwe, Muhammad (s.a.w), anthu ako mokhwiriziridwa ndi Ayuda) za Mzimu. Nena: “Mzimu ndi chinthu chomwe akuchidziwa Mbuye wanga Yekha; ndipo inu simudapatsidwe nzeru (zozindikilira zinthu) koma pang’ono chabe, (poyerekeza ndi nzeru za Allah).”

    [86] “Ndipo tikadafuna kufufuta Qur’an (pachifuwa chako) yomwe takuvumbulutsira, (tikadatha kutero). Kenako sukadapeza kwa Ife wokuimilira ndi kukupulumutsa

    [87] “Koma (taisiya mu mtima mwako) chifukwa cha chifundo chochokera kwa Mbuye wako; ndithu ubwino Wake pa iwe ngwaukulu

    [88] “Nena: “Ngakhale atasonkhana anthu ndi ziwanda (mothandizana) kuti abwere ndi buku longa ili la Qur’an (mukayalidwe ka mawu ndi matanthauzo ake), sangathe kubweretsa longa ilo, ngakhale atathandizana wina ndi mnzake.”

    [89] “Ndipo ndithu tawalongosolera anthu, m’Qur’an iyi; mkulongosola kwa njira zosiyanasiyana ndikupereka fanizo lamtundu uliwonse. Ndipo anthu ambiri akukana (zonsezo) koma kusakhulupirira basi

    [90] “Ndipo (pamene adalephera kubwera ndi Qur’an yawo,) adati: “Sitingakukhulupirire mpaka utatitulutsira kasupe wosaphwa m’dziko (lathu ili la Makka).”

    [91] “Kapena ukhale ndi munda wazipatso za kanjedza ndi mphesa (kuno ku Makka), ndipo utulutse mitsinje yambiri pakati pa mundapo

    [92] “Kapena utigwetsere zidutswa za thambo pa mitu yathu monga momwe umatiopsezera, apo ayi, um’bweretse Allah ndi angelo (kuti) tionane nawo nkhope kwa nkhope (mwamasomphenya.)”

    [93] “Kapena ukhale ndi nyumba ya golide, kapena ukwere kumwamba. Ndipo sitikukhulupirira kukwera kwako pokhapokha utatibweretsera buku (lochokera kwa Allah lomwe likulongosola za kuona kwako), kuti tidziliwerenga.” Nena (kwa iwo): “Mbuye wanga alemekezeke ndikupatukana ndi mbiri zopunguka! Ine sindine kanthu koma munthu, mtumiki (monga atumiki ena).”

    [94] “Ndipo palibe chimene (Amushirikina a m’Makka) chawaletsa kukhulupirira choona pamene chiongoko chawadzera, koma kunena kwawo (kwa umbuli) kwakuti: “Kodi Allah amatuma munthu kukhala Mtumiki (Wake)

    [95] “Nena: “Padziko pakadakhala angelo omayendayenda ndi okhazikika (m’malo awo ndi m’nyumba zawo), tikadawatsitsira m’ngelo monga mtumiki kuchokera kumwamba.”

    [96] “Nena: “(Ngati mukutsutsa uthenga wanga) Allah wakwanira kukhala Mboni (ndi Muweruzi) pakati panga ndi pakati panu (zakuona kwa uthenga wanga kwa inu). Ndithu Iye Ngodziwa za akapolo Ake (zilakolako zawo) Ngowona (zochita zawo)

    [97] “Ndipo yemwe Allah wamuongola, (chifukwa cha kukonzeka kwake kwa ubwino), iyeyo ndi amene waongoka; ndipo amene wamulekelera kusokera, (chifukwa cha kuipa kwa khalidwe lake), simungampezere athandizi kupatula Iye (Allah). Ndipo pa tsiku la chiweruziro tidzawasonkhanitsa uku akukokedwa ndi nkhope zawo ali osapenya, osalankhula ndi osamva. Malo awo okhala ndi ku Jahannam. Nthawi iliyonse (Motowo) ukatotobwa, tidzauonjezera kwa iwo kuyaka mwaukali

    [98] “(Chilango) chimenecho ndiyo mphoto yawo chifukwa cha kusakhulupirira kwawo zisonyezo (zomwe tidasonyeza kwa iwo), ndi kunena kwawo koti: “Kodi tikadzakhala mafupa ndi zidutswa zonyenyekanyenyeka, tidzaukitsidwanso kukhala zolengedwa zatsopano?”

    [99] “Kodi (onyalanyaza) sadadziwebe kuti Allah Yemwe adalenga thambo ndi nthaka Ngokhoza kulenga ena onga iwo? Ndipo wawaikira nthawi (yodziwika) yopanda chikaiko, (yowaukitsira ku imfa). Koma achinyengo akukana (zonsezi) koma kusakhulupirira basi

    [100] “Nena (kwa opembedza mafano): “Mukadakhala kuti muli nazo nkhokwe za chifundo cha Mbuye wanga, mukadachita umbombo (posagawira ena) kuopa umphawi. Ndipo munthu ali ndi khalidwe loumira.”

    [101] “Ndipo ndithu tidampatsa Mûsa zizizwa zoonekera zisanu ndi zinayi (komabe osakhulupirira sadazikhulupirire). Afunse ana a Israyeli pamene adawadzera (Musayo), Farawo adati kwa iye (Mûsa): “Ndithu ine ndikukuona iwe Mûsa kuti walodzedwa.”

    [102] “(Mûsa) adati: “Ndithu wadziwa kuti palibe amene watumiza (mitsutso) iyi kupatula Mbuye wathambo ndi nthaka kuti zikhale chiphanula maso. Koma ine ndikukuona iwe Farawo kuti waonongeka.”

    [103] “Choncho (Farawo) adafuna kuwatulutsa m’dziko (la Iguputo Mûsa ndi ana a Israyeli) koma tidammiza iye ndi onse omwe adali naye

    [104] “(Mûsa ndi anthu ake tidawapulumutsa). Ndipo tidati, kwa ana a Israyeli, pambuyo pake (pommiza Farawo): “Khalani m’dziko (loyera la Shami); ndipo likazadza lonjezo la moyo winawo, tidzakubweretsani nonsenu (muli m’chipwirikiti.)”

    [105] “Ndipo chifukwa chobweretsa choonadi pa dziko tidaitumiza (Qur’an); ndipo mwachoonadi, yavumbulutsidwa. Ndipo sitidakutume (ndi china) koma kuti ukhale wouza (okhulupirira) nkhani zabwino, ndi wochenjeza (osakhulupirira)

    [106] “Ndipo Qur’an iyi taigawa (m’zigawo zosiyanasiyana poivumbulutsa pang’onopang’ono) kuti uwawerengere anthu mwa chifatse ndipo taivumbulutsa pang’onopang’ono

    [107] “Nena (kwa osakhulupirira a m’Makka mowachenjeza): “Ikhulupirireni (iyi Qur’an) kapena musaikhulupirire, (zonse zili m’chifuniro chanu.) Ndithu amene adapatsidwa nzeru kale (yozindikira za m’mabuku a Allah Qur’an isanadze) ikamalakatulidwa kwa iwo (Qur’aniyi) amagwa ndi zibwano zawo molambira

    [108] “Ndipo amanena: “Mbuye wathu Ngoyera! Ndithu lonjezo la Mbuye wathu ndi lokwaniritsidwa!”

    [109] “Ndipo amagwa ndi zibwano zawo uku akulira, ndipo (Qur’an) imawaonjezera kudzichepetsa

    [110] “Nena (kwa Amushirikina): “Mpempheni Allah, m’dzina la Allah kapena mpempheni m’dzina la Rahman; (dzina) lililonse, limene mungamtchulire (zithandizabe); Iye ali nawo maina abwino. Ndipo usawerenge (Qur’an) pa Swala yako ndi mawu okweza, ndiponso usatsitse mawu kwambiri, koma tsata njira yolingana pakati pa zimenezo (pokweza kwambiri kapena kutsitsa zedi).”

    [111] “Ndipo nena: “Kutamandidwa kwabwino nkwa Allah, yemwe saadadzipangire mwana, ndipo alibe m’phatikizi mu ufumu (Wake); ndipo alibe mthandizi (womthandiza) mkufooka; ndipo mkuzeni, kumkuza kwakukulu!”

    Phanga

    Surah 18

    [1] “Kutamandidwa konse kwabwino nkwa Allah, Yemwe adavumbulutsa kwa kapolo Wake (Mtumiki Muhammad{s.a.w}), buku (ili lopatulika), ndipo sadalikhotetse (koma m’menemo muli zoona zokhazokha)

    [2] “(Walichita kukhala) loongoka kuti lichenjeze anthu za chilango chokhwima chochokera kwa Iye (Allah), ndikuti liwasangalatse okhulupirira omwe akuchita zabwino, kuti adzapeza malipiro abwino

    [3] “Adzakhalamo (mumtendere wosathawo) muyaya

    [4] “Ndikuti liwachenjeze amene akunena (kuti): “Allah wadzipangira Mwana.”

    [5] “Iwo pabodza lawolo alibe kuzindikira chinthu chilichonse chanzeru ngakhale makolo awo. Lakula kwabasi liwu lomwe likutuluka mkamwa mwawo. Sanena china koma bodza basi

    [6] “Mwina udziwononga wekha pakuwadandaulira chikhalidwe chawo kuti sakhulupirira nkhani iyi. (Iyayi! Usakhale wodandaula ndi zimenezo)

    [7] “Ndithu Ife tazichita zomwe zili pamwamba pa nthaka kukhala zokometsera nthakayo, ndikuti (mwa izo) tiwayese mayeso kuti (ndani) mwa iwo ali wochita zabwino kwambiri

    [8] “Ndipo ndithu Ife ndi Amene tidzazichita zomwe zili pamenepo kukhala monga nthaka yoguga (yopanda mmera)

    [9] “Kodi ukuganiza kuti eni phanga ndi eni nkhani zomwe zidalembedwa m’mabuku, adali mwa zizindikiro zathu zododometsa kwambiri? (Iyayi, zilipo zododometsa kwabasi kuposa zimenezo)

    [10] “Pamene anyamata adathawira kuphanga nati: “Mbuye wathu! Tipatseni chifundo chochokera kwa Inu, ndipo tikonzereni chiongoko m’zochita zathu.”

    [11] “Tidagonthetsa makutu awo, (ndikugona kosamva nako kanthu) kwa zaka zambirimbiri m’phanga

    [12] “Kenako tidawautsa, kuti tiwayese (kuti) ndani mwa magulu awiriwa amadziwa kuwerengera nthawi imene (anyamatawa) adakhala (m’phangamo)

    [13] “Ife tikusimbira (iwe mtumiki{s.a.w}) nkhani zawo mwachoonadi; ndithu iwo adali anyamata amene adakhulupirira Mbuye wawo, ndipo tidawaonjezera chiongoko

    [14] “Ndipo tidalimbikitsa mitima yawo pa chikhulupiliro pamene adaimilira (pamaso pa mfumu yawo yosakhulupirira) ndikunena: “Mbuye wathu ndi Mbuye wa thambo ndi nthaka. Sitipembedza mulungu wina m’malo mwa Iye. Ngati titatero ndiye kuti tanena zoipa zopyola muyeso

    [15] “Awa anthu athu adzipangira milungu ina kusiya Allah, nanga bwanji sakubweretsa pa za iyo (milunguyo) umboni woonekera (wosonyeza kuti iyo ndi milungudi)? Kodi ndani wachinyengo wamkulu woposa yemwe akupekera bodza Allah

    [16] “(Adauzana pakati pawo): “Ndipo ngati muwapatuka ndizimene akuzipembedza kusiya Allah, thawirani kuphanga; Mbuye wanu akutambasulirani chifundo Chake ndikukufewetserani zinthu zanu zonse.”

    [17] “(Zidali tere) ukadakhala ukuliona dzuwa pamene linkatuluka (ndikuyamba kukwera), ukadaliona likulambalala kumbali kwa phanga lawo mbali yakudzanjadzanja, ndipo pamene linkalowa limawadutsa mbali yakumanzere (popanda kuwalunjika) pomwe iwo adali pamtetete mmenemo. Zimenezo ndi zina mwa zisonyezo za Allah (zosonyeza kukhoza Kwake). Amene Allah wamuongola iyeyo ndiye woongoka; ndipo amene wamulekelera kuti asokere, simungampezere mtetezi kapena muongoli

    [18] “Ndipo ungawaganizire kuti ali maso pomwe iwo ali mtulo, uku tikuwatembenuzira mbali yakumanja ndi yakumanzere (kuti nthaka isadye matupi awo), ukunso galu wawo atatambasula miyendo yake (yakutsogolo) pakhomo. Ngati ukadawaona ukadatembenuka kuwathawa; ndipo ndithu ukadadzadzidwa mantha ndi iwo

    [19] “Ndipo momwemonso tidawautsa kuti afunsane pakati pawo (zanthawi imene akhala ali chigonere). Adanena wonena mwa iwo: “Kodi mwakhala nthawi yotani muli mtulo?” Adati: “Takhala tsiku limodzi kapena gawo la tsiku.” (Ena) adati: “Mbuye wanu akudziwa kwambiri za nyengo imene mwakhala. Choncho mtumeni mmodzi wa inu ndindalama zanuzi za siliva kumudzi ndipo akayang’ane chakudya chake nchotani chomwe chili choyera bwino, ndikubwerera nacho chakudyacho; koma izi akachite mochenjera ndipo asamzindikiritse aliyense za inu.”

    [20] ““Ndithu iwo akakudziwani (pamene mulipa), akugendani ndi miyala; apo ai akubwezerani ku chipeinbedzo chawo (chopotoka), zikatero ndiye kuti simudzapambananso mpaka kalekale.”

    [21] “(Koma anthu anazindikira pamene adaona ndalama yakale), momwemonso tidawazindikiritsa (kwa anthu) kuti adziwe kuti lonjezo la Allah (loukitsa ku imfa zolengedwa) nloona, ndikuti nthawi ya chimaliziro njosakaikitsa, (ndipo kumbukani) pamene adakangana pakati pawo pa chinthu chaochi, ena adati: “Mangani chomanga pa iwo (kuti anthu asamadze kudzawasuzumira), Mbuye wawo za iwo akudziwa bwino, koma amene adapambana paganizo lawolo adanena: “Ndithu ife timanga Msikiti wa iwowa (pa phanga lawoli).”

    [22] “(Ena) akhala akunena (kuti) adali anthu atatu, wachinayi ndi galu wawo; ndipo (ena) akuti adali asanu, wachisanu ndichimodzi ndigalu wawo. (Akunena) mwakungoganizira chabe zomwe sakuzidziwa; ndipo (ena) akuti adali asanu ndi awiri, ndipo wachisanu ndi chitatu ndi galu wawo. Nena: “Mbuye wanga ndiye akudziwa bwinobwino za chiwerengero chawo. Palibe amene akudziwa (za iwo) koma ndi ochepa chabe.” Choncho usatsutsane nawo za iwo, kupatula kutsutsana kwa pa zinthu zodziwika, ndipo usamfunse aliyense mwa iwo za iwo

    [23] “Ndipo usanene ngakhale pang’ono zachilichonse kuti: “Ndichita mawa.”

    [24] ““Koma (utsogoze liwu lakuti): Insha Allah, (Allah akafuna!)” Ndipo mukumbuke Mbuye wako ukaiwala ponena kuti: “Mwina Mbuye wanga anditsogolera pa njira yapafupi pachiongoko kuposa iyi.”

    [25] “Ndipo adakhala m’phanga lawolo (ali mtulo) zaka zikwi zitatu ndikuonjezera zisanu ndi zinayi

    [26] “Nena: “Allah akudziwa bwinobwino nyengo imene (iwo) adakhala; zobisika za kumwamba ndi za pansi nza Iye (Allah basi); taona Allah kuonetsetsa! Taona Allah kumvetsetsa! (Allah Ngoona chilichonse, ndipo Ngwakumva chilichonse). Ndipo iwo alibe mtetezi popanda Iye (Allah); ndipo Iye sagawira aliyense udindo Wake wakulamula

    [27] “Ndipo werenga zomwe zavumbulutsidwa kwa iwe za m’buku la Mbuye wako, palibe amene angathe kusintha mau Ake, ndipo nawe sungapeze potsamira ndi pothawira (kuti Allah asakupeze)

    [28] “Ndipo dzikakamize kukhala pamodzi ndi amene akupempha Mbuye wawo m’mawa ndi madzulo uku akufunafuna nkhope Yake (chiyanjo Chake), ndipo maso ako asachoke pa iwo ndi (kuyang’ana ena) ncholinga chofuna zokongoletsa za moyo wa dziko lapansi; ndipo usamumvere amene mtima wake tauiwalitsa kutikumbukira ndikumangotsatira zilakolako zake, ndipo zinthu zake nkukhala zotaika (zosalongosoka)

    [29] “Ndipo nena (kwa osakhulupirirawo, kuti): “Ichi ndi choonadi chimene chachokera kwa Mbuye wanu.” Choncho amene afuna, akhulupirire; ndipo amene afuna (kusachikhulupirira) asakhulupirire. Ndithu achinyengo tawakonzera Moto, womwe mipanda yake ikawazinga. Ndipo akakapempha chithandizo (chifukwa cha ludzu loopsya lomwe likawapeza), akathandizidwa popatsidwa madzi (otentha kwambiri) monga madzi a chitsulo chosungunuka, omwe adzasupula nkhope zawo. Taona kuipa chakumwa! ndi kuipa malo wotsamira

    [30] “Ndithu amene akhulupirira ndi kumachita ntchito zabwino, (tidzawalipira pa ubwino wawowo), ndithu Ife sitisokoneza malipiro a amene wagwira ntchito yabwino

    [31] “Iwo adzapeza minda yamuyaya; yomwe pansi (ndi patsogolo) pake pakuyenda mitsinje; m’menemo adzawakongoletsa powaveka zibangiri za golide, ndipo adzavala nsalu zobiriwira; zasilika wopyapyala ndi silika wokhuthala uku atatsamira makhushoni mmenemo. Taonani kukhala bwino malipiro! Ndi pamalo potsamira pokongola (popeza mpumulo wabwino)

    [32] “Ndipo apatse fanizo la anthu awiri mmodzi wa iwo tidampangira minda iwiri ya mphesa ndi kuizunguliza ndi mitengo ya kanjedza; ndipo pakati pa iyo tidaikapo mbewu (zina)

    [33] “Minda yonse iwiriyi idapatsa zipatso zake ndipo siidapungule chilichonse mzipatso zake. Ndipo pakati pake tidapititsapo mitsinje

    [34] “Ndipo iye adali ndi chuma (china) nati kwa mnzakeyo mokambirana naye: “Ine ndili ndi chuma chambiri kuposa iwe, (ndilinso) ndi mphamvu zambiri chifukwa cha onditsatira (omwe ndili nawo).”

    [35] “Ndipo adalowa m’munda mwake uku akudzichitira yekha zoipa. Adati: “Sindiganiza ngakhale mpang’ono pomwe kuti (munda) uwu udzaonongeka.”

    [36] ““Ndiponso sindiganiza kuti Qiyâma (chimaliziro) idzachitikadi. Ngati (itapezekadi Kiyamayo), ine nkubwezedwa kwa Mbuye wanga, ndithu ndikapeza malo abwino wobwererako kuposa awa. (Monga momwe ndapezera mwayi kuno, ukonso ndikapeza, ngati Kiyamayo ilikodi).”

    [37] “Mnzake adanena kwa iye mokambirana naye: “Kodi ukumukana yemwe adakulenga ndi dongo, kenako ndi dontho lamadzi a umuna ndiponso adakupanga kukhala munthu wolingana?”

    [38] ““Koma ine ndikukhulupirira kuti Iye ndi Mulungu Mbuye wanga, ndipo sindiphatikiza aliyense ndi Mbuye wanga.”

    [39] ““Ndipo pamene umalowa m’munda wako ukadanena kuti izi ndi zimene wandifunira Allah, mphamvu sizikadapezeka koma kupyolera mwa Allah (zikadakhala zabwino kwa iwe). Ngati ukundiona ine kuti ndili ndi chuma chochepa ndi ana ochepa kuposa iwe (koma sindisiya kutamanda Allah).”

    [40] ““Mwina Mbuye wanga angandipatse zabwino kuposa munda wakowo ndi kuutumizira mliri wachiphaliwali kuchokera kumwamba, ndipo ndikusanduka nthaka yotelera (yoguga).”

    [41] ““Kapena madzi ake nkumangophwa kotero kuti sungathe kuwapeza.”

    [42] “Tsono mliri unagwa pa zipatso zakezo (ndikuziononga motheratu), ndipo adayamba kutembenuza manja modandaulira zomwe adaonongera m’menemo; (mindayo) mitengo yake itagwera pansi. Ndipo adati: “Kalanga ine! Ndikadapanda kumphatikiza Mbuye wanga ndi aliyense (zoterezi sizikadachitika.)”

    [43] “Ndipo sadakhale ndi anthu omthangata pamene Allah adamtaya, ngakhale iye mwini sadadzithandize

    [44] “Pamalo potere chitetezo chimakhala cha Allah Yekha Woona. Iye Ngolipira bwino, ndiponso Wabwino (pakudza) ndi malekezero abwino

    [45] “Ndipo apatse fanizo la moyo wadziko lapansi, uli ngati madzi amene tikutsitsa kuchokera kumitambo kenako (madziwo) amasakanikirana ndi mmera wa m’nthaka (ndikuyamba kumera mokongola), kenako (mmerawo) nkukhala masamba ouma odukaduka omwe mphepo ikuwaulutsa uku ndi uku. Ndipo Allah ali ndi mphamvu pachilichonse

    [46] “Chuma ndi ana ndizokometsera za moyo wa dziko lapansi, koma ntchito zabwino zopitirira ndizo zabwino kwa Mbuye wako, monga mphoto ndi chiyembekezo chabwino

    [47] “Ndipo (akumbutse) tsiku lomwe tidzayendetsa mapiri (powaulutsa ngati ubweya mu mlengalenga), ndipo udzaiona nthaka ili tetetee, (itatambasuka yosakhwinyata ndi mapiri kapena zitunda), ndipo tidzawasonkhanitsa (tsiku limenelo), ndipo sitidzasiya aliyense mwa iwo (oyamba ndi omaliza)

    [48] “Ndipo adzabwera nawo kwa Mbuye wako atandanda m’mizere (ndikuuzidwa): “Ndithu mwatidzera monga tidakulengerani pachiyambi (opanda nsapato, amaliseche ndiponso opanda chilichonse chuma ndi ana). Koma mumaganiza kuti sitikuikirani lonjezo (ili louka ku imfa ndi kuweruzidwa).”

    [49] “Ndipo kaundula adzaikidwa (pamaso pawo), ndipo udzaaona oipa ali oopa chifukwa cha zomwe zili m’menemo, ndipo adzanena: “Kalanga ife taonongeka! Ngotani kaundula uyu, sasiya chaching’ono ngakhale chachikulu, koma zonse kuzilemba.” Ndipo adzapeza zonse zimene adazichita zitalembedwa m’menemo. Ndipo Mbuye wako sapondereza aliyense (pomusenzetsa zomwe sizake, kapena kumchitira zomwe sizikumuyenera)

    [50] “Ndipo (kumbuka) pamene tidawauza angelo: “Mchitireni sijida Adam (mugwadireni momulemekeza).” Onse adachitadi sijida kupatula Iblis. Iye adali mmodzi wa ziwanda, ndipo adatuluka m’chilamulo cha Mbuye wake. Kodi iye ndi mbumba yake mukuwalola kukhala abwenzi (anu) kusiya Ine, pomwe iwo ndiadani anu? Taonani kuipa kusintha kwa anthu oipa

    [51] “Sindidawachite (iwo) kukhala mboni nkulenga kwa thambo ndi nthaka, ngakhale kuwalenga kwawo ndipo sindidawalole osokeretsa kukhala athandizi (Anga)

    [52] “Ndipo (kumbukani) tsiku lomwe (Allah) adzanena: “Aitaneni aja omwe munkandiphatikiza nawo omwe munkati (ndi milungu inzanga).” Choncho, adzaiitana koma siidzawayankha; ndipo tidzaika chionongeko pakati pawo (ndipo sadzakumananso)

    [53] “Ndipo woipa adzauona moto (panthawi imeneyo) ndikutsimikiza kuti iwo alowa m’menemo. Ndipo sadzapeza pouzembera

    [54] “Ndipo ndithu tawafotokozera anthu mwatsatanetsatane m’Qur’aniyi fanizo la mtundu uliwonse; koma munthu wapambana chinthu chilichonse pa makani

    [55] “Ndipo palibe chimene chaletsa anthu kukhulupirira (tsopano) pamene chiongoko choonadi chawadzera ndikupempha chikhululuko kwa Mbuye wawo, koma akuyembekezera kuti chiwadzere chikhalidwe cha anthu oyamba, kapena chiwadzere chilango masomphenya

    [56] “Ndiponso sitituma atumiki (ndi cholinga choti adzetse chilango), koma kuti akhale onena nkhani zabwino ndi ochenjeza. Ndipo amene sadakhulupirire, akuchita makani ndi chabodza kuti kupyolera m’chabodzacho achotse choonadi, ndipo Ayah Zanga ndi zomwe achenjezedwa nazo, akuzichitira chipongwe

    [57] “Ndindani woipitsitsa kwabasi woposa yemwe akukumbutsidwa ndi Ayah za Mbuye wake, koma iye nkuzinyoza, ndipo nkuiwala (zoipa) zimene manja ake adatsogoza? Ndithu Ife taika m’mitima mwawo zitsekelero kuti asazizindikire. Ndiponso m’makutu mwawo mwalemedwa ndi ugonthi. Ndipo ukawaitanira kuchiongoko (choonadi), salola kuongoka ngakhale pang’ono

    [58] “Ndipo Mbuye wako Ngokhululuka kwambiri mwini chifundo. Ndipo akadawathira m’dzanja pa zoipa zomwe akhala akuchita, ndiye kuti ndithu akadawapatsa chilango mwachangu; koma iwo ali nalo lonjezo ndipo sadzapeza pothawira paliponse ndikulipewa

    [59] “Ndipo imeneyo ndi midzi tidawaononga (okhalamo) pamene adadzichitira zoipa; ndipo tidawaikira lonjezo la nthawi yoikidwa la kuonongeka kwawo

    [60] “Ndipo (kumbukani) pamene Mûsa adanena kwa mnyamata wake (Yusha’ Ibn Nun): “Ndipitiriza kuyenda kufikira ndikafike pamajiga pa nyanja ziwiri, kapena ndizingoyenda zaka ndi zaka (kufikira nditakumana naye amene ndikumfunayo).”

    [61] “Choncho pamene adafika pamajiga (pa nyanja ziwirizo) adaiwala nsomba yawo yomwe idatenga njira yake kunka m’nyanja ngati una (Mûsa adaiwala kumfunsa mnyamata wake za nsombayo; naye mnyamata adaiwala kumfotokozera Mûsa zomwe zidachitika ndi nsoinbayo)

    [62] “Pamene adapita patsogolo, adauza mnyamata wake, (kuti): “Tipatseni chakudya chathu chammawa; ndithu pa ulendo wathuwu takumana ndi zotopetsa.”

    [63] “(Mnyamata) adati: “Kodi mwaona pamene tidapumula paja, pathanthwe ndipomwe ndidaiwala (kuti ndikuuzeni) za nsombayo ndipo palibe wandiiwalitsa koma satana basi, kuti ndisaikumbukire. Iyo idatenga njira yake kunka m’nyanja, mododometsa.”

    [64] “(Mûsa) adati : “Pamenepo ndi pomwe timafuna.” Choncho adabwerera m’mbuyo potsatira njira yawo (yomweyo)

    [65] “Ndipo adampeza kapolo (Khidwiri) yemwe ndi m’modzi wa akapolo athu amene tidampatsa chifundo chochokera kwa Ife, (yemwenso) tidamphunzitsa maphunziro ambiri kuchokera kwa Ife

    [66] “Mûsa adati kwa iye: “Kodi ndingakutsate kuti undiphunzitse chiongoko chomwe waphunzitsidwa?”

    [67] “Adati: “Ndithu iwe siutha kupirira nane! (Uwona zomwe sungathe kupirira nazo).”

    [68] ““Kodi ungapirire bwanji ndi zinthu zomwe sukuzidziwa chinsinsi chake?”

    [69] “(Mûsa) adati: “Ngati Allah afuna, undipeza ndili wopirira; ndipo sindinyoza lamulo lako.”

    [70] “Adati: “Ngati unditsata usandifunse za chilichonse (chimene uchione) kufikira ine nditakuuza.”

    [71] “Choncho onse awiri adanyamuka kufikira pamene adakakwera m’chombo adachiboola. (Mûsa) adati: “Kodi wachiboola kuti uwamize ali m’menemo? Ndithu wachita chinthu chachikulu choipa.”

    [72] “Adati: “Kodi sindidanene kuti iwe sutha kupirira nane?”

    [73] “(Mûsa) adati: “Usandidzudzule chifukwa chakuiwala kwanga, ndipo usandipatse zovuta kwambiri pa khumbo langali (lofuna kukutsata).”

    [74] “Ndipo adanyamuka; mpaka pomwe adakumana ndi mnyamata wochepa, ndipo (mneneri Khidir) adamupha. Mûsa adati: “Ha! Wapha munthu wopanda cholakwa, pomwe sadaphe munthu mnzake? Ndithu wachita chinthu choipitsitsa.”

    [75] “۞ Adati: “Kodi sindidakuuze (kuti) ndithu iwe sutha kupirira nane?”

    [76] “(Mûsa) adati: “Ngati ndikufunsanso chilichonse pambuyo pa ichi, usandilole kutsagana nawe. Ndiye kuti wakwaniritsa dandaulo lako pa ine.”

    [77] “Choncho adamuka; kufikira pamene adawapeza eni mudzi ndipo adawapempha eni mudziwo chakudya, koma adakana kuwalandira monga alendo. Ndipo adapezamo khoma lili pafupi kugwa, (ndipo Khidhiriyo) adaliimika. (Mûsa) adati: “Ngati ukadafuna, ukadalandira malipiro (pa ntchitoyi kuti tigulire chakudya).”

    [78] “(Khidhiri) adati: “Awa ndiwo malekano pakati pa ine ndi iwe. Tsopano ndikuuza tanthauzo la zomwe sudathe kupirira nazo.”

    [79] ““Tsopano chombo chija, chidali cha masikini ogwira ntchito pa nyanja, ndipo ndidafuna kuchiononga (mwadala) chifukwa patsogolo pawo padali mfumu yomwe imatenga chombo chilichonse (chabwino) molanda.”

    [80] ““Ndipo mnyamata uja, makolo ake adali okhulupirira, ndipo tidaopera kuti angawachititse zoipa (makolo akewo) ndi za kusakhulupirira (mwa Allah)

    [81] “Choncho tidafuna kuti Mbuye wawo awasinthire ndi wabwino kuposa iye pa kuyera, ndi wachifundo chapafupi (kwa makolo ake.)”

    [82] ““Tsopano chipupa chija, chidali cha ana awiri amasiye mu mzindamo; ndipo pansi pake padali chuma chawo (chimene adawasiira bambo wawo) ndipo tate wawo adali munthu wabwino choncho Mbuye wako adafuna kuti akule misinkhu yawo ndipo adzadzitulutsire chuma chawocho; ichi ndi chifundo chochokera kwa Mbuye wako. Ndipo ine sindidachite zinthu zimenezi mwandekha. Limenelo ndilo tanthauzo la zomwe sudathe kupirira nazo.”

    [83] “Ndipo akukufunsa nkhani za Thul-Qarnain. Auze: “Ndikulakatulirani zina mwa nkhani zake.”

    [84] “Ndithu tidampatsa mphamvu zokhalira pa dziko ndikumpatsa njira yopezera chilichonse

    [85] “Choncho adatsata njira

    [86] “Mpaka pomwe adafika kumlowero kwa dzuwa (ku maiko a kuzambwe), adaliona (ngati) likulowa pa dziwe la matope ambiri. Ndipo pompo adapeza anthu; tidati: “E iwe Thul-Qarnain! Alange, kapena achitire zabwino.”

    [87] “Adati: “Koma amene achita zosalungama timulanga; ndipo kenako adzabwezedwa kwa Mbuye wake; ndipo akamukhaulitsa ndi chilango choipa

    [88] “Koma amene akhulupirire ndikuchita ntchito zabwino, apeza mphoto yabwino; ndipo timuuza zomwe zili zofewa m’zinthu zathu.”

    [89] “Kenako adatsata njira

    [90] “Mpaka adafika ku mtulukiro kwa dzuwa (ku maiko akuvuma). Adalipeza (dzuwalo) likuwatulukira anthu omwe sitidawaikire chowatchinga ku ilo

    [91] “Momwemo, tidali kudziwa bwino nkhani zonse zomwe zidali ndi iye

    [92] “Kenako adatsata njira

    [93] “Mpaka pomwe adafika pakatikati pa mapiri awiri adapeza pafupi ndi mapiriwo anthu omwe sikudali kwapafupi kumva chiyankhulo

    [94] “Adati: “E iwe Zul-Qarnain! Ndithu Yaajuju ndi Maajuju akuononga pa dziko. Kodi sikungatheke kuti tikupatse malipiro kuti uike pakati pathu ndi pakati pawo, chotchinga (mpanda)?”

    [95] “(Iye) adati: “Zomwe Mbuye wanga wandipatsa ndi zabwino. Choncho ndithandizeni ndi mphamvu zanu (zonse pantchito imeneyi) ndiika chotchinga cholimba pakati panu ndi pakati pawo.”

    [96] ““Ndipatseni zidutswa za zitsulo.” Kufikira pamene adadzaza ndi zitsulozo mpata umene udalipo pakati pa mapiri awiriwo, adati: “Pemelerani (moto).” Mpaka (chitsulocho) chidafiira monga moto, adati: “Ndibweretsereni mtovu wosungunuka ndiuthire pamwamba pake (pa chitsulocho).”

    [97] “Choncho (Yaajuju ndi Maajuju) sadathe kukwera pamwamba pake, ndiponso sadathe kuchiboola

    [98] “(Iye) adati: “Ichi ndi chifundo chochokera kwa Mbuye wanga; koma likadzafika lonjezo la Mbuye wanga (kudza kwa Qiyâma), adzachiswanyaswanya; ndipo lonjezo la Mbuye wanga nloona.”

    [99] “Ndipo patsiku limenelo tidzawasiya ena a iwo (oipa) akuchita chipolowe pa ena; ndipo lidzaimbidwa lipenga. Pamenepo tidzawasonkhanitsa onse pamodzi

    [100] “Ndipo tsiku limenelo, tidzayionetsa poyera Jahannam kwa osakhulupirira

    [101] “(Osakhulupirira) omwe maso awo adali ophimbidwa pakusalabadira ulaliki Wanga, ndipo sadali kutha kumva (zimene akuuzidwa)

    [102] “Kodi osakhulupirira akuganiza kuti angawasandutse akapolo Anga kukhala atetezi kusiya Ine? Ndithu taikonza Jahannam kukhala malo ofikirapo osakhulupirira

    [103] “Nena: “Kodi tikudziwitseni eni kuluza (kulephera) pa zochita zawo?”

    [104] ““Iwo ndi omwe khama lawo lataika m’moyo wa pa dziko lapansi, pomwe iwowo akuganiza kuti akuchita zabwino”

    [105] “Iwowo ndi amene sadakhulupirire zisonyezo za Mbuye wawo, ndipo (sadakhulupirire) zakukumana Naye. Choncho zochita zawo zaonongeka (zapita pachabe), ndipo pa tsiku la chiweruziro sitidzawaikira sikelo

    [106] “Zimenezo, mphoto yawo ndi Jahannam chifukwa cha kusakhulupirira kwawo, ndipo Ayah Zanga ndi atumiki Anga adazichitira chipongwe

    [107] “Ndithu amene akhulupirira ndikumachita zabwino, malo awo ofikira adzakhala ku minda ya “Firdaus.”

    [108] “Adzakhalamo nthawi yaitali. Ndipo sadzafuna kuchokamo

    [109] “Nena: “Ngakhale nyanja ikadakhala inki yolembera mawu a Mbuye wanga, nyanjayo ikadatha mawu a Mbuye wanga asadathe, ngakhale tikadabweretsa nyanja ina ndikuionjezera pa iyo (nyanjazo zikadatha, mawu a Allah akalipobe).”

    [110] “Nena: “Ndithu ine ndi munthu monga inu, (chosiyana nchakuti) ine ndikupatsidwa chivumbulutso (chonena kuti) ndithu Mulungu wanu ndi Mulungu mmodzi Yekha. Ndipo amene afuna kukumana ndi Mbuye wake, achite zochita zabwino ndipo asaphatikizepo aliyense pa mapemphero a Mbuye wake.”

    Mariamu

    Surah 19

    [1] “Kâf-Hâ-Yâ- ‘Aîn-Sâd

    [2] “Ichi (ndi) chikumbutso cha chifundo cha Mbuye wako pa kapolo Wake Zakariya

    [3] “Pamene adaitana Mbuye wake, kuitana kwa chinsinsi

    [4] “Adati: “E Mbuye wanga! Ndithu mafupa anga afooka, ndipo mutu wanga wayaka (ukung’anima) ndi imvi; sindidali watsoka pokupemphani Mbuye wanga (koma nthawi iliyonse ndikakupemphani mumandivomereza)

    [5] ““Ndipo ndithu ine ndikuopera abale anga (kuononga chipembedzo) pambuyo panga; ndipo mkazi wanga ndi chumba; choncho ndipatseni (mwana) mlowammalo wanga wochokera kwa Inu.”

    [6] ““Adzandilowe chokolo (pa nzeru za utsogoleri ndi uneneri) ndikulowanso ufumu wa banja la Ya’qub; ndipo Mbuye wanga nchiteni kukhala woyanjidwa (ndi Inu)”

    [7] “(Adauzidwa): “E iwe Zakariya! Ife tikukuuza nkhani yabwino yakuti ubereka mwana dzina lake Yahya palibe patsogolo pake amene tidamutcha dzina longa lake.”

    [8] “(Zakariya) adati: “Mbuye wanga! Ndingapeze bwanji mwana pomwe mkazi wanga ndi nkhalamba yosabereka ndipo ine ndafikanso pa ukulu wopyola muyeso?”

    [9] “Adati: “Ndimomwemo. Mbuye wako wanena (kuti): ‘Izi nzofewa kwa Ine; ndithu ndidakulenga kale pomwe iwe sudali kanthu.”

    [10] “Adati: “Mbuye wanga ndipatseni chizindikiro (chodziwitsa kuti mkazi wanga ali ndi pakati).” Adati: “Chizindikiro chako ndikuti sudzatha kuyankhula ndi anthu mpaka masiku atatu pomwe iwe uli bwinobwino.”

    [11] “Ndipo adatuluka kuchipinda chopemphelera ndikuonekera kwa anthu ake, ndipo adawalozera (pomwe sadathe kuyankhula) kuti: “Lemekezani Allah m’mawa ndi madzulo.”

    [12] ““E iwe Yahya! Gwira buku ili mwamphamvu (ndi mwachidwi).” Ndipo tidampatsa nzeru ali mwana

    [13] “Ndi chisoni chochokera kwa Ife ndi kumuyeretsa (mwanayo), ndipo adali woopa (Allah)

    [14] “Komanso wochitira zabwino makolo ake ndipo sadali wodzitukumula (kwa anthu) kapena kunyoza (Allah)

    [15] “Ndipo mtendere wa Allah udali pa iye kuyambira tsiku lomwe adabadwa ndi tsiku lomwe adamwalira, ndi tsiku limene adzaukitsidwa ku imfa kukhala wamoyo

    [16] “Ndipo mtchule Mariya m’buku ili pamene adadzipatula ku anthu a kubanja lake (ndikunka) kumalo ambali ya kummawa

    [17] “Ndipo adadzitsekereza kwa iwo (kuti athe kutumikira Allah mokwanira), choncho tidatuma Mzimu Wathu (Mngelo Gabriel) kwa iye ndipo adadzifanizira kwa iye monga munthu weniweni

    [18] “(Mariya) adati: “Ndithu ndikudzichinjiriza ndi (Allah) Mwini chifundo chambiri, kwa iwe ngati umaopa (Allah).”

    [19] “(Mngelo) adati: “Ndithu ine ndine Mtumiki wa mbuye wako, (ndadza) kuti ndikupatse mwana woyera.”

    [20] “Adati: “Ndingakhale bwanji ndi mwana pomwe sadandikhudze mwamuna (aliyense), ndipo ine sindili (mkazi) wachiwerewere?”

    [21] “(Mngelo) adati: “Ndimomwemo.” Mbuye Wako akuti: “Zimenezi kwa Ine nzosavuta. Ndipo timchita kukhala chozizwitsa kwa anthu ndi chifundo chochokera kwa Ife. (Nchifukwa chake tachita izi;) ndipo ichi ndi chinthu chimene chidalamulidwa kale. (Chichitika monga momwe Allah adafunira).”

    [22] “Choncho adatenga pakati pake, ndipo adachoka ndi pakatipo kunka kumalo akutali

    [23] “Ndipo matenda auchembere (atakwana), adampititsa ku thunthu la mtengo wa kanjedza (wouma kuti awutsamire pomubala mwanayo) adati: “Kalanga ine! Ndiponi ndikadafa izi zisanachitike ndikadakhala nditaiwalidwa ndithu.”

    [24] “Kenaka (Mngelo) adamuitana kuchokera chapansi pake (kumuuza kuti): “Usadandaule. Ndithu Mbuye wako wakupangira kamtsinje pansi pako.”

    [25] “Ndipo ligwedezere kumbali yako thunthu la mtengo wakanjedza (woumawo), zipatso zabwino zakupsa zikugwera.”

    [26] “Choncho udye ndi kumwa ndikutonthoza diso lako, (khala ndi mpumulo wabwino). Ndipo ukaona munthu aliyense (akafunsa za mwanayo), nena: “Ndithu ine ndalonjeza kwa (Allah) Mwini chifundo chambiri kusala kuti lero sindiyankhula ndi munthu aliyense.”

    [27] “Ndipo adadza naye (mwanayo) kwa anthu ake atamnyamula. (Anthu) adati: “E iwe Mariya! Ndithu wabwera ndi chinthu chachikulu; (chododometsa).”

    [28] ““E iwe mlongo wa Harun! Bambo wako sadali munthu woipa, ngakhalenso mayi wako sadali wachiwerewere.”

    [29] “(Mariya sadawayankhe) koma adaloza kwa iye (mwanayo kuti ayankhule naye). Ndipo iwo adati: “Timuyankhula chotani mwana yemwe ali m’chikuta?”

    [30] “(Mwanayo) adanena: “Ine ndine kapolo wa Allah. Wandipatsa buku ndikundichita kukhala Mneneri.”

    [31] ““Ndipo wandichita kukhala wodala paliponse pomwe ndili, ndipo wandilamula kuswali ndi kupereka Zakaat pomwe ndili moyo.”

    [32] ““Ndipo wandilangiza kuchitira mayi wanga zabwino, ndipo sadandichite kukhala wodzikuza, watsoka (woipa).”

    [33] ““Ndipo mtendere uli pa ine kuyambira tsiku lomwe ndidabadwa ndi tsiku limene ndidzamwalira, ndi tsiku limene ndidzaukitsidwa (kwa akufa tsiku la chiweruziro) ndikukhala ndi moyo.”

    [34] “Uyu ndi Isa (Yesu) mwana wa Mariya; (awa ndi) mau owona omwe (Akhrisitu) akuwakaikira

    [35] “Sikoyenera kwa Allah kudzipangira mwana. Iye (Allah) wapatukana ndi zimenezi. Akafuna chinthu, amangonena kwa chinthucho: “Chitika,” ndipo icho chimachitikadi

    [36] “(Isa (Yesu) adati:) “Ndipo ndithu Allah ndi Mbuye wanga ndiponso Mbuye wanu. Choncho mpembedzeni; iyi ndinjira yolunjika (yokufikitsani ku mtendere)

    [37] “Koma magulu (a Akhrisitu ndi Ayuda) adapatukana pakati pawo; (ena adamuyesa Isa (Yesu) kuti ndimwana wa Mulungu, ndipo ena adamuyesa Mulungu weniweni, pomwe Ayuda ankati ndi mwana wobadwa m’njira ya chiwerewere), choncho chilango chaukali chidzatsimikizika pa amene sadakhulupirire pokaonekera tsiku lalikululo (kwa Allah)

    [38] “Taona kumvetsetsa kwawo ndi kupenyetsetsa kwawo tsiku lodzatidzera, (kudzanenedwa kuti:) “Koma osalungama lero ali m’kusokera koonekera.”

    [39] “Ndipo achenjeze (anthu) za tsiku la madandaulo, pamene chiweruzo chidzagamulidwa, (abwino kulowa ku munda wamtendere, oipa kulowa ku Moto); koma iwo (pano pa dziko lapansi) ali m’kusalabadira ndipo sakhulupirira

    [40] “Ndithu Ife Tidzaitenga nthaka ndi amene ali pamenepo; (zonse zidzakhala za Ife) ndipo kwa Ife adzabwerera

    [41] “Ndipo mtchule m’buku ili, Ibrahim. Ndithu iye adali wonena zoona zokhazokha, Mneneri

    [42] “(Akumbutse) pamene iye adauza bambo wake: “E inu bambo wanga! Bwanji mukupembedza zomwe sizimva ndiponso sizipenya, ndiponso Zosakupindulitsani chilichonse?”

    [43] ““E inu bambo wanga! Ndithu ine zandidzera nzeru (zomuzindikira Allah) zomwe sizidakudzereni; choncho nditsateni. Ndikutsogolereni ku njira yolungama.”

    [44] ““E bambo wanga! Musapembedze satana (potsatira malangizo ake). Ndithu satana ngopandukira (Allah) Mwini chifundo chambiri.”

    [45] “E bambo wanga! Ndithu ine ndikuopa kuti chilango chingakukhudzeni chochokera kwa (Allah) Mwini chifundo chambiri, ndipo potero mdzakhala bwenzi la satana.”

    [46] “(Bambo wake) adati: “Kodi iwe ukuda milungu yanga, E iwe Ibrahim? Ngati susiya (kunyoza milungu yanga) ndikugenda ndi miyala; choncho ndichokere kwa nthawi yaitali (tisaonanenso).”

    [47] “(Ibrahim) adati: “Mtendere ukhale pa inu! Ndikupempherani chikhululuko kwa Mbuye wanga (ngakhale mwandipirikitsa). Ndithu iye amandichitira chisoni kwambiri.”

    [48] ““Ndipo ine ndikupatukirani ku zomwe mukuzipembedzazo kusiya Allah ndipo ndipempha Mbuye wanga; ndithu sindikhala watsoka popempha Mbuye wanga.”

    [49] “Ndipo pamene adawapatukira ndi zimene adali kuzipembedza kusiya Allah, tidampatsa iye Ishaq, ndi Ya’qub, ndipo aliyense wa iwo tidampanga kukhala m’neneri

    [50] “Ndipo tidawapatsa iwo chifundo Chathu, ndi kuwayikira iwo kutchulidwa kwabwino, kwapamwamba (pakati pa zolengedwa)

    [51] “Ndipo mtchule Mûsa m’buku (ili). Ndithu iye adali wosankhidwa ndi woyeretsedwa: ndipo adali Mtumiki M’neneri

    [52] “Ndipo tidamuitana kumbali yakudzanjadzanja la phiri la Turi, ndipo tidamuyandikitsa ndi kuyankhula Nafe momunong’ oneza

    [53] “Ndipo mwachifundo Chathu tidampatsa (Mûsa) m’bale wake Harun kukhala mneneri (womuthangata)

    [54] “Mtchulenso m’buku (ili) Ismaila; ndithu iye adali woona palonjezo, ndipo adali Mtumiki Mneneri

    [55] “Adali kulamula anthu ake Swala ndi Zakaat, ndipo kwa Mbuye wake adali woyanjidwa

    [56] “Mtchulenso m’buku (ili) Idris, ndithu iye adali wonena zoona zokhazokha, Mneneri

    [57] “Ndipo tidamunyamula (kumuika pa) malo apamwamba

    [58] “Iwowo ndi omwe adawadalitsa Allah, mwa aneneri mu ana a Adam, ndi (m’mbumba ya) amene tidawatenga pamodzi ndi Nuh (m’chombo), ndi m’mbumba ya Ibrahim ndi Israyeli, ndi amene tidawaongola ndi kuwasankha. Ndipo zikawerengedwa kwa iwo Ayah za (Allah) Mwini chifundo chambiri, amagwa ndi kulambira uku akulira

    [59] “Koma pambuyo pa iwo padadza anthu oipa. Adasokoneza Swala (adasiya kupemphera) natsatira zilakolako zoipa; choncho adzakumana ndi chilango choipa

    [60] “Kupatula amene ati alape ndikukhulupirira ndikuchita zabwino; iwowo adzalowa ku Munda wamtendere ndipo sadzachitidwa chinyengo pa chilichonse

    [61] “Munda wamuyaya umene (Allah) Wachifundo chambiri walonjeza akapolo Ake mobisika, ndithu lonjezo Lake ndilakudza

    [62] “Sakamva m’menemo mawu achibwana, koma mawu a mtendere; ndipo akapeza rizq (chakudya) lawo m’menemo m’mawa ndi madzulo

    [63] “Umenewo ndiwo Munda wamtendere umene tikawapatsa ena mwa akapolo athu omwe adali oopa Allah

    [64] “(Mtumiki adapempha Gabriel kuti akhale akum’bwerera pafupipafupi. Ndipo Gabriel adamuuza kuti): “Ndipo sitimatsika koma mwa lamulo la Mbuye wako. Zapatsogolo pathu ndi zapambuyo pathu ndi zapakati pa zimenezi zonse Nzake (akuzidziwa bwinobwino). Ndipo Mbuye wako sali woiwala.”

    [65] ““Mbuye wa thambo ndi nthaka ndi zapakati pa izo: Choncho mpembedze Iye basi. Ndipo pitiriza ndikupirira popembedza Iye. Kodi ukumudziwa (wina) yemwe ali wofanana Naye (Allah)?”

    [66] “Ndipo munthu (wokanira) amanena: “Kodi ndikadzafa nzoonadi kuti Ndidzatulutsidwa (m’manda) nkukhala wamoyo?”

    [67] “Kodi munthu sakumbukira kuti tidamulenga kale pomwe sadali chilichonse

    [68] “Choncho ndikulumbira Mbuye wako, ndithu tidzawasonkhanitsa iwo pamodzi ndi asatana; ndipo tidzawafikitsa m’mphepete mwa Jahannam uku atagwada

    [69] “Kenako, m’gulu lililonse tidzachotsamo yemwe adali wopyola malire polakwira (Allah) Mwini chifundo chambiri

    [70] “Ndipo Ife tikuwazindikira kwambiri amene ali oyenera kulowa m’Moto

    [71] “Ndipo palibe aliyense mwa inu koma adzaifika (Jahannamyo). Ndithu ili ndi lamulo la Mbuye wako lomwe lidalamulidwa kale

    [72] “Ndipo kenako tidzawapulumutsa amene ankaopa Allah, ndipo osalungama tidzawasiya m’menemo atagwada

    [73] “Ndipo Ayah Zathu zomveka bwino zikawerengedwa kwa iwo, omwe sadakhulupirire amanena kwa omwe akhulupirira: “Ndi gulu liti pa magulu awiri awa, (lanu ndi lathu) lomwe lili ndi pokhala pabwino ndikukhalanso ndi anthu olemekezeka?”

    [74] “Ndipo mibadwo yambiri tidaiononga patsogolo pawo, yomwe idali ndi ziwiya zabwino ndi maonekedwe abwino

    [75] “Nena: “Amene ali mkusokera, (Allah) Mwini chifundo chambiri amuonjezera nthawi yamoyo kufikira azione zomwe akulonjezedwa - kapena chilango kapena kudza nthawi (ya Qiyâma) - pamenepo ndipomwe adzadziwa kuti ndani mwini kukhala pamalo poipa, ndi mwini wa ankhondo ofooka (iwo kapena Asilamu)?”

    [76] “Ndipo Allah amawaonjezera chiongoko amene aongoka. Ndipo zochita zabwino zonkerankera (mpaka tsiku lachimaliziro), ndizo zili zabwino kwa Mbuye wako monga mphoto, ndiponso ndiko kobwerera kwabwino, (osati za mdziko zomwe anthu osalungama akunyadira)

    [77] “Kodi wamuona yemwe watsutsa Ayah Zathu ndikunena kuti: “Ndithu ndidzapatsidwa chuma ndi ana (pa tsiku lachimaliziro monga momwe andipatsira pano pa dziko?)”

    [78] “Kodi adadziwa zamseri, kapena adalandira lonjezo kwa Allah mwini chifundo Chambiri (kotero kuti ali ndi chikhulupiliro pa zimene akunenazo)

    [79] “Sichoncho, ndithu tikulemba zonse zomwe akunena, ndipo tidzamuonjezera nyengo yotalika m’chilango

    [80] “Ndipo tidzamlowa mmalo zimene akunenazi, (chuma ndi anawo), nadzatidzera ali yekhayekha (wopanda chuma ndi zonse zomwe ankanyadira)

    [81] “Eti adzipangira milungu ina m’malo mwa Allah kuti milunguyo iwapatse mphamvu (ndi ulemelero)

    [82] “Iyayi! Idzawakanira mapemphero awo ndikuwaukira

    [83] “Kodi suona kuti Ife timawatuma asatana kwa osakhulupirira ndipo akuwakhwirizira kwambiri (kuchita zoipa)

    [84] “Choncho, usawachitire changu (kuti alangidwe tsopano), ndithu Ife tikuwawerengera chiwerengero (cha masiku awo; masiku akakwana, tiwalanga)

    [85] “(Kumbukira iwe Mtumiki) tsiku lomwe tidzawasonkhanitsa oopa (Allah) kunka nawo kwa Mwini chifundo Chambiri ali m’magulumagulu monga nthumwi (Zake kuti apatsidwe ulemu)

    [86] “Ndipo oipa tidzawakusa kunka nawo ku Moto ali ndi ludzu lalikulu monga momwe ziweto zimathamangira kupita kumadzi zikakhala ndi ludzu lalikulu

    [87] “Sadzakhala ndi mphamvu yoombolera (ena) koma kupatula omwe adagwiritsa lonjezo la (Allah) Mwini chifundo chambiri

    [88] “Ndipo (osakhulupirira omwe ndi Ayuda ndi Akhirisitu) akuti: “(Allah) Mwini chifundo chambiri wadzipangira mwana!”

    [89] “Ndithu mwadza ndi chinthu choipitsitsa (pazimene mukunenazi)

    [90] “Thambo layandikira kusweka ndi mawuwo, ndipo nthaka kuphwasuka, ndipo mapiri kugwa ndikudukaduka

    [91] “Chifukwa chakumunamizira (Allah) Mwini chifundo chambiri kuti ali ndi mwana

    [92] “Ndipo nkosayenera kwa (Allah) Mwini Chifundo chambiri kudzipangira mwana

    [93] “Palibe aliyense yemwe ali kumwamba ndi pansi koma adzadza kwa (Allah) Mwini Chifundo chambiri ali kapolo (Wake)

    [94] “Ndithu (Allah) wawadziwa mokwanira ndipo adzawawerenga aliyense payekhapayekha

    [95] “Ndipo, aliyense wa iwo adzadza kwa Iye (Allah) ali payekhapayekha

    [96] “Ndithu amene akhulupirira ndikumachita zabwino, (Allah) Mwini chifundo chambiri adzaika chikondi pakati pawo

    [97] “Ndithu taifewetsa (Qur’an) m’chiyankhulo chako kuti ndi iyo uwawuze nkhani zabwino oopa Allah ndipo ndi iyo uwachenjeze anthu amakani

    [98] “Kodi ndi mibadwo ingati tidaiononga patsogolo pawo? Kodi ukumuona mmodzi wa iwo, kapena ukumva mgugu wawo

    Ta-Ha

    Surah 20

    [1] “Tâ-Hâ

    [2] “Sitidakuvumbulutsire iwe Qur’an kuti uvutike (nayo)

    [3] “Koma kuti ikhale ulaliki ndi chikumbutso kwa yemwe akuopa (ndikudzichepetsa kwa Allah)

    [4] “Chovumbulitsidwa chochokera kwa Yemwe adalenga nthaka ndi thambo lotukuka kumwamba

    [5] “(Iye ndi Allah), Wachifundo Chambiri; pa Arsh (Mpando wachifumu) adakhazikika, (kukhazikika koyenerana ndi ulemelero Wake kopanda kukufanizira ndi kukhazikika kwa chilichonse; pakuti Iye salingana ndi chilichonse pa chikhalidwe ndi mbiri Zake)

    [6] “Zonse za kumwamba ndi za pansi ndi za pakati pake ndi za pansi pa nthaka, nza Iye

    [7] “Ndipo ngati ulankhula mokweza mawu, (iwe munthu), ndithu Iye akudziwa zobisika ndi zobisika kwambiri (zomwe mwazibisa mu mtima mwanu)

    [8] “Allah! Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Iye ali ndi maina abwino (ndi mbiri zabwinonso)

    [9] “Ndipo kodi yakufika nkhani ya Mûsa? (Yomwe njododometsa)

    [10] “Pamene adaona moto adauza banja lake: “Yembekezani (pano); ndithu ndaona moto; mwina ndingakakutengereni chikuni chamoto (kuti muothe), kapena ndikapeza ondiongolera njira pa motopo

    [11] “Koma pamene adaudzera motowo Anaitanidwa (kuti), “E, iwe Mûsa

    [12] “Ndithu ine ndine Mbuye wako! Vula nsapato zakozo; ndithu iwe uli pa chigwa chopatulika, chotchedwa Tuwa.”

    [13] “Ndipo Ine ndakusankha (kuti ukhale Mtumiki); choncho mvera zonse zomwe zikuvumbulutsidwa (kwa iwe)

    [14] “Ndithu Ine ndine Allah palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Ine; choncho ndipembeze, pemphera Swala moyenera pondikumbukira

    [15] “Ndithu nthawi ya tsiku lachimaliziro idza; (choncho ikonzekere ndi ntchito zabwino); ndikuibisa dala (kwa anthu) kuti mzimu uliwonse udzalipidwe zimene udachita

    [16] “Ndipo asakutsekereze (ku khulupirira) zimenezo yemwe saikhulupirira (Kiyamayo), ndipo akungotsata zilakolako za mtima wake; kuopa kuti Ungadzaonongeke.”

    [17] ““Kodi nchiyani icho chili kudzanja Lako ladzanjadzanja, iwe Mûsa?”

    [18] “(Mûsa) adati: “Iyi ndi ndodo yanga, ndimaitsamira (poyenda) ndi kuphopholera masamba a mbuzi zanga; ndiponso (m’ndodomo) muli zina zondithandiza.”

    [19] “(Allah) adati: “Iponye iwe Mûsa!”

    [20] “Ndipo adaiponya; pompo idasanduka njoka yoyenda mothamanga

    [21] “(Allah) adati: “Igwire, usaope. Tiibwezera m’chikhalidwe chake Choyamba.”

    [22] ““Ndipo lipane dzanja lako m’khwapa mwako lituluka lili loyera (ngati kuwala kwadzuwa ndi mwezi). Osati mwamatenda, (ichi chikhala) chozizwitsa china.”

    [23] ““Kuti tikusonyeze zina mwa zozizwitsa zathu, zazikuluzikulu.”

    [24] ““Pita kwa Farawo, ndithu iye wapyola malire.”

    [25] “(Mûsa) adati: “E Mbuye wanga! Nditsakulireni chifuwa changa.”

    [26] ““Ndi kundifewetsera ntchito yangayi (imene mwandipatsa kuti uthengawu ndikaufalitse m’njira yoyenera).”

    [27] ““Ndipo masulani mfundo yomwe ili ku lirime kwanga, (ndimasulireni kumangika kwa lirime langa kuti mawu anga akakhale opanda chibwibwi).”

    [28] ““Kuti (anthu) akamvetse mawu anga.”

    [29] ““Ndipo ndipatseni nduna (mthandizi) yochokera kubanja langa.”

    [30] ““M’bale wanga Harun.”

    [31] ““Limbitsani nyonga zanga ndi iye.”

    [32] ““Ndipo mphatikeni ku ntchito yangayi.”

    [33] ““Kuti tikulemekezeni kwambiri.”

    [34] ““Ndi kukutamandani kwabasi.”

    [35] ““Ndithu inu (nthawi zonse) mumationa (ndi kutisunga).”

    [36] “(Allah) adati: “Ndithu wapatsidwa zomwe wapempha, E, iwe Mûsa.”

    [37] ““Ndipo ndithu tidakuchitira ubwino nthawi ina (popanda iwe kutipempha).”

    [38] ““Pamene mayi wako tidamuzindikiritsa zimene tidamzindikiritsa (kuti azichite).”

    [39] “(Kuti): “Mponye (mwanayo) m’bokosi ndipo ponya bokosilo mu mtsinje; ndipo mtsinje umponya m’mbali kuti amtenge mdani wanga ndi mdani wake (ndi kuti aleredwe mwaubwino ndi Farawo); ndipo ndidaika kukondeka pa iwe kochokera kwa Ine (kuti ukhale wokondedwa ndi anthu onse) ndikuti uleredwe moyang’aniridwa ndi Ine.”

    [40] “(Kumbuka) pomwe mlongo wako ankayenda (kunka kubanja la Farawo) Ndipo adati: “Kodi ndikulondolereni munthu amene angathe kumlera?” Ndipo tidakubwezera kwa mayi wako kuti maso ake atonthole, ndipo asadandaule. Ndipo kenaka udapha munthu (mwangozi), ndipo tidakupulumutsa ku madandaulo; tidakuyesa ndi mayeso ambiri. Udakhala zaka zambiri ndi anthu a ku Madiyan. Kenaka wabwera (apa) monga mwachikonzero, E, iwe Mûsa

    [41] “Ndipo ndakusankha ndekha (kuti ukhale Mtumiki Wanga)

    [42] “Pita iwe ndi m’bale wako ndi zozizwitsa Zanga, ndipo musatope (musasiye) kundikumbukira

    [43] “Pitani kwa Farawo, ndithu iye wapyola malire

    [44] “Kamuuzeni mawu ofewa mwina akalingalira (uthengawo) kapena akaopa

    [45] “(Iwo) adati: “Mbuye wathu ndithu ife tikuopa kuti angatimbwandire kapena kutipyolera malire (tisananene kanthu).”

    [46] “(Allah) adati: “Musaope. Ndithu Ine ndili nanu pamodzi. ndikumva, ndiponso ndikuona.”

    [47] “Choncho mpitireni, ndikumuuza (kuti): “Ndithu ife ndife atumiki a Mbuye wako. Asiye ana a Israyeli achoke ndi ife, ndipo usawazunze; ndithu takudzera ndi chozizwitsa chochokera kwa Mbuye wako (chomwe ndi mboni yathu pa zomwe tikukuuzazi), ndipo mtendere ukhala pa yemwe atsate chiwongoko.”

    [48] ““Ndithu zavumbulutsidwa kwa ife kuti chilango chiwapeza amene akutsutsa (zimenezi) ndikuzitembenukira kumbali.”

    [49] “(Farawo) adati: “Kodi Mbuye wanu ndani, iwe Mûsa?”

    [50] “(Mûsa) adati: “Mbuye wathu ndi yemwe adapatsa chinthu chilichonse chilengedwe chake, kenako adachiongolera (kutsata chimene chikulingana ndi chilengedwe chake).”

    [51] “(Farawo) adati: “Nanga mibadwo yakale ili bwanji, (imene idapita iwe usadadze?”)

    [52] “(Mûsa) adati: “Kudziwa kwa zimenezo nkwa Mbuye wanga, m’kaundula (Wake momwe mwasonkhanitsidwa chilichonse), Mbuye wanga sasokera, ndipo saiwala

    [53] “Yemwe adakupangirani nthaka monga choyala, ndipo m’menemo adakuikirani njira ndikutsitsa madzi kuchokera kumwamba.” Ndipo kupyolera m’madziwo tidameretsa mmera wosiyanasiyana

    [54] “Idyani ndikudyetsa ziweto zanu. Ndithu m’zimenezo muli zisonyezo kwa eni nzeru

    [55] “Kuchokera (m’nthaka) umu tidakulengani, ndipo momwemo tidzakubwezani, ndipo kuchokera m’menemo tidzakutulutsani nthawi ina (muli moyo)

    [56] “Ndipo, ndithu tidamuonetsa (Farawo) zozizwitsa zathu zonse, koma adatsutsa ndipo adakana

    [57] “Adati: “Kodi watidzera kuti utitulutse m’dziko lathu, ndi matsenga ako, E, iwe Mûsa

    [58] “Choncho nafe tikubweretsera matsenga onga amenewo! Choncho ika lonjezo (la msonkhano) pakati pathu ndi iwe; lonjezo lomwe tisaliswe ife ndi iwe, (tidzakumane) pamalo poyenera.”

    [59] “(Mûsa) adati: “Lonjezo lanu likhale pa tsiku lodzikongoletsa (tsiku la chikondwelero), ndipo anthu adzasonkhanitsidwe m’mawa.”

    [60] “Ndipo Farawo adabwerera ndikusonkhanitsa matsenga ake, ndipo kenako adabwera (ndi amatsenga ake pa tsiku la chipanganolo)

    [61] “Mûsa adawauza: “Tsoka kwa inu! Musampekere bodza Allah, kuopera kuti angakuphwasuleni ndi chilango. Ndipo, ndithu wataika amene akupeka bodza.”

    [62] “Choncho (amatsengawo) adakangana pakati pawo pa zinthu zawo ndipo adakambirana mwachinsinsi

    [63] “(Iwo) adati (mkunong’onezana kwawo): “Ndithu anthu awiriwa ndi amatsenga; kupyolera mmatsenga awo akufuna kukutulutsani m’dziko mwanu, ndikuchotsa chikhalidwe chanu chomwe chili chabwino.”

    [64] ““Choncho sonkhanitsani matsenga anu (onse), kenako mudze (kwa iwo) mutandanda pamzere; ndithu lero, apambana amene akhale wapamwamba.”

    [65] “(Iwo) adati: “E iwe Mûsa! Kodi ukhale ndiwe woyamba kuponya (matsenga ako), kapena tikhale oyamba ndife kuponya?”

    [66] “(Mûsa) adati: “Koma inu ndinu muponye!” (Choncho adaponya matsengawo). Mwadzidzidzi zingwe zawo ndi ndodo zawo zamatsenga awo, zimaoneka pamaso pake (Mûsa) kuti zikuyenda mothamanga

    [67] “Ndipo Mûsa adadzazidwa ndi mantha mu mtima mwake

    [68] “Tidati: “Usaope (zomwe ukuzionazi), ndithu iwe ukhala wopambana.”

    [69] ““Ndipo ponya chimene chili kudzanja lako ladzanjadzanja (ndodo); chimeza zomwe apanga; ndithu iwo apanga matsenga a mfiti ndipo mfiti siingapambane paliponse pamene yadza.”

    [70] “Choncho amatsenga adagwa molambira uku akuti: “Tamkhulupirira Mbuye wa Harun ndi Mûsa.”

    [71] “(Farawo) adanena: “Ha! Mwamkhulupirira ndisadakupatseni chilolezo? Ndithu iye ndi mkulu wanu amene adakuphunzitsani matsenga! Choncho ndikudulani manja anu ndi miyendo yanu, mosemphanitsa:; (dzanja lakudzanjadzanja ndi mwendo wakumanzere. Pomwe wina, mkono wakumanzere ndi mwendo wakudzanjadzanja), ndipo kenako ndikupachikani pa mathunthu a mitengo ya kanjeza; ndithu mudziwa (panthawiyo) kuti ndani mwa ife, (ine kapena Mulungu wa Mûsa), wachilango chaukali ndi chopitilira.”

    [72] “(Amatsenga) adati: “Sitisankha iwe kusiya zomwe zatidzera; zisonyezo zachoonadi zoonekera poyera! Ndipo tikumlumbilira Yemwe adatilenga, (sitikusankha iwe), chita zomwe ufuna kuchita; ndithu iwe utha kupititsa chiweruzo chokhudzana ndi moyo uno wapansi, basi.”

    [73] ““Ndithu takhulupirira Mbuye wathu kuti atikhululukire zolakwa zathu ndi matsenga amene watikakamiza (kuchita); ndipo Allah ndi Yemwe ali Wabwino ndi Wamuyaya (osati iwe).”

    [74] “Ndithu amene adzadze kwa Mbuye wake uku ali wamachimo, adzapeza moto wa Jahannam; sadzafa m’menemo, ndipo sadzakhalanso ndi moyo wabwino

    [75] “Koma amene adzamdzera uku ali wokhulupirira, yemwe adachita ntchito zabwino, iwo ndi amene adzapeze ulemewero wapamwamba

    [76] “Minda yamuyaya, yomwe pansi pake (ndi patsogolo pake) pakuyenda mitsinje. Adzakhala mmenemo nthawi yaitali. Ndipo zimenezo ndi mphoto za yemwe wadziyeretsa

    [77] “Ndipo ndithu Mûsa tidamtumizira chivumbulutso, (tidamzindikiritsa kuti): “Yenda usiku ndi akapolo Anga (kutuluka m’dziko la Iguputo,) ndipo ukawapangire panyanja njira youma, ndipo usaope kukupeza adani ndiponso usaope (kumira).”

    [78] “Choncho Farawo pamodzi ndi ankhondo ake, adawatsata, ndipo m’nyanjamo chidawaphimba chimene chidawaphimba

    [79] “Ndipo Farawo adawasokeretsa anthu ake, ndipo sadawaongolere

    [80] “E inu ana a Israyeli! Ndithu tidakupulumutsani kwa mdani wanu, ndipo tidakulonjezani (kuti mudze) mbali yakudzanjadzanja ya phiri (kuti tikupatseni malamulo ndi zina), ndipo tidakutsitsirani Manna ndi Saluwa

    [81] “Idyani zinthu zabwino zomwe takupatsani, ndipo musapyole malire pa zimenezo kuti mkwiyo Wanga usakutsikireni; ndipo amene mkwiyo Wanga wamtsikira, ndiye kuti ameneyo waonongeka

    [82] “Ndipo ndithu Ine ndi Wokhululuka kwambiri kwa amene walapa ndi kukhulupirira, ndikuchita ntchito zabwino, kenako ndikutsata chiongoko mwaubwino

    [83] ““Nchiyani chakufulumizitsa (kudza kuno) kusiya anthu ako, E, iwe Mûsa?”

    [84] “Adati: “Iwo ali pambuyo panga akunditsata. Ndachita changu kudza kwa Inu, Mbuye wanga, kuti mundiyanje kwambiri.”

    [85] “(Allah) adati: “Ndithu Ife tawayesa Mmayeso anthu ako pambuyo pako; tero Samiriyyu wawasokeretsa.”

    [86] “Mûsa adabwerera kwa anthu ake ali wokwiya ndi wodandaula. Adati: “E inu anthu anga! Kodi Mbuye wanu sadakulonjezeni lonjezo labwino? Kapena nyengo yalonjezolo idatalika kwa inu? Kapena mudafuna kuti mkwiyo ukutsikireni kuchokera kwa Mbuye wanu; tero mwaswa lonjezo langa”

    [87] “(Iwo) adati: “Sitidaswe lonjezo lako mwachifuniro chathu; koma tidasenzetsedwa mitolo ya zodzikometsera za anthu (ziwiya zagolide zomwe tidabwereka kwa akazi a chimisiri), ndipo tidaziponya (pa moto, ndipo zidasungunuka ndikupangidwa mwana wang’ombe.) Ndipo momwemonso Samiriyyu adaponya.”

    [88] “Ndipo adawatulutsira (kuchokera m’golide wosungunukayo) mwana wang’ombe wokhala ndi thupi lokwanira, yemwe amatulutsa mawu (ngati kulira kwa ng’ombe), (iwo) adati: “Uyu ndi mulungu wanu ndiponso mulungu wa Mûsa, koma (Mûsa) wamuiwala, (choncho wapita kukamfuna ku phiri)!”

    [89] “Kodi sadaone kuti (mwana wang’ombe) sabweza mawu kwa iwo, ndiponso sangathe kudzetsa matsautso kwa iwo ngakhale zothandiza

    [90] “Ndipo ndithu Harun adawauza kale (kuti): “E inu anthu anga! Ndithu inu mwasokonezeka ndi (chinthu) ichi. Ndithu Mbuye wanu ndi (Allah) Wachifundo chambiri; choncho nditsateni, ndipo mverani lamulo langa, (siyani kupembedza fano ili).”

    [91] “(Iwo) adati: “Sitisiya ngakhale pang’ono kumpembedza. Kufikira Mûsa abwelere kwa ife.”

    [92] “(Pamene Mûsa adabwerera) adati: “E iwe Harun! Nchiyani chidakuletsa pamene udawaona atasokera,”

    [93] “Kuti usanditsate? Udanyozera lamulo langa?”

    [94] “(Harun) adati: E iwe mwana wa mayi anga! Usagwire ndevu zanga, ngakhale mutu wanga (poukoka chifukwa cha mkwiyo). Ndithu ine ndidaopa (kuchoka ndi ena, kusiya ena) kuti ungati: “Wawagawa ana a Israyeli, ndipo sudayembekezere mawu anga.”

    [95] “(Mûsa) adati: “E iwe Samiriyyu! Nchiyani wachita?”

    [96] “(Iye adati:) “Ndidaona zomwe sadazione (ena) ndipo ndidatapa pang’ono mapazi a Mtumiki (Gabriele) ndikuwaponya (mu fano la mwana wa ng’ombe). Ndipo zimenezi ndi zomwe zidakomera mtima wanga.”

    [97] “(Mûsa) adati: “ Choka, ndithu pa iwe (pali chilango) pa moyo (wako) choti uzingonena (kuti): “Musandikhudze musandikhudze.” (Ndipo palibe amene adzakuyandikira ndipo iwe sudzayandikira aliyense). Ndithu pa iwe pali lonjezo la (Allah) losaswedwa; ndipo muyang’ane mulungu wako, yemwe wakhala ukupitiriza kumpembedza. Timtentha, kenako chipala chakecho tichimwaza m’nyanja

    [98] “Ndithu wompembedza wanu, ndi Allah Yekha, Yemwe, palibe woti nkupembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Ndipo wakwanira pa chilichonse kuchidziwa ndi nzeru (Zake zopanda malire)

    [99] “Umo ndi momwe tikukusimbira nkhani za (zinthu) zomwe zidatsogola (za aneneri). Ndithu takupatsa uthenga waukulu kuchokera kwa Ife (omwe ndi Qur’an)

    [100] “Amene aunyozere, ndithu iye tsiku la Qiyâma adzasenza mitolo (ya machimo)

    [101] “Adzakhala m’menemo m’chilango. Ndipo ndi zoipa zedi (kwa anthu) kusenza mitolo (imeneyo) tsiku la Qiyâma

    [102] “(Kumbuka Mtumiki Muhammad {s.a.w}), tsiku lomwe lipenga lidzaimbidwa. Ndipo tidzasonkhanitsa oipa tsiku limenelo maso awo ali a buluu (blue, chifukwa cha mantha)

    [103] “Adzanong’onezana pakati pawo (ponena kuti): “Simudakhalitse pa dziko lapansi koma masiku khumi okha basi.”

    [104] “Ife tikudziwa kwambiri zimene azidzanena pamene abwino awo pamayendedwe azidzanena: “Inu simudakhale koma tsiku limodzi basi (poyerekeza ndi kuchuluka kwa masiku a ku Moto).”

    [105] “Ndipo akukufunsa zamapiri (kuti adzatani tsiku la Qiyâma); auze: “Mbuye wanga adzawagumulagumula ndikuwaululutsa (ngati fumbi).”

    [106] ““Ndipo adzaisiya (nthaka yonse) ngati bwalo losalazidwa myaa!”

    [107] ““Sudzaona kukhota m’menemo ngakhale chitunda (chikweza).”

    [108] “Tsiku limenelo adzamtsatira woitana; sadzatha kumpatuka, ndipo mawu (azolengedwa) adzatonthola (kuti chete) kwa (Allah) Wachifundo chambiri; ndipo sudzamva, koma kunong’ona basi (ndi mididi ya mapazi)

    [109] “Tsiku limenelo chiombolo (cha aliyense) sichidzathandiza, kupatula yemwe wapatsidwa chilolezo ndi (Allah) Wachifundo chambiri, ndi kumuyanja kuti alankhule

    [110] “(Allah) akudziwa za patsogolo pawo ndi zapambuyo pawo. Ndipo iwo sangathe kumzindikira (Allah) mmene alili

    [111] “Ndipo nkhope (tsiku limenelo) zidzalobodoka pamaso pa (Allah) Wamoyo wamuyaya, Wochita chilichonse. Ndithu adzataika kwathunthu yense wochita zosalungama

    [112] “Ndipo amene achite zabwino uku ali wokhulupirira, sadzaopa kuchitiridwa zoipa kapena kumchepetsera (choyenera chake)

    [113] “Ndipo momwemo taivumbulutsa (Qur’an) m’Chiarabu ndipo tafotokoza m’menemo mwatsatanetsatane za machenjezo (amtundu uliwonse), kuti aope (Allah), ndikuti nthawi iliyonse (Qur’aniyo), iwapatse chikumbutso chatsopano

    [114] “Chomwecho watukuka Allah, Mfumu ya choonadi, ndipo usaifulumizitse Qur’an (powerenga) chivumbulutso chake chisanamalizike kwa iwe, ndipo nena (popempha) kuti: “Mbuye wanga! Ndionjezereni nzeru (kuzindikira).”

    [115] “Ndipo tidamulangiza (Mneneri) Adam kale, koma adaiwala. Ndipo sitidapeze Mwa iye kulimba mtima (potsatira lamulo Lathu loti asadye zipatso za mtengo woletsedwa)

    [116] “Ndipo (kumbukirani) pamene tidauza angelo: “Muchitireni sajida (mugwadireni momulemekeza) Adam,” dipo adachita Sajida kupatula Iblis, adakana

    [117] “Tsono tidati: “E iwe Adam! Ndithu uyu ndi mdani wako iwe ndi mkazi wako; choncho asakutulutseni m’Munda wamtendere, mungadzavutike.”

    [118] ““Ndithu iwe sumva njala m’menemo ndipo sukhala wamaliseche.”

    [119] ““Ndipo iwe sumva ludzu m’menemo, ndiponso sumva kutentha (kwa dzuwa).”

    [120] “Koma satana (adamsokoneza) pomunong’oneza (zoipa) adati: “E iwe Adam! Kodi ndikusonyeze mtengo wamuyaya ndi (wopatsa) ufumu wosatha?”

    [121] “Ndipo (onse awiri) adaudya, ndipo umaliseche wawo awiriwo udaonekera poyera; ndipo adayamba kudziphatika masamba a m’mundamo; ndipo Adam adalakwira Mbuye wake, choncho adasokera

    [122] “Kenako Mbuye wake adamsankha pomulandira kulapa kwake ndikumuongola

    [123] “(Allah) adati: “Chokani nonsenu m’menemo, uku pali chidani pakati pa wina ndi mnzake, (padzakhala chidani pakati pa ana anu); koma chikadzakudzerani chiongoko kuchokera kwa Ine, tero amene adzachitsate chiongoko changacho, sadzasokera ndiponso sadzavutika.”

    [124] “Ndipo amene anyozere ulaliki wanga, ndithu moyo wamavuto udzakhala pa iye ndipo tidzamuukitsa m’manda tsiku la chimaliziro ali wakhungu.”

    [125] “Adzanena: “Mbuye wanga! Chifukwa ninji mwandiukitsa ndili wakhungu, pomwe ndidali wopenya?”

    [126] “(Allah) adzanena: “Zimenezo nchifukwa chakuti zidakudzera Ayah zathu koma udaziiwala (chifukwa chosalabadira), momwemo lero uiwalidwa, (salabadilidwa).”

    [127] “Ndipo umo ndimomwe tidzamulipirire aliyense wopyola malire, wosakhulupirira Ayah za Mbuye wake. Ndipo chilango cha tsiku la chimaliziro nchaukali, ndiponso chamuyaya

    [128] “Kodi sizidadziwikebe kwa iwo kuti ndi mibadwo ingati tidaiononga patsogolo pawo? Ndipo awa (osakhulupirira atsopano) akuyenda m’malo awo, (kodi saona zizindikiro zakuonongeka kwawo)? Ndithu m’zimenezo muli zisonyezo kwa eni nzeru

    [129] “Ndipo pakadapanda liwu lomwe lidatsogola kuchokera kwa Mbuye wako (lochedwetsera chilango) ndi nthawi yomwe idaikidwa, ndithu (chilango) chikadawafika (tsopano lomwe lino)

    [130] “Choncho pirira pa zomwe akunenazo, ndipo lemekeza Mbuye wako ndi kumtamanda, dzuwa lisanatuluke (popemphera swala ya Fajr), ndiponso lisanalowe (popemphera swala ya Asr); ndiponso nthawi za usiku umulemekeze (popemphera swala ya Magrib ndi Isha), ndi pansonga za masana (pakatikati pa usana popemphera swala ya Dhuhr); kuti udzakhale wokondwa (ndi malipilo amene azakupatse tsiku la Qiyâma)

    [131] “Ndipo usazitong’olere maso ako (mozidololokera zinthu) zimene tawasangalatsa nazo ena mwa anthu pakati pawo; zimenezo nzokongoletsa za moyo wa pa dziko basi, kuti tiwayese mayeso pazimenezo; koma chopatsa cha Mbuye wako (chomwe nchololedwa ngakhale chikhale chochepa) nchabwino kwambiri ndiponso chokhalitsa

    [132] “Ndipo lamula banja lako kupemphera Swala ndi kuipirira iwe mwini Swalayo. Sitikukupempha rizq, (chakudya) koma Ife ndi amene tikukudyetsa ndipo malekezero abwino ali mukuopa (Allah)

    [133] “Ndipo (osakhulupirira) adanena: “Chifukwa ninji sakutibweretsera chizizwa kuchokera kwa Mbuye wake?” Kodi sudawafike umboni woonekera wa zomwe zili m’mabuku akale? (Kodi sadakhutitsidwe ndi Qur’an chomwe ndi chizizwa chachikulu).”

    [134] “Ndipo ngati tikadawaononga ndi chilango, asanadze uyo (Mtumiki), akadanena: “Mbuye wathu! Bwanji osatitumizira mtumiki kuti titsate Ayah Zanu tisanayaluke ndi kunyozeka?”

    [135] “Nena: “Aliyense (wa ife) akuyembekezera (mphoto yake); choncho yembekezerani. Posachedwapa mudziwa kuti kodi ndani mwini njira yolingana, ndipo ndani amene waongoka.”

    Aneneri

    Surah 21

    [1] “۞ Chiwerengero chayandikira kwa anthu pomwe iwo ali m’kusalabadira ndi M’kunyozera

    [2] “Palibe pamene ukuwadzera ulaliki watsopano wochokera kwa Mbuye wawo koma amaumvetsera uku akuchita zachibwana

    [3] “Mitima yawo ikunyozera (osalabadira za kudza kwa Qiyâma). Ndipo akunenezana mobisa amene adzichitira zoipa; (akuuzana motere): “Kodi uyu (Muhammadiyu) ndi ndani, simunthu monga inu? Kodi mukuudzera ufiti pomwe mukuuona?”

    [4] “(Mneneri Muhammad{s.a.w}) adati: “Mbuye wanga akudziwa zimene zikunenedwa kumwamba ndi pansi; ndipo Iye Ngwakumva; Ngodziwa

    [5] “Koma (osakhulupirira) adati: “(Izi zimene akufotokozazi) ndi maloto opanda pake.” (Ndipo nthawi zina amati:) “Koma zimenezi wazipeka.” (Penanso amati:) “Koma iyeyu ndi mlakatuli. Chonchotu, atibweretsere chizizwa monga mmene adatumiziridwa (aneneri) oyamba.”

    [6] “Sadakhulupirire apatsogolo pawo, eni midzi imene tidaiononga (ngakhale kuti zozizwitsa adaziona); nanga iwo akhulupirira

    [7] “Ndipo sitidawatume patsogolo pako, (iwe Mtumiki,) koma anthu, (osati angelo); tidawavumbulutsira (chivumbulutso Chathu.) Choncho, afunseni eni kudziwa ngati inu simukudziwa (nkhani zakale)

    [8] “Ndipo sitidawachite (aneneriwo) kukhala matupi osadya chakudya ndipo sadalinso okhala nthawi yaitali

    [9] “Kenako tidawatsimikizira lonjezo (la kuwathangata pa adani awo), ndipo tidawapulumutsa iwo ndi amene tidawafuna (mwa omwe adawatsata), ndipo olumpha malire (a Allah) Tidawaononga

    [10] “Ndithu tatumiza kwa inu buku lomwe m’kati mwake muli ulaliki wanu (malangizo kwa inu). Kodi simukuzindikira

    [11] “Ndi ambiri mwa eni midzi yomwe idali yosalungama, tidawaononga; ndipo pambuyo pake tidalenga anthu ena

    [12] “Pamene adazindikira za chilango chathu, pompo adayamba kuchithawa

    [13] “Musathawe, (kuthawa sikukupulumutsani), koma bwererani ku zimene mwasangalatsidwa nazo ndi m’malo mwanu, kuti mufunsidwe

    [14] “Adanena: “Tsoka lathu ndithu! Tidali ochita zoipa.”

    [15] “Kukuwa kwawoko sikudathe, kufikira tidawapanga ngati (mbewu) zokololedwa, mpaka kupuma kwawo kudazima (adafa)

    [16] “Ndipo sitidalenge thambo ndi nthaka ndi zapakati pake, mwamasewera

    [17] “Tikadafuna kupanga choti tiziseweretsa (sitidakapanga zomwe mukuzionazi) tikadapanga mwazomwe tili nazo, tikadakhala oti tichite (zachibwana)

    [18] “Koma (chimene timachita ndi ichi), timachiponya choona pa chachabe ndi kuchiswa bongo bwake, ndipo chachabecho chimachoka. Ndipo chilango chili pa inu chifukwa cha zomwe mukunena (kumnamizira Allah)

    [19] “Onse akumwamba ndi pansi, Ngake (Allah); ndipo amene ali kwa Iye (angelo), sadzitukumula pakumulambira, ndiponso satopa (ndi mapemphero)

    [20] “Amamlemekeza usiku ndi usana, ndipo sagwidwa ndi ulesi

    [21] “Kapena adzipangira milungu yochokera m’nthaka youkitsa akufa, (kotero kuti aichita kukhala milungu yawo mmalo mwa Allah)

    [22] “Kukadakhala kuti ilipo m’menemo milungu ina (kuthambo ndi pansi) kupatula Allah, (ziwirizi) zikadawonongeka, wapatukana Allah Mbuye wa Arsh (Mpando Wachifumu) ndi zimene akunena (osakhulupirira)

    [23] “Safunsidwa pa zimene akuchita, koma iwo adzafunsidwa

    [24] “Kapena adzipangira milungu ina m’malo mwa Iye? Nena: ‘“Bweretsani umboni wanu (pa zimenezi), (izi ndikuuzani) ndichikumbutso kwa awa ali pamodzi ndi ine, ndiponso ndichikumbutso kwa amene adalipo patsogolo panga.” Koma ambiri a iwo sadziwa za choonadi, tero iwo akunyozera

    [25] “Ndipo sitidatume patsogolo pako mtumiki aliyense koma tidali kumzindikiritsa kuti palibe mulungu wina wompembedza mwachoonadi, koma Ine; choncho ndilambireni

    [26] “Ndipo (osakhulupirira) akuti: “(Allah) Wachifundo chambiri wadzipangira mwana.” Allah wapatukana (ndi zimenezo) koma (awa angelo) ndi akapolo (a Allah) amene alemekezedwa

    [27] “Samutsogolera kuyankhula, ndipo iwo amachita molingana ndi malamulo Ake

    [28] “(Allah) akudziwa zapatsogolo pawo (angelowo) ndi zapambuyo pawo, ndipo (angelowo) sangaombole (aliyense) koma yekhayo (Allah) wamuyanja, ndipo iwo, chifukwa chomuopa, amanjenjemera

    [29] “Ndipo mwa iwo amene anganene kuti: “Ine ndi mulungu mmalo mwa Iye,” ndiye kuti timulipira Jahannam; umo ndi momwe timawalipirira ochita zoipa

    [30] “Kodi osakhulupirira sadaone kuti thambo ndi nthaka zidali zophatikizana, ndipo tidazilekanitsa? Ndipo ndi madzi tidalenga chilichonse chamoyo. Kodi sakhulupirira

    [31] “Ndipo tidaika mapiri panthaka molimbika kuti isagwedezeke ndi iwo, ndipo m’menemo tidaikamo misewu kuti alondole njira (ndikufika komwe afuna)

    [32] “Ndipo thambo tidalipanga monga tsindwi losungidwa (kuti lisagwe). Koma iwo akuzitembenukira kumbali zizindikiro zake

    [33] “Ndipo Iye ndi Yemwe adalenga usiku ndi usana, dzuwa ndi mwezi; chilichonse mwa izo chikusambira mozungulira m’njira mwake

    [34] “Ife sitidawachite anthu amene adalipo patsogolo pako kukhala okhala nthawi yaitali. Nanga ukafa, kodi iwo adzakhala okhala nthawi yaitali

    [35] “Chamoyo chilichonse chidzalawa imfa; ndipo tikukuyesani mayeso ndi zinthu zoipa ndi zabwino. Ndipo nonsenu mudzabwerera kwa Ife

    [36] “Ndipo amene sadakhulupirire akakuona, akungokuchitira chipongwe. “Kodi ndi uyu yemwe akutchula milungu yanu (mwachipongwe)?” Pomwe iwo ndi amene akukana zakutchula (Allah) Wachifundo chambiri

    [37] “Munthu walengedwa ndi chikhalidwe chokonda zinthu (zake zonse) mwachangu. Posachedwapa ndikusonyezani zisonyezo Zanga; choncho musandifulumizitse (kukubweretserani chilango changa)

    [38] “Ndipo (osakhulupirira) akuti: “Kodi malonjezo awa adzakwaniritsidwa liti, ngati mukunena zoona?”

    [39] “Chikhala kuti amene sadakhulupirire akudziwa chilango chimene chidzawapeza panthawi yomwe sangathe kutchinjiriza Moto kunkhope zawo ndi kumisana yawo ndipo kuti sadzathandizidwa, (sakadanena zimenezi)

    [40] “Koma (Qiyâma) idzawadzera mwadzidzidzi ndi kuwadzidzimutsa; kenako sadzatha kuibweza kapena kupatsidwa danga (kuti achite zomwe sadachite)

    [41] “Ndipo ndithu atumiki adachitidwa chipongwe patsogolo pako; choncho amene adachita chipongwe mwa iwo, zidawadzera zomwe adali kuzichita chipongwe

    [42] “Nena: “Kodi ndani angakutetezeni usiku ndi usana ku masautso a (Allah) Wachifundo Chambiri?” Koma iwo akunyozera kukumbuka Mbuye wawo

    [43] “Kapena ali nayo milungu yowatchinjiriza m’malo mwa Ife? (Milunguyo) siingathe kudzithandiza yokha (nanga ndiye ingathe kuthandiza ena?) Ndipo (milungu) imeneyo siidzasamalidwa ndi Ife

    [44] “Koma awa (osakhulupirira) tidawasangalatsa ndi makolo awo kufikira nthawi ya moyo wawo idatalika; kodi saona kuti tikulidzera dziko lawo ndikulichepetsa malire ake?. Nanga kodi iwo ndiwo opambana

    [45] “Nena: “Ndithu ndikukuchenjezani ndi chivumbulutso (cha Allah). Koma agonthi samva kuitana pamene akuchenjezedwa.”

    [46] “Ndipo kukadawakhudza kumenya kumodzi kwa chilango cha Mbuye wako, ndithudi, (akadadzichepetsa nthawi yomweyo). Akadanena: “Tsoka kwa ife ndithu tidali osalungama.”

    [47] “Ndipo tsiku la Qiyâma tidzaika masikero achilungamo, choncho mzimu uliwonse sudzachitidwa chinyengo pa chilichonse. Ngakhale (chinthucho) chili cholemera ngati njere ya mpiru, tidzachibweretsa; ndipo tikukwana (kukhala akatswiri) pa chiwerengero

    [48] “Ndipo ndithu Mûsa ndi Harun tidawapatsa (buku) losiyanitsa pakati pa choonadi ndi chonama, ndiponso muuni ndi ulaliki kwa anthu oopa (Allah)

    [49] “Omwe akumuopa Mbuye wawo ngakhale ali paokha, omwenso amaopa Qiyâma

    [50] “Ndipo iyi (Qur’an) ndi ulaliki wodalitsika umene tauvumbulutsa (kwa inu); kodi inu mukuikana

    [51] “Ndipo ndithu Ibrahim tidampatsa kulungama kwake kuyambira kale (kuubwana), ndipo tinkamudziwa (bwinobwino)

    [52] “(Akumbutse anthu) pamene adauza bambo wake ndi anthu ake, “Nchiyani mafano awa omwe inu nthawi zonse mukupitiriza kuwapembedza.”

    [53] “Adati: “Tidapeza makolo athu akuwapembedza. (Choncho nafenso Tikuwapembedza).”

    [54] “(Iye) adati: “Ndithu inu ndi makolo anu mudali mkusokera koonekera.”

    [55] “(Iwo) adati: “Kodi watibweretsera choonadi, kapena iwe ndi m’modzi mwa osereula?”

    [56] “(Iye) adati: (“Iyayi, ine siwosereula), koma Mbuye wanu, ndi Mbuye wa thambo ndi nthaka amene adalenga zimenezi; ine pa zimenezi, ndine m’modzi wochitira umboni.”

    [57] ““Ndipo ndikulumbilira Allah, ndiwachitira chiwembu mafano anuwo pambuyo ponditembenukira misana kupita komwe mukupita.”

    [58] “Choncho adawaphwanya (mafanowo) zidutswazidutswa kupatula lalikulu lawo (sadaliswe) kuti iwo alibwelere (ndi kulifunsa zimene zachitika)

    [59] “(Iwo parnene adafika kumafano awo) adati: “Ndani wachita ichi pa milungu yathu? Ndithu iye ndi m’modzi wa ochita zoipa.”

    [60] “Adati: “Tidamumva m’nyamata wina akuitchula (moipa); amatchedwa Ibrahim.”

    [61] “Adati: “Mubweretseni pamaso pa anthu kuti amuone.”

    [62] “Adati: “Kodi ndiwedi wachita ichi ku milungu yathu, E, iwe Ibrahim?”

    [63] “(Iye) adati: “(Iyayi), koma wachita ichi ndi mkulu wawoyu. Choncho afunseni (kuti akuuzeni zenizeni) ngati amatha kuyankhula.”

    [64] “Ndipo adadzitembenukira okha ndikunena kuti: “Ndithu inu ndinu oipa.”

    [65] “Kenako adazyolitsa mitu yawo (ndikubwerera kuumbuli wawo) nanena kuti: “Ndithu iwe ukudziwa kuti izi siziyankhula (nchifukwa ninji ukutichita chipongwe)?”

    [66] “(Iye) adati: “Kodi mukupembedza zomwe sizingakuthandizeni chilichonse, kusiya Allah, zomwenso sizingakupatseni masautso?”

    [67] ““Kuyaluka nkwanu ndi zomwe mukuzipembedzazo kusiya Allah. Kodi simuganizira?”

    [68] “(Iwo) adati: “Mtentheni; ndipo pulumutsani milungu yanu, ngati inu mungathe kuchita zimenezi.”

    [69] “Tidati: “E iwe Moto! Khala kuzizira ndiponso mtendere kwa Ibrahim.”

    [70] “Ndipo adamfunira chiwembu; koma tidawachita kukhala otaika zedi

    [71] “Ndipo tidampulumutsa iye ndi Luti kupita ku dziko lomwe tidalidalitsa ku zolengedwa

    [72] “Ndipo (Ibrahim) tidampatsa Ishaq ndi kuonjezera Ya’qub, ndipo tidawachita onse kukhala abwino

    [73] “Ndipo tidawasankha kukhala atsogoleri, owongolera mwa lamulo Lathu, ndipo tidawazindikiritsa kuchita zabwino ndi kupemphera Swala moyenera, ndi kupereka Zakaat; ndipo kwa Ife adali opembeza

    [74] “Ndipo Luti tidampatsa luntha ndi kuzindikira, ndipo tidampulumutsa ku mudzi womwe anthu ake ankachita zoipa; ndithu iwo adali anthu oipa otuluka m’chilamulo (cha Allah)

    [75] “Ndipo tidamulowetsa mu chifundo Chathu; ndithu iye adali m’modzi wa ochita zabwino

    [76] “Ndipo (akumbutse za) Nuh, pamene adatiitana kale (kutipempha). Ndipo Ife tidamuyankha ndi kupulumutsa iye ndi anthu ake ku sautso Ialikulu

    [77] “Ndipo tidampulumutsa pa anthu amene adatsutsa Ayah Zathu; ndithu iwo adali anthu oipa. Ndipo onse tidawamiza (ndi chigumula chamadzi)

    [78] “Ndipo (akumbutse za) Daud ndi Sulaiman, pamene ankaweruza mlandu wa munda, pomwe mbuzi za anthu zidadya ndi kuonongaononga usiku mmenemo ndipo Ife tidali mboni pa kuweruza kwawo

    [79] “Tero tidamzindikiritsa za mlanduwo Sulaiman (kuposa tate wake Daud). Yense wa iwo tidampatsa kuweruza ndi kudziwa; ndipo tidagonjetsa mapiri ndi mbalame kuti zikhale pamodzi ndi Daud zikulemekeza (Allah); ndipo Ife ndi ochita chimene tafuna

    [80] “Ndipo tidamphunzitsa (Daud) kapangidwe ka chovala chapankhondo chifukwa cha inu kuti chikutetezeni mkumenyana kwanu; kodi simungakhale othokoza

    [81] “Nayenso Sulaiman tidamugonjetsera mphepo yamphamvu; inkayenda mwa lamulo lake kunka ku dziko lomwe talidalitsa (dziko la Sham); ndipo Ife pa chilichonse Ngodziwa

    [82] “Ndipo (tidamugonjetseranso) asatana omwe ankamubilira m’madzi (ndikumtolera ngale), ndipo ankachita ntchito zina kuonjezera pa zimenezi; ndipo Ife tidali owasunga (owateteza)

    [83] “Ndipo akumbutsenso za Ayubu pamene adakuwira Mbuye wake (kuti): “Ndithu mavuto andikhudza, pomwe Inu ndi Achifundo kuposa achifundo!”

    [84] “Choncho tidavomera (pempho lake); ndipo tidamchotsera mavuto omwe adali nawo, ndipo tidampatsa ana ake ofanana ndi omwe adali nawo kale ndikuonjezeranso ena onga iwo, (zonsezi monga) chifundo chochokera kwa Ife, (ndikuti zikhale) chikumbutso kwa ochita mapemphero

    [85] “Ndipo (mutchule) Isimaila ndi Idrisa ndi Zul Kifli, onsewa adali mwa opirira

    [86] “Tidawalowetsanso ku chifundo Chathu, ndithu iwo adali mwa anthu abwino

    [87] “Ndipo (mtchulenso) Thun-Nun (Yunusu), pamene adachoka uku atakwiya, ndipo ankaganiza (kuti tamuloleza kusamuka) ndikuti sititha kumchita kanthu. Choncho adaitana mu mdima (mammimba mwa nsomba imene idamumeza, kuti): “Ndithu palibe mulungu wina wopembezedwa mwachoonadi koma Inu; mwayeretsedwa; ndithu ine ndidali m’modzi wa odzichitira zoipa.”

    [88] “Choncho tidavomereza (pempho lake) ndi kumpulumutsa ku madandaulo; umo ndi m’mene timawapulumutsira okhulupirira

    [89] “Ndipo (akumbutse za) Zakariya pamene adaitana Mbuye wake (kuti): “Mbuye wanga! Musandisiye ndekha; ndithu Inu ndinu wabwino kuposa alowa mmalo onse.”

    [90] “Choncho tidamuvomera (pempho), ndikumpatsa Yahya ndikumkonzera mkazi wake. Ndithu iwo adali achangu pochita zabwino; ankatipempha mwakhumbo ndi mwamantha, ndipo adali odzichepetsa kwa Ife

    [91] “Ndipo (atchulire za Mariya) yemwe adauteteza umaliseche wake (podzisunga); ndipo tidauzira mwa iye Mzimu Wathu, ndipo tidamchita iye ndi mwana wake kukhala chizizwa (cha Allah) kwa zolengedwa zonse

    [92] “Ndithu uwu mpingo wanu, ndimpingo umodzi, ndipo Ine ndine Mbuye wanu; choncho ndipembedzeni

    [93] “Koma iwo adaswa chinthu chawochi pakati pawo (tero adakhala mipingo yosiyanasiyana). Onse adzabwerera kwa Ife

    [94] “Ndipo amene achite ntchito zabwino uku ali wokhulupirira, khama lake silidzakanidwa; ndithunso Ife tikumlembera zonse zimene akuchita

    [95] “Ndipo nkosatheka kwa eni mudzi umene tidauononga chifukwa cha machimo awo kuti asabwelere kwa Ife; (koma ndithu abwerera)

    [96] “Kufikira pamene Yaajuju ndi Maajuju adzatsekulilidwa (mpanda wawo), ndipo iwo adzakhala akuthamanga kuchokera m’phiri lililonse

    [97] “Ndipo lonjezo la choonadi lidzafika; pamenepo maso a omwe sadakhulupirire, adzatong’oka uku akunena: “Tsoka pa ife! Ndithu tidali osalabadira (za chinthu) ichi; koma tidali oipa, (odzichitira tokha zoipa.)”

    [98] “Ndithu inu ndi amene mukuwapembedza kusiya Allah, ndinu nkhuni za ku Jahannam. Ndipo inu (Jahannamyo) mudzalowa

    [99] “Ngati awa akadakhala milungu yeniyeni, ndiye kuti sakadailowa, mmenemo onse adzakhala nthawi yaitali

    [100] “Mmenemo iwo adzakhala akubuula ndipo iwo mmenemo sadzamva (chifukwa makutu adzagontha)

    [101] “Ndithu amene ubwino wathu udawafika, iwo adzatalikitsidwa nawo (motowo)

    [102] “Sadzamva mavume ake, ndipo iwo adzakhala nthawi yaitali m’zomwe ikukhumba mitima yawo

    [103] “Kugwedezeka kwakukulu sikudzawadandaulitsa; ndipo angelo adzawalandira (ndikuwauza): “Ili ndi tsiku lanu lomwe mudali kulonjezedwa.”

    [104] “(Kumbukirani) tsiku lomwe tidzakulunga thambo monga momwe amakulungira makalata okhala ndi malembo m’kati mwake; monga tidayamba kulenga zolengedwa poyamba, tidzabwerezanso (kuzilenga kachiwiri. Ndipo aliyense adzalipidwa pa zomwe adali kuchita) ili ndilonjezo lomwe lili pa Ife. Ndithu Ife ndi Ochita (zomwe tikunena)

    [105] “Ndipo ndithu tidalemba m’zaburi (mu Masalimo buku la Daud) pambuyo polemba mu chikumbutso (Lauhil-Mahafudh) kuti: “Dziko (lapansi) adzalilowa akapolo Anga abwino.”

    [106] “Ndithu pazimenezi (nkhani za aneneri), pali miyambo kwa anthu, opembedza (Allah)

    [107] “Ndipo sitidakutume koma kuti ukhale mtendere kwa zolengedwa zonse

    [108] “Nena: “Ndithu kukuvumbulutsidwa kwa ine kuti mulungu wanu ndi Mulungu Mmodzi; nanga inu mudzagonjera (zofuna Zake polowa m’Chisilamu)?”

    [109] “Koma ngati anyozera, nena: “Ndalengeza (uthenga) kwa inu mofanana (popanda tsankho); sindidziwa kuti zomwe mukulonjezedwa zili pafupi kapena zili kutali.”

    [110] ““Ndithu Iye akudziwa mawu okweza, ndiponso akudziwa zomwe mukubisa.”

    [111] ““Ndipo sindikudziwa, mwina kuchedwetsa chilango chanu ndi mayeso akukuyesani ndikukusangalatsani ndi zokoma (za m’dziko) mpaka Idzakwane nthawi yoikidwayo.”

    [112] “Adati: “E Mbuye wanga! Weruzani moona.” “Ndipo Mbuye wathu ndi (Allah) Wachifundo chambiri; Wopemphedwa chithandizo pa zimene mukusimbazo.”

    Haji

    Surah 22

    [1] “E inu anthu! Opani Mbuye wanu (ndipo kumbukirani tsiku la Kiyâma). Ndithu kugwedezeka kwa Kiyâma ndichinthu chachikulu (kwabasi)

    [2] “Tsiku limene mudzaione (Qiyâmayo), mkazi aliyense woyamwitsa adzaiwala (mwana wake) womuyamwitsa, ndipo (mkazi) aliyense wapakati adzataya pakati pake; ndipo udzawaona anthu ataledzera, pomwe sadaledzere; koma ndi chilango chaukali cha Allah (chimene chawapeza)

    [3] “Ndipo alipo ena mwa anthu amene akutsutsa za Allah popanda kuzindikira, ndipo akutsatira satana aliyense wolakwa

    [4] “(Za satana), kwalembedwa kuti amene amsankhe kukhala bwenzi lake, ndithu iye amsokeretsa ndi kumtsogolera ku chilango cha Moto

    [5] “E inu anthu! Ngati muli m’chikaiko za kuuka ku imfa, (ndipo mukuona kuti nzosatheka, yang’anani mmene tidakulengerani). Ndithu Ife tidakulengani ndi dothi, ndipo (timakulengani) ndi dontho la umuna, komanso (umunawo udasanduka) gawo lamagazi, kenako gawo la mnofti woumbidwa (chithunzi cha munthu) ndi wosaumbidwa, kuti tikulongosolereni (kukhoza Kwathu;) ndipo Ife timachikhazikitsa mchiberekero; chimene tifuna kufikira nthawi yake yoyikidwa kenako timakutulutsani muli khanda, (tsono timakulerani) kuti mufike pa nsinkhu wanu. Ndipo ena mwa inu amamwalira (asanakule), pomwe ena mwa inu amabwezedwa ku moyo wofooka (waukalamba) kotero kuti asadziwe chilichonse pambuyo pakuti adali wodziwa. Ndipo umaiona nthaka ili chetee, koma tikatsitsa madzi pamwamba pake, imagwedezeka ndi kufufuma, ndi kumeretsa mtundu uliwonse wa mmera wokongola

    [6] “Zimenezo (monga kulenga munthu ndi kumeretsa mmera, ndi umboni wosonyeza) kuti Allah Woona alipo; ndikuti Iye amaukitsa akufa, ndiponso Iye ali ndi mphamvu pa chilichonse

    [7] “Ndipo, ndithu Qiyâma idza; palibe chikaiko pa zimenezi, ndipo ndithu Allah adzawatulutsa amene ali m’manda

    [8] “Ndipo alipo mwa anthu amene akutsutsa za Allah popanda kuzindikira, ngakhale chiongoko, ngakhalenso buku lounika, (koma makani basi ndi kungotsata zimene akuziganizira)

    [9] “(Yemwe) akupinda khosi lake (chifukwa chodzikuza) kuti asokereze (anthu powachotsa) kunjira ya Allah; pa iye pali chilango choyalutsa pa moyo uno, ndipo patsiku la Qiyâma tikamulawitsa chilango cha Moto wotentha

    [10] “(Tidzamuuza kuti): “Izi ndi zomwe manja ako adatsogoza; ndithu Allah siwachinyengo kwa akapolo (Ake).”

    [11] “Ndipo alipo wina mwa anthu amene akupembedza Allah cham’mphepete (mwachipembedzo). Chabwino chikampeza amatonthola nacho; koma masautso akamufika, amatembenuka ndi nkhope yake (posiya chikhulupiliro mwa Allah. Choncho) waluza moyo wa dziko lapansi ndi moyo wa tsiku la chimaliziro; kumeneko ndiko kuluza koonekera

    [12] “M’malo mwa Allah, amapembedza zomwe sizingampatse masautso (ngati ataleka kuzipembedza), ndiponso zomwe sizingampatse chithandizo (akamazipembedza), ndipo kumeneko ndiko kusokera konka nako kutali

    [13] “Akupembedza omwe masautso awo ali pafupi zedi poyerekeza ndi zabwino zawo, taonani kuipa atetezi ndiponso ndi abwenzi oipa

    [14] “Ndithu Allah adzawalowetsa ku Minda yamtendere amene akhulupirira ndikuchita zabwino, mitsinje ikuyenda pansi (pa mindayo). Ndithu Allah amachita chimene wafuna

    [15] “Amene akuganiza kuti Allah samthangata (Mtumiki Wake) pa dziko lapansi ndi patsiku la chimaliziro, amange chingwe kudenga, kenako adzipachike (ngati safuna kuona Chisilamu chikufala); ndipo aone kuti kodi ndale zakezo zichotsa zimene zamkwiitsazo

    [16] “Momwemonso taivumbulutsa (Qur’an) kuti ikhale mawu omveka; ndipo ndithu Allah amaongola amene wamfuna

    [17] “Ndithu amene akhulupirira, ndi amene ali m’chipembedzo cha Chiyuda, ndi chipembedzo cha Sabia; ndi Akhrisitu, ndi Maajusi (opembedza moto), ndi ophatikiza Allah ndi mafano, ndithu Allah adzaweruza pakati pawo tsiku la chiweruziro (Qiyâma). (Osokera adzaponyedwa ku Moto ndipo olungama adzawalowetsa ku Munda wamtendere). Ndithu Allah ndi Mboni pa chinthu chilichonse

    [18] “Kodi suona kuti Allah zikumulambira zimene zili kumwamba ndi zimene zili m’nthaka, kudzanso dzuwa, mwezi, nyenyezi mapiri, mitengo, nyama ndi anthu ambiri. Koma ambirinso chilango chatsimikizika pa iwo. Ndipo amene Allah wamuyalutsa, palibe amene angampatse ulemelero; ndithu Allah amachita chimene wafuna

    [19] “Awa ndi magulu awiri amene akangana pa za Mbuye wawo (pa zomwe zili zomuyenera, ndi zosamuyenera, ndipo ena sadakhulupirire.) Choncho amene sadakhulupirire, adzawadulira nsalu za ku Moto ndi kuwaveka; ndipo pamwamba pa mitu yawo padzathiridwa madzi otentha

    [20] “Chifukwa cha madziwo zidzasungunuka zomwe zili m’mimba mwawo ndiponso makungu (awo)

    [21] “Ndipo (kuonjezera pa zimenezi) adzakhala nazo nyundo zachitsulo (zowamenyera)

    [22] “Nthawi iliyonse akafuna kutuluka m’menemo, chifukwa chakumva kupweteka, adzabwezedwa momwemo (ndipo angelo uku akuwamenya ndi nyundo), ndi (kuwauza): “Chilaweni chilango chootcha.”

    [23] “Ndithu Allah adzalowetsa amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, ku Minda ya mtendere komwe mitsinje ikuyenda pansi (ndi pasogolo) pake; m’menemo akavekedwa (ndi angelo) zibangili za golide ndi ngale; ndipo zovala zawo m’menemo zidzakhala za silika

    [24] “Ndipo adzatsogozedwa (kupita kumalo) kokamba mawu abwino okhaokha; ndiponso adzatsogozedwa ku njira ya Mwini kutamandidwa (kunjira yonkera ku Jannah)

    [25] “Ndithu. amene sadakhulupirire (Allah ndi Mtumiki Wake) ndipo nkumatsekereza ena ku njira ya Allah, (ndiponso nkumatsekereza kulowa) mu Msikiti Wopatulika umene tidauchita kuti ukhale wa anthu onse mofanana kwa amene akukhala m’menemo ndi kwa alendo, (anthu otere tidzawalanga ndi chilango chaukali), ndipo aliyense wofuna kuchita zopotoka m’menemo mosalungama, timulawitsa chilango chowawa zedi

    [26] “Ndipo (kumbukira) pamene tidamkhazika Ibrahim (ndi kumlondolera) pamalo pa Nyumba (yopatulikayo; tidamuuza kuti): “Usandiphatikize ndi chilichonse; ndipo iyeretse nyumba yanga chifukwa cha amene akuizungulira ndi kumakhala pompo (pochita mapemphero awo); ndi omwe amawerama ndi kugwetsa nkhope zawo pansi

    [27] “Ndipo (tidamuuza): “Lengeza kwa anthu za Hajj; akudzera (ena) oyenda ndi mapazi, ndipo (ena ali) pamwamba pa chiweto choonda (chifukwa chamasautso a paulendo); adza kuchokera kunjira zamtalimtali

    [28] “Kuti adzaone zabwino zawo, ndikuti (achulukitse) kutchula dzina la Allah m’masiku odziwika (ubwino wake), kupyolera m’zimene wawapatsa monga ziweto za miyendo inayi. Ndipo idyani ina mwa nyamayo ndi kum’dyetsa wovutika, wosauka

    [29] “Kenako adziyeretse kuzitakataka zawo, ndipo akwaniritse naziri (malonjezo) zawo ndikuzungulira nyumba yakale

    [30] “Umo ndi momwe zikhalire; ndipo amene alemekeze zinthu zopatulika za Allah kutero ndi bwino kwa iyeyo pamaso pa Mbuye wake. Ndipo ziweto za miyendo inayi nzovomerezeka kwa inu kuzidya, kupatula zomwe zatchulidwa kwa inu (m’Qur’an kuti nzoletsedwa); choncho upeweni uve wa mafano, ndiponso pewani mawu abodza

    [31] “Uku mutapendekera kwa Allah Yekha, osati kum’phatikiza (Allah). Ndipo amene akuphatikiza Allah ndi mafano, ali ngati wogwa kuchokera kumwamba, kenako mbalame nkumuwakha, kapena mphepo kukamtaya malo akutali

    [32] “Zimenezo ndikuti amene alemekeze zizindikiro za chipembedzo cha Allah, kutero ndichinthu choonetsa kuopa Allah m’mitima

    [33] “(Ziweto zimene mukutumiza ku Makka monga nsembe) muli nazo zithandizo mmenemo (monga kukwera ndi kukama mkaka) kufikira nthawi yodziwika, (yomwe ndi nthawi yozizingira); kenako malo ozizingira ndi pafupi ndi Nyumba yakalekaleyo

    [34] “Ndipo mpingo uliwonse tidaupangira malo ozingira nsembe zamapemphero kuti atchule dzina la Allah pa zomwe wawapatsa monga ziweto zamiyendo inayi. Choncho mulungu wanu ndi Mulungu m’modzi Yekha; gonjerani kwa Iye; ndipo odzichepetsa auze nkhani yabwino

    [35] “Omwe Allah akatchulidwa, mitima yawo imanjenjemera ndiponso amapirira pa zomwe zawapeza, ndipo amapemphera Swala moyenera ndi kupereka chopereka kuchokera m’zomwe tawapatsa

    [36] “Ndipo ngamira (ng’ombe, mbuzi ndi mbelere) tadzichita kwa inu kuti zikhale mwa zizindikiro za chipembedzo cha Allah; m’zimenezo muli zabwino kwa inu; choncho litchuleni dzina la Allah pa izo pamene zikuima mondanda (uku mukuzizinga,) ndipo zikagwa cham’nthiti, idyani (nyama yake) ndikumdyetsa yemwe akungozungulirazungulira, wosapempha ndi wopempha yemwe. Momwemo tazigonjetsa kwa inu (pochita kuti zikugonjereni) kuti muthokoze

    [37] “(Nyamazo) Allah siimfika minofu yake ngakhale magazi ake, koma kuopa kuchokera mwa inu ndiko kumene kumamfika; momwemo wazichita (nyamazo) kukhala zogonjera inu kuti mumlemekeze Allah chifukwa cha kukuongolaniku. Auze nkhani yabwino ochita zabwino

    [38] “Ndithu Allah amawateteza amene akhulupilira, ndithu Allah sakonda aliyense wachinyengo, wosathokoza

    [39] “Chaperekedwa chilolezo kwa (Asilamu) amene akuputidwa (ndi adani awo kuti abwezere) chifukwa chakuti iwo achitiridwa zoipa; ndipo ndithu Allah ngokhoza kuwathandiza

    [40] “Omwe atulutsidwa m’nyumba zawo popanda chilungamo, koma pachifukwa chakuti akunena: “Mbuye wathu ndi Allah.” Ndipo pakapanda Allah kukankha anthu ena kupyolera mwa ena, (popatsa ena mphamvu kuti agonjetse ena), ndiye kuti Masinagogi, Matchalitchi, nyumba zina zopempheleramo ndi Misikiti momwe dzina la Allah likutchulidwa mochuluka zikadagumulidwa. Ndithu Allah am’thangata amene akuthangata chipembedzo Chake; ndithu Allah Ngwanyonga, Wogonjetsa chilichonse

    [41] “Omwe akuti tikawakhazika pa dziko mwa ubwino, amachita mapemphero a Swala moyenera ndi kupereka Zakaat, ndi kulamula zabwino ndi kuletsa zoipa; ndipo mabwelero a zinthu nkwa Allah basi

    [42] “Ndipo ngati akukuyesa wabodza, (awa Akafiri, sizachilendo), ndithu adatsutsanso (aneneri awo) patsogolo pawo anthu a Nuh, Aadi, a Samudu

    [43] “Anthu a Ibrahim, anthu a Luti

    [44] “Ndi anthu a ku Madiyan; nayenso Mûsa adayesedwa wabodza (adamkana). Ndipo osakhulupirira ndidawapatsa nthawi, kenako ndidawathira m’dzanja. Nanga chidali bwanji chilango changa

    [45] “Ndi midzi ingati tidaiononga yomwe inkachita zoipa? Zipupa zitagwera pa madenga ake. Ndipo ndi zitsime (zingati) zomwe zidasiidwa, ndi nyumba zikuluzikulu zomwe zidali zolimba

    [46] “Kodi sayendayenda pa dziko kuti akhale ndi mitima (yanzeru) yowazindikiritsa ndi makutu omvera? Ndithu maso sagwidwa khungu, (khungu loononga chipembedzo), koma mitima yomwe ili m’zifuwa ndi imene imagwidwa khungu (loononga chipembedzo)

    [47] “Ndipo akukufulumizitsa kuti udzetse chilango. Komatu Allah sadzaswa lonjezo Lake (limene adaliika lakuti chilango chenicheni chidzakhala patsiku la chimaliziro). Ndipo ndithu tsiku limodzi kwa Mbuye wako lili ngati zaka chikwi chimodzi mukawerengedwe kanu

    [48] “Kodi ndi (anthu a) midzi ingati amene ndidawapatsa nthawi pomwe ankachita zoipa? Kenako ndidawathira m’dzanja. Ndipo kwa Iye nkobwerera

    [49] “Nena: “E inu anthu! Ndithu ine kwa inu ndine Mchenjezi woonekera.”

    [50] ““Tsono amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, chikhululuko ndi rizq laulemu zili pa iwo.”

    [51] ““Ndipo amene akulimbikira kulimbana ndi Ayah Zathu, iwowo ndi anthu a ku Moto.”

    [52] “Ndipo palibe pamene tidatuma mtumiki ngakhale m’neneri patsogolo pako, koma akamawerenga, satana amaponya (zosokoneza) m’kuwerenga kwakeko; koma Allah amachotsa zomwe satana akuponya; kenako nkuzilongosola Ayah Zake. Ndipo Allah Ngodziwa kwambiri, Wanzeru zakuya

    [53] “(Izi zimachitika) kuti achichite chimene satana akuponya kukhala mayeso kwa omwe m’mitima mwawo muli matenda ndi ouma mitima yawo; ndithu osalungama ali m’kusiyana komwe kuli kutali (ndi choonadi)

    [54] “Ndipo kuti adziwe amene apatsidwa kuzindikira kuti chimenechi n’choonadi chochokera kwa Mbuye wako ndi kuchikhulupirira ndikuti mitima yawo idzichepetse kwa Iye; ndithu Allah ndi Woongolera ku njira yolunjika amene akhulupirira

    [55] “Ndipo amene sadakhulupirire apitilira kukhala m’chikaiko ndi chimenecho (wadza nachocho) kufikira tsiku la chimaliziro liwadzera mowatutumutsa, kapena chiwadzera chilango pa tsiku lopanda chabwino (kwa iwo)

    [56] “Ufumu tsiku limenelo ngwa Allah; adzaweruza (mwachilungamo) pakati pawo; choncho amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, adzakhala m’Minda yamtendere

    [57] “Ndipo amene sadakhulupirire (Allah ndi Mtumiki Wake) ndikutsutsa Ayah Zathu, iwo adzapeza chilango choyalutsa

    [58] “Ndipo amene asamuka chifukwa cha chipembedzo cha Allah, kenako ndikuphedwa kapena kufa, ndithu Allah adzawapatsa (patsiku la chiweruziro) zopatsa zabwino. Ndithu Allah Ngwabwino popatsa kuposa opatsa

    [59] “Ndithu adzawalowetsa pamalo pomwe adzapayanja. Ndithu Allah Ngodziwa; Ngodekha

    [60] “Zimenezi zili chonchi, ndipo yemwe akubwezera kulanga molingana ndi momwe iye adalangidwira; kenakonso nkuchitidwa mtopola, ndithu Allah amthangata; Allah Ngofufuta uchimo; Wokhululuka kwambiri

    [61] “Zimenezo nchifukwa chakuti Allah amalowetsa usiku mu usana ndikulowetsa usana mu usiku, ndi chifukwanso chakuti ndithu Allah Ngwakumva Ngopenya

    [62] “Zimenezo nchifukwa chakuti Allah ndi Wowona (alipo;) ndipo zimene akuzipembedza kusiya Iye, nzachabe. Ndipo Allah Ngwapamwambamwamba Ngwamkulu

    [63] “Kodi suona kuti Allah amatsitsa madzi kuchokera ku mitambo, ndipo nthaka imakhala yobiriwira? Ndithu Allah Ngodziwa zobisika ndiponso Ngodziwa zoonekera

    [64] “Zakumwamba ndi zapansi zonse ndizake; ndithu Allah Ngwachikwanekwane; Wotamandidwa

    [65] “Kodi sudaone kuti Allah wakufewetserani zonse zam’nthaka ndi zombo zomwe zikuyenda panyanja mwa lamulo Lake? Ndipo wagwira thambo kuti lisagwe panthaka koma kupyolera m’chilolezo Chake; ndithu Allah Ngodekha kwa anthu Ngwachifundo

    [66] “Ndipo Iye ndi Amene adakupatsani moyo; kenako adzakupatsani imfa, ndipo kenako adzakuukitsani; ndithu munthu ngosathokoza

    [67] “Mpingo uliwonse tidauikira machitidwe amapemphero omwe akuwatsata; choncho asatsutsane nawe pachinthu ichi, ndipo itanira anthu ku chipembedzo cha Mbuye wako. Ndithu iwe uli pachiongoko changwilo

    [68] “Ndipo ngati atsutsana nawe, nena: “Allah Ngodziwa koposa zimene mukuchita.”

    [69] ““Allah adzaweruza pakati panu tsiku la Qiyâma pa zimene mudali kusiyana.”

    [70] “Kodi sudziwa kuti Allah akudziwa zakumwamba ndi zapansi? Ndithu zonsezo zili m’kaundula (Wake), ndithu (kudziwika kwa) zimenezo kwa Allah nzosavuta

    [71] “Ndipo akupembedza milungu yabodza, kusiya Allah, yomwe (Allah) sadaitumizire umboni wakuti (ipembedzedwe) yomwenso iwo sakuidziwa bwino. Ndipo anthu osalungama sadzakhala ndi owathandiza

    [72] “Koma Ayah Zathu zomveka zikawerengedwa kwa iwo, uona kunyansidwa pankhope za amene sadakhulupirire. Ndipo amakhala pafupi kuwamenya amene amawawerengera Ayah Zathu. Nena: “Kodi ndikuuzeni zoipa kwambiri kuposa izi? Ndi Moto (wa Allah) umene wawalonjeza amene sadakhulupirire (Allah ndi Mtumiki Wake) amenewo ndi mabwelero oipa zedi.”

    [73] “E inu anthu! Fanizo laperekedwa; choncho limvereni. Ndithu amene mukuwapembedza m’malo mwa Allah, sangathe kulenga ntchentche ngakhale Atasonkhana (kuti athandizane) pachimenechi. Ndipo ngati ntchenche itawalanda chinthu, sangathe kuchilanda kuntchentcheyo. Wafooka kwenikweni wopempha ndi wopemphedwa

    [74] “Sadamlemekeze Allah, kulemekeza komuyenera. Ndithu Allah Ngwamphamvu Ngogonjetsa chilichonse

    [75] “Allah amasankha atumiki mwa angelo ndi mwa anthu. Ndithu Allah Ngwakumva; Ngopenya

    [76] “Akudziwa zimene zili patsogolo pawo ndi zimene zili pambuyo pawo; kwa Allah Yekha ndiko kobwerera zinthu

    [77] “E inu amene mwakhulupirira! Weramani ndikugwetsa nkhope zanu pansi ndipo mpembedzeni Mbuye wanu ndikuchita zabwino kuti mupambane

    [78] “Ndipo menyerani chipembedzo cha Allah, kumenyera kwa choonadi; Iye ndi Amene adakusankhani (kuti mukhale mpingo wabwino;) ndipo sadaike pa inu zinthu zolemera pa chipembedzo, ndi chipembedzo cha tate wanu Ibrahim. Iye (Allah) adakutchani Asilamu kuyambira kale (m’mabuku akale) ndi mu iyi, (Qur’an) kuti Mtumiki akhale mboni pa inu, inunso kuti mukhale mboni pa anthu. Choncho pempherani Swala moyenera, perekani Zakaat ndipo gwirizanani chifukwa cha Allah. Iye ndiye Mbuye wanu, Mbuye wabwino zedi, ndi Mthandizi wabwino zedi

    Okhulupirira

    Surah 23

    [1] “۞ Ndithu apambana okhulupirira (mwa Allah)

    [2] “Amene amakhudzumuka pa mapemphero awo (poipereka mitima yawo kwa Allah modzichepetsa)

    [3] “Ndi omwe amapewa zinthu zopanda pake (zachabe)

    [4] “Ndi omwe amakwaniritsa (nsanamira ya) chopereka (Zakaat)

    [5] “Ndi omwe amasunga umaliseche wawo

    [6] “Kupatula kwa akazi awo ndi adzakazi omwe manja awo akumanja apeza. Choncho iwo (pakukumana ndi amenewo) saali odzudzulidwa

    [7] “Koma omwe angafune zosemphana ndi izi (kulumikizana ndi mkazi posiya njira ziwirizi) iwowo ndiwo opyola malire (a Allah)

    [8] “Ndi amene amasunga malonjezo awo ndi zomwe akhulupirika nazo

    [9] “Ndi omwe akusunga mapemphero awo (popemphera mu nthawi zake ndi kutsata malamulo ake uku ali odzichepetsa)

    [10] “Iwo ndi olandira (zabwino tsiku la Qiyâma)

    [11] “Amene adzalandira Munda wamtendere (wotchedwa) Fir’dausi (Munda wapamwamba kwambiri). M’menemo iwo adzakhala nthawi yaitali

    [12] “Ndipo ndithu tidamlenga munthu kuchokera ku dongo labwino

    [13] “Kenako tidalenga ana ake ndi dontho lamadzi (ambewu ya munthu) lomwe lidaikidwa pamalo osungidwa

    [14] “Kenako tidalisintha dontholo kukhala magazi oundana; ndipo kenako magaziwo tidawasintha kukhala m’nofu; ndipo kenako m’nofu tidausintha kukhala mafupa; ndipo mafupawo tidawaveka minofu, kenako tidamsintha kukhala cholengedwa china. Choncho watukuka Allah, Wabwino polenga

    [15] “Kenako ndithu inu pambuyo pa zimenezo mudzamwalira

    [16] “Ndithu inu, kenako mudzaukitsidwa pa tsiku la Qiyâma

    [17] “Ndipo ndithu tapanga njira zisanu ndi ziwiri (mitambo) pamwamba panu, ndipo ndithu (Ife) sitisiya kulabadira zolengedwa

    [18] “Ndipo tatsitsa madzi mwamuyeso kuchokera kumwamba, ndi kuwakhazikitsa m’nthaka; ndipo ndithu Ife ndi okhoza kuwachotsa (kuti musathandizike nawo, koma sitidachite zimenezo chifukwa chokuchitirani chifundo)

    [19] “Ndi madzi amenewo, tidakupangirani minda ya kanjedza ndi mpesa, m’menemo inu mulinazo zipatso zambiri; ndipo mwazimenezo mumadya

    [20] “Ndipo (tidakupangirani) mtengo womera pa phiri la Sinai, womwe umatulutsa mafuta; ndipo ndindiwo kwa amene amadya. (Mtengo wake ndi mzitona)

    [21] “Ndipo ndithu m’ziweto muli lingaliro kwa inu. Timakumwetsani zomwe zili m’mimba mwake; ndipo m’zimenezo mukupeza zothandiza zambiri; ndipo zina mwa izo mumadya

    [22] “Ndipo pa msana pa izo ndi pamwamba pa zombo, mumanyamulidwa

    [23] “Ndipo ndithu tidamtuma Nuh kwa anthu ake, ndipo adati: “E inu anthu anga! Mpembedzeni Allah! Mulibe mulungu wina woti nkumpembedza kupatula Iye. Kodi simuopa (chilango Chake)

    [24] “Akuluakulu mwa anthu ake amene sadakhulupirire, adati: “Uyu sali kanthu, koma ndi munthu ngati inu; akufuna kuti adzipezere ubwino pa inu; ndipo Allah akadafuna (kukuphunzitsani) akadatuma angelo. Zoterezi sitidamvepo kumakolo athu akale.”

    [25] ““Uyu sali kanthu, koma ndi munthu wamisala; choncho muyembekezereni mpaka nthawi (yofera.”)

    [26] “(Nuh) adati: “Mbuye wanga ndipulumutseni pazomwe anditsutsa!”

    [27] “Choncho tidamuvumbulutsira (mawu akuti): “Panga chombo moyang’aniridwa ndi kudziwitsidwa ndi Ife.” Ndipo lamulo Lathu likadza ndi kufwamphuka madzi mu uvuni, lowetsa mkati mwake (mwa chombocho) chilichonse ziwiriziwiri, chachimuna ndi chachikazi ndi banja lako, kupatula yemwe liwu latsogola pa iye kuti aonongeke mwa iwo. Ndipo usandilankhule za omwe adzichitira (okha) zoipa ndithu iwo amizidwa (m’madzi)

    [28] “Ndipo ukakhazikika m’chombocho, iwe ndi amene uli nawo, nena: “Tikuthokoza Allah, amene watipulumutsa ku anthu osalungama.”

    [29] “Ndipo (potsika), nena: “E Mbuye wanga! Nditsitseni; kutsitsa kwa madalitso, pakuti Inu ndinu wotsitsa bwino kwambiri kuposa otsitsa.”

    [30] “Ndithu m’zimenezi muli zisonyezo. Ndithu Ife tili (ndi udindo) wowayesa ndi mayeso osiyanasiyana

    [31] “Kenako tidabweretsa m’badwo wina pambuyo pawo (omwe ndi Âdi)

    [32] “Ndipo tidatuma kwa iwo mtumiki (Hûd) wochokera mwa iwo, (yemwe ankati): “Pembedzani Allah! Mulibe mulungu wina kupatula Iye. Kodi simuopa

    [33] “Ndipo akuluakulu a mwa anthu ake amene adali osakhulupirira, ndikutsutsa za kukumana ndi tsiku la chimaliziro, omwe tidawapatsa kulemera pa moyo wa padziko lapansi, adati: “Uyu saali kanthu, koma ndi munthu monga inu; amadya zimene inu mumadya, ndi kumwa zomwe inu mumamwa

    [34] “Koma ngati mumvera munthu wonga inu, ndiye kuti mukhala otaika (oluza)

    [35] “Kodi akukulonjezani kuti mukadzafa ndikusanduka dothi ndi mafupa, mudzaukitsidwanso (m’manda)

    [36] “Sizingachitike, sizingachitike, zimene mukulonjezedwazi

    [37] “Palibe (moyo wina) koma moyo wathu wapadziko lapansiwu basi! Tikufa ndiponso kukhala ndi moyo! Ndipo sitidzaukitsidwa m’manda

    [38] “Uyu saali kanthu (amene akudzitcha kuti ndi Mtumiki) koma ndi munthu basi, akupekera Allah bodza, ndipo ife sitimkhulupirira.”

    [39] “(Mtumikiyo) adati: “E Mbuye wanga! Ndipulumutseni pachifukwa chakuti anditsutsa.”

    [40] “(Allah) adati: “Posachedwapa akhala odzinena.”

    [41] “Choncho, mkuwe wa (chilango) choonadi udawaononga, ndipo tidawachita ngati zinyalala (zongotengedwa ndi madzi). Choncho, kuonongeka kudatsimikizika pa anthu osalungama

    [42] “Ndipo titatero tidalenga mibadwo ina pambuyo pawo

    [43] “Palibe mtundu ungaifulumizitse kapena kuichedwetsa nthawi yake yofera

    [44] “Kenaka tidatuma atumiki Athu motsatizana; (wina pambuyo pa mnzake). Ndipo mbadwo uliwonse pamene adaufikira mtumiki wake, udamtsutsa; ndipo tidawaononga motsatana; ndipo tidawachita kukhala nkhani (za anthu.) Ndipo kuonongeka kudatsimikizika pa anthu osakhulupirira

    [45] “Zitatero tidatuma Mûsa ndi m’bale wake Harun ndi zozizwitsa Zathu, ndi umboni woonekera poyera

    [46] “Kwa Farawo ndi nduna zake. Koma onse adadzitukumula; ndipo adali anthu odzikweza

    [47] “Ndipo adati: “Ha! Tikhulupirire anthu awiri onga ife, omwe mtundu wawo ndi akapolo athu!”

    [48] “Choncho adawatsutsa onse awiri, ndipo adali m’gulu la oonongedwa

    [49] “Ndipo ndithu Mûsa tidampatsa buku kuti iwo aongoke

    [50] “Ndipo tidamchita mwana wa Mariya ndi mayi wake kukhala chisonyezo (choonetsa kukhoza kwathu). Ndipo tidawapatsa malo othawirapo, pachikweza, chokhazikika pomwenso padali akasupe

    [51] “E inu Atumiki! Idyani zakudya zabwino, ndipo chitani zabwino. Ndithu Ine ndi Wodziwa zonse zimene muchita

    [52] “(Tidauza mibadwo yawo): “Ndithu mpingo wanuwu ndi mpingo umodzi, ndipo Ine Ndine Mbuye wanu; choncho ndiopeni.”

    [53] “Koma adadula chinthu chawochi (chipembedzo chawo) pakati pawo mipatukomipatuko; gulu lililonse limasangalalira chimene lili nacho

    [54] “Choncho, asiye mu umbuli wawo kufikira nthawi (yakufa kwawo)

    [55] “Kodi akuganiza kuti tikamawapatsa chuma ndi ana

    [56] “Tikuwafulumizitsira zabwino? Sichoncho, koma iwo sakuzindikira

    [57] “Ndithu amene amakhala amantha chifukwa choopa Mbuye wawo, (ndi m’mene mathero awo adzakhalire)

    [58] “Ndi omwe amakhulupirira Ayah za Mbuye wawo

    [59] “Ndi omwenso saphatikiza Mbuye wawo ndi mafano

    [60] “Ndi omwenso amapereka (Zakaat ndi sadaka kuchokera m’chuma) chimene apatsidwa, uku mitima yawo ili yoopa kuti adzabwerera kwa Mbuye wawo

    [61] “Amenewa ndiamene akuchita changu pa zinthu zabwino, ndipo iwo akutsogolera (ena) pa zimenezo

    [62] “Ndipo sitikakamiza munthu, koma chimene angathe (kuchichita). Ndipo tili naye kaundula (wosunga chilichonse) yemwe adzayankhula choonadi ndipo iwo sadzaponderezedwa

    [63] “Koma mitima yawo ili m’kusalabadira mu ichi; ndipo iwo ali ndi ntchito zimene akuchita, osati izi

    [64] “Kufikira tikadzawaika m’chilango amene ali opeza bwino awo, pompo adzakuwa (ndi kupempha chipulumutso)

    [65] “(Kudzanenedwa kwa iwo): “Musalire lero (ndi kupempha chipulumutso)! Ndithu inu simupulumutsidwa ndi Ife.”

    [66] ““Ndipo Ayah Zanga zinkawerengedwa kwa inu koma munkadzibwezera kumbuyo ndi zidendene zanu

    [67] “Uku mukudzikweza; nkumakambirana usiku za chabechabe zoinyoza (Qur’an).”

    [68] “Kodi sadaganizire liwu (ili limene wadza nalo Mtumiki{s.a.w}), kapena zawadzera zomwe sizidawadzerepo makolo awo akale

    [69] “Kodi kapena sadam’dziwe Mtumiki wawoyu (makhalidwe ake) kotero kuti iwo akum’kana

    [70] “Kapena akunena kuti: “Ngwamisala?” Koma wawadzera ndi choonadi, ndipo ambiri a iwo amachida choonadi

    [71] “Ndipo choonadi chikadatsatira zofuna zawo, ndiye kuti thambo ndi nthaka ndi za m’menemo zikadaonongeka! Koma tawabweretsera chikumbutso chawo, koma iwo akuchipewa chikumbutso chawocho

    [72] “Kodi kapena ukuwapempha malipiro (nchifukwa chake akuchikana chipembedzochi)? Koma malipiro a Mbuye wako ndiwo abwino; ndipo Iye ndi Wopereka Wabwino kuposa opereka

    [73] “Ndipo ndithu iwe ukuwaitanira ku njira yolunjika; (supempha malipiro kwa iwo pa kuitanako)

    [74] “Ndipo ndithu amene sakhulupirira tsiku la chimaliziro, ali kutali ndi njira ya choonadi

    [75] “Ndipo tikadawachitira chifundo ndi kuwachotsera masautso omwe ali nawo, ndithu akadapitiriza kuyumbayumba m’kuchita kwawo zoipa

    [76] “Ndipo ndithu tidawalanga ndi chilango (chaukali), koma sadacheukire kwa Mbuye wawo ndikudzichepetsa

    [77] “Kufikira pamene tidawatsekulira khomo la chilango chaukali; pamenepo ndipo adataya mtima

    [78] “Ndipo Iye ndi Yemwe adakupangirani makutu, maso ndi mitima; nzochepa zimene mukuthokoza

    [79] “Iyenso ndi Yemwe wakufalitsani pa dziko; kenako mudzasonkhanitsidwa kwa Iye

    [80] “Ndipo Iye ndi Yemwe amapatsa moyo ndi imfa, ndipo kusinthana kwa usiku ndi usana Nkwake. Kodi simuzindikira

    [81] “Koma akunena monga (anthu) oyamba adanenera

    [82] “Akunena: “Kodi tikadzafa ndikukhala dothi ndi mafupa, tidzaukitsidwanso?”

    [83] ““Ndithudi ife ndi makolo athu kale tidalonjezedwa zimenezi, izi sikanthu koma nkhambakamwa za anthu akale.”

    [84] “Nena: “Kodi nthaka njayani ndi zomwe zili m’menemo, ngati inu mukudziwa (kanthu)!”

    [85] “Adzanena kuti: “Nza Allah!” Nena: “Nanga bwanji simukumkumbukira (kuti Iye Ngokhoza chilichonse)

    [86] “Nena: “Kodi ndani Mbuye wa thambo zisanu ndi ziwiri, ndi Mbuye wa Arsh (Mpando wachifumu) yaikulu?”

    [87] “Anena (kuti): “Nza Allah.” Nena: “Nanga bwanji simukumuopa?”

    [88] “Nena: “Kodi ndani yemwe m’manja mwake muli mphamvu yolamulira chinthu chilichonse? Ndipo Iye amateteza zonse. Ndipo palibe chimene chingatetezedwe kuchilango Chake. Ngati inu mukudziwa.”

    [89] “Anena (kuti): “Ndi Allah.” Nena: “Nanga mukulodzedwa bwanji (ndi satana)?”

    [90] “Koma tawabweretsera choonadi; ndithu iwo ngabodza (potsutsana ndi choonadicho)

    [91] “Allah sadadzipangire mwana, ndipo padalibe pamodzi ndi Iye mulungu (wina), ngati zikadakhala choncho ndiye kuti mulungu aliyense akadatenga zimene adalenga, ndipo milungu ina ikadaipambana milungu inzawo (polimbanirana ufumu), Allah wapatukana nazo kwambiri zimene akusimbazo

    [92] “Wodziwa zamseri ndi zapoyera; watukuka ku zimene akumphatikiza nazozo

    [93] “Nena: “E Mbuye wanga! Ngati mungandionetse zomwe akulonjezedwa (ndikadali ndi moyo)

    [94] “E Mbuye wanga! Musandiyike m’gulu la anthu osalungama.”

    [95] “Ndipo ndithu Ife ndi Wokhoza kukuonetsa (chilango) chimene tikuwalonjeza

    [96] “Chotsa zoipa (zimene akukuchitira) powabwezera zabwino; Ife tikudziwa zimene akunena

    [97] “Ndipo nena: “E Mbuye wanga! Ndikudzitchinjiriza ndi Inu kumanong’onong’o a satana.”

    [98] ““Ndiponso ndikudzitchinjiriza ndi inu Mbuye wanga kuti asandidzere.”

    [99] “Kufikira m’modzi wawo ikam’dzera imfa, amanena: “Mbuye wanga! Ndibwezereni (ku moyo wa pa dziko),”

    [100] ““Kuti ndikachite zabwino pa zimene ndidasiya.” (Angelo amayankha kuti): “Iyayi! Ndithu awa ndi mawu basi amene iye akuyankhula (imfa ikamfika).” Ndipo patsogolo pawo pali chiyembekezo; (moyo wamasautso kwa oipa; ndipo wamtendere kwa abwino) kufikira tsiku limene adzaukitsidwa

    [101] “Choncho, lipenga likadzaimbidwa, sipadzakhala chibale pakati pawo tsiku limenelo, ndipo sadzafunsana

    [102] “Tsono omwe mlingo (wa zochita zawo zabwino) udzalemere, iwowo ndiwo opambana

    [103] “Ndipo omwe miyeso yawo (ya zochita zabwino) idzatsike, iwowo ndi omwe adadziluzitsa okha; adzakhala ku Jahannam nthawi yaitali

    [104] “Moto ukawawula nkhope zawo, ndipo adzakhala m’menemo uku mano ali pamtunda

    [105] “(Adzauzidwa): “Kodi Ayah Zanga sizidali kuwerengedwa kwa inu ndipo inu nkumazitsutsa?”

    [106] “Adzati: “Mbuye wathu! Zoipa zathu zidatigonjetsa, choncho tidali anthu osokera.”

    [107] “Mbuye wathu! Titulutseni umu (m’moto ndikutibwezera ku dziko lapansi kuti tikachite ntchito yabwino); ngati titabwerezanso kuchita zoipa, ndiye kuti tidzakhaladi oipa (odziononga tokha).”

    [108] “(Allah) adzati: “Khalani chete m’menemo, monyozeka! Ndipo musandilankhule!”

    [109] “Ndithu mwa akapolo anga lidalipo gulu lomwe linkanena: “Mbuye wathu! Takhulupirira; choncho tikhululukireni ndi kutichitira chifundo; ndipo inu Ngabwino kwambiri kuposa (ena onse) ochita chifundo.”

    [110] ““Koma inu mudawachita chipongwe kufikira adakuiwalitsani kundikumbuka uku muli kuwaseka.”

    [111] ““Ndithu Ine lero ndawalipira (Munda wamtendere) chifukwa cha kupirira kwawo; kuti ndithu iwo ndiwo opambana.”

    [112] “Adzanena: “Kodi mudakhala nthawi yotani padziko pa chiwerengero cha zaka?”

    [113] “Adzayankha: “Tidakhala tsiku limodzi kapena gawo la tsiku; afunse owerengera.” (Adzatero poyerekeza ndi kutalika kwa moyo wamasautso ku Moto)

    [114] “Adzanena: “Inu simudakhale (kudzikoko) koma pang’ono basi, mukadakhala mukudziwa (chilango chomwe chakufikanichi, sibwenzi mukuchita zoipa).”

    [115] “Kodi mumaganiza kuti tidakulengani chabe, ndikuti simudzabwerera kwa Ife

    [116] “Watukuka Allah, Mfumu ya choonadi; palibe wompembedza mwachoonadi koma Iye, Bwana wa Arsh (Mpando wachifumu) yolemekezeka (kwambiri)

    [117] “Ndipo amene apembedza mulungu wina pomphatikiza ndi Allah, chikhalirecho iye alibe umboni pa zimenezo; basi chiwerengero chake chili kwa Mbuye wake. Ndithu osakhulupirira sangapambane

    [118] “Choncho nena: “Mbuye wanga! Ndikhululukireni ndikundichitira Chifundo! Inu Ngabwino kuposa achifundo.”

    Kuwala

    Surah 24

    [1] “Iyi ndi Sura; taivumbulutsa, ndipo taikamo malamulo. Ndipo m’menemo tatumizamo Ayah (ndime) zomveka kuti mukumbukire (malamulo ndi kuchita nawo m’njira yoyenera)

    [2] “Mkazi wachiwerewere ndi mwamuna wa chiwerewere aliyense wa iwo mkwapuleni zikoti zana limodzi . Musagwidwe chisoni ndi iwo pa chipembedzo (malamulo) cha Allah, ngati inu mukukhulupiriradi mwa Allah ndi tsiku la chimaliziro. Ndipo gulu la okhulupirira lionelere chilango chawo

    [3] “Mwamuna wa chiwerewere sakwatira mkazi (wabwino) koma wachiwerewere mnzake, kapena mkazi wopembedza mafano. Nayenso mkazi wachiwerewere sakwatiwa ndi mwamuna (wabwino) koma wachiwerewere mnzake, kapena wopembedza mafano. Ndipo zimenezi zaletsedwa kwa okhulupirira

    [4] “Ndipo amene akunamizira akazi odziteteza (powanamizira kuti achita chiwerewere), ndipo osabwera nazo mboni zinayi, akwapuleni zikoti ; ndiponso musauvomereze umboni wawo mpaka kalekale. Iwo ngotuluka m’chilamulo cha Allah

    [5] “Kupatula amene alapa pambuyo pa zimenezo, ndipo nkukonza (zochita zawo), ndithu Allah Ngokhululuka; Ngwachisoni, (awakhululukira)

    [6] “Ndipo amene akunamizira akazi awo (kuti achita chiwerewere) ndipo iwo nkukhala opanda mboni, koma (iwo) okha, choncho umboni wa mmodzi wa iwo (umene ungamchotsere chilango chomenyedwa zikoti ), ndikupereka umboni kanayi polumbilira Allah kuti ndithu iye ndi mmodzi mwa onena zoona

    [7] “Ndipo kachisanu (alumbire) kuti matembelero a Allah akhale pa iye ngati (iye) ali m’modzi mwa onama

    [8] “Ndipo (mkazi) chilango amchotsera atapereka umboni kanayi polumbilira Allah kuti (uyu mwamuna) ndi mmodzi mwa onama

    [9] “Ndipo kachisanu (alumbire) kuti mkwiyo wa Allah ukhale pa iye ngati (mwamuna wake) ali mmodzi mwa onena zoona

    [10] “Ndipo pakadapanda ubwino wa Allah ndi chifundo Chake pa inu (mukadavutika). Ndipo ndithu Allah Ngolandira kulapa;. Wanzeru zakuya

    [11] “Ndithu amene adza ndi bodza (ponamizira Mayi Aisha {r.a}, yemwe ndi Mkazi wa Mtumiki {s.a.w}, kuti wachita chiwerewere), ndi gulu la mwa inu. Musaganizire zimenezo kuti nzoipa kwa inu, koma kuti zimenezo nzabwino kwa inu. Ndipo munthu aliyense wa iwo apeza (chilango) pa machimo amene wawachitawo. Ndipo yemwe wasenza gawo lalikulu la uchimowo mwa iwo, adzapeza chilango chachikulu

    [12] “Nanga bwanji pamene mudaimva (nkhani) iyi okhulupirira achimuna ndi okhulupirira achikazi saadaganizire anzawo zabwino ndikunena kuti: “Ili ndi bodza loonekera?”

    [13] “Nanga bwanji sadabweretse mboni zinayi (pa zimenezi)? Ndipo pamene alephera kubweretsa mboni, iwo ngabodza kwa Allah

    [14] “Ndipo pakadapanda ubwino wa Allah ndi chifundo Chake pa inu, pa dziko lapansi ndi patsiku la chimaliziro, chilango chachikulu chikadakukhudzani pa zomwe munkazijijirikira

    [15] “Pamene mudalilandira (bodzalo) ndi malirime anu ndi kumanena ndi milomo yanu zomwe inu simukuzidziwa, ndipo mumaganizira kuti ndi chinthu Chochepa pomwe icho kwa Allah ndi chinthu chachikulu

    [16] “Ndipo nanga bwanji pamene mudalimva (bodzalo) simudanene (kuti): “Sikoyenera kwa ife kuyankhula izi; kuyera nkwanu (Mbuye wathu). Ili ndi bodza lalikulu.”

    [17] “Allah akukulangizani kuti: “Musabwerezenso kuchita zonga zimenezi mpaka kalekale, ngati inu muli okhulupirira enieni.”

    [18] “Ndipo Allah akukufotokozerani Ayah (ndime) Zake mwatsatanetsatane. Ndipo Allah Ngodziwa; Ngwanzeru zakuya

    [19] “Ndithu amene akukonda kuti zoipa zifale pa amene akhulupirira, chilango chowawa chili pa iwo padziko lapansi ndi patsiku la chimaliziro. Ndipo Allah ndi yemwe akudziwa (zoyenerana ndi inu), koma inu simudziwa

    [20] “Ndipo pakadapanda ubwino wa Allah ndi chifundo Chake pa inu, (pakadapezeka zauve). Koma ndithu Allah Ngoleza; Ngwachisoni chosatha

    [21] “E inu amene mwakhulupiliira! Musatsatire mapazi a satana. Ndipo amene atsatire mapazi a satana (asokera) ndithudi iye akulamula zauve ndi zoipa. Ndipo pakadapanda ubwino wa Allah ndi chifundo Chake pa inu, sakadayera aliyense mwa inu mpaka kalekale. Koma Allah amamuyeretsa amene wamfuna. Ndipo Allah Ngwakumva zonse; Wodziwa kwambiri

    [22] “Ndipo ochita zabwino (pa dziko lapansi), ndiponso eni kupeza bwino mwa inu, asalumbire kuti aleka kupatsa achinansi, masikini, ndi osamuka pa njira ya Allah. Koma akhululuke ndikuleka zimenezo. Kodi simufuna kuti Allah akukhululukireni? Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha (choncho, nanunso teroni)

    [23] “Ndithu amene akunamizira akazi oyera (kumachitidwe achiwerewere), odziteteza kumachitidwe oipa, okhulupirira, atembeleredwa pa dziko lapansi ndi patsiku la chimaliziro. Ndipo chilango chachikulu chili pa iwo

    [24] “Tsiku lomwe malirime awo, mikono yawo ndi miyendo yawo zidzawachitira umboni pazomwe adali kuchita

    [25] “Tsiku limenelo Allah adzawapatsa mphotho yawo ya choonadi, ndipo adzadziwa kuti Allah ndiye Mwini kulipira kwa choonadi koonekera poyera

    [26] “Akazi oipa ndi a amuna oipa, naonso amuna oipa ndi a akazi oipa; ndipo akazi abwino ndi a amuna abwino, naonso amuna abwino ndi a akazi abwino. Iwowa ngopatulidwa kuzimene akunenazo. Iwo adzapeza chikhululuko ndi rizq laulemu (ku Munda wamtendere)

    [27] “E inu amene mwakhulupirira! Musalowe m’nyumba zomwe sinyumba zanu kufikira mutapempha chilolezo poodira ndikupereka Salaam kwa eni nyumbazo. Kutero ndi kwa bwino kwa inu kuti mukumbukire (nkuona kuti zomwe mukuuzidwa nzabwino)

    [28] “Koma ngati simupeza munthu aliyense m’menemo, musalowe kufikira mutapatsidwa chilolezo. Ndipo mukauzidwa kuti: “Bwererani.” Bwererani; chimenechi nchokuyeretsani. Ndipo Allah akudziwa zimene muchita

    [29] “Sikulakwa kwa inu kulowa m’nyumba zosakhalidwa, (monga sitolo, hotela; popanda chilolezo), momwe muli zokuthandizani; ndipo Allah akudziwa zomwe mukuonetsera poyera ndi zimene mukubisa

    [30] “Auze okhulupirira achimuna kuti adzolitse maso awo (asayang’ane zoletsedwa), ndipo asunge umaliseche wawo. Ichi nchoyera kwambiri kwa iwo. Ndithu Allah akudziwa nkhani za zonse zomwe achita

    [31] “Ndipo auze okhulupirira achikazi kuti adzolitse maso awo, ndikusunga umaliseche wawo, ndipo asaonetse (poyera) zomwe amadzikongoletsa nazo kupatula zimene zaonekera poyera (popanda cholinga chotero). Ndipo afunde kumutu mipango yawo mpaka m’zifuwa zawo; ndipo asaonetse poyera zodzikongoletsa nazo koma kwa amuna awo, kapena atate awo, kapena apongozi awo, kapena ana awo, kapena ana a amuna awo, kapena abale awo, kapena ana a abale awo, kapena ana a alongo awo, kapena akazi anzawo (achisilamu). Kapena yemwe wapatidwa ndi dzanja lamanja (monga kapolo), kapena otsatira (antchito) omwe ndi amuna opanda zilakolako za akazi ndi ana omwe sadziwa za akazi. Ndipo asamenyetse miyendo yawo (pansi) kuti zidziwike zimene akubisa mwa zomwe amadzikongoletsa nazo. Ndipo tembenukirani kwa Allah, nonse inu okhulupirira kuti mupambane

    [32] “Ndipo zikwatitseni mbeta za mwa inu (mfulu), ndi akapolo anu amene ali abwino (achimuna) ndi adzakazi anu. Ngati ali osauka Allah awalemeletsa kuchokera m’zabwino Zake. Ndipo Allah za ufulu Zake nzambiri (zopanda muyeso, ndiponso) Ngodziwa kwabasi

    [33] “Ndipo amene sapeza chokwatilira apewe (uve wa chiwerewere) kufikira Allah atawalemeletsa ndi zabwino Zake. Ndipo amene afuna kuti awalembere (kuti apate ufulu) mwa amene manja anu akumanja apeza, alembereni (kuti adziombole) ngati mwaona zabwino mwa iwo. Ndipo apatseni gawo la chuma cha Allah chomwe akupatsani. Musawakakamize adzakadzi anu kuchita uhule ngati akufuna kudzisunga, ncholinga choti mupeze zinthu za moyo wa dziko lapansi. Ndipo amene angawakakamize, ndithu Allah, pambuyo pokakamizidwa kwawoko, Ngokhululuka; Ngwachisoni (kwa okakamizidwawo)

    [34] “Ndipo ndithu tatumiza kwa inu Ayah (ndime) zofotokoza (zofunika zonse) mwatsatanetsatane, ndi mafanizo (okuphanulani maso) pa za amene adamuka patsogolo panu, ndi phunziro kwa oopa (Allah)

    [35] “Allah ndiye Kuunika kwa kuthambo ndi nthaka. Fanizo la kuunika Kwake (powaongolera akapolo Ake) lili ngati “Mishikati” (chibowo cha pa khoma choikapo nyali) yomwe mkati mwake mwaikidwa nyali. Nyali ili m’galasi. Ndipo galasilo lili ngati nyenyezi yowala. Nyali imeneyo imayatsidwa ndi mafuta ochokera ku mtengo wodalitsidwa wa mzitona, womwe suli mbali yakuvuma ngakhale kuzambwe; (umamenyedwa kwambiri ndi dzuwa pamene likutuluka, ndi parnene likulowa). Mafuta ake ngoyandikira kuwala okha (chifukwa champhamvu yake) ngakhale moto usanawakhudze. Kuunika pamwamba pa kuunika! Allah amamuongolera ku kuunika Kwake amene wamfuna. Allah amaponya mafanizo kwa anthu (kuti aganizire ndi kupeza phunziro), ndipo Allah Ngodziwa chilichonse

    [36] “(Apezeke akupemphera kasanu) m’nyumba zomwe Allah walamula kuti zilemekezedwe; ndipo m’menemo dzina Lake litchulidwe; azimulemekeza m’menemo (m’misikiti) kum’mawa ndi kumadzulo

    [37] “Anthu omwe malonda ogulitsa ndi kugula sawatangwanitsa posiya kukumbukira Allah ndi kupemphera (Swala) ndi kupereka chopereka (Zakaat) naopa tsiku lomwe mitima ndi maso zidzatembenukatembenuka

    [38] “Kuti Allah adzawalipire zabwino pa zomwe adachita ndi kuwaonjezera zabwino Zake. Ndipo Allah amampatsa amene wamfuna popanda chiwerengero

    [39] “Ndipo amene sadakhulupirire, ntchito zawo (zimene akuziona ngati zabwino) zidzakhala ngati zideruderu m’chipululu chamchenga; waludzu nkumaganizira kuti ndimadzi; ndipo akapita pamenepo, osapezapo chilichonse. (Nawonso pomwe adzadza kuzochita zawo zabwino patsiku la Qiyâma sadzapeza mphotho iliyonse, chifukwa chakuti adachimenya nkhondo Chisilamu). Ndipo adzapeza Allah kumeneko, ndipo adzamkwaniritsira chiwerengero chake ndipo Allah Ngwachangu powerengera

    [40] “Kapena (ntchito zawo zoipazo) zili ngati m’dima mkati mwa nyanja yamadzi ochuluka yomwe yaphimbidwa ndi mafunde, ndipo pamwamba pa mafundewo pali mafundenso. Ndiponso pamwamba pake (mafundewo) pali mitambo. M’dima uwu pamwamba pa m’dima uwu. Akatulutsa mkono wake, sangathe kuuona (chifukwa cha kuchindikala kwa m’dima). Ndipo amene Allah sadampatse kuunika, sakhala nako kuunika

    [41] “Kodi suona kuti zonse zopezeka kumwamba ndi pansi zikumulemekeza Allah, kudzanso mbalame zikatambasula mapiko ake (ngakhalenso zikapanda kutambasula). Chilichonse (mwa zimenezo) chikudziwa pemphero lake ndi m’mene chingamulemekezere (Mlengi wake). Ndipo Allah Ngodziwa zonse zimene akuchita

    [42] “Ufumu wakumwamba ndi pansi, ngwa Allah (Yekha); ndipo kobwerera kwa zonse nkwa Allah

    [43] “Kodi suona kuti Allah akuyendetsa mitambo, kenako nkuikumanitsa pamodzi, ndipo kenako nkuikhazika m’milumilu? Nuona mvula ikutuluka pakati pa iyo. Iye akutsitsa mapiri amitambo kuchokera kumwamba momwe muli mvula yamatalala; ndipo amamenya nawo amene wamfuna, ndikumpewetsa amene wamfuna. Kung’anima kwake kumayandikira kuchititsa khungu

    [44] “Allah amasintha usiku ndi usana (pambuyo pa usiku, umadza usana, ndipo pambuyo pa usana, umadza usiku). Ndithu m’zimenezo muli phunziro kwa anthu ozindikira (zinthu)

    [45] “Ndipo Allah adalenga ndi madzi nyama iliyonse; (madzi ndicho chiyambi cha zolengedwa zonse). Zina mwa izo zimayendera mimba zawo; ndipo zina mwa izo zimayenda ndi miyendo iwiri; ndipo zina mwa izo zimayenda ndi inayi. Ndithu Allah amalenga chimene wafuna; ndithu Allah ali ndi mphamvu pa chilichonse

    [46] “Ndithu tavumbulutsa Ayah (ndime) zofotokoza momveka (chilichonse chofunika pa chipembedzo). Ndipo Allah amamuongolera ku njira yolunjika amene wamfuna

    [47] “Ndipo akunena (kuti): “Takhulupirira Allah ndi Mtumiki, ndipo tamvera.” Kenako ena a iwo amatembenuka pambuyo pa zimenezo; ndipo iwowo sali okhulupirira

    [48] “Ndipo akawaitanira kwa Allah ndi Mtumiki Wake kuti awaweruze pakati pawo, ena a iwo akukana zimenezo (akadzizindikira okha kuti ngolakwa)

    [49] “Koma akaona kuti chilungamo chili kwa iwo, amam’dzera (Mtumiki mwachangu) uku akusonyeza kumvera

    [50] “Kodi ali ndi matenda m’mitima mwawo? Kapena akukaika, kapena akuopa kuti Allah ndi Mtumiki Wake awachitira chinyengo? Koma iwo ndi amene ali osalungama

    [51] “Ndithu yankho la okhulupirira akaitanidwa kwa Allah ndi Mtumiki Wake kuti aweruze pakati pawo silikhala lina koma kunena kuti: “Tamva ndipo titsatira.” Iwowo ndiwo opambana

    [52] “Ndipo amene amvera Allah ndi Mtumiki Wake, ndikumalemekeza Allah ndi kumuopa, iwowo ndiwo opambana

    [53] “Ndipo akulumbilira dzina la Allah, kulumbira kwakukulu kuti ukawalamula (kupita ku nkhondo), ndithu apita. Nena: “Musalumbire; kumvera kwanu nkodziwika (kuti nkwabodza); ndithu Allah akudziwa nkhani zonse zomwe muchita

    [54] “Nena: “Mverani Allah, ndiponso Mverani Mtumiki. Koma ngati mutembenuka, iye ali nazo zimene wasenzetsedwa (kuti azifikitse kwa inu), (ndipo) inunso muli nazo zimene mwasenzetsedwa (kuti muzitsate). Ndipo mukamumvera, muongoka. Ndipo pa Mtumiki palibe china chake koma kufikitsa (uthenga) momveka

    [55] “Allah walonjeza mwa inu amene akhulupirira ndikuchita ntchito yabwino kuti ndithu awathandiza kukhala oyang’anira pa dziko monga momwe adawachitira amene adalipo kale kukhala oyang’anira; ndipo ndithu awalimbikitsira chipembedzo chawo chimene wawayanja nacho; ndipo awachotsera mantha awo kukhala opanda mantha.” Akhale akundilambira Ine, osandiphatikiza ndi chilichonse. Ndipo amene asiye kukhulupirira pambuyo pa zimenezi, iwo ngakuswa malamulo

    [56] “Choncho, pempherani Swala moyenera ndi kupereka “Zakaat;” ndiponso mverani Mtumiki kuti muchitiridwe chisoni

    [57] “Amene sadakhulupirire musawaganizire kuti angamulepheretse Allah pa dziko (kuwalanga), ndipo malo awo ndi ku Moto. Ha! Ayipirenji malo obwererako

    [58] “E inu amene mwakhulupirira! Akuodireni amene manja anu akumanja apeza ndi amene mwa inu sanathe nsinkhu, awodire nthawi zitatu: Isanapempheredwe Swala ya m’mawa, ndi pamene mukuvula nsalu zanu nthawi yamasana (kuti mupumule), ndi pambuyo pa Swala ya Isha (usiku). Izi ndi nthawi zitatu zomwe inu mumakhala wamba. Palibe uchimo pa inu ngakhale pa iwo pambuyo pa nthawi zimenezo (kulowa popanda kuodira); mumazungulirana pakati panu, umo ndi momwe akukufotokozerani Allah Ayah (ndime) Zake. Ndipo Allah Ngodziwa; Ngwanzeru zakuya

    [59] “Ndipo mwa inu ana akatha nsinkhu, aodire monga momwe adali kuodira omwe adalipo patsogolo pawo. Umo ndi momwe Allah akukufotokozerani Ayah (ndime) Zake. Ndipo Allah Ngodziwa; Ngwanzeru zakuya

    [60] “Nayonso mikwezembe (nkhalamba zachikhalire zazikazi) yomwe siyembekezera kukwatiwa, palibe uchimo pa iyo kusiya kufunda nsalu zawo (kumutu), popanda kuonetsa zodzikongoletsera zawo. Koma ngati zikudzikakamiza kuleka kuvula mipangoyo, ndibwino kwa iyo. Ndithu Allah Ngwakumva; Ngodziwa

    [61] “Palibe kulakwa pa akhungu (osapenya) ndiponso palibe kulakwa pa olumala; palibenso kulakwa pa odwala, ngakhalenso pa inu eni ngati muli kudya m’nyumba zanu kapena m’nyumba za atate anu, kapena m’nyumba za amayi anu, kapena m’nyumba za abale anu, kapena m’nyumba za alongo anu, kapena m’nyumba za abambo anu ang’ono kapena akulu, kapena m’nyumba za azakhali anu, kapena m’nyumba za atsibweni anu, kapena m’nyumba za amayi anu akulu kapena ang’ono, kapena m’nyumba za omwe mukuwasungira makiyi, kapena (m’nyumba za) anzanu; palibe kulakwa pa inu ngati mukudyera limodzi kapena payekhapayekha. Ndipo mukamalowa m’nyumba dziperekereni nokha salaamu. (lonjero ili) ndi malonje ochokera kwa Allah amadalitso, abwino. Umo ndi momwe Allah akukulongosolerani Ayah (ndime) Zake kuti muzindikire

    [62] “Ndithu okhulupirira (owona) ndiamene akhulupirira mwa Allah ndi Mtumiki Wake; ndipo akakhala naye pa chinthu chokhudza onse, sachoka mpaka atampempha (Mtumiki) chilolezo. Ndithu amene akukupempha chilolezo, iwowo ndi amene akukhulupirira Allah ndi Mtumiki Wake. Choncho akakupempha chilolezo chifukwa cha zinthu zawo zina, muloleze mwa iwo amene wamfuna (ngati utaona kuti chidandaulo chake nchoona), ndipo uwapemphere chikhululuko kwa Allah; ndithu Allah Ngokhululuka kwabasi; Ngwachisoni chosatha

    [63] “Kumuitana Mtumiki pakati panu musakuchite monga momwe mumaitanirana nokhanokha, ndithu Allah akudziwa amene akuchoka pamalo mozemba ndi modzibisa mwa inu. Choncho achenjere amene akunyozera lamulo lake kuti mliri ungawapeze, kapena kuwapeza chilango chowawa

    [64] “Mverani! Ndithu zili kumwamba ndi pansi nzake Allah, ndipo akudziwa zimene muli nazo. Ndipo patsiku limene adzabwezedwe kwa Iye, adzawauza zimene adachita ndipo Allah Ngodziwa chilichonse

    Chosiyanitsa

    Surah 25

    [1] “Watukuka Mwini kupereka madalitso, Yemwe wavumbulutsa Qur’an kwa kapolo Wake kuti ikhale mchenjezi kwa zolengedwa zonse

    [2] “(Allah) Yemwe Ngwake ufumu wa kumwamba ndi wa pansi. Ndipo sadabale mwana ndipo alibenso wothandizana naye pa ufumu (Wake). Adalenga chinthu chilichonse ndikuchilinga mlingo wake

    [3] “Ndipo m’malo mwa Iye (Mulungu weniweni, osakhulupirira) adzipangira milungu yomwe siilenga chilichonse koma iyo ndiyomwe idalengedwa; ndiponso ilibe mphamvu yodzichotsera masautso ngakhale kudzidzetsera zothandiza. Ndiponso ilibe mphamvu zoperekera irnfa ndi moyo, ngakhale kuukitsa akufa

    [4] “Ndipo osakhulupirira akunena: “Ichi sikanthu (Qur’an imene Muhammad {s.a.w} wadza nayo) koma ndi chonama chimene wachipeka, ndipo pachimenechi amthandiza anthu ena (eni mabuku).” Kunena zoona, iwo (osakhulupirira) adza ndi chinyengo ndi bodza (pazonena zawozi)

    [5] “Ndipo (osakhulupirira) akunena: “Iyi (Qur’an) ndi nthano za anthu akale zomwe (Muhammad {s.a.w}) adazilembetsa. Choncho zikulakatulidwa kwa iye m’mawa ndi madzulo (kuti aloweze).”

    [6] “Nena: “Adaivumbulutsa Yemwe akudziwa zobisika za m’thambo ndi m’nthaka. Ndithu Iye ali Wokhululuka; Wachisoni, (nchifukwa chake sakukulangani mwachangu pazimene mukunenazi).”

    [7] “Ndipo akunena: “Ndi Mtumiki wanji uyu, womadya chakudya nkumayenda m’misika? Kodi bwanji sadatumizidwe mngelo kwa iye kuti azikhala naye limodzi uku akuchenjeza?”

    [8] ““Kapena kuponyeredwa nkhokwe (za chuma), kapena kukhala ndi munda ndikumadya m’menemo?” Ndipo osalungama akuti: “Ndithudi, mukutsatira munthu wolodzedwa.”

    [9] “Ona momwe akukuponyera mafanizo (omwe sali oyenerana nawe, nthawi zina akuti ndiwe wolodzedwa wamisala, wabodza, wophunzitsidwa ndi anthu ena) choncho asokera, ndipo sangathe kupeza njira (yoongoka yokunenera)

    [10] “Watukuka Mwini kupereka madalitso ambiri, Yemwe akafuna, akuchitira zabwino kuposa zimenezi, (adzakupatsa pa tsiku lachimaliziro) Minda yamtendere yomwe pansi (ndi patsogolo) pake pakuyenda mitsinje; ndipo adzakupangira nyumba zikuluzikulu zachifumu

    [11] “Koma akutsutsa zanthawi ya Qiyâma. ndipo tawakonzera Moto woyaka (iwo) amene akutsutsa zanthawi ya Qiyâma (ya chimaliziro)

    [12] “(Motowo) ukadzawaona (naonso nkuuona) kuchokera pa malo apatali, (iwo) adzamva mkwiyo wa Motowo ndi mkokomo wake

    [13] “Ndipo akadzaponyedwa m’menemo, pamalo opanika uku manja atanjatidwa chakukhosi, pamenepo adzaitana imfa (kuti iwafike, afe apumule ku masautsowo)

    [14] “(Tidzawauza): “Lero musaitane imfa imodzi, koma itanani imfa zambiri (ndipo simupeza mpumulo koma mazunzo okhaokha).”

    [15] “Nena (kwa osakhulupirira): “Kodi izi ndizo zabwino, kapena munda wamuyaya umene alonjezedwa oopa Allah kuti udzakhale mphoto (yabwino) kwa iwo ndi kobwerera (kotamandika)?”

    [16] ““M’menemo adzapeza chilichonse chomwe adzafune. Adzakhala nthawi yaitali. Mtenderewu ndi lonjezo lochokera kwa Mbuye wako pa iwo lomwe adampempha kuti adzawakwaniritsire.”

    [17] “Ndipo (kumbuka) tsiku limene adzawasonkhanitse (awa osakhulupirira) ndi omwe adali kuwapembedza (monga Isa (Yesu), Uzairi ndi angelo) kusiya Allah; adzanena (Allah kuuza amene ankalambiridwawo): “Kodi ndinu mudasokeretsa anthu angawa, kapena ndi okha adasokera njira.”

    [18] “Adzanena: “E ulemelero ukhale kwa inu! Sizidali zoyenera kwa ife kudzikonzera atetezi mmalo mwa Inu, (nanji kuuza anthu kuti azitipembedza). Koma mudawasangalatsa iwo ndi makolo awo kufikira adaiwala malangizo (Anu). Ndipo adali anthu oonongeka.”

    [19] “(Allah adzati): “Ndithu yakutsutsani (milungu yanuyo) pa zimene mwanena (kuti iwo adakusokeretsani). Ndipo simutha kudzichotsera (chilango) ngakhale (kupeza) chithandizo.” Ndipo, ndithudi amene achite zoipa mwa inu, tidzamulawitsa chilango chachikulu

    [20] “Ndipo palibe pamene tidatuma atumiki patsogolo pako koma ndithu iwo, adali kudya chakudya; ankayendanso m’misika. Ndipo tawasankha ena mwa inu kuti akhale mayeso kwa ena (popereka masautso kwa olungama). kodi mupirira? Ndipo, Mbuye wako ali Wopenya (chilichonse)

    [21] “۞ Ndipo amene alibe chiyembekezo chakukumana Nafe akunena: “Bwanji angelo satumidwa kwa ife? Kapena timuone Mbuye wathu (kuti atitsimikizire kuti ndiwedi Mtumiki wake”? Ndipo Allah akunena): “Ndithu adzitukumula mmitima mwawo ndipo anyoza; kunyoza kwakukulu.”

    [22] “Tsiku lowaona angelo, sikudzakhala chisangalalo tsiku limenelo kwa ochimwa, (koma lidzakhala tsiku lochoka moyo wawo). Ndipo adzanena (tsiku limenelo): “Ha! Allah atitchinjirize kwambiri.” (Koma mawu awa, sadzathandiza chilichonse)

    [23] “Ndipo tidzaidzera ntchito iliyonse (yabwino) imene adachita, ndipo tizaichita monga fumbi louluka (ponseponse, yopanda phindu chifukwa cha kusakhulupirira Allah kwawo)

    [24] “Anthu a ku Munda wamtendere tsiku limenelo adzakhala ndi mokhala mwabwino, ndi pamalo pampumulo wabwino

    [25] “Ndipo akumbutse za tsikulo pomwe thambo lidzang’ambika ndikudzetsa mitambo (yomwe idzachititsa chimdima ponseponse). Ndipo angelo adzatsika ambirimbiri

    [26] “Tsiku limenelo ufumu wachoonadi ngwa (Allah) Wachifundo chambiri. Ndipo lidzakhala tsiku lovuta kwa osakhulupirira

    [27] “Ndipo tsiku (limenelo), wosalungama adzakukuta zala zake uku akunena: “Kalanga ine! Ndikadatsata njira ya Mtumiki.”

    [28] ““E tsoka langa! Ndikadapanda kumchita uje kukhala bwenzi wanga. (nkadapulumuka lero).”

    [29] ““Ndithu adandisokeretsa kufikira ndidasiya ulaliki (wa Allah) utandidzera. Zoonadi, satana amataya munthu (akaona kuti wamgwetsa m’chionongeko).”

    [30] “Ndipo Mtumiki (adasuma kwa Mbuye wake) adati: “E Mbuye wanga! Ndithu anthu anga aisandutsa Qur’aniyi kukhala chinthu chosiidwa, (sakuiwerenga. Ndiponso sakutsata ziphunzitso zake).”

    [31] “Momwemonso mneneri aliyense tidamkonzera mdani wochokera mwa (anthu) oipa. Ndipo Mbuye wako wakwana kukhala muongoli ndi mthandizi (wako)

    [32] “Ndipo amene sadakhulupirire akunena: “Bwanji Qur’an yonse siidavumbulutsidwe nthawi imodzi kwa iye? Momwemo (ukuoneramo, tikuitumiza pang’onopang’ono) kuti tiulimbikitse mtima wako ndi iyo, ndipo taiyala, mkayalidwe kabwino

    [33] “Ndipo sangakubweretsere fanizo lililonse koma tikubweretsera choonadi (choyankha fanizolo ndi kukudziwitsa) ndi kumasulira kwabwino

    [34] “Amene adzasonkhanitsidwe akukokedwa ndi nkhope zawo kunka ku Jahanama, iwowo adzakhala pamalo oipa ndipo ngosokera njira (yachoonadi)

    [35] “Ndipo ndithu Mûsa tidampatsa buku. Ndipo m’bale wake Harun (Aroni) tidamsankha kukhala nduna (yake)

    [36] “Choncho tidati: “Pitani kwa anthu omwe atsutsa zisonyezo Zathu. Tero, tidawaononga kotheratu.”

    [37] “Naonso anthu a Nuh, pamene adatsutsa atumiki, tidawamiza, ndipo tidawachita kukhala phunziro kwa anthu, ndipo anthu osalungama tawakonzera chilango chowawa

    [38] “Nawonso Âdi, Asamudu ndi eni chitsime ndi mibadwo yambiri pakati pa iwo

    [39] “Ndipo onse tidawaponyera mafanizo; ndiponso onse tidawaononga motheratu (pamene adakana kutsatira malamulo athu)

    [40] “Ndipo ndithu iwo (Aquraish, m’maulendo awo) adafika pa mudzi (Sodomu ndi Gomora) womwe mvula yoipa (ya sangalabwi) idawavumbwa. Kodi sadali kuuona? Koma sadali kuyembekezera zakuuka ku imfa

    [41] “Ndipo akakuona (iwe Mtumiki Muhammad {s.a.w}), amangokuchitira chipongwe: “Kodi uyu ndi yemwe Allah wamtuma kuti akhale mtumiki?”

    [42] ““Ndithu adatsala pang’ono kutisokeretsa ku milungu yathu, tikadapanda kupirira pa milunguyo.” Posachedwapa adziwa, pamene adzaona chilango, (kuti) ndani wosokera zedi njira

    [43] “Kodi wamuona yemwe wachichita chilakolako chake (chimene akuchikonda) kukhala mulungu wake? Kodi iweyo ungathe kukhala muyang’aniri wa iye (kotero kuti ungamkakamize chomwe safuna)

    [44] “Kapena ukuganiza kuti ambiri a iwo akumva kapena kuzindikira? Iwo sali kanthu kena koma ali ngati ziweto. Ndipo iwo asokera kwambiri njira

    [45] “Kodi sudaone momwe Mbuye wako wautambasulira mthunzi? Akadafuna, akadauchita kuti ukhale wokhazikika (wosasinthasintha). Ndipo talichita dzuwa kukhala chisonyezo chake

    [46] “Kenaka tikuufumbata kwa Ife m’kufumbata kwapang’onopang’ono (kufikira wonse wutachoka)

    [47] “Ndipo Iye ndi amene wakuchitirani usiku kukhala monga chovala, ndipo tulo monga mpumulo, ndipo usana wauchita kukhala monga nthawi youka (kuimfa)

    [48] “Iye ndi Yemwe amatumiza mphepo kukhala nkhani yabwino patsogolo pa chifundo chake (mvula), ndipo kuchokera kumitambo tikutsitsa madzi oyera

    [49] “Kuti ndi madziwo tiukitse dziko lakufa (lachilala), ndikumwetsa zina mwa zimene tidazilenga monga ziweto ndi anthu ochuluka

    [50] “Ndiponso ndithu tikuigawa (mvulayi) pakati pawo kuti akumbukire, ndipo anthu ambiri akukana (kuthokoza Allah) koma kupitiriza kusakhulupirira

    [51] “Ndipo tikadafuna, tikadatuma mchenjezi wawowawo m’mudzi uliwonse, (koma tatuma Muhammad {s.a.w} kuti akhale mchenjezi wa onse

    [52] “Choncho usawamvere osakhulupirira koma limbana nawo ndi iyo (Qur’an); kulimbana kwakukulu

    [53] “Ndipo Iye (Allah) ndi Yemwe wazikumanitsa nyanja ziwiri, iyi yamadzi okoma othetsa ludzu ndi iyi yamadzi amchere owawa. Ndipo waika malire ndi chitsekerezo chotsekereza pakati pa izo

    [54] “Ndipo Iye ndiye adalenga munthu ndi madzi ndiponso adamchitira chibale cha magazi ndi chibale cha ukwati. Ndipo Mbuye wako ali Wokhoza chilichonse

    [55] “Ndipo (ena mwa anthu) akupembedza zina zake kusiya Allah, zomwe sizingawathandize ndiponso sizingawadzetsere masautso (atasiya kuzipembedza). Ndipo wosakhulupirira ndi mthandizi wa zoipa poukira Mbuye wake

    [56] “Ndipo Ife sitidakutume koma kuti ukhale wouza nkhani zabwino (okhulupirira); ndi wochenjeza (osakhulupirira)

    [57] “Nena: “Sindikupemphani malipiro pa zimenezi (zomwe ndikukuphunzitsani) koma amene afuna ayende pa njira yopita kwa Mbuye wake, (popanda chopereka).”

    [58] “Ndipo tsamira kwa (Allah) Wamoyo, Wamuyaya Yemwe saafa. Ndipo mulemekeze pomtamanda ndi mbiri Zake. Ndipo Iye akukwana kudziwa bwinobwino machimo a akapolo Ake

    [59] “Yemwe adalenga thambo ndi nthaka ndi zimene zikupezeka mkati mwake. (Adazilenga) m’masiku asanu ndi limodzi, ndipo adakhazikika pa Arsh (Mpando Wake wachifumu, m’kukhazikika kodziwa Yekha). Iye Ngwachifundo chambiri; mufunseni wodziwa za Iye

    [60] “Ndipo akauzidwa (kuti): “Mulambireni (Allah) Wachifundo chambiri.” Amati: “Ndani Wachifundo chambiri? Kodi tilambire Yemwe iwe ukutilamula?” (Mawu amenewa) adawaonjezera iwo mwano

    [61] “Watukuka Mwini kupereka madalitso Yemwe adakhazikitsa nyenyezi ku thambo, ndipo m’menemo adaika nyali (dzuwa) ndi mwezi wounika

    [62] “Ndipo Iye ndi Yemwe adapanga usiku ndi usana kuti zizitsatana (ndikusinthana). (Izi zingapindulitse) kwa amene afuna kukumbukira kapena (amene) afuna kuthokoza

    [63] “Ndipo akapolo a (Allah) Wachifundo chambiri ndi omwe akuyenda pa dziko modzichepetsa, ndipo mbuli zikanena kwa iwo (mawu amwano), amaziyankha mawu abwino

    [64] “Ndi omwe amapititsa nthawi ina ya usiku uku akulambira ndi kuimilira chifukwa cha kulemekeza Mbuye wawo

    [65] “Ndi omwe akunena: “E Mbuye wathu tipewetsereni chilango cha Jahannam; ndithu chilango chake nchosasiyana nacho.”

    [66] ““Ndithu iyo ndi malo woipa; ndiponso pokhala poipa.”

    [67] “Ndi omwe amati akamagawira anthu ena chuma chawo, samwaza pachabe ndiponso sachita umbombo, koma amachita mwapakatikati

    [68] “Ndi omwe sapembedza milungu ina poiphatikiza ndi Allah, ndiponso saapha munthu yemwe Allah adaletsa kumupha kupatula pakakhala choonadi ndiponso saachita chigololo. Ndipo amene achite zimenezi, apeza masautso (pompano pa dziko lapansi)

    [69] “Chilango chidzawonjezeredwa kwa iye tsiku la Qiyâma, ndipo adzakhala m’chilango muyaya uku ali wonyozeka

    [70] “Kupatula amene walapa, naakhulupirira, ndikuchita ntchito yabwino. Tsono iwowo, Allah adzawasinthira zoipa zawo kukhala zabwino. Ndipo Allah ali Wokhululuka kwambiri, Wachisoni chosatha

    [71] “Ndipo amene akulapa ndikuchita zabwino, ndithu iye akulapa mwachoonadi kwa Allah

    [72] “Omwenso sachitira umboni za bodza, ndipo akadutsa pamalo pa zachibwana, amadutsa mwaulemu

    [73] “Ndiponso omwe amati akakumbutsidwa Ayah za Mbuye wawo, samazigwera mwa ugonthi ndi mwakhungu

    [74] “Ndi omwenso akunena: “E Mbuye wathu! Tipatseni mwa akazi athu ndi ana athu chotonthoza maso, ndipo tichiteni kukhala atsogoleri a oopa Allah.”

    [75] “Iwo adzalipidwa zipinda (za pamwamba ku Jannah) chifukwa cha mavuto omwe adawapirira. Ndipo akalandira m’menemo ulemu ndi mtendere

    [76] “Akakhala m’menemo nthawi yaitali; akongolerenji malo okhazikika ndi kukhalamo

    [77] “Nena: “Ndithu Mbuye wanga sakadalabadira chilichonse pa inu pakadapanda mapemphero anu, (akadakulangani pompano pa dziko lapansi.) Komabe inu mwatsutsa (uthenga wa aneneri). Choncho chilango chidzakugweranibe.”

    Ndemanga za ndakatulo

    Surah 26

    [1] “Tâ-Sîn-Mîm

    [2] “Izi ndi Ayah (ndime) za buku (la Qur’an) lofotokoza chilichonse (chofunika m’chipembedzo)

    [3] “Mwina iwe (Mtumiki Muhammad {s.a.w}) udziononga wekha (ndi madandaulo) chifukwa chakuti (iwo) sadakhale okhulupirira

    [4] “Tikadafuna, tikadawatsitsira chizizwa kuchokera kumwamba; kotero kuti makosi awo akadadzichepetsa ndi chizizwacho, (sakadatha kucheukira kwina koma sitifuna kukakamiza anthu kuti akhale Asilamu)

    [5] “Ndipo palibe pamene chikuwadzera chivumbulutso chatsopano chochokera kwa (Allah) Wachifundo chambiri koma amazipatula ku icho (chivumbulutso)

    [6] “Ndithu atsutsa; choncho posachedwapa ziwadzera nkhani zomwe adali kuzichitira chipongwe

    [7] “Kodi sadaone nthaka? Ndimmera ungati taumeretsa m’menemo kuchokera mu mtundu ulionse, wokongola

    [8] “Ndithu m’zimenezo muli zizindikiro (zosonyeza mphamvu za Allah). Koma ambiri a iwo sali okhulupirira

    [9] “Ndipo, ndithu Mbuye wako ndi Mwini mphamvu zoposa; Wachisoni chosatha

    [10] “Ndipo (akumbutse) pamene Mbuye wako adaitana (m’neneri) Mûsa; adamuuza: “Pita kwa anthu ochita zoipa.”

    [11] “Anthu a Farawo; (auze): “Kodi sawopa (Allah)?”

    [12] “(Mûsa) adati: “Mbuye wanga! Ine ndikuopa kuti anganditsutse

    [13] “Ndipo chingabanike chifuwa changa (ndi maganizo, chifukwa chakunditsutsa kwawo); ndiponso lirime langa siliyankhula momveka bwino. Choncho tumizaninso uthengawu kwa Harun (kuti tikhale awiri ndipo azikandithangata pantchito yangayi)

    [14] “Ndipo iwowo ndili nawo mlandu ndipo ndikuopa kuti angandiphe (pobwezera chimene ndidawalakwira powaphera munthu wawo)

    [15] “(Allah) adati: “Iyayi! Pitani pamodzi ndi zozizwa Zathu; ndithu Ife tikakhala nanu limodzi (pokuthangatani) uku tikumvetsera (zimene azikanena).”

    [16] ““Choncho mpitireni Farawo, ndipo kamuuzeni kuti: “Ife ndi atumiki a Mbuye wa zolengedwa zonse.”

    [17] ““(Tatumidwa) kuti uwapereke kwa ife ana a Israyeli (kuti tinke nawo ku Sham).”

    [18] “(Farawo) adati (kwa Mûsa): “Kodi sitidakulere kwathu uli mwana, ndi kukhala nafe pa moyo wako zaka zambiri?”

    [19] ““Ndipo udachita chochita chako chimene udachichita, ndipo iwe ndiwe mmodzi wa osathokoza!”

    [20] “(Mûsa) adati: “Ndidachita zimenezo pomwe ine ndidali mmodzi wa osazindikira zinthu.”

    [21] ““Choncho ndidakuthawani pomwe ndidakuopani; tsono Mbuye wanga wandipatsa nzeru zoweruzira (zinthu), ndi kundisankha kukhala mmodzi wa atumiki.”

    [22] ““Ndipo kodi umenewu ndimtendere wonditonzera pomwe mudawaika muukapolo ana a Israyeli!”

    [23] “Farawo adati: “Kodi ndani Mbuye wa zolengedwayo?”

    [24] “(Mûsa) adati: “Mbuye wa thambo ndi nthaka ndi zapakati pake, ngati muli ndi chitsimikizo. (Amachita chilichonse m’menemo mmene wafunira; kupereka moyo ndi imfa).”

    [25] “(Farawo) adauza omwe adali m’mphepete mwake (mwachipongwe): “Kodi simukumva (mawu achibwanawa)?”

    [26] “(Mûsa adapitiriza kunena) adati: “Allah ndi Mbuye wanu komanso Mbuye wamakolo anu oyamba.”

    [27] “(Farawo) adati (kwa anthu ake pofuna kuwakwiitsa): “Ndithu Mtumiki wanu amene watumidwa kwa inu, ngwamisala.”

    [28] “(Mûsa) adati: “Mbuye wakuvuma ndi kuzambwe, ndi zomwe ziri pakati pake ngati mumazindikira (zinthu, muzindikira izi).”

    [29] “(Farawo) adati: “Ngati udzipangira mulungu wina kusiya ine, ndikuchita kukhala mmodzi wa omangidwa kundende.”

    [30] “(Mûsa) adati: “Kodi ngakhale nditakubweretsera chinthu choonekera poyera (chosonyeza kuti zimene ndikunenazi ndizoona ndatumidwa ndi Allah)?”

    [31] “(Farawo) adati: “Chibweretse, ngati uli mwa onena zoona.”

    [32] “Ndipo (Mûsa) adaponya (pansi) ndodo yake, mwadzidzidzi idasanduka njoka yopenyeka

    [33] “Ndipo adatulutsa dzanja lake; pompo lidali loyera (kwambiri) kwa (onse) openya

    [34] “(Farawo) adauza akuluakulu omwe adali m’mphepete mwake: “Ndithu uyu ndi wamatsenga wodziwa kwambiri.”

    [35] ““Akufuna kukutulutsani m’dziko lanu ndi matsenga ake; kodi nanga mukuti chiyani?”

    [36] “(Anthu) adati (kwa Farawo): “Mpatse nthawi ndi m’bale wakeyo, ndipo tumiza (amithenga) m’mizinda yonse osonkhanitsa anthu.”

    [37] ““Ndipo akubweretsera amatsenga onse odziwa kwabasi (kotero kuti adzampambana Mûsa).”

    [38] “Choncho amatsenga adasonkhanitsidwa mu nthawi ya tsiku lodziwika

    [39] “Ndipo anthu adauzidwa: “Kodi inu musonkhana? (Choncho, sonkhanani).”

    [40] ““Mwina tingawatsatire amatsenga ngati iwo ndiamene apambane.”

    [41] “Ndipo pamene amatsenga adadza, adati kwa Farawo: “Kodi tidzakhala ndi mphoto ngati ife ndife tipambane?”

    [42] “(Farawo) adati: “Inde, (ndipo kuonjezera apo) ndithu inu mudzakhala mwa amene amakhala pafupi (ndi ine, monga nduna zanga).”

    [43] “Mûsa adati kwa iwo: “Ponyani zimene mufuna kuponya (zosonyeza kuya kwa matsenga anu).”

    [44] “Choncho adaponya zingwe zawo ndi ndodo zawo, ndipo adati: “Kupyolera mu mphamvu za Farawo, ndithu ife ndife opambana.”

    [45] “Kenako Mûsa adaponya ndodo yake; mwadzidzidzi iyo idameza zabodza zomwe iwo adakonza

    [46] “Pamenepo amatsenga adadzigwetsa pansi molambira

    [47] “Adati: “Tamkhulupirira Mbuye wa zolengedwa.”

    [48] ““Mbuye wa Mûsa ndi Harun.”

    [49] “(Farawo) adati: “Ha! Mwamkhulupirira chotani ndisanakulolezeni? Ndithu iyeyu ndimkulu wanu amene adakuphunzitsani matsenga. Choncho posachedwa mudziwa (chimene ndikuchiteni) ndithu ndidula manja anu ndi miyendo yanu mosinthanitsa (podula mkono wakumanja ndi mwendo wakumanzere; kapena kudula mkono wakumanzere ndi mwendo wakumanja), ndipo kenako ndikupachikani nonsenu.”

    [50] “(Amatsenga) adati: “Palibe vuto, ndithu ife (tonse) tibwerera kwa Mbuye wathu.”

    [51] ““Ndithu ife tikuyembekezera kuti Mbuye wathu atikhululukire zolakwa zathu; pokhala oyamba mwa okhulupirira.”

    [52] “Ndipo tidamvumbulutsira Mûsa (kuti): “Pita ndi anthu anga m’nthawi yausiku (musamuke m’dziko la Iguputo); ndithu inu mutsatidwa.”

    [53] “Choncho Farawo adatuma (owatuma) kuti asonkhanitse anthu m’mizinda (kuti aletse ana a Israyeli kutuluka)

    [54] “(Adawauza otumidwa aja kuti auze anthu kuti): “Ndithu awa (ana a Israyeli) ndikagulu kochepa

    [55] “Ndipo ndithu iwo akutikwiitsa

    [56] “Koma ndithu ife tonse (ndife ochuluka komabe ngakhale zili choncho) tikuwaopa.”

    [57] “Choncho tidawatulutsa m’minda ndi mwa akasupe

    [58] “Ndi m’nkhokwe za chuma ndi m’malo okongola

    [59] “Momwemo ndi mmene tidawachitira ndipo tidawalowetsera chokolo zinthu zawo zonse kwa ana a Israyeli

    [60] “Choncho (anthu a Farawo ndi iye mwini) adawatsatira (ana a Israyeli) dzuwa litatuluka

    [61] “Ndipo pamene magulu awiri adaonana (anthu a Farawo ndi anthu a Mûsa), anthu a Mûsa adati: “Ndithu ife tigwidwa.”

    [62] “(Mûsa) adati: “Iyayi! Ndithu Mbuye wanga ali nane pamodzi. Andiongolera (kuti ife tonse tipulumuke).”

    [63] “Ndipo tidam’vumbulutsira mawu Mûsa (akuti): “Menya nyanja ndi ndodo yako.” Ndipo idagawikana, mbali iliyonse idali ngati phiri lalikulu

    [64] “Ndipo tidawayandikitsa pamenepo anthu enawo, (Farawo ndi anthu ake nalowa pa njira yomweyo pambuyo pa Mûsa ndi anthu ake)

    [65] “Ndipo tidapulumutsa Mûsa ndi onse amene adali nawo (mpaka adaoloka nyanjayo, madzi ali chiimire mbali iyi ndi iyi)

    [66] “Kenako tidawamiza enawo, (Farawo ndi anthu ake)

    [67] “Ndithu pa zimenezi pali lingaliro. Koma ambiri a iwo sali okhulupirira

    [68] “Ndipo, ndithu Mbuye wako ndi Mwini mphamvu zoposa (amalanga ndi chilango choopsa omwe amunyoza); Wachisoni (kwa omkhulupirira ndi kumumvera)

    [69] “Ndipo awerengere (osakhulupirira) nkhani ya (M’neneri) Ibrahim

    [70] “Pamene adafunsa bambo wake ndi anthu ake (kuti); “Kodi mukupembedza chiyani?”

    [71] “Adati: “Tikupembedza mafano; ndipo tipitiriza kuwapembedza.”

    [72] “(Ibrahim) adati: “Kodi amakumvani mukawaitana?”

    [73] ““Kapena amakuthandizani (mukawapembedza) kapena amapereka masautso kwa inu (mukasiya kuwapembedza)?”

    [74] “(Iwo) adati: “Koma tidapeza makolo athu akuchita zimenezi.”

    [75] “(Ibrahim) adati: “Kodi mukuwaona awa amene mwakhala mukuwapembedza,”

    [76] ““Inu ndi makolo anu amene adatsogola?”

    [77] ““Ndithu iwo ndiadani anga, kupatula Mbuye wa zolengedwa zonse;”

    [78] ““Yemwe adandilenga, ndiponso Yemwe akundiongolera (kunjira yolungama);”

    [79] ““Ndiyemwe akundidyetsa ndi kundimwetsa.”

    [80] ““Ndipo ndikadwala ndiyemwe amandichiritsa.”

    [81] ““Ndi Amene adzandipatsa imfa, ndipo (tsiku la Qiyâma) adzandidzutsa;”

    [82] ““Ndi Yemwe ndikuyembekezera kuti adzandikhululukira zolakwa zanga tsiku la malipiro.”

    [83] ““E Mbuye wanga! Ndipatseni nzeru zoweruzira (zinthu), ndikundilumikiza ndi anthu abwino;”

    [84] ““Ndipatseni kutchulidwa kwabwino kwa anthu ena odza pambuyo;”

    [85] ““Ndichiteni kukhala mmodzi mwa olandira Munda wamtendere;”

    [86] ““Ndipo khululukirani bambo wanga; ndithu iye adali mmodzi wa osokera;”

    [87] ““Ndipo musadzandiyalutse pa tsiku loukitsidwa anthu (ku imfa);”

    [88] ““Tsiku lomwe chuma ndi ana sizidzathandiza (aliyense).”

    [89] ““Kupatula yemwe adzadza kwa Allah ndi mtima woyera (iye ndiamene adzathandizidwa patsikulo).”

    [90] “Ndipo Munda wamtendere udzayandikitsidwa kwa oopa (Allah)

    [91] “Ndipo Jahannam idzaonetsedwa kwa opotoka

    [92] “Ndipo kudzanenedwa kwa iwo: “Ali kuti amene mudali kuwapembedza aja

    [93] “M’malo mwa Allah? Kodi angathe kukuthandizani kapena kudzithandiza okha?”

    [94] “Ndipo iwo ndi opotoka ena adzaponyedwa ndi nkhope zawo m’menemo (mu Jahannam)

    [95] “Ndi magulu onse ankhondo a Iblis (omwe adali kukometsa kwa anthu zoipa ndi machimo)

    [96] “Adzanena (movomereza kulakwa kwawo) uku naonso ali m’menemo, akukangana (ndi anzawo omwe adawasokeretsa)

    [97] ““Ndikulumbira Allah, ndithu tidali m’kusokera kowonekera

    [98] “Pamene timakufananitsani ndi Mbuye wa zolengedwa

    [99] “Ndipo sadatisokeretse, koma oipa okha basi

    [100] “Choncho ife tilibe aomboli (otiombola)

    [101] “Ngakhalenso bwenzi wapamtima (woti angatipulumutse kumasautsowa)

    [102] “Tikadapeza mwayi wobwerera (ku moyo wa padziko), tikadakhala mwa okhulupirira.”

    [103] “Ndithu m’zimenezi, muli malingaliro akulu, koma ambiri a iwo sali okhulupirira

    [104] “Ndipo ndithu Mbuye wako, ndiye Mwini mphamvu zoposa; Wachisoni chosatha

    [105] “Anthu a Nuh adatsutsa atumiki

    [106] “Pamene adawauza Nuh m’bale wawo kuti: “Kodi simukuopa (Allah ngakhale nditakuuzani zoopsa zimene zikukudikirani)?”

    [107] ““Ndithu ine kwa inu ndine Mtumiki wokhulupirika;”

    [108] ““Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”

    [109] ““Ndipo sindikupemphani malipiro pa zimenezi; malipiro anga ali kwa (Allah) Mbuye wa zolengedwa.”

    [110] ““Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”

    [111] “(Iwo) adati: “Nchotani kuti tikukhulupirire iwe chikhalirecho anthu wamba ndi amene akukutsatira?”

    [112] “(Nuh) adati: “Sindikudziwa zimene adali kuchita (zomwe zachititsa kuti Allah awaongolere kunjira yoongoka).”

    [113] ““Chiwerengero chawo sichili kwina koma kwa Mbuye wanga, mukadakhala mukuzindikira.”

    [114] ““Ndipo sindine wopirikitsa okhulupirira (ku chipembedzo cha Allah kuti inu olemekezeka muchikhulupirire).”

    [115] ““Ine sikanthu , koma ndine mchenjezi woonekera.”

    [116] “(Iwo) adati: “Ngati susiya, iwe Nuh, (zonena zakozi) ndithu ukhala mmodzi mwa ogendedwa (miyala mpaka ufe).”

    [117] “(Nuh) adati (kwa Allah): “Mbuye wanga! Ndithu anthu anga anditsutsa.”

    [118] “Choncho weruzani pakati panga ndi pakati pa iwo (chiweruzo chabwino), ndipo ndipulumutseni pamodzi ndi amene alinane mwa okhulupirira.”

    [119] “Choncho, tidampulumutsa pamodzi ndi omwe adali naye m’chombo chodzadza (ndi chilichonse chamoyo chomwe chidalipo m’dziko, chachimuna ndi chachikazi chidaikidwa m’menemo)

    [120] “Pambuyo pake tidawamiza otsalawo

    [121] “Ndithu m’zimenezi muli malingaliro; koma ambiri a iwo sadali okhulupirira

    [122] “Ndipo ndithu Mbuye wako, Iye Ngwamphamvu zoposa; Ngwachisoni chosatha

    [123] “Naonso Âdi adatsutsa atumiki

    [124] “Pamene m’bale wawo (Mneneri) Hûd adawafunsa kuti: “Kodi simuopa (Allah)?”

    [125] ““Ndithu ine ndine Mtumiki wokhulupirika kwa inu;”

    [126] ““Choncho, muopeni Allah ndipo mverani ine.”

    [127] ““Ndipo pazimenezi sindikukupemphani malipiro; ndithu malipiro anga ali kwa (Allah) Mbuye wa zolengedwa.”

    [128] ““Kodi mukudzimangira nyumba pamalo paliponse pachitunda pokongola, moseweretsa?”

    [129] ““Ndipo mukudzimangira (nyumba zonga) linga ngati kuti mukuona kuti mudzakhala muyaya?”

    [130] ““Ndipo mukamamenya nkhondo mumamenya modzitukumula.”

    [131] ““Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”

    [132] ““Ndipo muopeni Yemwe adakupatsani zimene mukuzidziwa.”

    [133] ““Adakupatsani ziweto ndi ana.”

    [134] ““Ndi minda ndi akasupe.”

    [135] ““Ndithu ine ndikukuoperani chilango cha tsiku lalikulu.”

    [136] “Iwo adati: “Kwa ife nchimodzimodzi, utichenjeze kapena iwe usakhale mmodzi mwa ochenjeza.”

    [137] ““Ndithu kutero (anthu ena kudzitcha atumiki a Allah), sikanthu koma ndi machitidwe a anthu akale.”

    [138] ““Ndipo ife sitidzalangidwa (monga momwe ukunenera).”

    [139] “Choncho adamtsutsa, ndipo tidawaononga. Ndithu m’zimenezi muli malingaliro; koma ambiri a iwo sadali okhulupirira

    [140] “Ndipo ndithu Mbuye wako ndiye Wamphamvu zoposa; Wachisoni chosatha

    [141] “A Samudu (naonso) adatsutsa atumiki

    [142] “Pamene m’bale wawo Swalih adawauza kuti: “Kodi simuopa (Allah)?”

    [143] ““Ndithu ine ndimtumiki wokhulupirika kwa inu.”

    [144] ““Choncho muopeni Allah ndipo mverani ine.”

    [145] ““Ndipo sindikupemphani malipiro pa zimenezi. Palibe kumene kuli malipiro anga koma kwa Mbuye wa zolengedwa.”

    [146] ““Kodi (mukuganizira kuti) mudzasiidwa mwamtendere pa izi zili pano (popanda imfa kukudzerani?)”

    [147] ““M’minda ndi mu akasupe?”

    [148] ““Ndi (m’minda) yammera ndi mitengo yakanjedza yamikoko yakupsa yofewa?”

    [149] ““Ndipo mukugoba nyumba m’mapiri mwaluso.”

    [150] ““Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”

    [151] ““Ndipo musamvere za awo opyola malire.”

    [152] ““Amene akuononga pa dziko, ndipo sakonza.”

    [153] “Iwo adati: “Ndithu iwe ndi mmodzi wa olodzedwa.”

    [154] ““Iwe suli kanthu, koma munthu ngati ife; tabwera ndi chozizwitsa, ngati ndiwedi mmodzi wa onena zoona!”

    [155] “Iye adati: “(Ndakubweretserani) ngamira iyi yaikazi; (koma) ili ndi gawo lake lakumwa, ndipo inu muli ndi gawo lanu lakutunga (madzi) patsiku lodziwika. (Tsiku lina lotunga rnadzi anthu).”

    [156] ““Ndipo musaikhudze ndi choipa chilichonse kuopera kuti chingakupezeni chilango cha tsiku lalikulu.”

    [157] “Koma iwo adaipha; ndipo adali odzinena (pamene chidadza chilango cha Allah)

    [158] “Choncho chilango (cha Allah) chidawaononga, ndithu pa zimenezi pali phunziro; koma ambiri a iwo sadali okhulupirira

    [159] “Ndipo, ndithu Mbuye wako, Iye Ngwamphamvu zoposa; wachisoni chosatha

    [160] “Anthu a Luti adatsutsa atumiki

    [161] “Pamene m’bale wawo Luti adanena kwa iwo (kuti): “Kodi simuopa (Allah)?”

    [162] ““Ndithu ine ndine Mtumiki wokhulupirika kwa inu.”

    [163] ““Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”

    [164] ““Ndipo sindikupemphani malipiro pa zimenezi; palibe komwe kuli malipiro anga koma kwa Mbuye wazolengedwa.”

    [165] ““Kodi mukugonana ndi amuna (anzanu) muzolengedwa (za Allah)

    [166] ““Ndikusiya amene Mbuye wanu adakulengerani kuti akhale akazi anu? Ndithu inu ndinu anthu olumpha malire.”

    [167] “Iwo adati: “Ngati susiya (izi), E iwe Luti! ndithu ukhala mmodzi wa opirikitsidwa.”

    [168] “Iye adati: “Ndithu ine ndine m’modzi wakuzida izi zochita zanu (choncho Sindisiya kuzidzudzula).”

    [169] ““E Mbuye wanga! Ndipulumutseni ine ndi banja langa ku (matsoka a) zimene akuchita.”

    [170] “Ndipo tidampulumutsa iye ndi onse a pa banja lake

    [171] “Kupatula nkhalamba yaikazi idali mwa otsalira m’mbuyo

    [172] “Titatero tidawaononga enawo

    [173] “Ndipo tidawavumbwitsira mvula (yamiyala); iyipirenji, mvula ya ochenjezedwa

    [174] “Ndithu pazimenezi pali malingaliro. Koma ambiri a iwo sadali okhulupirira

    [175] “Ndipo, ndithu Mbuye wako, Ngwamphamvu kwambiri; Ngwachisoni chosatha

    [176] “Anthu a m’dziko lamitengo yambiri (Madiana) adatsutsa atumiki

    [177] “(Akumbutse) pamene (Mneneri) Shuaib adati kwa iwo: “Kodi simuopa (Allah)?”

    [178] ““Ndithu ndine Mtumiki wokhulupirika kwa inu.”

    [179] ““Choncho muopeni Allah ndipo ndimvereni.”

    [180] ““Ndipo sindikupemphani malipiro pa zimenezi; kulibe malipiro anga koma kwa (Allah) Mbuye wa zolengedwa.”

    [181] ““Kwaniritsani mulingo (pamalonda pamene mukupima), ndipo musakhale mwaopungula (mulingo).”

    [182] ““Ndipo yesani ndi sikelo yolungama (yolondola).”

    [183] ““Ndipo musawachepetsere anthu zinthu zawo, ndiponso musayende padziko uku mukuononga.”

    [184] ““Ndipo muopeni amene adalenga inu ndiponso zolengedwa zoyamba (zimene zidanka kale).”

    [185] “Iwo adati: “Ndithu iwe ndi mmodzi wa olodzedwa.”

    [186] ““Ndipo iwe suli kanthu koma munthu ngati ife, ndipo ndithu tikukutsimikizira kuti ndiwe mmodzi wa abodza.”

    [187] ““Choncho tigwetsere zidutswa za thambo (kuti zitiononge) ngati uli mmodzi wa onena zoona.”

    [188] “(Shuaib) adati: “Mbuye wanga Ngodziwa kwambiri zimene mukuchita. (Akadzaona kuti inu ngoyenera kulangidwa ndizidutswa za thambo, adzakulangani).”

    [189] “Koma adamutsutsa. Ndipo chidawagwera chilango chatsiku la mthunzi; ndithu chimenecho chidali chilango cha tsiku lalikulu

    [190] “Ndithu pa zimenezi pali lingaliro; koma ambiri a iwo sadali okhulupirira

    [191] “Ndipo, ndithu Mbuye wako Ngwamphamvu kwambiri; Ngwachisoni chosatha

    [192] “Ndipo, ndithu iyi (Qur’an) ndiyo chivumbulutso cha Mbuye wazolengedwa zonse

    [193] “Mzimu Wokhulupirika (Jiburil) udaivumbulutsa

    [194] “Pa mtima wako kuti ukhale mmodzi wa achenjezi

    [195] “M’chiyankhulo cha Chiarabu chomveka bwino

    [196] “Ndipo ndithu izi (zomwe zili m’Qur’an) zilipo m’mabuku akale

    [197] “Kodi sipadapezeke chisonyezo kwa iwo kuti akuidziwa (Qur’an) odziwa mwa ana a Israyeli (kotero kuti ena alowa m’Chisilamu)

    [198] “Ndipo tikadaivumbulutsa kwa wina amene sali Muarabu

    [199] “Kotero kuti nkuwawerengera momveka bwino, sakadaikhulupirira

    [200] “Momwemo ndimo tidalowetsera kuitsutsa (Qur’an) m’mitima ya oipa

    [201] “Sangaikhulupirire kufikira ataona chilango chowawa

    [202] “Choncho chidzawadzera mwadzidzidzi pomwe iwo sakuzindikira

    [203] “Tero adzayamba kunena: “Kodi ife tipatsidwa nthawi (yoti tilape)?”

    [204] “Kodi akuchifulumizitsa chilango Chathu

    [205] “Kodi ukuona bwanji, ngati titawasangalatsa zaka (zankhaninkhani)

    [206] “Kenako nkuwadzera (chilango) chomwe adalonjezedwa

    [207] “Sizidawathandize zomwe adali kusangalatsidwa nazozo

    [208] “Ndipo sitidauononge mudzi uliwonse koma udali ndi achenjezi

    [209] “(Kuti akhale) chikumbutso. Ndipo sitidali osalungama (powaononga popanda kuwachenjeza)

    [210] “Ndipo asatana sadaivumbulutse (iyi Qur’an monga osakhulupirira akunenera monyoza)

    [211] “Ndipo sikoyenera kwa iwo (kuivumbulutsa Qur’an) ndiponso sangathe

    [212] “Ndithu iwo ngotsekerezedwa kumvetsera (zimene angelo amalankhula kumwamba)

    [213] “Choncho usapembedze mulungu wina pamodzi ndi Allah, kuti ungakhale mwa olangidwa

    [214] “Ndipo achenjeze abale ako a pafupi

    [215] “Ndipo fungatira ndi phiko lako amene akutsata mwa okhulupirira. (Ukhale wachifundo kwa iwo)

    [216] “Ngati atakunyoza, nena: “Ine ndili kutali ndi zimene mukuchitazo.”

    [217] “Ndipo tsamira kwa (Mbuye wako) Mwini mphamvu zoposa; Wachisoni chosatha

    [218] “Yemwe akukuona pamene ukuimilira (pamapemphero)

    [219] “Ndikutembenukatembenuka kwako (pogwetsa mphumi yako pansi ndi kudzuka ndi kuimilira) pamodzi ndi ogwetsa mphumi pansi (polambira Allah)

    [220] “Ndithu Iye Ngwakumva; Ngodziwa chilichonse

    [221] “Kodi ndikuuzeni amene asatana amawatsikira

    [222] “Amamtsikira yense wabodza lamkunkhuniza; wamachimo

    [223] “Amawaponyera (asatana anzawo a mu anthu) zimene azimva. Koma ambiri a iwo ngabodza

    [224] “Ndipo alakatuli (olakatula zopanda phindu) amatsatidwa ndi (anthu) opotoka

    [225] “Kodi suona kuti iwo akungoyumbayumba m’chigwa chilichonse (chamawu)

    [226] “Ndithunso iwo akunena zomwe sachita

    [227] “Kupatula amene akhulupirira ndikumachita zabwino, ndikumamtchula Allah mowirikiza, ndikuzipulumutsa okha pambuyo pochitiridwa zoipa. Ndipo posachedwa amene adzichitira okha zoipa adziwa kotembenukira komwe adzatembenukire

    Chinziri

    Surah 27

    [1] “Tâ-Sîn. Izi ndi Ayah (ndime) (za Qur’an buku lodzazidwa ndi zothandiza), ndiponso buku lofotokoza (chilichonse chauzimu ndi chamoyo wadziko)

    [2] “(Qur’an) nchiongoko ndi nkhani yabwino kwa okhulupirira

    [3] “Amene akupemphera Swala (zisanu, modzichepetsa ndi mokwaniritsa malamulo ake) ndi kumapereka Zakaat (m’nthawi yake), ndipo iwo ali ndi chitsimikizo champhamvu cha (moyo wa) tsiku la chimaliziro

    [4] “Ndithu amene sakhulupirira za (moyo wa) tsiku la chimaliziro, tawakometsera zochita zoipa kukhala ngati zabwino; choncho iwo akungoyumbayumba (m’kusokera kwawo)

    [5] “Iwowo ndiamene adzapeza chilango choipa; iwo tsiku lachimaliziro ngotayika zedi, (adzaonongeka ku Moto motheratu)

    [6] “Ndipo ndithu iwe ukuphunzitsidwa Qur’an kuchokera kwa mwini nzeru zakuya, Wodziwa kwambiri

    [7] “(Kumbuka) Mûsa pamene adauza banja lake (mkazi wake): “Ndithu ine ndaona moto; posachedwapa ndikubweretserani nkhani za kumeneko, kapena ndikubweretserani chikuni cha moto kuti inu muothe

    [8] “Choncho pamene adaudzera (motowo) kudaitanidwa: “Wadalitsidwa yemwe ali m’moto ndi yemwe ali m’mphepete mwake; ndipo walemekezeka Allah Mbuye wa zolengedwa

    [9] “E iwe Mûsa! Ndithu ine ndine Allah, Wamphamvu zoposa; Wanzeru zakuya

    [10] “Ndipo ponya (pansi) ndodo yako! (Pamene adaiponya idasanduka njoka), tero pamene adaiwona ikugwedezeka (ndodo ija) ngati njoka, adatembenuka kuthawa, ndipo sadacheuke (kapena kudikira kuti amve mawu omvekawo): “E iwe Mûsa! Usaope. Ndithu Ine, saopa kwa Ine atumiki.”

    [11] ““Koma amene wadzichitira yekha zoipa, kenako nkusintha (pochita) zabwino pambuyo pa zoipa, (ndimkhululukira) pakuti Ine ndine Wokhululuka kwabasi, Wachifundo chambiri.”

    [12] ““Ndipo lowetsa dzanja lako palisani la mkanjo wako, ndipo lituluka lili loyera, (kuyera) kopanda matenda. (Ziwirizi) zili m’gulu la zododometsa zisanu ndi zinayi. Pita nazo kwa Farawo ndi anthu ake; ndithu iwo ndianthu otuluka m’chilamulo cha Allah.”

    [13] “Tero pamene zidawadzera zizindikiro Zathu zosonyeza (kuti iye ndimtumiki wa Allah) adati: “Awa ndimatsenga woonekera.”

    [14] “Ndipo adazitsutsa (zisonyezozo) mwachinyengo ndi modzikuza chikhalirecho mitima yawo idatsimikiza (kuti ndizoona zochokera kwa Allah); choncho, yang’ana adali bwanji malekezero a oononga

    [15] “Ndipo ndithu Daud ndi Sulaiman tidawapatsa nzeru (zazikulu; adayamika Allah) adati: “Kuyamikidwa konse kwabwino nkwa Allah Yemwe watichitira ubwino kuposa ambiri mwa akapolo ake okhulupirira.”

    [16] “Ndipo Sulaiman adalowa mmalo mwa Daud pa nzeru ndi uneneri ndipo (Sulaiman) adati: “E inu anthu! Ndithu taphunzitsidwa (mpaka tikudziwa) chiyankhulo cha mbalame, ndiponso tapatsidwa chilichonse; ndithu umenewu ndiubwino wopenyeka

    [17] “Ndipo adasonkhanitsidwa kwa Sulaiman ankhondo ake ochokera m’ziwanda, anthu ndi mbalame, ndipo adawandandika m’magulumagulu

    [18] “Kufikira pamene adadza pachigwa chanyelere, nyelere idanena (kuuza zinzake): “E inu nyelere, lowani m’nyumba zanu poopa kuti angakupondeni Sulaiman ndi magulu ake ankhondo pomwe iwo sakudziwa (za inu).”

    [19] “Choncho adamwetulira, mosekelera chifukwa cha mawu ake aja (mawu a nyelere); ndipo (Sulaiman) adati: “E Mbuye wanga! Ndipatseni nyonga zakuti ndizithokozera mtendere wanu umene mwandidalitsa nawo pamodzi ndi makolo anga, ndi kuti ndizichita zabwino (zomwe) mukuziyanja; Kupyolera m’chifundo chanu, ndiponso ndilowetseni m’gulu la akapolo anu abwino.”

    [20] “Ndipo adayamba kuyendera mbalame, adati: “Kodi bwanji sindikumuona Huduhudu? Kapena ali m’gulu la amene pano palibe?”

    [21] ““Ndithu ndimulanga chilango chokhwima, kapena ndimzinga (ndimdula khosi) pokhapokha andibweletsere umboni womveka (wosonyeza kuti adachoka pazifukwa zomveka).”

    [22] “Choncho (Hudhud) sadakhalitse nthawi yaitali; ndipo adati (kwa Sulaiman): “Ndatulukira zomwe iwe sudazitulukire, ndipo ndakubweletsera nkhani yotsimikizika kuchokera ku Saba.”

    [23] ““Ndithu ine ndapeza mkazi akuwalamulira (anthu a ku dziko la Saba), ndipo wapatsidwa chilichonse; ndiponso ali ndi chimpando chachifumu chachikulu.”

    [24] ““Ndampeza iye ndi anthu ake akulambira dzuwa kusiya Allah; ndipo satana wawakometsera zochita zawo zoipa; choncho wawatsekereza ku njira yolungama, tero sadaongoke.”

    [25] ““Kuti asamlambire Allah yemwe amatulutsa zobisika kumwamba ndi pansi; ndipo akudziwa zimene mukubisa ndi zimene muonetsa poyera.”

    [26] ““Allah! Palibe wina wopembedzedwa mwachoona koma Iye basi; Mbuye wa Arsh (Mpando wachifumu) waukulu.”

    [27] “(Sulaiman) adati “Tiona ngati wanena zoona kapena ngati) uli m’gulu la onama.”

    [28] ““Pita ndi kalata yangayi, kaiponye kwa iwo; kenako ukadzipatule kwa iwo (ukakhale pambali) ndi kuona momwe azikayankhira.”

    [29] “(Mfumukazi) idati; “E inu nduna! Ndithu kalata yolemekezeka yaponyedwa kwa ine.”

    [30] ““Yachokera kwa Sulaiman, ndipo mawu ake ndi awa: ‘Mdzina la Allah, Wachifundo chambiri, Wachisoni.’

    [31] “‘Musadzikweze kwa ine, ndipo idzani kwa ine muli ogonjera malamulo anga.”

    [32] “(Mfumukazi idaonjezera) kunena: “E inu nduna! ndilangizeni pankhani yangayi; sindilamula kanthu mpaka inu mutandibwerera.”

    [33] “(Nduna) zidati: “Ife ndife eni nyonga ndi eni kumenya nkhondo mwaukali; koma zonse zili ndi inu; choncho yang’anani mmene mungalamulire.”

    [34] “(Mfumukazi) idati: “Ndithu mafumu akamalowa m’mudzi (wa anthu), amauononga motheratu, ndi kuwachita olemekezeka a m’menemo kukhala onyozeka. Mmenemo ndimomwe amachitira (nthawi zonse).”

    [35] ““Koma ine nditumiza mitulo kwa iwo ndi kuyembekezera zimene abwere nazo otumidwawo.”

    [36] “Choncho pamene adafika (wamthenga wamkulu) kwa Sulaiman (ndi kupereka mphatso zija, Sulaiman adazikana) nati: “Mukundithandiza ndi chuma? zimene Allah wandipatsa ndizabwino kuposa zimene wakupatsani. Koma inu mukusangalala ndi mphatso zanu.”

    [37] “Bwerera (nazo) kwa iwo; ndithu tiwadzera ndi gulu lankhondo lomwe iwo sangathe kulimbana nalo; mtheradi, tikawatulutsa m’menemo ali onyozeka ndi oyaluka.”

    [38] “(Sulaiman adasonkhanitsa nduna zake) nati: “E inu nduna! Ndani abwere ndi mpando wake wachifumuwo kwa ine asadandidzere ali ogonja?”

    [39] “Chiwanda chotchedwa Ifrit chidati: “Ine ndikubweletsera chimenecho usadaimilire pamalo ako (oweruzira). Ndipo ndithu ine pa icho (chimpando) ndine wanyonga, wokhulupirika.”

    [40] “Yemwe adali ndi maphunziro (akuya) a m’buku adati: “Ine ndikubweletsera (chimpandocho) maso ako asadaphetire (usadatsinzine ndi kupenya).” Pamene adachiona chitakhazikitsidwa patsogolo pake, adati: “Izi nchifukwa cha ufulu wa Mbuye wanga kuti andiyese mayeso kodi ndithokoza kapena ndiusuliza (ufulu Wake). Ndipo amene akuthokoza ndithu ubwino wa kuthokozako udzakhala pa iye mwini. Ndipo amene akukana (mtendere wa Allah posathokoza), ndithu Mbuye wanga Ngokhupuka; Waulemu, (sasaukira chilichonse kwa anthu).”

    [41] “(Sulaiman) adati: “Msinthireni (maonekedwe a) mpando wake wachifumuwo kuti tione kodi auzindikira kapena akhala mwa omwe sazindikira (chinthu)

    [42] “Choncho pamene (mfumukazi) idadza, kudanenedwa: “Kodi mpando wako wachifumu uli ngati uwu?” Idati: “Uli ngati umenewu, ndithu ndipo ife tidapatsidwa kuzindikira (za uneneri wanu) tisadaone chozizwitsa ichi; ndipo, ndithu tidadzipereka (kwa Allah).”

    [43] “Ndipo (Sulaiman) adamuletsa zomwe amazipembedza kusiya Allah. Ndithu (mfumukaziyo) idali mwa anthu osakhulupirira (Allah)

    [44] “(Mfumukazi ija) idauzidwa kuti: “Lowa mkhonde la nyumba.” Koma pamene adaliona adaliganizira kuti ndidziwe; adakweza nsalu kumiyendo yake. (Sulaiman) adati: “Ndithu limeneli ndikhonde lomwe laziridwa ndi magalasi.” (Mfumukazi) idati: “E Mbuye wanga! Ndadzichitira ndekha chinyengo; choncho, ndagonjera kwa Allah, Mbuye wazolengedwa pamodzi ndi Sulaiman.”

    [45] “Ndipo ndithu Asamudu tidawatumizira m’bale wawo Swalih kuti awauze: “Mpembedzeni Allah.” Choncho adali magulu awiri omwe amakangana. (Ena adam’tsata pomwe ena adam’kana)

    [46] “(Swaleh) adati: “E inu anthu anga chifukwa ninji inu mukufulumizitsa choipa (kuti chidze) musanachite chabwino? Bwanji simukupempha chikhululuko kwa Allah kuti muchitiridwe chifundo?”

    [47] “(Iwo) adati: “Tapeza masoka oipa chifukwa cha iwe ndi omwe uli nawo.” (Iye) adati: “Tsoka lanu lili kwa Allah (chifukwa cha zolakwa zanu); koma inu ndinu anthu amene mukuyesedwa (ndi Allah kuti aone ngati mutsatire Mtumiki Wake kapena simutsatira).”

    [48] “Ndipo m’mudzimo adalipo anthu asanu ndi anayi omwe amaononga pa dziko, ndipo samakonza (chilichonse koma kuchiononga)

    [49] “(Iwo) adati: “Aliyense wa ife alumbire kwa Allah (kuti) iye (Swaleh) ndi banja lake timthira nkhondo usiku, ndipo kenako Timuuza mlowam’malo wake (kuti): “Sitidaone kuonongeka kwa m’bale wake; ndithu ife tikunena zoona.”

    [50] “Ndipo adakonza chiwembu ndi kutchera misampha yamphamvu, nafenso tidawatchera misampha yowaononga, iwo asakudziwa

    [51] “Tsono tayang’ana, kodi malekezero a chiwembu chawo adali otani! Tidawaononga iwo ndi anthu awo onse

    [52] “Izo ndinyumba zawo (zomwe zasanduka) mabwinja chifukwa cha chinyengo chawo. Ndithu m’zimenezo muli phunziro kwa odziwa

    [53] “Ndipo tidawapulumutsa amene adakhulupirira pakuti amamuopa (Allah)

    [54] “Ndipo (akumbutse nkhani ya) Luti pamene adanena kwa anthu ake: “Kodi mukuchita zadama uku inu mukuziona?”

    [55] ““Kodi inu mukugona ndi amuna pokwaniritsa chilakolako (cha chilengedwe) kusiya akazi? koma inu ndinu mbuli.”

    [56] “۞ Koma anthu ake sadayankhe yankho lina koma ili (lakuti): “Apirikitseni otsatira Luti m’mudzi mwanumu; ndithu iwo ndianthu odziyeretsa (asakhale pamodzi ndi ife adama).”

    [57] “Choncho tidampulumutsa iye ndi otsatira kupatula mkazi wake; tidamkozera kukhala mmodzi mwa otsalira (kuti aonongedwe pamodzi ndi oonongedwa, chifukwa cha ntchito zake zoipa ngakhale kuti adali mkazi wa mneneri)

    [58] “Ndipo tidawavumbwitsira mvula (yamiyala); iyipirenji mvula ya ochenjezedwa (koma osachenjezeka)

    [59] “Nena: “Kuyamikidwa konse kwabwino nkwa Allah, ndipo mtendere ukhale pa akapolo Ake omwe adawasankha. Kodi wabwino ndi Allah kapena zimene akumphatikiza nazozo?”

    [60] “(E iwe Mtumiki! Pitiriza kuwafunsa) kodi kapena (wabwino) ndiamene adalenga thambo ndi nthaka (ndi zam’menemo) ndi kukutsitsirani madzi (mvula yothandiza) kuchokera kumwamba, choncho ndi madziwo timameretsa madimba okongola. Inu simungathe kumeretsa mitengo yake. Kodi pamodzi ndi Allah pali mulungu (wina)? Koma iwo (Akafiri) ndi anthu opotoka

    [61] “Kodi kapena (wabwino) ndiamene adapanga nthaka kukhala malo okhazikika ndi kuika mitsinje pakati pake ndi kuipangira mapiri, ndi kuika chitsekerezo pakati pa nyanja ziwiri (nyanja ya madzi amchere, ndi yamadzi ozizira)? Kodi pamodzi ndi Allah pali mulungu wina? Koma ambiri a iwo sadziwa

    [62] “Kapena (wabwino) ndiyemwe amamuyankha wozunzika akamampempha ndi kumchotsera masautso ake ndi kukuchitani inu kukhala oyendetsa dziko lapansi? Kodi pamodzi ndi Allah pali mulungu wina? Ndithu kulangizika kwanu nkochepa

    [63] “Kapena (wabwino) ndiyemwe amakuongolerani mu mdima wa pamtunda ndi panyanja ndi kutumiza mphepo kuti ikudzetsereni nkhani yabwino patsogolo pa chifundo chake (mvula isanagwe)? Kodi pamodzi ndi Allah pali mulungu wina? Allah watukuka ku zimene akumuphatikiza nazo

    [64] “Kapena (wabwino) ndiamene adayambitsa zolengedwa, (ndipo) kenako adzazibweza, kapenanso amene amakupatsani rizq (chakudya) kuchokera kumwamba ndi m’nthaka? Kodi pamodzi ndi Allah pali mulungu winanso? Nena: “Bweretsani umboni wanu ngati mukunena zoona (wotsimikizira kuti Allah ali ndi mnzake).”

    [65] “Nena: “Palibe amene alipo kumwamba ndi pansi akudziwa zam’seri (zomwe zisanadze) kupatula Allah basi. Ndipo (amene akuwapembedza) sadziwa kuti ndiliti adzaukitsidwa ku imfa.”

    [66] “Kwakhwima liti kudziwa kwawo (za kudza) kwa tsiku la chimaliziro? Koma iwo ali mchikaiko ndi za tsikulo; koma iwo ngakhungu pa zatsikulo

    [67] “Ndipo adanena omwe adatsutsa (za Allah): “Kodi tikadzakhala dothi, ife ndi makolo athu akale, (nzoona) tidzatulutsidwanso (m’manda tili amoyo)?”

    [68] “Ndithu tidalonjezedwa izi, ife ndi makolo athu kale, izi sichina koma ndi nthano (zabodza) za anthu akale.”

    [69] “Nena: “Yendani pa dziko ndi kuona momwe adalili mapeto a oipa.”

    [70] “Ndipo usawadandaulire, ndiponso usakhale wobanika chifukwa cha ziwembu zomwe akuchita

    [71] “Ndipo (iwo) akuti: “Kodi lonjezoli lidzachitika liti, ngati mukunena zoona?”

    [72] “Nena: “Kapena zina mwa zomwe mukuzifulumizitsa zili pafupi kukupezani.”

    [73] “Ndipo ndithu Mbuye wako ndi mwini kupereka ubwino (waukulu) kwa anthu; koma ambiri a iwo sathokoza

    [74] “Ndipo ndithu Mbuye wako akudziwa zomwe zikubisa zifuwa zawo ndi zomwe akuonetsera poyera

    [75] “Ndiponso palibe chobisika kumwamba ndi m’nthaka koma chili m’buku lofotokoza chilichonse

    [76] “Ndithu Qur’an iyi, ikufotokoza kwambiri za ana a Israyeli pa zambiri zomwe iwo akutsutsana

    [77] “Ndipo ndithu iyi (Qur’an) ndichiongoko ndi chifundo kwa okhulupirira

    [78] “Ndithu Mbuye wako adzalamula pakati pawo ndi chiweruzo chake (choona); ndipo Iye Ngwamphamvu zoposa Ngodziwa chilichonse

    [79] “Choncho tsamira kwa Allah; ndithu iwe uli pa njira yachoonadi yoonekera

    [80] “Ndithu iwe sungathe kuwachititsa kuti amve kuitana kwako akufa, ndiponso sungathe kuwachititsa kuti agonthi amve kuitanako, pamene akucheuka kutembenuza misana (osafuna kumva ulaliki wako)

    [81] “Ndiponso suli owaongola akhungu m’kusokera kwawo, ndipo sungachititse kuti amve (uthenga wako) kupatula yemwe akukhulupirira Ayah (ndime) Zathu; iwowo ndiwo Asilamu (ogonjera malamulo Athu)

    [82] “Ndipo mawu (onena kudza kwa Qiyâma) akadzatsimikizika pa iwo, tidzawatulutsira chinyama m’nthaka chimene chidzawayankhula kuti ndithu anthu adalibe chitsimikizo pa Ayah (ndime) Zathu

    [83] “Ndipo (akumbutse za) tsiku lormwe tidzasonkhanitsa magulumagulu mu m’badwo uliwonse omwe amatsutsa Ayah (ndime) Zathu. Ndipo iwo adzakhala magulumagulu

    [84] “Kufikira pomwe adzaza; (Allah) adzati: “Kodi inu mudazitsutsa Ayah (ndime) Zanga popanda kuzidziwa bwinobwino, nanga mumachita chiyani?”

    [85] “Ndipo mawu onena za kuonongeka adzatsimikizika pa iwo, chifukwa cha chinyengo chawo (chodzichitira okha) ndipo iwo sadzawiringula

    [86] “Kodi saona kuti Ife tapanga usiku ndi cholinga chakuti apumule m’menemo, ndinso usana woyera (kuti aone)? Ndithu mu zimenezo muli zizindikiro kwa anthu okhulupirira

    [87] “Ndipo (akumbutse za) tsiku limene lipenga (la chiweruziro) lidzaimbidwa, adzadzidzimuka amene ali kumwamba ndi amene ali pansi kupatula yemwe Allah wamfuna (kuti adzadzidzimuke); ndipo onse adzamdzera (Allah) ali odzichepetsa (ofooka)

    [88] “Ndipo udzawaona mapiri ndi kuwaganizira kuti akhazikika pomwe akuyenda kuyenda kwa mitambo. Chimenecho ndichikonzero cha Allah chimene adakonzera chinthu chilichonse. Ndithu Allah akudziwa zonse zimene muchita

    [89] “Amene adzadza ndi chabwino, adzalandira mphoto yoposa chabwinocho; ndikuopsa kwa tsiku limenelo, iwo adzakhala nako mwamtendere

    [90] “Koma amene adzadza ndi choipa, adzaponyedwa ku Moto champhumi (ndipo kudzanenedwa kwa iwo): “Kodi mungalipidwe (zina) osati zomwe mumachita?”

    [91] “(Nena iwe Mtumiki): “Ndithu ndalamulidwa kumpembedza Mbuye wa mzinda uwu, Yemwe adaukhazika wopatulika. Ndipo zinthu zonse nza Iye (Allah), ndipo ndalamulidwa kukhala mmodzi wa ogonjera (Allah).”

    [92] ““Ndiponso (ndalamulidwa) kuti ndiwerenge Qur’an.” Ndipo amene waongoka, ubwino wa kuongokako uli pa iye; ndipo amene wasokera, (wadzisokeretsa yekha). Nena: “Ndithu ine sikanthu koma ndine mmodzi wa achenjezi. (Ndilibe udindo wina woposa uwu).”

    [93] “Ndipo nena: “Kuyamikidwa konse (kwabwino) nkwa Allah; posachedwapa akusonyezani zizindikiro Zake, ndipo muzizindikira.” Ndipo Mbuye wako sali woiwala zimene mukuchita

    Nkhani

    Surah 28

    [1] “Tâ-Sîn-Mîm

    [2] “Izi ndi Ayah (ndime) za m’buku (la Qur’an) lofotokoza (chilichonse chofunika pa Chipembedzo)

    [3] “Tikukulakatulira (iwe Mtumiki) nkhani za Mûsa ndi Farawo m’njira yoona kwa anthu okhulupirira. (Koma osakhulupirira sangapindule kanthu ndi nkhanizi)

    [4] “Ndithu Farawo adadzikuza pa dziko, ndipo adawakhazika (anthu a m’dzikolo) m’magulumagulu; gulu lina la mwa iwo adalifooketsa (poliyesa akapolo) ndi kupha ana awo achimuna, ndi kuwasiya a moyo ana awo achikazi. Ndithu iye adali mmodzi wa oononga kwambiri

    [5] “Ndipo tidafuna kuwachitira zabwino amene adafooketsedwa m’dziko (la Iguputo), ndi kuwachita kukhala atsogoleri ndi kuwachitanso kukhala amlowa mmalo ( a Baiti Al-Makadasi)

    [6] “Ndi kuwapatsa mphamvu za pa dziko (kuti azichita mmene angafunire) ndi kuti timuonetse Farawo ndi Hamana ndi magulu awo ankhondo kuchokera kwa iwo (ana a Israel), zomwe amaziwopa (kuti zingawathetsere ufumu wawo)

    [7] “Ndipo tidamzindikiritsa mayi wa Mûsa (tinati): “Muyamwitse (mwana wako), ndipo ukamuopera (chiwembu cha Farawo), mponye mu mtsinje usaope, ndipo usadandaule ndithu Ife tidzamubwezera kwa iwe, ndipo tidzamchita kukhala mmodzi wa atumiki.”

    [8] “Choncho adamtola anthu a Farawo kuti mapeto ake adzakhale m’dani kwa iwo ndi odandaulitsa. Ndithu Farawo ndi Hamana ndi magulu awo ankhondo adali olakwa

    [9] “Ndipo mkazi wa Farawo adati: “(Musamuphe, akhale) chosangalatsa diso langa ndi lako; musamuphe mwina angatithandize, kapena tingam’chite kukhala mwana (wathu.” Adanena izi) iwo asakudziwa (kuti adzakhala m’dani wawo)

    [10] “Ndipo mu mtima mwa mayi wa Mûsa mudali mopanda kanthu (mudalibe maganizo ena koma maganizo a mwana wake). Padatsala pang’ono kuti aonetse (chinsinsi cha mwanayo ponena kuti adali mwana wake), tikadapanda kulimbitsa mtima wake, kuti akhale mmodzi mwa okhulupirira (lonjezo la Allah)

    [11] “Ndipo (mayi wa Musayo) adauza mlongo wake (wa Mûsa): “Mtsatire, (komwe madzi akupita naye).” Choncho iye ankamuyang’ana chapatali pomwe iwo samadziwa (za ichi)

    [12] “Ndipo poyamba tidamuletsa kuti asayamwe mawere a woyamwitsa, (kufikira pomwe mlongo wake) adati: “Kodi ndikusonyezeni eni nyumba omwe angakulelereni ndi kukhala naye momteteza bwino mwanayo?”

    [13] “Choncho tidamubwezera kwa mayi wake kuti maso ake atonthole, (mtima wake ukhazikike) ndi kuti asadandaule; ndi kuti adziwe kuti lonjezo la Allah ndi loona. Koma ambiri a iwo sadziwa

    [14] “Ndipo (Mûsa) pamene adakula nsinkhu wake ndi kulingana bwino tidampatsa nzeru ndi maphunziro. Ndipo umo ndimomwe timawalipirira ochita zabwino

    [15] “Ndipo (tsiku lina) adalowa mu mzinda mozemba, eni m’zindawo osadziwa. Ndipo adapeza m’menemo anthu awiri akumenyana, mmodzi wochokera ku gulu lake, ndipo winayo wochokera kwa adani ake. Tsono wa kugulu lake uja adampempha chithandizo pa mdani wake uja, ndipo Mûsa adammenya chibagera mpaka kumupha (mdaniyo). Adanena: “Iyi (ndachitayi) ndintchito ya satana; ndithu iye ndimdani wosokeretsa, woonekera.”

    [16] “Adati: “E Mbuye wanga! Ndithu ndadzichitira zoipa ndekha! Choncho ndikhululukireni!” Tero (Allah) adamkhululukira (chifukwa sadalinge kupha). Ndithu Iye (Allah) Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha

    [17] “Adati: “E Mbuye wanga! Chifukwa cha kuti mwandidalitsa, sindidzakhala mthangati wa oipa.”

    [18] “Choncho kudamuchera mu mzindamo (m’mawa mwake) uku ali wodzazidwa ndi mantha akuyembekezera (kuti chiyani chimpeze pa zimene zidachitika); pompo munthu uja adampempha dzulo chithandizo ankamuitana (kuti amthandize kumenyana ndi m’dani wake wina). Mûsa adamuuza: “Ndithudi ndiwe wopotoka owonekera.”

    [19] “Choncho pamene adafuna kumpanda, yemwe ndi mdani wa awiriwo, (uja wofuna chithandizo kwa Mûsa adaganiza kuti Mûsa afuna kuti ampande iye), ndipo adati: “E iwe Mûsa! Kodi ukufuna kundipha monga momwe udaphera munthu uja dzulo? Iwe sufuna china koma kukhala wodzitukumula (wankhanza) pa dziko, ndipo sukufuna kukhala mmodzi mwa ochita zabwino (oyanjanitsa okangana ndi kukonza zinthu).”

    [20] “(Farawo zitamfika mphekesera kuti Mûsa wapha munthu pothangata mu Israyeli, adalamula kuti Mûsa paliponse pomwe angapezeke, agwidwe ndi kuphedwa). Choncho munthu adadza akuthamanga kuchokera kumalekezero a m’zindawo. Adati: “E iwe Mûsa! Akuluakulu akukuchitira upo kuti akuphe choncho choka (m’dziko muno). Ndithu ine ndine mmodzi mwa okufunira iwe zabwino.”

    [21] “Ndipo adachoka mu mzindawo ali woopa uku akuyembekezera (kumpeza choipa kuchokera kwa adani ake). Adati: “E Mbuye wanga! Ndipulumutseni kwa anthu ochita zoipa.”

    [22] “Ndipo pamene adalunjika (kumka) ku Madiyan adati: “Mwina Mbuye wanga andiongolera kunjira yoyenera.”

    [23] “Ndipo pamene adawafika madzi a ku Madiyan (pomwe anthu kumeneko ankatungapo madzi), adapeza gulu la anthu likumwetsa (ziweto zawo), ndipo pambali (pa gululo) adapeza akazi awiri akuletsa (ziweto zawo kuti zisapite kukamwa ndi ziweto zinazo). (Mûsa) adati: “Kodi mwatani? (Bwanji simukuzimwetsa ziweto zanu?)” Iwo Adati: “Sitingamwetse (ziweto zathu) mpaka abusa atachotsa (ziweto zawo, chifukwa sitingathe kulimbana nawo). Ndipo bambo wathu ndinkhalamba yaikulu kwabasi.”

    [24] “Choncho (Mûsa) adawamwetsera (ziweto zawo); kenako adapita pamthunzi, ndipo adati: “E Mbuye wanga! Ndithu ine ndiwosaukira chabwino chimene munditsitsire.”

    [25] “Kenako mmodzi mwa asungwana aja adadza kwa iye uku akuyenda mwa manyazi. (Msungwanayo) adati: “Ndithu tate wanga akukuitana kuti akakupatse malipiro pakutimwetsera (ziweto zathu).” Choncho pamene adamdzera, (mneneri Shuaib) ndikumulongosolera nkhani, adati: “Usaope; wapulumuka kwa anthu oipa.”

    [26] “Mmodzi wa iwo (asungwana aja) adanena: “E bambo wanga mulembeni ntchito (kuti akhale woweta ziweto m’malo mwa ife). Ndithu amene alibwino kuti mumulembe ntchito ndi yemwe ali wamphamvu wokhulupirika (zonse ziwiri mwa iyeyu zirimo)

    [27] “(Shuaib) adati (kwa iye): “Ine ndikufuna kukukwatitsa mmodzi mwa asungwana anga awiriwa, chiongo chake ndikundigwilira ntchito zaka zisanu ndi zitatu; ngati utakwaniritsa zaka khumi ndiye kuti nkufuna kwako. Sindikufuna kukuvutitsa (pokuchulukitsira zaka); undipeza, Allah akafuna, kuti ndine mmodzi wa anthu abwino, (wokwaniritsa lonjezo).”

    [28] “(Mûsa) adati: “Zimene mwandilonjezazi zili pakati pa ine ndi inu. Nyengo iriyonse imene ndikwaniritse pa ziwirizi (pogwira ntchitoyo, ndiye kuti ndakwaniritsa lonjezo lanu) musandichitire mtopola. Ndipo Allah ndiye Muyang’aniri pa zomwe tikukambazi.”

    [29] “Mûsa pamene adakwaniritsa nyengoyo, adanyamuka ndi banja lake (kubwerera kwao) adaona moto kumbali ya phiri. Adauza banja lake: “Dikirani ndithudi ine ndaona moto mwina mwake ndingakutengereni nkhani za kumeneko kapena chikuni cha moto kuti muothe.”

    [30] “Tsono pamene adaudzera, adaitanidwa kuchokera mbali ya kumanja ya chigwacho, pa malo wodalitsidwa kuchokera mu mtengo, ankati: “E iwe Mûsa! Ndithudi Ine ndi Allah Mbuye wa zolengedwa.”

    [31] ““Ndipo ponya (pansi) ndodo yakoyo.” Choncho pamene adayiona ikugwedezeka monga kuti iyo ndi njoka, adatembenuka kuthawa ndipo sadachewuke. (Adauzidwa): “E iwe Mûsa! Bwera kuno, usaope. Ndithu iwe ndiwe mmodzi wokhala ndi mtendere.”

    [32] “Lowetsa dzanja lako m’thumba mwako (palisani la mkanjo wako), lituluka lili loyera, popanda choipa. Ukachita mantha, fumbata dzanja lako chakukhwapa; (ukatero mantha akuchokera). Izi zidzakhala zizindikiro ziwiri zochokera kwa Mbuye wako kwa Farawo ndi nduna zake. Ndithu iwo ndianthu olakwa.”

    [33] “(Mûsa) adanena (moopa) “E Mbuye wanga! Ine ndidapha munthu mwa iwo, ndipo ndikuopa kuti akandipha.”

    [34] ““Ndipo m’bale wanga (Haaruni) ndikatswiri pakuyankhula kuposa ine. Mutumizeni pamodzi ndi ine monga mnthandizi, azikandivomereza (pa zimene ndizikanena). Ndithu ine ndikuopa kuti akanditsutsa.”

    [35] “(Allah) adati: “Tilimbitsa dzanja lako ndi m’bale wakoyo ndipo tikupatsani kupambana, iwo sangafikitse masautso pa inu; chifukwa cha zozizwitsa zathuzo inu awiri ndi amene akutsatireni, ndinu opambana.”

    [36] “Pamene Mûsa adawadzera ndi zizindikiro zathu zoonekera poyera, adati: “Ichi sichina koma ndi matsenga wopeka; sitidamvepo zimenezi kumakolo athu akale.”

    [37] “Ndipo Mûsa adanena: “Mbuye wanga akumudziwa yemwe wadza ndi chiongoko kuchokera kwa Iye ndi yemwe adzakhala ndi mathero a pokhala pabwino. Ndithu ochita zoipa sakapambana.”

    [38] “Ndipo Farawo adati: “E inu nduna (zanga)! Sindidziwa kuti inu muli ndi mulungu (wina) kupatula ine. Choncho, iwe Haamana! Ndiwotchere njerwa tero undimangire chipilala kuti mwina mwake ndingamsuzumire Mulungu wa Mûsa. Ndithu ine ndikumganizira kuti ndi mmodzi wa abodza.”

    [39] “Ndipo iye pamodzi ndi makamu ake ankhondo adadzitukumula pa dziko popanda chilungamo ndipo ankaganiza kuti iwo sadzabwelere kwa Ife

    [40] “Koma tidamulanga ndi magulu ake ankhondo ndi kuwaponya m’nyanja; yang’ana, kodi adali bwanji mathero a ochita zoipa

    [41] “Ndipo tidawachita kukhala atsogoleri oitanira (anthu) ku Moto; ndipo tsiku la chiweruziro (Qiyâma) sadzathandizidwa

    [42] “Tidawatsatiziranso matembelero padziko lino lapansi. Ndipo tsiku la chimaliziro iwo adzakhala oyipitsitsa (ndi kuthamangitsidwa ku chifundo cha Allah)

    [43] “Ndipo ndithu Mûsa tidampatsa buku pambuyo powononga mibadwo yoyamba kuti likhale chiphanulamaso cha anthu (kuti liwaunikire ku njira yolungama), ndi kuti likhale chiongoko ndi chifundo kuti iwo akumbukire

    [44] “Ndipo iwe sudali mbali ya kuzambwe (kwa phiri limenelo) pamene tidampatsa Mûsa lamulo; sudalinso mwa amene adalipo (pamalopo)

    [45] “Koma ife tidaumba mibadwo yambiri (pambuyo pa Mneneri Mûsa) kotero kuti zaka zidapitapo zambiri pakati pawo. Ndipo sudakhale nawo anthu a Madiyan ndi kumawawerengera Ayah (ndime) Zathu; koma Ife tidali kutuma (atumiki ndi kuwafotokozera zomwe zidachitika patsogolo ndi pambuyo pawo, monga momwe takutumira iwe ndi kukudziwitsa nkhani zakale ndi zimene zikudza pambuyo)

    [46] “Ndipo sudali kumbali kwa phiri pamene tidamuitana (Mneneri Mûsa). Koma (kutumidwa kwako) ndimtendere wochokera kwa Mbuye wako kuti uwachenjeze anthu omwe mchenjezi sadawadzere (mnthawi yaitali) iwe usadadze, kuti akumbukire

    [47] “(Ndipo sitikadatuma) koma kuti mavuto akawapeza ochokera (ku zoipa) zomwe atsogoza manja awo, amanena: “Mbuye wathu! Bwanji wosatitumizira Mtumiki kuti titsate mawu anu ndi kukhala mwa okhulupirira.”

    [48] “Koma choona pamene chidawadzera kuchokera kwa Ife, adati: “Bwanji sadapatsidwe zonga zomwe adapatsidwa Mûsa? (Monga kutembenuza ndodo kukhala njoka, ndi zina zotero).” Kodi kalelo sadazikane zomwe adapatsidwa Mûsa? Nkunena (za Taurati ndi Qur’an): “Ndimatsenga awiri amene akuthandizana.” Ndipo adati: “Ndithu ife tikuwakana onse.”

    [49] “Nena: “Bwerani nalo buku lochokera kwa Allah lomwe lili ndi chiongoko chabwino kuposa awiriwa (Taurati ya Mneneri Mûsa, ndi iyi Qur’an), kuti ndilitsate ngati inu mukunena zoona.”

    [50] “Koma ngati sadakuyankhe, dziwa kuti akutsatira zilakolako zawo. Kodi ndani wasokera kwambiri kuposa yemwe akutsatira zilakolako zake popanda chiongoko chochokera kwa Allah? Ndithu Allah saongola anthu odzichitira zoipa

    [51] “Ndipo ndithu tafikitsa mawu kwa iwo mochulukitsa, mwatsatanetsatane kuti iwo akumbukire

    [52] “Amene tidawapatsa buku kale ili lisadadze, akulikhulupirira ili (buku la Qur’an)

    [53] “Ndipo likawerengedwa kwa iwo, akuti: “Talikhulupirira; ndithu ichi nchoona chochokera kwa Mbuye wathu; ndithu ilo lisanadze ife tidali Asilamu (ogonjera Allah).”

    [54] “Iwo adzapatsidwa malipiro awo kawiri (chifukwa chotsatira Mneneri Mûsa Ndi Mneneri Isa (Yesu), kale; ndipo tsopano ndikumtsatira Mneneri Muhammad{s.a.w}) nchifukwa chakuti adapirira; amachotsa choipa (pochita) chabwino, ndipo m’zimene tawapatsa akupereka chopereka (Sadaka)

    [55] “Ndipo akamva zopanda pake amazipewa, ndipo amati (kwa achibwanawo): “Ife tili ndi zochita zathu inunso muli ndi zochita zanu, mtendere ukhale pa inu. Ife sitifuna (kutsutsana) ndi mbuli.”

    [56] “Ndithu iwe sungathe kumuongola amene ukumfuna, koma Allah amamuongola amene wamfuna. Ndipo Iye akudziwa za amene ali oongoka

    [57] “Ndipo akunena (akafiri a m’ Makka, kuuza Mtumiki): “Ngati titsatira chiongoko (ichi chimene wadza nacho) pamodzi ndi iwe, tifwambidwa m’dziko lathu (potimenya nkhondo mafuko ena a Arabu).” Kodi sitidawakhazike pamalo opatulika ndi pa mtendere pomwe zipatso za mitundumitundu zikudza pamenepo mwaulere (monga rizq) zochokera kwa Ife? Koma ambiri a iwo sadziwa

    [58] “Kodi ndimidzi ingati imene tidaiononga yomwe inkanyadira za moyo wawo (wosavutika ndi wodya bwino)! Umo m’malo mwawo simudakhalidwebe pambuyo pawo koma mochepa basi; ndipo ife tidalowa chokolo m’zimenezi

    [59] “Ndipo Mbuye wako sali owononga midzi pokhapokha akatuma mtumiki mu mzinda wawo waukulu ndi kuwawerengera mawu a m’ndime Zathu, (akakana ndi pamene timawaononga); ndiponso sitili owononga midzi pokhapokha anthu ake atakhala achinyengo

    [60] “Ndipo chilichonse chimene mwapatsidwa nchosangalatsa cha moyo wa pa dziko, ndiponso chokometsera chake (chomwe sichikhalira kutha); koma chomwe chili kwa Allah ndicho chabwino, chamuyaya; kodi bwanji simukuzindikira

    [61] “Kodi munthu yemwe tamulonjeza lonjezo labwino (kuti akalowa ku Munda wamtendere) kotero kuti iye akakumana nalo (lonjezolo), angafanane ndi yemwe tamsangalatsa ndi zosangalatsa za moyo wa pa dziko basi, kenako iye nkukhala mmodzi okaponyedwa (ku Moto) tsiku la chiweruziro (Qiyâma)

    [62] “Ndipo (akumbutse) tsiku limene (Allah) adzawaitana, adzati: “Ali kuti anzanga aja omwe mumanena (kuti ndianzananga)?”

    [63] “Adzanena amene mawu (onena za chilango) atsimikizika pa iwo: “Mbuye wathu! Awa ndiamene tidawasokeretsa; tidawasokeretsa monga momwe Tidasokelera. tikudzipatula ndi iwo kwa inu; samatilambira ife.”

    [64] “Ndipo kudzanenedwa: “Itanani aphatikizi anu.” Choncho adzawaitana koma sadzawayankha. Ndipo azawawona mavuto (pa nthawiyo azakhumba) akadakhala oongoka (pa dziko lapansi kotero kuti akadapeza mtendere pa tsiku la chimaliziro)

    [65] “Ndipo (akumbutse) tsiku limene adzawaitana, nkudzati: “Kodi mudawayankha chiyani Atumiki?”

    [66] “Basi tsiku limenelo nkhani zidzawasowa choncho iwo sadzatha kufunsana

    [67] “Koma amene walapa ndi kukhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, adzakhala mwa opambana

    [68] “Ndipo Mbuye wako amalenga chimene wafuna ndi kuchisankha (chimene wafuna). Iwo alibe chifuniro. Allah wapatukana ndi zonse zochepetsa ulemelero Wake, ndipo watukuka ku zomwe akumphatikiza nazo

    [69] “Ndiponso Mbuye wako akudziwa zimene zifuwa zawo zikubisa (maganizo awo) ndi zimene akuwonetsera (poyera)

    [70] “Ndipo Iye ndi Allah; palibe wopembedzedwa m’choonadi koma Iye. Kuyamikidwa konse (kwabwino) pachiyambi ndi kumapeto nkwake; ndipo kulamulanso nkwake, ndipo inu mudzabwerera kwa Iye

    [71] “Nena: “Tandiuzani ngati Allah atakupangirani usiku kuti usachoke mpaka tsiku la chiweruziro (Qiyâma), kodi ndimulungu wanji osati Allah amene angakudzetsereni kuunika? Kodi simumva?”

    [72] “Nena: “Tandiuzani ngati Allah ataupanga usana kuti usachoke mpaka tsiku la chiweruziro (Qiyâma), kodi ndimulungu wanji osati Allah amene angakudzetsereni usiku m’mene mumapumulamo? Kodi simuona (chifundo cha Allah)?”

    [73] “Ndipo mu chifundo Chake, adakupangirani usiku ndi usana kuti muzipumulamo ndi kufunafuna zabwino Zake (masana) kuti muthokoze

    [74] “Ndipo tsiku limene (Allah) adzawaitana, adzati: “Ali kuti anzanga aja amene mumati ndimilungu inzanga?”

    [75] “Ndipo mumpingo uliwonse tidzatulutsa mboni (yawo yowaikira umboni), ndipo tidzawauza: “Bwerani ndi umboni wanu.” Pamenepo adzadziwa kuti choonadi ncha Allah, ndipo zidzawasowa zimene amapeka

    [76] “Ndithu Qaruni adali mwa anthu a Mûsa; koma adazikweza kwa iwo, ndipo tidampatsa nkhokwe za chuma zomwe makiyi ake ngolemetsa kagulu ka anthu anyonga (kuwasenza). Anthu ake adamuuza: “Usanyade; ndithu Allah sakonda onyada.”

    [77] ““Ndipo uyifunefune kupyolera m’zomwe Allah wakupatsa, nyumba yabwino yomaliza, usaiwale gawo lako la m’dziko; chita zabwino monga momwe Allah wakuchitira zabwino, ndipo usafune kuononga pa dziko; ndithu Allah sakonda oononga.”

    [78] “Adati: “Ndithu ndapatsidwa izi chifukwa cha kudziwa kwanga komwe ndili nako.” Kodi iye sadadziwe kuti Allah adawaononga anthu patsogolo pake omwe adali anyonga kwambiri kuposa iye, komanso osonkhanitsa chuma chambiri? Ndipo oipa sadzafunsidwa zolakwa zawo. (Allah akudziwa zonse za iwo)

    [79] “Choncho, adatulukira kwa anthu ake (monyada) uku atadzikongoletsa. Amene akufuna moyo wa pa dziko adanena (mokhumbira): “Kalanga ife! Tikadapatsidwa monga wapatsidwa Qaruna! Ndithu iye ngodala kwakukulu.”

    [80] “Ndipo amene adapatsidwa kuzindikira adanena: “Tsoka lanu! Malipiro a Allah ngabwino kwa yemwe wakhulupirira ndi kuchita zabwino, (kuposa izi ali nazo Qaruni); ndipo sadzapatsidwa zimenezi koma okhawo ali opirira.”

    [81] “Kenako tidamdidimiza m’nthaka iye ndi nyumba yake; ndipo adalibe gulu lililonse lomuthangata popikisana ndi Allah, ndipo sadali mwa odzipulumutsa okha

    [82] “Ndipo amene ankalakalaka ulemelero wake dzulo adayamba kunena: “E zoonadi Allah amamuonjezera chuma amene akumfuna mwa akapolo Ake (chingakhale ali oipa wosayanjidwa ndi Iye), ndipo amamuchepetsera chuma (amene wamfuna kotero ngakhale ali woyanjidwa ndi Iye.) Pakadapanda Allah kutimvera chisoni. (Mkukhumbira kwathu pa zimene adampatsa Qaruna akadatikwilira m’nthaka. Ha! Zoonadi osakhulupirira sangapambane.”)

    [83] “Nyumba yomalizirayo tikawapangira amene sakufuna kudzikweza pa dziko ndi kuononga. Ndipo malekezero abwino adzakhala a wanthu owopa (Allah)

    [84] “Amene achite chabwino, adzapeza mphoto yoposa chimene adachitacho ndipo amene achite choipa sadzalipidwa (china chake) koma zoipa zomwezo zimene adali kuzichita

    [85] “Ndithudi yemwe wakulamula kuitsata Qur’an, mwachoonadi adzakubwezera pa malo pobwerera. Nena! “Mbuye wanga ndi yemwe akudziwa amene wadza ndi chiongoko ndi yemwe ali m’kusokera koonekera poyera.’’

    [86] “Ndipo iwe sudali kulakalaka kuti ungapatsidwe buku (pamodzi ndi uneneri) koma izi zidachitika pa chifundo chochokera kwa Mbuye wako; choncho usakhale m’thandizi wa anthu osakhulupirira (Allah)

    [87] “Ndipo asakutsekereze kutsatira ndime za (mawu a) Allah pa mbuyo povumbulutsidwa pa iwe, ndipo aitanire anthu kwa Mbuye wako, komatu usakhale m’gulu la anthu omphatikiza Allah ndi mafano

    [88] “Ndipo usapemphe mulungu wina pa modzi ndi Allah. Palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye Yekha. Chinthu chilichonse chidzaonongeka kupatula Nkhope Yake. Ulamuliro (wazinthu zonse) uli kwa Iye ndipo kwa Iye ndi kumene mudzabwerera nonsenu

    Kangaude

    Surah 29

    [1] “Alif-Lâm-Mîm

    [2] “Kodi anthu akuganiza kuti adzasiyidwa popanda kuyesedwa ndi masautso pakungonena kuti: “Takhulupirira?” (Iyayi, ayenera kuyesedwa ndithu ndi masautso osiyanasiyana pa matupi pawo ndi pachuma chawo kuti adziwike woona ndi wachiphamaso)

    [3] “Ndipo ndithu tidawayesa amene adalipo patsogolo pawo. Ndithu Allah awaonetsera poyera amene ali olankhula zoona, ndithu Allah awaonetsera poyera amene ali olankhula zabodza

    [4] “Kodi amene akuchita zoipa akuganiza kuti atipambana (kotero kuti sitingawalange)? Ndichiweruzo choipa chimene akuweruzacho

    [5] “Amene akuyembekezera kukumana ndi Allah, (agwire ntchito yabwino pamoyo wake kuti akakumane Naye ndi zabwino), pakuti ndithu nthawi ya Allah (tsiku la chimaliziro) ikudza (popanda chikaiko). Ndipo Iye Ngwakumva (zonena za akapolo Ake), Ngodziwa (zachinsinsi chawo)

    [6] “Ndipo amene akuchita khama (polimbana ndi Akafiri, kapena pogonjetsa mtima wake kuti utsatire malamulo a Allah), ndithu zabwino za khamalo zili pa iye mwini. Ndithu Allah siwosaukira chilichonse kwa zolengedwa Zake

    [7] “Ndipo amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, Tidzawafafanizira zoipa zawo, ndipo tidzawalipira zabwino kuposa zomwe amachita

    [8] “Ndipo tamulamula munthu kuchitira zabwino makolo ake. Koma ngati atakukakamiza (makolo ako) kuti undiphatikize Ine ndi (zinthu zina) zomwe iwe sukuzidziwa, usawamvere. Kwa Ine ndiko kobwerera kwanu, ndipo ndidzakuuzani zimene mumachita

    [9] “Ndipo amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, tidzawalowetsa m’gulu la anthu abwino

    [10] “Ndipo alipo ena mwa anthu omwe akunena: “Takhulupirira mwa Allah.” Koma akavutitsidwa chifukwa cha Allah, amawachita masautso a anthu monga chilango cha Allah, (sapirira; iwowa ndi achinyengo (achiphamaso). Ndipo chikadza chipulumutso chochokera kwa Mbuye wako amanena: “Ndithu ife tidali pamodzi ndi inu.” (Koma chikhalirecho akunena zonama). Kodi Allah sadziwa zomwe zili m’zifuwa za zolengedwa

    [11] “Ndipo ndithu Allah awaonetsera poyera amene akhulupirira (moona), ndiponso awaonetsera poyera achiphamaso (achinyengo)

    [12] “Ndipo amene sadakhulupirire adanena kwa okhulupirira: “Tsatani njira yathu; (musatsate njira ya Muhammad). Ife tidzakusenzerani machimo anu (kuti chilichonse chisakupezeni). Koma sadzasenza chilichonse cha machimo awo, ndithu iwo ngabodza

    [13] “Ndipo ndithudi, adzasenza mitolo ya machimo ndi mitolo yina yamachimo (ya omwe adawasokeretsa) poiphatikiza ku mitolo yawo ya machimo. (Nawonso osokezedwa, adzasenzanso mitolo ya machimo chifukwa cha kutsatira kwawo anthu owasokezawo). Ndipo pa tsiku la Qiyâma (chimaliziro,) ndithu adzafunsidwa pa zimene amapeka

    [14] “Ndipo ndithu tidamtuma Nuh kwa anthu ake ndipo adakhala nawo zaka chikwi chimodzi kupatulapo zaka makumi asanu. (Koma m’nthawi yonseyi sadatsatire ulaliki wake). Choncho chigumula chidawapeza (ndipo adamira onse), uku ali odzichitira zoipa

    [15] “Tidampulumutsa iye (ndi anthu ake) a m’chombo; ndipo tidachita ichi kuti likhale phunziro kwa zolengedwa

    [16] “Ndipo (akumbutse nkhani ya) Ibrahim pamene adawauza anthu ake: “Mpembedzeni Allah ndi kumuopa. Zimenezo nzabwino kwa inu ngati mukudziwa (kusiyana kwa chabwino ndi choipa).”

    [17] “Ndithu inu mukupembedza mafano kusiya (kupembedza) Allah ndipo mwadzipangira chonama. Ndithu amene mukuwapembedzawo kusiya Allah, sangakupatseni rizq (madalitso) choncho funani rizq (madalitso) kwa Allah, ndipo mpembedzeni Iye Yekha ndi kumthokoza. Kwa Iye ndikomwe mudzabwerera (tsiku la chimaliziro)

    [18] “Ndipo ngati mutsutsa, ndithu mibadwo ya omwe adalipo patsogolo panu idatsutsanso. Ndipo kwa Mtumiki kulibe udindo wina koma kufikitsa uthenga woonekera poyera, (womveka bwino)

    [19] “Kodi saona momwe Allah ayambitsira zolengedwa, kenako nkuzibwerezanso? Ndithu kwa Allah zimenezo nzosavuta

    [20] “Nena: “Yendani pa dziko ndi kuona momwe Allah adayambitsira chilengedwe; kenako Allah adzaumba, kuumba kwina. Ndithu Allah Ndiwokhoza chilichonse.”

    [21] ““Amamlanga yemwe wamfuna ndipo amamchitira chifundo amene wamfuna, ndipo kwa Iye nonse mudzabwezedwa.”

    [22] ““Ndipo inu simungampambane (Allah) pa dziko ngakhale kumwamba (pomuzemba kuti asakulangeni). Inu mulibe mtetezi kapena mpulumutsi kupatula Allah.”

    [23] “Ndipo amene akana Ayah (ndime) za Allah ndi kukumana Naye amenewo ndiwo ataya mtima pa zakupeza chifundo Changa, ndipo iwowo ndiwo adzapeza chilango chowawa

    [24] “Choncho yankho la anthu ake silidali lina koma adangoti: “Mupheni kapena mtentheni ndi moto.” Koma Allah adampulumutsa ku moto. Ndithu m’zimenezi muli zisonyezo (zosonyeza mphamvu za Allah) kwa anthu okhulupirira

    [25] “Ndipo adanena: “Ndithu inu mwasankha mafano kukhala milungu kusiya Allah, ndipo mukukondana pakati panu m’moyo wa pa dziko; (pokhalirana pamodzi ndi kupitiriza kupembedza mafanowo mwachimvano). Koma tsiku la Qiyâma, mudzakanana wina ndi mnzake, komanso mudzatembelerana wina ndi mnzake, malo anu adzakhala ku Moto, ndipo simudzapeza okupulumutsani.”

    [26] “Choncho (Mneneri) Luti adamkhulupirira iye. Ndipo (Mneneri Ibrahim) adanena: “Ndithu ine ndikusamukira kwa Mbuye wanga (ku dziko lomwe wandilamulira). Ndithu Iye Ngwamphamvu zoposa Ngwanzeru zakuya.”

    [27] “Ndipo tidampatsa (Mneneri Ibrahim) Ishâq ndi Ya’qub, ndipo tidaika uneneri ndi buku pa mbumba yake, ndipo tidampatsa malipiro ake pa dziko lapansi; ndithu iye pa tsiku la chimaliziro adzakhala mwa anthu abwino

    [28] “Ndipo (akumbutse nkhani ya Mneneri) Luti pamene adawauza anthu ake: “Ndithu inu mukuchita zadama; palibe amene adakutsogolerani kuzichita (zadamazo) mwa zolengedwa.”

    [29] ““Kodi inu mukuchita amuna anzanu ukwati ndi kutseka njira (pakuchita chifwamba) ndi kuchita zoipa m’mabwalo anu osonkhanirana?” Koma yankho la anthu ake silidali lina koma kunena kuti: “Tidzere ndi chilango cha Allah cho ngati uli mmodzi wa owona.”

    [30] “Iye adati: “Mbuye wanga! Ndipulumutseni kwa anthu oononga.”

    [31] “Ndipo pamene atumiki athu adamdzera Ibrahim ndi nkhani yabwino (yoti abereka Mneneri Ishaq), adanenanso: “Ndithu tiwaononga eni mudzi uwu (wa Sodom); ndithu iwowo ngochimwa.”

    [32] “(Mneneri Ibrahim) adati: “Koma mmenemo muli Luti.” Iwo adati: “Ife ndife odziwa kwambiri za omwe ali m’menemo; ndithu timpulumutsa iye ndi banja lake kupatula mkazi wake; iye ndi mmodzi wa otsalira (woonongeka).”

    [33] “Ndipo pamene atumiki athu adamdzera Luti, adawadandaulira ndi kuwadera nkhawa; (ndipo iwo) adati: “Usaope ndipo usadandaule. Ndithu ife tikupulumutsa ndi banja lako kupatula mkazi wako; iye ndi mmodzi wa otsalira (woonongeka).”

    [34] ““Ndithu ife tiwatsitsira chilango choipa kuchokera kumwamba eni mudzi uwu chifukwa cha kuchimwa kwawo (ndi kuukira malamulo a Allah).”

    [35] “Ndipo ndithu tidasiya chizindikiro mmenemo choonekera kwa anthu anzeru

    [36] “Ndipo ku Madiyan (tidatumako) m’bale wawo Shuaib, ndipo adati: “E inu anthu anga! Mpembedzeni Allah ndipo opani tsiku lachimaliziro musanke mu ononga pa dziko.”

    [37] “Koma adamutsutsa. Ndipo kugwedezeka kwa nthaka kudawachotsa moyo wawo, ndipo kudawachera ali gwadegwade m’nyumba zawo (atafa)

    [38] “Nawonso Âdi ndi Asamudu (tidawaononga). Ndipo mokhala mwawo mukudziwika kwa inu. Ndipo satana adawakometsera zochita zawo (zoipa), ndipo adawatsekereza ku njira (zabwino) chikhalirecho adali openya (anzeru zawo)

    [39] “Momwemonso Kaaruni, Farawo ndi Hamana (adaonongedwa). Ndithu adawadzera Mûsa ndi zozizwitsa (zooneka), koma adadzikweza pa dziko. Komatu sadathe kumpambana (Allah pomulepheretsa kuwalanga)

    [40] “Choncho aliyense wa iwo tidamlanga ndi machimo ake. Ena a iwo tidawatumizira chimphepo chamiyala; ena a iwo udawaononga mkuwe; ena a iwo tidawadidimiza m’nthaka, ndipo ena a iwo tidawamiza (m’madzi). Si Allah amene adawachitira zoipa, koma adadzichitira okha zoipa

    [41] “Fanizo la amene adzipangira milungu yabodza kusiya Allah, lili ngati fanizo la kangaude (yemwe) wadzipangira nyumba (kuti imsunge, pomwe nyumbayo siingathe kumsunga m’nyengo yozizira kapena yotentha), ndithu nyumba yomwe ili yofooka kwambiri ndi nyumba ya kangaude, akadakhala akudziwa

    [42] “Ndithu Allah akudziwa kupembedza kwawo zinthu zina kusiya Iye, Iye Ngwamphamvu zoposa, Ngwanzeru zakuya

    [43] “Ndipo amenewa ndimafanizo (omwe) tikuwaponyera anthu. Sangawazindikire kupatula odziwa

    [44] “Allah adalenga thambo ndi nthaka mwachoonadi; ndithu; m’menemo muli zizindikiro kwa okhulupirira

    [45] “Werenga zimene zavumbulutsidwa kwa iwe (za) m’buku, ndipo pemphera Swala moyenera; ndithu Swala (ikapempheredwa moyenera) imamtchinjiriza (woipempherayo) ku zinthu zauve ndi zoipa. Ndipo kukumbukira Allah, ndi chinthu chachikulu. Ndipo Allah akudziwa zimene mukuchita

    [46] “۞ Ndipo musatsutsane ndi anthu a buku koma kutsutsana kwabwino kupatula amene achita zoipa mwa iwo. Ndipo nenani: “Takhulupirira zomwe zavumbulutsidwa kwa ife ndi zomwe zavumbulutsidwa kwa inu, ndipo Mulungu wathu ndi Mulungu wanu ndi Mmodzi; ndipo ife ndife ogonjera Iye.”

    [47] “Ndipo umo ndimomwe takuvumbulutsira buku (ili la Qur’an). Choncho amene tidawapatsa buku, (ili lisadadze, monga Taurat ndi Injili), akulikhulupirira; akulikhulupiriranso ena mwa awa (Arabu omwe sitidawapatse buku). Ndipo sangawakane ma Ayah Athu kupatula osakhulupirira

    [48] “Ndipo iwe sumawerenga buku lililonse, ili lisanadze; ndipo sudalilembe ndi dzanja lako lakumanja. Zikadatero ndiye kuti anthu achabe akadakaikira

    [49] “Koma izi ndi Ayah zoonekera poyera zomwe zili m’zifuwa za amene apatsidwa nzeru. Ndipo sangazikane Ayah (ndime) zathu koma achinyengo

    [50] “Ndipo akunena: “Kodi bwanji sizinatsitsidwe kwa iye zozizwitsa kuchokera kwa Mbuye wake?” Nena: “Zozizwitsa zili kwa Allah; ndipo ine ndine mchenjezi woonekera, (ndilibe mphamvu zokudzetserani zozizwitsa koma pokhapo Allah atafuna).”

    [51] “Kodi sizidawakwanire kuti takuvumbulutsira buku (ili) lomwe likuwerengedwa kwa iwo? Ndithu mmenemo muli chifundo ndi phunziro kwa anthu okhulupirira

    [52] “Nena: “Allah akukwana kukhala mboni pakati panga ndi inu; akudziwa za kumwamba ndi zapansi ndipo amene akukhulupirira zachabe ndi kukana Allah, iwowo ndiwo otayika.”

    [53] “Ndipo akukupempha kuti chilango chidze mwachangu; kukadapanda kuti kudaikidwa nthawi yodziwika, chilango chikadawadzera. Ndipo ndithu chidzawadzera mwadzidzidzi asakudziwa

    [54] “Akukupempha kuti chilango chidze mwachangu; ndithu Jahannam idzawazinga osakhuiupirira

    [55] “Tsiku limene chidzawavindikira chilango kuchokera pamwamba pawo ndi pansi pa miyendo yawo; ndipo adzanena: “Lawani (chilango cha) zomwe munkachita.”

    [56] “E inu akapolo Anga amene mwakhulupirira! Ndithu nthaka Yanga njophanuka; (mukhoza kupita dziko lina ngati m’dziko lanulo simukupeza mwayi wopembedza Allah mokwanira); ndipo Ine ndekha ndipembedzeni

    [57] “Chamoyo chilichonse chidzalawa imfa. Kenako mudzabwezedwa kwa Ife

    [58] “Ndipo amene akhulupirira ndi kumachita zabwino ndithudi tidzawakhazika m’zipinda za ku Munda wamtendere, momwe pansi (ndi patsogolo) pake pakuyenda mitsinje; adzakhala m’menemo nthawi yaitali. Taonani kukhala bwino malipiro a ochita zabwino

    [59] “Amene adapirira ndipo kwa Mbuye wawo amatsamira

    [60] “Ndinyama zingati zomwe sizidzipezera rizq lake. Allah akuzipatsa izo pamodzi ndi inunso. Ndipo Iye Ngwakumva; Ngodziwa

    [61] “Ndipo ngati utawafunsa (kuti): “Kodi ndani adalenga thambo ndi nthaka, ndi kugonjetsa dzuwa ndi mwezi?” Ndithu anena: “Ndi Allah.” Nanga akutembenuzidwira kuti

    [62] “Allah amamtambasulira rizq amene wamfuna mwa akapolo Ake, ndi kumchepetsera (amene wamfunanso). Ndithu Allah Ngodziwa kwambiri za chilichonse

    [63] “Ndipo ngati utawafunsa (kuti): “Kodi ndani amene akutsitsa madzi kuchokera ku mitambo ndi kuiukitsa nthaka ndi madziwo pambuyo pakufa kwake?” Ndithu anena: “Ndi Allah.” Nena: “Kuyamikidwa konse nkwa Allah.” Koma ambiri a iwo sazindikira

    [64] “Ndipo moyo uwu wa pa dziko lapansi suli kanthu, koma chibwana ndi masewera. Ndipo ndithu nyumba ya tsiku la chimaliziro, ndiwo moyo weniweni, akadakhala akudziwa

    [65] “Ndipo akakwera m’chombo (ndi kukumana ndi zoopsa), amampempha Allah modzipereka ndikumuyeretsera pempho. Koma akawapulumutsa ndi kuwafikitsa ku ntunda, iwo amayambanso kumuphatikiza ndi mafano

    [66] “Posathokoza zimene tawapatsa. Aleke asangalale (ndi zoipa zawozo); posachedwa adzadziwa

    [67] “Kodi saona kuti dziko lawo (mzinda wa Makka) talichita kukhala lopatulika, lamtendere pomwe anthu ena akutsompholedwa m’mphepete mwawo? Kodi akukhulupirira zachabe ndi kuukana mtendere wa Allah

    [68] “Kodi wachinyengo wamkulu ndani woposa amene akupekera bodza Allah, kapena kutsutsa choona chikamdzera? Kodi si mu Jahannam momwe mudzakhala malo a osakhulupirira

    [69] “Ndipo amene akulimbikira m’njira yathu, (polimbana ndi satana, ndi mzimu woipa ndi zilakolako zoipa zam’thupi, ndi cholinga chofuna kukondweretsa Allah) ndithu tiwaongolera ku njira Zathu. Ndipo ndithu Allah ali pamodzi ndi ochita zabwino

    Aroma

    Surah 30

    [1] “Alif-Lâm-Mîm

    [2] “Aroma agonjetsedwa (ndi Aperezi)

    [3] “M’dziko loyandikira (kwa Arabu lomwe ndi dziko la Sham). Nawonso pambuyo pogonjetsedwa kwawo, adzagonjetsa (Aperezi)

    [4] “Mzaka zochepa (zosapyolera ). Zonse nza Allah, pambuyo ndi patsogolo (pankhondoyo). Ndipo tsiku limenelo okhulupirira adzasangalala

    [5] “Ndi chithandizo cha Allah (chimene iwo adzapatsidwa, chomwe ndikugonjetsa Aquraish tsiku lomwelo). (Allah) amamthandiza amene wamfuna, ndipo Iye Ngwamphamvu zoposa; Ngwachisoni chosatha

    [6] “Ili ndilonjezo la Allah (loona pa okhulupirira). Allah saswa lonjezo Lake. Koma anthu ambiri sadziwa

    [7] “Akudziwa zoonekera (zokhazokha) za moyo wa dziko lapansi (zomwe amadalira pa moyo wawo. Monga ulimi, malonda, zomangamanga ndi zina zotero). Ndipo iwo salabadira za tsiku la chimaliziro

    [8] “Kodi salingalira mwa iwo okha (nkuona kuti) Allah sadalenge thambo ndi nthaka ndi zapakati pake, koma mwachilungamo, ndiponso kwa nthawi yoikidwa? Ndithu anthu ambiri ngotsutsa za kukumana ndi Mbuye wawo

    [9] “Kodi sadayende pa dziko nkuona momwe adalili malekezero a omwe adaliko patsogolo pawo? Adali anyonga zambiri kuposa iwo. Adailima nthaka ndi kumangapo zomangamanga kuposa momwe iwo adamangirapo. Ndipo aneneri awo adawadzera ndi zizindikiro zoonekera (koma adawatsutsa, ndipo Allah adawawononga). Choncho Allah sadali owapondereza koma iwo ankadzipondereza okha

    [10] “Kenako malekezero a amene adaipitsa adali chilango choipa kamba koti adatsutsa Ayah za Allah ndipo ankazichitira chipongwe

    [11] “Allah amayambitsa kulenga (zolengedwa), kenako adzabwerezanso (kulengako pambuyo pa imfa yawo), kenako mudzabwezedwa kwa Iye (kuti mudzaweruzidwe)

    [12] “Ndipo tsiku limene nthawi ya chiweruziro (Qiyâma) idzakwana, oipa adzataya mtima (zakupeza mtendere wa Allah)

    [13] “Ndipo sadzakhala ndi aomboli ochokera m’mafano awo, ndipo mafano awowo adzawakana

    [14] “Ndipo tsiku limene nthawi ya chiweruziro (Qiyâma) idzakwana, tsiku limenelo adzalekana (ena kukalowa ku Munda wamtendere, pomwe ena akalowa ku Moto)

    [15] “Koma amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, adzakhala m’minda ya zipatso ndi maluwa akusangalatsidwa

    [16] “Ndipo amene sadakhulupirire ndi kutsutsa Ayah Zathu ndi za kukumana ndi tsiku lachimaliziro, iwo adzaperekedwa ku chilango cha Moto

    [17] “Choncho, lemekezani Allah pamene mukulowa m’nthawi za usiku (popemphera Magrbi ndi Isha); ndi pamene mukulowa m’nthawi ya m’bandakucha (popemphera pemphero la Fajr)

    [18] “Kutamandidwa konse, kumwamba ndi pansi nkwa Allah. Ndipo (mulemekezeni) m’nthawi ya madzulo (popemphera Asr) ndi pomwe mukulowa m’nthawi yamasana (Dhuhr)

    [19] “(Iye) amatulutsa chamoyo kuchokera mchakufa, ndipo amatulutsa chakufa kuchokera m’chamoyo, ndipo amaukitsa nthaka pambuyo pa kufa kwake. Ndipo momwemonso mudzatulutsidwa (m’manda)

    [20] “Ndipo zina mwa zizindikiro Zake (zosonyeza mphamvu Zake zoposa), ndiko kukulengani kuchokera ku dothi kenako inu nkukhala anthu omwe mukufala (ponseponse)

    [21] “Ndipo zina mwa zizindikiro Zake (zosonyeza chifundo Chake kwa inu) ndiko kukulengerani akazi a mtundu wanu kuti mukhazikike (mitima yanu) kwa iwo, ndipo adaika pakati panu chikondi ndi chisoni. Ndithu mzimenezi muli zizindikiro kwa anthu amene amalingalira

    [22] “Ndipo zina mwa zizindikiro Zake (zosonyeza kukhoza Kwake) ndiko kulenga kwa thambo ndi nthaka ndikusiyana kwa ziyankhulo zanu ndi utoto (wa makungu anu; chikhalirecho mudalengedwa kuchokera kwa munthu m’modzi). Ndithu m’zimenezi muli zizindikiro kwa odziwa

    [23] “Ndipo zina mwa zizindikiro Zake (zosonyeza luntha Lake), ndiko kukupatsani mpumulo watulo usiku, ndi (kudzuka) usana ndi kufunafuna kwanu zabwino Zake. Ndithu m’zimenezo muli zisonyezo kwa anthu amene amamva (ndi kuthandizidwa ndikumvako)

    [24] “Ndipo zina mwa zizindikiro Zake (zosonyeza mphamvu Zake zoposa) ndiko kukusonyezani kung’anima komwe kumakuchititsani mantha, ndi kukupatsani chiyembekezero (chakudza kwa mvula). Ndipo amatsitsa madzi kuchokera kumwamba. Kotero kuti amaukitsa nthaka ndi madziwo pambuyo pa kufa kwake (nthakayo). Ndithu m’zimenezi muli zizindikiro kwa anthu ozindikira

    [25] “Ndipo zina mwa zizindikiro Zake (zosonyeza kukhoza kwake), ndiko kuti thambo ndi nthaka zaima mwa lamulo Lake. Kenako akadzakuitanani; kuitana kumodzi nthawi imeneyo inu mudzatuluka m’nthaka

    [26] “Ndipo onse akumwamba ndi a pa dziko lapansi, Ngake. Onse amamvera Iye

    [27] “Ndipo Iye ndiamene adayambitsa zolengedwa. Ndipo ndi Yemwe adzazibwerezenso (kachiwiri). Ndipo kuzibwerezako, nkosavuta kwa Iye, ndipo ali ndi mbiri yabwino kumwmba ndi pansi. Ndiponso Iye Ngwamphamvu zoposa Ngwanzeru zakuya

    [28] “Wapereka kwa inu fanizo la chikhalidwe chanu. Kodi (akapolo) amene manja anu akumanja apeza ali ndi gawo pa chuma chimene takupatsani kotero kuti mumagawana chimenecho molingana? Kodi mumawaopa monga momwe muoperana wina ndi mzake? (Nanga nchotani inu kuti mumuyese Allah kuti ali ndi amzake mwa akapolo Ake?) Umo ndimomwe tikulongosolera Ayah (ndime Zathu) kwa anthu ozindikira

    [29] “Koma amene adadzichitira zoipa okha, atsata zofuna zawo popanda kudziwa. Kodi ndiyani angamulungamitse amene Allah wamsiya kuti asokere (chifukwa chakusafuna kwake kuongoka)? Ndipo iwo sadzakhala ndi apulumutsi

    [30] “Choncho lunjika nkhope yako ku chipembedzo moyenera; (pewa kusokera kwa okana Allah. Dzikakamize ku) chilengedwe chimene Allah adalengera anthu. (Ichi nchipembedzo cha Chisilamu chomwe nchoyenerana ndi chilengedwe cha munthu). Palibe kusintha m’kalengedwe ka zolengedwa za Allah. Ichi ndi chipembedzo choona (cholungama). Koma anthu ambiri sadziwa

    [31] “(Lunjikani nkhope zanu) modzichepetsa kwa Iye ndipo muopeni (potsatira malamulo Ake). Pempherani Swala moyenera, ndipo musakhale mwa opembedza mafano

    [32] “Mwa omwe agawa chipembedzo chawo nkukhala mipatukomipatuko; gulu lililonse likusangalalira chomwe lili nacho

    [33] “Ndipo mavuto akawakhudza anthu, amampempha Mbuye wawo modzichepetsa kwa Iye. Kenako akawalawitsa mtendere wochokera kwa Iye, pamenepo ena a iwo amamuphatikiza Mbuye wawo (ndi mafano)

    [34] “Posathokoza zimene tawapatsa. Choncho sangalalani (ndi zimene mukuzifunazo); posachedwapa mudziwa (kuipa kwake)

    [35] “Kodi kapena tidawatsitsira umboni womwe ukufotokoza zomwe adali kumuphatikiza nazo Iye (Allah)

    [36] “Ndipo anthu tikawalawitsa mtendere, amausangalalira. Koma choipa chikawapeza, chifukwa cha zomwe manja awo atsogoza, pamenepo iwo amataya mtima (kuti sangapezenso zabwino za Allah)

    [37] “Kodi saona kuti Allah amamchulukitsira rizq yemwe wamfuna, ndi kumchepetsera (yemwe wamfuna)? Ndithu m’zimenezi, muli zisonyezo kwa anthu okhulupirira

    [38] “Choncho mpatseni gawo lake wachibale, m’mphawi ndi wapaulendo (amene alibe chokamfikitsa kwawo). Zimenezo nzabwino kwa amene akufuna chiyanjo cha Allah, ndipo iwo ndiwo opambana

    [39] “Ndipo chuma chimene mukupatsana m’njira yamphatso kuti chichuluke m’chuma cha anthu, kwa Allah sichichuluka. Koma (chuma) chimene mukuchipereka m’njira ya Zakaat uku mukufuna chiyanjo cha Allah (chimachuluka). Iwowo ndi amene adzapeza mphoto yochuluka

    [40] “Allah ndi Yemwe adakulengani. Kenako adakupatsani (zokuthandizani kuti mukhale ndi moyo). Kenako adzakupatsani imfa (kuti mulowe m’manda). Ndipo kenako adzakuukitsani (kuti mukaweruzidwe pa zomwe mumachita). Kodi mwa amene mukuwaphatikiza (ndi Allah), alipo yemwe angachite chilichonse m’zimenezi? Wayera Iye (Allah) ndipo watukuka ku zimene akumphatikiza

    [41] “Chisokonezo chaonekera pamtunda ndi panyanja chifukwa cha zimene manja a anthu achita, kuti awalawitse (chilango cha) zina zomwe adachita; kuti iwo atembenukire (kwa Allah)

    [42] “Nena: “Yendani padziko ndi kuyang’ana momwe adalili mathero a omwe adalipo kale. Ambiri a iwo adali ophatikiza (Allah ndi mafano).”

    [43] “Choncho lunjika nkhope yako ku chipembedzo choongoka lisadadze tsiku losabwezedwa lochokera kwa Allah. Tsiku limenelo (anthu) adzagawikana, (abwino akalowa ku Munda wamtendere, pomwe oipa akalowa ku Moto)

    [44] “Amene sanakhulupirire, kuipa kwa kusakhulupirira kwake kuli pa iye (mwini). Ndipo amene achita zabwino iwo akudzikonzera okha (zabwino)

    [45] “Kuti awalipire zabwino Zake amene akhulupirira ndi kuchita zabwino. Ndithu Iye sakonda akafiri (osakhulupirira)

    [46] “Ndipo zina mwa zisonyezo Zake (zosonyeza mphamvu Zake ndi chifundo Chake) ndiko kutumiza mphepo yodza ndi nkhani yabwino (yakuti mvula ivumba) ndi kuti akulawitseni chifundo Chake, ndi kuti zombo ziyende (panyanja) mwa lamulo Lake, ndi kuti mufunefune zabwino Zake ndi kutinso muthokoze (mtendere Wake pomumvera ndi kumpembedza Iye Yekha)

    [47] “Ndipo, ndithu tidatuma aneneri kwa anthu awo patsogolo pako. Choncho (mneneri aliyense) adawadzera anthu ake ndi maumboni oonekera poyera (osonyeza kuona kwawo, koma adawakana). Tero tidawawononga amene adalakwa. Ndikofunika kwa Ife kupulumutsa okhulupirira

    [48] “Allah ndiyemwe akutumiza mphepo yomwe imagwedeza mitambo mwamphamvu, ndipo akuibalalitsa kumwamba mmene akufunira. Amaigawa zigawozigawo (kufikira) uyiona mvula ikutuluka mkati mwake (mitamboyo). Ndipo (Allah) akaitsitsa kwa amene wamfuna mwa akapolo Ake, pamenepo iwo amakondwa ndi kusangalala

    [49] “Ngakhale kuti isadawatsikire, adali otaya mtima (ndi kutekeseka kwambiri)

    [50] “Choncho, yang’ana (molingalira) zizindikiro za chifundo cha Allah momwe akuukitsira nthaka (pomeretsa mmera) pambuyo pa imfa yake. Ndithu Iye Ngoukitsa akufa. Ndipo Iye Ngokhoza chilichonse (palibe chokanika kwa Iye)

    [51] “Ndipo, ndithu tikaatumizira mphepo (yoononga mmera) nkuuona pambuyo pake uli wachikasu, akadakhala akupitiriza kukana (Allah chifukwa chokwiyitsidwa ndi zimenezi)

    [52] “(Usadandaule ndi makani awo). Ndithu iwe sungachititse kuti amve akufa (kuitana kwako). Ndiponso sungachititse kuti amve agonthi kuitana pamene akutembenukira nakuyang’anitsa msana (osafuna kumva mawu ako)

    [53] “Ndipo iwe sungathe kuwaongolera akhungu m’kusokera kwawo. Sungachititse kuti amve koma okhawo amene akhulupirira Ayah Zathu. Iwowo ndiwo odzipereka

    [54] “Allah ndi Yemwe adakulengani kuchokera mkufooka; kenako adakupatsani mphamvu pambuyo pakufooka, ndipo pambuyo pamphamvu adakupatsani kufooka ndi imvi, (Iye) akulenga chimene wafuna. Ndipo Iye Ngodziwa kwambiri, Ngokhoza chilichonse

    [55] “Ndipo tsiku limene chiweruziro (Qiyâma) chidzachitika, oipa adzakhala akulumbira (kuti) sadakhale (pa dziko lapansi kapena mmanda) koma ola limodzi. Umo ndimomwe amatembenuzidwira (kuchokera ku njira ya choonadi)

    [56] “Ndipo amene apatsidwa nzeru ndi chikhulupiliro, adzanena: “Ndithu inu mudakhala m’chilamulo cha Allah kufikira tsiku louka ku imfa; choncho ili ndi tsiku louka ku imfa koma inu simunali kudziwa.”

    [57] “Choncho tsiku limenelo, madandaulo a omwe adzichitira chinyengo sadzawathandiza ndipo sadzafunsidwa kuti amukondweretse Allah (ndi kulapa kwawo)

    [58] “Ndipo ndithu tawapatsa anthu mafanizo a mtundu uliwonse m’Qur’an iyi. Ndipo, ndithu ukawabweretsera mtsutso uliwonse, anena omwe sadakhulupirire: “Inu sikanthu, koma ndinu anthu ochita zachabe.”

    [59] “Mmenemo ndi momwe Allah akudindira (chidindo) m’mitima mwa amene sazindikira

    [60] “Choncho pirira (iwe Mtumiki ku masautso awo). Ndithu lonjezo la Allah, nloona, ndipo asakugwetse mphwayi amene alibe chikhulupiriro chotsimikizika

    Luqman

    Surah 31

    [1] “Alif-Lâm-Mîm

    [2] “Izi ndi Ayah za buku lodzadza ndi nzeru

    [3] “(Lomwe ndi) chiongoko ndi chifundo kwa ochita zabwino

    [4] “Amene akupemphera Swala moyenera ndi kupereka chopereka (Zakaat) omwenso akutsimikiza za tsiku lachimaliziro

    [5] “Iwowo ali pa chiongoko chochokera kwa Mbuye wawo; ndipo iwowo ndiwo opambana

    [6] “Koma alipo ena mwa anthu amene akusankha nkhani ya bodza (ndi kumaifotokoza kwa anthu) ndi cholinga choti awasokeretse ku njira ya Allah popanda kuzindikira. Ndipo akuichitira zachipongwe (njira ya Allah yi). Iwo adzapeza chilango chowasambula

    [7] “Ndipo pamene Ayah Zathu zilakatulidwa kwa iye, akuzitembenuzira msana modzikuza ngati kuti sanazimve, ngati kutinso m’makutu mwake muli ugonthi. Choncho muuze nkhani ya chilango chopweteka

    [8] “Ndithu amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, adzakhala ndi Minda yamtendere

    [9] “Adzakhala m’menemo nthawi yaitali. Ili nlonjezo la Allah lomwe lili loona. Ndipo Iye Ngwamphamvu, Ngwanzeru zakuya

    [10] “Adalenga thambo popanda mizati yomwe mukuiona. Ndipo adaika mapiri m’nthaka kuti isakugwedezeni. Ndipo (Iye) adafalitsa nyama m’menemo zamitundu yosiyanasiyana. Ndipo tidatsitsa madzi kuchokera ku mitambo, choncho tidameretsa m’menemo (m’nthaka) mmera wokongola wamitundu yosiyanasiyana

    [11] “Izi (zonse) nzolengedwa za Allah. Choncho, tandisonyezani, nchiyani adalenga amene sali Allah. Koma odzichitira okha zoipa ali mkusokera koonekera

    [12] “Ndipo ndithu tidampatsa Luqmân nzeru (ndipo tidati kwa iye): “Thokoza Allah (pazimene wakupatsa).” Ndipo, amene athokoze, ndithu kuthokozako kumthandiza yekha, ndiponso amene akana (mtendere wa Allah pakusiya kuthokoza), ndithu Allah Ngwachikwanekwane, Ngotamandidwa

    [13] “Ndipo (akumbutse) pamene Luqmân adauza mwana wake akumulangiza: “E iwe mwana wanga! Usaphatikize Allah ndi mafano. Ndithu kumuphatikiza (Allah), ndi kuipitsa kwakukulu.”

    [14] “Ndipo tamulangiza munthu kwa makolo ake (kuwachitira zabwino), mayi wake adatenga pathupi pake mofooka pamwamba pakufooka. (Adamuyamwitsa) ndi kumusiyitsa patapita zaka ziwiri, kuti: “Ndithokoze Ine ndi makolo ako, kwa Ine nkobwerera.”

    [15] “Ndipo (makolo ako) ngati atakukakamiza kuti undiphatikize Ine ndi zomwe iwe sukuzidziwa, usawamvere; koma khala nawo pa dziko mwaubwino; ndipo tsatira njira ya amene atembenukira kwa Ine. Ndipo kenako kobwerera kwanu nkwa Ine. Choncho ndidzakuuzani zimene mudali kuchita

    [16] ““E iwe mwana wanga! Ndithu icho (chabwino ndi choipa cha munthu) ngakhale chitakhala cholemera ngati njere ya mpiru ndi kukhala mkati mwa thanthwe kapena m’kati mwa thambo, kapena mkati mwa nthaka, Allah adzachibweretsa (ndi kumulipira amene adachita). Ndithu Allah Ngodziwa zinthu zobisika, (ndiponso) Ngodziwa zinthu zoonekera.”

    [17] ““E iwe mwana wanga! Pemphera Swala moyenera, lamula zabwino, letsa zoipa, ndipo pirira ndi masautso amene akukhudza. Ndithu zimenezo ndizinthu zofunika kuziikirapo mtima (munthu aliyense).”

    [18] ““Ndipo usatembenuze tsaya lako kwa anthu monyogodola, ndipo usayende pa dziko monyada. Ndithu Allah sakonda yense wodzitukumula, wonyada.”

    [19] ““Ndipo lingana m’kuyenda kwako (popanda kufulumira kwambiri kapena kuyenda pang’onopang’ono); ndipo tsitsa mawu ako, ndithu mawu oyipitsitsa ndi mawu a bulu.”

    [20] “Kodi simuona kuti Allah adakugonjetserani zakumwamba ndi zapansi ndi kukukwaniritsirani chisomo Chake, choonekera ndi chobisika? Ndipo alipo ena mwa anthu amene akukangana pa za Allah popanda kuzindikira ngakhale chiongoko, ngakhalenso buku lounika

    [21] “Ndipo akauzidwa kuti: “Tsatani zimene Allah watsitsa.” Akunena: “Koma tikutsata zimene tidawapeza nazo makolo athu.” Kodi ngakhale kuti satana akuwaitanira ku chilango cha Moto (woyaka, adzatsatirabe)

    [22] “Ndipo amene akupereka nkhope yake kwa Allah (amene akugonjera Allah kwatunthu) ali ochita zabwino, ndiye kuti wagwira chogwilira cholimba. Ndipo mapeto a zinthu zonse nkwa Allah basi

    [23] “Koma amene sadakhulupirire (Allah ndi mtima wake) choncho kusakudandaulitse kusakhulupirira kwake. Kobwerera kwawo nkwa Ife basi. Kumeneko tidzawauza zimene adachita. Ndithu Allah Ngodziwa zonse zam’zifuwa

    [24] “Tikuwasangalatsa pang’ono (apo pa dziko lapansi). Kenako tidzawakankhira ku chilango chokhwima

    [25] “Ndipo ukawafunsa: “Ndani adalenga thambo ndi nthaka?” Ndithu anena: “Ndi Allah.” Nena: “Kutamandidwa konse nkwa Allah.” Koma ambiri a iwo sadziwa

    [26] “Zonse zakumwamba ndi za pansi, nza Allah. Ndithu Allah Ngwachikwanekwane, Ngotamandidwa

    [27] “Ndipo ndithu ngakhale mitengo yonse ili m’nthaka ikadakhala zolembera, ndipo nyanja (nkukhala inki), ndipo pambuyo pake ndikuionjezeranso (madzi ake) ndi nyanja zisanu ndi ziwiri, mawu a Allah sakadatha. Ndithu Allah Ngwamphamvu, Wanzeru zakuya

    [28] “Kulengedwa kwanu, ngakhale kuukitsidwa kwanu m’manda sikuli kanthu koma kuli ngati (kulenga kapena kuukitsa kwa) munthu mmodzi. (Palibe chokanika kwa Allah). Ndithu Allah Ngwakumva, Ngopenya chilichonse

    [29] “Kodi suona (kuona kolingalira) kuti Allah amalowetsa nthawi ya usiku mu usana, ndipo amalowetsa nthawi ya usana mu usiku; ndipo adagonjetsa dzuwa ndi mwezi. Chilichonse chikuyenda mwa nthawi imene idaikidwa? Ndithu Allah akudziwa zonse zimene mukuchita

    [30] “Izi nchifukwa chakuti Allah, Iye Ngoona; ndipo zomwe akuzipembedza kusiya Iye, nzachabe. Ndipo ndithu Allah ndiye Wotukuka, Wamkulu

    [31] “Kodi suona kuti zombo zikuyenda pa nyanja mwachisomo cha Allah kuti akusonyezeni zisonyezo Zake (zamtendere Wake)? Ndithu M’zimenezo muli zisonyezo kwa yense wopirira, wothokoza

    [32] “Ndipo mafunde onga mitambo akawavindikira, amampempha Allah modzipereka kwambiri. Koma akawapulumutsira ku ntunda, ena a iwo amachita zolungama (koma ena a iwo amakana mtendere wa Allah). Ndipo sangazikane zisonyezo zathu koma yense wachinyengo wosathokoza

    [33] “E inu anthu! Muopeni Mbuye wanu (potsatira malamulo Ake ndi kusiya zoletsedwa); ndipo liopeni tsiku limene kholo silidzathandiza mwana wake, ngakhalenso mwana sadzathandiza kholo lake chilichonse. Ndithu lonjezo la Allah ndiloona; choncho usakunyengeni moyo wa dziko lapansi, ndiponso asakunyengeni mdyerekezi pa za Allah

    [34] “Ndithu kudziwa kwa nthawi (yakutha kwa dziko) kuli ndi Allah (Yekha). Iye ndiamene amavumbitsa mvula (nthawi imene wafuna); ndipo akudziwa zimene zili m’ziberekero. Ndipo aliyense sadziwa chomwe apeze mawa; (chabwino kapena choipa); ndiponso sadziwa aliyense kuti ndi dziko liti adzafera. Ndithu Allah Ngodziwa zedi, Ngozindikira kwambiri

    Kugwada

    Surah 32

    [1] “Alif-Lâm-Mîm

    [2] “Chivumbulutso cha buku (la Qur’an) chilibe chikaiko mkati mwake chochokera kwa Mbuye wa zolengedwa

    [3] “Kapena akunena kuti: “Walipeka yekha (bukulo)?” Iyayi, ichi nchoona chimene chachokera kwa Mbuye wako kuti uwachenjeze anthu ndi chimenechi, amene sadawadzere mchenjezi iwe usadadze. Kuti aongoke (ndi kutsatira njira yolungama)

    [4] “Allah ndi Yemwe adalenga thambo ndi nthaka ndi zapakati pake m’masiku asanu ndi limodzi; kenako adakhazikika pa Arsh (Mpando Wake wachifumu); (kukhazikika kolingana ndi ulemelero Wake, kumene Iye Mwini wake akukudziwa). Inu mulibe mtetezi ngakhale muomboli kupatula Iye. Nanga kodi bwanji simulingalira

    [5] “(Iye) akuyendetsa zinthu (zonse) kuchokera kumwamba kupita pansi. Kenako zidzakwera kubwerera kwa Iye, pa tsiku lolingana ndi zaka chikwi chimodzi (poyerekeza ndi zaka zadziko lapansi) mzomwe inu mumawerengera

    [6] “Ameneyo (ndi Allah), Wodziwa zobisika ndi zoonekera; Mwini mphamvu zoposa Wachisoni chosatha

    [7] “Yemwe adakonza bwino chilichonse (chomwe) adalenga. Ndipo adayambitsa chilengedwe cha munthu (Adam) kuchokera ku dongo

    [8] “Kenako adachita mbumba yake kuti ipangike kuchokera m’madzi enieni onyozeka

    [9] “Kenako adamkonza ndi kuuziramo mzimu Wake. Ndipo adakuikirani kumva, kupenya ndi mitima. Kuthokoza kwanu mpang’ono ndithu

    [10] “Ndipo (otsutsa kuuka ku imfa) akunena: “Kodi tikadzatayika m’nthaka (ndi kusakanikirana ndi dothi), tidzakhalanso mkalengedwe katsopano?” (Iyayi), koma iwo sakhulupirira za kukumana ndi Mbuye wawo

    [11] “Nena: “Adzachotsa mizimu yanu Mngelo wa imfa yemwe wapatsidwa udindo umenewu pa inu. Kenako mudzabwerera kwa Mbuye wanu.”

    [12] “Ndipo ukadawaona oipa atazolikitsa mitu yawo kwa Mbuye wawo (uku akunena): “E Mbuye wathu! Taona, ndipo tamva. Choncho tibwezeni tikachita ntchito zabwino. Ndithu tsopano tatsimikiza (kukhulupirira).”

    [13] “Ndipo tikadafuna, tikadaupatsa mzimu ulionse chiongoko chake (moukakamiza monga momwe tidawachitira angelo, koma mzimu udapatsidwa mphamvu ndi ufulu wodzisankhira chimene ufuna; chabwino kapena choipa). Koma mawu atsimikizika ochokera kwa Ine: “Ndithu ndizadzazitsa Jahannam ziwanda ndi anthu; onse pamodzi (amene ali oipa).”

    [14] ““Choncho, lawani chifukwa cha kuyiwala (kusalabadila) kwanu kukumana ndi tsiku lanu ili. Ifenso tikusiyani (ku chilango monga ngati takuiwalani). Tero lawani chilango chamuyaya, chifukwa cha zomwe munkachita.”

    [15] “Ndithu amene akukhulupirira Ayah Zathu, ndiamene akuti pamene akukumbutsidwa ndi Ayazo, amagwetsa nkhope zawo pansi (kusujudu) ndi kulemekeza Mbuye wawo pamodzi ndi kumthokoza. Ndipo iwo sadzitukumula

    [16] “Nthiti zawo zimalekana ndi malo ogona (usiku), uku akumpempha Mbuye wawo, moopa ndi mwachiyembekezo. Ndipo amapereka (Zakaat ndi sadaka) mzimene tawapatsa

    [17] “Mzimu uliwonse sudziwa zimene aubisira zotonthoza diso (zosangalatsa moyo ku Munda wa mtendere) monga mphoto pa zimene unkachita

    [18] “Kodi yemwe ali okhulupirira angafanane ndi wotuluka m’chilamulo cha Allah? Sangafanane

    [19] “Tsono amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, adzalandira Minda yokhalamo yokongola, monga phwando lawo pa zimene ankachita

    [20] “Koma kwa amene adachita zoipa potuluka m’chilamulo cha Allah, malo awo ndi ku Moto. Nthawi iliyonse akafuna kutulukamo, azikabwezedwamo ndipo azidzauzidwa: “Lawani chilango cha Moto, chomwe munkachitsutsa.”

    [21] “Ndipo ndithudi, tiwalawitsa chilango chocheperapo (pa dziko lapansi) chisanafike chilango chachikulu (cha tsiku lachimaliziro), kuti atembenuke, (alape)

    [22] “Kodi ndani wachinyengo kwambiri, woposa yemwe akukumbutsidwa Ayah za Mbuye wake, kenako nkuzikana? Ndithu Ife, tidzawabwezera zoipa anthu oipa

    [23] “Ndipo ndithu Mûsa tidampatsa buku. Choncho usakhale ndi chikaiko pa zakukumana Naye (Allah). Ndipo tidalichita (bukulo) kukhala chiongoko cha ana a Israyeli

    [24] “Ndipo ena mwa iwo tidawachita kukhala atsogoleri oongola (anthu) mwa lamulo lathu, pamene adapirira; ndipo adali kuvomereza motsimikiza Ayah Zathu

    [25] “Ndithudi Mbuye wako ndi Yemwe adzaweruze pakati pawo tsiku la Qiyâma pazimene amatsutsana

    [26] “Kodi sizidadziwike kwa iwo kuti ndimibadwo ingati imene tidaiononga patsogolo pawo; (chikhalirecho iwo) akudutsa mokhala mwawo? Ndithu m’zimenezo, muli zizindikiro, kodi sakumva

    [27] “Kodi sakuona kuti timapereka madzi ku nthaka youma; ndipo ndi madziwo tikumeretsa mrnera umene ziweto zawo zimadya ndi iwo omwe; kodi sakupenya

    [28] “Ndipo akunena: “Kulamulidwa kumeneku (kwa tsiku la chimaliziro) kudzachitika liti, ngati mukunenadi zoona?”

    [29] “Nena: “Tsiku la chiweruzirolo, amene sadakhulupirire, chikhulupiriro chawo sichidzawathandiza. Ndipo sadzapatsidwa nthawi yoyembekezera (kuti mizimu yawo isachoke ayambe akhulupirira kaye, mngero wa imfa akadzawadzera).”

    [30] “Choncho apatuke; ndipo yembekezera (zimene Allah wakulonjeza). Ndithu nawonso akuyembekezera (zimene Allah wawalonjeza)

    Magulu Ankhondo ophatikizana

    Surah 33

    [1] “E iwe Mneneri! Muope Allah, ndipo usamvere osakhulupirira ndi achiphamaso. Ndithu Allah Ngodziwa kwambiri; Wanzeru zakuya (m’zoyankhula ndi m’zochita Zake)

    [2] “Ndipo tsata zimene zikuvumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako (pozigwiritsa ntchito). Ndithu Allah Ngodziwa zonse zimene mukuchita

    [3] “Ndipo yadzamira kwa Allah; ndipo Allah akukwana kukhala Msungi ndi Mtetezi (wako)

    [4] “Allah sadaike m’chifuwa cha munthu mitima iwiri. Ndipo sadachite akazi anu amene mukuwayesa ena mwa iwo monga amayi anu, kukhala mayi anu enieni. Ndipo sadachite ana anu ongowalera kukhala ana anu enieni (monga inu mukuwatchulira). Zimenezo ndi zolankhula zanu za pakamwa panu chabe. Koma Allah akunena choona; Iye akuongolera ku njira yoongoka

    [5] “Aitaneni ndi maina a atate awo. Kutero ndichilungamo kwa Allah. Koma ngati simukuwadziwa atate awo, (aitaneni ngati) ndiabale anu pachipembedzo; ndiponso ndi anzanu. Palibe uchimo kwa inu pa zimene mwazichita molakwitsa (mosazindikira). Koma (pali uchimo) pa zimene mitima yanu yachita mwadala. Ndipo Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha

    [6] “Mneneri ngofunika kwambiri kwa okhulupirira kuposa moyo wawo, (matupi awo ndi chuma chawo); ndipo akazi ake ndi amayi awo (amayi a Asilamu; nkoletsedwa kuwakwatira pambuyo pa imfa yake). Ndipo achibale pakati pawo ngoyenera (kulandira zamasiye pamalamulo a) m’buku la Allah kuposa Asilamu ena ngakhalenso Amuhajirina (amene adasamuka ku Makka kupita ku Madina chifukwa cha chipembedzo cha Chisilamu). Kupatula ngati mutachita zabwino kwa anzanu (sikolakwika). Izi zidalembedwa kale m’buku

    [7] “Ndipo (akumbutse) pamene tidalandira kuchokera kwa Aneneri onse pangano lawo. Ndi kwa iwe, ndi kwa Nuh, Ibrahim, Mûsa, ndi Isa (Yesu) mwana wa Mariya. Ndipo tidatenga kwa iwo pangano lamphamvu (kuti adzafikitsa uthenga wa Allah kwa anthu ndi kuitanira anthu ku chipembedzo cha Allah)

    [8] “Kuti (Allah) adzafunse owona (aneneri) (tsiku la chimaliziro) pa zimene adanena (kwa anthu awo zakufikitsa uthenga woonadi kwa iwo). Ndipo Allah wawakonzera (osakhulupirira) chilango chopweteka

    [9] “E inu amene mwakhulupirira! Kumbukirani chisomo cha Allah chimene chili pa inu, pamene adakudzerani magulu a nkhondo. Ndipo tidawatumizira mphepo ndi magulu a nkhondo (a angelo) amene simudawaone. Ndipo Allah akuona (zonse) zimene mukuchita

    [10] “Pamene adakudzerani cha kumtunda kwanu, ndi kunsi kwanu (kumtunda kwa dambo ndi kumunsi kwake), pamene maso adangoti tong’oo chammbali ndipo mitima idafika kum’mero (chifukwa cha mantha ndi kunjenjemera) uku mukumganizira Allah maganizo osiyanasiyana

    [11] “Panthawi imeneyo okhulupirira adayesedwa mayeso aakulu. Adanjenjemeretsedwa kunjenjemera kwambiri

    [12] “Ndipo pamene ankanena achiphamaso (achinyengo) ndi omwe m’mitima mwawo muli matenda: “Palibe chomwe adatilonjeza Allah ndi Mtumiki Wake koma chinyengo basi.”

    [13] “Ndipo pamene gulu lina mwa iwo lidanena: “E inu nzika za mu Yathiriba (Madina)! Palibe njira kwa inu yokhalira (pa nkhondo yogonjayi). Choncho bwererani (ku nyumba zanu; msiyeni Muhammad alimbane yekha ndi adani ake).” Ndipo gulu lina la nkhondo lochokera mwa iwo limapempha chilolezo kwa Mneneri (s.a.w) ( chobwelera ku Madina) ponena (kuti): “Ndithu nyumba zathu nzamaliseche (zopanda chitetezo).” Koma izo sizamaliseche. Sakufuna china, koma kuthawa basi

    [14] “Ndipo akadawalowera (magulu ankhondo a adaniwo), mbali zonse (za Mzindawo), kenako nkupemphedwa kuti atuluke m’Chisilamu ndi kumenyana ndi Asilamu, akadachita zimenezo; ndipo sakadayembekezera koma nthawi yochepa basi

    [15] “Ndipo ndithu (awa amene adathawa pabwalo la nkhondo), adali atamulonjeza kale Allah (kuti iwo) sadzatembenuza misana (kuthawa). Ndipo lonjezo la Allah nlofunsidwa. (Choncho iwo adzafunsidwa pa zomwe adalonjeza kwa Allah)

    [16] “Nena: “Kuthawa sikungakuthandizeni ngati mukuthawa imfa kapena kuphedwa; choncho (kuthawa kwanuku) simusangalatsidwa (nako) koma pang’ono basi. (Kenako ikatha nthawi ya moyo wanu, mukufa).”

    [17] “Nena: “Kodi ndani amene angakutetezeni kwa Allah, ngati atafuna kukuchitirani choipa; kapena atafuna kukuchitirani chifundo?” Ndipo sadzapeza mthandizi ndi mtetezi kupatula Allah

    [18] “Ndithu Allah akuwadziwa amene akudziletsa mwa inu (kupita ku nkhondo pamodzi ndi Mtumiki (s.a.w) ndi kuletsanso anthu ena), ndi amene akuuza abale awo: “Bwerani kwa ife; (m’thaweni Muhammad {s.a.w}).” Ndiponso sapita ku nkhondo koma pang’ono pokha

    [19] “Okuchitirani inu umbombo (pa chikondi ndi pa chifundo; sakufunirani zabwino). Koma mantha akadza uwaona akukuyang’ana, uku maso awo akutembenuka (mophethiraphethira) monga a amene wakomoledwa ndi imfa. Koma mantha akachoka, akukupatsani masautso ndi malirime awo akuthwa; mbombo pa chabwino chilichonse. Iwowo sadakhulupirire ndipo choncho Allah wagwetsa malipiro a zochita zawo. Zimenezo nzosavuta kwa Allah

    [20] “(Kufikira tsopano chifukwa cha mantha awo) akuganiza kuti magulu a nkhondo (adani) sadapitebe; ndipo magulu amenewo akadadzanso, akadalakalaka akadakhala kuchipululu pamodzi ndi arabu a kuchimidzi ndi kuti azikangofunsa za nkhani zanu. Akadakhala pamodzi ndi inu sadakamenyana (ndi adani) koma pang’ono pokha

    [21] “Ndithu muli nacho chitsanzo chabwino mwa Mthenga wa Allah (m’kudzipereka kwake ndi khama lake pa njira ya Allah, ndi kupirira kwake ndi masautso) kwa yemwe akuopa Allah ndi tsiku lachimaliziro, namatchula Allah kwambiri

    [22] “Ndipo pamene okhulupirira adaona magulu a nkhondo (a adani atawazinga mbali zonse), adati: “Ichi ndichimene Allah ndi Mtumiki Wake adatilonjeza (kuti tidzapeza masautso, kenako nkupambana), ndipo Allah ndi Mtumiki Wake adanena zoona.” Ndipo (ichi) sichidawaonjezere china, koma chikhulupiliro (mwa Allah) ndi kudzipereka

    [23] “Mwa okhulupirira alipo amuna ena amene adakwaniritsa zomwe adamlonjeza Allah (kuti sadzathawa pa nkhondo pamodzi ndi Mtumiki (s.a.w), ena mwa iwo adamaliza moyo wawo (nakwaniritsa lonjezo lawo pofera pa njira ya Allah). Ndipo ena mwa iwo akuyembekezerabe (kufera pa njira ya Allah). Ndipo sadasinthe konse (lonjezo lawo)

    [24] “Kuti Allah awalipire owona chifukwa cha kuona kwawo; ndi kuti awalange achiphamaso ngati atafuna, kapena kuwalandira kulapa kwawo (ngati atalapa). Ndithu Allah Ngokhululuka kwabasi Ngwachisoni chosatha

    [25] “Ndipo Allah adawabweza amene sadakhulupirire uku ali odzazidwa ndi mkwiyo m’mitima mwawo; sadapeze chabwino; (sadagonjetse Asilamu ndi kupeza zimene ankaziyembekezera monga zotola za pa nkhondo). Ndipo Allah adawakwaniritsira okhulupirira nkhondo (powatumizira adani mphepo yamkuntho ndi angelo). Ndipo, Allah Ngwamphamvu, Ngopambana, (sapambanidwa ndi chilichonse)

    [26] “Ndipo adawatsitsa m’malinga mwawo amene adathandiza adaniwo mwa anthu a buku (Ayuda). Ndipo adathira mantha m’mitima mwawo. Ena mumawapha; ndipo ena mumawagwira

    [27] “Ndipo adakupatsani dziko lawo, nyumba zawo, chuma chawo, ndi nthaka imene simudaipondepo. Allah Ngokhoza chilichonse

    [28] “E iwe Mneneri! Nena kwa akazi ako (m’njira yowalangiza): “Ngati mufuna moyo wa dziko lapansi ndi zosangalatsa zake (ine ndilibe zosangalatsa za m’dziko, ndipo sindingakukakamizeni kuti mukhale ndi ine mu moyo wa umphawi; ngati mufuna) bwerani ndikupatsani cholekanira, chokusangalatsani, kenako ndikusiyeni kusiyana kwabwino (kopanda masautso).”

    [29] ““Ndipo ngati mukufuna Allah ndi Mtumiki Wake, ndi nyumba yomaliza, ndithu Allah wawakonzera ochita zabwino mwa inu malipiro aakulu.”

    [30] “E inu akazi a Mneneri! Amene achite choipa choonekera mwa inu, amuonjezera chilango kawiri; ndipo zimenezi nzosavuta kwa Allah

    [31] “۞ Koma yense mwa inu amene amvere Allah ndi Mneneri Wake, ndi kumachita zabwino, timpatsa malipiro ake kawiri ndi kumkonzera rizq laulemu

    [32] “E inu akazi a Mneneri! Inu simuli monga mmodzi wa akazi ena (omwe siakazi a Mtumiki, paulemelero) ngati muopa Allah. Choncho musalobodole mawu (mowakometsa poyankhulana ndi amuna,) kuti asalakelake (kuchita zoipa ndi inu) yemwe mu mtima mwake muli matenda (achiwerewere). Koma nenani zonena zabwino

    [33] “Ndipo khalani mnyumba zanu, ndipo musadzionetsere (kwa amuna) uku mutadzikongoletsa monga mmene ankaonetsera zokongoletsa zawo (akazi) a m’nthawi ya umbuli wakale. Ndipo pempherani Swala moyenera, perekani Zakaat, mverani Allah ndi Mtumiki Wake. Ndithu Allah akufuna kukuchotserani uve e, inu a kunyumba (ya Mneneri)! Ndi kuti akuyeretseni ndithu

    [34] “Ndipo lowezani pamtima zimene zikunenedwa m’nyumba zanu; ndime za mawu a Allah ndi (zonena za Mtumiki) zanzeru. Ndithu Allah Ngodziwa zinthu zobisika kwambiri, ndi zapoyera

    [35] “Ndithu Asilamu achimuna ndi Asilamu achikazi; okhulupirira achimuna ndi okhulupirira achikazi; omvera achimuna ndi omvera achikazi; owona achimuna ndi owona achikazi; opirira achimuna ndi opirira achikazi; odzichepetsa achimuna ndi odzichepetsa achikazi; opereka sadaka achimuna ndi opereka sadaka achikazi; osala achimuna ndi osala achikazi; osunga umaliseche wawo (kuchiwerewere) achimuna ndi osunga umaliseche wawo achikazi; otamanda Allah kwambiri achimuna ndi otamanda Allah kwambiri achikazi, Allah wawakonzera chikhululuko ndi malipiro aakulu

    [36] “Ndipo sikoyenera kwa wokhulupirira wachimuna ndi wokhulupirira wachikazi, Allah ndi Mtumiki Wake akalamula chinthu, iwo nkukhala ndi chisankho pa zinthu zawo. Ndipo amene akunyoza Allah ndi Mtumiki Wake, ndithu wasokera; kusokera koonekera

    [37] “Ndipo (kumbuka) pamene udamuuza yemwe Allah adampatsa mtendere (pomuongolera ku Chisilamu, ndipo) iwenso udampatsa mtendere (pomulera ndi kumpatsa ufulu, yemwe ndi Zaid Bun Haritha, udati kwa iye): “Gwirizana ndi mkazi wako, ndipo wopa Allah.” Ukubisa mu mtima mwako chimene Allah afuna kuchisonyeza poyera (chomwe ndi kuti Allah akulamula kumkwatira mkazi ameneyo akamuleka Zaid Bun Haritha kuti chichoke chizolowezi choti mwana wongomulera chabe nkumuyesa mwana wako weniweni). Ndipo ukuopa anthu (kuti akudzudzula pa zimenezo), pomwe woyenera kumuopa ndi Allah. Choncho pamene Zaid adamaliza chilakolako chake pa mkazi ameneyo, tidakukwatitsa iwe kuti pasakhale masautso pa okhulupirira pokwatira akazi a ana awo akungowalera chabe ngati (anawo) atamaliza zilakolako zawo pa akaziwo, ndipo lamulo la Allah ndilochitika, (palibe chingalepheretse kuti lisachitike)

    [38] “Palibe tchimo pa Mneneri pa zimene Allah wamulamula. Chimenechi ndichizolowezi cha Allah (njira ya Allah) pa amene adanka kale. Ndipo lamulo la Allah ndi chikonzero (chomwe) chidakonzedwa. (Ndipo sichisinthidwa)

    [39] “(Aneneri) amene amafikitsa uthenga wa Allah (kwa anthu) uku akumuopa Iye, ndipo samamuopa aliyense koma Allah (yekha). Ndipo Allah Akukwana kukhala wowerengera (zochita za akapolo Ake)

    [40] “Muhammad (s.a.w) sali tate wa aliyense mwa amuna anu, koma iye ndi Mtumiki wa Allah, ndiponso wotsiriza mwa Aneneri. Ndipo Allah Ngodziwa chilichonse

    [41] “E inu amene mwakhulupirira! Mkumbukireni Allah; kumkumbukira kwambiri

    [42] “Ndipo mulemekezeni m’mawa ndi madzulo

    [43] “Iye ndi Amene akukuchitirani chifundo (ndi kukufunirani zabwino) nawonso Angelo Ake (akukupemphelerani kwa Allah) kuti akutulutseni mu mdima ndi kukuikani m’kuunika. Ndipo (Iye) Ngwachisoni zedi kwa okhulupirira

    [44] “Kulonjerana kwawo tsiku lokumana Naye, kudzakhala koti: “Mtendere!” Ndipo wawakonzera malipiro a ulemu

    [45] “E iwe Mneneri (wa Allah)! Ndithu Ife takutuma (kuti ukhale) mboni (pa anthu ako ndi pa mibadwo yonse). Wonena nkhani zabwino (kwa oopa Allah), ndi mchenjezi (kwa onyoza Allah)

    [46] “Ndi kuti ukhale woitanira (anthu) kwa Allah kupyolera m’chifuniro Chake. Ndi (kutinso ukhale) nyali younikira (anthu)

    [47] “Ndipo auze nkhani yabwino okhulupirira kuti iwo ali ndi zabwino zazikulu kwa Allah

    [48] “Ndipo usawamvere osakhulupirira ndi achiphamaso (pa zimene akufuna kuti uwapeputsire malamulo a Allah), usalabadire masautso awo, ndipo tsamira kwa Allah. Ndipo Allah akukwanira kukhala Mtetezi

    [49] “E inu amene mwakhulupirira! Mukakwatira akazi okhulupirira, kenako ndikulekana nawo musadawakhudze, inu mulibe chiwerengero cha ‘Edda’ pa iwo choti nkuchiwerengera. Asangalatseni powapatsa cholekanira. siyananawoni; kusiyana kwabwino

    [50] “E iwe Mneneri! Ndithu Ife takuloleza (kukhala nawo pamodzi) akazi ako amene wawapatsa chiwongo chawo, ndi chimene dzanja lako lamanja lapeza (omwe ndi akazi ogwidwa pa nkhondo) chomwe Allah wakupatsa, ndi ana achikazi a m’bale wa atate ako, ndi ana achikazi a mlongo wa atate ako, ndi ana achikazi a atsibweni ako, ndi ana achikazi a m’bale wa mayi ako amene adasamuka pamodzi ndi iwe, ndi mkazi wokhulupirira atadzipereka yekha kwa Mneneri ngati Mneneri akufuna kumkwatira, chilolezo ichi ncha iwe wekha, osati okhulupirira onse. Ndithu tikudziwa malamulo amene tawakhazikitsa kwa iwo pa akazi awo, ndi chimene manja awo akumanja apeza; (takuchitira zimenezi iwe wekha Mneneri Muhammad {s.a.w}) kuti pasakhale masautso pa iwe (ngati ukufuna kukwatira mkazi wina chifukwa chofalitsa chipembedzo) ndipo Allah Ngokhululuka kwambiri Ngwachisoni chosatha

    [51] “Ukhoza kumchedwetsa (posagona m’nyumba mwake) amene wam’funa pakati pa iwo ndi kumuyandikitsa kwa iwe amene wam’funa. Ndipo amene wam’funa mwa amene udawapatuka, palibe tchimo pa iwe. Kuchita izi kuchititsa kuti maso awo atonthole (mitima yawo ikondwe) ndipo asadandaule; ndi kuyanjana nacho chimene wawapatsa onse. Ndipo Allah akudziwa zimene zili m’mitima mwanu. Ndipo Allah Ngodziwa kwambiri, Ngoleza, (salanga mwachangu)

    [52] “Pambuyo (pa akazi awa amene uli nawo) nkosaloledwa kwa iwe kukwatira akazi ena, (poonjezera pa chiwerengero cha akazi amene uli nawo). Ndiponso usasinthe (ofanana ndi chiwerengero chawo), (zonsezi nzoletsedwa kwa iwe) ngakhale kuti ubwino wawo utakusangalatsa, kupatula chimene dzanja lako lakumanja lapeza; ndipo Allah ndi M’yang’aniri wa chinthu chilichonse

    [53] “E inu amene mwakhulupirira! Musalowe m’nyumba za Mneneri pokhapokha chilolezo chitaperekedwa kwa inu kukadya, osati kukhala nkuyembekezera kupsa kwa chakudya. Koma mukaitanidwa, lowani. Ndipo mukamaliza kudya, balalikani; ndiponso musakambe nkhani zocheza. Chifukwa kutero kumavutitsa Mneneri. Ndipo iye amakuchitirani manyazi (kuti akutulutseni); koma Allah alibe manyazi ponena choona. Ndipo inu mukamawafunsa (akazi ake) za ziwiya, afunseni uku muli kuseri kwa Chotsekereza. Zimenezo ndi zoyera zedi ku mitima yanu ndi mitima yawo. Sikoyenera kwa inu kumvutitsa Mtumiki wa Allah, ndiponso nkosayenera kwa inu kukwatira akazi ake pambuyo pa imfa yake mpaka muyaya. Ndithu kutero ndi tchimo lalikulu kwa Allah

    [54] “Chilichonse chimene mungachionetse kapena kuchibisa Allah achidziwa. Ndithu chifukwa chakuti Allah Ngodziwa chilichonse

    [55] “Palibe tchimo pa iwo (akazi) kuonana ndi atate awo ngakhale ana awo, alongo awo, ana amuna alongo awo, ana a amuna a abale awo, akazi anzawo, ndi amene manja awo akumanja apeza. Ndipo opani Allah (inu akazi). Ndithu Allah ndimboni pa chilichonse

    [56] “Ndithu Allah akumtsitsira madalitso Mneneri; nawonso angelo Ake (akumpemphelera chifukwa cha zochita zake zabwino). E inu amene mwakhulupirira! Mpemphereni madalitso ndi kumpemphera mtendere (chifukwa chokusonyezani njira yolungama)

    [57] “Ndithu amene akumukwiyitsa Allah ndi kumuvutitsa Mtumiki Wake (ponyozera malamulo ake) Allah wawatembelera pa dziko lapansi (mpaka) pa tsiku la chimaliziro, ndipo wawakonzera chilango chosambula

    [58] “Ndipo amene akuvutitsa okhulupirira aamuna ndi okhulupirira aakazi popanda kuchimwa kulikonse, ndithu asenza chinyengo ndi tchimo loonekera

    [59] “E iwe Mneneri! Uza akazi ako, ndi ana ako aakazi, ndi akazi a okhulupirira, kuti adziphimbe ndi nsalu zawo (akamatuluka m’nyumba), kutero kuchititsa kuti adziwike, asazunzidwe (ndi anthu achipongwe). Ndipo Allah Ngokhululuka kwambiri Ngwachisoni

    [60] “Ngati sasiya (machitidwe awo oipa) achiphamaso (achinyengo), ndi amene m’mitima mwawo muli matenda (a chiwerewere), ndi ofalitsa mbiri zoipa mu mzinda, tikukhwirizira kwa iwo (kuti uwathire nkhondo). Kenako sadzakhala m’menemo pamodzi ndi iwe, koma nthawi yochepa

    [61] “(Iwo) ngotembeleredwa; paliponse pamene apezeke, agwidwe ndi kuphedwa ndithu

    [62] “(Awa ndi) machitidwe a Allah omwe adalipo pa omwe adamka kale. sungapeze kusintha pa machitidwe a Allah

    [63] “Anthu akukufunsa za (kudza kwa) nthawi (ya tsiku la chitsiriziro). Nena: “Kuzindikira kwa nthawiyo kuli ndi Allah (Yekha). Nanga nchiyani chikudziwitse kuti nthawi ya chimaliziro iri pafupi?”

    [64] “Ndithu Allah wawatembelera osakhulupirira ndi kuwakonzera Moto woyaka kwambiri

    [65] “Adzakhala nrmenemo nthawi yaitali. Sadzapeza bwenzi ngakhale mthandizi

    [66] “Tsiku limene nkhope zawo zikatembenuzidwa ku Moto (zikutenthedwa), uku akunena: “Kalanga ife! Tikadamumvera Allah ndi kumveranso Mtumiki (s.a.w), (sibwenzi tili m’chilangomu).”

    [67] “Ndipo adzanena: “E Mbuye wathu! Ndithu ife tidamvera olemekezeka athu ndi akuluakulu athu, choncho adatisokeza njira.”

    [68] “Mbuye wathu! Apatseni chilango pamwamba pa chilango ndipo atembelereni, kutembelera kwakukulu.”

    [69] “E inu amene mwakhulupirira! Musakhale monga amene adamvutitsa Mûsa; koma Allah adamuyeretsa kuzimene ankamnenera. Ndipo iye kwa Allah adali wolemekezeka

    [70] “E inu amene mwakhulupirira! Opani Allah (pokwaniritsa malamulo Ake, ndi kusiya zoletsedwa), ndipo nenani mawu olungama

    [71] “Akukonzerani bwino zochita zanu ndi kukukhululukirani machimo anu. ndipo amene akumvera Allah ndi Mtumiki Wake, ndithu apambana; kupambana kwakukulu

    [72] “Ndithu Ife tidapereka udindo (otsatira malamulo) ku thambo ndi nthaka ndi mapiri; koma zidakana kuwusenza (udindowo); ndipo zidauopa. Koma munthu adawusenza; ndithu iye ngwachinyengo kwambiri ndiponso mbuli

    [73] “Kuti Allah adzawalange achiphamaso aamuna ndi aakazi, ndi opembedza mafano achimuna ndi achikazi ndi kuti adzawakhululukire okhulupirira achimuna ndi achikazi. Ndipo Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha

    Sheba

    Surah 34

    [1] “Kuyamikidwa konse ndikwa Allah Yemwe zakumwamba ndi zapansi nzake. Ndipo kutamandidwa konse pa tsiku la chimaliziro Nkwake. ndiponso Iye Ngwanzeru zakuya, Ngodziwa chilichonse

    [2] “Akudziwa zimene zikulowa m’nthaka ndi zimene zikutulukamo; ndi zimene zikutsika kumwamba ndi zimene zikukwera kumeneko. Ndipo Iye Ngwachifundo kwabasi, Ngokhululuka kwambiri

    [3] “Ndipo osakhulupirira adanena: “Siizatidzera nthawi (Qiyâma).” Nena: “Iyayi! Ndikulumbira Mbuye wanga, ndithu ikudzerani. (Mbuye wanga) Wodziwa zobisika (zonse), sichingabisike kwa Iye cholemera ngati nyelere; chakumwamba, chapansi, ngakhale chochepa kuposa chimenecho; ngakhalenso chokulirapo, koma (zonsezo) zili m’buku (Lake) losonyeza poyera (chilichonse).”

    [4] “Kuti adzawalipire amene akhulupirira ndi kuchita zabwino; iwo adzapeza chikhululuko ndi zopatsidwa zaulemu

    [5] “Koma amene alimbika kutsutsana ndi Ayah Zathu pomaganiza kuti atigonjetsa, pa iwo pali chilango chopweteka

    [6] “Koma amene apatsidwa (dalitso la) kudziwa akuzindikira kuti zimene zavumbulutsidwa kwa iwe kuchokera kwa Mbuye wako nzoona, ndipo zikuongolera ku njira ya Mwini mphamvu zoposa, Wotamandidwa

    [7] “Ndipo osakhulupirira akunena (pouzana pakati pawo mwachipongwe): “Kodi Tikusonyezeni za munthu yemwe akukuuzani kuti (m’kadzafa) ndi kudukaduka m’dzakhala m’kalengedwe katsopano?”

    [8] “(Allah akunena): “Kodi (akum’ganizira Muhammad kuti) wamupekera Allah bodza, kapena wagwidwa ndi misala? Iyayi, koma osakhulupirira za tsiku la chimaliziro adzakhala m’chilango ndi m’kusokera kwakukulu.”

    [9] “Kodi (agwidwa ndi khungu) saona zomwe zili patsogolo pawo ndi pambuyo pawo monga thambo ndi nthaka (kuti adziwe kukhoza Kwathu kuchita zimene tafuna)? Tikadafuna tikadawakwilira ndi nthaka kapena kuwagwetsera zidutswa za thambo. Ndithu m’zimenezo muli malingaliro kwa kapolo aliyense wotembenukira (kwa Allah)

    [10] “Ndithudi, Daud tidampatsa chisomo chachikulu chochokera kwa Ife. (Ndipo tidauza mapiri kuti akhale akuvomereza mapemphero a Daud pothandizana naye. Tidati): “E inu mapiri pamodzi ndi iye Daud, lemekezani (Allah), ndi inunso mbalame.” Ndipo tidamufewetsera chitsulo

    [11] “(Tidati kwa iye:) “Panga zovala (za chitsulo) zophanuka (zokwana thupi lonse, zodzitetezera pa nkhondo), ndipo linga bwino m’kulumikiza ndi poluka. Potero chitani zabwino. Ndithu Ine ndikuona zonse zimene mukuchita.”

    [12] “Nayenso Sulaiman tidamgonjetsera mphepo (yomwe inkayenda mwa lamulo lake). Mayendedwe amphepoyo inkayenda kuyambira m’mawa mpaka masana ntunda wofanana ndi waulendo wa mwezi umodzi, ndiponso kuyambira masana mpaka madzulo inkayenda ntunda wofanana ndi waulendo wa mwezi umodzi. Ndipo tidamsungunulira kasupe wa mtovu. Ndiponso m’ziwanda (majini) zidaliponso zimene tidam’gonjetsera zomwe zinkam’gwilira ntchito mwa chilolezo cha Mbuye wake (Allah). Ndipo yense mwa iwo wonyoza lamulo Lathu (posiya kumumvera Sulaiman) timulawitsa chilango cha Moto woyaka

    [13] “Ziwandazi zimampangira zimene wafuna, monga: misikiti, zithunzi zokhala ndi matupi, ndi mabeseni onga madamu ndi midenga yokhazikika. (Tidawauza:) “Chitani ntchito zabwino, E inu akubanja la Daud! Pothokoza (madalitso amene mwapatsidwa). Komatu ndiochepa othokoza mwa akapolo Anga.”

    [14] “Pamene tidalamula imfa yake (Sulaiman), palibe chimene chidawasonyeza za imfa yake koma kachirombo ka m’nthaka (chiswe) kamene kadadya ndodo yake. Choncho pamene adagwa, ziwanda zidazindikira kuti zikadakhala zikudziwa zobisika sizidakakhala m’chilango chosambulacho

    [15] “Ndithu padali phunziro pa anthu a dziko la Saba mokhala mwawo: (Padali) minda iwiri, kumanja ndi kumanzere. (Tidati:) “Idyani zakudya zaulere zochokera kwa Mbuye wanu, ndipo mthokozeni. Mudzi wabwino ndi Mbuye Wokhululuka.”

    [16] “Koma adanyozera (lamulo la Allah); choncho tidawatumizira chigumula champhamvu chamadzi otchingidwa (chomwe chidawamiza ndi kuononga minda yawo). Ndipo tidawasinthira minda yawo (yabwino) kukhala minda iwiri yazipatso zowawa, ndi mitengo ya bwemba ndi mitengo pang’ono ya masawu

    [17] “Amenewo ndiwo malipiro tidawalipira chifukwa cha kusathokoza kwawo (mtendere wa Allah). Ndipo Ife sitilipira zoterezi koma kwa okhawo osathokoza

    [18] “Ndipo pakati pawo ndi pakati pa midzi imene tidaidalitsa, tidaikapo midzi imene idali yoonekera; ndipo tidapima m’menemo malo apaulendo. (kotero kuti amachoka malo nkufika malo ena mosavutika. Tidawauza): “Yendani m’menemo usiku ndi usana mwamtendere.”

    [19] “Koma (adauda mtendere umenewu;) adati: “E Mbuye wathu! Talikitsani ntunda pakati pa maulendo athu; (kuyandikirana kwa midzi, sikukutisonyeza kuti tili pa ulendo).” Ndipo adadzichitira okha zoipa. Choncho tidawachita kukhala miyambi (imene anthu a pambuyo ankauzana pakati pawo), ndipo tidawabalalitsa; kubalalikana zedi. (Ena adathawira dziko ili, ena dziko lina). Ndithu m’zimenezo muli malingaliro kwa yense wopirira kwabasi ndi wothokoza kwambiri

    [20] “Ndipo ndithu Iblis adatsimikiza ganizo lake pa iwo choncho adamtsatira kupatula gulu la okhulupirira (moona)

    [21] “Ndipo iye adalibe nyonga pa iwo, koma chifukwa chakuti tionetse poyera ndani wokhulupirira tsiku la chimaliziro ndiponso ndani amene akulikaikira. Ndipo Mbuye wako Ngosunga chilichonse

    [22] “Nena: “Itanani amene mukuwatcha kuti ndi milungu kusiya Allah (kuti akuthandizeni. Koma sangakuthandizeni chilichonse; pakuti iwo) alibe ngakhale kachinthu ka kumwamba ndi pansi kolemera ngati nyelere yaing’ono kwambiri; m’menemo iwo alibe gawo lililonse (lothandizana ndi Allah), ndipo ngakhale Iyenso alibe mthandizi wochokera mwa iwo

    [23] “Ndipo uwomboli sudzathandiza kwa Iye (Allah) kupatula amene wamuloleza. Kufikira pamene mantha adzachotsedwa m’mitima mwawo (popatsidwa chilolezo choti apulumutse ena), adzanena pakati pawo (mosangalala): “Kodi wanena chiyani Mbuye wanu?” (Adzayankha): “Ndithu Iye wanena choona; Iye Ngotukuka Ngwamkulu.”

    [24] “Nena (kwa iwo, iwe Mneneri {s.a.w}): “Kodi ndani amakupatsani rizq (zaulere) kuchokera kumwamba ndi pansi?” (Ngati sakuyankha chifukwa chodzitukumula), nena (kwa iwo): “Ndi Allah (Mmodzi, amene akukupatsani zopatsa zaulere zochokera kumwamba ndi pansi); ndipo ife kapena inu, tili pachiongoko kapena mkusokera koonekera.”

    [25] “Nena: “Simudzafunsidwa pa zimene (ife) talakwa, nafenso sitidzafunsidwa pazimene mukuchita.”

    [26] “Nena (kwa iwo): “Mbuye wathu adzatisonkhanitsa pakati pathu (pa tsiku la chiweruziro). Kenako adzaweruza pakati pathu mwa choonadi; Iye ndi Muweruzi Wodziwa kwambiri

    [27] “Nena (kwa iwo): “Ndisonyezeni amene mwawalumikiza ndi Iye monga othandizana Naye; iyayi, sizingatheke (Iye kukhala ndi anzake), koma Iye (Yekha) ndiye Allah, Mwini Mphamvu zoposa, Wanzeru zakuya.”

    [28] “Ndipo sitidakutumize (iwe, Mtumiki{s.a.w} kwa Arabu okha) koma kwa anthu onse, kuti ukhale wouza (okhulupirira) nkhani zabwino ndi wochenjeza otsutsa. Koma anthu ambiri sadziwa (za uthenga wako)

    [29] “Eti akunena: “Nliti lidzakwaniritsidwe lonjezo ili (lakudza kwa chiweruziro) ngati mukunenadi zoona?”

    [30] “Nena: “Muli nalo pangano (lotsimikizika) la tsiku limene simungathe kulichedwetsa ngakhale ola limodzi, kapena kulifulumizitsa.”

    [31] “Ndipo amene sadakhulupirire akunena: “Sitiikhulupirira Qur’an iyi, ngakhalenso (mabuku) aja apatsogolo pake.” Ndipo ukadawaona achinyengo pamene azikaimiritsidwa pamaso pa Mbuye wawo, (ukadaona zoopsa zazikulu), uku pakati pawo akubwezerana mawu. Amene adaponderezedwa adzanena kwa amene adadzikweza: “Kukadapanda inu (kutipondereza), tikadakhala okhulupirira.”

    [32] “Amene adadzikweza adzanena kwa amene adaponderezedwa: “Ha, kodi ife tidakutsekerezani ku chiongoko chitakudzerani? Iyayi, koma mudali oipa.”

    [33] “Ndipo amene adaponderezedwa adzanena kwa amene adadzikweza: “Iyayi, koma (mumachita) ndale za usiku ndi usana (zotitsekereza nazo ku chikhulupiliro) pamene mumatilamula kuti tinkanire Allah ndikumpangira Iye milungu inzake.” Iwo adzabisa madandaulo pamene adzaona chilango. Ndipo tidzaika magoli m’makosi mwa amene sadakhulupirire; kodi angalipidwe china, osati zija ankachita

    [34] “Palibe pamene tidatuma mchenjezi m’mudzi uliwonse koma opeza bwino a m’mudzimo ankanena: “Ndithu ife tikuzikana zimene mwatumidwa nazozi.”

    [35] “Ndipo ankanena (monyada): “Ife tili ndi chuma chambiri ndi ana (amhiri); choncho ife sitidzalangidwa (pa tsiku la chimaliziro).”

    [36] “Nena: “Ndithu Mbuye wanga amamchulukitsira rizq (zopatsa) laulere amene wamfuna (ngakhale ali woipa), ndipo amamchepetsera (amene wamfuna ngakhale kuti ndi munthu wabwino). Koma anthu ambiri sazindikira (zimenezi).”

    [37] “Ndipo sichuma chanu ndi ana anu zomwe zingakuyandikitseni kwa Ife ulemelero, koma (chikhulupiliro cha) amene wakhulupirira ndi kuchita zabwino. Iwo adzapeza malipiro owonjezeka kwambiri pa zomwe adachita. Iwo adzakhala mwamtendere m’zipinda za ku Minda ya mtendere

    [38] “Ndipo amene akuchita khama kulimbana ndi zizindikiro Zathu ndi cholinga choti alepheretse (zofuna Zathu,) iwowo adzabweretsedwa ku chilango (cha Moto)

    [39] “Nena (iwe Mneneri): “Ndithu Mbuye wanga amamchulukitsira rizq (zaulere) amene wamfuna mwa akapolo Ake; ndiponso amamchepetsera (amene wamfuna). Ndipo chilichonse chimene mupereka, Iye adzakupatsani china m’malo mwake; Iye Ngwabwino popatsa zaulere, kuposa opatsa

    [40] “Ndipo (kumbuka iwe Mneneri) tsiku limene (Allah) adzawasonkhanitsa onse ndi kunena kwa angelo: “Kodi awa amapembedza inu?”

    [41] “Adzanena: “Kuyera konse Nkwanu (simungakhale limodzi ndi milungu ina!) Inu ndinu Mtetezi wathu, osati iwo. Koma amagwadira majini (ziwanda); ambiri mwa iwo (anthu) adakhulupirira izo (ziwanda).”

    [42] “(Allah adzawauza iwo:) “Lero aliyense mwa inu sangathe kudzetsa zabwino ngakhale masautso pa ena.” Ndipo tidzawauza amene adadzichitira okha zoipa: “Lawani chilango cha Moto chimene munkachitsutsa.”

    [43] “Ndipo Ayah Zathu zofotokoza momveka zikamawerengedwa kwa iwo, amanena, “Sichina uyu (Muhammad {s.a.w}) koma ndi munthu yemwe akufuna kukutsekerezani mapemphero amene amapemphera makolo anu.” Ndipo akunena: “Sichina iyi (Qur’an) koma ndibodza lopekedwa.” Ndipo amene sadakhulupirire akunena pa choona pamene chawadzera: “Sikanthu ichi, koma ndi matsenga woonekera.”

    [44] “Ndipo (ngakhale awa Arabu) sitidawapatse mabuku oti aziwawerenga (buku ili lisanadze); ndipo sitidawatumizirenso mchenjezi patsogolo pako. (Nanga akudziwa bwanji kuti Qur’an iyi ndiyonama)

    [45] “Ndipo amene adalipo iwowo kulibe, adatsutsa, ndipo (awa Arabu) sadapeze gawo limodzi m’magawo khumi a zomwe tidawapatsa iwowo, koma adatsutsa atumiki Anga (pa zomwe adawabweretsera). Nanga chidali bwanji chilango Changa (pa iwo)

    [46] “Nena: “Ndithu ndikukulangizani chinthu chimodzi, kuti muimilire chifukwa cha Allah; awiriawiri ndi mmodzimmodzi, ndipo kenako mulingalire; (muona kuti uyu Muhammad {s.a.w} chilichonse chomwe akunena nchoona. Ndiponso muona kuti) mnzanuyu alibe misala. Iye, sichina, koma ndimchenjezi wanu chisanadze chilango chaukali.”

    [47] “Nena: “Chilichonse ndakupemphani kukhala malipiro (othandizira kufikitsa uthenga kwa anthu) ndichanu, malipiro anga ali kwa Allah basi. Ndipo Iye ndi Mboni pachilichonse.”

    [48] “Nena: “Ndithu Mbuye wanga amaponya choonadi (ponseponse kotero kuti chonama chimathawa). Ngodziwa zedi (zinthu) zobisika.”

    [49] “Nena: “Choonadi chadza (chisilamu); ndipo chabodza (chipembedzo cha mafano) sichidzetsa zachilendo, ndiponso sichibwerera (kukhala ndi nyonga monga kale).”

    [50] “Nena: “Ngati ndasokera, ndiye kuti ndadzisokeretsa ndekha (ndadziyika ndekha m’mavuto). Koma ngati ndaongoka, ndichifukwa cha zimene akundivumbulutsira Mbuye wanga. Ndithu Iye Ngwakumva; ali pafupi (ndi aliyense).”

    [51] “Ndipo ukadaona pamene adzanjenjemera (akadzachiona chilango cha Allah, adzayesera kuthawa), koma sipadzapezeka pothawira, ndipo adzagwidwa pamtunda wapafupi (asanafike kutali)

    [52] “Ndipo adzanena (mophuphaphupha): “Tachikhulupirira (tsopano chipembedzo cha Chisilamu).” Koma iwo angaulandire chotani (Usilamu) kumeneko (komwe) ndikumalo akutali

    [53] “Pomwe chikhalirenicho adachikana kale (Chisilamu). Ndipo chobisika ankachigenda (ndi bodza) kuchokera kumalo akutali

    [54] “Ndipo padzatsekeka pakati pawo ndi zimene akuzilakalaka, monga momwe adachitidwira anzawo akale. Ndithu iwo adali m’chikaiko chowakaikitsa (uthenga wa Allah)

    Woyambitsa

    Surah 35

    [1] “Kuyamikidwa konse nkwa Allah (Yekha) Muumbi wa thambo ndi nthaka (popanda chofanizira), amene adachita angelo kukhala atumwi eni mapiko, awiriawiri; atatuatatu; ndi anayianayi. Amaonjezera mkulenga monga momwe afunira, (palibe chimene chingakanike kwa Iye). Ndithu Allah Ngokhoza chilichonse

    [2] “Chifundo chimene Allah angatsekule kwa anthu, palibe amene angachitsekereze. Ndipo chimene angachiletse palibe amene angachipereke kupatula Iye. Ndipo Iye ndi Mwini mphamvu zoposa, Wanzeru zakuya

    [3] “E inu anthu! Kumbukirani chisomo cha Allah chomwe chili pa inu (pomthokoza). Kodi alipo Mlengi wina osati Allah amene angakupatseni rizq kuchokera kumwamba ndi pansi? Palibe wina wopembedzedwa mwachoonadi, koma Iye. Nanga mukutembenuzidwira kuti

    [4] “Ndipo ngati angakutsutse ndithu adatsutsidwanso atumiki amene adalipo patsogolo pako. Ndipo zinthu zonse zidzabwezedwa kwa Allah

    [5] “E inu anthu! Ndithu lonjezo la Allah ndi loona. Choncho usakunyengeni moyo wa dziko lapansi, ngakhale mdyerekezi uja wamkulu (Iblis), asakunyengeni pa za Allah

    [6] “Ndithu satana ndi mdani wanu; choncho mchiteni kukhala mdani. Iye amaliitanira gulu lake kuti likhale gulu la anthu a ku Moto

    [7] “Amene sadakhulupirire (Allah ndi Mtumiki Wake), pa iwo padzakhala chilango chaukali; koma amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, iwo adzapeza chikhululuko ndi malipiro aakulu

    [8] “Kodi amene zochita zake zoipa zakometsedwa kwa iye nkumaziona kuti nzabwino, (ngolingana ndi amene waongoka ndi chiongoko cha Allah kotero kuti chabwino nkuchiyesa chabwino; choipa nkuchiyesa choipa?) Ndithu Allah akumlekelera kuti asokere yemwe wamfuna (chifukwa chakuti safuna kuongoka), ndipo akuongola amene wam’funa. Choncho moyo wako usaonongeke chifukwa chowadandaula iwo. Ndithu Allah Ngodziwa zonse zimene (iwo) akuchita

    [9] “Ndipo Allah ndiamene amatumiza mphepo; choncho imagwedeza mitambo (ya mvula) ndipo timaifikitsa ku dziko lakufa. Ndipo kupyolera m’madzi otuluka mmitamboyo; timaiwukitsa nthaka pambuyo pakufa kwake, momwemonso ndimmene kudzakhalira kutuluka akufa (m’manda tsiku la chiweruziro)

    [10] “Amene akufuna ulemelero, (amvere Allah), chifukwa ulemelero wonse ngwa Allah. Kwa Iye amakwera mawu abwino. Ndipo zochita zabwino ndi zimene zimakweza mawu abwinowo. Ndipo amene akuchita ndale zoipa, adzapeza chilango chaukali; ndipo ndale zawo nzoonongeka

    [11] “Ndipo Allah adakulengani ndi dothi; kenako ndi dontho la umuna; kenako adakupangani amuna ndi akazi. Ndipo mkazi aliyense satenga mimba ndiponso sabala koma kupyolera m’kudziwa Kwake (Allah). Ndipo amene wapatsidwa moyo, sapatsidwa moyo wautali ndiponso sachepetsedwa moyo wake, koma zonsezo zili m’buku (la Allah). Ndithu zimenezo kwa Allah nzosavuta

    [12] “Ndipo nyanja ziwiri (ya madzi ozizira ndi yamadzi amchere) sizili zofanana, iyi yamadzi okoma, ozuna, ndi omweka bwino kamwedwe kake; ndi iyi (ya madzi) amchere owawa. Ndipo kuchokera m’zonsezi, mumadya nyama yamatumbi (nsomba zaziwisi). Ndipo mumatulutsa zodzikongoletsera (zimene) mumazivala; ndipo m’menemo ukuona zombo zikung’amba madzi kuti mufunefune ubwino Wake (wa Allah) ndi kutinso inu muthokoze

    [13] “Amalowetsa usiku mu usana, ndi kulowetsa usana mu usiku; dzuwa ndi mwezi adazichita kuti zigonjere (malamulo Ake). Zonse zikuyenda (usana ndi usiku) kufikira nthawi yake yodziwika. Ameneyo ndi Allah, Mbuye wanu, Mwini ufumu. Ndipo amene mukuwapembedza, osati Iye, alibe ngakhale khoko la chipatso cha kanjedza

    [14] “Ngati mutawapempha (mafanowo), sangamve kuitana kwanu, ndipo ngati atamva sangakuyankheni (chifukwa alibe kukhoza kulikonse). Ndipo pa tsiku lomalizira, adzakana kuphatikiza kwanu. Ndipo palibe (aliyense) angakuuze monga momwe akukuuzira (Allah) Wodziwa kwambiri

    [15] “E inu anthu! Inu ndiosaukira (chinthu chilichonse) kwa Allah; koma Allah Ngwachikwanekwane (sasaukira chilichonse kwa inu); Wotamandidwa (ndi zolengedwa zonse)

    [16] “Ngati atafuna angakuchotseni ndi kubweretsa zolengedwa zatsopano

    [17] “Ndipo zimenezo sizili zovuta kwa Allah

    [18] “Ndipo wosenza, sadzasenza mtolo wa wina. (Aliyense adzasenza mtolo wa machimo ake). Ngakhale amene walemedwa ndi mtolo wake ataitana (wina) chifukwa cha mtolo wake kuti amsenzere silidzatengedwa ngakhale gawo pang’ono la mtolowo (ndi munthu ameneyo), ngakhale atakhala m’bale wake. Ndithu ukuchenjeza okhawo amene akuopa Mbuye wawo pomwe sakumuona, ndipo akupemphera Swala moyenera, ndipo yemwe akudziyeretsa, ndithu akudziyeretsa yekha, (ubwino wake umubwerera iye mwini); ndipo mabwelero (a zolengedwa zonse) ndi kwa Allah (basi)

    [19] “Ndipo wakhungu ndi wopenya ngosafanana, (woyenda pa njira ya choona ndi wosokera ngosafanana)

    [20] “Ngakhale mdima ndi kuunika (nzosafanana)

    [21] “Ngakhale mthunzi ndi kutentha (nzosafanana)

    [22] “Ndipo amoyo ndi akufa safanana (amene mitima yawo ili ndi moyo pokhala ndi chikhulupiliro, ndi amene mitima yawo ili yakufa posakhala ndi chikhulupiliro, ngosafanana). Ndithu Allah akumumveretsa amene wam’funa; koma iwe sungathe kumumveretsa amene ali m’manda

    [23] “Iwe sindiwe chinthu china, koma ndiwe mchenjezi

    [24] “Ndithu Ife takutuma mwachoona kuti unene nkhani yabwino (yokalowa ku Munda wamtendere kwa amene akhulupirira), ndi kuti uchenjeze (za chilango cha Moto kwa amene sadakhulupirire). Ndipo palibe m’badwo uliwonse koma mchenjezi adapitamo

    [25] “Ndipo ngati angakutsutse (sichachilendo), ndithu amene adali patsogolo pawo adatsutsanso. Aneneri awo adawadzera ndi zizindikiro zoonekera poyera, ndi malemba ndi buku lounikira (njira yabwino)

    [26] “Kenako ndidawalanga (ndidawaononga) amene adatsutsa. Nanga chidali bwanji chilango Changa (pa iwo)

    [27] “Kodi sudaone kuti Allah amatsitsa madzi kuchokera ku mitambo? Choncho kupyolera m’madziwo tatulutsa zipatso zautoto wosiyanasiyana (zakuda, zofiira, zachikasu, zobiriwira, pomwe madzi ake ndiamodzi omwewo). Ndipo m’mapiri muli timizere; toyera ndi tofiira tosiyana utoto wake, ndi (tina) takuda kwambiri

    [28] “Ndipo mwa anthu ndi nyama zokwawa, ndi ziweto, nchimodzimodzinso; nzosiyana maonekedwe ake (utoto wake). Ndithu odziwa ndi amene amamuopa Allah mwa akapolo Ake. Ndithu Allah Ngwamphamvu zoposa; Ngokhululuka kwambiri

    [29] “Ndithu amene akuwerenga buku la Allah uku nkumapemphera Swala moyenera napereka m’zimene tawapatsa mwanseri ndi moonetsera, iwo akuyembekezera malonda osaonongeka

    [30] “Kuti akawakwaniritsire malipiro awo ndi kuwaonjezera zabwino Zake; ndithu Iye Ngokhululuka kwabasi; Ngothokoza kwambiri

    [31] “Ndipo buku limene takuvumbulutsira, nloona; likutsimikizira za mabuku omwe adali patsogolo pake. Ndithu Allah kwa akapolo Ake Ngodziwa kwambiri ndiponso akuwaona bwino

    [32] “Kenako tidawapatsa buku (Qur’an) amene tidawasankha mwa akapolo Athu, koma alipo ena mwa iwo odzichitira okha chinyengo (pochulukitsa machimo), ena mwa iwo ngaapakatikati; ndipo ena mwa iwo ngopikisana pochita zabwino mwa chifuniro cha Allah. Kuteroko ndiwo ubwino waukulu

    [33] “Adzailowa minda yamuyaya; m’menemo adzakongoletsedwa povekedwa zibangiri zagolide ndi ngale; nsalu ya silika ndicho chovala chawo m’menemo

    [34] “Ndipo adzanena (pakuthokoza kwawo): “Kutamandidwa konse nkwa Allah Amene watichotsera madandaulo; ndithu Mbuye wathu Ngokhululuka kwambiri, Ngothokoza kwabasi.”

    [35] ““Yemwe, chifukwa cha ubwino Wake, watikhazika m’nyumba yamuyaya; m’menemo mavuto satikhudza, ndiponso m’menemo kutopa sikutikhudza.”

    [36] “Koma amene sadakhulupirire, wawo ndi moto wa Jahannam sikudzaweruzidwa kwa iwo kuti afe, ngakhale chilango chake sichidzachepetsedwa pa iwo. Umo ndimmene tikumlipirira aliyense wokanira (mtendere wa Allah)

    [37] “Ndipo m’menemo iwo adzakuwa (adzalira uku akunena): “Mbuye wathu! Titulutseni (m’Moto ndi kutibweza pa dziko lapansi); tikachita ntchito zabwino, osati zija tinkachita.” (Allah adzawauza): “Kodi sitidakupatseni moyo wokwanira wotheka kukumbuka kwa wokumbuka? Ndiponso mchenjezi adakudzerani. Choncho lawani (chilango). Ndipo anthu ochita zoipa alibe mpulumutsi.”

    [38] “Ndithu Allah Ngodziwa zobisika za kumwamba ndi za pansi. Iye Ngodziwa kwambiri za m’zifuwa

    [39] “Iye ndi Yemwe wakuchitani kukhala osiyirana pa dziko lapansi (akufa ena, ena nkulowa m’malo mwawo). Ndipo amene sadakhulupirire, kuipa kwa kusakhulupirirako kuli kwa iye mwini. Ndipo kusakhulupirira kwa osakhulupirira sikuwaonjezera chilichonse kwa Mbuye wawo, koma mkwiyo basi. Ndiponso kusakhulupirira kwa osakhulupirira sikuwaonjezera chilichonse, koma kutayika basi

    [40] “Nena: “Kodi mwawaona aphatikizi anu (awa) amene mukuwapembedza m’malo mwa Allah? Tandionetsani, ndimbali iti ya nthaka adalenga; kapena iwo ali ndi gawo m’thambo; (gawo lakulenga thambo?) Kapena tidawapatsa buku (Qur’an iyi isadadze) kotero kuti ali ndi umboni wapoyera wochokera m’menemo (wotsimikizira chipembedzo chawo chamafano)? Koma ochita zoipa salonjezana ena kwa ena china chake koma zachinyengo basi

    [41] “Ndithu Allah amagwira thambo ndi nthaka kuti zisachoke. Ndipo ngati zitachoka, palibe aliyense amene angazigwire kupatula Iye. Ndithu Iye Ngoleza; Ngokhululuka kwabasi

    [42] “Ndipo (awa osakhulupirira, kale) adalumbilira Allah, kulumbira kwawo kwakukulu, kuti ngati adzawadzera mchenjezi, adzakhala oongoka kuposa mbadwo uliwonse. Koma pamene mchenjezi adawadzera, palibe chilichonse chidaonjezeka kwa iwo, koma kukana (choonadicho)

    [43] “Chifukwa cha kudzikweza pa dziko ndi kuchita chiwembu choipa. Ndipo chiwembu choipa sichingamuzinge aliyense koma mwini (yemwe) wachitayo. Kodi akuyembekeza china chosakhala machitidwe (a Allah) amene adawapititsa pa anthu akale. Koma supeza kusintha pa machitidwe a Allah. Ndipo supeza kutembenuka pa machitidwe a Allah

    [44] “Kodi sadayende pa dziko nkuona momwe adalili mathero a omwe adali patsogolo pawo? Ndipo adali anyonga kwambiri kuposa iwo? Ndipo palibe chinthu chonkanika Allah kumwamba ndi pansi. Ndithudi Iye Ngodziwa kwabasi Wokhoza

    [45] “Ndipo Allah akadamalanga anthu chifukwa cha zomwe alakwa, sakadasiya pamwamba pake (pa nthaka) chamoyo chilichonse; koma Iye amawalekelera mpaka nthawi yomwe adaiikayo. Choncho nthawi yawo ikadzawadzera, (pompo adzalangidwa). Ndithu Allah akuwadziwa bwino akapolo Ake

    Ya-Sin

    Surah 36

    [1] “Yâ-Sîn

    [2] “Ndikulumbira Qur’an (iyi yomwe yakonzedwa mwaluso) yodzazidwa ndi mawu anzeru

    [3] “Ndithu iwe (Muhammad {s.a.w}) ndimmodzi wa atumiki (amene Allah adawatuma kwa anthu kuti akawasonyeze chiongoko)

    [4] “(Uli) panjira yolunjika

    [5] “(Qur’an iyi) nchivumbulutso cha Mwini Mphamvu zoposa; (palibe chokanika kwa Iye) Wachisoni chosatha

    [6] “Kuti uwachenjeze anthu omwe makolo awo sadachenjezedwe; choncho iwo ngoiwala (zomwe zili zofunika kuchitira Allah ndi kudzichitira okha pamodzi ndi anthu ena)

    [7] “Ndithu mawu (onena za chilango) atsimikizika pa ambiri a iwo; poti iwo sakhulupirira

    [8] “Ndithu Ife taika magoli m’makosi mwawo ofika kuzibwano, kotero kuti mitu yawo yayang’ana mmwamba; (siingathe kutembenuka ndi kuyang’ana)

    [9] “Ndipo tawaikira chotsekereza patsogolo pawo ndi chotsekereza pambuyo pawo, ndipo (maso awo) tawaphimba, tero iwo saona (zapatsogolo ndi pambuyo pawo)

    [10] “Ndipo kwa iwo nchimodzimodzi, uwachenjeze ngakhale usawachenjeze sangakhulupirire

    [11] “Ndithu kuchenjeza kwako kupindulira amene watsatira Qur’an ndi kumuopa (Allah) Wachifundo chambiri ngakhale sakumuona. Wotere muuze nkhani yabwino ya chikhululuko (chochokera kwa Allah pa machimo ake) ndi malipiro aulemu

    [12] “Ndithu Ife tidzaukitsa akufa, ndipo tikulemba zimene atsogoza (m’dziko lapansi m’zochita zawo) ndi zomwe amasiya pambuyo (atafa, zonkerankera mtsogolo), ndipo chinthu chilichonse tachilemba m’kaundula wopenyeka (wofotokoza chilichonse)

    [13] “Ndipo pereka kwa iwo (iwe Mneneri) fanizo la (nkhani ya) eni mudzi pamene atumiki (a Allah) adaudzera mudziwo (kuti akaaongole eni mudziwo)

    [14] “Pamene tidatumiza atumiki awiri kwa iwo adawatsutsa; ndipo tidawalimbitsa iwo (awiriwo) potumiza wachitatu. (Atumiki atatuwo) adati: “Ife tatumidwa kwa inu.”

    [15] “(Eni mudzi) adati: “Inu ndi anthu ngati ife; (Allah) Wachifundo chambiri sadavumbulutse chilichonse (kwa munthu); inu simuli kanthu koma mukunena bodza.”

    [16] “(Atumiki) adati: “Mbuye wathu (Amene watituma kwa inu) akudziwa kuti ife ndi otumidwadi kwa inu.”

    [17] ““Ndipo palibe china pa ife, koma kufikitsa mwachimvekere (uthenga wa Allah).”

    [18] “(Eni mudzi) adati: “Ife tapeza tsoka chifukwa cha inu; ngati simusiya (ulaliki wanuwo wofuna kutichotsa ku chipembedzo chathu) tikugendani ndi miyala; ndipo kuchokera kwa ife chikukhudzani chilango chowawa.”

    [19] “(Atumiki) adati: “Tsoka lanu lili ndi inu (chifukwa cha kukana kwanu ndi kupitiriza kupembedza mafano). Kodi mukakumbutsidwa (ndi mawu omwe m’kati mwake muli mtendere wanu mukuti takudzetserani masoka; ndi kumatiopseza ndi chilango chowawa)? Koma inu ndi anthu olumpha malire.”

    [20] “Kenako munthu adadza akuthamanga kuchokera ku malekezero a mzindawo (ndipo) adati: “E inu anthu anga! Atsateni atumikiwa.”

    [21] ““Atsateni omwe sakupemphani malipiro (pa kukulangizani kwawo), ndipo iwo ngoongoka.”

    [22] ““Kodi nchiyani chingandiletse ine kupembedza Yemwe adandilenga? Ndipo kwa Iye ndi komwe inu nonse mudzabwerera.”

    [23] ““Kodi ndidzipangire milungu kusiya Iye (Allah)? Chipulumutso chawo sichingandipindulire chilichonse ngati (Allah) Wachifundo Chambiri atafuna kundichitira zoipa; ndipo siingandipulumutse.”

    [24] ““Ndithu ine ngati nditatero ndiye kuti ndili mchisokero choonekera poyera”

    [25] ““Ndithu ine ndakhulupirira Mbuye wanu choncho ndimvereni.”

    [26] “Kudanenedwa (kwa iye): “Lowa m’Munda wamtendere.” Iye adati: “Ha! Anthu anga akadadziwa!”

    [27] ““Momwe Mbuye wanga wandikhululukira ndikundichita kukhala mmodzi wa opatsidwa ulemu (akadakhulupirira).”

    [28] “Ndipo anthu ake sitidawatsitsire ankhondo ochokera kumwamba pambuyo pake (kuti awaononge). Ndipo pachizolowezi chathu sititsitsa (ankhondo kumwamba tikafuna kuononga, koma Mngelo mmodzi amakwanira)

    [29] “(Kuonongeka kwawo) kudali mkuwe umodzi, ndipo nthawi yomweyo adali akufa (izi zidachitika pamene mngelo Gabuliyele adawakuwira mkuwe wamphamvu)

    [30] “Ha! Nzodandaulitsa kwa akapolo! Palibe pamene mtumiki adawadzera popanda kumchitira chipongwe (ndi kukana kumtsata)

    [31] “Kodi sadalingalire za mibadwo yambirimbiri imene tidaiononga patsogolo pawo? Ndipo iwo sangabwelerenso kwa iwo

    [32] “Ndipo zolengedwa zonse zidzaonekera kwa Ife

    [33] “Ndipo chisonyezo chawo ndi nthaka yakufa; timaiukitsa (ndi madzi) ndi kutulutsa m’menemo njere, zomwe zina mwa izo amadya

    [34] “Ndipo tapanga m’menemo minda ya kanjedza ndi mphesa; ndipo tatulutsa m’menemo akasupe

    [35] “Kuti azidya zipatso zake pomwe sizidapangidwe ndi manja awo. Kodi bwanji sathokoza (Allah)

    [36] “Alemekezeke (Allah), Amene adalenga zinthu zonse, chachimuna ndi chachikazi, kuchokera m’zimene nthaka ikutulutsa, ndi iwo omwe ndi zina zimene (anthu) sakudziwa

    [37] “Ndiponso chisonyezo chawo ndiusiku. M’menemo timachotsamo usana (womwe umabisa usiku), ndipo (anthu) amangozindikira ali mu mdima

    [38] “۞ Ndipo dzuwa; limayenda m’njira ndi m’nthawi yake imene idakonzedwa kwa ilo. Chikonzero chimenecho ncha (Allah) Wamphamvu zoposa, Wodziwa kwambiri

    [39] “Ndiponso mwezi; tidaukonzera malo oimirapo mpaka kukafika pomwe umabwerera ndi kukhala wochepa ndi wokhota monga nthambi ya mtengo wa kanjedza, youma komanso yokhota

    [40] “Nkosatheka kwa dzuwa kukumana ndi mwezi (njira yake); nawonso usiku sungathe kupambana usana (pakudza nthawi yausana isadathe, koma zimasinthana). Ndipo chilichonse mwa izo chimasambira m’njira yake (imene Allah adachikonzera)

    [41] “Ndiponso pali chisonyezo kwa iwo (chosonyeza madalitso Athu pa iwo). Ndithu tidaukweza mtundu wawo mchombo chodzazidwa (ndi zonse zamoyo)

    [42] “Ndipo tidawapangira chonga icho chomwe akuchikwera

    [43] “Ndipo ngati titafuna tikhoza kuwamiza m’madzi, ndipo sangapezeke wowathandiza, ndiponso sangapulumutsidwe

    [44] “Koma (sitikuwamiza) chifukwa cha chifundo Chathu pa iwo ndi kuti asangalale kufikira nthawi yawo (yofera)

    [45] “Ndipo kukanenedwa kwa iwo: “Opani zomwe ziri patsogolo panu ndi zomwe ziri pambuyo panu kuti muchitiridwe chifundo.” (Iwo akunyoza malangizowo)

    [46] “Ndipo palibe chisonyezo chilichonse mwa zisonyezo za Mbuye wawo (zosonyeza umodzi Wake ndi kukhoza Kwake) chomwe chidawadzera popanda kuchinyoza (ndi kuchikana)

    [47] “Ndipo kukanenedwa kwa iwo: “Patsani (amphawi) zimene Allah wakupatsani.” Osakhulupirira amanena kwa okhulupirira: “Kodi tidyetse yemwe Allah akadafuna akadamdyetsa; (titsutsane ndi cholinga cha Allah)? Ndithu inu simuli kanthu koma muli m’kusokera koonekeratu.”

    [48] “Ndipo akunena (mwachipongwe kwa okhulupirira): “Kodi lonjezo ili (lakudza kwa chiweruziro), lidzachitika liti, ngati mukunena zoona?”

    [49] “Palibe chimene akuyembekeza, koma ndi mkuwe umodzi womwe udzawamaliza mwadzidzidzi uku iwo akukangana

    [50] “Ndipo sangathe kuuza wina mawu pa chinthu, ndiponso sangathe kubwerera ku maanja awo

    [51] “Ndipo lipenga lidzaimbidwa (loukitsa akufa); iwo adzangozindikira akutuluka m’manda kunka kwa Mbuye wawo uku akuthamanga

    [52] “Adzati: “Kalanga ife! Kodi ndani watidzutsa pogona pathu?” (Adzawauza): “Izi ndi zimene adalonjeza (Allah), Wachifundo chambiri ndi zimene adanena atumiki moona.”

    [53] “Sipadzakhala (china) koma mkuwe umodzi basi; adzangozindikira iwo onse atabweretsedwa patsogolo Pathu

    [54] ““Ndipo mzimu uliwonse lero suponderezedwa pa chilichonse. Ndipo mulipidwa pa zokhazo munkachita.”

    [55] “Ndithu anthu aku Jannah (Munda wamtendere) lero akhala wotanganidwa ndi chisangalalo

    [56] “Iwo ndi akazi awo ali m’mithunzi uku atatsamira mipando (ya mtengo wapamwamba)

    [57] “M’menemo apeza (mtundu uliwonse) wa zipatso ndiponso apeza chilichonse chimene akuchifuna

    [58] ““Mtendere (pa iwo)!” Limeneli ndi liwu lochokera kwa Mbuye (wawo), Wachisoni chosatha

    [59] “Ndipo dzipatuleni lero, inu oipa

    [60] “Kodi sindidakulangizeni, E inu ana a Adam kuti musapembedze satana? Ndithu, iye ndi mdani woonekera kwa inu

    [61] “Ndikuti ndipembedzeni Ine? Imeneyi ndi njira yolunjika

    [62] “Ndithu (satana) adasokeretsa anthu ambiri mwa inu. Kodi simumaganizira mwanzeru

    [63] “Iyi ndi Jahena yomwe mumalonjezedwa

    [64] “Iloweni lero, chifukwa cha kunkana kwanu (Allah)

    [65] “Lero titseka kukamwa kwawo. Ndipo manja awo atiyankhula ndipo miyendo yawo ichitira umboni pa zomwe amachita

    [66] “Ndipo tikadafuna, tikadafafaniza maso awo; ndipo akadakhala akuthamangira njira; koma akadapenya chotani

    [67] “Ndipo tikadafuna, tikadawasintha kukhala ndi maonekedwe a nyama pamalo pawo pomwepo (pamene adali), kotero kuti sakadatha kuyenda (kunka patsogolo) ngakhale kubwerera pambuyo

    [68] “Ndipo amene tikumtalikitsira moyo wake, timam’bwezeranso pambuyo m’kalengedwe kake (ndi kukhala ngati mwana). Kodi bwanji saganizira mwanzeru

    [69] “Ndipo sitidamphunzitse (Mtumiki {s.a.w}) ndakatulo, ndipo nkosayenera kwa iye (kukhala mlakatuli). Qur’an sichina, koma ndichikumbutso ndi buku lomwe likulongosola chilichonse

    [70] “Kuti liwachenjeze amene ali moyo, ndi kuti litsimikizike liwu (la chilango) pa osakhulupirira

    [71] “Kodi saona kuti Ife tawalengera nyama, m’zimene manja Athu akonza, zomwe iwo akuti nzawo

    [72] “Ndi kuti tazichita kukhala zowatumikira? Zina mwa izo amazikwerapo; ndipo zina mwa izo amazidya

    [73] “Ndipo m’menemo (m’nyama) muli zowathandiza (zambiri) ndiponso zakumwa. Nanga bwanji sathokoza

    [74] “Ndipo adzipangira milungu (yabodza) kusiya Allah kuti athandizidwe nayo

    [75] “(Koma) siingathe kuwathandiza; ndipo iwo (kwa milunguyo) ndi asilikali amene akonzedwa kulondera (mafanowo ndi kuwatumikira)

    [76] “Mawu awo (onyoza Allah ndi okutsutsa iwe) asakudandaulitse. Ndithu Ife tikudziwa zimene akubisa ndi zimene akuzionetsera poyera

    [77] “Kodi munthu sazindikira kuti Ife tidamulenga ndi dontho la umuna? Koma iye wakhala wotsutsa woonekera

    [78] “Ndipo akutiponyera fanizo (lotsutsa kukhoza Kwathu kuukitsa akufa) ndi kuiwala chilengedwe chake (chochokera kumadzi opanda pake). Akunena: “Ndani angaukitse mafupa pomwe ali ofumbwa?”

    [79] “Nena: “Adzawaukitsa Yemwe adawalenga panthawi yoyamba. Ndipo Iye Ngodziwa kalengedwe ka mtundu uliwonse

    [80] “Yemwe adakupangirani moto kuchokera mu mtengo wauwisi; kenako inu mumakoleza moto m’menemo

    [81] “Kodi Yemwe adalenga thambo ndi nthaka (mukuganiza kuti) siwokhoza kuwalenga (iwo kachiwiri) monga momwe alili? Inde! Iye ndi Mlengi Wamkulu, Wodziwa kwambiri

    [82] “Ndithu machitidwe Ake akafuna kuti chinthu chichitike, amangonena kwa icho: “Chitika!” Ndipo chimachitika (nthawi yomweyo)

    [83] “Kotero alemekezeke Yemwe m’manja Mwake muli ulamuliro pa chinthu chilichonse; ndipo kwa Iye (ndiko) mudzabweerera nonse

    Olunjika mizera

    Surah 37

    [1] “Ndikulumbira (angelo) amene amandanda m’mizere yondondozana, (popembedza ndi kugonjera Mbuye wawo)

    [2] “Ndi omwe amaletsa zoipa

    [3] “Ndi omwe amalalika ulaliki (wa Allah ndi kumtamanda mochulukira)

    [4] “Ndithu Mulungu wanu ndi mmodzi basi

    [5] “Mbuye wathambo ndi nthaka, ndi zapakati pake; ndiponso Mbuye wa kuvuma konse

    [6] “Ndithu tidalikongoletsa thambo lapafupi (ndi inu) ndi chokongoletsa cha nyenyezi (zowala)

    [7] “Ndi kuti lisungidwe ku satana aliyense wogalukira (lamulo la Allah)

    [8] “Kuti asamvere (zomwe zikunenedwa ndi) gulu lolemekezeka (la angelo). Ndipo akugendedwa (ndi kupirikitsidwa) mbali zonse

    [9] “Kuthamangitsidwa mwamphamvu; ndipo chilango chonkerankera patsogolo chili pa iwo

    [10] “Kupatula amene wazembetsa mawu (akumwamba), ndipo chikumtsatira iye chenje cha moto chowala kwambiri

    [11] “Tawafunsa (otsutsa zouka ku imfa): “Kodi iwo ngovuta kuwalenga kuposa zimene tidalenga, (monga: thambo, nthaka, nyenyezi ndi zina zotere)?” Ndithu Ife tidawalenga kuchokera ku dongo lonyata

    [12] “Koma iwe (Mneneri) ukudabwa (za kutsutsa kwawo kuuka ku imfa pomwe zisonyezo zilipo zambirimbiri), ndipo akukuchitira chipongwe (kudabwa kwako)

    [13] “Ndipo akalalikiridwa, salalikirika

    [14] “Ndipo akachiona chisonyezo (chosonyeza kukhoza kwa Allah,) amachichitira chipongwe

    [15] “Ndipo osakhulupirira amanena: “Palibe chilipo apa, koma ndi matsenga woonekera poyera.”

    [16] ““Kodi tikadzafa ndi kusanduka fumbi ndi mafupa, tidzatulutsidwanso (kuchokera m’manda tili amoyo)?”

    [17] ““Pamodzi ndi makolo athu akale?”

    [18] “Nena (iwe Mneneri): “Inde (mudzaukitsidwa inu pamodzi ndi makolo anu) uku inu muli onyozeka.”

    [19] “Ndithu (kuukako) ndimkuwe umodzi adzangodzidzimuka ali moyo, akuyang’ana

    [20] “Ndipo adzanena (okanawo): “Kalanga ife! Kuonongeka nkwathu! Ili nditsiku lija lamalipiro!”

    [21] “(Adzawauza): “Ili nditsiku la chiweruziro lomwe mumalitsutsa lija.”

    [22] “(Kudzanenedwa kwa angelo): “Asonkhanitseni amene adali osalungama pamodzi ndi akazi awo (okana Allah) ndi milungu yawo imene amaipembedza,”

    [23] ““Kusiya Allah, ndipo asonyezeni njira ya ku Jahannam.”

    [24] ““Koma aimikeni pano chifukwa iwo afunsidwa (za chikhulupiliro chawo ndi zochita zawo):”

    [25] ““Kodi nchifukwa ninji inu (opembedza mafano) simukupulumutsana (monga mumanenera pa dziko lapansi kuti mudzapulumutsana)?”

    [26] “Koma iwo pa tsikulo adzagonjera ndi kudzipereka (ku lamulo la Allah)

    [27] “Ndipo adzatembenukirana ndi kuyamba kufunsana (ndi kudzudzulana)

    [28] “Ndipo (ofooka) adzanena (kwa odzikweza): “Inu mumatidzera kumbali komwe timakuganizira kuti nkwabwino (ndi kutichotsako kunka nafe ku njira yopotoka)

    [29] “(Odzikweza) adzayankha: “Koma simudali okhulupirira.”

    [30] ““Ndipo tidalibe nyonga zokuponderezerani inu, koma mudali anthu opyola malire (ndi kutuluka ku choonadi cha Allah).”

    [31] ““Choncho mawu a Mbuye wathu (onena za chilango) atsimikizika pa ife; ndithu ife tichilawa (chilango).”

    [32] ““Tidakusokeretsani; nafenso tidali osokera. (Choncho musatidzudzule).”

    [33] “Ndithu iwo akathandizana chilango tsiku limenelo (la chiweruziro)

    [34] “Ndithu (chilango chonga chimenecho) ndimomwe timawachitira olakwira (Allah)

    [35] “Ndithu iwo ankati akauzidwa kuti palibe wopembedzedwa mwa choonadi koma Allah ankadzitukumula

    [36] “Ndipo ankanena: “Kodi ife tisiye kupembedza milungu yathu chifukwa cha zonena za mlakatuli, wopenga?”

    [37] “Iyayi koma adawadzera ndi choonadi (Mthenga wawo Muhammad yemwe siwamisala kapena wolakatula zopeka) ndipo adawatsimikizira za atumiki

    [38] “Ndithu inu (osakhulupirira) mudzalawa chilango chowawa

    [39] “Ndipo simudzalipidwa kupatula zokhazo zimene mumachita

    [40] “Kupatula akapolo a Allah oyeretsedwa

    [41] “Kwa iwo kuli zopatsidwa zodziwika (ndi Mbuye wawo Allah)

    [42] “Zipatso (zamtundu uliwonse); ndipo iwo adzalandira ulemu (waukulu)

    [43] “M’minda ya mtendere

    [44] “Adzakhala pa makama (a mtengo wapatali) uku akuyang’anizana

    [45] “Uku zikuwazungulira zikho zodzazidwa ndi zakumwa zochokera m’kasupe woyenda nthawi zonse

    [46] “Woyera, wokoma kwa akumwa (zakumwazo)

    [47] “(M’zakumwazo) mulibe zopweteketsa mutu (kwa ozimwa) ndiponso iwo sadzaledzera nazo

    [48] “Ndipo kwa iwo kudzakhala akazi oyang’ana iwo okha, ophanuka maso (okongola)

    [49] “Onga ngati dzira (la nthiwatiwa) losungidwa (m’mapiko)

    [50] “Ndipo adzayang’anizana ndi kuyamba kufunsana (pakati pawo)

    [51] “Adzanena wonena mmodzi wa iwo: “Ine ndidali ndi mnzanga (wopembedza mafano amene amatsutsana nane za chipembedzo ndi zophunzitsa za Qur’an yolemekezeka).”

    [52] “Yemwe amandiuza: “Kodi iwe ndiwe mmodzi wa ovomereza?”

    [53] ““Zakuti tikadzafa ndi kusanduka fumbi ndi mafupa, (tidzaukanso) ndi kulandira malipiro (pa zochita zathu)?”

    [54] “(Wokhulupirira) adzanena (kwa anzake: “Inu anthu a kumtendere) kodi simungasuzumire (nane ku moto kuti timuone)?”

    [55] “Choncho adzayang’ana ndipo adzamuona ali mkatikati mwa moto

    [56] “Adzanena: “Ndikulumbilira Allah! Udatsala pang’ono kuti undiononge (ndikadakuvomera paja pa dziko lapansi).”

    [57] ““Ndipo pakadapanda chisomo cha Mbuye wanga, ndikadakhala mmodzi mwa opezeka ku Moto.”

    [58] ““Kodi zili choncho kuti sitidzafanso (tizingosangalala m’Munda wamtendere).”

    [59] ““Kupatula imfa yathu yoyamba ija, ndi kutinso ife sitilangidwa?”

    [60] “Ndithu izi (zimene Allah waika m’Munda wamtendere) ndiko kupambana kwakukulu

    [61] “(Pofuna kupeza) zonga zimenezi ogwira ntchito agwire

    [62] “Kodi zimenezo ndilo phwando labwino kapena mtengo wa Zaqqum (wowawa kwambiri womwe anthu a ku Moto azikadya)

    [63] “Ndithu Ife taupanga (mtengo umenewu) kukhala mayeso ndi chilango cha anthu ochimwa (podzichitira okha chinyengo ndi kupembedza mafano)

    [64] “Umenewu ndimtengo omwe umatuluka pakatikati pa Jahannam (adaulenga kuchokera ku Moto)

    [65] “Zipatso zake (nzoipa) ngati mitu ya asatana

    [66] “Ndithu iwo akadya mtengowo ndi kudzaza mimba zawo ndi zipatso zake (pakuti sakapeza chakudya china kupatula zipatso za mtengowo)

    [67] “Kenako, ndithu kuwawa kwa mtengowo kosakanikirana ndi madzi owira kuzakhala pa iwo

    [68] “Kenako ndithu kobwerera kwawo ndi ku Jahannam

    [69] “Ndithu iwo adapeza makolo awo ali osokera

    [70] “Ndipo iwonso adatsata mapazi awo mothamanga

    [71] “Ndipo, ndithu akale ambiri adasokera patsogolo pawo

    [72] “Ndipo, ndithu tidatuma achenjezi kwa iwo

    [73] “Tapenya momwe adalili mapeto a omwe adachenjezedwa

    [74] “Kupatula akapolo a Allah, oyeretsedwa (iwo ndiwo anthu a ku Munda wamtendere)

    [75] “Ndithu Nuh adatiitana, (ndipo tidamuyankha mayankho abwino), taonani kukhala bwino Ife Oyankha

    [76] “Ndipo tidampulumutsa iye ndi anthu ake ku vuto lalikulu

    [77] “Ndipo tidazichita zidzukulu zake kukhala zotsala (pa dziko, oipa ataonongeka)

    [78] “Ndipo tidamsiira mbiri yabwino kwa mibadwo yodza pambuyo pake

    [79] “Mtendere ukhale pa Nuh pa zolengedwa zonse

    [80] “Ndithu umu ndimomwe Ife tilipirira ochita zabwino

    [81] “Ndithu iye ndi mmodzi mwa akapolo Athu okhulupirira

    [82] “Kenako tidawamiza enawo

    [83] “Ndipo ndithu m’gulu lake (la Nuh) muli Ibrahim

    [84] “Kumbuka pamene adadza kwa Mbuye wake ndi mtima wabwino (wogonjera malamulo)

    [85] “Pomwe adanena kwa bambo wake ndi anthu ake: “Mukupembedza chiyani?”

    [86] ““Ha! Milungu yopeka kusiya Allah, ndi imene mukuifuna?”

    [87] ““Kodi maganizo anu ngotani pa Mbuye wa zolengedwa zonse?”

    [88] “Ndipo adayang’ana nyenyezi mozama

    [89] “Ndipo adanena: “Ine ndine wodwala!”

    [90] “Choncho iwo adatembenuka ndi kumsiya

    [91] “(Ibrahim) adapita mozemba ku mafano awo, ndipo adawauza (mwachipongwe:) “Bwanji simukudya (chakudya chomwe chaikidwa patsogolo panupo)?”

    [92] ““Bwanji simukuyankhula?”

    [93] “Atatero adawatembenukira ndi kuwamenya (mwamphamvu) ndi dzanja lamanja

    [94] “(Pamene adamva eni mafanowo) adadza kwa iye akuthamanga

    [95] “Anati: “Kodi mukupembedza (miyala) imene mwasema?”

    [96] ““Chikhalirecho Allah ndiye adakulengani ndi zimene mukuchita!”

    [97] “Iwo adati: “Mmangireni ng’anjo, ndipo mponyeni m’motowo.”

    [98] “Adafuna kumchita chiwembu (kuti amuphe ndi moto), koma tidawachita kukhala onyozeka

    [99] “Ndipo (Ibrahim) adati: “Ndithu ine ndikupita kwa Mbuye wanga, Iye andiongolera.”

    [100] ““E Mbuye wanga! Ndipatseni mwana yemwe adzakhale (mmodzi) mwa olungama!”

    [101] “Ndipo tidamuuza nkhani yabwino ya mwana wofatsa, (mwanayo ndi Ismaila)

    [102] “Ndipo (adabadwa ndi kuyamba kukula.) Pamene adakwana nsinkhu woyenda pamodzi ndi tate wake pochitachita za m’dziko (Ibrahim adayesedwa mayeso kupyolera m’maloto omwe adalota). Adati: “E mwana wanga! Ine kutulo ndikuona maloto (owona ochokera kwa Allah omwe akundilamula) kuti ndikuzinge (monga nsembe yopereka kwa Allah). Nanga ukuti bwanji?” (Mwana wabwino) adanena: “Bambo wanga! Kwaniritsani chimene mukulamulidwa. Ngati Allah afuna, mundipeza ndili mmodzi mwa opirira.”

    [103] “Pamene adagonjera onse awiri (chofuna cha Allah), ndipo (Ibrahim) adam’goneka chakumphumi (ndipo adatsimikiza kumupha)

    [104] “Ndipo tidamuitana: “E iwe Ibrahim!”

    [105] ““Ndithu wavomereza maloto! (Choncho usamuphe mwana wakoyo).” Umo ndi momwe timawalipirira ochita zabwino

    [106] “Ndithu amenewa ndimayeso oonekera

    [107] “Ndipo tidampulumutsa pompatsa nyama yayikulu (yoti apereke nsembe)

    [108] “Ndipo tidamsiira (mbiri yabwino) kwa anthu ena (amene adadza pambuyo pake)

    [109] “Mtendere ukhale pa Ibrahim

    [110] “M’menemo ndi mornwe timawalipirira ochita zabwino

    [111] “Ndithu iye adali mmodzi mwa akapolo Athu okhulupirira

    [112] “Ndiponso tidamuuza nkhani yabwino (yoti akhala ndi mwana wotchedwa) Isihaqa; mneneri; wam’gulu la olungama

    [113] “Ndipo tidamdalitsa iye ndi (mwana wake) Isihaqa; ndipo m’mbumba ya awiriwa mudapezeka abwino ndi odzichitira zoipa owonekera

    [114] “Ndipo ndithu tidawachitira zabwino Mûsa ndi Haruna, (powapatsa uneneri ndi madalitso ambiri)

    [115] “Ndipo tidawapulumutsa (awiriwa) ndi anthu awo ku vuto lalikulu

    [116] “Ndipo tidawathangata (powagonjetsera adani awo), ndipo iwo adali opambana

    [117] “Ndipo tidawapatsa (Mûsa ndi Haruna) buku losonyeza poyera (malamulo)

    [118] “Ndipo tidawaongolera ku njira yolunjika

    [119] “Ndiponso tidawasiira (mbiri yabwino) kwa anthu ena (amene adadza pambuyo pawo)

    [120] “Mtendere ukhale pa Mûsa ndi Haruna

    [121] “Ndithu umu ndi momwe Ife timawalipirira ochita zabwino

    [122] “Ndithu awiriwa adali m’gulu la akapoio Athu okhulupirira

    [123] “Ndipo ndithu Iliyasa ndi mmodzi wa atumiki

    [124] “(Kumbuka) pamene adanena kwa anthu ake: “Bwanji simuopa (Allah)?”

    [125] ““Mukupembedza (fano lotchedwa) Ba’la ndi kusiya (kupembedza) Wabwino zedi mwa olenga onse.”

    [126] ““Allah, Mbuye wanu ndi Mbuye wa makolo anu akale?”

    [127] “Koma adamtsutsa; ndithu iwo adzaonekera (ku Moto)

    [128] “Kupatula akapolo a Allah amene ayeretsedwa (ndi Allah)

    [129] “Ndipo tidamsiira (mbiri yabwino) kwa anthu ena (amene adadza pambuyo pake)

    [130] “Mtendere ukhale pa Iliyasiin

    [131] “Ndithu umo ndi mmene Ife timawalipirira ochita zabwino

    [132] “Ndithu iye ndimmodzi mwa akapolo Athu okhulupirira

    [133] “Ndithu Luti ndi mmodzi wa atumiki

    [134] “(Kumbuka) pamene tidampulumutsa iye ndi anthu ake onse

    [135] “Kupatula nkhalamba yachikazi; idali mwa otsalira

    [136] “Kenako tidawaononga enawo (omwe adali oipa)

    [137] “Ndithu inu (a mumzinda wa Makka) mumadutsa pa malo pawopo m’mawa

    [138] “Ndi usiku. Kodi bwanji simuzindikira

    [139] “Ndithu Yunusu ndi mmodzi wa atumiki

    [140] “(Kumbuka) pamene adathawira m’chombo chodzazidwa (ndi katundu)

    [141] “Choncho adachita mayere, ndipo adali m’gulu la omgwera (mayerewo)

    [142] “Choncho nsomba idammeza uku ali wodzudzulidwa

    [143] “Kukadapanda kuti iye adali m’modzi mwa otamanda ndi kulemekeza Allah

    [144] “Akadakhala m’mimba mwake mpaka tsiku loukitsidwa (zolengedwa ku imfa)

    [145] “Koma tidamponya pa gombe uku ali wodwala

    [146] “Ndipo tidammeretsera mmera wa mtundu wa nkhaka

    [147] “Ndipo (atachira) tidamtuma ku anthu okwana zikwi zana limodzi (,000) kapena kupambana apa

    [148] “Ndipo adakhulupirira (ndi kuvomereza ulaliki wake); choncho tidawapatsa chisangalalo kufikira nthawi (ya imfa yawo)

    [149] “Choncho afunse: “Kodi Mbuye wako ndiye woyenera ana aakazi, ndipo iwo aamuna? (Pomwe iwo akabereka mwana wamkazi amanyansidwa naye)!”

    [150] “Kapena kuti tidalenga angelo kukhala akazi, iwo akuona

    [151] “Chenjera ndi bodza lawolo, ndithu iwo akunena

    [152] ““Allah wabereka.” Ndithu iwo ndi abodza

    [153] “Kodi Iye adasankha ana aakazi kusiya aamuna

    [154] “Kodi nchiyani chakupezani (kuti muweruze mopanda chilungamo); nanga mukuweruza bwanji (zimenezi)

    [155] “Kodi bwanji simukumbukira, (mwaiwala zisonyezo Zake zodabwitsa ndi kupatukana kwake ndi zimenezo)

    [156] “Kapena inu muli ndi umboni woonekera (wochokera kumwamba)

    [157] “Tabweretsani buku lanulo (momwe mwalembedwa zimenezi) ngati mukunena zoona

    [158] “Ndipo adapeka chibale pakati pa Iye (Allah) ndi ziwanda; (pomwe ziwanda nzobisika kwa iwo). Ndithu ziwanda zimadziwa kuti iwo osakhulupirira akaonekera (kwa Allah kuti aweruzidwe)

    [159] “Walemekezeka Allah! Ndi kupatukana ndi zimene akumnamizira

    [160] “Koma akapolo a Allah oyeretsedwa (ali kutali ndi zimene akusimba osakhulupirirazi)

    [161] “Ndithu inu (osakhulupirira) ndi zimene mukuzipembedza (kusiya Allah)

    [162] “Ndi zimenezo simungamsokeretse aliyense

    [163] “Kupatula yemwe (Allah adadziwa kuti) ngolowa ku Jahannam

    [164] “Ndipo (angelo adanena): “Aliyense mwa ife ali ndi malo ake odziwika.”

    [165] ““Ndipo ndithu (ena mwa) ife ngondanda m’mizere (ya mapemphero nthawi zonse).”

    [166] ““Ndipo (ena mwa) ife ngolemekeza (Allah nthawi zonse ndi kumtamanda ndi kumpatula ku zinthu zosayenerana ndi ulemelero wake).”

    [167] “Ndipo (osakhulupirira) ankati

    [168] ““Tikadakhala ndi buku monga lomwe anthu akale adali nalo.”

    [169] ““Tikadakhala akapolo a Allah, oyeretsedwa.”

    [170] “Koma (pamene lidawadzera bukulo), adalikana; choncho posachedwa adziwa (zotsatira zake)

    [171] “Ndipo ndithu liwu lathu lidatsogola kwa akapolo athu otumidwa

    [172] “(Kuti) ndithu iwo ngopulumutsidwa

    [173] “Ndipo ndithu asilikali Athu ndi opambana

    [174] “Choncho, asiye kwa kanthawi kochepa

    [175] “Ndipo ingowayang’ana basi; posachedwapa aona

    [176] “Kodi chilango chathu akuchifulumizitsa

    [177] “Choncho chikadzatsika pabwalo lawo, udzakhala mmawa woipa kwa ochenjezedwa

    [178] “Ndipo asiye kwa kanthawi kochepa

    [179] “Ndipo ingowayang’ana basi; posachedwapa aona

    [180] “Mbuye wako, Mwini ulemelero, wapatukana ndi zimene akumnamizira (osakhulupirira)

    [181] “Ndipo mtendere ukhale pa atumiki onse

    [182] “Ndipo kuyamikidwa konse nkwa Allah, Mbuye wa zolengedwa zonse

    Sad

    Surah 38

    [1] “Sad, ndikulumbira Qur’an (iyi) ya ulaliki (wothandiza)

    [2] “Koma amene sadakhulupirire ali mkudzitukumula ndi makani

    [3] “Kodi ndimibadwo ingati taiwononga patsogolo pawo? Adakuwa kuitana (panthawi imeneyo), koma nthawi yopulumuka idali itatha

    [4] “Ndipo anadabwa atawadzera mchenjezi wochokera mwa iwo. Ndipo osakhulupirira adati: “Uyu ndiwamatsenga; ngwabodza lamkunkhuniza!”

    [5] “Ha! Waichita milungu yambirimbiri ija kuti ikhale Mulungu Mmodzi Yekha? Ndithu ichi nchinthu chodabwitsa.”

    [6] “Ndipo adanyamuka akuluakulu a mwa iwo nati: “Nyamukani muzikapitiriza kupembedza milungu yanu. Ndithu chinthu ichi (nchoipa); chikulinga ife (kuti tisiyane ndi milungu yathu).”

    [7] ““Sitidamve zimenezi (zakuti Mulungu Ndimmodzi ngakhale) m’chipembedzo chakale (Chikhrisitu). Ichi sikanthu, koma ndibodza lopeka.”

    [8] ““Kodi uthengawo (wakuti Mulungu Ndimmodzi) wavumbulutsidwa kwa iye pakati pathu?” Koma iwo akukaika ndi ulaliki Wanga. Koma sadalawebe chilango Changa

    [9] “Kodi iwo ali nazo nkhokwe za chifundo cha Mbuye wako, Wamphamvu zoposa, Wopatsa mochuluka

    [10] “Kapena ufumu wa kumwamba ndi pansi ndi zapakati pake, ngwawo. Ngati zili choncho atakwera makwelero (kuti akafike pamalo poti akalamulire zimene akufuna, ngati angathe kutero)

    [11] “Awa (Aquraish kuonjezera pa kudzitama kwawo), nkagulu kochepa ndi kofooka. Kagonjetsedwa monga makamu ankhondo (omwe adagonjetsedwa kale omwe amatsutsana ndi aneneri akale)

    [12] “Patsogolo pawo, anthu a Nuh, Âdi ndi Farawo, mwini nyumba zitalizitali (Pyramid), adatsutsa (aneneri awo)

    [13] “Ndi Asamudu, ndi anthu a Luti ndi (anthu a Shuaib) eni mitengo yambiri yothothana, amenewo ndiwo makamu

    [14] “Onsewa adatsutsa atumiki; basi chilango Changa chidatsimikizika (pa iwo)

    [15] “Ndipo awa (Aquraish), sayembekeza china koma mkuwe umodzi wosabwereza. (Ndipo ukadzachitika, onse adzafa)

    [16] “Ndipo akunena (mwachipongwe): “E Mbuye wathu! Tipatsirenitu gawo la chilango chathu lisanafike tsiku lachiwerengero.”

    [17] “Pirira (iwe Mtumiki) ku zimene akunena (kwa iwe), ndipo kumbuka kapolo wathu Daud, wamphamvu (pa chipembedzo ndi za m’dziko lapansi). Ndithu iye ngotembenukira kwa Allah kwambiri

    [18] “Ndithu Ife tidawagonjetsa mapiri kuti pamodzi ndi iye alemekeze (Allah) mmawa ndi madzulo

    [19] “Ndi mbalame zomwe zidasonkhanitsidwa zonse zimamvera iye

    [20] “Ndipo tidaulimbikitsa ufumu wake ndi kumpatsa uneneri ndi kuyankhula kwa luntha (kosiyanitsira choona ndi chonama)

    [21] “Kodi yakufika nkhani ya okangana pamene adakwera chipupa mpaka kuchipinda (cha Daud chochitira mapemphero)

    [22] “Pamene adamulowera Daud, adachita nawo mantha adati: “Usaope; (ife) ndife okangana awiri, mmodzi wathu wamchenjelera wina. Weruza pakati pathu mwachilungamo, usakondere, ndipo tisonyeze njira yoongoka.”

    [23] ““Ndithu uyu m’bale wanga ali ndi nkhosa makumi asanu ndi anayi mphambu zisanu ndi zinayi , pomwe ine ndili ndi imodzi.” Ndipo akuti: “Ndipatse nkhosa imodziyo kuti ndizikusungira.” Ndipo wandiposa pakuyankhula

    [24] “(Daud) adati: “Zoona, wakuchitira zosalungama pokupempha nkhosa yako imodzi kuti aiphatikize ndi nkhosa zake. Ndithu ambiri mwa ophatikizana nawo zinthu, ena amachenjelera ena kupatula amene akhulupirira ndi kumachita zabwino; ndipo iwo ngochepa.” Basi pamenepo Daud adaona kuti tamuyesa mayeso (ndipo sadapambane). Choncho adapempha chikhululuko kwa Mbuye wake; adagwa ndi kulambira ndi kubwerera kwa Mbuye wake

    [25] “Choncho tidamkhululukira iye zimenezo; ndithu iye ali nawo ulemelero kwa Ife ndi mabwelero abwino

    [26] ““E iwe Daud! Ndithu ife takuchita iwe kukhala woyang’anira pa dziko; choncho weruza pakati pa anthuwa mwachilungamo; ndipo usatsatire zilakolako kuopa kuti zingakusokeretse ku njira ya Allah.” Ndithu amene akusokera ku njira ya Allah (potsatira zilakolako zawo), chilango chaukali chili pa iwo chifukwa cha kuiwala kwawo tsiku la chiwerengero

    [27] “Ndipo sitidalenge thambo ndi nthaka ndi zapakati pake popanda cholinga. Zoterezo ndi maganizo a amene sadakhulupirire. Choncho kuonongeka kwakukulu ku Moto kuli kwa iwo amene sadakhulupirire

    [28] “Kodi tingawachite amene akhulupirira (Allah) ndi kuchita zabwino kukhala monga oononga pa dziko? Kapena tiwachite oopa (Allah) monga oipa

    [29] “(Ili), ndibuku lochuluka madalitso lomwe talivumbulutsa kwa iwe kuti (anthu) azame kwambiri pomvetsetsa ndime zake; ndi kuti apeze nalo phunziro eni nzeru

    [30] “Ndipo Daud tidampatsa (dalitso lobereka) Sulaiman, amene adali munthu wabwino. Ndithu iye adali wochulukitsa kutembenukira kwa Allah (ndi kudzichepetsa m’chikhalidwe chake chonse)

    [31] “(Kumbuka) pamene adasonyezedwa kwa iye nthawi yamadzulo akavalo ofatsa akaima; othamanga kwambiri, akayenda

    [32] “Ndipo adati: “Ndikukonda zinthu zabwino chifukwa chokumbukira Mbuye wanga,” kufikira pomwe (akavalowo) adabisika kuseri kwa chotsekereza (poikidwa m’makola mwawo pomwe iye amafunitsitsa kumawaonabe)

    [33] “(Ndipo adati): “Abwezeni kwa ine.” Kenako adayamba kuwasisita m’miyendo ndi m’makosi (mwawo)

    [34] “Ndithu Sulaiman tidamuyesa (mayeso); ndipo tidaika thupi pa mpando wake wachifumu; kenako adabwerera kwa Allah

    [35] “Adati: “E Mbuye wanga! Ndikhululukireni ndipo ndipatseni ufumu (umene) sangaupeze aliyense pambuyo panga; ndithu inu ndiwopatsa mochulukitsa.”

    [36] “Kenako tidaichita mphepo yoomba moleza kuti imgonjere, yomwe imayenda mwachifuniro chake (Sulaiman), paliponse pomwe wafuna

    [37] “Ndiponso (tidamgonjetsera) asatana; ena mwa iwo omanga zomangamanga ndi obira m’nyanja zakuya

    [38] “Ndi ena (mwa asatana) onjatidwa mmagoli ndi unyolo, (kuti asiye kusokoneza ena)

    [39] “(Ndipo adauzidwa iye): “Izi (zomwc takudalitsa nazo) ndi zopatsa Zathu; choncho mpatse kapena mmane (amene wamfuna). Popanda kuwerengeredwa.”

    [40] “Ndithu (Sulaiman) ali nawo ulemelero waukulu woyandikira kwa Ife, ndi mabwelero abwino

    [41] “Kumbuka, (iwe Mtumiki {s.a.w}) kapolo Wathu Ayubu, pamene adaitana Mbuye wake: “Ine wandikhudza satana ndi masautso ndi zowawa!”

    [42] “(Tidamuyankha kuitana kwake, ndipo tidamuuza): “Menyetsa miyendo yako (panthaka; patuluka madzi) ozizira osamba ndi kumwa (zikuchokera zomwe uli nazo).”

    [43] “Ndipo tidamubwezera anthu ake, ndi kumpatsanso ena onga iwo (m’kuchuluka kwawo) powaphatikiza ndi omwe adali nawo; (tidachita zimenezi) chifukwa cha chifundo chochokera kwa Ife ndi kuti chikhale chikumbutso kwa eni nzeru

    [44] ““Ndipo gwira m’dzanja lako mtolo wa zikoti; menya ndi mtolowo ndipo usaswe lonjezo.” Ndithu Ife tidampeza ali wopirira. Taonani kukhala bwino kapolo! Ndithu iye ngotembenukira kwambiri kwa Allah

    [45] “Kumbukira, (iwe Mtumiki {s.a.w}) akapolo athu Ibrahim, Ishâq ndi Ya’qub, eni mphamvu (pa ntchito yachipembedzo) ndi kuyang’ana kozindikira

    [46] “Ndithu Ife tidawasankha powapatsa chikhalidwe chabwino (chomwe) ndi kukumbukira Nyumba yomaliza (nthawi zonse)

    [47] “Ndithu kwa Ife iwo adali mwa anthu abwino omwe adasankhidwa

    [48] “Ndipo kumbuka Ismail, Alyasa’ (Eliya), ndi Thulkifl (Yesaya); ndipo onsewo adali mwa anthu abwino

    [49] “Ichi ndichikumbutso (kwa iwe ndi anthu ako). Ndipo ndithu oopa Allah ali ndi mabwelero abwino

    [50] “(Awakonzera iwo) minda yamuyaya yotsekulidwa makomo ake kwa iwo

    [51] “(Azidzakhala m’menemo) uku atatsamira (makama amtengo wapatali, ndipo adzakhala akusangalala) akuitanitsa mmenemo zipatso ndi zakumwa zambiri

    [52] “Ndipo (ku Munda wamtenderewo) adzakhala ndi akazi oyang’ana amuna awo okha basi, ofanana misinkhu

    [53] “Izi ndi zomwe mukulonjezedwa pa tsiku la chiweruziro

    [54] “Ndithu izi ndizopatsa Zathu zosatha

    [55] “Awa ndimalipiro (a oopa Allah)! Koma opyola malire (ndi kunyoza aneneri awo), ali ndi mabwelero oipa

    [56] “(Omwe ndi) Jahannam adzailowa (ndi kupseleramo). Taonani kuipa kwa malo wokakhazikikamo

    [57] “Awa ndimadzi wotentha kwambiri, ndi mafinya (a anthu a ku Moto). Choncho awalaweko

    [58] “Ndi zilango zina zambiri zonga zimenezi zamitundumitundu

    [59] “(Kudzanenedwa kwa opyola malire, omwe ndiatsogoleri a opembedza mafano): “Gulu ili lalikulu, lilowa nanu ku Moto; (omwe adali okutsatirani. Ndipo atsogoleri adzati): Siolandiridwa (mwamtendere). Ndithu iwo ngolowa ku Moto.”

    [60] “(Otsatira adzanena): “Ndithu tembeleroli likuyenera inu, (limene mukutitembelera ife) chifukwa inu ndiamene mudadzetsa chilangochi potinyenga ife (ndi kutiitanira kunjira yopotoka), taonani kuipa malo okhazikikamo (Jahannam)!”

    [61] “(Otsatira) adzanena: “E Mbuye wathu! Muonjezereni chilango ku Moto pamwamba pa chilango amene watidzetsera chilangochi.”

    [62] “Ndipo (anthu a ku Moto) adzanena: “Kodi nchifukwa ninji sitikuwaona anthu aja omwe timawawerengera kuti ngoipa (pa dziko lapansi)

    [63] “Kodi tidawachitira chipongwe (pa dziko lapansi koma taonani sadalowe nafe ku Moto). Kapena kuti maso athu sakuwaona?”

    [64] “Ndithu zimenezo, zokangana anthu a ku Moto nzoona

    [65] “Nena (kwa iwo): “Ndithu ine ndine mchenjezi (wochenjeza za chilango cha Allah). Palibe wopembedzedwa mwachoonadi, koma Allah Mmodzi Yekha Wopambana

    [66] “Mbuye wathambo ndi nthaka, ndi zapakati pake; wamphamvu zoposa; Wokhululuka machimo kwambiri (kwa yemwe walapa ndi kumkhulupirira).”

    [67] “Nena (kwa iwo iwe Mtumiki {s.a.w}): “Ichi (chimene ndakuchenjezani nachochi) ndinkhani yaikulu.”

    [68] ““Inu, za chimenechi, mukunyozera!”

    [69] ““Sindimadziwa chilichonse za akuluakulu a pamwamba (angelo) pamene amakangana (za kulengedwa kwa Adam).”

    [70] “Palibe china chimene chavumbulutsidwa kwa ine, koma (kuti ndikuuzeni mawu awa oti): “Ine ndine mchenjezi (wanu) woonekera.”

    [71] “(Akumbutse) pamene Mbuye wako adanena kwa angelo: “Ine ndilenga munthu kuchokera ku dothi, (yemwe ndi Adam).”

    [72] ““Ndikammaliza ndi kumuuzira mzimu wochokera kwa Ine, igwani pansi momulemekeza.”

    [73] “Choncho angelo onse anagwa pansi momulemekeza

    [74] “Kupatula Iblis; adadzikweza, ndipo adali mmodzi mwa okana

    [75] “(Allah) adati: “E iwe Iblis! Nchiyani chakuletsa kugwa pansi ndi kuchilemekeza chimene ndachilenga ndi manja Anga (popanda kutuma wina)? Kodi wadzikweza kapena uli mmodzi wa odziika pamwamba?”

    [76] “(Iblis) adanena: “Ine ndine wabwino kuposa iye (Adam); chifukwa ine mudandilenga kuchokera ku Moto, ndipo iye mudamulenga kuchokera kudongo.”

    [77] “(Allah) adanena (kwa Iblis): “Tuluka m’menemo (m’gulu la angelo apamwamba); ndithu iwe ngopirikitsidwa (ku chifundo cha Allah).”

    [78] ““Ndipo ndithu matembelero Anga akhala pa iwe kufikira tsiku lamalipiro.”

    [79] “(Iblis) adati: “E Mbuye wanga! Ndipatseni nthawi kufikira tsiku louka ku imfa.”

    [80] “(Allah) adati: “Ndithu iwe ndiwe mmodzi wa wopatsidwa nthawi.”

    [81] ““Kufikira tsiku la nthawi yodziwika (imene yaikidwa).”

    [82] “(Iblis) adati: “Choncho kupyolera mu ulemelero Wanu ndikulumbira kuti ndiwasokoneza onse.”

    [83] ““Kupatula akapolo Anu omwe ali osankhidwa (oyeretsedwa) mwa iwo. (Pa iwo ndilibe nyonga zilizonse).”

    [84] “(Allah) adati: “Ndikulumbira mwachoonadi ndipo ndikunena choona.”

    [85] ““Ndithudi, ndidzazadzitsa Jahannam ndi ochokera ku mtundu wako ndi omwe adzakutsate mwa iwo (ana a Adam) onse.”

    [86] “Nena (iwe Mtumiki{s.a.w}, kwa anthu ako): “Sindikukupemphani malipiro pa zimenezi ndiponso ine simmodzi wa odzikakamiza (pa zinthu zosandiyenera)

    [87] “(Qur’an) sichina koma ndichikumbutso ndi chiphunzitso kwa zolengedwa zonse

    [88] “Ndipo posachedwa mudziwa, (inu otsutsa, kuona kwa) nkhani zake.”

    Magulu

    Surah 39

    [1] “Kuvumbulutsidwa kwa Buku ili kwachokera kwa Allah, Mwini mphamvu zoposa; Mwini nzeru zakuya

    [2] “Ndithu Ife takuvumbulutsira iwe buku ili mwamtheradi; choncho mpembedze Allah momyeretsera mapemphero Iye yekha

    [3] “Dziwani kuti Allah Ngolandira mapemphero oyera, (opanda kuphatikizidwa ndi zina). Koma amene adzipangira athandizi kusiya Allah, (akumanena kuti): “Ife sitikuwapembedza awa, koma tikutero ndi cholinga choti atifikitse pafupi ndi Allah.” Ndithu Allah, adzaweruza pakati pawo (pakati pa okhulupirira Allah, ndi okana) pa zimene akusiyana. Ndithu Allah saongola amene ali wabodza; wokanira zedi (Allah)

    [4] “Allah akadafuna kupeza mwana, akadasankha yemwe akum’funa mzomwe adalenga. Wapatukana ndi zimenezo! Iye ndi Allah Mmodzi; Wogonjetsa; (Wochita zimene wafuna)

    [5] “Adalenga thambo ndi nthaka mwamtheradi. Amakulunga usiku mu usana; ndipo amakulunga usana mu usiku. Ndipo dzuwa ndi mwezi wazichita kuti zitumikire monga momwe afunira. Zonsezi zikuyenda kufikira pa nthawi yake imene yaikidwa. Dziwani kuti Iye (Allah) Ngwamphamvu zoposa; Ngokhululuka kwambiri

    [6] “Adakulengani kuchokera mu mzimu umodzi (womwe ndi Adam; tate wa anthu). Ndipo kenako adalenga kuchokera mu mzimu umenewo mnzake, (mkazi wake, Hawa); ndipo adakutsitsirani mitundu isanu ndi itatu ya nyama ziwiriziwiri (zomwe ndi: Ngamira yaimuna ndi yaikazi, ng’ombe yaimuna ndi yaikazi, mbuzi yaimuna ndi yaikazi ndi nkhosa yaimuna ndi yaikazi. Zonse pamodzi, zisanu ndi zitatu, zomwe mumathandizidwa nazo kwambiri). Amakuumbani m’mimba mwa mayi anu mkaumbidwe kosiyanasiyana, mu mdima utatu; (mu mdima wa mimba, chiberekero ndi mdima wa nembanemba). Ameneyo (adakuchitirani zonsezi), ndi Allah, Mleri wanu; ufumu ngwa Iye. Palibe wopembedzedwa mwa choona, koma Iye. Kodi nanga mukutembunuzidwa bwanji (kusiya Allah)

    [7] “Ngati mukana ndithu Allah Ngodzikwaniritsa sasaukira kwa inu (chikhulupiliro chanu ndi kuthokoza kwanu); koma sakonda kukanira kwa anthu Ake. Ngati mumthokoza (pa mtendere Wake umene uli pa inu) akuyanja kuthokoza kwanuko. Ndipo mzimu wochimwa sungasenze machimo a mzimu wina. Kenako kobwerera kwanu nkwa Mbuye wanu, ndipo adzakuuzani zimene mudali kuchita. Ndithu Iye Ngodziwa (zinsinsi) za m’mitima

    [8] “Ndipo masautso akampeza munthu, amapempha Mbuye wake ndi kutembenukira kwa Iye (pomwe chikhalirecho adali kumnyoza). Kenako (Mbuye wake) akampatsa mtendere wochokera kwa Iye (waukulu), amaiwala (masautso aja) omwe adali kumpempha Allah kuti amchotsere asadampatse mtenderewo, ndipo kenako ndikumpangira Allah milungu inzake kuti asokeretse ku njira Yake. Nena (iwe Mtumiki kwa yemwe ali ndi chikhalidwe chotere): “Sangalala ndi kukanira kwako (mtendere wa Allah) kwa nthawi yochepa. Ndithu iwe ndi mmodzi wa anthu aku Moto.”

    [9] “Kodi yemwe akudzichepetsa (kwa Allah ndi kumpembedza) pakati pa usiku uku akugwetsa nkhope pansi ndi kuimilira, kuopa tsiku la chimaliziro ndi kuyembekezera chifundo cha Mbuye wake, (kodi angafanane ndi yemwe amapempha Allah akakhala pa mavuto pokha, akakhala pa mtendere ndikumuiwala?) Nena (kwa iwo, iwe Mtumiki {s.a.w}): “Kodi amene akudziwa ndi amene sakudziwa, ngofanana?” Ndithu ndi eni nzeru amene amalingalira

    [10] “Nena (kwa iwo mau Anga akuti): “E inu akapolo Anga amene mwakhulupirira! Muopeni Mbuye wanu. Ndithu amene achita zabwino zotsatira zake nzabwino padziko lapansi, ndipo dziko la Allah ndilophanuka. (Pirirani chifukwa chosiya midzi yanu ndi abale). Ndithu opirira adzalipidwa malipiro awo mokwana mopanda mulingo.”

    [11] “Nena: “Ine ndalamulidwa kuti ndimpembedze Allah momuyeretsera mapemphero Ake (posamphatikiza ndi aliyense pa mapemphero, kapena kupemphera mwa chiphamaso).”

    [12] ““Ndalamulidwanso kuti ndikhale woyamba mwa ogonjera (malamulo Ake).”

    [13] “Nena: “Ine ndikuopa chilango cha tsiku lalikulu, (loopsa), ngati ndinyoza Mbuye wanga.”

    [14] “Nena (kwa iwo, iwe Mneneri {s.a.w}): “Ndi Allah Yekha ndikumpembedza pomuyeretsera Iye mapemphero anga.”

    [15] ““Choncho pembedzani zimene mwafuna, kumsiya Iye.” Nena (kwa iwo): “Ndithu otaika ndi kuonongeka kwakukulu, ndi amene adzitaya okha, (adziluzitsa okha), ndi maanja awo, patsiku la Qiyâma. Dziwa, ndithu kumeneko ndiko kuluza koonekera.”

    [16] “Pa iwo padzakhala misanjikosanjiko ya moto ndiponso pansi pawo. Ndi (chilango) chimenechi, Allah akuwaopseza nacho akapolo Ake. “E inu akapolo Anga! Ndiopeni!”

    [17] “Ndipo amene apatukana nawo mafano ndi satana posiya kuzipembedza, ndikusiya kuziyandikira, ndipo mmalo mwake nkutembenukira kwa Allah (pa zochita zawo zonse), nkhani yabwino njawo (ponseponse). Auze nkhani yabwino akapolo Anga

    [18] “Amene akumvetsera mawu ndi kutsatira amene ali abwino kwambiri. Iwowo ndi amene Allah wawaongola. Ndipo iwowo ndiwo eni nzeru

    [19] “Kodi yemwe chiweruzo cha chilango chatsimikizika pa iye, (mungamteteze)? Kodi iwe ungampulumutse yemwe ali m’Moto

    [20] “Koma amene aopa Mbuye wawo, iwo adzakhala nazo Nyumba zikuluzikulu zimene zamangidwa mosanjikizana, mitsinje ikuyenda pansi pake. Ili ndi lonjezo lochokera kwa Allah. Allah saphwanya lonjezo

    [21] “Kodi suona kuti Allah amatsitsa madzi kuchokera kumwamba, ndipo amawalowetsa mu akasupe mkati mwa nthaka, kenako amatulutsa ndi madziwo mbewu zosiyana mitundu: (chimanga, mpunga, tirigu, ndi zina zotere). Ndipo kenako zimauma (pambuyo pokhala zobiriwira); umaziona zili zachikasu. Kenako amazichita kukhala zidutswazidutswa? Ndithu muzimenezo muli chikumbutso kwa eni nzeru (zofufuzira zinthu)

    [22] “Kodi amene Allah watsekula chifuwa chake povomereza Chisilamu, kotero kuti iye akuyenda mkuunika kwa Mbuye wake, (angafanane ndi yemwe akunyozera kupenyetsetsa zisonyezo za Allah?) Kuonongeka kwakukulu kuli pa ouma mitima yawo posakumbukira Allah (ndi kulabadira Qur’an). Iwo ali m’kusokera koonekera

    [23] “Allah wavumbulutsa nkhani yabwino zedi yomwe ndi buku logwirizana nkhani zake; (losasemphana). Lobwerezabwereza (malamulo ake). Makungu a omwe amaopa Mbuye wawo amanjenjemera ndi ilo. Kenako makungu awo ndi mitima yawo zimakhazikika pokumbukira Allah. Buku limeneli ndi chiongoko cha Allah; ndi ilo, akumuongola amene wamfuna. Ndipo amene Allah wamulekelera kuti asokere (chifukwa chonyozera kwake choona), sangakhale ndi womuongola (ndi ompulumutsa ku chionongeko)

    [24] “Kodi yemwe adzakhala akudzitchinjiriza ndi nkhope yake (uku manja atanjatidwa) ku chilango choipa pa tsiku la Qiyâma, (angafanane ndi yemwe adzakhala mchisangalalo mminda ya mtendere?” Ndipo kudzanenedwa kwa oipa: “Lawani zoipa za zochita zanu.”)

    [25] “Amene adalipo patsogolo pawo, adatsutsa. Ndipo chilango chidawadzera kuchokera komwe sadali kuyembekezera

    [26] “Choncho Allah adawalawitsa kunyozeka pa moyo wa pa dziko lapansi; koma ndithu chilango cha tsiku la chimaliziro nchachikulu zedi (kuposa chilango cha m’dziko lapansi) akadakhala akudziwa

    [27] “Ndithu m’buku ili la Qur’an taperekamo mafanizo osiyanasiyana kwa anthu kuti akumbukire

    [28] “Qur’an ya Chiarabu yopanda zokhota, kuti iwo aope (Allah)

    [29] “Allah wapereka fanizo la munthu wotumikira mabwana awiri omwe ngokangana pa za iye, ndi munthu yemwe akutumikira bwana mmodzi. Kodi awiriwa ngofanana? Kuyamikidwa konse nkwa Allah! Koma ambiri a iwo sadziwa

    [30] “Ndithu iwe udzafa; naonso adzafa

    [31] “(Ndipo) kenako, inu patsiku la Qiyâma mudzakangana pamaso pa Mbuye wanu

    [32] “۞ Kodi ndiyani wachinyengo wamkulu woposa yemwe akumnamizira Allah zabodza, ndi kutsutsa choona chikamdzera? Kodi Jahannam simalo a okanira

    [33] “Ndipo amene wadza ndi choona, naachikhulupirira, iwowo ndiwo oopa Allah

    [34] “Adzapeza zomwe adzakhumba kwa Mbuye wawo. Imeneyo ndiyo mphoto ya ochita zabwino

    [35] “Kuti Allah awafafanizire zoipa za zochita zawo, ndi kuti awalipire malipiro awo chifukwa cha zabwino zomwe adali kuchita

    [36] “Kodi Allah sali Wokwanira kwa kapolo Wake? Koma akukuopseza ndi zina zosakhala Iye! Ndipo yemwe Allah wam’lekelera kuti asokere, ndithu alibe womuongola

    [37] “Ndipo amene Allah wamuongola, palibe amene angathe kumsokeretsa. Kodi Allah sali Mwini mphamvu zoposa; Wokhoza kubwezera chilango

    [38] “Ndipo ukawafunsa (kuti) ndani adalenga thambo ndi nthaka, ndithu anena (kuti ndi) “Allah.” Nena: “Kodi mukuona bwanji, amene mukuwapembedza kusiya Allah angandichotsere masautso ake ngati Allah atafuna kundipatsa masautso? Kapena Allah atafuna kundichitira chifundo, kodi iwo angatsekereze chifundo Chakecho?” Nena: “Allah akundikwanira! Kwa Iye, atsamire otsamira.”

    [39] “Nena: “E inu anthu anga! Chitani zochita zanu mmene mungathere. Nanenso ndichita (mmene ndingathere). Koma posachedwa mudziwa

    [40] “Amene chim’dzere chilango chomuyalutsa, ndi kum’fikira iye chilango chamuyaya.”

    [41] “Ndithu ife takuvumbulutsira buku ili chifukwa cha anthu (onse) kuti Tiwafotokozere choona. Choncho amene waongoka, zabwino zake nza iye mwini. Koma amene wakhota, ndiye kuti akudzikhotetsa yekha. (Ndipo zoipa za kukhotako zidzakhala pa iye yekha). Ndipo iwe si muyang’anili wawo

    [42] “Allah ndiye amatenga mizimu pa nthawi ya imfa yake ndipo amatenga mizimu yomwe siidafe panthawi yogona tulo. Ndipo amaigwira mizimu imene wailamula kufa, (osaibwezera ku matupi awo). Koma inayo amaitumiza (kumatupi awo, yomwe nthawi yake siidakwane) kuti ikwaniritse nthawi yake imene idaikidwa. Ndithu m’zimenezi muli zisonyezo kwa anthu olingalira

    [43] “Kodi adzipangira awomboli kusiya Allah? Nena: “Ngakhale kuti (awombolio) alibe mphamvu ndi kuzindikira pa chilichonse?”

    [44] “Nena: “Chiombolo chonse chili kwa Allah; ufumu wa kumwamba ndi pansi Ngwake; kenako kwa Iye m’dzabwezedwa.”

    [45] “Ndipo pamene Allah Yekha akutchulidwa, mitima ya amene sakhulupirira tsiku la chimaliziro imanyansidwa; koma akatchulidwa amene sali Iye, iwo amakondwa

    [46] “Nena: “E Allah! Mlengi wa thambo ndi nthaka! Wodziwa zobisika ndi zooneka! Inu mudzaweruza pakati pa akapolo Anu pa zimene adali kusemphana.”

    [47] “Ndipo amene adzichitira zoipa, ngakhale kukadakhala kuti ali nazo zonse za mnthaka pamodzi ndi zina zonga izo, akadadziombola nazo ku chilango choipa cha tsiku la Qiyâma (koma sizikanatheka). Ndipo zidzawaonekera kuchokera kwa Allah, zomwe sadali kuziyembekezera

    [48] “Kukawaonekera kuipa kwa zimene adazichita, ndipo zikawazinga zimene adali kuzichitira chipongwe

    [49] “Pamene munthu mavuto amkhudza, amatipempha (uku ali wodzichepetsa); koma tikampatsa mtendere wochokera kwa Ife, amanena kuti: “Ndapatsidwa mtendere uwu chifukwa chakudziwa kwanga (njira zoupezera).” (Sichoncho) koma mtendere umenewu ndi mayeso; koma ambiri a iwo sadziwa

    [50] “Ndithu adanenanso zonga zimenezi omwe adalipo patsogolo pawo, koma sizidawathandize zimene adali kuchita

    [51] “Choncho, zidawapeza zoipa za zomwe adazichita. Ndipo amene achita chinyengo mwa awa, posachedwa kuwapeza kuipa kwa zomwe achita, ndipo iwo sangamlempheretse (Allah)

    [52] “Kodi iwo sadziwa kuti Allah amamtambasulira zopatsa zake yemwe wamfuna, ndi kumchepetsera (amene wamfuna)? Ndithu m’zimenezi muli malingaliro kwa anthu okhulupirira

    [53] “Nena (kwa iwo mau anga akuti): “E inu akapolo anga! Amene mwadzichitira chinyengo, musataye mtima ndi chifundo cha Allah. Ndithu Allah amakhululuka machimo onse. Ndithu Iye Ngokhululuka kwambiri, Wachisoni chosatha.”

    [54] “Ndipo tembenukirani kwa Mbuye wanu, ndipo m’gonjereni chilango chisadakudzereni. Ndipo zitatero, sim’dzapulumutsidwa

    [55] “Ndipo tsatirani zabwino, zimene zavumbulutsidwa kwa inu kuchokera kwa Mbuye wanu chisadakufikeni chilango mwadzidzidzi pomwe inu simukudziwa!”

    [56] “Kuti mzimu usadzanene: “Kalanga ine! Mzomwe sindidalabadire kumbali ya Allah; ndithu ndidali mmodzi wa ochitira chibwana (zinthu za chipembedzo).”

    [57] “Kapena ungadzanene: “Allah akadandiongola, ndithu ndikadakhala mwa oopa (Allah).”

    [58] “Kapena kunena utaona chilango: “Ndikadatha kubwerera (pa dziko lapansi), ndikadakhala mmodzi wa ochita zabwino.”

    [59] “(Adzauzidwa: “Nchiyani iwe?) Ndithu zidakufika zisonyezo Zanga, ndipo udazitsutsa ndi kudzitukumula; ndipo udali mmodzi wa okanira.”

    [60] “Ndipo tsiku la Qiyâma udzawaona omwe adamnamizira Allah, nkhope zawo zili zakuda. Kodi Jahannam simalo a odzitukumula

    [61] “Ndipo Allah adzawapulumutsa amene adamuopa, chifukwa cha kupambana kwawo. Zoipa sizikawakhudza, ndipo iwo sakadandaula

    [62] “Allah ndiye Mlengi wa chilichonse, ndipo Iye ndi Myang’aniri wa chilichonse

    [63] “Makiyi a kumwamba ndi pansi ali kwa Iye. Ndipo amene akanira zisonyezo za Allah, iwo ndiwo oluza, (otaika)

    [64] “Nena: “Kodi mukundilamula kuti ndipembedze yemwe sali Allah, E inu mbuli?”

    [65] “Ndipo ndithu kwavumbulutsidwa kwa iwe, ndi kwa amene adalipo patsogolo pako (mawu awa:) “Ngati umphatikiza (Allah ndi milungu yabodza), ndithu ntchito zako zionongeka, ndipo ukhala mwa oluza (otaika).”

    [66] “Koma pembedza Allah yekha, ndipo khala mwa othokoza

    [67] “Koma sadamlemekeze Allah, kulemekeza koyenerana Naye, pomwe pa tsiku la Qiyâma nthaka yonse (idzakhala) chofumbata Chake mmanja; ndipo thambo lidzakulungidwa ndi dzanja Lake lamanja. Walemekezeka Allah. Ndipo watukuka ku zimene akum’phatikiza nazozi

    [68] “Ndipo (pamene) lipenga lidzaimbidwa, onse a kumwamba ndi pansi adzakomoka kupatula amene Allah wamfuna. Kenako lidzaimbidwa lachiwiri; pamenepo (onse) adzauka; adzakhala akuyang’ana (modabwa: “Nchiyani chachitika!”)

    [69] “Ndipo nthaka (tsiku limenelo) idzawala ndi kuunika kwa Mbuye wake; ndipo akaundula a zochita, adzaikidwa. Ndipo adzabweretsedwa aneneri ndi mboni (kuti aikire umboni pa anthu). Ndipo padzaweruzidwa pakati pawo mwachoonadi; ndipo iwo sadzaponderezedwa

    [70] “Ndipo mzimu uliwonse udzalipidwa zimene udachita; ndipo Iye (Allah) Ngodziwa kwambiri zimene akuchita

    [71] “Ndipo amene adakanira, adzakusidwa kunka ku Jahannam ali magulumagulu kufikira pomwe adzaifikira, makomo ake adzatsekulidwa, ndipo alonda ake adzawauza: “Kodi sadakudzereni aneneri ochokera mwa inu okulakatulirani zisonyezo za Mbuye wanu, ndi kukuchenjezani za kukumana kwanu ndi tsiku lanuli?” Adzayankha (nati): “Inde, adatidzera; koma lidatsimikizika liwu la chilango pa okanira.”

    [72] “Kudzanenedwa: “Lowani makomo a ku Jahannam; mukakhalitse mmenemo (nthawi yaitali).” Taonani kuipa malo a odzitukumula

    [73] “Ndipo amene adamuopa Mbuye wawo, adzakusidwa kunka ku Munda wamtendere ali magulumagulu, mpaka kufikira pomwe adzaufika. (Adzapeza kuti) makomo ake atsekulidwa. Alonda ake adzanena kwa iwo: “Mtendere ukhale pa inu mwachita bwino! Lowani mmenemo, khalani nthawi yaitali.”

    [74] “Ndipo iwo adzanena: “Kuyamikidwa konse nkwa Allah, Amene watitsimikizira lonjezo Lake, ndipo watipatsa dziko (kuti n’lathulathu). Tikukhala m’Minda yamtendereyi paliponse tafuna.” Taonani kukoma malipiro aochita zabwino

    [75] “Ndipo udzaona angelo atazungulira mphepete mwa Arsh (Mpando wachifumu) uku akulemekeza ndi kutamanda Mbuye wawo. Ndipo padzaweruzidwa pakati pawo mwachoonadi, ndipo kudzanenedwa (ndi zolengedwa zonse): “Kuyamikidwa nkwa Allah, Mbuye wa zolengedwa!”

    Wokhululukira

    Surah 40

    [1] “Hâ-Mîm

    [2] “Kuvumbulutsidwa kwa buku (ili) kwachokera kwa Allah Wamphamvu zoposa, Wodziwa kwambiri

    [3] “Wokhululuka machimo, Wolandira kulapa (kwa yemwe walapa), Wolanga mwaukali (kwa yemwe wapitiriza kunyoza Allah), Mwini kupereka mtendere. Palibe wopembedzedwa mwa choona koma Iye; kobwerera nkwa Iye

    [4] “Sangatsutsane pa zisonyezo za Allah kupatula amene akanira. Choncho kusakunyenge kuyendayenda kwawo pa dziko (kunka nachita malonda ndi kupeza phindu lalikulu ndi malondawo popanda chovuta; posachedwa tiwalanga)

    [5] “Iwo kulibe, anthu a Nuh adakaniranso pamodzi ndi makamu a anthu omwe adali kuda aneneri, m’badwo wa Nuh utatha; ndipo m’badwo uliwonse udaikira mtima kuchita choipa pa mneneri wawo kuti am’gwire (ndi kumupha). Adali kutsutsana poteteza chachabe kuti ndi uwo (mtsutso wawowo) achotse choona. Ndipo ndidawaononga kotheratu. Tayang’ana, chidali bwanji chilango Changa (pa iwo)

    [6] “Chonchonso latsimikizika liwu la chilango pa amene akanira (iwe Mtumiki {s.a.w}) chifukwa iwo ndi anthu a ku Moto (kamba kosankhakukanira ndi kusiya kukhulupirira)

    [7] “Amene akusenza Arsh (Mpando wachifumu) ndi amene ali mmphepete mwake, akulemekeza ndi kutamanda Mbuye wawo, ndiponso akumkhulupirira Iye; ndipo akupemphera chikhululuko amene akhulupirira (ponena kuti): “E Mbuye wathu! Chifundo ndi kudziwa kwanu kwakwanira pa chinthu chilichonse. Khululukirani amene alapa ndi kutsatira njira Yanu; ndipo apewetseni ku chilango cha Jahena!”

    [8] ““E Mbuye wathu! Alowetseni ku Minda yamuyaya imene mudawalonjeza, ndi amene adachita zabwino mwa makolo awo ndi akazi awo ndi ana awo. Ndithu inu ndi Amphamvu zoposa, Anzeru zakuya.”

    [9] ““Ndipo apewetseni ku zoipa; tsono amene mudzampewetsa ku zoipa tsiku limenelo, ndiye kuti mwamchitira chifundo. Ndipo kumeneko ndiko kupambana kwakukulu.”

    [10] “Ndithu amene akanira adzaitanidwa (ndi kuuzidwa kuti): “Mkwiyo wa Allah pa inu udali waukulu kuposa mkwiyo wanu pa mitima yanu (yomwe yakulowetsani ku chilango) pamene mudali kuitanidwa ku chikhulupiliro, (ku Chisilamu); ndipo mudali kukanira.”

    [11] “Adzanena: “E Mbuye wathu! Mudatipatsa imfa kawiri; (imfa yoyamba tisanabadwe, ndipo imfa ya chiwiri pa dziko). Ndipo mudatipatsa moyo kawiri; (moyo woyamba wa pa dziko lapansi, ndipo moyo wachiwiri wakuuka kwa akufa). Choncho tavomereza machimo athu. Kodi pali njira yotulukira (ku chilango kuno)?”

    [12] “Zimenezi nchifukwa chakuti akapemphedwa Allah Yekha, mudali kutsutsa. Koma akaphatikizidwa (ndi milungu yabodza) mudali kukhulupirira. Choncho chiweruzo ncha Allah, Wotukuka, Wamkulu

    [13] “Iye ndi Yemwe akukuonetsani zisonyezo Zake (zosonyeza mphamvu Yake yoposa), ndipo akukutsitsirani madzi kumwamba chifukwa cha inu kuti abweretse zokupatsani moyo (monga chakudya ndi zina). Koma palibe amene akukumbukira kwenikweni kupatula amene watembenukira (kwa Allah)

    [14] “Choncho mpempheni Allah pomuyeretsera mapemphero Ake ngakhale (kumuyeretsera kwanu kwa mapempheroko) kuwaipire okanira

    [15] “Iye Ngotukuka ulemelero, Mwini Arsh (Mpando wachifumu); amapereka chivumbulutso (Chake) mwa lamulo lake kwa yemwe wamfuna mwa akapolo Ake kuti achenjeze (anthu za) tsiku lokumana (anthu onse)

    [16] “Tsiku lomwe iwo adzaonekera poyera (kwa Allah). Ndipo palibe chilichonse chidzabisidwa kwa Allah (mzinthu zawo). (Ndipo adzamva kufunsa koopsa ndi yankho loopsa): “Kodi ufumu ngwayani lero? Ngwa Allah, Mmodzi yekha, Wogonjetsa, (woweruza mmene akufunira kwa anthu Ake).”

    [17] “Mzimu uliwonse lero, ulipidwa zimene udachita; palibe kupondereza lero (pochepetsa mphoto kapena kuonjeza chilango). Ndithu Allah Ngwachangu (pa) chiwerengero Chake

    [18] “Achenjeze (iwe Mtumiki {s.a.w}) za tsiku lomwe lili pafupi (Qiyâma), pamene mitima idzakhala ku mmero (chifukwa cha mantha oopsa) atadzadzidwa ndi nkhawa. Wodzichitira chinyengo sazakhala ndi bwenzi ngakhale mpulumutsi womveredwa (powateteza iwo)

    [19] “Iye (Allah ) akudziwa kuyang’ana kwa maso a chinyengo ndi zimene zifuwa zikubisa (mzobisika zonse)

    [20] “Ndipo Allah amaweruza mwa chilungamo. Koma omwe akuwapembedza kusiya Allah, saweruza chilichonse (chifukwa cha kufooka ndi kulephera kwawo). Ndithu Allah Yekha ndiye Wakumva, Woona (chilichonse)

    [21] “Kodi sadayende padziko ndikuona momwe mathero a anthu akale adalili? Adali opambana panyonga ndi mzochitachita zawo za mdziko kuposa iwo, (monga kumanga nyumba zikuluzikulu). Koma Allah adawaononga, psiti! chifukwa cha machimo awo, ndipo adalibe mtetezi ku chilango cha Allah

    [22] “Zimenezo nchifukwa chakuti ankawadzera aneneri awo ndi zizizwa zoonekera poyera, koma adazikanira. Choncho Allah adawaononga motheratu. Iye Ngwanyonga zambiri, Wolanga mokhwima

    [23] “Ndipo ndithu tidamtuma Mûsa ndi zizizwa zathu ndi zisonyezo zamphamvu zoonekera poyera

    [24] “Kwa Farawo ndi Haamana ndi Kaaruna. Ndipo adati: “(Uyu) ndi wamatsenga, wabodza.”

    [25] “Ndipo pamene (Mûsa) adawadzera ndi choona chochokera kwa Ife, (Farawo pamodzi ndi omtsatira) adati: “Iphani ana achimuna a amene akhulupirira naye limodzi; ndipo siyani ana awo achikazi.” Koma ndale za okanira sizakanthu, nzotaika

    [26] “Ndipo Farawo adati: “Ndilekeni ndimuphe Mûsa; ampemphe Mbuye wakeyo (kuti ampulumutse kwa ine). Ine ndikuopera kuti angasinthe chipembedzo chanu, kapena kufalitsa chisokonezo pa dziko.”

    [27] “Ndipo Mûsa adati (kwa Farawo pa modzi ndi anthu ake): “Ine ndadzitchinjiriza ndi Mbuye wanga amenenso ali Mbuye wanu (ku chiwembu) chochokera kwa aliyense wodzikweza, wosakhulupirira za tsiku la chiwerengero

    [28] “Ndipo munthu wokhulupirira, wochokera kubanja la Farawo yemwe adali kubisa chikhulupiliro chake, adawalankhula (anthu ake): “Kodi muphe munthu chifukwa chakuti iye akunena kuti: ‘Mbuye wanga ndi Allah,’ chikhalirecho wakubweretserani zisonyezo zoonekera poyera, zochokera kwa Mbuye wanu? Ndipo ngati ali wabodza pa zomwe akunena ndiye kuti kuipa kwa bodzalo kum’bwerera yekha. Koma ngati ali woona (pazomwe akukulonjezani), ndiye kuti gawo lina la zomwe (chilango) akukulonjezani likupezani; ndithu Allah saongola munthu wopyola malire, wabodza la mkunkhuniza!”

    [29] ““E inu anthu anga! Ufumu walero ngwanu: mwagonjetsa dziko (la Iguputo). Ndani amene angatipulumutse ku chilango cha Allah ngati chitatidzera?” Farawo adati: “Sindikukupatsani maganizo koma okhawo ndikuwaona (kuti ndi abwino) ndiponso sindikukuwongolerani koma kunjira yoongoka.”

    [30] “Ndipo munthu wokhulupirira uja adanena: “E inu anthu anga! Ine ndikukuoperani (za tsiku la masautso) monga tsiku la magulu (omwe adaukira aneneri awo).”

    [31] ““Monga chikhalidwe cha anthu a Nuh, Âdi, Samudi ndi anthu omwe adadza pambuyo pawo. Koma Allah safuna kupondereza akapolo Ake.”

    [32] ““Ndiponso anthu anga! Ine ndikukuoperani tsiku la kuitanizana (anthu).”

    [33] ““Tsiku limene mudzathawa ndi kutembenuza misana yanu; pomwe simudzakhala ndi mtetezi ku chilango cha Allah; ndipo amene Allah wamulekelera kusokera (chifukwa cha zochita zake zoipa), ndiye kuti sangapeze muongoli.”

    [34] “Ndithu adakudzerani kale Yûsuf ndi zisonyezo zoonekera poyera (Mûsa asadadze). Koma simudaleke kuzikaikira zimene adadza nazo kwa inu, kufikira pamene adamwalira, mudati: “Allah sadzatumiza mneneri wina pambuyo pake.” Motero Allah amamulekelera kusokera yemwe ali opyola malire poononga, wokaikira kwambiri

    [35] “Amene akutsutsana za zisonyezo za Allah popanda umboni uliwonse umene wawadzera. (Kutsutsa zisonyezo za Allah) nchokwiitsa Allah kwakukulu ndi kwa amene akhulupirira (mwa Allah). Momwemo ndi momwe Allah amadindira pamtima wa aliyense wodzikuza, wodzitukumula

    [36] “Ndipo Farawo adati: “E iwe Haamana! Ndimangire chipilala kuti ndikafike kunjira,”

    [37] ““Njira za kumwamba kuti ndikamuone Mulungu wa Mûsa. Koma ndithu ine ndikudziwa kuti ameneyu ngonama.” Umo ndi momwe zochita zoipa za Farawo zidakongoletsedwera kwa iye, ndipo adatsekeretsedwa ku njira yoona, ndipo chiwembu cha Farawo sichakanthu, koma choonongeka

    [38] “Ndipo uja adakhulupirira adati: “E inu anthu anga! Nditsatireni; ndikuongolerani ku njira yoongoka.”

    [39] ““E inu anthu anga! Ndithu moyo wa pa dziko lapansi ndichisangalalo (chakutha). Ndithu tsiku lachimaliziro ndiye nyumba yokhazikikamo.”

    [40] ““Amene akuchita choipa sadzalipidwa chinachake koma chofanana ndi chomwe adachita. Ndipo yemwe akuchita zabwino, mwamuna kapena mkazi, uku iye ali okhulupirira, iwowo adzalowa ku Minda ya mtendere. Adzapatsidwa zopatsidwa mmenemo zopanda chiwerengero.”

    [41] ““E inu anthu anga! Chifukwa ninji, ine ndikukuitanirani ku chipulumutso ndipo inu mukundiitanira ku Moto?”

    [42] ““Mukundiitanira kuti ndimkane Allah, ndi kuphatikiza ndi milungu yonama yomwe ine sindikuidziwa, pomwe ine ndikukuitanirani kwa Mwini mphamvu zoposa, Wokhululuka kwambiri?”

    [43] ““Palibe chikaiko, ndithu zomwe mukundiitanirazo (kuti ndizipembedze) zilibe (kuyankha) pempho lililonse pano pa dziko lapansi ngakhale tsiku lachimaliziro. Ndipo kobwerera kwathu nkwa Allah basi. Ndipo, wopyola malire (a Allah) iwowo ndiwo anthu a ku Moto.”

    [44] ““Choncho posachedwa, mudzakumbukira zimene ndikukuuzanizi. Ndipo ine ndikutula zinthu zanga kwa Allah, ndithu Allah akuona za anthu Ake.”

    [45] “Choncho Allah adam’teteza ku zoipa zomwe adam’tchera. Ndipo chilango choipa chidawazungulira anthu a Farawo (pamodzi ndi iye mwini)

    [46] “Zilango za kumoto zikusonyezedwa kwa iwo mmawa ndi madzulo. Ndipo tsiku lomwe Qiyâma idzafika (kudzanenedwa): “Alowetseni anthu a Farawo ku chilango cha ukali kwambiri (choposa chomwe adalandira mmanda mwawo).”

    [47] “Ndipo (akumbutse) pamene azidzatsutsana m’Moto! Pamene ofooka (amene amatsatira) adzanena kwa omwe adali kudzikweza: “Ndithu ife tidali otsatira anu; kodi simungathe kutichotsera gawo lina la chilango cha Moto?”

    [48] “Awo amene adadzikweza adzati: “Ndithu ife tonse tili mommuno. Ndithu Allah waweruza kale pakati pa akapolo (Ake). (Choncho palibe chilichonse chimene tingaphulepo).”

    [49] “Ndipo a ku Moto adzayankhula kwa (angelo) olondera Jahannam: “Mpempheni Mbuye wanu, atipeputsire chilangochi tsiku limodzi.”

    [50] “(Alonda aja) adzati: “Kodi sadakudzereni aneneri anu ndi umboni oonekera poyera?” Iwo adzati: “Inde, (adatidzera. Koma ife tidanyoza).” (Ndipo) adzawauza: “Choncho pemphani nokha. Koma pempho la okanira silili la kanthu, ndi lotaika basi.”

    [51] “Ndithu Ife timapulumutsa aneneri Athu ndi amene akhulupirira pa moyo wa dziko lapansi ndi tsiku limene zidzaimilira mboni (kupereka umboni)

    [52] “Tsiku limene achinyengo sadzawathandiza madandaulo awo, ndipo matembelero adzakhala pa iwo, ndipo pokhala pawo padzakhala poipa kwambiri

    [53] “Ndithu Mûsa tidampatsa chiongoko, ndipo tidawasiira buku ana a Israyeli

    [54] “(Lomwe lidali) chiongoko ndi chikumbutso kwa eni nzeru

    [55] “Choncho pirira, ndithu lonjezo la Allah ndi loona. Ndipo pempha chikhululuko cha machimo ako (ukachimwa), ndipo lemekeza Mbuye wako ndi kumtamanda madzulo ndi m’mawa

    [56] “Ndithu amene akutsutsana pa zisonyezo za Allah popanda umboni umene udawadzera, mmitima mwawo mulibe chilichonse koma kudzitukumula (ndikufuna ukulu), koma saufikira. Dzitchinjirize mwa Allah, ndithu Iye Ngwakumva, Ngopenya

    [57] “Ndithu kulenga kwa thambo ndi nthaka nkwakukulu kuposa kulenga kwa anthu. Koma anthu ambiri sakudziwa

    [58] “Ndipo sali wolingana wakhungu ndi wopenya ndiponso amene akhulupirira ndi kumachita zabwino ndi wochita zoipa. Zimene inu mukumbukira nzochepa, ndithu

    [59] “Ndithu Qiyâma idza; ndipo za iyo palibe chikaiko. Koma anthu ambiri sakhulupirira

    [60] “Ndipo Mbuye wanu wanena: “Ndipempheni, ndikuyankhani; koma amene akudzikweza posiya kundipembedza, adzalowa ku Jahannam ali oyaluka.”

    [61] “Allah ndi Yemwe adakupangirani usiku kuti mupumule mmenemo, ndi usana kukhala wounika (kuti muthe kuchita ntchito zanu). Ndithu Allah ndi Mwini kupereka ufulu kwa anthu. Koma anthu ambiri sathokoza

    [62] “Iyeyo ndiye Allah, Mbuye wanu; Mlengi wa chilichonse palibe wina wopembedzedwa mwa choona, koma Iye. Nanga kodi mukutembenuzidwa chotani (kuchoka ku zoona)

    [63] “Momwemo ndi mmene adatembenuziridwa amene adali kutsutsa zisonyezo za Allah

    [64] “Allah ndi Amene adakupangirani nthaka kukhala pamalo anu okhalapo, ndi thambo kukhala ngati denga (losagwa); ndipo adakujambulani maonekedwe ndikukongoletsa maonekedwe anu; ndipo adakupatsani zinthu zabwino. Ameneyo ndiye Allah, Mbuye wanu. Choncho walemekezeka Allah, Mbuye wa zolengedwa.”

    [65] “Iye Ngwamoyo Wamuyaya; palibe wopembedzedwa wina, koma Iye. Choncho mpembedzeni momuyeretsera chipembedzo. (Musapembedze milungu ina mophatikiza ndi Iye). Kuyamikidwa konse nkwa Allah, Mbuye wa zolengedwa

    [66] “Nena: “Ine ndaletsedwa kupembedza amene mukuwapembedza kusiya Allah, pamene zidandidzera zisonyezo zoonekera kuchokera kwa Mbuye wanga; ndipo ndalamulidwa kugonjera Mbuye wa zolengedwa zonse.”

    [67] “Iye ndi Amene adakulengani kuchokera ku dothi, kenako kuchokera ku dontho la umuna, kenako kuchokera mmagazi; kenako ndikukutulutsani muli khanda; ndipo kenako (adakusiyani) kuti mufike nthawi yanyonga zanu. Ndipo kenako (adakulekani) kuti mukhale nkhalamba. Ndipo ena a inu amapatsidwa imfa asadaifike (nthawi ya ukalamba) nkuti muifikire nthawi imene yaikidwa; (zoterezi nkuti inu) mukhale ndi nzeru

    [68] “Iye ndi Yemwe amapereka moyo ndi kupereka imfa; ndipo akafuna kuchita chinthu ndithu amanena kwa chinthucho: “Chitika,” ndipo chimachitika

    [69] “Kodi sukuona amene akutsutsana za zisonyezo za Allah? Kodi nchotani akutembenuzidwa (kusiya choonadi)

    [70] “Amene alitsutsa buku ndi zomwe tidawatuma nazo atumiki athu; koma posachedwa adziwa

    [71] “Pamene magoli ali m’makosi mwawo ndi unyolo (uli mmiyendo) akukokedwa

    [72] “M’madzi otentha, kenako m’moto akuotchedwa

    [73] “Kenako adzauzidwa: “Ili kuti (milungu) imene mudali kuiphatikiza (ndi Allah),”

    [74] ““Mmalo mopembedza Allah?” Adzanena: “Yatisowa, koma chiyambire kale sitidali kupembedza chilichonse (kupatula Inu).” Umo ndi momwe Allah akuwalekelera kusokera okanira

    [75] ““Izi, (zimene zakupezani ku Moto kuno), nchifukwa chakuti mudali kudzikweza pa dziko mosayenera. Ndiponso chifukwa chakuti mudali kunyada

    [76] “Lowani m’makomo a Jahannam; mukhala mmenemo nthawi yaitali. Taonani kuipa malo a odzikweza!”

    [77] “Chonco pirira, ndithu lonjezo la Allah ndiloona. Mwina tikusonyeza zina mwa zomwe tawalonjeza, kapena tikupatsa imfa (usadazione. Basi, palibe chikaiko, zichitika chifukwa chakuti onse) adzabwezedwa kwa Ife

    [78] “Ndithu tidawatuma atumiki patsogolo pako; ena mwa iwo tidakusimbira (nkhani zawo ndi maina awo). Ena mwa iwo sitidakusimbire. Sikudali kotheka kwa mtumiki aliyense kudzetsa chozizwitsa mwa yekha, koma ndi chifuniro cha Allah. Ndipo lamulo la Allah likadzadza, kudzaweruzidwa mwa choonadi. Ndipo ochita zachabe panthawi imeneyo adzataika; (adzaluza)

    [79] “Allah ndi Yemwe wakupangirani nyama kuti mudzizikwera zina mwa izo, ndipo zina mwa izo kuti muzidya

    [80] “Ndipo mmenemo mulinazo zokuthandizani zambiri; ndipo kupyolera mzimenezo mukupeza zokhumba za mitima yanu; pa izo, ndi pa zombo, mukunyamulidwa

    [81] “Ndipo (Iye) amakuonetsani zisonyezo Zake. Kodi ndi ziti m’zisonyezo za Allah zimene mukuzikana

    [82] “Kodi sadayende padziko ndikuona momwe adalili mathero a omwe adali patsogolo pawo? Adali ochuluka kwambiri kuposa iwo; ndiponso adali anyonga kwambiri ndi ochulukitsa zomangamanga mdziko. Koma sizidawathandize zimene adali kuchita

    [83] “Koma pamene atumiki awo adawadzera ndi zisonyezo zoonekera, adakondwera ndi kudziwa komwe adali nako, (ndipo sadalabadire zomwe atumiki adadza nazo). Choncho zidawazinga zimene adali kuzichitira chipongwe

    [84] “Ndipo pamene adachiona chilango Chathu, adanena (kuti): “Takhulupirira mwa Allah Yekha, ndipo tikuzikana zimene tidali kumphatikiza nazo.”

    [85] “Koma chikhulupiliro chawo sichidali chowathandiza panthawi imeneyo, pomwe adali atachiona kale chilango Chathu. Ichi ndi chizolowezi cha Allah chomwe chidapita pa akapolo (Ake onse kuti chilango chikadza, kulapa sikuvomerezedwa). Choncho pamenepo, okanira adaluza

    Zofotokozedwa Mwatsatanetsatane

    Surah 41

    [1] “Hâ-Mîm

    [2] “(Qur’an iyi) ndichivumbulutso chochokera kwa (Allah) Wachifundo chambiri, Wachisoni chosatha

    [3] “(Ili) ndi buku lomwe ma Ayah ake afotokozedwa (bwino pokhudza malamulo a zamdziko ndi tsiku lachimaliziro); chowerengedwa (chimene chavumbulutsidwa) m’chiyankhulo cha Chiarabu kwa anthu ozindikira (tsatanetsatane wa malamulo ake)

    [4] “Likunena nkhani yabwino (kwa ochita zabwino) ndi kuchenjeza (anthu ochita zoipa); koma ambiri a iwo (Aquraish) ainyoza kotero kuti sakumva; (kumva kothandizidwa nalo ndi kulilingalira)

    [5] “Ndipo akunena (kuti): “Mitima yathu (yaphimbidwa) m’zivindikiro, ku zomwe ukutiitanirazo, ndipo m’makutu mwathu muli kulemera kwa ugonthi; choncho pakati pathu ndi pakati pa iwe pali chotsekereza (chotchinga); tero chita (zakozo); nafe tichita (zathu; aliyense wa ife asalowelere za mnzake).”

    [6] “Nena: “Ndithu, ine ndi munthu monga inu; kukuvumbulutsidwa kwa ine (kuchokera kwa Allah) kuti ndithu Mulungu wanu ndi Mulungu Mmodzi; choncho lungamani kwa Iye ndipo mpempheni chikhululuko (pa zimene mwakhala mukumchimwira)” Ndipo kuonongeka kwakukulu kuli pa ophatikiza (Allah ndi zinthu zina)

    [7] “Amene sapereka chopereka (Zakaat), ndiomwe akukanira za tsiku lachimaliziro

    [8] “Ndithu amene akhulupirira ndi kumachita zabwino, pa iwo padzakhala malipiro osadukiza (osatha)

    [9] “Nena: “Kodi inu mukumkanira yemwe adalenga nthaka mmasiku awiri (okha)? Ndipo mukumpangira milungu (ina)? Iyeyo ndiye Mbuye wa zolengedwa zonse.”

    [10] “Ndipo adaika pamenepo mapiri ataliatali pamwamba pake, ndi kudalitsapo (ndi madzi, mmera, ndi ziweto), ndipo adayesa mmenemo zakudya zake (za okhala pa nthakapo; zimenezi adadzichita) mmasiku anayi; (izi) nzokwanira kwa ofunsa (zakalengedwe ka nthaka ndi zamkati mwake)

    [11] “Kenako adalunjika ku thambo (malunjikidwe ogwirizana ndimomwe Iye alili mosafanana ndi zolengedwa zake), pomwe ilo (thambolo) lidali utsi. Ndipo adati kwa ilo ndi nthaka: “Idzani, mofuna kapena mokakamizidwa (tsatirani lamulo Langa).” Izo zidayankha kuti: “Tadza mofuna.”

    [12] “Choncho adakwaniritsa kulenga thambo zisanu ndi ziwiri mmasiku awiri, ndipo thambo lililonse adalidziwitsa ntchito yake (polilamula zochita zake). Ndipo tidakongoletsa thambo lapafupi (ndi inu) ndi nyenyezi (zounikira dziko lapansi), ndiponso kuti zizilondera kumwamha (kuti ziwanda zisamapite kukamvera za kumwamba). Uwu ndi muyeso wa Mwini mphamvu, Wodziwa kwambiri

    [13] “Koma ngati anyozera (kukhulupirira), nena: “Ndikukuchenjezani za chilango monga chilango cha Âdi ndi Samud.”

    [14] “Pamene aneneri adawadzera patsogolo pawo ndi pambuyo pawo (ndikuwauza): “Musapembedze (milungu ina), koma Allah,” adati: “Mbuye wathu akadafuna, akadatsitsa angelo (kudzatilalikira, osati anthu monga inu). Choncho ndithu ife tikuzikana zimene mwatumidwa nazozo.”

    [15] “Tsono Âdi adadzikweza pa dziko mosayenera, ndipo adati: “Ndani wamphamvu kuposa ife?” Kodi saona kuti Allah Yemwe adawalenga ndi Mwini mphamvu zambiri kuposa iwo? Koma adapitiriza kukanira zozizwitsa Zathu

    [16] “Choncho tidawatumizira mphepo ya mkuntho yozizira kwabasi mmasiku amatsoka, kuti tiwalawitse chilango chowasambula pamoyo wa pa dziko lapansi; ndipo chilango cha tsiku lachimaliziro ndi choyalutsa kwambiri; ndipo iwo sadzapulumutsidwa

    [17] “Naonso Asamudu tidawasonyeza (njira yabwino ndi njira yoipa), ndipo adakonda ndi kusankha kusokera kusiya chiongoko; ndipo udawapeza nkuwe wa chilango choyalutsa chifukwa cha machimo amene adali kuchita

    [18] “Koma tidawapulumutsa (ku chilango chimenechi) amene adakhulupirira ndipo anali kumuopa (Allah)

    [19] “Ndipo (akumbutse, iwe Mtumiki), tsiku lomwe adani a Allah adzasonkhanitsidwa kunka nawo ku Moto, uku akukusidwa (onse, oyamba ndi omalizira)

    [20] “Kufikira pomwe adzaufikira (Moto); makutu awo ndi maso awo ndi khungu lawo zidzawachitira umboni pa zomwe adali kuchita (pa dziko lapansi)

    [21] “Ndipo adzanena (adani a Allah) ku makungu awo: “Bwanji mukutiperekera umboni woipa?” Zidzati: “Allah watiyankhulitsa, Amene amayankhulitsa chilichonse; ndipo Iye ndi Amene adakulengani (mkulenga) koyamba (pomwe simudali kanthu), ndiponso kwa Iye Yekha ndiko mudzabwezedwa

    [22] “Simudathe kubisa (ntchito zanu zoipa ku ziwalo zanu) poopera kuti kumva kwanu ndi kuyang’ana kwanu ndi makungu anu zingakuperekereni umboni woipa! Koma mudali kuganiza kuti Allah sadziwa zambiri zomwe mukuchita (mobisa)

    [23] “Ndipo amenewo ndi maganizo anu omwe mudali kumganizira (nawo) Mbuye wanu adakuonongani, ndipo (lero tsiku la Qiyâma) muli m’gulu la otaika.”

    [24] “Choncho ngakhalc atapirira (ku zopweteka zawo), moto ndiwo mabwelero awo ndi kokhazikika kwawo kwa muyaya. Ngati atapempha chiyanjo cha Allah pa iwo, iwo sadzakhala m’gulu la oyanjidwa

    [25] “Ndipo tidawakonzera iwo abwenzi oipa (padziko lapansi), choncho adawakometsera zamtsogolo mwawo ndi za pambuyo pawo ndipo liwu la chilango lidatsimikizika pa iwo pamodzi ndi mibadwo yomwe idapita kale ya ziwanda ndi anthu, ndithu iwo adali otaika

    [26] “Akunena okanira (kuuzana okhaokha): “Musamvetsere Qur’an iyi, koma sokoserani pomwe ikuwerengedwa (kuti asaimvere aliyense) kuti mwina mupambane.”

    [27] “Ndithu tiwalawitsa amene akanira chilango choopsa (pa zochita zawo zoipa, makamaka pakuithira Qur’an nkhondo), ndipo ndithu tiwalipira malipiro oipitsitsa chifukwa cha zoipa zomwe adali kuchita

    [28] “Imeneyo ndi mphoto yoyenera ya adani a Allah, yomwe ndi Moto. Mmenemo adzakhala muyaya. Imeneyi ndi mphoto ya zimene adali kuzikanira m’zisonyezo Zathu

    [29] “Ndipo okanira adzanena (ali mkati mwa Moto): “E Mbuye wathu! Tisonyezeni (magulu awiri) amene adatisokeretsa ochokera m’ziwanda ndi anthu kuti tiwaike pansi pa mapazi athu, kuti akhale mwa apansi (mu ulemelero ndi malo).”

    [30] “Ndithu amene anena (kuti): “Mbuye wathu ndi Allah,” (povomereza umodzi Wake), kenako nkupitiriza kulungama pa malamulo Ake, angelo amawatsikira iwo nthawi yakufa (uku akuti): “Musaope (pa zomwe mukumane nazo). Ndipo musadandaule (pazomwe mwazisiya). Ndipo sangalalani ndi Munda wamtendere umene mudalonjezedwa (kupyolera mmalirime a aneneri).”

    [31] “(Angelo amanena kwa iwo): “Ife ndi athangati anu pamoyo wa pa dziko lapansi (pokulimbikitsani panjira yolungama), ndi tsiku lachimaliziro (pokupempherani chipulumutso kwa Allah); inu mukapeza kumeneko chilichonse chomwe mitima yanu ikafune (zokoma ndi zabwino); ndipo, mukapeza mmenemo chilichonse chomwe mukachilakelake.”

    [32] “(“Limeneli ndi) phwando lochokera kwa (Mbuye) Wokhululuka kwambiri, Wachisoni chosatha.”

    [33] “Kodi ndani yemwe ali ndi zonena zabwino kuposa yemwe akuitanira kwa Allah (ndi kumumvera), ndikuchita, (pamodzi ndi zimenezo), zabwino uku akunena: “Ine ndi mmodzi mwa ogonjera (malamulo a Allah).”

    [34] “Ndipo chabwino sichingafanane ndi choipa. Chotsa (choipa) ndi chomwe chili chabwino; mapeto ake akhala kuti yemwe padali chidani pakati pako ndi pakati pake (akhala) ngati mthandizi wodalirika

    [35] “Ndipo palibe angapatsidwe zimenezi (zochotsa choipa pochita chabwino) kupatula amene apirira. Ndiponso sangapatsidwe zimenezi kupatula mwini gawo la ubwino waukulu

    [36] “Ndipo ngati satana atakusokoneza kuti akuchotse ku zomwe walamulidwa, pempha chitetezo kwa Allah. Ndithu Iye Ngwakumva zonse, Ngodziwa zonse; (adzakuteteza kwa iye)

    [37] “Ndipo zina mwa zisonyezo Zake, ndi usiku, usana, dzuwa ndi mwezi. Musalambire dzuwa ngakhale mwezi, koma lambirani Allah, Amene adazilenga ngati inu mukumpembedza mwachoonadi

    [38] “Koma ngati adzikweza (opembedza mafano ndi kusiya kutsatira lamulo lako, usade nkhawa). Ndipo, amene ali kwa Mbuye wako; (angelo), akulemekeza Iye usiku ndi usana, ndipo iwo satopa (ndi kutamanda Allah)

    [39] “Ndipo zina mwa zisonyezo Zake (zoposa), ndithu iwe umaona nthaka ili youma; koma tikatsitsa madzi pa iyo imagwedezeka ndi kufufuma; ndithu Amene waiukitsa nthaka itauma, Ngoukitsa akufa. Iye Ngwamphamvu zoposa pa chilichonse

    [40] “Ndithu amene akupotoza choonadi mzisonyezo Zathu sangabisike kwa Ife. (Ndipo tidzawalipira zimene akuyenerana nazo). Kodi wabwino ndi uti, yemwe adzaponyedwa ku Moto, kapena yemwe adzadza pa tsiku la chiweruziro uku ali wokhazikika mtima? Chitani zimene mukufuna; ndithu Iye Ngopenya chilichonse chimene mukuchita. (Aliyense adzamulipira pa zochita zake)

    [41] “Ndithu amene atsutsa Qur’an yolemekezeka ikawadzera (popanda kulingalira, kwa iwo kudzakhala chilango chosasimbika). Ndipo ndithu limeneli ndi buku lopambana (chilichonse cholipinga)

    [42] “Silifikidwa ndi chonama patsogolo pake ngakhale pambuyo pake. Ndi lovumbulutsidwa kuchokera kwa Wanzeru zakuya, Woyamikidwa kwambiri (mzochita Zake)

    [43] “Palibe chimene chinenedwa kwa iwe (Mtumiki {s.a.w) kuchokera kwa adani ako) koma chomwe chidanenedwa kwa aneneri akale (kuchokera kwa adani awo). Ndipo Mbuye wako ndi Mwini chikhululuko chambiri (kwa amene walapa kwa Iye), ndiponso Mwini chilango chowawa (kwa yemwe wapitiriza kunyozera)

    [44] “Ndipo tikadaichita Qur’an iyi kukhala mchiyankhulo chachilendo osati Chiarabu, akadanena: “Nchifukwa ninji ma Ayah ake sadafotokozedwe bwino; buku la chilankhulo chachilendo olalikidwa nkukhala mwarabu?” Nena (iwe Mtumiki): “Limeneli ndi chiongoko ndi chochiritsa kwa okhulupirira. Koma kwa amene salikhulupirira, (zili ngati kuti) mmakutu mwawo muli ugonthi (chifukwa cholinyoza) umene ukuwachititsa khungu (chifukwa choti saona chilichonse mmenemo chowapindulira), iwo (okanirawo ali ngati) akuitanidwa (ndi woitana) kuchokera pamtunda wapatali (kuti amkhulupirire).”

    [45] “Ndipo ndithu tidampatsa Mûsa buku ((la Tarat)) ndipo (anthu ake) adatsutsana za ilo. Kukadapanda kutsogola liwu lochokera kwa Mbuye wako (loti adzachedwetsa chilango kwa okutsutsa) kukadaweruzidwa pakati pawo (powaononga). Ndithu iwo ali m’chikaiko choikaikira iyo (Qur’an)

    [46] “Amene achite chabwino, akudzichitira yekha; ndipo amene akuipitsa (m’zochita zake), machimo ake ali pa iye yekha. Mbuye wako sali wopondereza akapolo (Ake polanga wina ndi tchimo la wina)

    [47] “۞ Kudziwa kwa tsiku la Qiyâma kukubwezedwa kwa Iye (Allah;) zipatso sizituluka m’mikoko yake ndipo mkazi satenga pakati ndi kubereka popanda Allah kudziwa. (Koma amadziwa zonsezo bwinobwino). Ndipo (kumbukira) tsiku limene Allah adzawaitane (ndi kuwafunsa kuti): “Ali kuti aphatikizi Anga aja (amene mudali kuwapembedza kusiya Ine)?” Adzanena (modandaula): “Tikukudziwitsani, (E Inu Allah)! Palibe aliyense mwa ife angaikire umboni (kuti Inu muli ndi mnzanu).”

    [48] “Ndipo zomwe adali kuzipembedza kale zidzawasowa. Ndipo adzatsimikiza kuti alibe pothawira

    [49] “Munthu satopa kupempha zabwino (za m’dziko lapansi kwa Mbuye wake). Koma choipa chikamkhudza iye amakhala wotaya mtima kwambiri

    [50] “Ndipo ndithu tikamulawitsa chisomo chochokera kwa Ife atapeza mavuto kwambiri amene adamkhudza, ndithu amanena, (monyada): “Izi nzangazanga. (Ndazipeza chifukwa cha khama langa ndi nzeru zanga). Ndipo za tsiku lachimaliziro sindikhulupirira kuti lilipo. Ndipo ngati nditabwezedwa kwa Mbuye wanga, ndiye kuti ine ndidzakhala nazo zabwino kwa Iye.” Choncho tidzawauza omwe adakanira zimene adachita, ndipo tidzawalawitsa chilango chokhwima (chosanjikana china pamwamba pa chinzake)

    [51] “Ndipo munthu tikam’dalitsa (ndi chisomo Chathu), amanyoza ndi kudziika kutali (ndi chipembedzo Chathu). Koma vuto likam’khudza umuona uyo akuchulukitsa maduwa (mapemphero)

    [52] “Nena (kwa iwo, iwe Mtumiki): “Tandiuzani ngati (Qur’aniyi) ilidi yochokera kwa Allah, kenako inu nkuikanira; (nanga zingakhale bwanji?) Kodi ndiyani wosokera kwambiri kuposa uyo amene ali mu mtsutso wakutali (ndi choona)?”

    [53] “Posachedwa tiwaonetsa (awa okanira), zisonyezo Zathu (zosonyeza kuona kwa Qur’an ndi iwe) kumbali zonse, ndi mwa iwo eni kufikira zionekere kwa iwo kuti chimene wadza nachochi nchoona. Kodi Mbuye wako siwokwanira kuti Iye akuona chilichonse

    [54] “Chenjerani! Ndithu awa ali m’chikaiko za kukumana ndi Mbuye wawo. Ndithu Iye (Mbuye wawo) wachizungulira chinthu chilichonse mkudziwa Kwake

    Kufunsirana

    Surah 42

    [1] “Hâ-Mîm

    [2] “‘Aîn-Sîn-Qâf

    [3] “Chomwecho akukuvumbulutsira iwe ndi atumiki amene adadza kale, Allah Ngopambana Wanzeru zakuya

    [4] “Zonse za kumwamba ndi pansi ndi za Iye Yekha. Ndipo Iye ndi Wotukuka, Wamkulu

    [5] “(Chifukwa chakukula Kwake ndi ulemelero Wake) mitambo ikuyandikira kuphwasuka pamwamba pa iyo. Ndipo angelo akulemekeza ndi kutamanda Mbuye wawo, ndi kuwapemphera chikhululuko amene ali pa dziko lapansi. Dziwani kuti ndithu Allah Yekha ndiye Wokhululuka kwabasi, Wachisoni chosatha

    [6] “Ndipo awo amene adzipangira athandizi (a mafano) kusiya Allah, Allah ndi Wolondera (zochita) zawo; ndipo iwe si muyang’anili wawo (wosunga zochita zawo)

    [7] “Chomwechonso (monga chilili chivumbulutso chapoyerachi) takuvumbulutsira Qur’an m’Chiarabu (popanda chikaiko) kuti uchenjeze (eni) manthu wa mizinda (Makka) ndi amene ali m’mbali mwake, ndikutinso uchenjeze (anthu) za tsiku la msonkhano, lopanda chikaiko. (Pa tsikulo anthu adzagawikana mmagulu awiri): gulu lina ku Jannah, ndipo gulu lina ku Moto

    [8] “Ndipo akadafuna Allah akadawachita iwo kukhala mpingo umodzi; koma amamulowetsa ku chifundo Chake amene wamfuna ndipo odzichitira okha chinyengo (pokana Allah) alibe mtetezi kapena mthandizi

    [9] “Kapena adzichitira athandizi ena kusiya Iye (Allah)? Pomwe Allah Yekha ndiye Mthandizi woona ndipo Iye amaukitsa akufa. Ndipo Iye ndi Wokhoza pa chilichonse

    [10] “Ndipo chilichonse chimene mwasiyana mmenemo (mchipembedzo: za kukhulupirira ndi kusakhulupirira) chiweruzo chake nkwa Allah; (bwererani ku Buku la Allah ndi Hadith za mtumiki Wake). Ndipo Ameneyo ndi Allah, Mbuye wanga; kwa Iye Yekha ndatsamira, ndipo kwa Iye Yekha (ndiko) ndikutembenukira

    [11] “(Iye ndi) Mlengi wa kumwamba ndi pansi. Adakupangirani akazi kuchokera mwa inu nomwe, ndipo nazo ziweto mitundu iwiri, (zazimuna ndi zazikazi. Choncho) akukuchulukitsani mmenemo (mchikonzero Chake chanzeru) palibe chilichonse chofanana ndi Iye. Iye ndi Wakumva zonse ndiponso Woona zonse

    [12] “Makiyi a kumwamba ndi pansi ndi Ake. Amamchulukitsira rizq amene wamfuna ndipo amamchepetsera amene wamfuna. Ndithu Iye Ngodziwa chilichonse (pochiika pamalo oyenera)

    [13] “Wakhazikitsa kwa inu chipembedzo chonga chomwe adam’langiza Nuh. Ndipo chimene takuvumbulutsira iwe ndi chimenenso tidavumbulutsira Ibrahim, Mûsa, ndi Isa (Yesu) kuti: Mulimbike chipembedzo (potsatira malamulo) ndikuti musalekane pa chipembedzo. Koma ndizovuta kwa opembedza mafano (kuvomera) zimene ukuwaitanira. Allah amadzisankhira amene wam’funa ndipo amamuongolera amene akutembenukira kwa Iye

    [14] “Ndipo sadagawikane (pa chipembedzo otsatira a aneneri oyamba) kufikira pamene kudawadzera kudziwa kwa choonadi, chifukwa chachidani ndi dumbo pakati pawo. Kukadapanda liwu lochokera kwa Mbuye wako pachiyambi (lowachedwetsera chilango) mpaka nthawi yoikidwa kukadaweruzidwa pakati pawo koma ndithu amene adalandira buku pambuyo pawo (makolo awo, ndipo ndikukumana ndi nthawi yako,) ali mchikaiko cholikaikira (buku lawo)

    [15] “(Chifukwa cha umodzi wa zipembedzo ndikuti pasakhale kugawikana pa chipembedzo) choncho aitanire (ku chipembedzo chimodzi); ndipo lungama (poitanapo) monga momwe walamulidwira. Ndipo usatsatire zofuna zawo. Ndipo nena: “Ndakhulupirira mmabuku onse omwe adawavumbulutsa Allah; ndipo ndalamulidwa kuchita chilungamo pakati panu. Allah ndiye Mbuye wathu ndiponso Mbuye wanu; ife tili ndi ntchito zathu (zomwe tidzalipidwa nazo); inunso muli ndi ntchito zanu (zomwe mudzalipidwa nazo). Palibe kukangana pakati pa ife ndi inu (chifukwa chakuonekera poyera choona). Allah adzatisonkhanitsa (kuti atiweruze); kwa Iye yekha ndiko kobwerera

    [16] “Ndipo amene akutsutsana ndi Allah pambuyo povomerezedwa (ndi anthu ambiri), mtsutso wawo ndiwachabe kwa Mbuye wawo; mkwiyo waukulu (wa Allah) uli pa iwo. Ndipo iwo adzakhala ndi chilango chokhwima

    [17] “Allah ndi Amene wavumbulutsa buku (la Qur’an ndi mabuku ena) moona ndi mwachilungamo. Nanga nchiyani chikudziwitse kuti mwina Qiyâma ili pafupi

    [18] “Akuifulumizitsa amene sakuikhulupirira; koma amene akhulupirira ali oopa za iyo, ndipo akudziwa kuti imeneyo ndiyoonadi, (za kupezeka kwake palibe chikaiko). Dziwani kuti ndithu amene akutsutsana za nthawi (ya Qiyâma) ali mkusokera konka nako kutali

    [19] “Allah Ngoleza kwa akapolo (Ake). Amapereka rizq kwa amene wamfuna. Ndipo Iye ndi Wamphamvu zoposa, Wopambana

    [20] “Amene akufuna (pantchito yake) zokolola za tsiku lachimaliziro, timuonjezera zokolola zakezo; ndipo amene akufuna pa ntchito yake yabwino zokolola za chisangalalo cha m’dziko lapansi timpatsa chimene chidagawidwa kwa iye, ndipo iye sadzakhala ndi gawo (la zabwino) pa tsiku lachimaliziro

    [21] “Kodi iwo alinayo milungu imene idawakhazikitsira m’zipembedzo zimene Allah sadaziloleze? Ndipo pakadapanda kutsogola (lonjezo lochedwetsa) liwu la chiweruziro (mpaka pa tsiku la Qiyâma); pakadaweruzidwa pakati pawo (okanira ndi okhulupirira pompano pa dziko lapansi). Ndipo ndithu opondereza chawo nchilango chowawa

    [22] “Udzawaona (tsiku la Qiyâma) amene adadzichitira okha zoipa (popembedza mafano) akuopa chifukwa cha (zoipa) zomwe adachita, ndipo (chilangocho) chidzawapezabe. Koma amene adakhulupirira ndi kuchita zabwino (udzawaona akusangalala) m’Madimba abwino a ku Minda ya mtendere. Iwo akapeza chilichonse chimene akafune kwa Mbuye wawo. Umenewo ndiwo ulemelero wawukulu

    [23] “Umenewu ndi (ulemelero) umene Allah akuwasangalatsira akapolo Ake nkhani yabwino; amene akhulupirira ndi kuchita zabwino. Nena (iwe Mtumiki {s.a.w} kwa iwo): “Sindikupemphani malipiro (kapena chuma) pofikitsa uthenga (kwa inu), koma kuti musunge chikondi pachibale chimene chili pakati pathu. (Musandizunze kufikira ndifikitse kwa inu uthenga wa Mbuye wanga.)” Amene achita chabwino timuonjezera pachabwinocho ndithu Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngolandira kuthokoza

    [24] “Kapena akunena kuti: “Wampekera Allah bodza?”Allah akadafuna akadadinda mu mtima mwako (kuti usathe kunena chilichonse; koma kuti chilichonse chimene ukunena chikuchokera kwa Iye). Ndipo Allah amachotsa chabodza (shirik), ndi kuchilimbikitsa choona (Chisilamu), ndi mau Ake (amene adawavumbulutsa kwa Mneneri Wake). Ndithu Iye Ngodziwa (zobisika) za mmitima

    [25] “Ndipo Iye (Yekha) ndi amene amalandira kulapa (kuchokera) kwa akapolo Ake. Ndipo amakhululuka machimo (awo); komanso akudziwa zimene mukuchita

    [26] “Ndipo Iye (Allah) akuwayankha amene akhulupirira ndi kuchita zabwino; ndi kuwaonjezera ubwino Wake. Ndipo okana, chilango chaukali chili pa iwo

    [27] “Allah akadachulukitsa rizq (chuma) kwa akapolo Ake onse (monga anthuwo akufunira), akadapyola malire poononga pa dziko; koma (Allah) akutsitsa (chumacho) mwamuyeso monga momwe Iye afunira. Ndithu Iye pa za akapolo Ake Ngodziwa, Ngopenya

    [28] “Ndipo Iye yekha ndi amene akutsitsa mvula (pambuyo poti anthu)atataya mtima (pa zamvulayo); ndipo amafalitsa madalitso Ake ndipo ndi Mthandizi Wotamandidwa

    [29] “Ndipo zina mwa zisonyezo zake ndi kulenga kwa thambo ndi nthaka, ndi zamoyo zimene wazifalitsa mmenemo (zooneka ndi zosaoneka). Ndipo Iye ndi Wamphamvu zowasonkhanitsira (anthu kuchokera ku imfa) akadzafuna

    [30] “Ndipo mavuto amtundu uliwonse amene akukupezani nchifukwa cha (zochita zoipa) zimene achita manja anu, koma (Allah) akukhululuka zambiri

    [31] “Ndipo simungathe kum’lepheretsa (Allah kukutsitsirani mavuto) padziko lapansi (ngati mutachimwa); ndipo inu mulibenso mthandizi kapena mpulumutsi kupatula Allah

    [32] “Ndipo zina mwa zisonyezo Zake ndi zombo zoyenda panyanja zonga mapiri ataliatali (koma osabira)

    [33] “Atafuna akhoza kuiyimitsa mphepo choncho nkungokhala duu, (osayenda) pamwamba pake (panyanja). Ndithu mzimenezi muli zisonyezo kwa aliyense wopirira ndi wothokoza

    [34] “Kapena akhoza kuziononga (potumiza mphepo yamkuntho) chifukwa cha machimo amene adawachita. Koma amakhululuka zambiri

    [35] “Ndipo adzadziwa (tsiku la Qiyâma) amene akutsutsana ndi zisonyezo Zathu kuti alibe pothawira (kuchilango cha Allah)

    [36] “Ndipo chilichonse chimene mwapatsidwa, nzosangalatsa za moyo wa pa dziko. Koma zimene zili kwa Allah ndi zabwino ndiponso zamuyaya za amene akhulupirira ndi kutsamira kwa Mbuye wawo

    [37] “Ndipo amene akupewa machimo akuluakulu omwe Allah waletsa ndi machimo onse oipitsitsa; ndipo iwo akakwiya (chifukwa choputidwa) iwo amakhululuka

    [38] “Ndipo amene adayankha kuitana kwa Mbuye wawo ndi kusunga mapemphero (popemphera mnthawi yake mkapempheredwe koyenera); ndipo zinthu zawo zonse zimakhala zokambirana pakati pawo; ndipo mzimene tawapatsa amapereka (pa njira ya Allah)

    [39] “Ndi amene amati akachitiridwa mtopola amadzipulumutsa

    [40] “Malipiro a choipa ndi choipa chonga icho; (wochita choipa alipidwe choipa chonga chimene wachita). Koma amene wakhululukira wochita choipa (pomwe akhoza kubwezera), ndi kuyanjana naye (mdani wakeyo), malipiro ake ali kwa Allah; ndithu Allah sakonda ochitira anzawo mtopola

    [41] “Koma amene abwezera pambuyo pakuchitiridwa mtopola, kwa iwo palibe njira yowadzudzulira

    [42] “Ndithu njira yodzudzulidwira ili kwa amene akupondereza anthu ndi kuchita mtopola pa dziko popanda chifukwa choyenera. Iwowo ndi amene adzalandira chilango chowawa

    [43] “Ndipo amene akupirira ndi kukhululuka, (Allah adzamlipira mphoto yaikulu); ndithu kupirirako ndi chimodzi mwa zinthu zazikulu (chofunika kudzilimbikitsa nacho Msilamu pa chikhalidwe chake)

    [44] “Ndipo amene Allah wamsiya kuti asokere, alibe mthandizi (wina) kupatula Iye (Allah). ndipo udzawaona osalungama pamene adzachiona (masomphenya) chilango, adzanena (modandaula): “Kodi pali njira yobwerera (padziko lapansi kuti tikachite zabwino tidzalowe ku Jannah)?”

    [45] “Udzawaona (osalungama) akusonyezedwa ku Moto ali okhumata chifukwa chakunyozeka uku akuyang’ana (Moto) mkayang’anidwe kobisa (kotsinzina). Ndipo amene adakhulupirira adzanena pa tsiku la Qiyâma: “Ndithu otaika ndi amene adadzitaya okha pamodzi ndi maanja awo.” Dziwani kuti osalungama adzakhala mchilango chamuyaya

    [46] “Ndipo sadzakhala ndi athangati owapulumutsa (kuchilango cha Moto) kupatula Allah. Ndipo amene Allah wamusiya kuti asokere (chifukwa cha zochita zake zoipa) sangapeze njira (yopezera kulungama)

    [47] “Muyankheni Mbuye wanu lisadadze tsiku losapeweka lochokera kwa Allah; tsiku limenelo simudzapeza pothawira, ndipo simudzakhala ndi njira (yokanira zimene mudzachitidwa)

    [48] “Ngati anyalanyaza (Allah awalanga) sitidakutume kwa iwo kukhala muyang’aniri. Udindo wako ndikufalitsa uthenga. Ndipo ndithu tikamulawitsa munthu mtendere wochokera kwa Ife, akuunyadira (modzikweza), koma choipa chikawapeza kupyolera mzoipa zimene manja awo adatsogoza, pompo munthuyo sathokoza (Allah)

    [49] “Ufumu wakumwamba ndi pa dziko lapansi ngwa Allah; amalenga zimene wafuna; amene wam’funa amampatsa ana achikazi (okhaokha) ndiponso amene wamfuna amampatsa ana achimuna (okhaokha)

    [50] “Kapena kuphatikiza (ana) achimuna ndi achikazi, ndipo amene wam’funa amamchita kukhala chumba. Ndithu Iye Ngodziwa, Wokhoza (chilichonse)

    [51] “Nkosayenera kwa munthu kuti Allah alankhule naye koma kupyolera mkumzindikiritsa, kapena kuchokera kuseri kwa chotsekereza, kapena pomtuma mtumiki (Jiburil) kuti amvumbulutsire zimene Iye akufuna mwa chilolezo Chake. Ndithu Iye Ngwapamwamba, Ngwanzeru zakuya

    [52] “Momwemonso takuvumbulutsira chivumbulutso (Chathu) mwa lamulo Lathu. Siudali kudziwa kuti buku ndi chiyani, chikhulupiliro ndi chiyani; koma bukuli (Qur’an) talichita kukhala kuunika; ndi kuunikaku tikumuongola amene tam’funa mwa akapolo Athu. Ndithu iwe ukuongolera kunjira yoongoka

    [53] “Njira ya Allah Amene zonse za kumwamba ndi za mdziko lapansi ndi Zake. Dziwani kuti zinthu zonse zimabwerera kwa Allah

    Zokongoletsa Zagolide

    Surah 43

    [1] “. Hâ-Mîm

    [2] “Ndikulumbilira buku lofotokoza momveka

    [3] “Ndithu Ife talichita bukuli (Qur’an) kukhala chowerengedwa m’Chiarabu kuti muzindikire

    [4] “Ndipo ndithu bukuli (Qur’an) lili m’manthu wa mabuku onse (Lawhi Mahfudh) limene lili kwa Ife; (ndipo ndi buku) lotukuka, la mawu anzeru

    [5] “Kodi tisiye kukukumbutsani chifukwa chakuti ndinu anthu opyola malire (pochita zoipa)

    [6] “Ndipo tidatumiza aneneri ambiri kwa anthu akale

    [7] “Ndipo palibe mneneri aliyense amene amawadzera koma amam’chitira chipongwe

    [8] “Choncho tidawaononga amene adali amphamvu kuposa iwo (Aquraish) ndipo ladutsa fanizo la (zilango zomwe zidawapeza) anthu akale

    [9] “Ndipo ukawafunsa: “Ndani adalenga thambo ndi nthaka?” Ndithu ayankha kuti: “Adazilenga (Allah) Mwini Mphamvu, Wodziwa.”

    [10] “Amene wakupangirani nthaka kukhala choyala ndipo adakupangirani njira mmenemo kuti muongoke (ndikukafika kumene mukufuna)

    [11] “Ndiponso amene watsitsa madzi kuchokera kumwamba mwamuyeso; chifukwa cha madziwo tidaukitsa mudzi wakufa. Momwemonso inu mudzatulutsidwa (mmanda)

    [12] “Ndiponso amene walenga zinthu zonse ziwiriziwiri (chachimuna ndi chachikazi). Ndipo adakupangirani zombo ndi ziweto zimene mukukwera

    [13] “Kuti mukhazikike mwaubwino pamisana paizo, kenako mukumbukire mtendere wa Mbuye wanu mukakhazikika pamenepo, ndipo munene: “Walemekezeka Amene watifewetsera ichi; ndipo sitikadatha kuchifewetsa ndi kuchigwiritsa ntchito.”

    [14] ““Ndipo ndithu ife kwa Mbuye wathu ndiko kobwerera.”

    [15] “Ndipo amuikira gawo mwa akapolo Ake. (Kuti ndi ana a Allah.) Ndithu munthu, ngwamsulizo woonekera poyera

    [16] “Kodi wadzichitira ana achikazi mzimene wazilenga ndipo wakusankhirani inu ana achimuna

    [17] “Koma akauzidwa (kuti wabereka mwana wamkazi) mmodzi wa iwo chomwe amamfanizira (Allah) Wachifundo chambiri, nkhope yake imakhala yakuda ndi kudandaula kwambiri

    [18] “Ha! Kodi amene waleredwa monga chokongoletsa, potsutsana iye sangathe kunena momveka? (Ameneyo ndiye mwampatsa Allah; omwe ndi ana aakazi)

    [19] “Ndipo angelo omwe ndi akapolo a (Allah) Wachifundo chambiri akuwatcha akazi. Kodi adaona kalengedwe kawo? Umboni wawo ulembedwa ndipo adzafunsidwa (pazimenezo)

    [20] “Ndipo (otsutsa) akunena: “Akadafuna (Allah) Wachifundo chambiri (kuti tisamapembedze mafano awa), sitikadawapembedza!” Iwo alibe kudziwa pa zimenezi (zomwe akunenazi). Koma akungonena mawu opeka

    [21] “Kapena tidawapatsa buku lina tisadapereke ili, kotero kuti iwo agwiritsitsa limenelo (ndi kugwirizana nazo zili mmenemo)

    [22] “Koma akunena: “Ndithu ife tidawapeza makolo athu pa chipembedzo chimenechi, ndipo ife tikutsatira mapazi awo.”

    [23] “Ndipo momwemo, sitidatumize mchenjezi patsogolo ku mudzi uliwonse koma olemera ammenemo adanena: “Ndithu tidawapeza makolo athu pa chipembedzochi (akuchita mmene tikuchitiramu), ndipo ife titsatira mmapazi awo.”

    [24] “Adanena (mneneri wawo): “Ngakhale ndakubweretserani chipembedzo chabwino kuposa chomwe mudawapeza nacho makolo anu (mupitirizabe kutsatira chipembedzo cha makolo anucho)?” Adanena: “Ife tikuzikana zimene mwatumidwa nazozi.”

    [25] “Choncho tidawalanga iwo. Taona m’mene adalili mapeto a otsutsa aja

    [26] “Ndipo (kumbuka) pamene Ibrahim adauza bambo wake ndi anthu ake (kuti): “Ndithu ine ndadzipatula ku zimene mukuzipembedzazi.”

    [27] ““Kupatula Amene adandilenga; ndithu Iye andiongola.”

    [28] “Ndipo adalichita liwu ili kukhala losatha ku mtundu wake, kuti abwelere (ku malankhulidwe amenewa)

    [29] “Koma ndidawasangalatsa awa (Aquraish) pamodzi ndi makolo awo kufikira choonadi chawadzera ndi Mtumiki wolongosola (za choonadichi)

    [30] “Ndipo pamene choonadi (Qur’an) chidawadzera, adanena: “Awa ndi matsenga; ndithu ife tikuwakana.”

    [31] “Ndipo adatinso: “Nchifukwa ninji Qur’an iyi siidavumbulutsidwe pa munthu wamkulu mmidzi iwiriyi (Makka ndi Twaif).”

    [32] “(Choncho Allah akunena): “Kodi iwo ndi amene akugawa mtendere wa Mbuye wako (kumpatsa amene wamfuna ndi kummana amene sakumfuna? Chikhalirecho) Ife ndi Amene timagawa pakati pawo zofunika pa moyo wawo mu moyo wadziko lapansi; ndipo tawatukula ena mwa iwo pa ulemelero pamwamba pa ena, choncho ena mwa iwo akuwachita anzawo kukhala antchito awo koma mtendere wa Mbuye wako ndi wabwino kuposa zimene akusonkhanitsa.”

    [33] “Ndipo pakadapanda kuopera kuti anthu adzakhala gulu limodzi (lokanira Allah), ndithu tikadazichita nyumba za amene akumkana (Allah) Wachifundo chambiri kukhala ndi madenga a Siliva, ndi makwelero amene amakwelera (kukhalanso a Siliva)

    [34] “Ndipo nyumba zawo kukhala ndi zitseko ndi makama (mabedi) omwe amayadzamira (zonsezo kukhala za Siliva)

    [35] “Ndiponso ndi zokongoletsa za golide. Koma zonsezo sikanthu ayi, ndi chisangalalo chabe cha dziko lapansi (chosakhalira kutha); ndipo tsiku lachimaliziro lomwe lili kwa Mbuye wako ndi la oopa Allah (potsatira malamulo Ake ndi kusiya zoletsedwa)

    [36] “Ndipo amene akunyozera kukumbukira (Allah) Wachifundo chambiri, timpatsa satana, kuti iye akhale bwenzi lake (lotsagana nalo)

    [37] “Ndipo iwo amawatsekereza ku njira zabwino ndi kumaganiza kuti iwo ngoongoka

    [38] “Kufikira pamene adzatidzera (tsiku la Qiyâma, uku akulowetsedwa ku Moto). Adzati (kumuuza satana): “Kalanga ine! Pakati pa ine ndi iwe pakadakhala ntunda wa pakati pa kuvuma ndi kuzambwe (kutalikirana kwathu).” Ha! Taonani kuipa kwa bwenzi

    [39] “(Allah adzawauza kuti): “Ndipo lero sikukuthandizani kukhala limodzi kwanu m’chilango pakuti mudadzichitira nokha zoipa.”

    [40] “Kodi ungathe kuwamveretsa agonthi, kapena ungathe kuwaongola akhungu ndi amene ali mkusokera koonekera

    [41] “Ngati titakuchotsa (padziko usadaone chilango chawo, usakhale ndi chikaiko), ndithu Ife tiwalanga iwo

    [42] “Kapena tikusonyeza zimene tidawalonjeza (uona ndi maso ako usadafe). Ndithu Ife tili ndi mphamvu pa iwo

    [43] “Choncho, gwiritsa zimene zavumbulutsidwa kwa iwe, ndithu iwe uli pa njira yolunjika

    [44] “Ndithu iyi (Qur’an) ndi ulemelero wako ndi anthu ako; ndipo posachedwa mufunsidwa (za ulemelero umenewu)

    [45] “Ndipo afunse atumiki Athu amene tidawatumiza iwe usadadze: “Kodi tidapanga milungu ina kuti ipembedzedwe, osati (Allah) Wachifundo chambiri?”

    [46] “Ndithu tidamtumiza Mûsa pamodzi ndi zozizwitsa Zathu kwa Farawo ndi nduna zake; ndipo adati: “Ndithu ine ndine Mtumiki wa Mbuye wa zolengedwa.”

    [47] “Koma pamene adawadzera ndi zisonyezo zathu, basi iwo adali kuziseka

    [48] “Ndipo chisonyezo chilichonse chomwe tidawasonyeza chidali chachikulu kuposa chinzake (komabe sadakhulupirire). Ndipo tidawalanga ndi chilango kuti abwelere (kwa Ife)

    [49] “Ndipo adati (kwa Mûsa): “E iwe wamatsenga! Tipemphere kwa Mbuye wako pa chomwe adakulonjeza; ndithu ife tiongoka, (tikhulupirira).”

    [50] “Choncho, pamene tidawachotsera chilangocho, basi iwo adayamba kuswa pangano

    [51] “Ndipo Farawo adaitana anthu ake, adati: “E inu anthu anga! Kodi ulamuliro wa mu Iguputo siwanga pamodzi ndi mitsinje iyi imene ikuyenda pansi panga (pa nyumba zanga?) Kodi simukuona?”

    [52] ““Kodi kapena ine sindine woposa uyu (Mûsa) wonyozeka, ndipo sangathe kuyankhula momveka?”

    [53] ““Nanga bwanji sadavekedwe zibangiri zagolide kapena angelo kudza pamodzi ndi iye uku akumtsatira?”

    [54] “Adawapeputsa anthu ake. Ndipo adamvera; iwo adali anthu otuluka mchilamulo (cha Allah)

    [55] “Pamene adatikwiitsa, tidawalanga ndipo tidawamiza onse mmadzi

    [56] “Tidawachita (Farawo ndi anthu ake) kukhala chitsanzo cha okanira a pambuyo pawo ndikukhala mbiri kwa anthu amene akudza

    [57] “Ndipo pamene lidaperekedwa fanizo la mwana wa Mariya, pamenepo anthu anu adali kufuula (monyoza)

    [58] “Ndipo adati: “Kodi milungu yathu ndi yabwino, kapena iye?” Sadamfanizire kwa iwe koma kufuna kutsutsana basi (kopanda kufuna choona). Koma iwo ndi anthu amtsutso

    [59] “Iye sadali kanthu koma ndi kapolo amene tidampatsa mtendere; ndipo tidamchita kukhala chitsanzo (chodabwitsa) cha ana a Israyeli

    [60] “Ndipo tikadafuna tikadawachita angelo kukhala pa dziko mmalo mwa inu ndi kumasiirana iwo kwa iwo (kuti mudziwe kuti angelo akugonjera malamulo a Allah. Iwo siAllah)

    [61] “Ndipo iye (Isa (Yesu) adzakhala chizindikiro cha Qiyâma (kuti yayandikira). Choncho musaikaikire, koma nditsatireni. Imeneyi ndi njira yolunjika

    [62] “Asakutsekerezeni satana; iye kwa inu ndi mdani woonekera

    [63] “Ndipo pamene Isa (Yesu) adadza ndi zisonyezo zoonekera poyera, adati: “Ndakudzerani ndi nzeru (yopindulitsa), ndikuti ndikulongosolereni zina zimene mudali kusiyana mu izo; choncho, muopeni Allah ndiponso ndimvereni.”

    [64] ““Ndithu Allah ndiye Mbuye wanga ndi Mbuye wanunso; choncho mupembedzeni; imeneyi ndiyo njira yolunjika.”

    [65] “Koma magulu adasemphana pakati pawo. Ndipo kuonongeka kuchokera mu chilango cha tsiku lowawa kudzakhala pa amene adzichitira okha zoipa

    [66] “Palibe chimene akuyembekeza, koma Qiyâma basi yomwe iwadzera mwadzidzidzi pomwe iwo sakuzindikira (ali otanganidwa ndi za m’dziko)

    [67] “Abwenzi tsiku limenelo adzakhala odana, wina ndi mnzake, (chifukwa chakuti adali kuthandizana pa zinthu zosalungama ndi zamachimo) kupatula oopa Allah (amene adachita chibwenzi mwa Allah, pothandizana kukwaniritsa malamulo a Allah ndi kusiya zimene Allah waletsa)

    [68] “(Allah adzati): E inu akapolo Anga (abwino)! Palibe kuopa kwa inu lerolino ndiponso simudandaula

    [69] “Amene adakhulupirira zisonyezo Zathu ndipo adali Asilamu (ogonjera Allah)

    [70] “Lowani ku Munda wamtendere, inu ndi akazi anu musangalatsidwa

    [71] “Adzakhala akupititsidwa mbale zagolide ndi matambula (agolide); zonse zokomera moyo zidzakhala mmenemo ndi zokomera maso, ndipo inu mudzakhala mmenemo nthawi yaitali

    [72] “Ndipo umeneo ndi munda umene mwapatsidwa chifukwa cha (zabwino) zimene munkachita

    [73] “Inu mupeza mmenemo zipatso zambiri zomwe muzidya

    [74] “Ndithu ochimwa (okanira) adzakhala m’chilango cha Jahannam nthawi yaitali

    [75] “Sadzapatsidwa nthawi yopumula, ndipo mmenemo iwo akataya mtima (zakupeza moyo wabwino)

    [76] “Ndipo sitidawapondereze koma adali kudzipondereza okha

    [77] “Ndipo (okanira) adzaitana E iwe Malik! (yemwe ndi mngelo woyang’anira moto): ‘‘Mbuye wako atipatse imfa (kuti tipumule kuchilangochi!)” Adzanena (Malik): “Ndithu inu mukhala momwemo!”

    [78] “Ndithu tidakubweretserani choona; koma ambiri a inu mudali kuchida choona

    [79] “Kodi akonza bwino chikonzero (chawocho chomwe ndi chiwembu chofuna kumupha Mtumiki {s.a.w})? Ndithu nafenso ndife okonza chikonzero chabwino (cholepheretsa chiwembu chawocho)

    [80] “Kodi akuganiza kuti sitikumva zobisa zawo ndi zonong’oneza zawo? Iyayi, (tikuzimva zonse), ndipo atumiki Athu (angelo) ali nawo pamodzi; akulemba

    [81] “Nena (kwa omphatikiza Allah ndi mafano): “Zikadakhala kuti (Allah) Wachifundo chambiri ali ndi mwana, ndiye kuti ine ndikadakhala woyamba kumpembedza (mwanayo).”

    [82] “Mbuye wa kumwamba ndi pansi, Mbuye wa Arsh (Mpando wachifumu), Wapatukana ndi mbiri zimene akum’nenerazo (zoti Allah ali ndi mwana)

    [83] “Asiye azingonena zachabezo ndi kusewera kufikira adzakumana ndi tsiku lawo limene akulonjezedwa

    [84] “Ndipo Iye ndiamene akupembedzedwa kumwamba, ndiponso ndi Iye Amene akupembedzedwa pansi. Iye ndi Wanzeru zakuya, Wodziwa kwambiri

    [85] “Ndipo watukuka kwambiri Yemwe ufumu wa kumwamba ndi pansi ndi pakati pa zimenezi ndi Wake. Ndiponso kwa Iye ndiko kuli kudziwa kudza kwa tsiku la Qiyâma; ndipo kwa Iye Yekha ndi kumene m’dzabwezedwa

    [86] “Ndipo omwe akuwapembedzawo kusiya Iye (Allah), sangathe kupulumutsa (aliyense) kupatula amene akuikira umboni choonachi, pomwe iwo akuchidziwa bwino

    [87] “Ndipo ngati utawafunsa: “Ndani adawalenga?” Anena motsimikiza kuti: “Ndi Allah.” Nanga akutembenuzidwa bwanji (kusiya choona)

    [88] “Ndipo zonena zake (Mneneri Muhammad{s.a.w} nthawi zonse): “E Mbuye Wanga! Ndithu awa ndi anthu osakhulupirira (nditani nao)?”

    [89] “Choncho, akhululukire, ndipo auze mawu a mtendere. Posachedwa adzadziwa

    Utsi

    Surah 44

    [1] “Hâ-Mîm

    [2] “Ndikulumbilira buku lofotokoza momveka

    [3] “Ndithu tidaivumbulutsa (Qur’an) mu usiku wodala. Ife ndithu Ndiachenjezi

    [4] “Mu (usiku) umenewu chinthu chilichonse chanzeru chimaweruzidwa ndi kulongosoledwa

    [5] “Mwa chilamulo chochokera kwa Ife. Ndithu Ife ndife otumiza atumiki (kuti achenjeze anthu)

    [6] “(Chifukwa cha) chifundo chochokera kwa Mbuye wako. Ndithu Iye Ngwakumva zonse, Wodziwa kwabasi

    [7] “Mbuye wa thambo ndi nthaka ndi zapakati pake, ngati muli otsimikiza

    [8] “Palibe wopembedzedwa moona koma Iye basi. Amapereka moyo ndikupereka imfa, Mbuye wanu ndi Mbuye wa makolo anu oyamba

    [9] “Koma iwo (okanira) ali mchikaiko akungosewera, (potsatira zilakolako zawo zoipa)

    [10] “Basi, yembekezera tsiku limene thambo lidzadze ndi utsi woonekera (konsekonse)

    [11] “Udzawaphimba anthu onse (ndipo adzakhala akunena:) “Ichi ndi chilango chowawa

    [12] “E Mbuye wathu! Tichotsereni chilangochi, ndithu ife tikhulupirira.”

    [13] “(Kodi lero) kukumbukira kuwapindulira chiyani iwo? Chikhalirecho mtumiki wolongosola chilichonse adawadzera

    [14] “Koma sadamlabadire uku akumnena kuti: “Waphunzitsidwa (ndi anthu), ndiponso wopenga.”

    [15] “Ndithu Ife tichotsa chilangocho pang’ono (koma) inu mubwerezanso (machimo anu)

    [16] “(Kumbuka, iwe Mtumiki), tsiku limene tidzawalanga chilango chachikulu; ndithu Ife ndife olanga

    [17] “Ndipo ndithu iwo asadadze, tidawayesa anthu a Farawo. Ndiponso adawadzera mtumiki wolemekezeka

    [18] “Kuti: “Ndipatseni akapolo a Allah. Ndithu ine kwa inu ndi Mtumiki wokhulupirika.”

    [19] ““Ndipo musadzikweze kwa Allah. Ndithu ine ndikubweretserani chisonyezo choonekera.”

    [20] ““Ndipo Ine ndadzitchinjiriza ndi Mbuye Wanga ndiponso Mbuye wanu (ku chiwembu chofuna kundipha) pondigenda (ndi miyala).”

    [21] ““Ndipo ngati simundikhulupirira, ndipatukeni (musandivutitse).”

    [22] ““(Koma adamchitira mtopola). Ndipo iye adaitana Mbuye wake kuti: “Awa ndithu ndi anthu oipa.”

    [23] “(Allah adamuuza kuti): “Pita ndi akapolo Anga usiku; ndithu inu mulondoledwa.”

    [24] ““Ndipo isiye nyanja ili momwemo, zii. ndithu iwo ndikhamu (lankhondo) limene limizidwa.”

    [25] “Kodi ndi minda ingati ndi akasupe zomwe adazisiya atamizidwa

    [26] “Ndiponso mmera ndi malo abwino

    [27] “Ndi mtendere (waukulu) umene adali kusangalala nawo mmenemo

    [28] “Umo ndi mmene zidalili. Ndipo tidawapatsa anthu ena zimenezo

    [29] “Thambo ndi nthaka sizidawalilire ndipo sadapatsidwe mpata (wobwereranso pa dziko)

    [30] “Ndipo ndithu tidapulumutsa ana a Israyeli ku chilango choyalutsa

    [31] “Chochokera kwa Farawo; ndithu iye adali wodzikweza ndiponso mmodzi wa opyola malire

    [32] “Ndipo ndithu tidawasankha (Ayuda nthawi imeneyo) pa mitundu ina m’kudziwa Kwathu

    [33] “Ndipo tidawapatsa zisonyezo (kupyolera m’dzanja la Mûsa) momwe mudali mayeso oonekera poyera kwa iwo

    [34] “Ndithu awa (Aquraish) akunena (kuti)

    [35] ““Palibe china choposera pa imfa yathu yoyambayi, ndipo ife sitidzaukitsidwa.”

    [36] ““Choncho tibweretsereni makolo athu (amene adafa), ngati mukunena zoona (kuti kuli kuuka).”

    [37] “Kodi iwo ndi abwino (ndi kupambana pa nyonga), kapena anthu a Tubba (mafumu a kudziko la Yemen) ndi amene adalipo kale iwo asadadze? Tidawaononga. Ndithu iwo adali oipa

    [38] “Ndipo sitidalenge thambo ndi nthaka ndi zimene zili pakati paizo, mwachibwana

    [39] “Sitidalenge ziwirizi koma mwachoonadi; koma anthu ambiri sakudziwa

    [40] “Ndithu tsiku lachiweruziro ndiyo nthawi yawo onse (imene alonjezedwa)

    [41] “Tsiku limene m’bale sadzathandiza m’bale wake pa chilichonse (ku chilango cha Allah), ngakhale iwo sadzapulumutsidwa

    [42] “Kupatula amene Allah adzawachitira chifundo. Ndithu Iye Ngwamphamvu zoposa, Ngwachisoni chosatha

    [43] “Ndithu mtengo wa Zakkumi

    [44] “Ndi chakudya cha ochimwa

    [45] “(Kutentha kwake) ngati mtovu wosungunulidwa, (wotentha kwambiri;) udzakhala ukuwira mmimba

    [46] “Monga kuwira kwa madzi otentha kwambiri

    [47] “(Kudzanenedwa): “Mgwireni; mkokereni (ndi kumponya) pakatikati pa Jahena!”

    [48] ““Kenako mthireni pamwamba pamutu wake chilango chamadzi otentha!”

    [49] “(Adzauzidwa mwachipongwe): “Lawa! Ndithu iwe ndiwe wamphamvu zambiri, wolemekezeka, (monga momwe udali kudzitamira muja).”

    [50] ““Ndithu izi ndi zimene mudali kuzikaikira zija!”

    [51] “Ndithu oopa Allah adzakhala pa malo a chitetezo

    [52] “Mminda ndi mu akasupe

    [53] “Adzavala (nsalu) za silika wopyapyala ndi silika wokhuthala uku atayang’anizana (nkhope)

    [54] “Umo ndi mmene zidzakhalire; ndipo tidzawakwatitsa ndi akazi okongola amaso aakulu

    [55] “Mmenemo adzakhala akuitanitsa mtundu uliwonse wa zipatso, mwamtendere

    [56] “Sadzalawa imfa mmenemo, kupatula imfa yoyamba ija; ndipo adzawateteza kuchilango cha Jahena

    [57] “Chifundo chochokera kwa Mbuye wako! Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu

    [58] “Ndithu taifewetsa (Qur’an) mchiyankhulo chako (cha Chiarabu) kuti akumbukire

    [59] “Choncho yembekeza; iwonso akuyembekezera, (kodi ndani chimtsikire chilango pakati panu)

    Atagwada

    Surah 45

    [1] “Hâ-Mîm

    [2] “Chivumbulutso cha buku (ili) chochokera kwa Allah Wamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya

    [3] “Ndithu kuthambo ndi m’nthaka muli zisonyezo (zazikulu zosonyeza kuti Allah alipo) kwa okhulupirira

    [4] “Ndiponso mkalengedwe kanu ndi zimene wazifalitsa mmenemo, mu zamoyo ndizisonyezo kwa anthu amene akutsimikiza

    [5] “Ndi kusinthana kwa usana ndi usiku, ndi mvula imene Allah akutsitsa kuchokera kumwamba, akuukitsa nthaka ndi mvulayo, itafa (itauma), ndi kuyendetsa mphepo mosinthasintha; (zonsezi) ndi zisonyezo kwa anthu anzeru

    [6] “Izi ndi Ayah (ndime) za Allah; tikukuwerengera iwe mwachoonadi. Kodi ndi nkhani yanji adzaikhulupirire atapanda kulabadira nkhani ya Allah ndi Ayah Zake

    [7] “Kuonongeka kuli pa aliyense wopeka zinthu, wamachimo ambiri

    [8] “Amene akumva Ayah za Allah zikuwerengedwa kwa iye kenako nkumapitiriza (zochita zake zosalungama) uku akudzikweza ngati kuti sadazimve ayazo; muuze nkhani ya chilango chowawa

    [9] “Ndipo akadziwa chinthu chochepa chochokera mma Ayah athu, amachichitira chipongwe; amenewa ndi amene adzakhala ndi chilango chosambula

    [10] “Jahannam ili (kuwayembekezera) kuseri kwawo; ndipo zimene adachita sizidzawathandiza chilichonse, ngakhale atetezi amene adadzipangira kusiya Allah (sadzawathandiza); ndipo adzapeza chilango chachikulu

    [11] “Ichi ndi chiongoko; ndipo amene adakanira Ayah za Mbuye wawo, adzakhala ndi chilango chachikulu chochokera mchilango chowawa

    [12] “Allah ndi Amene wakugonjetserani nyanja kuti zombo ziziyenda mmenemo mwa lamulo Lake; ndikuti munke mufunafuna chifundo Chake kuti muthokoze

    [13] “Ndipo wakugonjetserani za kumwamba ndi zam’nthaka, zonse zikuchokera kwa Iye. Ndithu mzimenezo muli zisonyezo kwa anthu amene amalingalira

    [14] “Nena kwa amene akhulupirira kuti awakhululukire amene sakuopa masiku a Allah (a chilango; mmasiku amenewo) kuti awalipire anthu pa zomwe amachita (zoipa)

    [15] “Amene akuchita chabwino akudzichitira yekha ndipo amene akuchita zoipa, zidzakhala paiye mwini. Kenako m’dzabwezedwa kwa Mbuye wanu

    [16] “Ndithu tidawapatsa ana a Israyeli buku, ulamuliro ndi uneneri; ndiponso tidawapatsa zina mwa zinthu zabwino ndikuwalemekeza pamwamba pa mitundu ina (ya nthawiyo)

    [17] “Ndipo tidawapatsa zisonyezo zoonekera pazinthu zachipembedzo chawo; sadapatukane mpaka pomwe kudawadzera kudziwa, chifukwa chadumbo pakati pawo. Ndithu Mbuye wako adzalamula pakati pawo tsiku la Qiyâma pa zimene adali kutsemphana

    [18] “Kenako tidakuika iwe pa malamulo a zinthu za chipembedzo (Chathu). Choncho tsatira malamulo (Athu), ndipo usatsate zilakolako za amene sadziwa (njira yoona)

    [19] “Ndithu iwo (amene akutsata njira zonama) sangakuthandize chilichonse kwa Allah; ndithu achinyengo ena a iwo amatetezana wina ndi nzake; koma Allah ndi Mtetezi wa oopa (Iye potsatira malamulo Ake ndi kusiya zoletsedwa)

    [20] “Iyi (Qur’an imene yavumbulutsidwa kwa iwe), ndizisonyezo kwa anthu chiongoko ndi chifundo kwa anthu omwe akutsimikiza (kuti lilipo tsiku la chiweruziro)

    [21] “Kodi amene adadzichitira zoipa akuganiza kuti tingawachite monga omwe adakhulupirira ndi kuchita zabwino kuti afanane pa moyo wawo ndi pa imfa yawo? Ndi kuweruza koipa kumene iwo akuweruza

    [22] “Ndipo Allah adalenga thambo ndi nthaka moona ndi kuti mzimu uliwonse ulipidwe zimene udadzichitira, (zoipa kapena zabwino) ndipo iwo sadzaponderezedwa

    [23] “Kodi wamuona amene wachichita chilakolako chake kukhala mulungu wake wompembedza? Ndipo Allah wamlekelera kuti asokere, kupyolera mkudziwa Kwake; ndipo wamdinda (chidindo) mmakutu mwake ndi mu mtima mwake ndi kumuika chivindikiro mmaso mwake. Choncho ndani angamuongole pambuyo pa Allah? Kodi simukumbukira

    [24] “Ndipo (okanira kuuka ku imfa) adanena: “Kulibe (moyo wina) koma moyo wathu womwewu wa padziko lapansi; timafa ndi kukhala ndi moyo; palibe chikutiononga koma nthawi basi.” Koma iwo alibe kudziwa pa zimene akunenazo; akungoganizira chabe

    [25] “Ndipo Ayah Zathu zikawerengcdwa kwa iwo zolongosola chilichonse momveka, alibe mtsutso wina koma kunena kuti: “Tibweretsereni makolo Athu (aukitseni akhale ndi moyo) ngati inu muli owona!”

    [26] “Nena (kwa iwo iwe Mtumiki): “Allah amakupatsani moyo. Kenako amakupatsani imfa. Kenako adzakusonkhanitsani tsiku la Qiyâma lopanda chikaiko.” Koma anthu ambiri sakudziwa

    [27] “Ndipo ufumu wa kumwamba ndi pansi ngwa Allah, ndipo tsiku limene Qiyâma idzachitika, (anthu) ogwirizana ndi zonama adzaonongeka patsikulo

    [28] “Ndipo udzaliona gulu lililonse litagwada (uku nkhope zili zyoli); gulu lililonse lidzaitanidwa ku kaundula wake (kukamuwerenga): “Lero mulipidwa zimene mudali kuchita!”

    [29] ““Uyu kaundula Wathu akunena zoona za inu; ndithu Ife tidali kulemba zimene mudali kuchita.”

    [30] “Koma amene adakhulupirira ndi kuchita zabwino, Mbuye wawo adzawalowetsa ku chifundo Chake; kumeneko ndiko kupambana koonekera

    [31] “Ndipo amene adakanira, (adzauzidwa kuti): “Kodi Ayah Zanga sizidali kuwerengedwa kwa inu? Koma inu mudadzikweza; ndipo mudali anthu oipa.”

    [32] “Ndipo kukanenedwa kuti lonjezo la Allah ndiloona, ndikuti Qiyâma ilibe chikaiko, mudali kunena: “Sitikudziwa Qiyâma kuti nchiyani; tikungoganizira chabe, ndipo tilibe chitsimikizo (cha Kiyamayo).”

    [33] “Choncho, kuipa kwa zimene adachita kudzawaonekera, ndipo zidzawazinga zimene ankazichitira chipongwe

    [34] “Kudzanenedwanso kwa iwowa: “Lero tikuiwalani (pokusiyani mchilango) monga momwe inu mudaiwalira kukumana ndi tsiku lanu ili. Ndipo malo anu ndi ku Moto, ndipo mulibe wokupulumutsani.”

    [35] ““Zimenezi nchifukwa chakuti inu mudazichitira chipongwe Ayah za Allah, ndipo moyo wa pa dziko udakunyengani.” Choncho lero satulutsidwa mmenemo ndipo madandaulo awo savomerezedwa

    [36] “Tero kutamandidwa konse ndi kwa Allah, Mbuye wakumwamba ndi Mbuye wa pa dziko lapansi; Mbuye wazolengedwa

    [37] “Ndipo ukulu ndi Wake, kumwamba ndi pansi; ndipo Iye ndi Wamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya

    Malo Amchenga

    Surah 46

    [1] “۞ Hâ-Mîm

    [2] “Chivumbulutso cha bukuli nchochokera kwa Allah Wamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya

    [3] “Sitidangolenga thambo ndi nthaka ndiponso zonse zapakati pa izo koma mwachoonadi ndi nyengo yoikidwa (yodziwika). Koma amene akana kukhulupirira (Allah) ngonyozera zimene achenjezedwa

    [4] “Nena: Tandiuzani amene mukuwapembedza ndi kumusiya Allah, ndisonyezeni chimene adalenga panthaka? Kapena ali ndi gawo la kuthangata polenga thambo? Ndibweretsereni buku limene lidadza kale, ili lisanadze, kapena zizindikiro zanzeru, ngati inu mukunena zoona

    [5] “Kodi ndindani amene ali osokera kwambiri kuposa amene akupembedza zina kusiya Allah zomwe sizingathe kumuyankha mpaka tsiku la chiweruziro ndipo izo (zimafano) sizikuzindikira za mapemphero awo

    [6] “Ndipo anthu onse akadzasonkhanitsidwa adzakhala adani awo ndikuwakanira mapemphero awo

    [7] “Ndipo pamene zikuwerengedwa kwa iwo Ayah Zathu zolongosola chilichonse (cha m’chipembedzo), amene sadakhulupirire amanena pa choonadi chikawadzera: “Awa ndi matsenga oonekera.”

    [8] “Kapena akunena kuti: “Waipeka (Qur’an)?” Nena: “Ngati ine ndaipeka, tero simungapeze chondithandizira nacho kwa Allah (ku chilango Chake). Iye ndiwodziwa kwambiri zimene mukuzijijirikira. Iye akukwana kukhala mboni pakati pa ine ndi inu ndipo Iye Ngokhululuka kwabasi, Wachisoni chosatha.”

    [9] “Nena: “Ine sindine woyamba pa aneneri, ndipo sindikudziwa zimene zidzachitike kwa ine ngakhale kwa inu. Sinditsatira koma zokhazo zimene zikuvumbulutsidwa kwa ine; ndipo ine sindili kanthu koma mchenjezi wolongosola (zofunika).”

    [10] “Nena: “Tandiuzani, ngati (buku ili) litachokera kwa Allah, ndipo inu nkulikana uku mboni yochokera mu ana a Israyeli itachitira umboni kuti idaliona longa limeneli, ndipo iyo nkulikhulupirira (bukuli) pomwe inu mwadzitukumula, ndithu Allah saongola anthu osalungama.”

    [11] “Ndipo amene sadakhulupirire adanena kwa amene adakhulupirira: “(Chipembedzo ichi) chikadakhala chabwino, awa sakadakhala otsogola ku chimenechi pa ife.” Ndipo chifukwa choti sadaongoke nalo (bukuli), akhala akunena: “Ili ndi bodza lakale.”

    [12] “Ndipo lisadadze ili lidalipo buku la Mûsa monga mtsogoleri ndi chifundo. Ndipo buku ili likuikira umboni (za bukulo) m’chiyankhulo cha Chiarabu kuti liwachenjeze amene adzichitira okha chinyengo, ndi kuti likhale uthenga wabwino kwa ochita zabwino

    [13] “Ndithu amene anena (kuti): “Mbuye wathu ndi Allah.” Kenako ndikulungama, sadzakhala ndi mantha (tsiku lakufa kwawo ngakhale pambuyo pake), ndiponso sadzadandaula

    [14] “Iwowo ndiwo anthu aku Jannah adzakhala kumeneko nthawi yaitali kukhala mphoto ya zimene amachita

    [15] “Ndipo tamulangiza munthu kuchitira zabwino makolo ake. Mayi wake adatenga pathupi pake mwamasautso; ndipo adam’bala mwamasautso. Kutenga pakati pake ndi kumsiitsa kuyamwa ndi miyezi makumi atatu. Kufikira atakula nsinkhu nkukwana zaka makumi anayi, (akakhala mwana wabwino) amanena: “E Mbuye wanga! Ndilimbikitseni kuthokoza mtendere Wanu umene mwandipatsa pamodzi ndi makolo anga, ndipo ndilimbitseni kuti ndizichita zabwino zimene (Inu) muziyanja ndipo ndikonzereni ndi kundilungamitsira ana anga. Ine ndatembenukira kwa Inu; ndiponso ine ndine m’modzi mwa ogonjera (Inu).”

    [16] “Iwowo ndiamene tikuwalandira zabwino zimene adachita ndipo tikuwakhululukira zolakwa zawo. Adzakhala m’gulu la anthu a ku Jannah. Ili ndi lonjezo loona lomwe adalonjezedwa

    [17] “Tsono (mwana woipa) amene akunena kwa makolo ake, (akamuitanira ku chikhulupiliro kuti): “Ndithu ndinu oipa (pa zimene mukundiitanirazi)! Mukundilonjeza kuti ndidzatulutsidwa mmanda ndili wamoyo, chikhalirecho mibadwo ndi mibadwo idapita kumanda ine kulibe (koma mpaka lero siidauke)?” Ndipo uku makolo ake akupempha Allah kuti ampulumutse ndi kumuongola ndi kunena kwa iye: “Tsoka kwa iwe khulupirira (Allah ndi kuuka ku imfa, ngati sutero waonongeka). Ndithu lonjezo la Allah ndiloona.” Koma iye nkumanena (kuti): “Mukunenazi sikanthu koma ndi nthano za anthu akale.”

    [18] “Iwowo ndiamene latsimikizika pa iwo liwu (la chilango) pamodzi ndi mibadwo ya ziwanda ndi anthu, imene idanka kale iwo kulibe; ndithu iwo adali otaika

    [19] “Ndipo aliyense wokhulupirira adzakhala ndi nyota molingana ndi zimene adachita, ndi kuti (Allah) awalipire zochita zawo ndipo iwo sadzaponderezedwa

    [20] “Ndipo (akumbutse za) tsiku limene adzaikidwa pafupi ndi moto amene sadakhulupirire (adzawauza kuti) “Mudaononga zabwino zanu mmoyo wa dziko lapansi, (choncho lero simuzipezanso), ndipo inu mudasangalala nazo zimenezo, choncho lero mupatsidwa chilango chokusambulani chifukwa cha kudzikweza kwanu pa dziko popanda choona, ndiponso chifukwa cha kulakwa kwanu.”

    [21] “Ndipo kumbuka za m’bale wa Âdi, (mtumiki Hûd) pamene adachenjeza anthu ake kudziko la milu ya mchenga. Ndithu adaliponso achenjezi iye asadadze ndiponso iye atapita. (Iye adawauza anthu ake): “Musampembedze aliyense koma Allah; ndithu ine ndikukuoperani chilango cha tsiku lalikulu.”

    [22] “Adanena: “Ha! Kodi watidzera kuti utipatule ku milungu yathu? Choncho tibweretsere zimene ukutilonjezazo ngati uli mwa onena zoona.”

    [23] “Adanena (Hûd): “Ndithu kudziwa (kwenikweni kwa zimenezo) kuli kwa Allah; ndipo ine ndikungofikitsa kwa inu zimene ndatumidwa koma ine ndikukuonani kuti inu ndinu anthu amene mukuchita (zinthu za) umbuli

    [24] “Kenako pamene adauona (mtambo) ukulunjika ku zigwa zawo, adanena: “(Mtambo) uwu ndi wotivumbwitsira mvula!” (Adauzidwa): “Iyayi, chimenechi ndichimene mudachifulumizitsa chija (kuti chidze mwachangu), mphepo (ya mkutho) yomwe mkati mwake muli chilango chowawa

    [25] “Yoononga chinthu chilichonse mwa lamulo la Mbuye wake!” Kenako adali osaonedwanso, kupatula nyumba zawo (ndizimene zidatsalira). Umo ndim’mene timawalipirira anthu oipa

    [26] “Ndipo ndithu tidawapatsa mphamvu (yochitira zinthu ndi kukhala ndi chuma chambiri ndi moyo wautali) zomwe sitidakupatseni inu (Aquraish) ndipo tidawapatsa makutu ndi maso ndi mitima, koma makutu awo ndi maso awo ndi mitima yawo sizidawapindulire chilichonse chifukwa chotsutsa Ayah za Allah; ndipo zidawazinga zomwe adali kuzichitira chipongwe

    [27] “Ndithu tidaiononga midzi imene yakuzungulirani; ndipo tidawafotokozera momveka Ayah Zathu kuti abwelere

    [28] “Chifukwa chiyani siidawapulumutse milungu imene adaipangayo kusiya Allah kuti iwayandikitse kwa Iye (Allah)? Koma idasoweka kwa iwo (pomwe iwo adali pamavuto ofuna kulandira chithandizo). Ndipo zimenezo ndizo zotsatira zabodza lawo ndi zomwe adali kupeka

    [29] “Ndipo (kumbuka iwe Mtumiki{s.a.w}) pamene tidakutumizira gulu la ziwanda (majini) kudzamvera Qur’an ndipo pamene izo zidafika pamalopo zidanena pakati pawo: “Khalani chete!” Pomwe kuwerenga (kwa Qur’an) kudatha, zidabwerera ku mtundu wawo kukawachenjeza (za chilango cha Allah)

    [30] “Zidanena: “E inu anzathu! Ife tamva (zowerengedwa) za m’buku (lolemekezeka) lomwe lavumbulutsidwa pambuyo pa Mûsa, loikira umboni zimene zidalitsogolera; likuongolera ku choona ndi kunjira yolunjika.”

    [31] ““E inu anzathu! Muvomereni woitana wa Allah, ndipo mkhulupirireni; (Allah) akukhululukirani machimo anu ndi kukutetezani ku chilango chowawa

    [32] “Ngati wina samuvomera woitanira kwa Allah, sangamulepheretse (Allah) pa dziko (akafuna kumuchita kanthu), ndipo iye alibe atetezi ena kupatula Iye (Allah). Otere akusokera koonekera poyera.”

    [33] “Kodi iwo saona kuti Allah Amene adalenga thambo ndi nthaka, ndipo sadatope pozilenga, ndi Wakutha kuwaukitsa anthu ku irnfa? Inde, ndithu Iye Ngokhoza kuchita chilichonse

    [34] “Ndipo (akumbutse za) tsiku limene adzaperekedwa ku moto amene sadakhulupirire (uku akuuzidwa): “Kodi izi sizoona?” Adzanena: “Inde, pali Mbuye wathu!” (Allah) adzanena: “Choncho, lawani chilango chifukwa cha kukana kwanu (choonadi).”

    [35] “Choncho pirira (Mtumiki {s.a.w}) monga adapirira aneneri, eni mphamvu ndi kulimba pa chipembedzo, (monga Nuh. Ibrahimu, Mûsa ndi Isa (Yesu); ndipo usawachitire changu. Tsiku limene adzaziona zimene adalonjezedwa kudzakhala monga iwo sadakhalitse pa dziko koma ngati adakhala ola limodzi lokha lamasana. (Zomwe mukuuzidwazi) ndi ulaliki okwana. Palibe adzaonongedwe (ndi chilango cha Allah), kupatula anthu ochimwa (otuluka m’chilamulo cha Allah)

    Muhammad

    Surah 47

    [1] “Amene adam’kana (Allah ndi Mthenga Wake) ndi kutsekereza anthu kuyenda panjira ya Allah (powaletsa kulowa m’Chisilamu), Allah waononga zonse zabwino zimene adachita

    [2] “Ndipo amene akhulupirira nkumachita zabwino, nkuzikhulupirira zimene zavumbulutsidwa kwa Muhammad (s.a.w), zimene zili zoona zochokera kwa Mbuye wawo, wawafafanizira zolakwa zawo, ndipo awakonzera chikhalidwe chawo (patsiku lachimaliziro ndi padziko lapansi)

    [3] “Zimenezi nchifukwa chakuti amene sadakhulupirire adatsata chonama, ndipo amene adakhulupirira adatsatira choonadi chochokera kwa Mbuye wawo. M’menemu ndim’mene Allah akuperekera kwa anthu mafanizo awo (kuti alingalire ndi kupeza phunziro)

    [4] “Ndipo mukakumana nawo pankhondo amene sanakhulupirire amenyeni makosi awo (aduleni), mpaka mwafooketse pochuluka ophedwa mwa iwo; kenako amangeni ndi zingwe (otsalawo). Ngati mutafuna kuwamasula popanda dipo kapena kuti apereke dipo, (zili kwa inu). Kufikira nkhondo itatha. Limenelo ndi lamulo la Allah. Ndithu Allah akadafuna akadathana nawo Iye mwini powaononga onse psiti; koma (wakulamulani kuti muchite nkhondo) ncholinga choti awayese mayeso ena a inu pa ena (okhulupirira pa okanitsitsawo). Ndipo amene aphedwa panjira ya Allah, ntchito yawo sadzaipititsa pachabe

    [5] “Awaongolera (ku zimene zingawapindulitse pa dziko lapansi ndi patsiku lachimaliziro) ndi kuwakonzera zinthu zawo ndi chikhalidwe chawo

    [6] “Ndi kukawalowetsa ku Munda wamtendere umene adawadziwitsa

    [7] “E inu amene mwakhulupirira! Ngati muteteza chipembedzo cha Allah, (Iye) adzakutetezani (kwa adani anu) ndi kulimbikitsa mapazi anu (pa nkhondo)

    [8] “Koma amene akana (Allah ndi Ayah Zake) kuwonongeka nkwawo ndipo awaonongera zochita zawo

    [9] “Zimenezo nchifukwa chakuti iwo azida zomwe Allah adavumbulutsa (monga Qur’an ndi malamulo ake;) choncho waziononga zochita zawo

    [10] “Kodi sadayendeyende padziko nkuona kuti adali bwanji mapeto a amene adawatsogolera (monga Âdi ndi Samudi, ndi anthu a Luti ndi ena otero)? Allah adawaononga psiti, ndipo chilango ngati chimenecho chidzakhalanso kwa osakhulupirira

    [11] “Zimenezo nchifukwa chakuti Allah ndi Mtetezi wa amene akhulupirira, koma osakhulupirira alibe mtetezi

    [12] “Ndithu Allah adzawalowetsa ku Minda ya mtendere amene adakhulupirira ndi kuchita zabwino, (momwe) pansi pake ikuyenda mitsinje; koma amene sadakhulupirire akusangalala (padziko lapansi) ndi kudya momwe zidyera ziweto (popanda lingaliro lililonse kupatula lingaliro la mimba zawo ndi kukwaniritsa zilakolako za chilengedwe chawo); ndipo Moto ndiwo malo awo

    [13] “Ndi ambiri mwa eni mizinda (yakale) omwe adali amphamvu kuposa eni mzinda wakowu umene akutulutsamo (eni ake,) tidawaononga (ndi zilango zosiyanasiyana) koma padalibe wowateteza (kwa Ife)

    [14] “Kodi angafanane, (polandira mphoto,) amene ali ndi umboni wodziwika wochokera kwa Mbuye wake, (kotero kuti nkumamumvera, ndi amene wakometsedwa ndi zochita zake zoipa natsatira zilakolako zawo)

    [15] “Fanizo la Munda wamtendere (Jannah) umene alonjezedwa oopa Allah (potsatira malamulo Ake ndi kusiya zoletsedwa, udzakhala chonchi): M’menemo muli mitsinje yamadzi osasintha fungo lake; ndi mitsinje yamkaka wosasasa mkakomedwe kake; ndi mitsinje yavinyo wokoma kwa akumwa ndi mitsinje ya uchi woyeretsedwa (ku phula), ndiponso iwo adzapeza m’menemo mtundu uliwonse wa zipatso ndi chikhululuko chochokera kwa Mbuye wawo. Angafanane ndi wokhala nthawi yaitali ku Moto, ndi kumwetsedwa madzi owira omwe akadula matumbo awo

    [16] “Ndipo ena mwa iwo (okana Allah) amamvetsera kwa iwe, (popanda kupindula chilichonse), ndipo akachoka pamalo pakopo, amanena kwa amene apatsidwa nzeru (mwa omtsatira ake): “Kodi (Mtumiki) wanena chiyani posachedwapa?” Iwowo ndiamene Allah wawadinda m’mitima mwawo (ndi chidindo chokana Allah), ndipo amatsatira zilakolako zawo (zachabe)

    [17] “Ndipo amene aongoka, (Allah) amawaonjezera chiongoko ndi kuwapatsa kuopa kwawo (komuopa Allah)

    [18] “Kodi pali chimene akuyembekezera posakhala tsiku lachiweruziro limene liwadzere mwadzidzidzi (uku iwo ali otanganidwa ndi zam’dziko)? Ndithu zizindikiro zake zadza kale; kodi kudzawapindulira chiyani kukumbuka kwawo likadzawadzera (tsikulo)

    [19] “Dziwa kuti palibe wompembedza m’choonadi koma Allah, ndipo pempha chikhululuko pa zolakwa zako ndi zolakwa za okhulupirira aamuna ndi aakazi; ndipo Allah akudziwa malo anu opita ndi kubwera ndi malo anu Wokhazikika

    [20] “Ndipo amene akhulupirira akunena (chifukwa cha mazunzo omwe amawapeza kuchokera kwa osakhulupirira kuti) kodi nchifukwa ninji siikuvumbulutsidwa sura (yotiloleza kumenyana ndi osakhulupirira Allah amene akutiputa)? Koma ikavumbulutsidwa Sura yokhazikika (lamulo lake), ndipo mkati mwake ndi kutchulidwa nkhani zankhondo, uwaona amene ali ndi matenda m’mitima mwawo akukuyang’ana m’mayang’anidwe a yemwe akukomoka ndi imfa, (chifukwa cha kulida lamulo lomenyana ndi osakhulupirira), basi kuonongeka ndi kwawo

    [21] “(Zofunika ndi) kumvera ndi mawu abwino ndi kuti chinthu chikatsimikizika (achichite). Ngati akadamumvera Allah, ndithu zikadakhala zabwino kwa iwo

    [22] “Mwina mwake inu mukanyoza (Chisilamu), mubwerera m’mbuyo ku zomwe mudali nazo (m’nthawi ya umbuli) monga kuononga pa dziko ndi machimo) ndi kudula chibale chanu

    [23] “Oterewo ndiamene Allah wawatembelera ndi kuwagonthetsa ndi kuwachititsa khungu maso awo

    [24] “Kodi sakuilingalira Qur’an? Kapena m’mitima mwawo m’motsekedwa ndi akabali (maloko) ake

    [25] “Ndithu amene akubwerera m’mbuyo (kusiya chipembedzo chawo nkubwerera ku zosakhulupirira Allah) chiongoko chitawaonekera poyera satana ndiamene wawanyenga, ndipo Allah akuwapatsa nthawi

    [26] “Zimenezo nkaamba kakuti iwo adanena kwa omwe amada zimene Allah wavumbulutsa (kuti): “Tidzakumverani m’zinthu zina (zimene mukutsutsana ndi Mtumiki{s.a.w}).” Ndipo Allah akudziwa zobisika zawo

    [27] “Kodi adzakhala bwanji pamene angelo azidzatenga mizimu yawo uku akumenya nkhope zawo ndi misana yawo

    [28] “Zimenezi (imfa yoopsayi) nkaamba kakuti iwo adatsata zomwe zidakwiitsa Allah ndi kuda zomusangalatsa (Allah); choncho adaziwononga zochita zawo

    [29] “Kodi amene ali ndi matenda m’mitima mwawo akuganiza kuti Allah sangaonetsere poyera kaduka kawo

    [30] “Ndipo tikadafuna tikadakuonetsa iwo (amene akuchitira kaduka Chisilamu) ndipo ukadawadziwa ndi zizindikiro zawo. Koma ndithu uwadziwa m’kayankhulidwe (kawo) kokometsa ndipo Allah akudziwa zochita zanu zonse

    [31] “Ndipo ndithu tikuyesani mayeso mpaka tiwaonetsere poyera (adziwike) amene akumenya nkhondo mwa inu (chifukwa cha dini) ndi opirira (pamavuto); ndi kuzionetsera poyera nkhani zanu (zochita zanu)

    [32] “Ndithu amene akana (Mtumiki {s.a.w}) ndi kuwatsekereza anthu ku njira ya Allah, ndi kutsutsana ndi Mtumiki chiongoko chitadziwika kwa iwo, sangamsautse Allah ndi chilichonse, koma adzawaonongera ntchito zawo

    [33] “E inu amene mwakhulupirira! Mvereni Allah ndiponso mvereni mtumiki (Wake) ndipo musaononge ntchito zanu

    [34] “Ndithu amene sadakhulupirire ndi kwatsekereza anthu kunjira ya Allah, kenako nkufa uku ali osakhulupirira Allah sadzawakhululukira (zolakwa zawo)

    [35] “Musafooke ndi kufuna chimvano, (koma menyanani ndi adani anu); inu ndinu opambana. Ndipo Allah ali nanu (pokuthangatani ndi kukupulumutsani,) ndipo sakuchepetserani (mphoto ya) ntchito zanu

    [36] “Ndithu moyo wapadziko lapansi ndi masewera ndi chibwana. Ndipo ngati mukhulupirira ndi kudzipatula kumachimo (Allah) akupatsani malipiro anu, ndipo sakukupemphani chuma chanu

    [37] “Ngati akadachifuna (kuchokera) kwa inu chumacho ndi kukuchulukitsirani (chopereka),mukadachita umbombo (ndi chumacho), ndipo akadatulutsira (poyera) kaduka kanu

    [38] “Ha! Ndinu amene mukuitanidwa kuti mupereke (chuma) mu njira ya Allah. Koma alipo ena a inu akuumira ndipo amene akuumira akuzimana yekha. Allah Ngwachikwanekwane ndipo inu ndinu amphawi. Ngati munyoza (Chisilamu) ndi kubwerera m’mbuyo posakhulupirira) Allah adzabweretsa m’malo mwanu anthu ena; iwo sadzakhala ngati inu

    Chigonjetso

    Surah 48

    [1] “Ndithu takugonjetsera (iwe Mtumiki{s.a.w}mzinda wa Makka) kugonjetsa kwakukulu koonekera poyera

    [2] “Kuti Allah akukhululukire zolakwa zako zapatsogolo ndi zapambuyo, ndi kukukwaniritsira mtendere Wake, ndi kukuongolera kunjira yolunjika

    [3] “Ndikuti Allah akuteteze ndi chitetezo champhamvu

    [4] “Iye ndiamene adatsitsa chikhazikiko (kudekha) m’mitima mwa okhulupirira kuti awonjezera chikhulupiliro pachikhulupiro chawo. Makamu ankhondo akumwamba ndi pansi, nga Allah, (monga angelo, ziwanda, nyama ziphaliwali, mphepo yamkuntho ndi zivomerezi ndi zina zotero); ndipo Allah Ngodziwa chilichonse, ndiponso Wanzeru zakuya

    [5] “(Wachita izi) kuti okhulupirira aamuna ndi aakazi akawalowetse m’minda yomwe pansi pake ikuyenda mitsinje; adzakhala nthawi yaitali mmenemo, ndi kuti awafafanizire zolakwa zawo; kumeneko, kwa Allah ndiko kupambana kwakukulu

    [6] “Ndi kuti awalange achiphamaso aamuna ndi aakazi ndi omphatikiza Allah aamuna ndi aakazi oganizira Allah maganizo achabe. Kutembenuka koipa kuli kwa iwo ndipo Allah wawakwiyira ndiponso wawatembelera ndi kuwakonzera Jahannamu. Ndipo kumeneko nkobwerera koipa

    [7] “Ndipo magulu ankhondo akumwamba ndi pansi nga Allah; ndipo Allah ndi Wamphamvu zoposa, Wa nzeru zakuya

    [8] “Ndithu takutumiza kuti ukhale mboni ndi wolengeza nkhani zabwino ndiponso mchenjezi

    [9] “Ncholinga choti mumkhulupirire Allah ndi Mtumiki Wake, ndi kuti mumtukule ndi kumulemekeza (Mtumiki) ndi kutinso mumtamande (Allah) m’mawa ndi madzulo

    [10] “Ndithu amene akukulonjeza, ndiye kuti akulonjeza Allah. Dzanja la Allah lili pamwamba pa manja awo. Amene ati aswe lonjezo, ndiye kuti wadziswera yekha (mavuto ali pa iye). Koma yemwe akwaniritse zomwe adalonjeza kwa Allah, amulipira malipiro aakulu

    [11] “Adzanena kwa iwe Arabu am’midzi otsala (ku nkhondo, amene adalibe zifukwa zomveka m’kutsala kwawo): “Chuma ndi ana athu zidatitangwanitsa; choncho tipemphereni chikhululuko.” Akunena ndi malirime awo (mawu) omwe m’mitima mwawo mulibe. Nena: “Kodi ndani angathe kukuthandizani chilichonse kwa Allah ngati atafuna kukupatsani masautso, kapena atafuna kukupatsani zabwino? Koma Allah Akudziwa zonse zimene mukuchita.”

    [12] ““Koma mudali kuganiza kuti Mtumiki ndi okhulupirira sabwereranso ku maanja awo, (akaphedwa konko); zimenezo zidakukondweretsani m’mitima mwanu, ndipo mumaganiza ganizo loipa; ndipo mudali anthu oonongeka.”

    [13] “Ndipo amene sakhulupirira Allah ndi Mtumiki Wake, ndithu Ife tawakonzera okanira chilango cha Moto woyaka

    [14] “Ndipo ufumu wakumwamba ndi pansi ngwa Allah. Amakhululukira amene wamfuna (ngati atatembenukira kwa Iye) ndi kumlanga amene wamfuna (ngati sanatembenukire kwa Iye). Ndipo Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha

    [15] “Otsala (kunkhondo) aja, mukapita kukatenga zotola za a nkhondo, adzanena: “Tiloleni tikutsatireni.” Akufuna kuti asinthe mawu a Allah. Nena: “Simutitsatira! Umo ndimo Allah adanenera kale.” (Apo) adzanena (kuti): “Koma mukutichitira dumbo.” Iyayi, koma nzochepa zomwe adali kuzindikira

    [16] “Nena kwa otsala (kunkhondo) mwa Arabu a m’midzi: “Mudzaitanidwa (kukamenyana) ndi anthu eni mphamvu zaukali; mudzamenyana nawo kapena adzagonja (ndi kulowa m’Chisilamu). Ngati mudzamvera, Allah adzakulipirani malipiro abwino, koma ngati mutembenuka monga mudatembenukira kale adzakulangani ndi chilango chowawa.”

    [17] “Palibe tchimo pa wakhungu, palibenso tchimo pa olumala, palibenso tchimo pa wodwala (atasiya kupita ku nkhondo). Ndipo amene angamumvere Allah ndi Mtumiki Wake, adzam’lowetsa m’minda momwe mukuyenda mitsinje pansi pake; ndipo amene anyozere, amulanga ndi chilango chowawa

    [18] “Ndithu Allah adawayanja okhulupirira pamene amagwirana nawe (Mtumiki) chanza pansi pa mtengo pomwe amakulonjeza (kuti adzamenya nkhondo mpaka imfa) Allah adadziwa zomwe zidali m’mitima mwawo ndipo adatsitsa pa iwo kukhazikika (ndi kudekha;) ndipo adawalipira kupambana kwapafupi

    [19] “Ndipo zofunkha zambiri za pa nkhondo adzazitenga; ndipo Allah Ngwamphamvu zoposa, Wanzeru zakuya

    [20] “Allah wakulonjezani zofunkha zambiri zapankhondo (zomwe) mudzazitenga, ndipo wachita changu kukupatsani izi, (zinazo asanakupatseni). Ndipo watsekereza manja a anthu pa inu (kuti asakumenyeni). Ndi kuti chikhale chisonyezo cha okhulupirira (amene akudza pambuyo panu), ndi kuti akuongolereni kunjira yolunjika

    [21] “Ndi zina zimene simudazithe (kuzipeza); Allah wazidziwa. Ndipo Allah Ngokhoza chilichonse

    [22] “Ndipo akadayesa kumenyana nanu amene sadakhulupirire; akadatembenuza misana kuthawa; kenako sakadapeza mthandizi kapena mtetezi

    [23] “Iyi ndinjira ya Allah imene idapita kale, ndipo sungapeze kusintha pa njira ya Allah

    [24] “Ndipo Iye ndi amene adatsekereza manja awo pa inu; ndi manja anu pa iwo, pa chigwa cha Makka, pambuyo pokupambanitsani pa iwo. Ndipo Allah akuona zonse zimene mukuchita

    [25] “Iwowo ndiamene sadakhulupirire, ndipo adakutsekerezani kulowa mu Msikiti Wopatulika pomwe nyama zansembe zidangomangika osakafika pamalo pake. Kukadakhala kuti kulibe amuna okhulupirira ndi akazi okhulupirira omwe simudawadziwe kuti mungawaponde potero inu kukanakupezani kudzudzulidwa kuchokera kwa iwo popanda kudziwa, (Allah akadakulolezani kumenyana nawo. Koma wachita izi) kuti Iye amulowetse ku mtendere Wake amene wamfuna. Akadadzipatula, tikadawalanga ndi chilango chowawa amene sadakhulupirire pakati pawo

    [26] “Pamene omwe sadakhulupirire adaika mkwiyo m’mitima, mkwiyo waumbuli, Allah adatsitsa chikhazikiko Chake ndi kudekha pa Mtumiki Wake ndi pa okhulupirira, ndipo adawalimbikitsa ndi mawu woopa Allah; ndipo adali eni mawuwo ndi oyenerana nawo. Ndipo Allah Ngodziwa chilichonse

    [27] “Ndithu Allah adamtsimikizira Mtumiki Wake za maloto ake owona: “Ndithu inu mudzalowa mu Msikiti Wopatulika mwamtendere Allah akafuna; mutameta mitu yanu mpala kapena (ena) kuyepula (tsitsi lawo), simudzaopa (nthawi imeneyo); ndipo Allah amadziwa zimene simumazidziwa, ndipo zisanapezeke zimenezo, akupatsani kupambana kumene kuli pafupi

    [28] “Iye ndi Yemwe adatumiza Mtumiki Wake ndi chiongoko ndi chipembedzo choona kuti achiike pamwamba pa zipembedzo zonse. Ndipo Allah akukwanira kukhala mboni (yake)

    [29] “Muhammad (s.a.w) ndi Mtumiki wa Allah; ndipo amene ali pamodzi ndi iye ngamphamvu kwa osakhulupirira (Allah), ngachifundo chambiri pakati pawo. Uwaona akugwira m’maondo ndi kugwetsa nkhope zawo pansi ncholinga chofuna zabwino za Allah ndi chikondi (Chake). Zizindikiro zawo zili pa nkhope zawo zosonyeza kulambira kwawo. Ili ndi fanizo lawo m’Chipangano chakale, Ndipo fanizo lawo m’Chipangano chatsopano nkuti iwo ali monga mmera womwe watulutsa nthambi zake; kenako (nthambizo) nkuulimbitsa ndi kukhala waukulu ndi kuima bwinobwino ndi tsinde lake, nkuwasangalatsa omwe adaubzala. (Choncho) zotsatira zake, nkuwakwiyitsa osakhulupirira chifukwa cha iwo. Allah walonjeza chikhululuko ndi malipiro aakulu (kwa) amene akhulupirira ndi kuchita zabwino mwa iwo

    Zipinda

    Surah 49

    [1] “E inu amene mwakhulupirira! Musamatsogoze (kulamula chinthu chapachipembedzo kapena cham’dziko) patsogolo pa (mawu a) Allah ndi Mthenga Wake. Ndipo muopeni Allah, ndithu Allah Ngwakumva, Ngodziwa

    [2] “E inu amene mwakhulupirira! Musamakweze mawu anu pamwamba pa mawu a Mneneri; musakweze mawu pokamba naye monga momwe mumayankhulira nokhanokha, kuopa kuti zochita zanu zingaonongeke (ndi kukhala zopanda mphoto) pomwe inu simukuzindikira

    [3] “Ndithu amene akutsitsa mawu awo pamaso pa mtumiki wa Allah, iwo ndiamene Allah wawayeretsa mitima yawo pomuopa Iye; chikhululuko ndi malipiro akulu zidzakhala pa iwo

    [4] “Ndithu amene akukuitana (uku ali) kuseri kwa zipinda (za nyumba), ambiri a iwo sazindikira

    [5] “Ndipo iwo akadapirira ndi kuyembekeza (kuti) mpaka utuluke ndi kudza kwa iwo, zikadakhala zabwino kwa iwo; koma Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachisoni chosatha

    [6] “E inu amene mwakhulupirira! Ngati atakudzerani munthu wosakhulupirika ndi nkhani (iliyonse, musamuvomereze); ifufuzeni (kaye) kuopa kuti mungachitire anthu (mtopola) mwa umbuli, ndikuti mungazanong’oneze bondo pa zomwe mwachita

    [7] “Ndipo dziwani kuti ndithu mwa inu muli Mtumiki wa Allah, (mumvereni iye zimene akukuuzani) kukadakhala kuti iye akukumverani pa zinthu zambiri (zimene mukumuuza), mukadavutika. Koma Allah wachichita chikhulupiliro kukhala chokondeka kwa inu ndipo wachikometsa m’mitima mwanu ndipo wakuchitani kuti mukude kusakhulupirira ndi ufasiki (kutuluka m’malamulo a Allah) ndi kunyoza (Allah.) Iwowo ndiwo oongoka

    [8] “(Chifukwa cha) ubwino wochokera kwa Allah ndi mtendere (Wake, mwapeza zimenezi); ndipo Allah Ngodziwa, Ngwanzeru zakuya

    [9] “Ndipo ngati magulu awiri aokhulupirira atamenyana ayanjanitseni pakati pawo. Ngati gulu limodzi mwa magulu awiriwo likuchitira mtopola linalo, limenyeni limene likuchita mtopola mpaka libwelere ku lamulo la Allah; ngati litabwerera, ayanjanitseni pakati pawo mwachilungamo, ndipo chitani chilungamo; ndithu Allah amakonda ochita chilungamo

    [10] “Ndithu okhulupirira onse ndi pachibale choncho yanjanitsani pakati pa abale anu; (musanyozere lamulo la kuyanjanitsa) ndipo muopeni Allah kuti akuchitireni chifundo

    [11] “E inu amene mwakhulupirira! Amuna asanyoze amuna anzawo; mwina (onyozedwa) nkukhala abwino (kwa Allah) kuposa iwo (onyoza). Nawonso akazi asanyoze akazi anzawo; mwina onyozedwa nkukhala abwino (kwa Allah) kuposa iwo (onyoza). Ndipo musatukwanizane pokumbana mitundu kapena kuitanana ndi maina oipa. Taonani kuipa kumuyitanira munthu ndi dzina loti fasiki (wotuluka m’malamulo a Allah) atakhulupirira kale; ndipo amene salapa (ku zimenezi), iwo ndiwo (ochimwa) odzichitira okha chinyengo

    [12] “E inu amene mwakhulupirira! Dzitalikitseni kuwaganizira kwambiri zoipa (anthu abwino). Ndithu kuganizira (anthu) maganizo (oipa) nditchimo. Ndipo musafufuzefufuze (nkhani za anthu) ndiponso musajedane pakati panu. Kodi mmodzi wa inu angakonde kudya minofu ya m’bale wake wakufa? Simungakonde zimenezo ndipo muopeni Allah. Ndithu Allah Ngolandira kulapa, Ngwachisoni chosatha

    [13] “E inu anthu! Tidakulengani (nonse) kuchokera kwa mwamuna (m’modzi; Adam) ndi mkazi (m’modzi; Hawa), ndipo tidakuchitani kukhala a mitundu ndi mafuko (osiyanasiyana) kuti m’dziwane (basi). Ndithu wolemekezeka kwambiri mwa inu kwa Allah, ndi yemwe ali woopa. Ndithu Allah Ngodziwa, ndipo Ngodziwa kwambiri nkhani zonse

    [14] “Arabu akumidzi adanena (kuti): “Takhulupirira.” Nena, Simudakhulupirire (kwenikweni); koma nenani (kuti): “Tagonjera (Allah).” Ndipo mpaka pano chikhulupiliro sichidalowe m’mitima mwanu (ndi kukhazikika bwinobwino). Koma ngati mumvera Allah ndi Mtumiki Wake, sakuchepetserani chilichonse m’zochita zanu. Ndithu Allah Ngokhululuka kwabasi, Ngwachifundo chambiri

    [15] “Ndithu amene ali okhulupirira (moona) ndiomwe akhulupirira Allah ndi Mtumiki Wake, ndipo kenako nkukhala osakaika, nkuchita nkhondo panjira ya Allah, ndi chuma chawo, ndi matupi awo, iwowo ndiwo owona (pa chikhulupiliro chawo)

    [16] “Nena: “Kodi mukumdziwitsa Allah za chipembedzo chanu? Koma chikhalirecho Allah akudziwa zonse za kumwamba ndi za m’dziko lapansi. Ndipo Allah Ngodziwa chilichonse

    [17] “Akukukumba iwe chifukwa cha kulowa kwawo m’Chisilamu (ngati kuti akuchitira ufulu). Nena: “Kulowa kwanu m’Chisilamu musakuyese kuti mwandichitira ine ubwino, koma Allah ndiAmene wakuchitirani ubwino pokuongolerani ku chikhulupiliro, ngati muli owona.”

    [18] “Ndithu Allah akudziwa zobisika za kumwamba ndi za mnthaka. Ndipo Allah akuona zimene mukuchita

    Qaf

    Surah 50

    [1] “Qaf. Ndikulumbira Qur’an yolemekezeka

    [2] “Koma akudabwa chifukwa chowadzera Mchenjezi wochokera mwa iwo. Ndipo osakhulupirira adanena: “Ichi nchinthu chodabwitsa.”

    [3] “Kodi tikadzafa ndi kukhala fumbi (tidzaukanso?) Kubwerera kumeneko nkwakutali kwambiri, (nkosatheka).”

    [4] “Ndithu tikudziwa chimene nthaka ikuchepetsa m’matupi mwawo (akalowa m’manda). Ndipo kwa Ife kuli kaundula wosungidwa

    [5] “Koma adatsutsa choona pamene chidawadzera. Ndipo iwo ali m’chinthu chosokonezeka

    [6] “Kodi sawona thambo pamwamba pawo m’mene tidalimangira ndi kulikongoletsa? Ndipo lilibe ming’alu

    [7] “Ndipo nthaka tidaiyala; ndi kuika mapiri m’menemo ndi kumeretsamo m’mera Wokongola wamtundu uliwonse

    [8] “(Kuti zimenezi zikhale) chotsekula maso ndi chikumbutso kwa munthu aliyense wotembenukira (kwa Allah)

    [9] “Ndipo tatsitsa madzi odalitsidwa kuchokera ku mitambo, ndipo kupyolera m’madziwo, tameretsa (mmera) m’minda ndi mbewu zokololedwa

    [10] “Ndi mitengo italiitali ya kanjedza yokhala ndi mikoko yazipatso zothothana

    [11] “(Kuti chikhale) chakudya cha akapolo (a Allah); ndi madziwo taukitsa dziko lakufa (louma). Momwemo ndimmene kudzakhalira kutuluka m’manda (muli moyo)

    [12] “Kale, iwo kulibe, adatsutsa anthu a Nuh ndi eni chitsime ndi Asamudu

    [13] “Ndi Âdi, ndi Farawo ndi Abale a Luti

    [14] “Ndi anthu a m’mitengo (ya Aika), ndi anthu a Tubba; onsewo adatsutsa Aneneri; choncho chenjezo Langa lidatsimikizika (pa iwo)

    [15] “Kodi tidatopa nkulenga koyamba? Koma iwo ali m’maganizo osokonezeka m’zakalengedwe katsopano

    [16] “Ndithu tidamulenga munthu, ndipo Ife tikudziwa zimene mtima wake ukumunong’oneza; ndipo Ife tili pafupi ndi iye kuposa mtsempha wam’khosi mwake (wolumikizana ndi mtima)

    [17] “Ndipo pamene amalandira olandira awiri (angelo), wina amakhala kudzanja lamanja, wina kudzanja lamanzere

    [18] “Palibe chilichonse chimene amayankhula koma pafupi ndi iye pali mlonda amene wakonzekera (kulemba)

    [19] “Ndipo kuledzera kwa imfa kukam’dzera mwa choona, (pamenepo adzauzidwa): “Ichi ndi chomwe mumachithawa chija.”

    [20] “Ndipo lipenga lidzaimbidwa; limenelo ndilo tsiku lamavuto (tsiku lachiweruziro)

    [21] “Ndipo udzadza mzimu uliwonse pamodzi ndi m’busa (wake) ndi mboni (yake)

    [22] “(Adzauzidwa): “Ndithu udali wosalabadira zinthu izi; basi takuvundukulira (chomwe) chimakuphimba, ndipo kuyang’ana kwako lero nkwakuthwa!”

    [23] “Ndipo (Mngelo) yemwe adali naye (pamodzi ndikumalemba zochita zake) adzanena (kwa Mngelo wachilango): “Izi ndizimene zidakonzedwa ndi ine.”

    [24] “Mponyeni ku Moto aliyense wokanira, wamakani,”

    [25] ““Wotsekereza zabwino, wolumpha malire, wokaika.”

    [26] ““Amene adampangira Allah mulungu wina. Chomwecho mponyeni ku chilango chaukali.”

    [27] “Mnzake (satana) adzanena: “E Mbuye wathu! Sindidamsokeretse, koma iye mwini adali wosokera kutali kwambiri ndi choonadi”

    [28] “(Allah) adzanena: “Musakangane kwa Ine; ndidakutsogozerani kale chenjezo (Langa).”

    [29] “Liwu Langa silisinthidwa kwa Ine, ndipo Ine siwopondereza akapolo (Anga)

    [30] “Tsiku limene tidzaifunsa Jahannam: “Kodi wadzaza?” Iyo idzanena: “Kodi kuli zoonjezera?”

    [31] “Ndipo Munda wamtendere udzayandikitsidwa pafupi kwa oopa (Allah)

    [32] ““Izi ndizimene mumalonjezedwa, za aliyense wotembenukira kwa Allah, Wosunga (malamulo Ake)

    [33] “Amene adaopa (Allah), Wachifundo chambiri, pomwe samamuona ndi maso, ndipo adadza ndi mtima wotembenukira (kwa Iye).”

    [34] “(Adzauzidwa): “Uloweni mwamtendere.” Limeneli ndi tsiku lokhazikika mpaka muyaya

    [35] “M’menemo adzapeza chilichonse (chimene) adzafune, ndipo kwa Ife kuli zoonjezera

    [36] “Ndipo kodi ndi mibadwo ingati tidainonga kale iwo kulibe, yamphamvu kuposa iwo? Adayendayenda padziko. Kodi padalipo pothawira

    [37] “Ndithu m’zimenezi muli chikumbutso kwa yemwe ali ndi mtima ndi yemwe akutchelera khutu (uku) iye ali pompo (ndi maganizo ake)

    [38] “Ndithu tidalenga thambo ndi nthaka ndi zapakati pake m’masiku asanu ndi limodzi, ndipo sikudatikhuze kutopa kulikonse

    [39] “Choncho, pirira nazo zomwe akunenazo, ndipo lemekeza Mbuye wako pomutamanda dzuwa lisadatuluke, (Swala ya Subh), ndi (dzuwa) lisadalowe, (Swala ya Asr)

    [40] “Ndi gawo lausiku, (Swala ya Maghrib ndi Isha); ndiponso (mulemekeze) pambuyo pa mapemphero (popemphera Swala za Sunna)

    [41] “Ndipo mvetsera (za) tsiku limene woitana adzaitana kuchokera pamalo apafupi

    [42] “Tsiku limene adzamva phokoso mwa choonadi: limenelo ndilo tsiku lodzatuluka (m’manda)

    [43] “Ndithu Ife ndi amene timapereka moyo ndi kupereka imfa; ndipo kobwerera Nkwathu

    [44] “(Akumbutse za) tsiku limene nthaka idzang’ambike kwa iwo mwachangu; kusonkhanitsa kumeneko nkosavuta kwa Ife

    [45] “Ife tikudziwa bwino zimene akunena; iwe siuli wowakakamiza. Choncho mukumbutse ndi Qur’an yemwe akuopa chilango Changa

    Mphepo zowomba

    Surah 51

    [1] “. Ndikulumbilira mphepo imene ikubalalitsa mitambo ya mvula

    [2] “Ndi imene imasenza mitolo yolemera (ya madzi)

    [3] “Ndi kuyenda (nawo madziwo) mwaubwino

    [4] “Ndi awo amene amagawa rizq (limene Allah amalipereka kwa amene wamfuna)

    [5] “Ndithu zimene mukulonjezedwa nzoonadi, (zidzachitika)

    [6] “Ndipo, ndithu malipiro (pa zochita zanu) adzapezekadi

    [7] “Ndikulumbilira thambo lomwe njira zake zambiri nzoikidwa mwaluso

    [8] “Ndithu inu muli m’mau otsutsana, (pa zimene mukunena)

    [9] “(Kupyolera m’mawu amenewa) akuchotsedwa ku icho (chikhulupiliro chalonjezo loona) amene adachotsedwa (ku chikhulupilirocho)

    [10] “Aonongeka abodza (amene akunena za tsiku lachiweruziro mongoganizira)

    [11] “Iwo amene akubira mu umbuli, osalabadira (za tsiku lachimaliziro)

    [12] “Akufunsa (mwachipongwe ponena kuti) “Lidzakhala liti tsiku lamalipiro?”

    [13] “(Limenelo ndi) tsiku lomwe iwo adzalangidwa ku Moto

    [14] “(Adzawauza kuti): “Lawani chilango chanu ichi chimene munkachifulumizitsa (kuti chikufikeni).”

    [15] “Ndithu oopa (Allah) adzakhala (akusangalala) m’minda ndi mu akasupe okongola

    [16] “Uku akulandira zimene wawapatsa Mbuye wawo (malipiro aulemu); ndithu iwo ankachita zabwino asanapeze izi

    [17] “Nthawi yausiku amagona pang’ono. (Amadzuka nachita mapemphero mochulukitsa)

    [18] “Ndipo kum’bandakucha, iwo amapempha chikhululuko

    [19] “Ndipo m’chuma chawo mudali gawo (lodziwika) la opempha ndi osapempha (mwa osauka)

    [20] “M’nthaka muli zizindikiro kwa otsimikiza, (zosonyeza kuti Allah alipo)

    [21] “Ndi mwa inu nomwe; kodi simuona

    [22] “Ndipo kumwamba kuli zokuthandizani (pa moyo wanu), ndi zimene mukulonjezedwa

    [23] “Ndikulumbilira Mbuye wa kumwamba ndi pansi, ndithu zimenezo ndi zoona monga kulili kuyankhula kwanu

    [24] “Kodi yakufika nkhani ya alendo a Ibrahim; (angelo) olemekezeka

    [25] “Pamene adalowa kwa iye ndi kunena kuti: “Salaam,” (“Mtendere”)! Iye adayankha: “Salaam,” (“Mtendere) inu ndinu anthu osadziwika (achilendo).”

    [26] “Adatembenukira kwa akunyumba ake (mwakachetechete), ndipo adadza ndi nyama ya mwana wa ng’ombe yonona (yowotcha)

    [27] “Naipereka kwa iwo (koma sadadye); iye adanena (modabwa): “Kodi bwanji simukudya?”

    [28] “Mumtima mwake adadzazidwa mantha ndi iwo. Iwo adati: “Usaope,” ndipo adamuuza nkhani yabwino ya kubala mwana wodziwa

    [29] “Adadza mkazi wake ndi mkuwe (pamene adamva nkhani yabwino ija). Adadzimenya kunkhope (ndi dzanja lake kusonyeza kudabwa ndi kusatheka). Ndipo adati: (“Ine ndine) nkhalamba (ndiponso) chumba; (ndingabereke bwanji)?”

    [30] “Iwo adati: “Momwemo, Mbuye wako wanena. Iye Ngwanzeru zakuya (pa chilichonse chimene akulamula); Ngodziwa; (palibe chimene chingabisike kwa Iye)

    [31] “۞ (Ibrahim) adati: “Kodi nkhani yanu ndiyotani E inu otumidwa?”

    [32] “Iwo adati: “Tatumizidwa kwa anthu oipa.”

    [33] ““Kuti tiwagende ndi miyala yotenthedwa kuchokera kudongo.”

    [34] ““Yoikidwa chizindikiro cha aliyense wochimwa kuchokera kwa Mbuye wako.”

    [35] “Tidawatulutsa okhulupirira omwe adali m’mudzimo

    [36] “Sitidapeze mmenemo (okhulupirira ambiri) kupatula mnyumba imodzi ya Asilamu

    [37] “Ndipo tidasiya pamenepo chizindikiro (chosonyeza kuonongeka kwa eni mudziwo kuti chikhale lingaliro) kwa amene akuopa chilango chopweteka

    [38] “M’nkhani ya Mûsa (muli phunziro) pamene tidamtuma kwa Farawo uku atalimbikitsidwa ndi chisonyezo choonekera

    [39] “Koma Farawo adanyoza (kukhulupirira Mûsa) chifukwa chotama nyonga zake, ndipo adati: “Uyu ndi wamatsenga kapena wamisala.”

    [40] “Tidamlanga pamodzi ndi khamu lake la nkhondo ndi kuwaponya mnyanja; iye ali wodzudzulidwa

    [41] “Ndipo m’nkhani ya Âdi (muli phunziro) pamene tidawatumizira chimphepo (chamkuntho) chopanda chabwino mkati mwake

    [42] “Chomwe sichisiya chinthu chimene chachidutsa koma kuchichita monga chofumbwa

    [43] “Ndipo m’nkhani ya Samudu (muli chisonyezo) pamene kudanenedwa kwa iwo kuti: “Sangalalani (mnyumba zanu) mpaka nthawi yaikika.”

    [44] “Koma adadzikweza (ponyozera) lamulo la Mbuye wawo. Choncho chiphokoso chidawaononga uku akupenya

    [45] “Sadathe kuimilira ndi (kuthawa) ndiponso sadali wodzipulumutsa

    [46] “Naonso anthu a Nuh (tidawaononga) kale chifukwa iwo adali anthu otuluka mchilamulo (cha Allah)

    [47] “Thambo tidalimanga mwamphamvu (ndi luntha); ndipo tingathe kuchita zochuluka (kuposa zimenezi)

    [48] “Ndipo nthaka tidaiyala; taonani kukonza bwino Ife amene tidakonza nthaka

    [49] “Ndipo m’chinthu chilichonse talenga ziwiriziwiri kuti inu mulingalire (ndi kukhulupirira mphamvu Zathu)

    [50] “Thawirani kwa Allah. Ine ndine mchenjezi woonekera kwa inu wochokera kwa Iye

    [51] “Ndipo musadzipangire mulungu wina wompembedza ndi kumuphatikiza ndi Allah. Ndithu ine ndine mchenjezi woonekera poyera kwa inu wochokera kwa Iye

    [52] “Momwemo (ndimo idalili mibadwo yakale pamodzi ndi aneneri awo); palibe Mthenga amene adawadzera anthu akale, anthu akowa kulibe, popanda kumnena kuti: “Ndiwamatsenga kapena wamisala.”

    [53] “Kodi adalangizana za mawuwa pakati pawo? Iyayi, koma iwo ndianthu opyola malire

    [54] “Choncho apatukire iwo (amakani), iwe suli wodzudzulidwa (pakuleka kwawo kuyankha kuitana)

    [55] “Kumbutsa. Ndithu kukumbutsa kumawathandiza okhulupirira

    [56] “Sindidalenge ziwanda (majini) ndi anthu koma kuti azindipembedza

    [57] “Sindifuna kwa iwo chithandizo ndiponso sindifuna kuti azindidyetsa

    [58] “Ndithu Allah ndi Amene amapereka rizq; Iye ndi Mwini mphamvu zoposa; Wolimba, (salaphera kanthu)

    [59] “Ndithu amene adzichitira okha chinyengo (pokana ndi kutsutsa) ali nalo gawo la chilango monga gawo la anzawo (a mibadwo yakale); choncho asandifulumizitse (kutsitsa chilango nthawi yake isanafike)

    [60] “Kuonongeka kuli pa amene atsutsa za tsiku lawo limene alonjezedwa

    Phiri

    Surah 52

    [1] “Ndikulumbilira phiri la Turi (ku Sinai pamene Mûsa adalankhulana ndi Allah)

    [2] “Ndi buku lolembedwa

    [3] “M’mipukutu yazikopa zotambasuka (zosavuta kuwerenga)

    [4] “Ndi nyumba yopitako kawirikawiri (pochitamo mapemphero)

    [5] “Ndi thambo limene latukulidwa (popanda mzati)

    [6] “Ndi nyanja yodzadza ndi madzi

    [7] “Ndithu chilango cha Mbuye wako (chimene wawalonjeza nacho osakhulupirira) chiwapeza (popanda chipeneko)

    [8] “Palibe wochichotsa (pa iwo)

    [9] “Pa tsikulo thambo lidzagwedezeka; kugwedezeka kwamphamvu

    [10] “Ndipo mapiri adzayenda mwamphavu (kuchoka m’malo mwake)

    [11] “Kuonongeka koopsa pa tsiku limenelo kuzakhala pa otsutsa choonadi

    [12] “Iwo amene akungosewera mzinthu zopanda pake

    [13] “Tsiku limene adzakankhidwira mwamphamvu ku Jahannam (ku Moto Woopsa)

    [14] “(Kudzanenedwa kwa iwo): “Uwu ndi Moto uja umene mudali kuutsutsa (pa dziko lapansi)

    [15] “Kodi awa ndi matsenga kapena inu simukuona

    [16] “Lowanimo, (mulawe kupsereza kwake) pirirani (ndi mavuto ake) kapena musapirire, ndichimodzimodzi kwa inu. Ndithu mulipidwa pazimene munkachita.”

    [17] “Ndithu oopa Allah adzakhala m’Minda yamtendere ndi chisangalalo chachikulu

    [18] “Uku akukondwelera pazimene wawapatsa Mbuye wawo ndipo Mbuye wawo azawatchinjiriza ku chilango cha Jahena

    [19] “(Kudzanenedwa kwa iwo): “Idyani (chakudya chamtendere); ndipo imwani mosangalala kukhala malipiro pazimene munkachita (pa dziko lapansi).”

    [20] “Uku atakhala moyadzamira pa makama ondandika bwino ndi kuyalidwa bwino; ndipo tidzawakwatitsa akazi ophanuka maso mokongola

    [21] “Ndipo amene akhulupirira ndipo ana awo nkuwatsatira pa chikhulupiliro tidzawakumanitsa iwo ndi ana awowo ndipo sitikawachepetsera kalikonse m’mphoto za ntchito zawo; munthu aliyense adzakoledwa ndi zochita zake

    [22] “Ndipo tidzawaonjezera zipatso ndi nyama imene adzakhala akuilakalaka

    [23] “Azikalandirana m’menemo (mwachikondi wina ndi mnzake) chikho chodzaza ndi zakumwa; sipakakhala kwa iwo zolankhula zachabe ngakhale zochita zamachimo

    [24] “Ndipo azikawazungulira anyamata owatumikira onga ngale yosungidwa m’chigoba chake (kukongola kwawo)

    [25] “Azidzatembenukirana wina ndi mnzake uku akufunsana (za kukula kwa mtendere umene adzakhala nawo ndi kuti adaupeza chotani)

    [26] “Adzanena: “Ife tidali oopa chilango cha Allah pakati pa maanja athu (tisadalandire mtenderewu)

    [27] “Ndipo Allah watidalitsa ndipo watitchinjiriza ku chilango cha Moto

    [28] “Ndithu ife timampembedza (kalero pa dziko lapansi) ndithu Iye Yekha Ngwabwino, Ngwachifundo.”

    [29] “Choncho kumbutsa, iwe suli mlosi kapena wamisala pamtendere wa Mbuye wako

    [30] “Kapena akunena kuti ndiwe mlakatuli, tikumuyembekezera imfa impeze

    [31] “Nena: “Yembekezerani! Ndithu ine ndili nanu mwa mmodzi woyembekezera.”

    [32] “Kapena nzeru zawo ndizo zikuwauza izi kapena iwo ndi anthu opyola malire

    [33] “Kodi akunena kuti: “Wadzipekera (Mtumiki {s.a.w} Qur’an)?” Iyayi, koma iwo sakukhulupirira

    [34] “Tero abwere ndi nkhani yofanana ndi iyo (Qur’an) ngati ali owona m’kuyankhula kwawo (koti Mtumiki{s.a.w} wapeka Qur’an

    [35] “Kapena adalengedwa popanda Mlengi kapena iwo adadzilenga okha (nchifukwa sakuvomereza za Mlengi Wopembedzedwayo)

    [36] “Kapena ndiwo adalenga thambo ndi nthaka? Koma satsimikiza (zoyenera kumchitira Mlengi)

    [37] “Kapena nkhokwe (za zabwino) za Mbuye wako zili ndi iwo (kotero kuti akuzigwiritsa ntchito mmene angafunire?) Kapena iwo ngopambana

    [38] “Nanga kapena ali nawo makwelero (amene akukwelera kumwamba) kotero kuti akumvetsera zimene Allah akulamula? Choncho, omvetsera awo abwere nawo umboni owonekera (osonyeza kuona kwawo pa zimene akunenazi)

    [39] “Kapena Iye (Allah) ndiye ali ndi ana akazi ndipo inu muli ndi ana amuna

    [40] “Kapena ukuwapempha malipiro alionse (pofikitsa uthenga); kotero kuti iwo akulemedwa ndi kulipira (uthengawu)

    [41] “Kapena iwo amadziwa zamseri kotero kuti iwo akumalemba (zimene afuna)

    [42] “Kapena akufuna kukuchitira chiwembu (ndikuononga uthenga wako?) Koma amene sadakhulupirire ndiwo omwe chiwabwelere chiwembu (chawo)

    [43] “Kodi ali naye wompembedza, osati Allah (amene angawateteze ku chilango cha Allah)? Allah wapatukana ndi zimene akumuphatikiza nazo

    [44] “Koma akaona gawo lathambo likugwa (kuti liwalange) akunena (mwamakani ndi kunyada): “Uwu ndi mtambo umene wasonkhanitsa madzi a mvula.”

    [45] “Choncho asiye; (usalabadire za iwo) mpaka pomwe adzakumana ndi tsiku lawo limene adzaonongedwa

    [46] “Tsiku lomwe chiwembu chawo sichidzawathandiza chilichonse; ndipo iwo sadzapulumutsidwa

    [47] “Ndipo ndithu amene achita zosalungama ali nacho chilango china chosakhala chimenecho (chisanawapeze chilango cha ku Âkhira)! Koma ambiri a iwo sadziwa (zimenezi)

    [48] “Ndipo pirira ndi lamulo la Mbuye wako ndithu iwe ndiwe wosungidwa ndi kuyang’aniridwa ndi Ife; ndipo lemekeza ndi kumuyamika Mbuye ako pamene ukuimilira (kupemphera)

    [49] “Ndipo m’gawo la usiku mlemekeze Iye ndi nthawi yolowa nyenyezi

    Nyenyezi

    Surah 53

    [1] “Ndikulumbira nyenyezi pamene zikulowa

    [2] “Sadasokere m’bale wanu (Mtumiki panjira ya choonadi) ndipo sadakhulupirire zonama

    [3] “Ndipo sayankhula zofuna za mtima wake

    [4] “Iyoyi (Qur’an imene akuinena), sichina, koma ndichivumbulutso chovumbulutsidwa

    [5] “Adamphunzitsa (chivumbulutsochi) (Jibril) wanyonga zambiri

    [6] “Wanzeru zakuya; ndipo adakhazikika (m’maonekedwe ake)

    [7] “Ali m’chizimezime kumwamba

    [8] “Kenako (Jibril) adamuyandikira (Mtumiki {s.a.w}) ndikuonjezera kumuyandikira

    [9] “(Kumuyandikira kwake) kudali ngati (mpata wa) nsonga ziwiri za uta, kapena kuyandikira kuposa apo

    [10] “(Choncho Jibril) adavumbulutsira kapolo wake (wa Allah) zimene adazivumbulutsa

    [11] “Sudaname mtima (wa Mtumiki) pazimene adaziona

    [12] “Kodi mukutsutsana naye (Mthenga wa Allah) pazimene adaziona

    [13] “Ndipo ndithu adamuona (Jibril) m’kuona kachiwiri mkaonekedwe kake

    [14] “Pa ‘Sidratil Muntaha’ (mtengo wamasawu pothera zinthu zonse)

    [15] “Pafupi pake pali Janatu Ma’awa, (munda wokhalamo)

    [16] “Pomwe chophimba chidaphimba msawuwo

    [17] “Maso ake sadaphonye kapena kupyola malire (oikidwa)

    [18] “Ndithu (Mneneri Muhammad {s.a.w}) adaona zina mwa zizindikiro zikuluzikulu za Mbuye wake (zosonyeza mphamvu Zake)

    [19] “Kodi mwamuona Laat ndi Uzza

    [20] “Ndi Manata; (fano lanu) lina lachitatu, (kuti iwowa ndi milungu)

    [21] “Kodi mwadzisankhira ana aamuna (kukhala anu), ndi aakazi nkukhala a Iye (Allah)

    [22] “Choncho kugawa kumeneko nkopanda chilungamo (pompatsa Allah zimene mumazida)

    [23] “Sali (mafanowo) chilichonse koma ndi maina basi omwe mudawatcha inu ndi makolo anu, (molingana ndi zilakolako zanu zachabe); Allah sadatsitse umboni pazimenezo (wotsimikiza pamawu anuwo). Sakutsatira koma zoganizira basi ndi zimene ikufuna mitima (yawo yopotoka). Ndithu chidawadzera chiongoko kuchokera kwa Mbuye wawo (chomwe m’kati mwake mudali kuongoka kwawo akadachitsatira)

    [24] “Kodi munthu akuganiza kuti adzapeza chilichonse chimene akuchilakalaka

    [25] “Moyo wa tsiku lachimaliziro ndi wadziko lapansi ngwa Allah Yekha

    [26] “Ndipo kuli angelo ambiri kumwamba omwe kuchondelera kwawo sikungathandize china chilichonse pokhapokha Allah ataloleza kwa amene wamfuna ndi kumuyanja

    [27] “Ndithu amene sakhulupirira za (Moyo wa) tsiku lachimaliziro, amawatcha angelo kuti ndiakazi

    [28] “Ndipo alibe kudziwa kulikonse pa zimenezo sakutsata china koma maganizo. Ndipo ndithu kuganizira sikuthandiza chilichonse pofuna kupeza choonadi

    [29] “Choncho apewe (osakhulupirirawa) amene anyozera chikumbutso Chathu (Qur’an); ndipo palibe chimene akufuna koma moyo wa padziko lapansi basi

    [30] “Zimenezo ndiwo mapeto a kudziwa kwawo. Ndithu Mbuye wako Ngodziwa kwambiri za amene akusokera njira Yake ndiponso akudziwa bwino za yemwe wawongoka

    [31] “Ndipo zonse za kumwamba ndi zadziko lapansi nza Allah Yekha, (pozilenga ndi kuziyang’anira), kuti adzawalipire amene adaipitsa pa zimene adachita ndi kutinso adzawalipire zabwino amene adachita zabwino

    [32] “Amene akuwapewa machimo akuluakulu ndi zadama, kupatula timachimo tating’onoting’ono (timene Allah amatikhululuka); ndithu Mbuye wako ndiwokhululuka kwakukulu. Iye akudziwa chikhalidwe chanu kuyambira pomwe adakulengani kuchokera m’nthaka ndi pamene inu mudali makanda m’mimba mwa amayi anu (mosinthasintha; mosiyanasiyana). Choncho musadzitame nokha kuyera mtima; Iye Ngodziwa kwambiri za yemwe akumuopa (Allah)

    [33] “Kodi wamuona yemwe wadzipatula (pakusiya kutsatira choonadi)

    [34] “Ndipo wapereka (chuma) chochepa nasiyanso kuperekako

    [35] “Kodi akudziwa zamseri, kotero kuti akuziwona (zomwe wadza nazo (Mtumiki {s.a.w) kuti sizoona

    [36] “Kapena sadauzidwe zomwe zidali m’mabuku a Mûsa

    [37] “Ndi Ibrahim amene adakwaniritsa (lonjezo la Allah)

    [38] “Kuti mzimu wamachimo sungasenze machimo a mzimu wina

    [39] “Ndi kutinso munthu sakalipidwa koma zimene adachita

    [40] “Ndipo ndithu ntchito zake zidzaonekera

    [41] “Kenako (munthu) adzalipidwa malipiro okwanira (pa ntchito zake zimene amachita)

    [42] “Ndipo ndithu kwa Mbuye wako yekha ndiwo malekezero (a chilichonse)

    [43] “Ndithu Iye ndiAmene amapereka chisangalalo ndi zoliritsa

    [44] “Ndipo Iye yekha ndi Amene amapereka imfa ndi moyo

    [45] “Ndipo Iye ndiAmene adalenga mitundu iwiri: chachimuna ndi chachikazi, (anthu ndi zamoyo zina)

    [46] “Kuchokera m’mbewu ya moyo pamene imafwamphukira (m’chiberekero)

    [47] “Ndipo ndithu ndi udindo Wake kuukitsa kwina (pambuyo pa imfa)

    [48] “Ndipo Iye ndiAmene amapatsa chokwanira ndipo ndi amene amapatsa chosunga

    [49] “Ndipo ndithu Iye ndi Mbuye wa nyenyezi yotchedwa Shiira

    [50] “Ndipo Iye ndi amene adaononga Âdi oyamba; (anthu a Mneneri Hûd)

    [51] “Ndi Samudu; (anthu a Mneneri Swaleh;) choncho sadasiye (ndi mmodzi yemwe wa iwo)

    [52] “Ndipo (adawaononganso) anthu a Nuh, kale (asadaononge Âdi ndi Samudu). Ndithu iwo adali osalungama ndi olumpha malire kwambiri (kuposa Âdi ndi Samudu)

    [53] “Ndi midzi yotembenuzidwa kumwamba kukhala pansi, pansi kukhala kumwamba, (ya anthu a Luti) adaigwetsa

    [54] “Tero chidaivindikira (midziyo) chomwe chidaivindikira (chilango)

    [55] “Kodi ndimtendere uti (mumtendere) wa Mbuye wako umene ukuukaikira

    [56] “Uyu (Mtumiki) ndimchenjezi mwa achenjezi oyamba (amene adachenjezedwa nawo anthu a mibadwo yakale)

    [57] “Chayandikira choyandikira (Qiyâma)

    [58] “Palibe amene angachionetse koma Allah Yekha

    [59] “Kodi mukuidabwa nkhaniyi (ya Qur’an moikana)

    [60] “Mungoseka (mwachipongwe) ndipo simukulira (pamene mukuimva monga momwe akuchitira okhulupirira)

    [61] “Ndipo mukunyozera

    [62] “Mlambireni ndi kumpembedza Allah (amene wavumbulutsa Qur’an kuti ikhale chiongoko cha anthu)

    Mwezi

    Surah 54

    [1] “Nthawi ya chimaliziro (Qiyâma) yayandikira ndipo mwezi wagawikana

    [2] “Koma akaona chozizwitsa akunyoza ndi kunena kuti: “Awa ndi matsenga womkeramkera patsogolo.”

    [3] “Ndipo adatsutsa (choonadi) ndi kutsatira zilakolako (zawo zoipa) koma chinthu chilichonse (cha Allah) nchokhazikika

    [4] “Ndipo ndithu zidawafika nkhani zomwe zili zokwanira kuwaopseza

    [5] “Nzeru zokwana koma machenjezo (kwa iwo) sanawathandize

    [6] “Choncho, apewe (iwe Mtumiki) osakhulupirira, (yembekezani) tsiku loitana woitana (wa Allah) ku chinthu chovuta kwambiri, (chodedwa ndi mitima)

    [7] “Maso awo ali zyoli chifukwa chakuopsa; adzatuluka m’manda uku ali ngati dzombe lobalalika (chifukwa cha kuchuluka)

    [8] “Akuthamangira kwa woitana (uku atatukula mitu yawo, osatha kucheukira kwina). Adzanena osakhulupirira (tsiku lachiweruziro): “Ili nditsiku lovuta kwambiri.”

    [9] “Patsogolo pawo (Aquraishi) anthu a Nuh nawo adatsutsa, adamtsutsa kapolo Wathu nanena kuti: “Uyu ngwamisala!” Ndipo adaopsezedwa (ndi kuzunzidwa ndi mazunzo osiyanasiyana)

    [10] “(Nuh) adaitana Mbuye wake (nati): “Ine ndagonjetsedwa (ndi anthu anga); choncho ndipulumutseni (kwa iwo).”

    [11] “Tero tidatsekula makomo akumwamba ndi madzi otsika mopitiriza, mwamphamvu

    [12] “Ndipo tidaing’amba nthaka kukhala ndi akasupe (ofwamphuka madzi mwamphamvu). Choncho adakumana madzi (akumwamba ndi am’nthaka kuti awaononge) pamuyeso wopimidwa ndi kulamulidwa (ndi Allah)

    [13] “Ndipo tidamnyamula Nuh pa chombo chamatabwa chokhomedwa ndi misomali (yamitengo)

    [14] “Chinkayandama pamadzi ndi kuyang’aniridwa ndi Ife. Iyi ndi mphoto ya (Nuh) yemwe adakanidwa ndi anthu ake

    [15] “Ndipo ndithu tidachisiya (chigumula) kukhala phunziro (pakuonongeka kwa osakhulupirira ndi kupulumuka kwa okhulupirira). Kodi alipo wolikumbukira (ndi kupeza nalo malango abwino)

    [16] “Kodi chidali bwanji chilango Changa ndi machenjezo Anga (kwa onyoza)

    [17] “Ndipo ndithu taifewetsa Qur’an kuti ikhale chikumbutso. Kodi alipo woikumbukira (ndi kupeza nayo malangizo abwino)

    [18] “Âdi adamtsutsa (mneneri wawo Hud), kodi chidali bwanji chilango Changa ndi machenjezo Anga (kwa onyoza)

    [19] “Ndithu Ife tidawatumizira mphepo yozizira, yaphokoso, m’tsiku latsoka lopitilira

    [20] “Idawazula anthu (kuchoka m’malo mwawo ndi kuwaponya panthaka ali akufa) ngati matsinde a mitengo yakanjedza ozulidwa m’malo mwake

    [21] “Kodi chidali bwanji chilango Changa ndi machenjezo Anga (kwa onyoza)

    [22] “Ndipo ndithu taifewetsa Qur’an kuti ikhale chikumbutso. Kodi alipo woikumbukira (ndi kupeza nayo malangizo abwino)

    [23] “Asamudu adatsutsa machenjezo

    [24] “Ndipo adati: “Kodi titsatire munthu mmodzi wochokera mwa ife? Ndithu ife ngati titamtsatira ndiye kuti tili nkusokera ndiponso misala.”

    [25] “Kodi am’vumbulutsira iye chikumbutso pakati pathu, (pomwe tili nawo oposa iye pa ulemelero)? Koma iye ndiwabodza ndi wodzitukumu.”

    [26] “Mawa lino adzadziwa (tsiku lakuwatsikira chilango,) kuti ndiyani wabodza wodzitukumula (iwo kapena Swaleh)

    [27] “(Tidamuuza mneneriyo kuti) ndithu Ife titumiza ngamira yaikazi kuti ikhale mayeso kwa iwo. Choncho adikire, ndipo pirira

    [28] “Ndipo auze kuti madzi agawidwa pakati pawo (ndi ngamira). Aliyense ali ndi tsiku lopita kukatunga

    [29] “Koma adaitana mnzawo (wa mphulupulu). Choncho adakonzeka kupha ngamirayo ndipo adaipha

    [30] “Kodi chidali bwanji chilango Changa ndi machenjezo Anga (kwa anthu otsutsa)

    [31] “Ndithu tidawatumizira nkuwe umodzi choncho adakhala ngati udzu ndi mitengo youma yaomanga khola

    [32] “Ndipo ndithu taifewetsa Qur’an kuti ikhale chikumbutso. Kodi alipo woikumbukira (ndi kupeza nayo malangizo abwino)

    [33] “Anthu a Luti adatsutsa machenjezo (a mneneri wawo)

    [34] “Ndithu Ife tidawatumizira chimphepo champhamvu choulutsa miyala (ndi kuwagenda), kupatula akubanja la Luti; tidawapulumutsa (ku chilangocho) m’bandakucha

    [35] “(Choncho kupulumukako kudali) chisomo chochokera kwa Ife (pa iwo). Momwemo ndimo timamlipirira wothokoza

    [36] “Ndipo ndithu (Luti) adawachenjeza anthu ake za kulanga Kwathu koopsa. Koma adakaikira machenjezo (ake ndi kumtsutsa)

    [37] “Ndipo ndithu adafuna kwa iye kuti awapatse alendo ake (kuti achite nawo zauve), koma tidafafaniza maso awo (kuti ikhale mphoto pa zimene adafunazo). (Ndipo tidawauza): “Choncho lawani chilango Changa ndi machenjezo Anga.”

    [38] “Ndipo ndithu chidawadzera mwadzidzidzi chilango chokhazikika, nthawi yam’mamawa

    [39] “Choncho (kudanenedwa kwa iwo) “Lawani chilango Changa ndi machenjezo Anga.”

    [40] “Ndipo ndithu taifewetsa Qur’an (kuti ikhale chikumbutso). Kodi alipo woikumbukira (ndi kupeza nayo malangizo abwino)

    [41] “Ndipo ndithu machenjezo (ondondozana) adawadzera anthu a Farawo (ndi iye mwini)

    [42] “Adatsutsa zozizwitsa Zathu zonse (zimene zidadza kupyolera m’manja mwa aneneri Athu). Choncho tidawalanga, kulanga kwa Wamphamvu (Wosapambanidwa), Wokhoza

    [43] “Kodi osakhulupirira anuwa ndi abwino kuposa iwo (kotero kuti sadzaonongedwa)? Kapena zalembedwa m’mabuku kuti inu mdzasiyidwa (sadzakuonongani monga momwe adawaonongera akale)

    [44] “Kapena akunena kuti: “Ife ndiochuluka titha kudziteteza (palibe angatipambane)?”

    [45] “(Auze): Gululo ligonjetsedwa ndipo athawa ndi kutembenuza misana

    [46] “Koma lonjezo la chilango chawo ndi tsiku la chiweruziro, ndipo tsiku la chiweruziro ndi latsoka lalikulu, lowawa kwabasi (kwa osakhulupirira)

    [47] “Ndithu oipa (mwa awa ndi aja) ali nkusokera ndi misala

    [48] “Tsiku limene adzakokedwera ku Moto ndi nkhope zawo, (kudzanenedwa kwa iwo:) “Lawani zowawa za Jahena (ndi kutentha kwake)

    [49] “Ndithu Ife tachilenga chinthu chilichonse ndi muyeso (kulingana ndi zolinga)

    [50] “Ndipo silili lamulo Lathu (pa chinthu tikachifuna) koma liwu limodzi, (timangoti kwa chinthucho: “Chitika.” Ndipo chimachitika mwachangu) ngati kuphethira kwa diso

    [51] “Ndipo ndithu tidawaononga anzanu (onga inu osakhulupirira): Kodi alipo wokumbuka

    [52] “Ndipo chinthu chilichonse adachichita iwowo (pa dziko lapansi) chili mkaundula

    [53] “Ndipo ntchito iliyonse, yaing’ono kapena yaikulu, idalembedwa; (palibe chimene chingamsowe)

    [54] “Ndithu oopa Allah adzakhala m’Minda ya ulemelero waukulu ndi Mitsinje (yosiyanasiyana)

    [55] “Pokhala pabwino pachoonadi, (popanda mawu achabe ndi machimo), kwa Mfumu yokhoza chilichonse

    Wachifundo chambiri

    Surah 55

    [1] “(Allah) Wachifundo chochuluka

    [2] “Waphunzitsa Qur’an

    [3] “Adalenga munthu

    [4] “Adamphunzitsa kuyankhula

    [5] “Dzuwa ndi mwezi zikuyenda mwachiwerengero

    [6] “Zomera zopanda tsinde ndi mitengo, zikulambira (Allah pachilichonse chimene wafuna mwa izo)

    [7] “Ndipo thambo adalitukula kumwamba ndipo adakhazikitsa sikelo (ya chilungamo)

    [8] “Kuti musapyole malire ndi kuchita chinyengo poyesa

    [9] “Choncho yesani sikelo mwachilungamo ndipo musapungule muyeso

    [10] “Ndipo nthaka adaiyala (ndi kuikonza) kuti ikhale ya zolengedwa

    [11] “M’menemo muli zipatso ndi mitengo ya kanjedza yokhala ndi mapava (a zipatso)

    [12] “Ndi mbewu zamakoko (kuti chikhale chakudya cha inu ndi ziweto zanu), ndipo mulinso m’menemo mmera wafungo labwino

    [13] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [14] “Adalenga munthu kuchokera ku dongo lolira monga ziwiya zadongo

    [15] “Ndipo adalenga ziwanda kuchokera ku malawi a moto (wopanda utsi)

    [16] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [17] “Mbuye wa kuvuma kuwiri ndiponso Mbuye wa kuzambwe kuwiri

    [18] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [19] “Adaika nyanja ziwiri zokumana (yamadzi amchere, ndi yamadzi ozizira)

    [20] “Pakati pake pali chitsekerezo, sizilowana

    [21] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [22] “M’menemo mumatuluka ngale zing’onozing’ono ndi ngale zikuluzikulu

    [23] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [24] “Ndipo (Iye) ali nazo zombo (zimene zapangidwa ndi manja anu), zoyenda panyanja, zazikuluzikulu ngati mapiri

    [25] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [26] “Zonse zili pamenepo (pa dziko) nzakutha

    [27] “Ndipo idzatsala nkhope ya Mbuye wako yaulemelero ndi mtendere

    [28] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [29] “(Onse) akumwamba ndi pansi akupempha Iye (zofuna zawo)! Tsiku lililonse Iye ali ndi zochita (monga kupatsa uyu ulemelero, ndi kutsitsa uyu)

    [30] “(Inu zolengedwa zamitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [31] “Posachedwapa (patsiku la chiweruziro), tidzaikapo mtima pa chiwerengero chanu (cha zochita zanu) inu anthu ndi ziwanda

    [32] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [33] “E inu ziwanda ndi anthu! Ngati mungathe kutuluka m’mphepete mwa thambo ndi nthaka (pothawa Allah), tulukani! Simungathe kutuluka pokhapokha ndi mphamvu. (Koma inu simungathe kutero)

    [34] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [35] “Mudzathiridwa malawi a moto ndi mtovu wa moto wosungunuka ndipo simungathe kupulumuka (ku chilango chimenechi)

    [36] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [37] “(Kumbuka) pamene thambo lidzang’ambika ndi kukhala lofiira ngati chikopa chofiira (kapena ngati mafuta oyaka)

    [38] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [39] “Ndipo patsikulo munthu ndi chiwanda, sadzafunsidwa (aliyense) za tchimo lake

    [40] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [41] “Adzadziwika oipa (pakati pa anthu ndi ziwanda) ndi zizindikiro zawo (zowazindikiritsa). Ndipo adzagwidwa maliombo awo ndi mapazi awo (ndi kuponyedwa ku Jahena)

    [42] “((Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [43] “(Kudzanenedwa mowadandaulitsa): Iyi ndi Jahannam yomwe adali kuitsutsa oipa

    [44] “Adzakhala akuyenda pakati pa moto ndi pakati pa madzi owira, otentha kwambiri

    [45] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [46] “Koma amene waopa kuti adzaimitsidwa kwa Mbuye wake (pa nthawi ya chiweruziro), adzalandira minda iwiri (yaikulu yamtendere)

    [47] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [48] “(Minda ya mitengo) yanthambi zofwanthamuka

    [49] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [50] “M’menemo muli akasupe awiri, omwe akuyenda

    [51] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [52] “M’menemo muli zipatso za mtundu uliwonse, mitundu iwiri iwiri

    [53] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [54] “Atatsamira pa zoyala, mkati mwake mosokelera veleveti wochindikala; ndipo zipatso zam’minda iwiriyi nzapafupi (kuzithyola)

    [55] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [56] “M’mindamo muli akazi oyang’ana amuna awo okha basi, (mawuthu) omwe sadakhalepo malo amodzi ndi munthu kapena chiwanda asadakumane ndi iwo

    [57] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [58] “Kukongola kwake (akaziwo) kuli ngati ngale zikuluzikulu ndi zing’onozing’ono

    [59] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [60] “Malipiro a ntchito zabwino ndikulandira zabwino basi

    [61] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [62] “Ndipo kuonjezera paminda iwiri (ija) palinso minda ina iwiri

    [63] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [64] “Yobiriwira, kwambiri

    [65] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [66] “M’menemo muli akasupe awiri ofwamphuka madzi mwaphamvu

    [67] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [68] “Mmenemo muli zipatso, mitengo yakanjedza ndi yamikangaza

    [69] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [70] “M’menemo muli akazi amakhalidwe abwino, owala nkhope

    [71] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [72] “Okongola maso, achikhalire m’mahema (m’matenti) awo

    [73] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [74] “Amene sadakhalepo malo amodzi ndi munthu kapena chiwanda asadakumane ndi iwo

    [75] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [76] “Uku atatsamira misamiro yawofuwofu yokutidwa ndi zobiriwira; ndi zoyala zokongola, zakapangidwe kabwino

    [77] “(Inu zolengedwa za mitundu iwiri, anthu ndi ziwanda), kodi ndi mtendere uti wa Mbuye wanu umene mukuukana (kuti si Wake)

    [78] “Latukuka ndi kudalitsika dzina la Mbuye wako Mwini ulemelero ndi ufulu

    Zosapeŵeka

    Surah 56

    [1] “Chikadzachitika chochitikacho (Qiyâma)

    [2] “Palibe wotsutsa za kuchitika kwake

    [3] “Chidzatsitsa (oipa) ndi kutukula (abwino)

    [4] “Nthaka ikadzagwedezeka kwamphamvu

    [5] “Ndipo mapiri akadzaperedwaperedwa

    [6] “Nkukhala fumbi longouluka

    [7] “Choncho, inu mudzakhala m’magulu atatu (kulingana ndi zochita zanu)

    [8] “Anthu akumanja (abwino;) taonani kukula kwa ulemelero wa anthu akumanja

    [9] “Ndi anthu akumanzere (oipa;) taonani kuipa khalidwe la anthu akumanzere

    [10] “Ndipo otsogola (pochita zabwino pa dziko) adzakhalanso otsogola (polandira ulemu tsiku lachimaliziro)

    [11] “Iwowo ndioyandikitsidwa (kwa Allah)

    [12] “M’minda yamtendere

    [13] “(Iwowo oyandikitsidwawo), gulu lalikulu lochokera kumibadwo yakale

    [14] “Ndipo ochepa ochokera ku mbadwo wotsirizira

    [15] “Uku ali m’makama (m’mabedi) olukidwa ndi zingwe zagolide

    [16] “Atatsamira m’makamawo uku akuyang’anizana (mwachikondi)

    [17] “Anyamata osasintha adzakhala akuwazungulira iwo (ndi kuwatumikira)

    [18] “Uku atatenga matambula ndi maketulo (odzaza ndi zakumwa za ku Jannah), ndi zipanda zodzaza ndi zakumwa zochokera mu akasupe oyenda

    [19] “(Zakumwa zake) zosapweteketsa mutu ndiponso zosaledzeretsa

    [20] “Ndi zipatso (zamitundumitundu) zimene azikazisankha

    [21] “Ndi nyama yambalame imene mitima yawo izikafuna

    [22] “Ndi akazi ophanuka maso mokongola

    [23] “(Kukongola kwawo) ndiye ngati ngale zosungidwa bwino mzigoba zake

    [24] “Kukhala mphoto chifukwa cha zimene amachita (zabwino padziko lapansi)

    [25] “M’menemo sakamva mawu achabe ngakhale (mawu a) machimo

    [26] “Koma mawu oti: “Mtendere! Mtendere!”

    [27] “Anthu akudzanja lamanja. Taonani kukula malipiro a anthu akudzanja lamanja

    [28] “(Adzakhala m’mithunzi ya) mitengo ya masawu yopanda minga

    [29] “Ndi mitengo ya nthochi yobereka kwambiri

    [30] “Ndi m’mithunzi yotambasuka kwambiri, yosachoka

    [31] “Ndi madzi oyenda mosalekeza

    [32] “Ndi zipatso zambiri

    [33] “Zopezeka mnyengo zonse, ndiponso zosaletsedwa (kwa amene akuzifuna)

    [34] “Ndi zoyala zapamwamba (zawofuwofu)

    [35] “Ndithu tidzawalenga (akazi okhulupirira) m’kalengedwe kapamwamba

    [36] “Tidzawapanga kukhala anamwali

    [37] “Okondedwa ndi amuna awo; ofanana misinkhu

    [38] “A anthu akudzanja la manja

    [39] “Gulu lalikulu lochokera ku m’badwo woyamba

    [40] “Ndiponso gulu lalikulu lochokera ku mibadwo yotsiriza

    [41] “Anthu akudzanja lakumanzere. Taonani chilango choopsa kwa anthu akudzanja lakumanzere

    [42] “Adzakhala mu mvuchi wamoto ndi m’madzi owira

    [43] “Ndi mumthunzi wa utsi wakuda

    [44] “Siwoziziritsa ndiponso siwosangalatsa

    [45] “Ndithu iwo amakhala kalelo mosangalala (samalabadira kumvera Allah)

    [46] “Ndipo amapitiriza kuchita machimo aakulu (polinga kuti palibe kuuka ku imfa)

    [47] “Ndipo amanena (motsutsa); “Kodi tikadzafa nkusanduka fumbi ndi mafupa ofumbwa, tidzaukitsidwanso?”

    [48] ““Kodi ndi makolo athu akale (adzaukitsidwanso!)”

    [49] “Nena kwa iwo (poyankha kutsutsa kwawo). Ndithudi, amibadwo yoyamba ndi mibadwo yomaliza (omwe inu muli m’gulu lawo)

    [50] “Adzasonkhanitsidwa m’nthawi ya tsiku lomwe lakhazikitsidwa

    [51] “Kenako inu osokera (njira yachilungamo), otsutsa (za kuuka)

    [52] “Mudzadya (ku Jahannam) mtengo wa Zakkum, (mtengo wowawa wopezeka mu Jahannam)

    [53] “Mudzakhutitsa mimba zanu ndi umenewu (chifukwa cha njala yadzaoneni)

    [54] “(Mkhuto wa mtengowo) adzamwera madzi owira

    [55] “Adzamwa monga mmene imamwera ngamira yodwala matenda aludzu

    [56] “Ili ndi phwando lawo tsiku lamalipiro

    [57] “Ife tidakulengani kodi nchifukwa ninji simukukhulupirira

    [58] “Tandiuzani za madzi (ambewu ya munthu) amene mumawathira m’chiberekero

    [59] “Kodi inu ndiamene mumawalenga (madziwo ndi kumayang’anira mkusinthasintha kwake kuti akhale cholengedwa) kapena Ife ndiamene timawalenga

    [60] “Ife tidalamula imfa pakati panu ndipo Ife sitili wolephera

    [61] “Kubweretsa ena m’malo mwanu ndi kukulengani mwamaonekedwe ena omwe simumawadziwa

    [62] “Ndipo ndithu mukdziwa kalengedwe koyamba; nanga bwanji simukukumbukira

    [63] “Tandiuzani za zimene mukubzala

    [64] “Kodi ndinu amene mukuzimeretsa kapena ndife Amene tikuzimeretsa

    [65] “Tikadafuna tikadazitembenuza (mbewu zimenezo kukhala zouma isanakwane nthawi yake yozithyola) choncho mukadakhala mukudandaula

    [66] “(Uku mukunena:) “Ndithu ife tangotaya chuma chathu (padera);”

    [67] ““Koma ife tamanidwa (phindu la khama lathu).”

    [68] “Kodi mukuwaona madzi amene mukumwa

    [69] “Kodi ndinu amene mudawatsitsa ku mitambo kapena ndife Amene timawatsitsa

    [70] “Tikadafuna tikadawapanga kukhala amchere; nanga nchifukwa ninji simuthokoza

    [71] “Kodi mukuwuona moto umene mumaukoleza

    [72] “Kodi ndinu amene mudameretsa mitengo yake kapena Ndife tidaipanga

    [73] “Ife taupanga kuti ukhale chikumbutso (cha Moto watsiku lachimaliziro akauona), ndikuti ukhale chothandiza kwa anthu apaulendo (amene akuyenda m’chipululu)

    [74] “Choncho, pitiriza kulemekeza dzina la Mbuye wako Wamkulu

    [75] “Ndikulumbilira motsimikiza, mmene mumatsikira nyenyezi (pomwe zikulowa)

    [76] “Ndithu kulumbira uku, mukadakhala olingalira, nkwakukulu kwabasi (pazimene kukusonya)

    [77] “Ndithu iyi ndi Qur’an yolemekezeka (ndipo mkati mwake muli zithandizo zambiri)

    [78] “Idachokera mu buku lotetezedwa

    [79] “Salikhudza kupatula okhawo oyeretsedwa (angelo)

    [80] “Chivumbulutso chochokera kwa Mbuye wa zolengedwa zonse

    [81] “Kodi nkhani iyi (ya Qur’an) ndiyomwe inu mukuinyozera

    [82] “Kodi mwakuchita kukanira kukhala kuthokoza kwanu pa zimene wakupatsani

    [83] “Mmaona bwanji (mzimu wa mmodzi wa inu) ukafika kummero (panthawi ya imfa)

    [84] “Uku inu panthawi imeneyo mukuona zimenezo

    [85] “Pomwe Ife tili pafupi ndi iye kuposa inu, koma inu simuona

    [86] “Mukadakhala kuti simuzalipidwa (pa zomwe mukuchita)

    [87] “Bwenzi mukuubweza (mzimuwo) ngati mukunena zoona

    [88] “Ngati (amene yamfikira imfayo) adali mmodzi wa woyandikitsidwa (kwa Allah)

    [89] “Kobwerera kwake ndi kumpumulo ndi mtendere ndi kupatsidwa zonunkhira ndiponso Munda wamtendere

    [90] “Ndipo ngati adali mmodzi wa anthu akudzanja lamanja

    [91] “(Kudzanenedwa kwa iye:) “Mtendere ukhale pa iwe, amene udali m’gulu la anthu akudzanja lakumanja (anthu abwino).”

    [92] “Koma ngati adali mmodzi wa anthu otsutsa, osokera

    [93] “Phwando lamadzi owira (ndilake)

    [94] “Ndi kupsa m’moto wa Jahena

    [95] “Ndithu izi ndizoona, zotsimikizika

    [96] “Choncho lemekeza dzina la Mbuye wako Wamkulu

    Chitsulo

    Surah 57

    [1] “Chilichonse chakumwamba ndi chapansi chikulemekeza Allah (ndi kumuyeretsa kumakhalidwe opunguka) ndipo Iye ndi Mwini Mphamvu, Wanzeru zakuya

    [2] “Ufumu wakumwamba ndi pansi, Ngwake amapereka moyo ndi imfa. ndipo Iye Ngwamphamvu pa chilichonse

    [3] “Iye ndi Oyamba (adalipo chilichonse chisadayambe); Wamuyaya (zonse zikadzatha); Woonekera (mzisonyezo pa chinthu chilichonse), Wobisika mkati kwambiri (saonedwa ndi maso pamoyo uno), Iye Ngodziwa chilichonse (kunja ndi mkati mwake)

    [4] “Iye ndi Amene adalenga kumwamba ndi pansi (ndi zonse zammenemo) m’masiku asanu ndi limodzi kenako adakhazikika pa Arsh (Mpando Wake wachifumu monga momwe Iye adziwira polongosola ufumu Wake). Akudziwa chilichonse cholowa m’nthaka ndi chimene chikutuluka m’menemo; ndi chilichonse chimene chikutsika kuchokera kumwamba ndi chimene chikukwera kumeneko. Ndipo Iye ali nanu paliponse pamene muli. Ndithu Allah amaona chilichonse chimene mukuchita, (sichibisika chilichonse kwa Iye)

    [5] “Ufumu wakumwamba ndi pansi Ngwake ndipo kwa Allah nkobwerera zinthu (zonse)

    [6] “Usiku amawulowetsa mu usana, ndipo usana amawulowetsa mu usiku. (Choncho kumasiyana kutalika kwake); ndipo Iye Ngodziwa zobisika za m’zifuwa (ndi zoganiza za m’mitima)

    [7] “Khulupirirani Allah ndi Mthenga Wake, ndipo perekani (pa njira ya Allah m’chuma chimene Allah wakupatsani uchiyang’anira. Choncho mwa inu amene akhulupirira (mwa Allah ndi mthenga Wake) ndikupereka (zimene awapatsa) iwo ali ndi malipiro aakulu (kwa Allah)

    [8] “Kodi nchifukwa ninji simukhulupirira Allah pomwe Mtumiki akukuitanani kuti mukhulupirire Mbuye wanu (ndi kukulimbitsani pa zimenezo) chikhalirecho (Iye) adalandira lonjezo lanu, (muli mumsana wa tate wanu Adam kuti mdzakhulupirira,) ngati mulidi okhulupirira

    [9] “Iye ndi Amene akuvumbulutsa kwa kapolo Wake Ayah (ndime) zofotokoza mwatsatanetsatane kuti akutulutseni mum’dima (wa kusokera) ndi kukuikani ku chiongoko cha kuunika. Ndipo ndithu Allah Ngoleza kwa inu, Ngwachisoni

    [10] “Kodi ndichifukwa chiani simukupereka pa njira ya Allah (chuma chanu) pamene Allah Ndimwini wa zosiyidwa zonse za kumwamba ndi za m’dziko lapansi. Sali ofanana mwa inu amene adapereka chuma (panjira ya Allah) pamodzi ndi kumenya nkhondo usadagonjetsedwe (mzinda wa Makka), iwowo ndiomwe ali ndi ulemelero waukulu kuposa amene apereka chuma chawo ndi kumenya nkhondo pambuyo. Koma onsewo Allah wawalonjeza zabwino (ngakhale ali osiyana ulemelero wawo); ndipo Allah akudziwa zonse zimene muchita. (Choncho aliyense adzalipidwa molingana ndi zimene amachita)

    [11] “Kodi ndani (okhulupirira) amene angamkongoze Allah ngongole yabwino kuti amuchulukitsire malipiro ake? Ndipo iye adzalandira malipiro aulemu (pa tsiku la chiweruziro)

    [12] “Tsiku limene udzaona okhulupirira aamuna ndi aakazi dangalira lawo likuyenda patsogolo pawo ndi mbali ya kumanja kwao (uku angelo akunena kwa iwo): “Chisangalalo chanu lero ndi minda imene pansi pake pakuyenda mitsinje. Mukhala m’menemo nthawi yaitali! Kumeneku ndiko kupambana kwakukulu (kwa inu)

    [13] “Tsiku limene achinyengo aamuna ndi achinyengo aakazi adzauza okhulupirira (kuti:) “Tidikireni kuti tipeze kuunika kwanu!” Kudzanenedwa (mwachipongwe): “Bwererani pambuyo panu mukafune kuunika kumeneko!” Choncho padzaikidwa mpanda pakati pawo (okhulupirira ndi achinyengo) umene udzakhala ndi khomo, mkati mwake muli chifundo ndi mtendere; kunja kwake kuli mazunzo ndi chilango

    [14] “(Achinyengo) adzaitana okhulupirira ponena kuti: “Kodi sitidali nanu limodzi (pa dziko ndi kumatsagana nanu?” (Okhulupirira) adzati: “Inde! (Mudali nafe monga momwe mukunenera). Koma inu munadziononga nokha ndipo mumayembekezera (kuti okhulupirira awapeze mavuto ndi kuonongeka); mudakaikira (zinthu za chilengedwe chanu); choncho zikhulupiliro zanu zonama zidakunyengani pomwe mudali angwiro mpaka lamulo la Allah (imfa) lidakupezani, komanso adakunyengani onyenga (satana) za Allah

    [15] “Basi lero sililandiridwa dipo lochokera kwa inu (limene mungalipereke kuti mudzipulumutse ku chilango ngakhale likhale lamtengo wotani). Ndiponso sililandiridwa dipo lochokera kwa osakhulupirira (amene adalingana nanu n’kusakhulupirira kwawo Allah) malo anu nonsenu ndi ku Moto basi. Amenewa ndi malo okuyenerani. Kumeneko ndiko kobwerera koipa kwabasi

    [16] “Kodi siidakwane nthawi kwa okhulupirira kuti mitima yawo idzichepetse pokumbukira Allah ndi zomwe zidavumbulutsidwa za chowonadi (Qur’an yolemekezeka)? Ndi kuti asakhale monga omwe adapatsidwa buku kale (Ayuda ndi Akhrisitu) amene nthawi yawo yosiyana ndi aneneri awo idali yaitali. Choncho mitima yawo idauma ndipo ambiri a iwo adatuluka m’chilamulo (cha Allah)

    [17] “Dziwani kuti ndithu Allah amaukitsa nthaka itauma (poitsitsira mvula kuti mmera umere). Choncho takulongosolerani zisonyezo kuti inu mukhale ndi nzeru

    [18] “Ndithu amene akupereka sadaka amuna ndi akazi, ndi kumamkongoza Allah ngongole yabwino (Allah) adzawaonjezera malipiro pa zimenezi. Ndipo ali ndi malipiro aulemu

    [19] “Ndipo amene akhulupirira Allah ndi aneneri Ake, iwowo ndiwo owona (pa chikhulupiliro); ndi ofera pa njira ya Allah (onsewo) azapeza malipiro awo ndi kuwala kwawo kwa Mbuye wawo. Koma amene sadakhulupirire ndi kutsutsa zisonyezo zathu iwowo ndi eni a ku Jahena

    [20] “Dziwani kuti ndithu moyo wa pa dziko lapansi ndimasewera, chibwana, chokometsera chabe, chonyadiritsana pakati panu (pa ulemelero) ndi kuchulukitsa chuma ndi ana (pomwe zonsezo sizikhala nthawi yayitali;) fanizo lake lili ngati mvula yomwe mmera wake umakondweretsa alimi; kenako umafota, ndipo uuona uli wachikasu; kenako nkukhala odukaduka (oonongeka). Koma tsiku lachimaliziro kuli chilango cha ukali; ndi chikhululuko komanso chikondi chochokera kwa Allah. Moyo wa pa dziko lapansi suli kanthu, koma ndichisangalalo chonyenga basi

    [21] “Chitani changu (pa zinthu zokupatitsani) chikhululuko chochokera kwa Mbuye wanu ndi Munda wamtendere womwe mulifupi mwake muli ngati kutambasuka kwa kumwamba ndi pansi; wakonzedwera amene akhulupirira Allah ndi aneneri Ake; umenewo ndi ubwino wa Allah womwe akuupereka kwa amene wamfuna. Allah ndi Mwini ubwino waukulu

    [22] “Silipezeka tsoka lililonse panthaka (monga chilala) ngakhale pamatupi anu koma lidalembedwa kale m’buku (la Allah) tisadalilenge ndi kulipereka. Ndithu zimenezo kwa Allah nzofewa

    [23] “(Takudziwitsani zimenezi) kuti musadandaule ndi chimene chakudutsani, ndi kutinso musakondwere monyada ndi chimene wakupatsani. Allah sakonda aliyense wodzitama, wonyada

    [24] “Amene akuchita umbombo (ndi chuma chawo; ndipo osapereka pa njira ya Allah) ndi kumalamula anthu ena kuchita umbombo. Ndipo amene atembenuke (adzalandira chilango chachikulu), ndithu Allah Ngolemera, (sasaukira chilichonse kwa wina), Ngotamandidwa

    [25] “Ndithu tidatuma atumiki Athu pamodzi ndi zozizwitsa. Ndipo tidavumbulutsa pamodzi ndi iwo mabuku ndi muyeso wa choonadi kuti anthu achite chilungamo. Ndipo tidalenga chitsulo momwe muli mphamvu zambiri (pa nkhondo) ndiponso chithandizo kwa anthu (akakhala pa mtendere ndi kupindula nacho pochita zowathandiza pa moyo wawo). Ndi kuti Allah amuonetsere poyera, amene angachiteteze (chipembedzo Chake) ndi atumiki Ake (kupyolera m’chitsulocho) pomwe Iye sakumuona. Ndithu Allah Ngwamphamvu (pa chilichonse) Ngopambana

    [26] “Ndipo ndithu tidatuma Nuh ndi Ibrahim ndi kukhazikitsa uneneri m’mbumba yawo ndi mabuku (achiongoko). Ena mwa iwo adayenda pa njira yolungama, koma ambiri a iwo adapatuka pa njira yolungamayo

    [27] “Kenako tidatsatiza pambuyo pawo ndi atumiki Athu ndipo tidasatiza ndi Isa (Yesu) mwana wa Mariya, ndipo tidampatsa Injili ndipo tidaika kufatsa ndi chifundo m’mitima ya omwe adamtsatira. Koma kusakwatira, adakuyambitsa okha; sitidawalamule zimenezo koma (adayambitsa zimenezo) chifukwa chofuna chikondi cha Allah; koma sadazisunge moyenera. Choncho amene adakhulupirira pakati pawo tidawapatsa malipiro awo, koma ambiri a iwo ngopandukira malamulo

    [28] “E inu amene mwakhulupirira! Opani Allah, ndipo khulupirirani mthenga Wake, akupatsani zigawo ziwiri za chifundo Chake. Ndipo akupangirani kuunika koongoka nako (poyenda patsiku la chiweruziro.) Ndiponso akukhululukirani ndipo Allah Ngokhululuka mochuluka kwambiri, Ngwachisoni chosatha

    [29] “(Allah akupatsani zonsezi) kuti adziwe amene adapatsidwa buku (omwe sadamkhulupirire Mtumiki{s.a.w}) kuti iwo sangathe kudzisankhira okha chilichonse mu mtendere wa Allah. Ndipo ndithu ubwino wonse uli m’manja mwa Allah Yekha. Amapatsa amene wamfuna mwa akapolo Ake. Ndipo Allah ndi Mwini ubwino wochuluka

    Mkazi wopempha

    Surah 58

    [1] “۞ Ndithu Allah wamva mawu a (mkazi) amene akubwezeranabwezerana nawe (mawu) pa za mwamuna wake (amene adamsala); ndipo akusuma kwa Allah. Ndipo Allah akumva kukambirana kwanu; ndithu Allah Ngwakumva, Ngopenya (chilichonse)

    [2] “Amene akufanizira mwa inu (Asilamu) akazi awo (ndi amayi awo) iwo siamayi awo; amayi awo ndiamene adawabereka. Ndithu iwo akunena mawu oipa ndi onama. Koma ndithu Allah ali Wofafaniza (machimo) ndi Wokhululuka (kwa amene walapa)

    [3] “Ndipo amene akuwafanizira akazi awo (ndi amayi awo) kenako nkubweza zimene adanena, apereke ufulu kwa kapolo asanakhale malo amodzi (ndi mkaziyo). Amenewa ndi malamulo a Allah kwa inu (amene) mukuchenjezedwa nawo. Ndipo Allah akudziwa zimene mukuchita (zoonekera poyera ndi zosaonekera choncho sungani malamulo amene Allah wakhazikitsa pa inu)

    [4] “Ndipo amene sadapeze (kapolo) asale miyezi iwiri yondondozana asadakhalirane pamodzi (ndi mkaziyo), koma amene sadathe kusala adyetse masikini makumi asanu ndi limodzi . Izi (zalamulidwa) kuti mukhulupirire mwa Allah ndi Mthenga Wake. Amenewo ndiwo malire a Allah; (malamulo okhazikitsidwa ndi Allah choncho musawalumphe). Ndipo chilango chopweteka chili pa osakhulupirira

    [5] “Ndithu amene akutsutsana ndi Allah kudzanso Mthenga Wake, ayalutsidwa monga momwe adayalutsidwira amene adalipo patsogolo pawo; ndithu tavumbulutsa Ayah zolongosola, momveka (pa zololedwa ndi zoletsedwa). Ndipo chilango choyalutsa chili pa osakhulupirira

    [6] “(Kumbuka) tsiku limene Allah adzaukitsa akufa onse ndi kuwafotokozera zimene adachita (pa moyo wa dziko lapansi: zoipa ndi zabwino); Allah adazisunga mozilemba koma iwo adaziiwala. Ndipo Allah ndi mboni wa zonse (palibe chingabisike kwa Iye)

    [7] “Kodi sukudziwa (iwe, womvera wanzeru) kuti Allah akudziwa zakumwamba ndi zam’dziko lapansi? Sipakhala manong’onong’o a (anthu) atatu koma Iye Ngwachinayi wawo (ndi kudziwa kwake kosabisika chilichonse cha kumwamba ndi m’dziko), ngakhale a (anthu) asanu koma Iye Ngwachisanu ndi chimodzi wawo (mkudziwa Kwake), ngakhale ali ochepera kuposera pamenepa kapena ochulukira koma Iye ali nawo paliponse pomwe ati akhale (Allah ali nawo pamodzi mukudziwa Kwake kosabisika chilichonse), kenako adzawafotokozera pa tsiku la chiweruziro zimene adachita; ndithu Allah Ngodziwa chilichonse (mokwanira)

    [8] “Kodi siudaone! Kwa amene aletsedwa kunong’onezana zoipa pakati pawo, kenako akubwereza zimene adaletsedwa? Akunong’onezana za machimo, mtopola ndi kunyoza Mtumiki. Akakudzera akukulonjera (ndi malonje achinyengo) amene Allah sadakulonjerepo nawo ndipo akunena m’mitima mwawo: “Kodi nchifukwa chiyani Allah sakutilanga ndi mawu tikunenawa (ngati iyeyu ndi Mtumikidi wa Allah?” Jahannam ikuwakwanira: adzailowa. Ndipo taonani kuipa malo (awo) wobwerera

    [9] “E inu amene mwakhulupirira! Ngati mukunong’onezana, musamanong’onezane za machimo ndi mtopola ndi kunyoza Mtumiki; koma nong’onezanani za kulungama ndi kuopa Allah ndipo muopeni Allah, kwa Iye nkumene mudzasonkhanitsidwe (ndi kuweruzidwa)

    [10] “Ndithu manong’onong’o oipa amachokera kwa satana kuti adandaulitse amene akhulupirira; koma sangawapweteke nawo chilichonse kupatula Allah atafuna ndipo okhulupirira atsamire kwa Allah Yekha, (asalabadire zonong’onezana zawo)

    [11] “E inu amene mwakhulupirira! Kukapemphedwa kwa inu kuti perekani malo pabwalo (pokhala), perekani malowo (kuti anzanu apeze pokhala; mukatero) Allah akuphanulirani (chifundo Chake pano pa dziko ndi kumwamba). Ndipo kukanenedwa kuti imilirani, muimilire (musanyozere, apatseni ena malo); Allah awakwezera (ulemelero) mwa inu amene akhulupirira ndi amene apatsidwa nzeru. Ndipo Allah akudziwa bwino zimene mukuchita

    [12] E inu amene mwakhulupirira! Mukafuna kuyankhula ndi Mtumiki (s.a.w) tsogozani pa zoyankhula zanuzo, sadaka: kutero ndibwino kwa inu ndiponso ndichoyeretsa (mitima yanu). Koma ngati simudapeze (sadakayo) ndithu Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni

    [13] “Kodi mwaopa kutsogoza sadaka pakunena naye (Mtumiki)? Ngati simudachite zimenezi basi Allah wakukhululukirani; choncho pempherani Swala moyenera ndipo perekani Zakaat ndiponso mverani Allah pamodzi ndi Mtumiki Wake. Ndipo Allah akudziwa zonse zimene mukuchita

    [14] “Kodi sukuwaona amene apalana ubwenzi ndi anthu amene Allah wawakwiira; iwo sali mwa inu ndiponso sali mwa iwo. Ndipo akulumbira zabodza uku akudziwa (kuti limeneli ndibodza)

    [15] “Allah wawakonzera chilango chaukali, ndithudi nzoipa zimene amachita

    [16] “Kulumbira kwawo adakuchita kukhala chodzitetezera (iwo, ana awo ndi chuma chawo); choncho adatsekereza (anthu) ku njira ya Allah; choncho chilango choyalutsa chili pa iwo

    [17] “Chuma chawo, ngakhale ana awo, sizidzawathandiza konse ku chilango cha Allah. Iwowo ndi anthu a ku Moto m’menemo iwo adzakhala nthawi yaitali

    [18] “(Alikumbukire) tsiku limene Allah adzawaukitsa (ku imfa) onse, adzayamba kulumbira kwa Iye (zabodza) monga akulumbira (zabodza) kwa inu. Ndipo akuganiza kuti apezapo kanthu (pakulumbira kwawo). Dziwani, ndithudi, iwo ndi abodza

    [19] “Satana wawapambana ndipo wawaiwalitsa kukumbukira Allah. Iwowa ndiachipani cha satana. Dziwani kuti chipani cha satana nchotayika, (choonongeka)

    [20] “Ndithudi amene akutsutsana ndi Allah ndi Mthenga Wake, iwowo adzakhala m’gulu la onyozeka

    [21] “Allah adalamula (kuti): “Ndithu ndipambana Ine ndi atumiki Anga.” Ndithu Allah ndiwanyonga zokwana, Wopambana (sapambanidwa ndi aliyense)

    [22] “Supeza anthu okhulupirira mwa Allah ndi tsiku lachimaliziro akukonda amene akutsutsana ndi Allah ndi Mthenga Wake, ngakhale atakhala atate awo, ana awo abale awo ndi akumtundu wawo; kwa iwo (Allah) wazika chikhulupiliro (champhamvu) m’mitima mwawo, ndipo wawalimbikitsa ndi mphamvu zochokera kwa Iye. Ndipo adzawalowetsa m’minda yomwe pansi pake pakuyenda mitsinje; adzakhala m’menemo nthawi yaitali. Allah adzakondwera nawo ndipo (iwonso) adzakondwera Naye. Iwowa ndi chipani cha Allah. Dziwani kuti chipani cha Allah ndichopambana

    Ukapolo

    Surah 59

    [1] “Zonse za kumwamba ndi za pansi zimalemekeza Allah (ndi kumuyeretsa ku khalidwe losayenera ndi ulemelero Wake). Ndipo Iye Ngopambana (salephera kanthu), Ngwaluntha (m’kakonzedwe Kake ndi m’zochita Zake)

    [2] “Iye ndi Amene adatulutsa osakhulupirira ena mwa anthu a buku m’nyumba zawo mkusamusidwa koyamba (pa chilumba cha Arabu). Simunkaganizira kuti angatuluke (m’nyumba zawozo). Ndipo iwo amaganiza kuti malinga awo awateteza kwa Allah. Koma Allah adawalanga kupyolera mmene samayembekezera, ndipo adathira mantha oopsa m’mitima mwawo (potumiza Mtumiki Wake kwa iwo), adagumula nyumba zawo ndi manja awo ndi manja a okhulupirira. Choncho lingalirani (zimenezi) E inu eni nzeru

    [3] “Ndipo kukadapanda kuti Allah adawalembera (pachiyambi) kusamuka (m’nyumba zawo), akadawalanga pa dziko pompano; koma chilango cha Moto chili pa iwo tsiku lachimaliziro

    [4] “Zimenezo nchifukwa chakuti iwo adamtsutsa Allah ndi Mthenga Wake, (kutsutsa kopyola muyeso); ndipo amene akutsutsa Allah (sangapulumuke ku chilango Chake). Ndithu Allah Ndiwolanga mwaukali

    [5] “Sim’dadule mtengo uliwonse wa zipatso za kanjedza, (inu Asilamu), kapena kuusiya uli chiimire ndi thunthu lake koma nchifuniro cha Allah ndi kuti awayalutse otuluka m’malamulo Ake

    [6] “Ndipo chuma chimene wapereka Allah kwa Mtumiki Wake chochokera kwa iwo (Bani Nadhiri), chimenecho inu simudathamangitse mahachi kapena ngamira (pakuchipeza), koma Allah amapereka mphamvu kwa atumiki Ake zogonjetsera amene wamfuna. Ndipo Allah ali ndi Mphamvu (pa) chilichonse

    [7] “Chuma chimene Allah wachipereka kwa mtumiki Wake kuchokera kwa anthu am’midzi (yapafupi ndi mzinda wa Madina) chimenecho ncha Allah, ndi Mtumiki, ndi abale a mtumiki ndi amasiye, ndi masikini, ndiponso apaulendo; kuti chisakhale chongozungulira pakati pa olemera okha mwa inu. Ndipo chimene wakupatsani Mtumiki, chilandireni; ndipo chimene Wakuletsani chisiyeni. Muopeni Allah (potsatira malamulo Ake). Ndithu Allah Ngwaukali polanga

    [8] “(Chiperekedwe) kwa osauka osamuka omwe adatulutsidwa m’nyumba zawo ndi (kusiya) chuma chawo chifukwa chofuna zabwino za Allah ndi chikondi (Chake) ndi kupulumutsa (chipembedzo cha) Allah ndi Mthenga Wake (pogwiritsira ntchito matupi awo ndi chuma chawo); iwowa ndi (Asilamu) owona

    [9] “Koma amene adakhala kale mu mzinda uwu (wa Madina) ndi kukhulupirira akukonda amene adasamukira kwa iwo. Ndipo sakupeza vuto m’mitima mwawo pa zimene anzawo apatsidwa, ndipo akutsogoza zofuna za anzawo pa zawo, ngakhale iwo akuzifunitsitsa. Ndipo amene atetezedwa (ndi Allah) ku umbombo wa mitima yawo, amenewo ndiwo opambana

    [10] “Ndipo (okhulupirira) amene adadza pambuyo (pa Amuhajirina ndi Answari) akunena kuti: “Mbuye wathu tikhululukireni ndi anzathu amene adatitsogolera pa chikhulupiliro, ndipo musaike m’mitima mwathu njiru ndi chidani kwa amene adakhulupirira. E Mbuye wathu! Inu ndinu Wodekha, Wachisoni chosatha.”

    [11] “Kodi wawaona amene achita uchiphamaso? Amene akunena kwa anzawo amene sadakhulupirire pakati pa anthu a mabuku: “Ndithu ngati (mukakamizidwa) kutuluka mu mzinda wa Madina, ndithudi tidzatuluka nanu pamodzi ndipo sitingamvere aliyense za inu mpaka muyaya; ngati mutamenyedwa nkhondo (ndi Asilamu) tidzakuthandizani. Koma Allah akuikira umboni kuti iwo ndionama (pa zimene alonjeza)

    [12] “Ngati atatulutsidwa, sangatuluke nawo limodzi; ngati atamenyedwa, sangawathandize ndipo ngati atawathandiza atembenuza misana (kuthawa) kenako sapulumutsidwa

    [13] “Ndithu inu (Asilamu) mukuopedwa kwambiri m’mitima mwawo kuposa mmene akumuopera Allah. Zimenezo nchifukwa chakuti iwo ndi anthu osazindikira (chilichonse)

    [14] “(Ayuda) sangamenyane ndi inu ali pa gulu kupatula m’midzi yotetezedwa ndi malinga, kapena kuseri kwa zipupa. Nkhondo yawo pakati pawo njaukali; ungawaganizire kuti ali pamodzi pomwe mitima yawo njosiyana; zimenezo nchifukwa chakuti iwo ndianthu opanda nzeru

    [15] “Fanizo (la Ayuda a Banu Nadhiri) lili ngati (amene adatsutsa mwa Ayuda a Qainuka) amene awatsogolera (kupeza mavuto) posachedwapa, adalawa chilango (pa dziko lapansi) cha zochita zawo (ndi kuswa mapangano). Ndipo iwo adzalandira chilango (china) chowawa kwambiri, (pa tsiku la chiweruziro)

    [16] “Fanizo la achinyengo (achiphamaso pakuwanyenga Banu Nadhiri kuti amupandukire Mneneri wa Allah) lili ngati satana (ponyenga munthu kusiya chikhulupiliro). Adati kwa Iye: “Mkane (Allah).” Ndipo pamene adamkana, (satana) adati: “Ine sindili ndi iwe; ndithu ine ndikuopa Allah, Mbuye wa zolengedwa.”

    [17] “Choncho mapeto a onse awiriwo, kudali kukalowa ku Moto ndi kukhala m’menemo nthawi yaitali. Iyi ndiyo mphoto ya anthu onyenga (ochenjelera anzawo)

    [18] “E inu amene mwakhulupirira! Muopeni Allah (potsatira malamulo Ake ndi kusiya zimene waletsa) ndipo alingalire munthu aliyense zamawa zimene watsogoza. Ndipo muopeni Allah, ndithu Allah Ngodziwa zimene mukuchita (ndipo adzakulipirani pa zimenezo)

    [19] “Ndipo musakhale monga amene aiwala (zoyenera kuchitira) Allah; choncho (naye Allah) wawaiwalitsa mitima yawo (powachotsera kuzindikira zimene zingawathandize). Amenewa ndiwo olakwa kwakukulu (otuluka ku chilamulo cha Allah)

    [20] “Sangafanane anthu a ku Moto, (olangidwa), ndi anthu a ku Jannah, (opeza mtendere). Anthu aku Jannah ndiwo opambana

    [21] “Chikhala kuti tidaivumbulutsa Qur’an iyi pamwamba pa phiri, ukadaliona phirilo lili lodzichepetsa ndi kung’ambika chifukwa choopa Allah. Ndipo awa ndi mafanizo omwe tikuwapereka kwa anthu kuti aganizire

    [22] “Iye ndi Allah, Amene palibenso wina wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye, Wodziwa zamseri ndi zooneka. Iye Ngwachifundo chambiri, Ngwachisoni chosatha

    [23] “Iye ndi Allah, Amene palibenso wina wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye, Mfumu, Woyera, Mwini mtendere, Wotsimikizira (aneneri Ake mphamvu yochitira zozizwitsa,) Msungi wa chilichonse (yemwe akuona zochita za akapolo Ake;) Wamphamvu zopambana, Mgonjetsi Wotukuka muulemelero; Wamkulukulu. Wayeretsedwa Allah kuzimene akumuphatikiza nazo

    [24] “Iye ndi Allah; Mlengi wa (zinthu, palibe chomfanizira); Muumbi wa chilichonse, Mkonzi wa maonekedwe a zinthu, Ake ndi maina abwino, zonse za kumwamba ndi pansi zikumulemekeza Iye ndi kumyeretsa ku makhalidwe osayenerana ndi ulemelero Wake. Iye Ngopambana ndiponso Wanzeru zakuya

    Iye amene ayenera kufufuzidwa

    Surah 60

    [1] “E inu amene mwakhulupirira! Musawachite adani Anga ndi adani anu kukhala athandizi anu ndi kumawauza (nkhani zanu) mwa chikondi, pomwe iwo sanakhulupirire choonadi chimene chakudzerani. Adamtulutsa Mtumiki ndi inu nomwe (m’nyumba zanu) chifukwa chakuti mumakhulupirira Allah, Mbuye wanu, (palibe cholakwa chilichonse chimene mudawachitira,) ngati mwatuluka kukachita Jihâd pa njira Yanga ndi kufunafuna chikondi Changa (musapalane nawo ubwenzi). Mukuwatumizira chinsinsi (chanu cha nkhondo) chifukwa cha chikondi (chanu ndi iwo); (musachitenso zimenezi) pomwe Ine ndikudziwa zimene inu mukubisa ndi zimenene mukuzisonyeza (poyera); amene akuchita zimenezi mwa inu, ndiye kuti wataya njira yoongoka

    [2] “Akakumana nanu (pankhondo) akukhala adani anu ndipo akukutambasulirani manja ndi malirime awo moipa (pokumenyani ndi kukutukwanani); ndipo akulakalaka mukadakhala osakhulupirira (kuti mufanane nawo)

    [3] “Abale anu ngakhale ana anu sadzakuthandizani tsiku la Qiyâma (Allah) adzaweruza (pakati panu), ndipo Allah akuona zimene mukuchita

    [4] “Ndithu inu muli ndi chitsanzo chabwino cha (mtumiki) Ibrahim ndi amene adali naye pamene adawauza anzawo (osakhulupirira kuti): “Ndithu ife tapatukana nanu pamodzi ndi milungu yanu imene mukuipembedza kusiya Allah; takukanani, ndipo chidani ndi kusakondana zaonekera poyera pakati pa inu ndi ife mpaka muyaya, kufikira, mutakhulupirira mwa Allah mmodzi (inunso chitani chimodzimodzi, muwakane abale anu amene ali akafiri), kupatula mawu a Ibrahim pamene adamuuza tate wake (kuti): “Ndithu ndikupempherani chikhululuko. Palibe chimene ndingakutetezereni nacho kwa Allah (ngati mutamuphatikiza Allah ndi zina.”) E Mbuye wathu! Kwa Inu tatsamira. Ndipo kwa Inu tatembenukira ndiponso kobwerera nkwa Inu

    [5] “E Mbuye wathu! Musatichite kukhala mayeso kwa amene sadakhulupirire, tikhululukireni Mbuye wathu! Ndithu Inu, Ndinu Amphamvu zopambana ndiponso Anzeru zakuya

    [6] “Ndithu muli nacho inu kwa iwo (Ibrahim ndi omtsatira) chitsanzo chabwino kwa amene akuyembekezera kukumana ndi Allah ndi tsiku lachimaliziro. Ndipo amene anyozere ndithu Allah Ngolemera (ndiponso) Ngotamandika

    [7] “Mwina Allah angaike chikondi pakati panu ndi ena mwa amene mumawada (poiongolera mitima yawo kukhulupirira mwa Allah), ndipo Allah Ngokhoza chilichonse ndiponso Allah Ngokhululuka; Ngwachisoni chosatha

    [8] “Allah sakukuletsani kuwachitira zabwino ndi chilungamo amene sadakumenyeni ndi kukutulutsani m’nyumba zanu chifukwa cha chipembedzo. Ndithu Allah amakonda achilungamo

    [9] “Allah akukuletsani kugwirizana nawo amene adakumenyani chifukwa cha chipembedzo ndi kukutulutsani m’nyumba zanu, ndi amene adathandiza kukutulutsani. Amene ati agwirizane nawo iwowo ndiwo achinyengo

    [10] “E inu amene mwakhulupirira! Akakudzerani okhulupirira aakazi osamuka, ayeseni mayeso (kuti mudziwe chikhulupiliro chawo); Allah ali wodziwa kwambiri za chikhulupiliro chawo; ngati mutawadziwa kuti ndiokhulupirira musawabwezere kwa osakhulupirira. Akaziwo saloledwa kukwatiwa ndi osakhulupirira, iwonso saloledwa kuwakwatira. Abwezereni chiwongo chimene adapereka amuna osakhulupirirawo. Ndipo palibe tchimo kwa inu kuwakwatira, (ngakhale adasiya amuna awo achikafiri (ku Makka) ngati muwapatsa chiwongo chawo. Musakakamire maukwati ndi akazi achikafiri (osakhulupirira amene adatsalira ku Makka). Itanitsani zimene mudapereka kwa akazi anu (achikafiriwo), naonso Akafiri aitanitse zimene adapereka (kwa akazi awo akalowa m’Chisilamu). Limeneli ndi lamulo la Allah limene akulamula pakati panu. Allah ndiwodziwa kwambiri ndiponso Ngwanzeru (poika malamulo)

    [11] “Ndipo ngati mmodzi mwa akazi anu atakuthawani kupita kwa Akafiri, ndipo (mwadzidzidzi) mwakachita nkhondo (ndi kupeza chuma chosiya adani anu), apatseni amene awathawa akazi awo chofanana ndi chimene adapereka (pokwatira). Ndipo muopeni Allah amene inu mukumkhulupirira

    [12] “E iwe Mtumiki! Akakudzera akazi okhulupirira kudzakulonjeza kuti samphatikiza Allah ndi chilichonse ndi kuti saziba, sazichita chiwerewere, sazipha ana awo ndi kuti sazinena bodza lamkunkhuniza, lomwe akulipeka pakati pa manja awo ndi miyendo yawo (pompachika mwana kwa wina amene sali tate wake), ndi kutinso sadzakunyoza pa chinthu chabwino (chimene ukuwaitanira), landira lonjezo lawolo, ndipo apemphere chikhululuko kwa Allah. Ndithu Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni

    [13] “E inu amene mwakhulupirira! Musagwirizane ndi anthu amene Allah wawakwiyira. Ndithu iwo ataya mtima wopeza mphoto tsiku lachimaliziro (chifukwa cha machimo awo ochuluka) monga momwe atayira mtima akafiri za kuuka kwa amene ali m’manda

    Mizera

    Surah 61

    [1] “Zonse zakumwamba ndi zapansi zimalemekeza Allah (ndi kumuyeretsa kumakhalidwe osayenera ndi ulemelero Wake). Ndipo Iye Yekha Ngopambana pa chilichonse; Wanzeru zakuya

    [2] “E inu amene mwakhulupirira! Bwanji mukunena zimene simuchita

    [3] “Nzomuipira zedi Allah kunena zinthu zimene simuchita

    [4] “Ndithu Allah amakonda amene akumenya nkhondo pa njira Yake (yofalitsa chipembedzo Chake), ali pa mzere (umodzi) uku ali monga chomanga, chomangika mwamphamvu

    [5] “Ndipo kumbuka (iwe Mneneri{s.a.w}) pamene Mûsa adanena kwa anthu ake kuti: “Ndichifukwa ninji mukundivutitsa ine pomwe mukudziwa kuti ine ndine Mtumiki wa Allah kwa inu?” Ndipo pamene adapitiriza kupandukira choonadi, Allah adaipinda mitima yawo (kuti isalandire chiongoko); ndipo Allah saongola anthu otuluka m’chilamulo Chake

    [6] “Ndiponso (kumbuka) pamene adanena (Mtumiki) Isa (Yesu) mwana wa Mariya, kuti: “E inu ana a Israelil! Ndithu ine ndine Mtumiki wa Allah kwa inu, amene ndikuchitira umboni zimene zidadza patsogolo panga za buku la Chipangano chakale (Torah) ndipo ndikuuzani nkhani yabwino ya mthenga amene adzadze pambuyo panga, dzina lake Ahamad (Muhammad{s.a.w}).” Koma pamene adawadzera (Mtumiki wolonjedzedwayo) ndi zisonyezo zowonekera poyera (kuti iye ndi Mtumiki wa Allah). Adati: “Awa ndi matsenga owonekera.”

    [7] “Kodi ndani oipitsitsa kuposa yemwe wapekera Allah bodza, pomwe iye akuitanidwira ku Chisilamu (chipembedzo choona ndi chabwino)? Ndipo Allah saongola anthu achinyengo

    [8] “Akufuna kuti azimitse dangalira la Allah ndi pakamwa pawo ndipo Allah Ngokwaniritsa dangalira Lake ngakhale ziwaipire osakhulupirira

    [9] “Iye ndi amene adatuma Mtumiki Wake (Muhammad{s.a.w}) ndi chiongoko ndi chipembedzo choona, kuti achiike pamwamba pa zipembedzo zonse, ngakhale kuti ophatikiza Allah ndi mafano zikuwaipira

    [10] “E inu amene mwakhulupirira! Kodi ndikudziwitseni malonda amene angakupulumutseni ku chilango chowawa

    [11] “Muzimkhulupirira Allah ndi Mtumiki Wake; ndipo muzichita Jihâd pa njira ya Allah ndi chuma chanu, ndi matupi anu. Zimenezo nzabwino kwa inu ngati muli odziwa

    [12] “Akukhululukirani machimo anu ndipo akulowetsani m’minda momwe mitsinje ikuyenda pansi pake, ndiponso (adzakupatsani) mokhala mwabwino ku minda yamuyaya. Kumeneko ndiko kupambana kwakukulu

    [13] “Ndizina zomwe mukuzifuna. Thandizo (lonse) lichokera kwa Allah ndi kugonjetsa kumene kuli pafupi; ndipo auze nkhani yabwino okhulupirira

    [14] “E inu amene mwakhulupirira! Khalani othangata (kufalitsa chipembedzo cha) Allah (pamene Mtumiki akukuitanani kuti mumthangate) monga momwe adanenera Isa (Yesu) mwana wa Mariya powauza otsatira ake: “Ndani adzandithangata pa ntchito ya Allah (yofalitsa chipembedzo Chake)? Otsatira ake adanena: “Ife ndife othangata (kufalitsa chipembedzo cha) Allah.” Choncho gulu lina la ana a Israyeli lidakhululupirira, ndipo gulu lina silidakhululupirire, tero tidawapatsa mphamvu amene adakhulupirira pa adani awo, ndipo adali opambana

    Tsiku la Chisanu

    Surah 62

    [1] “Zonse zakumwamba ndi dziko lapansi zikulemekeza Allah; Mfumu, Woyera, Wamphamvu zopambana ndi nzeru zakuya (ndi kumyeretsa ku makhalidwe osayenerana ndi ulemelero Wake)

    [2] “Iye ndiAmene adatumiza kwa Ummiyyina (osadziwa kulemba ndi kuwerenga), Mtumiki wochokera mwa iwo kuti awawerengere ndime Zake ndi kuti awayeretse (ku uchimo ndi kumakhalidwe oipa) ndi kuwaphunzitsa Qur’an ndi mawu anzeru (a mtumiki) ndithu kale adali osokera kowonekera (Mtumiki {s.a.w} asadadze kwa iwo

    [3] “Ndipo (adamtumizanso) kwa ena mwa iwo, omwe sadakumane nawo, ndipo Iye (Allah) Ngopambana (pa chinthu chilichonse ndi Wamphamvu zoposa ndiponso) Ngwanzeru zakuya

    [4] “Umenewo ndiwo ubwino wa Allah akuupereka kwa amene wamfuna (mwa akapolo Ake); ndipo Allah yekha ndi Mwini ubwino waukulu

    [5] “Fanizo la (Ayuda) amene adawasenzetsa Taurat (pokakamizidwa kuti atsatire zophunzitsa za bukulo, koma osatsatira), ali ngati bulu amene akusenza mabuku akuluakulu anzeru, (koma osathandizika nawo). Taonani kuipa fanizo la anthu amene atsutsa zisonyezo za Allah. Ndipo Allah saongola anthu achinyengo

    [6] “Nena: “E inu Ayuda! Ngati mwadziganizira kuti ndithu ndinu okondedwa a Allah kuposa (mitundu ina ya) anthu, ilakelakeni imfa (kuti mukalowe ku mtendere wa Allah) ngati mukunena zoona

    [7] “Ndipo sangailakelake mpang’ono pomwe chifukwa cha (zoipa) zimene manja awo atsogoza! Ndipo Allah akudziwa bwino za (anthu) osalungama

    [8] “Nena (kuti): “Ndithu imfa imene mukuithawa (palibe chipeneko) ikumana nanu; kenako muzabwezedwa kwa wodziwa zobisika ndi zooneka; ndipo adzakuuzani zimene mudali kuchita

    [9] “E inu amene mwakhulupirira! Kukaitanidwa ku Swala (pemphero la Ijuma) tsiku la Ijuma, pitani mwachangu kukamtamanda Allah. Ndipo siyani malonda; zimenezo (mwalamulidwazo) nzabwino kwa inu ngati mukudziwa

    [10] “Choncho Swala (ya Ijumayo) ikatha, balalikanani pa dziko, ndipo funani ubwino wa Allah; ndipo mtamandeni Allah kwambiri kuti mupambane (pa dziko lapansi ndi pa tsiku lachimaliziro)

    [11] “Ndipo akaona malonda kapena masewero, akubalalika kunka ku zimenezo ndi kukusiya uli chiimire (ukuchita khutuba ndi anthu ochepa). Nena (kwa iwo): “Zimene zili kwa Allah nzabwino kwa inu kuposa masewero ndi malonda. Ndipo Allah Ngwabwino kwambiri kuposa opatsa onse.”

    Achinyengo

    Surah 63

    [1] “Akakudzera achiphamaso akunena kuti: “Tikuikira umboni kuti ndithu iwe ndiwe Mtumiki wa Allah, ndipo Allah akudziwa kuti iwe ndiwe mtumiki Wake. Ndipo Allah akuikira umboni kuti achiphamaso ngabodza (pa zomwe akunena)

    [2] “Kulumbira kwawo (kwa bodza) akuchita kukhala chotetezera (chuma chawo ndi matupi awo). Tero atsekereza (anthu kuyenda) panjira ya Allah. Ndithu nzoipa zedi zimene amachita

    [3] “Zimenezo nchifukwa chakuti iwo adakhulupirira (modzionetsera), kenako adakana (mobisa). Choncho mitima yawo idatsekedwa kotero kuti iwo sangathe kuzindikira (chimene chingawapulumutse ku chilango cha Allah)

    [4] “Ndipo ukawaona, akukondweretsa matupi awo; ndipo akayankhula umvetsera zoyankhula zawo (chifukwa chakuthwa kwa malirime awo, pomwe mkati mwawo ndiming’oma yopanda kanthu); iwo ali ngati matsinde a mitengo yomwe yayadzamiritsidwa (ku chipupa); (mwa iwo mulibe moyo). Mkuwe uliwonse (umene akuumva) akuganiza kuti ukulinga iwo, (chifukwa cha kuzindikira chinyengo chawo); iwowa ndiadani; chenjerani nawo. Allah awatembelere! Mwanjira yanji akuchotsedwa (ku choonadi)

    [5] “Kukanenedwa kwa iwo kuti: “Bwerani, akupemphereni chikhululuko mthenga wa Allah, akutembenuza mitu yawo (monyoza ndi modzitukumula), ndipo uwaona akunyoza uku akudzikweza (osatsatira langizo).”

    [6] “Kwa iwowa nchimodzimodzi kuwapemphera kwako chikhululuko, kapena kusawapemphera. Allah sangawakhululukire (chifukwa cha kuzama kwawo m’kusakhulupirira). Ndithu Allah saongola anthu otuluka m’chilamulo (Chake)

    [7] “Amenewa ndiwo omwe akunena kwa Answari; (Asilamu aku Madina, kuti): “Musawapatse chuma (chanu) amene ali ndi Mtumiki wa Allah kuti abalalikane.” Pomwe nkhokwe zonse (zachuma) za kumwamba ndi dziko lapansi zili m’manja mwa Allah (ndipo amachipereka kwa amene wamfuna); koma achiphamaso sakuzindikira (zimenezo)

    [8] “Akunena kuti: “Ngati tibwerera ku Madina wolemekezeka adzatulutsa wonyozeka m’menemo. “Pomwe ulemelero ngwa Allah ndi Mthenga Wake ndi okhulupirira; koma achinyengo sakudziwa (zimenezo).”

    [9] “E inu amene mwakhulupirira! Chuma chanu ngakhalenso ana anu zisakutangwanitseni ndi kusiya kukumbukira Allah (ndi kukwaniritsa zimene wakulamulani). Ndipo amene achite zimenezo iwo ndi otaika

    [10] “Perekani (mwachangu pa njira ya Allah) zina mwa zomwe takupatsani, isanamfikire mmodzi wa inu imfa (mwadzidzidzi) ndi kuyamba kunena (modandaula): “Mbuye wanga! Bwanji osandichedwetsa nthawi pang’ono kuti ndipereke sadaka (ndi kuti ndikonze zina zimene sindinazikwaniritse) ndi kutinso ndikhale mwa anthu anu abwino.”

    [11] “Ndipo Allah sangauchedwetse mzimu (ngakhale ndi mphindi imodzi) ukaidzera nthawi yake ya imfa; ndipo Allah Ngodziwa zonse zimene mukuchita, (ndipo adzakulipirani pa zimenezo)

    Kusokonezana

    Surah 64

    [1] “Zonse zakumwamba ndi zam’dziko lapansi zikulemekeza Allah (ndi kumyeretsa ku zinthu zosayenerana ndi ulemelero Wake; ufumu Ngwake ndipo kutamandidwa kwabwino Nkwake. Ndipo Iye ali ndi mphamvu pa chilichonse)

    [2] “Iye ndiamene adakulengani (nonsenu popanda kuchokera ku chilichonse) choncho mwa inu alipo wosakhulupirira ndiponso mwa inu alipo wokhulupirira. Ndipo Allah Ngopenya zonse zimene mukuchita (ndipo adzakulipirani nazo)

    [3] “Adalenga thambo ndi nthaka mwachoonadi ndipo adakujambulani majambulidwe abwino; ndipo kobwerera nkwa Iye (pa tsiku lachiweruziro)

    [4] “(Allah) akudziwa za kumwamba ndi za m’dziko lapansi, ndiponso akudziwa zimene mukuzibisa ndi zimene mukuzilengeza (zochita ndi zoyankhula); Allah Ngodziwa za m’zifuwa

    [5] “Kodi siidakufikeni nkhani ya omwe sadakhulupirire kale? Adalawa (zowawa) za zoipa za zinthu zawo (pa dziko lapansi). Ndipo chilango chowawa chidzakhala pa iwo (tsiku lachimaliziro)

    [6] “Zimenezo nchifukwa chakuti atumiki awo amawadzera ndi zozizwitsa koma iwo amanena (mwachipongwe): “Ha! Anthu anzathu (onga ife) angationgole?” Choncho sadakhulupirire (utumiki wawo) ndipo adanyoza (choonadi) potero Allah adawasiya (ndi kupanda chikhulupiliro kwawo) ndipo Allah Ngokwanira ndiponso Ngoyamikidwa

    [7] “Amene sadakhulupirire akumazinamiza kuti sadzaukitsidwa ku imfa. Nena (kwa iwo iwe Mtumiki{s.a.w}): “Sizili choncho pali Mbuye wanga, ndithu mudzaukitsidwa ku imfa, ndipo mudzauzidwa zimene mumachita (pa dziko lapansi). Zimenezo kwa Allah nzosavuta (kuzichita).”

    [8] “Khulupirirani Allah ndi Mtumiki Wake, ndi dangalira limene talivumbulutsa (Qur’an). Ndipo Allah Ngodziwa kwambiri zimene mukuchita

    [9] “(Kumbukirani) tsiku limene adzakusonkhanitsani chifukwa cha tsiku lakusonkhana (zolengedwa zonse), limenelo ndi tsiku lolephera; ndipo amene akhulupirira mwa Allah ndi kuchita zabwino, amfafanizira zoipa zake, ndipo akamulowetsa m’minda momwe pansi pake pakuyenda mitsinje; adzakhala m’menemo muyaya; kumeneko ndiko kupambana kwakukulu

    [10] “Koma amene sadakhulupirire natsutsa zozizwitsa Zathu (zimene zidaperekedwa kwa Aneneri Athu;) iwowo ndi anthu a ku Moto; adzakhala mmenemo nthawi yaitali, amenewo ndiwo mabwelero oipa

    [11] “Palibe vuto lililonse lingapezeke pokhapokha Allah atafuna; ndipo amene akhulupirira Allah, (Allah) aongola mtima wake (kuti ukhale wokhutira ndi chiweruzo cha Allah). Ndipo Allah Ngodziwa chinthu chilichonse

    [12] “Choncho mverani Allah ndipo mverani Mtumiki, ngati munyozera (ndi zanu), ndithu udindo wa Mtumiki Wathu ndikufikitsa uthenga omveka

    [13] “Allah, palibe wina wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Ndipo kwa Allah Yekha, okhulupirira atsamire

    [14] “E inu amene mwakhulupirira! Ndithu ena mwa akazi anu ndi ana anu ndiadani anu (chifukwa chakuti amakuchotsani kumbali yomvera Allah pofuna kuti mukwaniritse zofuna zawo). Chenjerani nawo. Ngati muwakhululukira ndi kunyalanyaza ndi kubisa zolakwa zawo ndibwino kwambiri, ndithu Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha

    [15] “Ndithu chuma chanu ndi ana anu ndimayesero (kwa inu); koma kwa Allah kuli malipiro akulu (kwa yemwe wasankha kumvera Allah)

    [16] “Choncho muopeni Allah mmene mungathere, mverani (zophunzitsa Zake) ndipo tsatirani (malamulo Ake) komanso perekani zimene wakupatsani zikhala zabwino kwa inu. Dzichitireni nokha zabwino. Ndipo amene watchinjirizidwa ku umbombo wa mtima wake, iwowo ndiwo opambana

    [17] “Ngati mungamkongoze Allah ngongole yabwino aiwonjezera kwa inu (malipiro ake) ndipo akukhululukirani (zolakwa zanu.) Ndipo Allah Ngolandira kuthokoza, Ngoleza

    [18] “Ngodziwa zobisika ndi zoonekera, Ngwamphamvu zopambana, Ngwanzeru zakuya

    Chisudzulo

    Surah 65

    [1] “E iwe Mneneri (s.a.w) ngati mufuna kusudzula akazi ukwati, asudzuleni mnyengo yowerengera Edda yawo (kuwerengera Edda kumayambika mkazi akakhala ndi Twahara akachira matenda akumwezi), ndipo werengerani nyengo ya Edda. Ndipo muopeni Allah Mbuye wanu. Ndipo musawatulutse m’nyumba zawo ndiponso asatuluke kupatula akachita tchimo lalikulu loonekera (loyenera chilango, apo atha kutulutsidwa). Ndipo amenewa ndiwo malire a Allah (amene wawakhazikitsa kwa anthu Ake). Ndipo amene apyola malire a Allah wadzichitira yekha zoipa. Sukudziwa (cholinga cha malamulo amenewa) mwina Allah adzadzetsa chinthu pambuyo pake (chosonyeza kuyanjana)

    [2] “Choncho pamene iwo (osiyidwawo) nyengo yawo (Edda) itayandikira kutha, abwelereni mwa ubwino kapena asiyeni mwaubwino (polekelera nyengoyo kuti ithe); ndipo (powabwerera) funani mboni ziwiri zolungama zochokera mwa inu (zimene zichitire umboni kuti inu mukubwererana) ndipo perekani umboni chifukwa choopa Allah. Zimenezo ndizo akulangizidwa nazo amene akhulupirira mwa Allah ndi tsiku lachimaliziro. Ndipo amene akumuopa Allah (potsatira malamulo Ake), amkonzera njira yotulukira (m’mavuto)

    [3] “Ndipo ampatsa rizq kuchokera momwe samayembekezeramo. Ndipo amene akutsamira kwa Allah (pa zinthu zake zonse), ndiye kuti Allah ali wokwana kwa iye (kumkonzera chilichonse), ndithu Allah Ngokwaniritsa cholinga Chake ndi chofuna Chake. Ndithu chinthu chilichonse Allah wachipatsa mlingo wake woyenera (ndipo sichingaupyole)

    [4] “Ndipo Edda ya amene asiya kudwala kumwezi mwa akazi anu chifukwa cha kukula, ngati mukukaika (nthawi ya Edda yawo), Edda yawo ndi miyezi itatu. Ndi omwe sadathe nsinkhu Edda yawo ndi momwemonso. Tsono akazi apakati nthawi yothera Edda yawo ndipomwe abereka. Ndipo amene aopa Allah amfewetsera zinthu zake (kuti zikhale zosavuta)

    [5] “Limenelo ndilamulo la Allah (lomwe) walikhazikitsa kwa inu. Ndipo amene aopa Allah (posunga malamulo ake), amam’fafanizira zoipa zake, ndiponso amamkulitsira malipiro ake

    [6] “Akhazikeni (osiyidwawo) m’mene mukukhala inumo monga momwe kulili kupeza kwanu (ndi mphamvu zanu ngakhale kuti mwawasiya ukwati). Musawavute ndi cholinga chowapana (kuti athawe okha). Ngati ali ndi pakati, apatseni zonse zofunika pa moyo mpaka adzabereke. Ngati akukuyamwitsirani ana anu apatseni malipiro awo mokwanira; gwirizanani pakati panu mwa ubwino ndi mofatsa. Ngati wina apereka mavuto kwa mnzake (ndiye kuti mwanayo) adzamuyamwitsira (mkazi) wina

    [7] “Wopeza bwino apereke malinga ndi kupeza bwino kwake; ndipo amene wachepekedwa rizq lake, apereke (kangachepe) pa zomwe Allah wampatsa. Allah sakakamiza aliyense kupatula zomwe wampatsa. Allah apereka kupeza bwino pambuyo pa masautso

    [8] “Ndipo ndimidzi ingati yomwe idanyoza lamulo la Mbuye wawo ndi Atumiki Ake, ndipo tidawawerenga ndi chiwerengero chokhwima (posanthula zochita zawo zonse). Ndiponso tidawalanga ndi chilango chaukali

    [9] “Choncho adalawa kuipa kwa zinthu zawo ndipo mapeto azinthu zawo adali kutayika (kuonongeka kwakukulu)

    [10] “Allah wawakonzera iwo chilango chokhwima, choncho muopeni Allah, E inu eni nzeru, amene mwakhulupirira, ndithu Allah wavumbulutsa chikumbutso (cholemekezeka kwa inu)

    [11] “Mtumiki (amene) akukuwerengerani ndime za Allah zolongosola (choonadi ndi chonama) kuti awatulutse mu mdima ndi kuwaika ku dangalira amene wakhulupirira ndi kumachita zabwino. Ndipo amene akhulupirira Allah ndi kumachita zabwino, adzamlowetsa m’minda momwe mitsinje ikuyenda pansi pake; akakhala m’menemo muyaya. Ndithu Allah wamkonzera rizq (dalitso) labwino (Jannah)

    [12] “Allah ndiYemwe adalenga thambo zisanu ndi ziwiri, nthakanso chimodzimodzi. Malamulo Ake akutsika pakati pa izo kuti mudziwe kuti ndithu Allah pachilichonse ndi Wokhoza ndikutinso Allah wachizinga chilichonse m’kuchidziwa

    Choletsa

    Surah 66

    [1] “E iwe Mneneri (s.a.w)! Nchifukwa ninji ukudziletsa chimene Allah wakuloleza kuchita? Ukufuna kukondweretsa akazi ako (nchifukwa Chake wachita izi?) Koma Allah Ngokhululuka kwambiri, Ngwachisoni chosatha

    [2] “Ndithu Allah wakhazikitsa kamasulidwe kakulumbira kwanu, ndipo Allah ndiye Mtetezi wanu, Iye Ngodziwa kwambiri ndiponso Ngwanzeru zakuya (pa malamulo amene wawakhazikitsa kwa inu)

    [3] Ndipo kumbuka pamene Mneneri (s.a.w) adauza wina mwa akazi ake nkhani mwachinsinsi, choncho (mkaziyo) pamene adaiulula, Allah adamdziwitsa (Mtumiki) za kuululidwa kwa nkhaniyo, (ndipo Mtumiki) adaifotokoza mbali ina ya nkhaniyo, koma mbali ina adaisiya. Pamene adamfotokozera (mkazi wake) zankhaniyo adati: “Ndani wakuuza zimenezi?” (Mtumiki {s.a.w}) adati: “Wandiuza Wodziwa kwambiri ndiponso Wodziwa zazing’ono ndi zazikulu (Amene sichibisika kwa Iye chobisika chilichonse)

    [4] “Ngati awirinu mulapa kwa Allah pazimene mwachita (chitani changu kulapa) chifukwa chakuti mitima yanu yapotoka pang’ono (chifukwa cha nsanje pa zimene Mneneri akufuna zosunga chinsinsi Chake); koma ngati awirinu muthandizana pazimene zingamvutitse, ndithu Allah ndiye Mtetezi wake ndi Jibril (Gabriele) ndiponso okhulupirira abwino; naonso angelo, kuonjezera apa ndiathandizi (ake)

    [5] “Ngati (Mtumiki) akakusudzulani, ndithu Mbuye wake, ampatsa akazi ena mmalo mwa inu, abwino kuposa inu: ogonjera (Allah), okhulupirira (ndi mitima yawo), omvera, olapa, odzichepetsa (pamaso pa Allah) ochita mapemphero (kwambiri), oyenda (pa chikhulupiliro cha Allah kapena ochulukitsa kusala) amene adakwatiwapo kale ndi osakwatiwapo.”

    [6] “E inu amene mwakhulupirira! Dzitchinjirizeni inu ndi mawanja anu ku Moto umene nkhuni zake ndi anthu ndi miyala; oyang’anira ake ndi angelo ouma mtima, amphamvu, sanyoza Allah pa zimene Wawalamula, ndipo amachita (zokhazo) zimene alamulidwa

    [7] “(Adzawauza osakhulupirira pa tsiku la chiweruziro) E inu amene simdakhulupirire! Musadandaule lero, ndithu mukulipidwa pa zimene mumachita (padziko lapansi)

    [8] “E inu amene mwakhulupirira! Lapani kwa Allah; kulapa koona; ndithu Mbuye wanu akufafanizirani zoipa zanu ndi kukakulowetsani m’minda momwe mitsinje ikuyenda pansi pake, tsiku limene Allah sadzayalutsa mneneli ndi amene adakhulupirira pamodzi naye. Dangalira lawo lidzayenda chapatsogolo pawo ndi mbali yakumanja kwawo, uku akunena: “Mbuye wathu! Tikwanitsireni dangalira lathu (mpaka likatifikitse ku Munda wamtendere), ndiponso tikhululukireni ndithu Inu ndi Wokhoza chilichonse.”

    [9] “E iwe Mneneri! Limbana ndi akafiri (osakhulupirira) ndi Amunafikina (Achiphamaso), aumire mtima. Ndipo malo awo ndi ku Jahannam, taonani kuipa kobwerera (kwawo)

    [10] “Allah wapereka fanizo la osakhulupirira monga mkazi wa Nuh ndi mkazi wa Luti. Awiriwa adali pansi pa akapolo Athu awiri abwino, koma adali osakhulupirika kwa amuna awo, (ndipo amuna awo) sadawateteze kalikonse ku chilango cha Allah, ndipo kudanenedwa kwa iwo “Lowani ku Moto pamodzi (ndi ena) olowa.”

    [11] “Ndiponso Allah wapereka fanizo la amene akhulupirira monga mkazi wa Firiauna (Farawo) pamene adanena: “Mbuye wanga! Ndimangireni kwa inu Nyumba mu Jannah, ndipo ndipulumutseni kwa Firiauna ndi zochita zake, ndiponso ndipulumutseni kwa anthu oipa (ndi amtopola.)”

    [12] “Ndi (fanizo lina la wokhulupirira monga) Mariya mwana wa Imran amene adasunga umaliseche wake; ndipo tidauzira mmenemo Mzimu Wathu ndipo adavomereza mawu a Mbuye wake (omwe adali zolamula Zake ndi zoletsa Zake) ndi mabuku Ake (amene adavumbulutsidwa kwa Aneneri Ake); ndipo adali mmodzi wa opitiriza kudzichepetsa (ndi kumvera Allah)

    Ufumu

    Surah 67

    [1] “۞ Watukuka ndi kudalitsika (Allah) Amene m’manja Mwake muli ufumu (wochita chilichonse pazolengedwa zonse); ndipo Iye ali ndi mphamvu yokwanira pachilichonse

    [2] “Amene adalenga imfa ndi moyo kuti akuyeseni (mayeso) ndani mwa inu ali wochita zabwino (kwambiri). Ndipo Iye ndiWopambana m’mphamvu (salephera kanthu) ndiponso Wokhululukira (olakwa)

    [3] “Amene adalenga thambo zisanu ndi ziwiri mosanjikana (kapena zolingana mkalengedwe kake). Suona kusiyana m’zolenga za Wachifundo chambiri. Bwereza kuyang’ana, kodi ukuona pena pong’ambika

    [4] “Bwerezanso kuyang’ana kachiwiri, kuyang’anako kukubwerera wekha (uku maso) ali olobodoka ndiponso otopa. (Suona polakwika paliponse)

    [5] “Ndipo ndithu talikongoletsa thambo loyandikirali ndi nyali (nyenyezi) ndipo tazichita kukhala (mochokera zenje) zolasila asatana. Ndipo tawakonzera (patsiku lachimaliziro) chilango cha Moto woyaka

    [6] “Ndipo kwa amene sakhulupirira Mbuye wawo ali nacho chilango cha Jahannam; ndipo kuipirenji kobwerera

    [7] “Akadzaponyedwa m’menemo adzamva mavume ake (oipa) uku ukuwira mwaukali

    [8] “Udzayandikira kudukaduka chifukwa cha mkwiyo (kukwiira oipa); nthawi iliyonse gulu (la oipa) likadzaponyedwa m’menemo, Angelo oyang’anira Motowo adzawafunsa (mowadzudzula): “Kodi sadakufikeni mchenjezi (wokuchenjezani za tsikuli?).”

    [9] “Adzayankha “Inde, adatifika mchenjezi koma tidatsutsa, ndipo tidati: ‘Allah sadavumbulutse chilichonse (kwa iwe ngakhale kwa anzako). Koma inu muli m’kusokera kwakukulu.”

    [10] “Ndipo adzanena: “Tikadakhala kuti tidamvera (zimene ankatiuza) kapena kuziganizira mwanzeru sitikadakhala m’gulu la anthu a ku Moto.”

    [11] “Choncho adzavomereza machimo awo (koma sipadzakhala chopindula;) tero kuonongeka ndi kukhala kutali (ndi chifundo cha Allah) kuli pa anthu a ku Moto

    [12] “Ndithudi amene akumuopa Mbuye wawo pomwe iwo sakumuona, adzapeza chikhululuko pa machimo awo ndi malipiro aakulu (pa zabwino zomwe ankachita)

    [13] “Ndipo bisani mawu anu, kapena aonetseni poyera; (zonsezi nchimodzimodzi kwa Allah) ndithudi Iye Ngodziwa zobisika za m’mitima

    [14] “Kodi asadziwe amene adalenga (zinthu zonse)? Pomwe Iye Ngodziwa zinthu zingo’nozing’no kwambiri mmene zilili (ndiponso) Ngodziwa nkhani zonse

    [15] “Iye ndi Amene wakupangirani nthaka kuti ikhale yogonjera (pa chilichonse chimene mufuna). Choncho yendani mbali zake zonse; ndipo idyani rizq lake, (limene Allah akukutulutsirani). Ndipo kwa Iye Yekha ndiko kobwerera kwanu (nonse mutapatsidwa moyo wachiwiri)

    [16] “Kodi muli m’chitetezo kwa Amene ali kumwamba kuti sangakukwilireni m’nthaka (ndikukudzidzimutsani) pamene nthaka ikugwedezeka molimba

    [17] “Kapena muli m’chitetezo kwa Amene ali kumwamba kuti sangakutumizireni mphepo yamkuntho ya miyala (ndi kukuonongani ndi miyalayo?) Choncho mdzadziwa mmene lilili chenjezo Langa (pa inu)

    [18] “Ndithudi amene adalipo kale iwo asanabadwe adakana mithenga yawo. Nanga udali bwanji mkwiyo Wanga pa iwo (pakuwaononga onse)

    [19] “Kodi, sadaone mbalame pamwamba pawo mmene zikutambasulira (mapiko ake) ndi kuwafumbata. Palibe amene akuzigwira kuti zisagwe koma (Allah) Wachifundo chambiri; ndithudi Iye pachilichonse Ngopenya

    [20] “Kodi ndani amene ali asilikali anu okutetezani kuchilango posakhala (Allah) Wachifimdo chambiri? Ndithudi osakhulupirira ali mkunyengeka (pa zimene akuganizira)

    [21] “Kodi ndani uyo amene angakupatseni rizq (limene mungakhalire ndi moyo ndi kupezera mtendere) ngati Iye atatsekereza rizq Lake (kwa inu)? Koma Akafiri akupitiriza kudzikweza kwawo, ndi kudziika kutali ndi choonadi

    [22] “Kodi amene akuyenda mozyolika ndi nkhope yake angakhale wolungama kapena amene akuyenda moongoka panjira yosakhota

    [23] “Nena: “Iye ndi Amene adakulengani (pomwe simudali kanthu) ndipo adakupatsani makutu, maso ndi mitima, (zimene mukhoza kupeza nazo mtendere). Koma kuyamika kwanu (kwa Yemwe adakupatsani zimenezi) nkochepa kwambiri

    [24] “Nena: “Iye ndi amene adakuchulukitsani pa dziko ndipo kwa Iye (Yekha) ndiko mudzasonkhanitsidwa (kuti adzakuwerengereni ndi kukulipirani)

    [25] “Akunena (monyada osakhulupirira za kuuka): “Ndiliti (lidzakwaniritsidwa) lonjezo ili ngati inu muli owona?”

    [26] “Nena (iwe Mtumiki{s.a.w}): “Ndithu kudziwa (kwa izi) nkwa Allah yekha, ndipo ndithudi ine, ndine mchenjezi wowonekera.”

    [27] “Koma akadzaziona (zimene akulonjezedwazo) zili pafupi (ndi iwo), nkhope za amene sadakhulupirire zidzakhumudwa ndikuyaluka kwambiri, ndipo kudzanenedwa (mowadzudzula): “Izi ndi zija mudali kuzipempha (kuti zidze, zadza tsopano)

    [28] “Nena (iwe Mtumiki{s.a.w}): “Tandiuzani ngati Allah atandiononga pamodzi ndi amene ndili nawo (monga momwe mukufunira) kapena kutichitira chifundo (ndikutalikitsa nthawi ya moyo wathu). Nanga ndani amene adzawateteza wosakhulupirira ku chilango chowawa?”

    [29] “Nena: “Iye ndiye (Allah) Wachifundo chambiri, takhulupirira mwa Iye ndiponso kwa Iye ndikumene tatsamira. Choncho posachedwapa mudziwa (chilango chikatsika kuti) ndani (m’magulu awiriwa) yemwe ali m’kusokera koonekera.”

    [30] “Nena: “Tandiuzani ngati madzi anuwa ataphwa (kulowelera pansi penipeni); choncho ndani amene angakubweretsereni madzi oyenda (ochokera mkati mwanthaka)

    Peni

    Surah 68

    [1] “Nûn. Ndikulumbilira cholembera (chimene akulembera angelo), ndi zimene amalemba

    [2] “Pa chisomo cha Mbuye wako iwe sindiwe wamisala (pokupatsa uneneri)

    [3] “Ndipo ndithu udzakhala ndi malipiro akulu osaduka, (onkerankera mtsogolo chifukwa cha mavuto amene ukukumana nawo pofikitsa uthenga)

    [4] “Ndipo ndithu uli nawo makhalidwe abwino kwambiri (omwe Allah adakulenga nawo)

    [5] “Basi, posachedwapa uona, iwonso aona

    [6] “Kuti ndani mwa inu wamisala (iwe kapena iwo)

    [7] “Ndithu Mbuye wako akum’dziwa bwino amene wasokera panjira yake. Ndiponso akuwadziwa bwino amene ali oongoka

    [8] “Choncho, usawamvere otsutsa; (usasiye zimene uli nazo ngakhale sakugwirizana nazo)

    [9] “Akufuna kuti ukadakhala wofewa kwa iwo (pa zinthu zina) nawo akadakhala ofewa (kwa iwe)

    [10] “Ndipo usamumvere aliyense wochulukitsa kulumbira, woyaluka

    [11] “Wojeda, woyenda ndi ukazitape (ndi cholinga choononga umodzi wawo)

    [12] “Wotsekereza zabwino, wamtopola, wamachimo ambiri

    [13] “Wouma mtima; pamwamba pa izi ndi wodzipachika mu mtundu wa ena (pomwe iye sali m’menemo)

    [14] “Chifukwa choti iye ndi mwini chuma ndi ana (ndi zimene ali kunyadira)

    [15] “Zikawerengedwa kwa iye Ayah Zathu amanena: “Izi ndi nthano za akale (ndi zabodza zawo, zopeka).”

    [16] “Timuika pamphuno pake chizindikiro (chosasiyana nacho kuti ayaluke nacho pamaso pa anthu)

    [17] “Ndithu ife tidawayesa (eni mzinda wa Makka ndi mtendere omwe udali pa iwo, koma adakana monga) momwe tidawayesera eni munda, pamene adalumbira kuti akathyola (zipatso za m’munda wawozo) mbandakucha (kuti osauka asawaone angawapemphe)

    [18] “Ndipo sadapatule (ngakhale wosauka ndi m’modzi yemwe ponena kuti uje timpatse, uje tisampatse, kapena sadanene kuti: “Ngati Allah afuna).”

    [19] “Mliri woopsa wochokera kwa Mbuye wako udauzinga (mundawo nthawi yausiku) iwo ali mtulo

    [20] “Choncho udakhala ngati wokololedwa (chifukwa cha mliri uja)

    [21] “Tero adaitanizana nthawi ya mbandakucha

    [22] ““Lawilirani kumunda wanu kuja ngati mukufuna kukolola (kuopera kuti angakuoneni osauka).”

    [23] “Adanyamuka uku akunong’ onezana

    [24] “(Akunena kuti): “Asakulowelereni wosauka lero mmenemo.”

    [25] “Ndipo adalawilira ali ndi chitsimikizo choti atha kuwamana (osauka)

    [26] “Choncho pamene adauona, adanena (uku akunjenjemera): “Ndithu ife tasokera (sikuno ayi, munda wathu uja siuno).”

    [27] ““Iyayi, ndiwomwewu; koma tamanidwa zinthu zake.”

    [28] “Wolungama mwa iwo adanena: “Kodi sindinakuuzeni (pamene mudali kulangizana zomana osowa) kuti bwanji osamkumbukira Allah (ndi kusintha cholinga chanu)?”

    [29] “(Iwo) adanena: “Alemekezeke Mbuye wathu ndithu ife tidali achinyengo (chifukwa cha kuipa kwa cholinga chathu).”

    [30] “Ndipo adatembenukirana ndikuyamba kudzudzulana

    [31] “Adati: “E chionongeko chathu! Ndithu Ife tidapyola malire (m’chinyengo chathu).”

    [32] ““Mwina Mbuye wathu angatipatse zabwino m’malo mwa munda wathuwu. Ndithu ife tikufunitsitsa kwa Mbuye wathu (chikhululuko Chake).”

    [33] “Umo ndi mmene chimakhalira chilango (Changa chomwe ndimachitsitsa pa dziko lapansi kwa amene chamuyenera); koma chilango cha tsiku lachimaliziro nchachikulu zedi, akadakhala akudziwa

    [34] “Ndithu oopa Allah adzakhala ndi Minda ya mtendere kwa Mbuye wawo

    [35] “Kodi tiwachite Asilamu monga ochimwa

    [36] “Kodi nchiyani chakupezani! Nanga mukuweruza bwanji (maweruzo opanda chilungamo)

    [37] “Kapena muli ndi buku limene mukuwerenga

    [38] “Kuti ndithu mulinazo mmenemo zomwe mukudzisankhira

    [39] “Kapena muli nawo mapangano ndi Ife okafika mpaka tsiku lachimaliziro akuti inu mudzapeza zimene mukudziweruzira

    [40] “Afunse (iwe Mtumiki) ndani mwa iwo amene ali mtsogoleri (pa malamulo amenewa)

    [41] “Kapena iwo ali nawo othandidzana nawo (pa mau awa)? Chomwecho atabweretsa othandizana nawo ngati akunena zowona

    [42] “(Akumbukire) tsiku la mavuto okhwima, ndipo adzaitanidwa (akafiri) kuti achite sijida (polambira Allah) koma sadzatha

    [43] “Maso awo adzangoti pansi zyoli, manyazi ndi kunyozeka kudzawaphimba; chikhalirecho adali kuitanidwa (pa dziko lapansi) kuti agwetse nkhope pansi pomwe iwo adali ndi moyo wa ngwiro (koma ankakana)

    [44] “Choncho ndisiye, (iwe Mtumiki), ndi amene akukanira nkhani iyi tiwakokera kuchilango pang’onopang’ono pamene iwo sakudziwa (mmene chiti chiwadzere chilangochi)

    [45] “Ndipo ndikuwalekelera (pochedwetsa chilango); ndithudi makonzedwe Anga ngokhwima, (palibe angapulumuke mmenemo)

    [46] “Kapena ukuwapempha malipiro (pofikitsa uthenga) kotero kuti iwo akulemedwa ndi kulipira

    [47] “Kapena ali nazo (nzeru) zobisika kotero kuti iwo akulemba (zimene akuweruzazo)

    [48] “Choncho pirira ndi lamulo la Mbuye wako (chifukwa chowalekelera ndi kuchedwetsa chipulumutso chako); ndipo usakhale ngati mwini nsomba (Yunusu pa changu ndi mkwiyo kwa anthu ake) pamene adaitana (Mbuye wake) uku ali wodzazidwa ndi mkwiyo (kupempha kuti chidze mwachangu chilango kwa anthu ake)

    [49] “Chikadapanda kumfikira chisomo chochokera kwa Mbuye wake (ndi kuvomera kulapa kwake), akadaponyedwa (kuchokera m’mimba mwa chinsomba chija) pagombe (popanda kanthu) ali wodzudzulidwa

    [50] “Koma adamsankha Mbuye wake (povomera kulapa kwake) ndipo adamchita kukhala mmodzi wa anthu abwino

    [51] “Ndithudi anthu amene sadakhulupirire adayandikira kukuteleretsa ndi kunyogodola kwa maso awo (chifukwa chachidani ndi mkwiyo) pamene adamva chikumbutso (Qur’an), ndipo akunena kuti iyeyo ngwamisala

    [52] “Ndipo ichi sichina, koma (ndi phunziro, ndi nzeru) ndi chikumbutso kwa zolengedwa zonse

    Zoona zenizeni

    Surah 69

    [1] “Chakudza cha choonadi (chomwe ndi Qiyâma)

    [2] “Kodi chakudza cha choonadi nchiyani

    [3] “Nanga nchiyani chikudziwitse za chakudza cha choonadicho

    [4] “Asamudu ndi Âdi adatsutsa zakudza kwa Qiyâma (yomwe idzadzidzimutsa zolengedwa mwamphamvu ndi zoopsa zake)

    [5] “Tsono Asamudu adaonongedwa ndi phokoso lopyola muyeso, (lamphamvu kwambiri)

    [6] “Ndipo Âdi adaonongedwa ndi chimphepo cha mkuntho, chozizira, champhamvu kwambiri

    [7] “Allah adachitumiza kwa iwo pa usiku usanu ndi uwiri ndi masana asanu ndi atatu mosadukiza; kotero ukadawaona ali lambalamba mmenemo ngati mathunthu a mitengo ya kanjedza yopanda kanthu m’kati mwake

    [8] “Kodi nanga ukumuona wotsala mwa iwo

    [9] “Ndipo Firiaun ndi amene adalipo iye asadabadwe, ndi khamu la anthu amidzi yotembenuzidwa (anthu a Luti) adadza ndi machimo (akulu)

    [10] “Ndipo (yense wa iwowa) adanyoza Mtumiki wa Mbuye wawo; choncho adawalanga chilango chopitilira muyeso

    [11] “Ndithu pamene madzi adasefukira mopyola muyeso (mpaka kumeza mapiri nthawi ya chigumula cha Nowa) Ife tidakukwezani mchombo choyandama ndi kuyenda

    [12] “Kuti tichichite (chochitikacho chomwe okhulupirira adapulumuka nacho; osakhulupirira adaonongeka nacho) kukhala lingaliro ndi phunziro kwa inu, ndikuti lisunge (nkhaniyi) khutu losunga

    [13] “Choncho likadzaimbidwa lipenga, kuimba kumodzi kokha (zamoyo zonse zidzafa)

    [14] “Ndipo nthaka ndi mapiri nkuchotsedwa m’malo mwake ndi kuphwanyidwa kamodzi nkamodzi

    [15] “Chomwecho tsiku limenelo, chochitika chidzachitika (imene ili Qiyâma)

    [16] “Ndipo thambo lidzasweka choncho ilo tsiku limenelo lidzakhala lofooka (pamene lidali lolimba)

    [17] “Ndipo angelo adzakhala m’mphepete mwake, ndipo pamwamba pawo tsiku limenero (angelo) asanu ndi atatu adzasenza Arsh (Mpando wachifumu) ya Mbuye wako

    [18] “Tsiku limenelo mudzabweretsedwa ku chiweruzo; sichidzabisika chilichonse chobisika mwa inu

    [19] “Tsono amene adzapatsidwa kaundula wake chakudzanja lakumanja kwake adzanena (mokondwa kwa amene ali m’phepete mwake): “Tengani! Werengani kaundula wanga!”

    [20] ““Ndithudi ine ndidatsimikiza (pa dziko lapansi) kuti ndidzakumana ndi chiwerengero changa.”

    [21] “Choncho, iye adzakhala m’moyo wosangalatsa

    [22] “M’munda wapamwamba

    [23] “Zipatso zake zoyandikira pansi (zosavuta kuzithyola)

    [24] “(Adzawauza kuti:) “Idyani, ndipo imwani mosangalala pa zimene mudatsogoza mmasiku aja adapita (a pa dziko lapansi).”

    [25] “Ndipo amene adzapatsidwe kaundula wake kudzanja lake lamanzere, adzanena (modandaula): “Kalanga ine! Ndiponi ndikadapanda kupatsidwa kaundula wangayu!”

    [26] ““Nkusadziwa chiwerengero changa!”

    [27] ““Ha! imfa ija ikadandimaliziratu (ndi kundilekanitsa ine ndi zimenezi).”

    [28] ““Chuma changa sichidandithandize!”

    [29] ““Mphamvu zanga (ndi moyo wanga wathanzi) zandichokera!”

    [30] “(Kudzanenedwa kwa angelo oyang’anira Jahena): Mgwireni ndipo mnjateni (pomphatikiza manja ndi khosi)

    [31] “Kenako mponyeni ku Moto

    [32] “Kenakonso mulowetseni mtcheni lotalika mikwamba makumi asanu ndi awiri

    [33] “Ndithudi, iye sadali kukhulupirira mwa Allah wamkulu

    [34] “Sadalinso kulimbikitsa zodyetsa osauka

    [35] “Basi, lero kuno alibe bwenzi (lomthandiza)

    [36] “Ngakhale chakudya kupatula mafinya (a anthu a ku Moto)

    [37] “Zomwe palibe angazidye kupatula ochimwa (mwadala)

    [38] “Choncho ndikulumbilira zimene mukuziona

    [39] “Ndi zimene simukuziona

    [40] “Ndithudi iyi (Qur’an) ndiliwu la mthenga wolemekezeka (Jibril)

    [41] “Ndipo simawu a mlakatuli, ndi zochepa zimene mukuzikhulupirira

    [42] “Ndiponso simawu a mlosi, ndizochepa zimene mmakumbukira

    [43] “(Ichi ndi) chivumbulutso chochokera kwa Mbuye wa zolengedwa

    [44] “Ndipo (Mneneri) akadatipekera bodza linalake

    [45] “Tikadamgwira (mwamphamvu) ndimkono wamanja

    [46] “Ndipo tikadadula mwa iye mtsempha wa moyo (kotero kuti ndikuferatu nthawi yomweyo)

    [47] “Sipakadapezeka aliyense mwa inu womteteza (kuchilango Chathu)

    [48] “Ndithu iyi (Qur’an) ndi phunziro labwino kwa owopa (Allah)

    [49] “Ndithu Ife, tikudziwa kuti ena mwa inu ndiotsutsa (Qur’an)

    [50] “Ndipo ndithu iyi (Qur’an) idzakhala chowadandaulitsa (chachikulu) osakhulupirira (pamene adzaona chilango chawo ndi mtendere wa okhulupirira)

    [51] “Ndithu iyoyi ndichoonadi Chotsimikizika; (mulibe chikaiko)

    [52] “Basi, lemekeza dzina la Mbuye wako Wamkulu (pitiriza kutamanda dzina Lake)

    Njira Zokwera

    Surah 70

    [1] “Wopempha adapempha kuti chiwadzere msanga chilango chopezekacho, (m’kupempha kwa chipongwe ndi kotsutsa)

    [2] “Kwa okanira palibe angachitsekereze

    [3] “Chochokera kwa Allah Mwini makwelero

    [4] “Angelo ndi Jiburil amakwera kwa Iye (Allah) m’tsiku lomwe kutalika kwake kuli ngati zaka zikwi makumi asanu

    [5] “Choncho, pirira (iwe Mtumiki (s.a.w) kupirira kwabwino

    [6] “Ndithu iwo akuliona (tsiku la Qiyâma) kuti lili kutali (silingachitike)

    [7] “Koma Ife tikuliona kuti lilipafupi (ndilochitika)

    [8] “Tsiku limene thambo lidzakhala ngati mtovu wosungunuka

    [9] “Ndipo mapiri adzakhala ngati ubweya (wongouluka wokha)

    [10] “Ndipo m’bale sadzafunsa za m’bale wake

    [11] “Ngakhale adzawalole kuti aonane ndi kudziwana pakati pawo (sadzafunsana). Wochimwa adzalakalaka kuti akadaziwombola ku chilango cha tsiku limenelo ndi ana ake

    [12] “Ndi mkazi wake, ndi m’bale wake

    [13] “Ndi akumtundu wake amene amamsunga

    [14] “Ndi (kulipira) zonse za m’dziko, kuti zimpulumutse

    [15] “Iyayi, (siya iwe wamachimo zimene ukulakalakazo)! Ndithu umenewu ndi Moto wa malawi

    [16] “Wosupula mwamphamvu khungu

    [17] “Udzaitana (potchula dzina la aliyense) amene adachitembenuzira msana choona ndi kunyoza

    [18] “Adasonkhanitsa (chuma) ndi kusunga (m’nkhokwe zake popanda kuperekera chopereka cha Allah)

    [19] “Ndithu munthu walengedwa kukhala wosapirira

    [20] “Mavuto akamkhudza amada nkhawa

    [21] “Koma zabwino zikamkhudza amamana (ena ndi kuiwala mavuto amene adali nawo)

    [22] “Kupatula opemphera Swala, (iwo alibe mbiri zoipazi)

    [23] “Iwo amene sadukiza mapemphero awo a swala; (sakuwaleka ngakhale zivute chotani)

    [24] “Ndi amene mchuma chawo muli gawo lodziwika (Zakaat)

    [25] “La wopempha ndi wosapempha

    [26] “Ndi amene akuvomereza za tsiku la malipiro (ndi kumalikonzekera)

    [27] “Ndi iwo amene akuopa chilango chochokera kwa Mbuye wawo

    [28] “Ndithu chilango cha Mbuye wawo nchosapulumuka nacho (munthu woipa)

    [29] “Ndiponso iwo amene akusunga umaliseche wawo (posachita chiwerewere)

    [30] “Kupatula kwa akazi awo ndi amene manja awo akumanja apeza; ndithu pazimenezo iwo sangadzudzulidwe

    [31] “Koma amene angafune (zina) kusiya zimenezi iwowo ndiwo olumpha malire

    [32] “Ndi iwo amene amasunga mwaubwino zimene amasungitsidwa ndi zimene alonjeza

    [33] “Ndi iwo amene amaima molungama popereka umboni wawo

    [34] “Ndiponso iwo amene amasunga (mwaubwino) mapemphero awo a swala

    [35] “Amene ali ndi mbiri zimenezi adzakhala m’Minda (yamtendere) ali olemekezedwa

    [36] “Kodi kuli chiyani kwa amene akana (chikhulupiliro) akuthamangira kwa iwe (maso ali pamtunda)

    [37] “Atakuzungulira ena chakumanja ena chakumanzere

    [38] “Kodi akulakalaka aliyense mwa iwo kuti akalowetsedwe ku Munda wamtendere

    [39] “Asiye (kukhumba kwawo kokalowa ku Munda wamtendere)! Ndithu Ife tidawalenga kuchokera m’zimene akudziwa (madzi opanda pake)

    [40] “Ndikulumbilira Mbuye wa kuvuma ndi kuzambwe konse ndithu Ndife Wokhoza

    [41] “Kuwasintha ndi kudzetsa abwino kuposa iwo; Ife palibe (chilichonse) chotipambana

    [42] “Asiye azingolankhula zopanda pake ndi kumangosewera mpaka adzakumane ndi tsiku lawo limene akulonjezedwa

    [43] “Tsiku limene adzatuluke m’manda uku akuthamanga (kudza kwa woitana) ngati kuti akuthamangira kumafano awo (amene adali kuwapembedza)

    [44] “Maso awo ali zyoli, (osatha kuwakweza); kuyaluka kutawaphimba! Limenelo ndilo tsiku lomwe adali kulonjezedwa (pomwe adali padziko lapansi)

    Nowa

    Surah 71

    [1] “Ndithu Ife tidamtuma Nuh kwa anthu ake, (ndikumuuza kuti): “Chenjeza anthu ako chisadawafike chilango chowawa.”

    [2] “Adanena (Nuh): “E inu anthu anga! Ndithu ine ndimchenjezi kwa inu woonekera poyera (wolongosola za uthenga wa Mbuye wanu m’chiyankhulo chimene mukuchidziwa).”

    [3] ““Mpembedzeni Allah ndipo rnuopeni ndikutinso mundimvere (pazimene ndikukulangizani).”

    [4] ““(Ngati mutero) adzakukhululukirani machimo anu ndi kukutalikitsirani moyo wanu kufikira m’nthawi imene yaikidwa (kuti ndiwo malire a kutalika kwa moyo). Ndithu nthawi ya Allah ikabwera siyichedwetsedwa (ngakhale pang’ono) mukadakhala mukudziwa.”

    [5] “Adanena (Nuh): “E Mbuye wanga! Ndithu ine ndaitanira anthu anga (ku chikhulupiliro) usiku ndi usana (popanda kufooka).”

    [6] ““Kuitana kwanga sikudaonjezere (chilichonse) koma kuthawa basi (kuchikhulupiliro Chanu).”

    [7] “Ndipo ine nthawi iliyonse ndikawaitanira (ku chikhulupiliro Chanu) kuti mwakhululukire, akuika zala zawo m’makutu mwawo (kuti asamve uthenga Wanu), ndipo akudziphimba ndi nsalu zawo (kuti asaone nkhope yanga), ndipo akupitiriza kukana kwawo ndi kudzikweza kwakukulu

    [8] “Kenaka ine ndawaitanira (kwa Inu) ndi mawu ofuula

    [9] “Kenakanso (ine ndawaitanira) molengeza poyera ndiponso mwachinsinsi mobisa

    [10] “Choncho ndidati (kwa anthu anga): Pemphani kwa Mbuye wanu chikhululuko (pa kukana kwanu ndi kutonza kwanu), ndithu Iye ali Wokhululuka kwambiri

    [11] “Akutumizirani mvula yotsika mochuluka

    [12] “Ndikukupatsani chuma ndi ana, (zomwe ndi zokongoletsa za dziko lapansi), ndi kukupangirani minda (yokongola) ndi kukupangirani mitsinje (yothilira mbewu zanu ndi kumwetsa ziweto zanu)

    [13] “Kodi chifukwa ninji simupereka ulemu kwa Allah (woyenera Umulungu Wake kuti akakuchitireni chifundo ndi kukupulumutsani ku chilango)

    [14] “Pomwe Iye adakulengani mnjira zosiyanasiyana; (madzi a umunthu, kenako magazi, kenako magazi ochindikala, kenako mafupa ndipo kenako mnofu)

    [15] “Kodi simudaone momwe Allah adalengera thambo zisanu ndi ziwiri mosanjikizana

    [16] “Ndi kuyika mwezi mthambomo kukhala kuunika, ndiponso kuyika dzuwa kukhala nyali

    [17] “Ndipo Allah adakulengani kuchokera m’nthaka monga mmera

    [18] “Kenako adzakubwezerani momwemo ndikudzakutulutsaninso (popanda cholepheretsa)

    [19] “Ndipo Allah wakupangirani nthaka kukhala ngati choyala

    [20] “Kuti muziyendayenda m’menemo m’njira zazikulu.”

    [21] “Adanena Nuh: “Mbuye wanga! Ndithu anthu anga andinyoza (pa zimene ndawalamula kuti akhulupirire Inu ndi kupempha chikhululuko chanu), ndipo (ofooka mwa iwo) amtsatira yemwe chuma chake ndi ana ake sizidzamuonjezera (chilichonse chabwino) koma kutaika (ndi kuonongeka pa tsiku lachimaliziro)

    [22] “Ndipo (eni chuma ndi ana) awatchera (otsatira awo) ndale zazikulu (ndi zopyola muyeso kuti asakhulupirire).”

    [23] “Ndipo adanena (kwa owatsatira awo): “Musasiye kupembedza milungu yanu; musamusiye Wadda, Suwaa’, Yaghutha, Ya’uqa ndi Nasra” (maina a mafano awo)

    [24] “Ndipo ndithu iwo asokeretsa (anthu) ambiri; ndipo musawaonjezere ochita zoipa (china chake) koma kusokera basi.”

    [25] “Chifukwa cha zochimwa zawo adamizidwa ndi kulowetsedwa ku Moto (waukulu woyaka); sadapeze owapulumutsa ndi kuwateteza m’malo mwa Allah

    [26] “Ndipo adanena Nuh (atataya mtima za anthu ake): “Mbuye wanga! Musasiye aliyense mwa osakhulupirira kukhala pa dziko.”

    [27] ““Ndithu Inu Mbuye wanga ngati muwasiya (popanda kuwaononga ndi kuwathetsa) asokeretsa akapolo anu (kunjira yolungama). Ndipo sangabereke (ana abwino) koma oipa; osakhulupirira (okhala kutali ndi choonadi, ndiponso onyoza Inu).”

    [28] ““Mbuye wanga! Ndikhululukireni ndi makolo anga, ndi aliyense walowa m’nyumba yanga ali okhulupirira ndi okhulupirira amuna ndi okhulupirira akazi. Ndipo musawaonjezere anthu achinyengo chinachake koma kuwaononga basi.”

    Majini

    Surah 72

    [1] “Nena (iwe Mtumiki (s.a.w), kwa anthu ako): “Kwavumbulutsidwa kwa ine kuti gulu la ziwanda lidamvetsera (kuwerenga kwanga kwa Qur’an) ndipo lidanena (kumtundu wawo): ndithu tamvetsera Qur’an yodabwitsa (ikuwerengedwa)

    [2] “Ikuitanira kuchilungamo, ndipo taikhulupirira. Ndipo sitimphatikiza aliyense ndi Mbuye wathu, (pa mapemphero)

    [3] “Ndipo ndithu ukulu ndi ulemelero wa Mbuye wathu watukuka; sadadzipangire mkazi kapena mwana

    [4] “Ndipo ndithu mbuli za mwa ife zakhala zikunenera Allah mawu abodza (okhala kutali ndi choonadi)

    [5] “Ndipo ndithu ife tinkaganiza kuti anthu ndi ziwanda sangamnenere Allah zabodza (zosayenera ulemelero Wake)

    [6] “Ndipo ndithu padali amuna a mu wanthu amapempha chitetezo kwa amuna amziwanda, ndipo adawaonjezera (amuna amziwanda) kupitiriza machimo (awo, kupulikira ndi kuchenjelera anthu)

    [7] “Ndipo ndithu iwo amaganiza monga momwe mumaganizira inu kuti Allah sadzaukitsa aliyense

    [8] “Ndithu ife tidafuna kukafika kumwamba; tidakupeza kutadzala alonda (angelo) amphamvu ndi zenje za moto

    [9] “Ndithu ife tidali kukhala m’menemo (kale) mokhala momvetsera; (mobera nkhani zakumwamba). Koma amene afune kumvetsera tsopano apeza chenje cha moto chikudikilira (kuti chimgwere iye ndi kumuononga)

    [10] “Ndithu ife sitikudziwa chilango chimene akuwafunira a m’dziko (polondera kumwamba, kuletsa kumvetsera nkhani zakumeneko); kapena Mbuye wawo akuwafunira zabwino ndi chilungamo (pa zimenezo)

    [11] “Ndithu ena mwa ife ndi abwino koma ena sali choncho. Tili njira zosiyanasiyana

    [12] “Ndithu ife tidadziwa kuti Allah sitingathe kumlepheretsa (lamulo Lake pa ife paliponse tingakhale) pa dziko lapansi, ndipo sitingamlepheretsenso pomzemba ndi kuthawira (kumwamba)

    [13] “Ndipo ife pamene tachimva chiongoko (Qur’an) tachikhulupirira ndipo amene ati akhulupirire mwa Mbuye wake saopa kumchepetsera (chabwino kapena kumuonjezera machimo ake)

    [14] “Ndithu mwa ife alipo Asilamu ndiponso mwa ife alipo opatuka (mu njira ya chilungamo); amene walowa m’Chisilamu, iwowo ndi amene alunjika njira ya choonadi

    [15] “Koma opatuka (kunjira ya chilungamo) adzakhala nkhuni za Jahannam.”

    [16] “Ndithu (anthu ndi ziwanda) akadalungama panjira ya chilungamo tikadawamwetsa madzi ambiri (okwanira nyengo zonse)

    [17] “Kuti tiwayese ndi zimenezo (mmene angamyamikire Allah pa mtendere Wake pa iwo). Koma amene anyozera kupembedza Mbuye wake, amlowetsa ku chilango chovuta (chimene sangathe kupirira nacho)

    [18] “Ndithu misikiti ndi ya Allah yekha! Choncho, musapembedze aliyense pamodzi ndi Allah

    [19] “Ndipo ndithu pamene adaima kapolo wa Allah (Muhammad{s.a.w}, pa Swala yake) uku akumpembedza (Allah), ziwanda zidatsala pang’ono kumgwera (chifukwa cha kuchuluka kwawo ndi kumzinga podabwa ndi zimene adaziona ndi kuzimva)

    [20] “Nena: “Ndikumpembedza Mbuye wanga M’modzi (Yekha) ndipo sindingamphatikize ndi aliyense (m’mapemphero Ake).”

    [21] “Nena: “Ine ndilibe udindo wokupatsani mavuto kapena chilungamo (ndi zabwino).”

    [22] “Nena: “Ine palibe anganditeteze ku chilango cha Allah (ngati nditamnyoza) sindingapeze malo (othawira kuchilango Chake) kupatula kwa Iye.”

    [23] ““Koma (mphamvu imene ndili nayo) ndikufikitsa uthenga wa Allah umene adanditumizira; ndithu amene anyoza Allah ndi Mtumiki Wake (ndi kupatuka pa chipembedzo cha (Allah) ndithu moto wa Jahannam ndi wake, akakhala m’menemo muyaya.”

    [24] “Mpaka pomwe adzaziona zimene alonjezedwa ndipamene adzadziwa (kuti) kodi ndani mwini mthandizi wofooka ndiponso wochepekedwa mchiwerengero (cha omtsatira, iwo kapena Asilamu).”

    [25] “Nena (kuti): “Sindikudziwa ngati zomwe mukulonjezedwa (za chilango) zili pafupi, kapena Mbuye wanga azitalikitsa.”

    [26] ““(Iye) ndi wodziwa zobisika; sazionetsa zobisika Zake kwa aliyense (mzolengedwa Zake),”

    [27] ““Kupatula Mtumiki (Wake) amene wamuyanja; (iyeyo amamdziwitsa zobisikazo) ndipo ndithu amamuikira alonda kutsogolo kwake ndi kumbuyo kwake (omulonda).”

    [28] ““Kuti adziwe ngati afikitsa uthenga wa Mbuye wawo, ndipo wawazungulira (podziwa zonse zili kwa iwo) ndipo wadziwa kuchuluka kwa zinthu zonse zimene zilipo; (palibe chobisika kwa Iye).”

    Wodzitukumula

    Surah 73

    [1] “E iwe wadzifunditsa (ndi nsalu)

    [2] “Imilira usiku (upemphere), kupatula nthawi yochepa

    [3] “Theka lake kapena chepetsa thekalo pang’ono (mpaka ufike chimodzi mwa zigawo zitatu za usiku)

    [4] “Kapena wonjezapo (mpaka ufike zigawo ziwiri mwa zigawo zitatu za usiku;) ndipo werenga Qur’an mofatsa (lemba ndi lemba)

    [5] “Ife tikuvumbulutsira iwe (Mneneri) mawu olemera (yomwe ndi Qur’an)

    [6] “Ndithu kudzuka usiku ndi kuchita mapemphero kumalowelera (mu mtima) kwambiri, ndipo zoyankhula zake zimakhala zoongoka ndi zolunjika bwino (kuposa mapemphero amasana)

    [7] “Ndithu masana uli ndi zochitachita zambiri; (umatanganidwa ndi ntchito yauthenga; dzipatse danga usiku polimbika kupemphera)

    [8] “Ndipo tchula dzina la Mbuye wako (Amene adalenga ndi kulera zinthu), ndipo udzipereke kwathunthu kwa Iye

    [9] “(Iye ndiye) Mbuye wa kuvuma ndi kuzambwe; palibe wopembedzedwa mwachoonadi koma Iye. Mchiteni kukhala Mtetezi (wanu pa zinthu zanu zonse)

    [10] “Ndipo pirira pa zimene akunena. Ndipo apewe (ndi mtima wako); kupewa kwabwino

    [11] “Ndisiye Ine ndi otsutsa eni kupeza bwino; ndipo alekelere kanthawi kochepa

    [12] “Ndithudi, tili ndi mitundumitundu ya unyolo ndi Moto woyaka

    [13] “Ndi chakudya chotsamwitsa ndi chilango chowawa

    [14] “Tsiku limene nthaka ndi mapiri zidzagwedezeka; (kugwedezeka kwa mphamvu kotero kuti) mapiri adzakhala ngati mulu wa mchenga woyoyoka

    [15] “Ndithu Ife takutumizirani Mthenga amene adzakhala mboni yanu (tsiku la chimaliziro; monga momwe tidamtumizira (Mûsa) kukhala Mtumiki kwa Firiauni

    [16] “Koma Firiauni adamnyoza Mtumikiyo; ndipo tidamulanga chilango chokhwima

    [17] “Kodi mungadzitchinjirize chotani ngati mukana (chilango cha) tsiku (lomwe) lidzachititsa ana kukhala ndi imvi

    [18] “Thambo (pamodzi ndi mphamvu zake ndi kukula kwake), lidzang’ambika (tsiku limenelo) chifukwa cha kuopsa kwa tsikulo, lonjezo la (Allah) lidzakwaniritsidwa (palibe wolipinga)

    [19] “Ndithudi, ma Ayah awa (amene akunena za kuwopsa kwa Qiyâma) ndichikumbutso. Choncho amene akufuna (kuthandizika nawo) ayende panjira ya Mbuye wake (pokwaniritsa malamulo Ake ndi kuleka zoipa)

    [20] “Ndithu Mbuye wako akudziwa kuti iwe ukuima (kupemphera) pafupifupi magawo awiri mwa magawo atatu a usiku kapena theka lake, kape’nanso gawo limodzi mwa magawo atatu a usiku, pamodzi ndi gulu la omwe uli nawo. Ndipo Allah ndi Amene amadziwa bwino muyeso wa (nthawi za) usiku ndi usana, wadziwa kuti simungathe kuwerengera zimenezo, choncho wakukhululukirani. Werengani ndime imene yapepuka yochokera m’Qur’an. Wadziwa kuti ena mwa inu adzakhala odwala; (kudzawavuta kuimilira ndi kuchezera usiku), ndipo ena adzakhala akuyendayenda pa dziko (ndi cholinga cha malonda ndi ntchito) kunka nafunafuna ubwino wa Allah. Ndipo ena adzakhala akumenya nkhondo pa njira ya Allah (ncholinga chotukula mawu Ake), werengani chimene chapepuka chochokera mmenemo (m’Qur’an). Ndipo pitirizani kupemphera Swala, perekani chopereka (chimene chakakamizidwa kwa inu). Ndipo mkongozeni Allah ngongole yabwino. Ndipo chilichonse chabwino chimene mwadzitsogozera mudzachipeza kwa Allah chili chabwino (kuposa zomwe mudazisiya m’mbuyo) ndi malipiro akulu zedi ndipo mpempheni Allah chikhululuko (pa uchimo wanu ndi chikhululuko pakunyozera kwanu kuchita zabwino). Ndithu Allah Ngokhululuka, Ngwachisoni chosatha

    Wodzibisa

    Surah 74

    [1] “E iwe wadziphimba (nsalu)

    [2] “Imilira ndipo uwachenjeze (anthu za chilango cha Allah)

    [3] “Ndipo Mbuye wako (Yekha) umkulitse (pomulemekeza)

    [4] “Ndipo nsalu zako uziyeretse (ndi madzi ku uve)

    [5] “Ndiponso zoipa (monga mafano ndi zina zonse ) zipewe

    [6] “Usapatse (anthu) ncholinga choti ulandire zambiri

    [7] “Chifukwa cha Mbuye wako, pirira (ku malamulo Ake poleka zomwe waletsa ndi kuchita zimene walamula)

    [8] “Ndipo likadzaimbidwa lipenga

    [9] “Tsiku limenelo lidzakhala tsiku lovuta

    [10] “Kwa osakhulupirira, silidzakhala lofewa

    [11] “Ndisiye ndiamene ndidamlenga Ndekha

    [12] “Ndipo ndampatsa chuma chambiri

    [13] “Ndi ana okhala nawo (paliponse)

    [14] “Ndipo ndamkonzera (ulemelero), kumkonzera (kwabwino)

    [15] “Kenako ali ndi dyera kuti ndimuonjezere (zina popanda kuthokoza)

    [16] “Koma sichoncho! Ndithu iye adali kutsutsa zizindikiro Zathu

    [17] “Ndidzamkakamiza kuchilango chovuta; (kukwera phiri la ku Moto limene sakatha kulikwera)

    [18] “Iye adalingalira (mu mtima mwake) ndi kukonza bwino (chonena chonyoza Qur’an)

    [19] “Choncho waonongeka! Adakonza bwanji (poinyoza Qur’an)

    [20] “Ndiponso waonongeka! Adakonza bwanji (poinyoza Qur’an)

    [21] “Kenako adayang’anayang’ana (nkhope za anthu)

    [22] “Kenakonso adachita tsinya ndikukwinya nkhope (kwambiri ndi mkwiyo)

    [23] “Kenakonso adanyoza choonadi ndi kudzikweza (posachivomereza)

    [24] “Adati: “Sichina ichi (Qur’an) koma ndi matsenga amene adalandiridwa (kuchokera kwa amatsenga akale)

    [25] “Sichina ichi koma ndi mawu a anthu!”

    [26] “Posachedwa ndimlowetsa ku ‘Saqara.’

    [27] “Nanga ndi chiyani chingakudziwitse za ‘Saqara?’

    [28] “(Ndi moto umene) siusiya (mnofu) ndiponso siusiya (fupa)

    [29] “Wopsereza ndi kudetsa khungu

    [30] “Kumeneko kuli khumi ndi asanu ndi anayi (alonda oyang’anira Motowo)

    [31] “Ndipo sitidaike oyang’anira ku Moto (kukhala anthu) koma angelo; ndipo sitidaike chiwerengero chawo koma ndimayesero kwa amene sadakhulupirire, kuti atsimikize amene adapatsidwa mabuku (zimene Qur’an ikunena za chiwerengero cha angelo a ku Moto) ndiponso kuti chionjezeke chikhulupiliro kwa amene akhulupirira, ndikuti asapeneke amene adapatsidwa mabuku pamodzi ndi okhulupirira. Ndiponso kuti amene m’mitima mwawo muli matenda (matenda achinyengo) komanso osakhulupirira anene: “Kodi Allah akulinganji pa fanizo limeneli?” Momwemo Allah akumulekelera kusokera amene wamfuna, ndipo akumuongola amene wamfuna ndipo palibe amene angadziwe magulu a nkhondo a Mbuye wako kupatula Iye mwini. (Kutchula moto ndi zam’kati mwake) sichina koma ndichenjezo kwa anthu

    [32] “Sichoncho; ndikulumbilira mwezi

    [33] “Ndi usiku pamene ukuchoka

    [34] “Ndi m’bandakucha pamene kukuyera

    [35] “Ndithu uwo, (moto wa Jahannam) ndi chimodzi mwa malodza akulu

    [36] “Ndi chenjezo kwa anthu

    [37] “Kwa yemwe wafuna mwa inu kutsogola (pochita zabwino zokamthandiza tsiku louka kwa akufa) kapena kutsalira (ndi za m’dziko)

    [38] “Mzimu uliwonse ukakhala chikole ndi zimene udachita

    [39] “Kupatula akudzanja lamanja (Asilamu amene adadzimasula okha potembenukira kwa Allah)

    [40] “(Iwo) adzakhala m’minda (yosasimbika kukongola kwake) akufunsana wina ndi mnzake

    [41] “Za anthu oipa

    [42] “(Kuti): “Nchiyani chakulowetsani ku Moto?”

    [43] “Adzanena: “Sitidali m’gulu la omwe adali kupemphera (Swala)

    [44] “Ndiponso sitidali kuwadyetsa masikini

    [45] “Koma tinkangomira (m’zachabe ndi zabodza) pamodzi ndi omira (m’menemo)

    [46] “Ndiponso tidali kutsutsa za tsiku la malipiro

    [47] “Mpaka imfa idatifika.”

    [48] “Choncho siwudzawathandiza uwomboli wa awomboli

    [49] “Kodi ali ndi chiyani iwo pakuti azinyozera chenjezoli (limene lili Qur’an)

    [50] “(Akuyenda mothamanga kuti asamve chenjezoli) ngati kuti iwo ndi mbidzi zothawa

    [51] “(Zimene) zikuthawa mkango

    [52] “Ati akufuna aliyense mwa iwo apatsidwe kalata zotambasulidwa (zimene zitsimikize uthenga wa Mneneri Muhammad{s.a.w)

    [53] “Sichoncho! Koma kuti iwo sakuopa tsiku lachimaliziro

    [54] “Sichoncho! Ndithu ichi (Qur’an) ndichikumbutso (chokwanira)

    [55] “Choncho amene wafuna achikumbukire (amene sakufuna ndizake)

    [56] “Ndipo sangakumbukire pokhapokha Allah atafuna. Iye ndiye Amene ali woyenera kumuopa, ndiponso ndiye Mwini kukhululukira (amene akumuopa)

    Kuwuka

    Surah 75

    [1] “Ndikulumbilira tsiku lachimaliziro

    [2] “Ndikulumbiliranso mzimu wodzidzudzula (pa cholakwa chimene wachita. Ndithu mudzaukitsidwa; mafupa anu omwazikana atasonkhanitsidwa)

    [3] “Kodi munthu akuganiza kuti Ife (Amene tidamlenga kuchokera popanda chilichonse) sitidzatha kusonkhanitsa mafupa ake (ofumbwa)

    [4] “Iyayi, Ife tikhoza (kutisonkhanitsa) ndi kutilongosola bwino timizere takunsonga kwa zala zake. (Mafupa ake ndiye osanena)

    [5] “Koma munthu akufuna kuti apitirize kuchimwa (mmasiku akudza) mtsogolo mwake

    [6] “Akufunsa (mwa chipongwe): “Kodi lidzakhala liti tsiku la chimaliziro?”

    [7] “Pamene maso adzangoti tong’oo (ndi mantha)

    [8] “Ndi kuchoka kuwala kwa mwezi

    [9] “Ndipo dzuwa ndi mwezi ndikusonkhanitsidwa

    [10] “Munthu adzanena tsiku limenelo: “Nkuti kothawira (chilangochi?)”

    [11] “(Adzauzidwa): “Iyayi, (iwe munthu) palibe pothawira (pako)!”

    [12] “Tsiku limenelo kobwerera (anthu) ndi kwa Mbuye wako basi

    [13] “Tsiku limenelo munthu adzauzidwa zochita zake zimene adazitsogoza ndi zimene adazichedwetsa

    [14] “Koma munthu adzadzichitira umboni yekha pa mzimu wake

    [15] “Ngakhale atapereka madandaulo ake (otani kuti apulumuke nawo sadzapulumuka)

    [16] “Usaigwedezere (Qur’an) lirime lako (pamene ikuvumbulutsidwa) kuti uifulumilire (kuiwerenga ndi kuisunga mu mtima)

    [17] “Ndithu ndiudindo wathu kuisonkhanitsa (mu mtima mwako) ndi kukhazikitsa kawerengedwe kake (palirime lako)

    [18] “Choncho pamene tikukuwerengera iwe tsatira kuwerenga kwakeko (uku uli chete)

    [19] “Kenako, ndithu ndiudindo Wathu kulongosola (zimene siukumvetsa)

    [20] “Iyayi koma mukukonda moyo wa pa dziko

    [21] “Ndipo mukusiya moyo wa tsiku lachimaliziro

    [22] “Nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zowala

    [23] “Zili kumuyang’ana Mbuye wawo

    [24] “Ndipo nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zoziya (zokhwinyata)

    [25] “Zikuyembekezeka kuti zilandira tsoka lodula msana

    [26] “Sichoncho! Pamene mzimu udzafika pa nthitimtima, (pomwe pakumana mafupa am’mapewa)

    [27] “Ndipo ndikunenedwa ndani angamchiritse

    [28] “Ndipo (iye mwini wake), nkutsimikiza kuti ndithu uku ndikusiyana (ndi dziko lapansi)

    [29] “Ndipo miyendo idzasanjikizana; (iyi ndi nthawi yochoka mzimu)

    [30] “Tsiku limenelo koperekedwa (anthu onse) nkwa Mbuye wako

    [31] “Ndipo sadakhulupirire komanso sadapemphere Swala (zisanu)

    [32] “Koma (m’malo mwake) adatsutsa ndi kunyoza

    [33] “Kenaka adapita kubanja lake (uku akuyenda) monyada

    [34] “Kuonongeka nkwako (iwe wotsutsa)! Kuonongeka zedi

    [35] “Ndiponso kuonongeka nkwako! kuonongeka zedi

    [36] “Kodi munthu akuganiza kuti angosiidwa chabe? (Sadzaweruzidwa)

    [37] “Kodi sadali dontho la umuna umene udafwamphukira (m’chiberekero)

    [38] “Kenako adakhala nthinthi (ntchintchi) ya magazi, ndipo adamlenga ndi kumlinganiza (monga munthu)

    [39] “Ndipo adalenga kuchokera mmenemo mitundu iwiri: mwamuna ndi mkazi

    [40] “Kodi (Iye amene adayambitsa chilengedwe choyambachi) sangathe kuwapatsa moyo akufa

    Nthawi

    Surah 76

    [1] “Ndithu munthu idampita nthawi yaitali kwambiri (asanauziridwe mzimu) pomwe sadali chinthu chotchulidwa

    [2] “Ndithu Ife tamlenga munthu kuchokera ku mbewu ya munthu yosakanikirana (ya mkazi ndi ya mwamuna) kuti timuyese mayeso (ndi malamulo Athu); choncho tidampanga kukhala wakumva ndi wopenya; (amve mawu a Allah ndi kuti aone zisonyezo Zake)

    [3] “Ndithu Ife tidamlongosolera njira yoongoka: kukhala wokhulupirira kapena wotsutsa (Zonse zili kwa iye)

    [4] “Ndithu Ife okana tawakonzera unyolo (wam’miyendo yawo) ndi magoli (am’manja ndi m’makosi awo) ndi Moto waukali woyaka

    [5] “Ndithu ochita zabwino adzamwa vinyo, chosakanizira chake chidzakhala (madzi a) kaafura

    [6] “(Kaafura ameneyo) ndikasupe amene adzikamwapo akapolo a Allah ndi kumtulutsa (paliponse pamene afuna) kumtulutsa mofewa

    [7] “(Amene) akukwaniritsa zimene adalonjeza (okha kwa Allah), ndiponso akuopa tsiku (lalikulu) limene zoipa zake zidzakhala zofalikira ponseponse

    [8] “Ndipo amadyetsa chakudya masikini, amasiye ndi ogwidwa pa nkhondo, pomwe iwo akuchifunanso

    [9] “Amanena (chamumtima akamapereka chakudyacho): “Tikukudyetsani chifukwa chofuna chikondi cha Allah basi; sitikufuna kwa inu malipiro kapena kuthokoza

    [10] “Ndithu ife tikuopa kwa Mbuye wathu tsiku lokhwinyata nkhope ndi mavuto akulu.”

    [11] “Ndipo Allah adzawateteza mu mavuto a tsiku limenelo ndiponso adzawapatsa mtendere ndi chisangalalo

    [12] “Ndipo adzawalipira chifukwa cha kupirira kwawo Munda wamtendere ndi nsalu zaveleveti

    [13] “Atatsamira m’menemo pa makama (amtengo wapatali); sadzamva m’menemo kutentha kwa dzuwa kapena kuzizira

    [14] “Mithunzi yake ikawayandikira iwo ndipo mikoko yazipatso idzatewa pafupi (moti munthu atha kuthyola ali chigonere)

    [15] “Ndipo adzakhala akuzunguliridwa (ndi otumikira) uku atatenga zomwera za siliva ndi matambula onyezimira ndiponso olangala

    [16] “Zolangala zopangidwa ku siliva, atalinga bwino zakumwazo (malinga ndi kufuna kwawo)

    [17] “Ndipo (anthu abwino) akamwetsedwa kumeneko vinyo, chosakanizira chake chikafanana ndi Zanjabila (chikasu)

    [18] “M’menemo muli kasupe wotchedwa Salisabila

    [19] “Ndipo azikawazungulira anyamata osasinthika (chilengedwe chawo,) utawaona (chifukwa cha kukongola kwawo ndi kuwala kwa nkhope zawo) ungawaganizire kuti ndi ngale zomwazidwa

    [20] “Ndipo ukadzaona kumeneko (ku Jannah) ukaona mtendere ndi ufumu waukulu

    [21] “Pamwamba pawo padzakhala nsalu zaveleveti zopyapyala, zobiriwira ndi nsalu zaveleveti zochindikala, akavekedwa m’manja mwawo zibangiri zasiliva; Mbuye wawo akawamwetsa chakumwa china choyera kwambiri

    [22] “(Akawauza kuti:) “Ndithu iyi ndi mphoto yanu ndipo ntchito zanu ndi zolandiridwa.”

    [23] “Ndithu Ife taivumbulutsa kwa iwe Qur’an mwapang’onopang’ono (kuti uisunge bwino, usaiwale)

    [24] “Choncho, pirira ndi lamulo la Mbuye wako ndipo usamvere wamachimo kapena wokanira aliyense mwa iwo

    [25] “Ndipo kumbukira dzina la Mbuye wako; mmawa, ndi madzulo (Swala za Subuhi, Dhuhr ndi Asri)

    [26] “Ndipo usiku mlambire Iye, (Swala ya Maghrib ndi Isha); ndiponso umulemekeze usiku nthawi yaitali (popemphera sunna za tahajjudi)

    [27] “Ndithu awa akukonda moyo wa dziko lapansi, ndipo akulisiya kumbuyo kwao tsiku lovuta

    [28] “Ife ndi amene tidawalenga ndipo tidalimbika kalengedwe kawo; ndipo titafuna tingabweretse ena onga iwo (omvera Allah) kulowa m’malo mwawo

    [29] “Ndithu ichi ndichikumbutso choncho amene afuna atsata njira yopitira kwa Mbuye wake (pomukhulupirira ndi kumumvera)

    [30] “Koma simungafune nokha chilichonse pokhapokha atafuna Allah, ndithu Allah ndi Wodziwa zedi, Wanzeru zakuya

    [31] “Akumlowetsa amene wamfuna ku chifundo Chake; koma oyipa wawalinganizira chilango chowawa kwambiri

    Othenga

    Surah 77

    [1] “Ndikulumbilira mphepo yomwe ikuomba motsatizana

    [2] “Ndi mphepo yamkuntho ikamakuntha

    [3] “Ndi mphepo yobalalitsa mitambo ndi mvula

    [4] “Ndi ma Ayah osiyanitsa pakati pachoona ndi chonama

    [5] “Ndi angelo opereka chivumbulutso kwa aneneri

    [6] “Kuti chichotse madandaulo kapena chikhale chenjezo

    [7] “Ndithu zimene mukulonjezedwa (kuti chimaliziro chidzakhalapo) zidzachitikadi (popanda chipeneko)

    [8] “Pamene nyenyezi zidzafafanizidwa (kuwala kwake ndi kuchotsedwa m’malo mwake)

    [9] “Ndiponso pamene thambo lidzang‘ambidwa

    [10] “Ndi pamenenso mapiri adzachotsedwa m’malo mwake ndi kuperedwa (kukhala fumbi)

    [11] “Ndi pamene atumiki adzasonkhanitsidwa pa nthawi yake, (kuti apereke umboni ku mibadwo yawo)

    [12] “Kodi nditsiku lanji azichedwetsera (zinthu zikuluzikulu kuti zidzachitike)

    [13] “Nditsiku loweruza (pakati pa zolengedwa)

    [14] “Nchiyani chingakudziwitse za tsiku la chiweruzirolo

    [15] “Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo Lathu lakuuka ku imfa)

    [16] “Kodi sitidawaononge (anthu) akale (chifukwa cha machimo awo, monga anthu a Nuh, Âdi ndi Samudu)

    [17] “Kenako titsatiza ena (okana Allah m’kuonongekako monga tidawachitira oyamba)

    [18] “Chomwecho tiwachitiranso ochimwa

    [19] “Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo Lathu lakuuka ku imfa)

    [20] “Kodi sitidakulengeni kuchokera ku madzi onyozeka, (madzi ambewu ya munthu)

    [21] “Kenako tidawaika pamalo okhazikika (kuti chilengedwe chake chikwanire pamenepo)

    [22] “Mpaka nyengo yodziwika (imene tidaipima kuti mwana abadwe)

    [23] “Tidaipima nyengoyo; taonani kupima bwino Ife opima

    [24] “Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo Lathu lakuuka ku imfa)

    [25] “Kodi sitidaichite nthaka kukhala yofungatira

    [26] “Amoyo ndi akufa

    [27] “Ndipo tidaika m’menemo mapiri ataliatali (olimbitsa nthaka), ndipo takumwetsani madzi okoma

    [28] “Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo Lathu lakuuka ku imfa)

    [29] “(Kudzanenedwa kwa okana tsiku la chimaliziro:) Pitani kuzimene mudali kuzitsutsa zija

    [30] “Pitani kumthunzi (wautsi wa ku Moto) wa nthambi zitatu

    [31] “Simthunzi (wamtendere) ndiponso siwotchinjiriza ku malawi a Moto.”

    [32] “Ndithu motowo umaponya mphalikira (mbaliwali) zazikulu ngati nyumba

    [33] “Zonga ngati ngamira zachikasu

    [34] “Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (zimenezi)

    [35] “Ili ndi tsiku lomwe sadzayankhula

    [36] “Ndipo sadzapatsidwa chilolezo (choyankhulira) kuti apereke madandaulo awo

    [37] “Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (za tsiku limenelo)

    [38] “(Adzauzidwa kuti): Ili ndi tsiku loweruza (pakati pa abwino ndi oipa takusonkhanitsani inu (otsutsa Muhammad {s.a.w}), ndi akale (otsutsa aneneri akale)

    [39] “Ngati muli ndi ndale (yodzipulumutsira ku chilango Changa) ndichiteni ndaleyo

    [40] “Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (lonjezo la Allah)

    [41] “Ndithu oopa (Allah tsiku limenelo) adzakhala mu mthunzi ndi mitsinje

    [42] “Ndipo adzakhala ndi zipatso zomwe azidzazifuna

    [43] “(Kudzanenedwa kwa iwo): “Idyani, imwani mokondwa chifukwa cha zabwino zomwe mudali kuchita (mu moyo wa dziko lapansi)

    [44] “Ndithu umo ndi mmene Ife timawalipirira ochita zabwino

    [45] “Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (mtendere wa Allah)

    [46] “Idyani, sangalalani pang’ono m’kanthawi kochepa; ndithu inu ndinu ochimwa (chifukwa chakumphatikiza Allah ndi zolengedwa)

    [47] “Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (mtendere wa Allah)

    [48] “Ndipo kukanenedwa kwa iwo: “Weramani, (pembedzani Allah).” sawerengera

    [49] “Kuonongeka kwakukulu tsiku limenelo kuli pa otsutsa (malamulo a Allah)

    [50] “Kodi ndi nkhani iti imene adzaikhulupirira pambuyo pa Iyi (Qur’an)

    Nkhani

    Surah 78

    [1] “۞ Kodi akufunsana zachiyani

    [2] “Za nkhani yayikulu ija

    [3] “Imene iwo akusiyana (maganizo)

    [4] “Aleke (zimenezo) adzadziwa posachedwapa

    [5] “Ayi, ndithu aleke (zimenezo); posachedwapa adzadziwa zoona zake (pamene chilango chidzawatsikira)

    [6] “Kodi sitidachite nthaka kukhala ngati choyala

    [7] “Ndi mapiri ngati zichiri (zolimbitsa nthaka)

    [8] “Ndipo takulengani mitundu iwiri (amuna ndi akazi)

    [9] “Ndipo tidachita tulo tanu kukhala mpumulo (ku mavuto a ntchito)

    [10] “Ndipo taupanga usiku kukhala ngati chovala (pokuvindikirani ndi mdima wake)

    [11] “Ndipo tapanga masana kukhala nthawi yopezera zofunika pa moyo

    [12] “Ndipo tamanga pamwamba panu thambo zisanu ndi ziwiri zolimba

    [13] “Ndipo tidapanga nyali yowala ndi yotentha kwambiri (dzuwa)

    [14] “Ndipo tawatsitsa madzi otsika mwamphamvu kuchokera ku mitambo, ya mvula

    [15] “Kuti titulutse ndi madziwo mbewu ndi m’mera, (chomwe ndi chakudya cha anthu ndi nyama)

    [16] “Ndi minda yothothana nthambi za mitengo

    [17] “Ndithu tsiku la chiweruziro ndinthawi imene idakhazikitsidwa kale

    [18] “Tsiku limene lipenga (lakuuka) lidzaimbidwa ndipo inu mudzabwera (kubwalo losonkhanirana) muli magulumagulu

    [19] “Ndipo thambo lidzatsegulidwa (mbali zonse): choncho lidzakhala makomomakomo

    [20] “Ndipo mapiri adzachotsedwa m’malo mwake, adzakhala ngati zideruderu

    [21] “Ndithu moto wa Jahannam ukuwadikilira (oipa)

    [22] “Mbuto ya opyola malire

    [23] “Adzakhala m’menemo muyaya

    [24] “Sadzalawa m’menemo kuzizira (kowachotsera kutentha), kapena chakumwa (chowachotsera ludzu lawo)

    [25] “Kupatula madzi otentha kwambiri ndi mafinya (otuluka mmatupi a anthu a ku Moto)

    [26] “Kukhala malipiro olingana ndi ntchito zawo

    [27] “Ndithu iwo sadali kuyembekezera chiwerengero (cha Allah)

    [28] “Adatsutsa zizindikiro Zathu (zosonyeza kuuka kwa akufa) ndi mtsutso waukulu

    [29] “Ndipo chinthu chilichonse tachisunga mochilemba

    [30] “Basi, lawani (lero chilango Changa); sitikuonjezerani chinthu china koma chilango pamwamba pa chilango

    [31] “Ndithu anthu oopa Allah adzakhala ndi malo wopambana

    [32] “Minda ndi zipatso za mphesa

    [33] “Ndi mabuthu (anamwali) ofanana misinkhu

    [34] “Ndi zipanda zodzaza ndi zakumwa

    [35] “Sakamva m’menemo mawu opanda pake kapena bodza

    [36] “Amenewa ndi malipiro ochokera kwa Mbuye wako zopereka zokwanira

    [37] “Mbuye wa kumwamba ndi pansi ndi zimene zili pakati pake; Wachifundo chambiri. Palibe amene adzakhala ndi mphamvu yolankhulana naye (pa tsiku limenero)

    [38] “Tsiku limene adzaima Jibril ndi angelo pa mzere (ali odzichepetsa); sadzayankhula aliyense mwa iwo kupatula yekhayo amene adzaloledwa ndi (Allah) Wachifundo chambiri (kuyankhula) ndipo adzanena zolondola

    [39] “Limenelo ndi tsiku loona, (lopanda chikaiko); choncho amene akufuna adzipezere malo (njira yonkera) kwa Mbuye wake. (Pomugonjera Iye pa moyo uno wadziko lapansi)

    [40] “Ndithu tikukuchenjezani zachilango chomwe chili pafupi kudza; tsiku limene munthu adzayang’ana zimene adatsogoza manja ake, ndipo wosakhulupirira adzanena: Kalanga ine! Ndikadakhala dothi, (kuti ndisalangidwe chilango chikundiyembekezachi)

    Amene akukoka

    Surah 79

    [1] “Ndikulumbilira (angelo) amene amazula mwamphamvu (mizimu ya osakhulupirira)

    [2] “Ndikulumbiliranso (angelo) amene amachotsa moleza (mizimu ya okhulupirira)

    [3] “Ndi omwe amasambira (nayo mizimuyo) mu mlengalenga (ponka nayo ku malo ake oyembekezera)

    [4] “Ndi iwo amene akupikisana pokwaniritsa malamulo a Allah

    [5] “Ndi iwo (angelo) amene akulongosola malamulo (Ake). (Ndithudi inu anthu mudzauka kwa akufa)

    [6] “Patsiku lomwe (lipenga loyamba lidzaimbidwa), dziko lapansi ndi mapiri ake zidzagwedezeka (ndipo aliyense adzafa)

    [7] “Ndipo kudzatsatira kuyimba kwa lipenga lachiwiri (kumene kudzaukitsa akufa onse)

    [8] “Tsiku limenelo mitima idzanjenjemera ndi kuopa

    [9] “Maso a eni mitimayo adzakhala ozyolika (chifukwa chamadandaulo)

    [10] “(Osakhulupirira) akunena: “Kodi nzoona tidzabwezedwa pambuyo pa imfa monga tidalili kale?”

    [11] ““Pomwe ife titakhala mafupa ofumbwa (tingabwezedwe ndi kuukitsidwa mwa tsopano)?”

    [12] “Adanena (mokanira ndi mwachipongwe): “Choncho kubwerera kumeneko ngati kudzakhalepodi kudzakhala kotaika (ndi kopanda phindu kwa ife. Pomwe ife sindife oyenera kutaika).”

    [13] “(Musaganize kubwererako nchinthu chovuta). Ndithundithu Kiyamayo ndi nkuwo umodzi

    [14] “Mwadzidzidzi (zolengedwa zonse) zidzangoona zili pa dziko latsopano (zili zamoyo)

    [15] “Kodi yakufika (iwe Mtumiki) (s.a.w) nkhani ya Mûsa

    [16] “Pamene Mbuye wake adamuitana pa chigwa choyera (chotchedwa) Tuwaa

    [17] “(Adamuuza kuti) pita kwa Farawo ndithu iye wapyola malire, (mkudzitukumula kwake ndikupondereza anthu)

    [18] “Choncho ukamuuze kuti: “Kodi ukufuna kudziyeretsa?”

    [19] ““Ndikuti ndikuongolere kwa Mbuye wako kuti uzimuopa?”

    [20] “(Basi Mûsa) adamuonetsa (Farawo) chozizwitsa chachikulu

    [21] “Koma (Farawo) adatsutsa (Mûsa pazimene adadza nazo zija) ndi kunyoza

    [22] “Kenaka adabwerera uku akulimbika kutsutsana naye (Allah)

    [23] “Adawasonkhanitsa (afiti) uku akuitana anthu

    [24] “Nanena: “Ine ndine mbuye wanu wapamwambamwamba!”

    [25] “Pamenepo Allah adamulanga chifukwa cha mawu ake omaliza ndi oyamba

    [26] “Ndithu pa zimenezi pali phunziro (lalikulu) kwa yemwe akuopa Allah

    [27] “Kodi kulengedwa kwanu, (inu osakhulupirira kuti muuke) nkovuta kapena thambo limene adalimanga (posonkhanitsa mbali zake zosiyanasiyana ndikukhala chinthu chimodzi)

    [28] “Adatukula nsinkhu wake ndikulikonza bwino (popanda pena pong’ambika kapena posiyana ndi pena)

    [29] “Ndipo amauvindikira usiku wake ndi mdima ndipo amatulutsa kuwala wake

    [30] “Ndipo pambuyo pazimenezo, nthaka adaiyala (kuti ikhale yoyenera kuikhala)

    [31] “Adatulutsa m’menemo madzi ake (potulutsa akasupe) ndikumeretsa msipu wake

    [32] “Ndipo mapiri adawakhazikitsa (ndikuwalimbika)

    [33] “(Adachita zonsezi) chifukwa chokusangalatsani inu ndi ziweto zanu

    [34] “Choncho likadzafika tsoka lalikulu (tsiku la Qiyâma)

    [35] “Tsiku limenelo munthu adzakumbukira zimene adachita, (zabwino ndi zoipa)

    [36] “Ndipo Moto waukali udzawonetsedwa kwa yense openya

    [37] “Tsono amene adapyola malire (pochita machimo)

    [38] “Ndikudzisankhira (yekha) moyo wa pa dziko lapansi

    [39] “Ndithu Jahannam ndiwo malo ake

    [40] “Tsono amene akuopa kuti adzaimilira pamaso pa Mbuye wake, nauletsa mtima wake ku zilakolako zoipa

    [41] “Ndithu Munda wamtendere ndiwo adzakhale malo ake

    [42] “Akukufunsa (iwe Mtumiki) (s.a.w) za nthawi (ya tsiku lachimaliziro kuti): “Idzakhala liti?”

    [43] “Uli ndi mphamvu yanji iwe yofotokozera za tsikulo? (Iwe ulibe kuzindikira za nthawiyo kotero kuti ungaitchule kwa iwo)

    [44] “Kwa Mbuye wako ndiko kuli mathero ake

    [45] “Iwe (ntchito yako) ndikuwachenjeza amene akuiopa; (osati kulengeza zanthawi yake)

    [46] “Tsiku limene adzaiona adzakhala ngati sadakhale (pa dziko nthawi yayitali), koma ngati madzulo amodzi kapena masana ake (nthawi ya m’mawa)

    Anakwiya

    Surah 80

    [1] “Adachita tsinya (Mneneri) ndi kuyang’ana kumbali

    [2] “Chifukwa chakuti adamdzera wakhungu (kudzamfunsa zokhudzana ndi chipembedzo chake pamene iye adali kuyankhula ndi atsogoleri Achiquraishi)

    [3] “Nanga chingakudziwitse nchiyani kuti mwina iye angadziyeretse (pomvera ulaliki wako watsopano)

    [4] “Kapena akumbukira, ndipo kukumbukirako kumthandiza

    [5] “Koma amene wadzikwaniritsa (ndi chuma chake ndi mphamvu zake)

    [6] “Ameneyo ndi yemwe ukumchitira chidwi

    [7] “Palibe chilichonse pa iwe ngati sadziyeretsa

    [8] “Koma amene wakudzera uku akuthamanga (kufuna maphunziro ndi chiongoko)

    [9] “Ndipo iye akuopa (Allah mu mtima mwake)

    [10] “Za iye, iwe sukusamala, (ukuyikira chidwi kwa wina)

    [11] “Sichoncho! Ndithudi iyi (Qur’an) ndi chikumbutso (chenjezo)

    [12] “Basi, amene wafuna alangizika (ndi Qur’an, ndipo amene sakufuna msiye)

    [13] “(Malangizowa akuchokera) mmakalata olemekezeka (kwa Allah)

    [14] “Apamwamba ndiponso oyeretsedwa (kumbiri iliyonse yopunguka)

    [15] “Omwe ali m’manja mwa Alembi (Angelo)

    [16] “Olemekezeka, omvera

    [17] “Waonongeka (watembeleredwa) munthu. Nkotani kusayamika kwake kotereku

    [18] “Kuchokera mchinthu chanji chimene iye adamulenga

    [19] “Kuchokera ku dontho lamadzi (onyozeka) adamulenga, namkonzeratu mkalengedwe kosiyanasiyana

    [20] “Kenako adamfewetsera njira (yotulukira m’mimba mwa mai ake)

    [21] “Ndipo amamchititsa kuti amwalire namukumbula m’manda

    [22] “Kenako akadzafuna adzamuukitsa (pambuyo pa imfa)

    [23] “Ayi ndithu (munthu) sanakwaniritsebe zimene adamulamula Mbuye wake (Allah chingakhale wakhala nthawi yaitali pa dziko lapansi)

    [24] “Alingalire munthu (mmene chilili) chakudya chake

    [25] “Ndithu Ife timagwetsa mvula yambiri (kuchokera ku mitambo)

    [26] “Kenako timaing’amba nthaka kuti mmera utuluke

    [27] “Ndipo timameretsa m’menemo njere (ya chakudya cha anthu ndi zina zimene amasunga mnkhokwe)

    [28] “Ndi mphesa ndi msipu

    [29] “Ndi mzitona (wabwino) ndi (zipatso za) kanjedza

    [30] “Ndi minda yothothana nthambi za mitengo

    [31] “Ndi zipatso (zodyedwa ndi anthu) ndi msipu (wodyedwa ndi nyama)

    [32] “(Tazimeretsa zimenezo kuti) zikondweretse inu ndi ziweto zanu

    [33] “Choncho likadzafika lipenga logonthetsa mkhutu (ndi kuumitsa makosi)

    [34] “Patsikuli munthu adzathawa m’bale wake

    [35] “Mayi wake ndi bambo wake

    [36] “Mkazi wake ndi ana ake

    [37] “Munthu aliyense mwa iwo, tsiku limenelo adzakhala ndi zakezake zotangwanika nazo. (Sadzalabadira za anzake)

    [38] “Tsiku limenelo nkhope zina zidzakhala zowala

    [39] “Zosekelera ndi zachimwemwe (chifukwa cha nkhani yabwino ya ku Munda wamtendere)

    [40] “Ndipo nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zokutidwa ndi fumbi

    [41] “Mdima udzazikuta

    [42] “Iwo ndi anthu osakhulupirira oipa (olakwira Allah)

    Kugwetsa

    Surah 81

    [1] “Pamene dzuwa lidzakulungidwe (ndikuchotsedwa kuwala kwake)

    [2] “Ndi pamene nyenyezi zidzathothoke (ndi kuchoka dangalira lake)

    [3] “Ndi pamene mapiri adzayendetsedwe (kuchoka mmalo mwake)

    [4] “Ndi pamene ngamira zabere lamiyezi khumi zidzasiidwe (zopanda oziyang’anira)

    [5] “Ndi pamene nyama za mtchire zidzasonkhanitsidwe pamodzi (kuchokera mmalo osiyanasiyana chifukwa chakuopsa kwakukulu kwa tsikulo)

    [6] “Ndi pamene nyanja zidzayatsidwe moto

    [7] “Ndi pamene mizimu idzalumikizidwe (ndi matupi ake)

    [8] “Ndi pamene mwana wamkazi yemwe adaikidwa m’manda wamoyo adzafunsidwe

    [9] “Ndi tchimo lanji adaphedwera

    [10] “Ndi pamene makalata (momwe mudalembedwa zochita za aliyense) adzatambasulidwe ndi kugawidwa (kuti awerengedwe)

    [11] “Ndi pamene thambo lidzayalulidwe (kuchoka mmalo mwake)

    [12] “Ndi pamene Jahena idzasonkhezeredwe mwamphamvu

    [13] “Ndi pamene Jannah idzayandikitsidwe

    [14] “(Zikadzachitika zimenezi) mzimu uliwonse udzadziwa zimene wabweretsa (zabwino ndi zoipa)

    [15] “Ndikulumbilira nyenyezi zimene zimabwerera masana ndi kutulukanso usiku

    [16] “Zomwe zimayenda kenako nkubisika

    [17] “Ndi usiku pamene ukulowa

    [18] “Ndi m’mawa kukamacha

    [19] “Ndithu iyi (Qur’an) ndi liwu la mthenga wa Allah (Jibril) wolemekezeka

    [20] “Mwini mphamvu ndi mwini ulemelero kwa Mwini Arsh (Mpando wa chifumu)

    [21] “Womveredwa kumeneko ndiponso wokhulupirika (pachivumbulutso)

    [22] “Ndipo m’bale wanuyu siwamisala ayi

    [23] “Ndithu ndikulumbira kuti (iye Mtumiki) (s.a.w) adamuona (Jibril) mchizimezime (chakum’mawa) chooneka bwino

    [24] “Ndipo sali iye (Mtumiki) waumbombo ndi chivumbulutso (koma amafikitsa zonse ndi kuziphunzitsa kwa anthu)

    [25] “(Chivumbulutso chomwe chavumbulutsidwachi kwa iye) si mawu a satana wothamangitsidwa (mchifundo cha Allah)

    [26] “Nanga mukupita kuti

    [27] “(Qur’ani) iyi sichina koma ndi chikumbutso cha zolengedwa zonse

    [28] “Kwa yemwe mwa inu akufuna kuyenda mu njira yoongoka

    [29] “Ndipo simungafune chinthu mwa inu nokha pokhapokha atafuna Allah Mbuye wa zolengedwa zonse

    Kugawanika

    Surah 82

    [1] “Pamene thambo lidzasweke

    [2] “Ndi pamene nyenyezi zidzayoyoke (ndi kumwazikana)

    [3] “Pamenenso nyanja zikuluzikulu zidzaphwasulidwe

    [4] “Ndiponso pamene manda adzafukulidwe (ndikutuluka akufa omwe adali mmenemo)

    [5] “(Panthawiyo) mzimu uliwonse udzadziwa zimene udatsogoza (zabwino ndi zoipa) ndi zimene udasiya m’mbuyo

    [6] “E iwe munthu! Nchiani chakunyenga kumsiya Mbuye wako wa ufulu (kufikira pomnyoza)

    [7] “Amene adalenga iwe nakulinganiza (ziwalo zako) ndi kukulongosola (moyenera)

    [8] “Ndipo maonekedwe amtundu uliwonse omwe adawafuna adakuveka (popanda chifuniro chako)

    [9] “Ayi, sichoncho! Koma inu mukutsutsa za (tsiku) lamalipiro

    [10] “Ndithu pa inu alipo okuyang’ anirani

    [11] “Olemekezeka, olemba (zochita zanu)

    [12] “Akudziwa (zonse) zimene mukuchita (zabwino ndi zoipa)

    [13] “Ndithudi ochita zabwino adzakhala mu mtendere

    [14] “Ndipo ndithu amene ali olakwira malamulo a Allah adzakhala ku Moto wopsereza

    [15] “Adzaulowa tsiku la malipiro

    [16] “Ndipo iwo kumeneko sadzachokako

    [17] “Kodi nchiyani chingakudziwitse za tsiku la malipiro

    [18] “Ndipo nchiyani chingakudziwitse za tsiku lamalipiro

    [19] “Limeneli ndi tsiku limene mzimu uliwonse sudzakhala ndi mphamvu (yodzetsa mtendere kapena yochotsa chovuta) pa mzimu wina. Ndipo lamulo pa tsiku limeneli ndi la Allah yekha

    Kusalungama

    Surah 83

    [1] “Kuonongeka koopsa kukawapeza opunguza miyeso ya malonda

    [2] “Amene amati akamadziyezera zinthu kwa anthu amafuna kulandira miyeso yodzadza

    [3] “Koma pamene iwo akamawayesera pa muyeso wa mbale kapena wa sikelo amapungula (choyenera kulandira ogulawo)

    [4] “Kodi amenewa (akupungula miyeso pamalondawo) sakuganiza kuti adzaukitsidwa

    [5] “Pa tsiku lalikulu (ndiponso loopsa)

    [6] “Tsiku limene adzaimilira anthu pamaso pa Mbuye wa zolengedwa

    [7] “Ayi! Ndithu (siyani chinyengo pamalonda ndi kusalabadira kuuka mmanda); zolembedwa za ntchito ya oipa zili mu Sijjin

    [8] “Nanga nchiyani chitakudziwitse za Sijjin

    [9] “Ameneyu ndi kaundula wamkulu yemwe walembedwa (mkati mwake ntchito za anthu oipa)

    [10] “Chilango chaukali tsiku limenelo chili pa otsutsa

    [11] “Amene akutsutsa za tsiku la malipiro

    [12] “Ndipo palibe angalitsutse koma yekhayo wopyola malire (pochita zoipa), wa machimo ambiri

    [13] “Pamene ma Ayah Athu akuwerengedwa kwa iye (onena za tsiku la malipiro ndikuuka mmanda) amanena kuti: “Izi ndi nthano za anthu akale.”

    [14] “Iyayi, sichoncho! Koma yaphimbidwa mitima yawo ndi dzimbiri (la machimo) omwe akhala akukolola

    [15] “Ayi ndithu iwo (okanira) tsiku limenelo) adzatchingidwa kwa Mbuye wawo; (sadzamuona)

    [16] “Pambuyo pake adzalowa ku Moto; (oyaka)

    [17] “Kenaka adzauzidwa (powaliritsa) “Ichi nchilango chomwe mudali kuchitsutsa (pa dziko lapansi).”

    [18] “Zoona, ndithu kaundula wa anthu abwino (ochita ntchito zabwino) ali mu Illiyyun

    [19] “Nanga nchiyani chitakudziwitse za Illiyyun

    [20] “Ameneyu ndi kaundula (wamkulu) yemwe walembedwa (mkati mwake ntchito za anthu abwino)

    [21] “Amamuyikira umboni (angelo) amene ayandikitsidwa (kwa Allah)

    [22] “Ndithu ochita zabwino adzakhala mu mtendere

    [23] “Atakhala pa mipando ya ulemu uku akuyang’ana (zimene Allah wawapatsa monga mtendere ndi ulemelero)

    [24] “Udzaona kuwala kwa mtendere pa nkhope zawo

    [25] “Adzamwetsedwa vinyo (woyeretsedwa) wotsekeredwa ndi zitsekerero zolimba

    [26] “Komalizira kwake (kwa vinyoyo) kuzikatuluka fungo la misk; kuti akapeze zimenezi, apikisane opikisana

    [27] “Ndipo chosakanizira cha vinyoyo ndi madzi a Tasnim

    [28] “(Tasnim ameneyo) ndi kasupe amene azikamwa amene ayandikitsidwa (kwa Allah)

    [29] “Ndithu amene adachita machimo adali kuwaseka (mwachipongwe) okhulupirira (pa dziko lapansi)

    [30] “(Okhulupirira) akadutsa pafupi ndi iwo ankakodolerana maso (mwachipongwe)

    [31] “Ndipo akabwerera kwa anzawo amabwerera akusangalala (ndi kunyozedwa kwa okhulupirira)

    [32] “Ndipo (nthawi zonse) akawaona Asilamu amanena: “Ndithu awa ndi osokera (chifukwa chomkhulupirira Mtumiki).” (s.a.w)

    [33] “Sanatumizidwe (Akafiri) kukhala ayang’aniri kwa okhulupirira (ndikuwaweruza zakulungama ndi kusokera)

    [34] “Basi lero okhulupirira awaseka osakhulupirira (powabwezera chipongwe chawo chimene ankachita pa dziko lapansi)

    [35] “Atakhala pa mipando ya ulemu uku akuyang’ana (mtendere umene Allah wawapatsa)

    [36] “Kodi alipidwa osakhulupirira pa zomwe ankachita zija (pa dziko lapansi)

    Kung'ambika

    Surah 84

    [1] Pamene thambo lidzang’ambike (kusonyeza mapeto ake)

    [2] “Ndikudzamvera lamulo la Mbuye wake; ndipo lidzayenera kutero

    [3] “Ndiponso pamene nthaka idzatambasulidwe (pogumuka mapiri ake ndikuchoka zitunda zake)

    [4] “Ndi kutaya zomwe zidali mkati mwake ndi kukhala yopanda kanthu

    [5] “Ndikudzamvera lamulo la Mbuye wake; ndipo lidzayenera kutero. (Choncho zikadzachitika zimenezi ndiye kuti munthu adzalandira mphoto ya zochita zake)

    [6] “E iwe munthu! Ndithudi iwe ukubwerera kwa Mbuye wako (ndi zochita zako zabwino kapena zoipa), kubwerera kotsimikizika, ndipo iwe ukumana (ndi zotsatira za zochitachita zako)

    [7] “Tsono amene adzapatsidwe kaundula wa zochita zake kudzanja la manja

    [8] “Basi iye, adzawerengedwa, kuwerengedwa kopepuka

    [9] “Ndipo adzabwerera kwa anthu ake (okhulupirira) ali wokondwa

    [10] “Koma yemwe adzapatsidwe kaundula wa zochita zake chakumanzere kudzera kumbuyo kwa msana wake (chifukwa chomunyoza)

    [11] “Basi, iye adzaitana imfa (kuti imufikire; kuti afe apumule, koma siidzamufikira)

    [12] “Ndipo adzalowa ku Moto woyaka

    [13] “Kamba kakuti iye adali wokondwa; (kukondwa kwa machimo) pamodzi ndi anthu ake (osaganizira za mathero ake)

    [14] “Ndithudi, amaganiza kuti sadzabwerera (kwa Allah ndiponso sadzawerengedwa)

    [15] “Chifukwa ninji (asabwelere)? Ndithu Mbuye wake adali kumuona. (Choncho alipidwa zimene adachita)

    [16] “Choncho ndikulumbilira kufiira kwa dzuwa (pamene likulowa)

    [17] “Ndi usiku ndi zimene wasonkhanitsa

    [18] “Ndi mwezi ukakwanira dangalira (lake)

    [19] “Ndithudi mudzachoka apa kunka apa (pa moyo uno mpakana umene uli nkudza)

    [20] “Kodi nchiyani chikuwaletsa iwo (okanira) kukhulupirira (Allah ndi kuuka kumanda, zisonyezo zake zitaonekera poyera)

    [21] “Ndipo ikawerengedwa kwa iwo Qur’an, sagwetsa pansi nkhope zawo (modzichepetsa)

    [22] “Koma amene sadakhulupirire akutsutsa basi (chifukwa cha makani ndi kudzikweza)

    [23] “Ndipo Allah akudziwa (bwinobwino) zimene akuzisonkhanitsa

    [24] “Choncho, auze nkhani yachilango chopweteka

    [25] “Kupatula awo amene akhulupirira ndikuchita ntchito zabwino, kwa iwo kuli malipiro osatha

    Magulu a Nyenyezi

    Surah 85

    [1] “Ndikulumbilira thambo lomwe liri ndi Buruj (Nyenyezi zikuluzikulu)

    [2] “Ndi tsiku lolonjezedwa (kuwerengedwa ndi kulipidwa)

    [3] “Ndi woikira umboni, ndi woikiridwa umboni

    [4] “Atembeleredwa eni ngalande zamoto (zomwe adali kuwazunzira okhulupirira Allah, achimuna ndi achikazi)

    [5] “(Ngalande) za moto wankhuni (zambiri zomwe adali kuzikoleza ndikuotchera okhulupirira)

    [6] “Pamene iwo adali chikhalire m’mphepete mwa ngalandezo

    [7] “Uku iwo akuyang’ana zomwe amawachitira okhulupirira, (pootchedwa ndi moto)

    [8] “Sadaone choipa chilichonse mwa iwo koma chifukwa choti adakhulupirira Allah mwini mphamvu zonse ndiponso mwini kuyamikidwa

    [9] “Yemwe ufumu wakumwamba ndi pansi ndiWake; ndipo Allah ndi mboni pachilichonse

    [10] “Ndithu amene ayesa mayeso okhulupirira achimuna ndi achikazi (pa chipembedzo chawo ndi mazunzo ndi chilango cha moto), pambuyo pake osalapa (pa zimenezi), adzalandira chilango cha Jahena ndiponso chilango cha moto wopsereza

    [11] “Ndithudi amene akhulupirira ndi kuchita ntchito zabwino, adzakhala ndi Minda yamtendere (momwe) mitsinje ikuyenda pansi pake; kumeneko ndiko kupambana kwakukulu

    [12] “Ndithu kulanga kwa Mbuye wako (kwa anthu achinyengo), ndi kwaukali kwambiri

    [13] “Iye, (Mmodzi yekha) ndi amene adayambitsa zolengedwa ndiponso ndi Yemwe adzazibweze (pambuyo poonongeka)

    [14] “Iye, ndi Wokhululuka (kwa amene walapa kwa Iye), ndiponso Wokonda kwambiri (amene akumkonda ndi kumumvera)

    [15] “Mwini Arsh (Mpando wachifumu), (ndiponso) Wolemekezeka (mmene alili ndi mbiri Zake)

    [16] “Wochita zimene wafuna, (ndipo chimene wafuna sichikanika)

    [17] “Kodi yakufika nkhani ya magulu a nkhondo

    [18] “Firiaun (Farawo) ndi Samudu, (ndi chilango chimene chidawapeza chifukwa chakulimbikira kwawo pa zinthu zopanda pake)

    [19] “Koma amene sadakhulupirire ali mkati motsutsa basi

    [20] “Koma Allah awazinga mbali zonse

    [21] “Koma iyi ndi Qur’an yolemekezeka

    [22] “Yomwe idachokera mu ubawo (chisileti chachikulu) wotetezedwa (ndi manja alionse, osintha kanthu kapena kuonjezerapo)

    Nyenyezi ya m'mawa

    Surah 86

    [1] “Ndikulumbilira ku mwamba ndi Nyenyezi imene imadza usiku

    [2] “Chitakudziwitse nchiyani za Nyenyezi yodza usikuyo

    [3] “Imeneyo ndi nyenyezi yowala kwambiri (mu mdima)

    [4] “Ndithudi palibe mzimu uliwonse koma uli ndi msungi wake (amene akuuyang’anira ndikulemba zonse zochita zake)

    [5] “Aganizire munthu, kodi adalengedwa kuchokera kuchiyani

    [6] “Adalengedwa kuchokera ku madzi ofwamphuka

    [7] “Amatuluka kuchokera pakati pa mafupa a msana (wa mwamuna) ndi chifuwa (cha mkazi)

    [8] “Ndithu Iye ndiwakutha, kumbwezeranso (ku moyo pa mbuyo pa imfa)

    [9] “Tsiku limene zobisika zonse zidzaonekera poyera

    [10] “Munthu sadzakhala ndi mphamvu (tsiku limenelo zodzitetezera iye mwini) ndiponso sadzakhala ndi mtetezi

    [11] “Ndikulumbiliranso mitambo yobweretsabweretsa mvula

    [12] “Ndi nthaka imene imang’ambika (potulutsa m’mera)

    [13] “Ndithudi iyi (Qur’an) ndi mawu olekanitsa (Haqq ndi Bâtwil - choona ndi chonama)

    [14] “Imeneyi sinkhambakamwa

    [15] “Ndithudi iwo akukonza chiwembu

    [16] “Nanenso ndikuwakonzera chiwembu (champhamvu kwambiri chimene sangathe kuchipewa)

    [17] “Basi, apatse nthawi osakhulupirira apatse nthawi pang’ono, (aona posachedwa)

    Wapamwambamwambi

    Surah 87

    [1] “Lemekeza dzina la Mbuye wako Wapamwambamwamba (ndikuliyeretsa ku zinthu zosayenera)

    [2] “Amene adalenga (chilichonse) ndikuchikonza bwinobwino (mkalengedwe kolingana)

    [3] “Amene adalamuliratu (chilichonse zochita zake) ndi kuchiongolera

    [4] “Ndi Yemwenso akumeretsa msipu

    [5] “Ndipo nausandutsa kukhala wouma ndi wodera

    [6] “Tikulakatulira (chivumbulutso Chathu) ndipo siuyiwala

    [7] “Kupatula chimene wafuna Allah (kuti uchiiwale); ndithu Iye amadziwa zoonekera ndi zimene zimabisika

    [8] “Ndipo tikufewetsera (njira yochitira zinthu) zabwino

    [9] “Choncho akumbutse (wanthu powalalikira) ngati kukumbutsa kuthandiza

    [10] “(Palibe chikaiko ulalikiwo) aukumbukira (ndikuthandizidwa nawo) amene akuopa Allah

    [11] “Ndipo wamavuto ambiri, (wamakani ndi wokanira), adzitalikitsa ndi ulalikiwo

    [12] “Amene adzalowa ku moto waukulu (umene wakonzedwa kuti udzakhale malipiro ake)

    [13] “Ndipo sakafa m’menemo (ndikupumula kumazunzo), ndiponso sakakhala ndi moyo (wamtendere)

    [14] “Ndithu wapambana amene wadziyeretsa (ku machimo)

    [15] “Ndikukumbukira dzina la Mbuye wake (ndi mtima wake, ndi lirime lake) uku akumapemphera

    [16] “Koma inu mukukonda kwambiri moyo wa dziko lapansi

    [17] “Pamene moyo wa tsiku lachimaliziro ndiwabwino kwambiri ndiponso wamuyaya

    [18] “Ndithu izi (mukuuzidwa m’Qur’an) zilipo m’mabuku oyamba, akale

    [19] “Mabuku a Ibrahim ndi Mûsa

    Zochititsa mantha

    Surah 88

    [1] “Kodi yakudzera, (iwe Mtumiki) (s.a.w) nkhani ya Qiyâma (imene idzaphimba anthu ndi zoopsa zake)

    [2] “Nkhope zina tsiku limenelo, zidzakhala zonyozeka

    [3] “Zogwira ntchito yotopetsa kwambiri

    [4] “Zikalowa ku Moto wotentha kwambiri

    [5] “Zikamwetsedwa mu kasupe wotentha kwabasi

    [6] “Sadzakhala ndichakudya koma minga

    [7] “Yosanenepetsa (thupi) ndiponso yosathetsa njala

    [8] “Nkhope zina tsiku limenelo zidzakhala zosangalala

    [9] “Zidzakondwera ndi malipiro a zochita zake (za pa dziko lapansi)

    [10] “M’minda ya pamwamba (Jannah)

    [11] “Sizikamva m’menemo mawu oipa, (otukwana ndi kulaula)

    [12] “Mmenemo muli kasupe woyenda (mokongola)

    [13] “Mmenemo muli makama a pamwamba

    [14] “Ndi zikho zoikidwa bwino (pamaso pawo)

    [15] “Ndi misamiro yoikidwa bwino m’mizeremizere

    [16] “Ndi mphasa (zamtengo wapatali, carpet) zoyalidwa ponseponse

    [17] “Kodi (akunyozera kulingalira zisonyezo za Allah), sakulingalira kungamira idalengedwa motani

    [18] “Ndi thambo (limene akuliona nthawi zonse) m’mene lidatukulidwira (kutali popanda mzati)

    [19] “Ndi mapiri momwe adakhazikitsidwira (molimba)

    [20] “Ndi nthaka momwe idayalidwira

    [21] “Basi, kumbutsa (anthu) ndithu iwe, ndiwe mkumbutsi

    [22] “Sindiwe wokakamiza anthu (kuti akhulupirire)

    [23] “Koma amene anyoza ndi kukanira (ulaliki wako)

    [24] “Allah amulanga chilango chachikulu zedi

    [25] “Ndithu kobwerera kwawo ndi kwa Ife basi

    [26] “Ndipo ndithu kuwerengedwa kwawo kuli kwa Ife

    Kutuluka kwa mbanda

    Surah 89

    [1] “Ndikulumbilira kuyera kwa m’bandakucha; (pamene usiku uthawa)

    [2] “Ndi masiku khumi (a mwezi wa Dhul-Hijjah omwe ngopatulika kwa Allah)

    [3] “Ndi Shaf’i ndi Witri: (nambala yogawika ndi yosagawika)

    [4] “Ndi usiku pamene ukupita (chifukwa cha kuyenda kwa dziko kodabwitsa)

    [5] “Kodi m’zimene zatchulidwazi simuli kulumbira kokwanira, kwa munthu wa nzeru

    [6] “Kodi sudadziwe momwe Mbuye wako adawalangira Âdi (anthu a mneneri Hûd)

    [7] “Aku Irama; ataliatali ngati zipilala

    [8] “Omwe onga iwo sadalengedwe m’maiko ena

    [9] “Ndi Asamudu, (anthu a mneneri Swaleh) amene adali kudula matanthwe ku chigwa (chotchedwa Wadi Qura ndi kumamanga nyumba zikuluzikulu)

    [10] “Komanso Firiauna (Farawo) mwini magulu ankhondo (omwe amalimbikitsa ufumu wake monga momwe zichiri zimalimbikitsira tenti)

    [11] “Amene adaipitsa m’maiko mopyola malire

    [12] “Ndipo adachulukitsa m’menemo kuononga (pamwamba pa kuononga)

    [13] “Choncho Mbuye wako adawathira ndi mitundu ya zilango (zoopsa)

    [14] “Ndithu Mbuye wako ali tcheru (ndi zochita za anthu. Ndipo akuwasungira kuti adzawalipire)

    [15] “Pamene munthu Mbuye wake akumuyesa (mayeso) ndikumulemekeza ndi kumpatsa mtendere (wachuma, ulemelero ndi mphamvu) amanena monyada: Mbuye wanga wandilemekeza (chifukwa zimenezi nzondiyenera ine)

    [16] “Koma akamuyesa mayeso ndi kumchepetsera rizq lake, (chuma) amanena (motaya rntima): Mbuye wanga wandinyoza

    [17] “Sichoncho ayi, (monga momwe mukuganizira) koma inu simuchitira za ufulu ana amasiye

    [18] “Ndipo simulimbikitsana za kudyetsa osauka

    [19] “Ndipo mukudya chuma cha masiye; kudya kosusuka

    [20] “Ndiponso mukukonda chuma; kukonda kopyola muyeso

    [21] “Sichoncho! (Siyani machitidwe amenewa); nthaka ikadzapondedwa (ndikuifafaniza)

    [22] “Ndikubwera Mbuye wako (mmabweredwe omwe akuwadziwa Iye Mwini) ndi angelo ali mmizeremizere

    [23] “Ndi kubweretsedwa Jahannam pa tsikulo, basi tsiku limenelo munthu adzakumbukira, koma kukumbuka kumeneko kudzamthandiza chiyani

    [24] “Adzanena: Kalanga ine! Ndikadatsogoza zabwino pa za moyo wanga uno

    [25] “Motero patsikuli, palibe wina amene adzalange monga momwe (Allah) adzalangire

    [26] “Ndiponso sanganjate aliyense monga kunjata kwa iye (Allah)

    [27] “E iwe mzimu wokhazikika (ndi choona)

    [28] “Bwerera kwa Mbuye wako uli wokondwera (ndi zomwe wapatsidwa), ndipo uli woyanjidwa (ndi Allah pa zomwe udatsogoza)

    [29] “Lowa mgulu la akapolo anga abwino

    [30] “Ndipo lowa m’munda Wanga (mnyumba ya mtendere wa muyaya)

    Mzinda

    Surah 90

    [1] “Ndikulumbilira mzinda uwu (wa Makka)

    [2] “Ndipo iwe udzatsikira mu mzindawu mwa ufulu (ndi kuuonjezera ulemelero)

    [3] “Ndiponso ndikulumbilira chobereka ndi choberekedwa, (kudzera mwa iwo mtundu wa anthu udasungidwa)

    [4] “Ndithudi tamulenga munthu mmavuto (kuyambira chiyambi chake mpaka malekezero a moyo wake)

    [5] “Kodi (munthu wolengedwa ndi mavutoyu) akuganiza kuti palibe amene angamuthe

    [6] “Akunena (monyadira kuti): “Ndaononga chuma chambiri (chifukwa choletsa Chisilamu kufala).”

    [7] “Kodi akuganiza kuti palibe akumuona

    [8] “Kodi sitidampangire maso awiri (amene akuyang’anira)

    [9] “Ndilirime ndi milomo iwiri (zimene akulankhulira)

    [10] “Ndipo tamlongosolera njira ziwiri: (yabwino ndi yoipa, ndipo tampatsa mphamvu yosankhira njira imene akufuna)

    [11] “Kodi walikwera phiri lovutalo (lomwe lingakamfikitse ku Jannah)

    [12] “Nanga nchiyani chakudziwitsa za kukwera phiri lovutalo

    [13] “(Kutero ndiko) kupereka ufulu kwa kapolo

    [14] “Kapena kuwadyetsa (osowa) pa tsiku la njala

    [15] “Amasiye achibale

    [16] “Kapena wosauka wa fumbi lokhalokha (chifukwa cha kuvutika kwambiri)

    [17] “Komanso nakhala mmodzi mwa okhulupirira ndikumalangizana za kupirira, ndi kumalangizananso za chifundo

    [18] “Otero ndiwo (anthu abwino) a ku dzanja lamanja

    [19] “Koma amene sanakhulupirire Ayah Zathu, ndi anthu a kudzanja lamanzere (oipa)

    [20] “Moto wozungulira mbali zonse udzakhala pa iwo (ndikuwatsekera makomo)

    Dzuwa

    Surah 91

    [1] “Ndikulumbilira dzuwa ndi dangalira lake

    [2] “Ndi mwezi pamene ukulitsatira (dzuwalo ndikulowa mmalo mwake powalitsa dziko dzuwalo litalowa)

    [3] “Ndi usana pamene ukulisonyeza poyera (kuti lisaphimbidwe)

    [4] “Ndi usiku pamene ukuliphimba

    [5] “Ndi thambo ndi (Mwini mphamvu zonse Wamkulu) Yemwe adalimanga ndi kulitukula (mwaluso)

    [6] “Ndi nthaka ndi (Mwini mphamvu zonse Wamkulu), Yemwe adaiyala (mbali zonse ndi kuichita kukhala ngati choyala)

    [7] “Ndi mzimu ndi Yemwe adawulinganiza (powupatsa mphamvu)

    [8] “Ndipo adaudziwitsa zoipa zake ndi zabwino zake; (ndi kuwupatsa ufulu ndi mphamvu zochitira zimene ukufuna)

    [9] “Ndithu wapambana amene wauyeretsa

    [10] “Ndipo ndithu wataika amene wauononga

    [11] “Thamud (Samudu) adakanira (Mneneri wawo) chifukwa cha kulumpha malire kwawo

    [12] “Pamene woipitsitsa wawo adadzipereka (kupha ngamira yozizwitsa)

    [13] “Pamenepo Mneneri wa Allah (Swaleh) adawauza: “Isiyeni ngamira ya Allah (idye mdziko la Allah). Musailetse kumwa madzi (pa tsiku lake).”

    [14] “Koma adamutsutsa ndikuipha; kwa chifukwa chimenecho Mbuye wawo (Allah) adawaononga chifukwa cha tchimo lawo; adangowafafaniza (onse mnthaka)

    [15] “Iye saopa zotsatira za chilangochi (chifukwa amenewa ndi malipiro a chilungamo pa zomwe adachita)

    Usiku

    Surah 92

    [1] “Ndikulumbilira usiku pamene ukuphimba (chilichonse)

    [2] “Ndi usana pamene kukuyera

    [3] “Ndiponso Yemwe adalenga chachimuna ndi chachikazi

    [4] “Ndithu zochita zanu nzosiyanasiyana

    [5] “Tsono yemwe akupereka (pa njira ya Allah) ndikumamuopa (Mbuye wake ndikupewa zoletsedwa)

    [6] “Ndikumavomereza zinthu zabwino; (komwe kuli kukhulupirira Allah mwanzeru)

    [7] “Choncho timufewetsera njira yompititsa ku zabwino

    [8] “Koma uyo achite umbombo ndikuganiza za kuti iye payekha ngokwana

    [9] “Ndi kumatsutsa zinthu zabwino

    [10] “Choncho timufewetsera njira yompititsa ku mavuto (a muyaya)

    [11] “Ndipo chuma chake sichidzamthandiza (chilichonse) akadzagwera ku Moto

    [12] “Ndithu Ife ndi amene timawalongosolera anthu njira yabwino ndi njira yoipa

    [13] “Ndipo ndithu moyo womaliza ndi moyo woyamba uli m’manja mwathu

    [14] “Basi, ndikukuchenjezani za Moto woyaka mwa mphamvu

    [15] “Sakaulowa koma (kafiri) woipitsitsa kwambiri

    [16] “Yemwe amatsutsa (choona) ndi kunyoza (zisonyezo za Allah)

    [17] “Koma yemwe akuopa Allah kwambiri akatalikitsidwa ndi Moto

    [18] “Amene akupereka chuma chake ndi cholinga chodziyeretsa

    [19] “Ndipo palibe aliyense kwa iye, amene adamchitira za chifundo zomwe zikulipidwa

    [20] “Koma (akuchita zimenezi) kufuna chikondi cha Mbuye wake Wapamwambamwamba

    [21] “Ndipo posachedwa adzasangalala

    Maola a m'mawa

    Surah 93

    [1] “Ndikulumbilira mmawa dzuwa litakwera (imene ili nthawi yantchito)

    [2] “Ndi usiku pamene ukuvindikira

    [3] “Sadakusiye Mbuye wako (iwe Mneneri) (s.a.w) ndiponso sadakude

    [4] “Ndithu moyo watsiku lirimkudza ndi wabwino kwa iwe kuposa umoyo woyambawu

    [5] “Ndithu posachedwapa akupatsa Mbuye wako (zabwino zamdziko lapansi ndi tsiku lachimaliziro) ndipo ukondwera

    [6] “Kodi sadakupeze uli wa masiye ndipo adakupatsa pokhala pabwino

    [7] “Ndipo adakupeza uli wosazindikira (Qur’an) nakuongola (pokuzindikiritsa Qur’aniyo ndi malamulo a chipembedzo)

    [8] “Ndiponso adakupeza uli wosauka nakulemeretsa

    [9] “Basi, wamasiye usamchitire nkhanza

    [10] “Ndiponso wopempha usamukalipire

    [11] “Tsono mtendere wa Mbuye wako uwutchule (pothokoza ndi kugwira ntchito zabwino)

    Mpumulo

    Surah 94

    [1] “Kodi sitidachiphanule chifuwa chako (pokupatsa chiongoko ndi chikhulupiliro ndi nzeru zambiri)

    [2] “Ndipo takuchotsera mtolo wako (pa ntchito yolalikira pokuthandiza ndi kukufewetsera zinthu zako)

    [3] “Mtolo umene udalemetsa msana wako

    [4] “Ndipo takukweza kutchulidwa kwako

    [5] “Ndipo ndithu pali chovuta palinso zabwino (Zambiri)

    [6] “Ndithu pali chovuta palinso zabwino (zambiri)

    [7] “Basi, ukamaliza ntchito (yolalikira ndi Jihâd) limbikira kupemphera

    [8] “Ndipo khala wolakalaka (zabwino zomwe zili) kwa Mbuye wako

    Mkuyu

    Surah 95

    [1] “Ndikulumbilira mitengo ya Mkuyu ndi Zitona (pansi pa mitengo imeneyi Ibrahim ndi Nuh (Nowa) adapeza uneneri

    [2] “Ndi phiri la Sinai (pamene Allah adamulankhulira Mûsa)

    [3] “Ndiponso mzinda uwu (wolemekezeka) wamtendere; (Makka, womwe adapatsiridwa uneneri Muhammad) (s.a.w)

    [4] “Palibe chikaiko, tamulenga munthu mkalengedwe kabwino, kolingana (ndipo ali ndi mbiri zabwino)

    [5] “Pambuyo pake tamubwezera pansi kumposa wa pansi

    [6] “Kupatula amene akhulupirira ndikumachita zabwino, adzakhala nawo iwo malipiro osatha

    [7] “Tsono nchiyani chakuchititsa kuti ukanire kuuka ndi malipiro pambuyo (poona mphamvu zathu pa chilichonse)

    [8] “Kodi Allah si Muweruzi wa nzeru kuposa aweruzi onse

    Chinthu chotsekeka

    Surah 96

    [1] “Werenga! (Iwe Mneneri (s.a.w), zomwe zikuvumbulutsidwa) mdzina la Mbuye wako Yemwe adalenga (zolengedwa zonse)

    [2] “Adalenga munthu kuchokera ku magazi owundana

    [3] “Werenga! Ndipo Mbuye wako ndi Wopereka kwambiri

    [4] “Yemwe waphunzitsa (munthu kulemba) ndi cholembera

    [5] “Waphunzitsa munthu zinthu (zambiri) zomwe (iye) sadali kuzidziwa

    [6] “Zoona ndithu koma munthu akupyola malire (podzikweza)

    [7] “Chifukwa chodziona kuti walemera

    [8] “Palibe chikaiko, (iwe Mneneri (s.a.w) kobwerera (onse) nkwa Mbuye wako basi; (adzawaukitsa)

    [9] “Kodi wamuona yemwe akuletsa

    [10] “Kapolo (wa Allah) akamapemphera

    [11] “Tandiuza ngati ali pachiongoko

    [12] “Kapena kuti akulamulira zoopa Allah

    [13] “Tandiuza (za woletsayo) ngati akutsutsa (zimene wadza nazo Mneneri) ndikunyoza (chikhulupiliro ndi ntchito yabwino)

    [14] “Kodi sakudziwa kuti Allah akuona (machitidwe ake. Ndipo adzamlipira)

    [15] “Ayi ndithu ngati sasiya timukoka tsitsi lapatsumba (tiligwira mwamphamvu tsumba lake ndikukamponya ku Moto)

    [16] “Tsumba labodza (ndiponso) lamachimo

    [17] “Basi aliitane gulu lakelo, (la amene amakhala nawo pabwalo kuti amthandize pano pa dziko kapena tsiku lachimaliziro)

    [18] “Nafe tiitana azabaniya (angelo a ku Moto)

    [19] “Ayi ndithu usamumvere (pa zimene akukuletsazo); koma gwetsa nkhope yako pansi, ndipo dziyandikitse kwa Mbuye wako

    Mphamvu

    Surah 97

    [1] “Ndithu taivumbulutsa (Qur’an) mu usiku wa Qadr (usiku wolemekezeka)

    [2] “Ndi chiyani chingakudziwitse za usiku wolemekezekawu

    [3] “Usiku olemekezekawu uli wabwino kuposa miyezi chikwi chimodzi ( yomwe mulibe Laila-tul-Qadr)

    [4] “Amatsika angelo ndi Jiburil mmenemo mwa chilolezo cha Mbuye wawo kudzalongosola chinthu chilichonse

    [5] “Mtendere usiku umenewo! (Palibe mavuto ndi zoipa) mpaka m’bandakucha

    Umboni woonekera

    Surah 98

    [1] “Amene adakanira (Allah ndi Mthenga Wake) mwa omwe adapatsidwa buku ndi opembedza mafano sadali olekana (ndi umbuli wawo ndi kusalabadira kwawo choona) mpaka pomwe chidawadzera chisonyezo choonekera poyera

    [2] “(Yemwe ndi) Mtumiki wochokera kwa Allah akuwawerengera makalata oyeretsedwa (ku zonama)

    [3] “Omwe mkati mwake muli malamulo oongoka (ofotokoza za choona)

    [4] “Sadalekane omwe adapatsidwa mabuku mpaka pomwe chidawafikira chisonyezo (chosonyeza kuti Muhammad (s.a.w) ndi mthenga wa Allah yemwe adalonjezedwa mmabuku awo

    [5] “Ndipo sadalamulidwe (china) koma kuti ampembedze Allah (Mmodzi yekha) ndikuyeretsa chipembedzo chake popendekera ku choona (ndi kusiya njira zonama) ndi kuti asunge Swala ndiponso apereke chopereka (cha pachuma chawo); chimenecho (ndicho) chipembedzo choongoka

    [6] “Ndithu amene sadakhulupirire (Mneneri) (s.a.w) pakati pa anthu a mabuku ndi opembedza mafano adzalowetsedwa ku Jahannam ndikukhala m’menemo nthawi yaitali; iwowo ndiwo zolengedwa zoipa

    [7] “Ndithu amene akhulupirira (mwa Allah ndi Mthenga Wake) ndikumachita zabwino, iwo ndiwo zolengedwa zabwino

    [8] “Malipiro awo kwa Mbuye wawo, ndi minda yamuyaya momwe ikuyenda pansi pake mitsinje; adzakhala m’menemo muyaya. Allah adzawayanja nawonso adzamuyanja (chifukwa cha zomwe adzawapatse); zimenezo ndi za yemwe awope Mbuye wake (Allah)

    Chivomezi

    Surah 99

    [1] “Likadzagwedezedwa dziko lapansi kugwedezeka kwake kwamphamvu

    [2] “Ndipo nthaka idzatulutsa mitolo yake (zinthu zomwe zidali mkati mwake, monga akufa ndi miyala ya mtengo wapatali)

    [3] “Ndipo munthu adzanena (mwa mantha, ndikudabwa nthawi imeneyo). Ha! Yatani nthaka, (kodi Qiyâma yafika)

    [4] “Tsiku limenelo idzanena nkhani zake zonse, (zabwino kapena zoipa)

    [5] “Pakuti Mbuye wako adzailamula kutero (kuti igwedezeke ndikunena zimene zinkachitika pamwamba pake)

    [6] “Tsiku limenelo anthu adzachoka (m’manda) ali m’magulu obalalika kuti akasonyezedwe ntchito zawo (ndikudziwa chiwerengero chawo chimene chili kwa Allah)

    [7] “Choncho, amene angachite chabwino cholemera ngati kanjere kakang’ono, adzaona malipiro ake

    [8] “Ndipo amene angachite choipa cholemera ngati kanjere kakang’ono, adzaona malipiro ake. (Allah sachitira chinyengo aliyense)

    Othamanga

    Surah 100

    [1] “Ndikulumbilira akavalo othamanga ali ndi phuma

    [2] “Ndi otulutsa moto ku zikhotwa (pomenyetsa miyendo m’miyala)

    [3] “Ndi othira nkhondo adani mmawa (dzuwa lisadatuluke)

    [4] “Ndi kuulutsa fumbi lambiri (kwa adani) nthawi imeneyo

    [5] “Ndikulowelera mkatikati mwa adani

    [6] “Ndithu munthu ali wokanira Mbuye wake, (sathokoza Allah pa zimene amdalitsa nazo)

    [7] “Ndithudi iye pa zimenezi ndi mboni (yodzichitira yekha kupyolera mzochitachita zake)

    [8] “Ndipo ndithu iye ndiwokonda chuma kwambiri (ndiponso ngwamsulizo)

    [9] “Kodi sakudziwa zikadzatulutsidwa za m’manda

    [10] “Ndikudzasonkhanitsidwa ndi kuonekera poyera zomwe zidali m’mitima

    [11] “Ndithu tsiku limenelo Mbuye wawo adzawadziwa kwambiri (ndikuwalongosolera zonse zochita zawo)

    Tsoka

    Surah 101

    [1] “Kugunda kwa phokoso (la Qiyâma)

    [2] “Kodi kugunda kwa phokosolo ndi chiyani

    [3] “Ndichiyani chingakudziwitse za kugunda kwa phokoso (la Qiyâma komwe kudzawakomole anthu)

    [4] “Limenelo ndi tsiku limene anthu adzakhala ngati agulugufe obalalika

    [5] “Ndipo mapiri adzakhala ngati ubweya womwazidwa (wongouluka uku ndi uku mumlengalenga)

    [6] “Tsono amene muyeso wake (wa zinthu zabwino) udzalemere (ndikupepuka zoipa)

    [7] “Ndiye kuti iye adzakhala mu umoyo wosangalatsa (patsiku la chiweruziro)

    [8] “Ndipo yemwe muyeso wake (wa zinthu zabwino) udzapepuka (ndi kulemera zoipa)

    [9] “Ndiye kuti mbuto yake ndi ku Hawiya

    [10] “Kodi ndi chiyani chingakudziwitse za Hawiya

    [11] “Umenewo ndi Moto woyaka mwa ukali

    Mpikisano wapadziko lonse lapansi

    Surah 102

    [1] “Kwakutangwanitsani kusonkhanitsa (chuma chambiri ndi ana)

    [2] “Mpakana mwapita kumanda (mwamwalira ndikukalowa m’manda)

    [3] “Sichoncho! Mudziwa posachedwapa

    [4] “Ndiponso sichoncho! Mudziwa posachedwapa

    [5] “Sichoncho! mukadakhala mukudziwa, kudziwa kwachitsimikizo (sibwenzi mukutangwanika ndi za mdziko)

    [6] “Ndithudi mudzauona Moto

    [7] “Kenako mudzauona ndithu ndi diso lachitsimikizo

    [8] “Tsono patsikulo ndithudi mudzafunsidwa za mtendere (omwe munapatsidwa)

    Tsiku lotsika

    Surah 103

    [1] “Ndikuilumbilira nthawi

    [2] “Ndithu munthu aliyense ndi wotaika (chifukwa chakugonjetsedwa ndi zilakolako zake)

    [3] “Kupatula amene akhulupirira (mwa Allah) ndi kumachita zabwino, ndikumalangizana kutsatira choona ndiponso ndi kumalangizana za kupirira (potsatira malamulo a Allah ndi zina za mdziko)

    Wachipongwe

    Surah 104

    [1] “Kuonongeka koopsa kudzampeza aliyense wojeda ndi wonyoza anthu polozera (ndi maso kapena kuyankhula ndi lirime)

    [2] “Yemwe wasonkhanitsa chuma ndikumachiwerengera

    [3] “Akuganiza kuti chuma chakecho chimkhazika (pa dziko) nthawi yaitali (ndikumteteza ku zimene sakuzifuna)

    [4] “Sichoncho! (Asiye maganizo amenewo) ndithudi, akaponyedwa ku Moto woononga (chifukwa cha kuipa kwa zochita zake)

    [5] “Ndi chiyani chingakudziwitse za Moto woonongawu

    [6] “Umenewu ndi Moto wa Allah woyaka (nthawi zonse, woononga chilichonse choponyedwa mmenemo)

    [7] “Umene umakwera mpaka ku mtima

    [8] “Ndithu motowo ukawazinga (ndi kuwatsekera makomo)

    [9] “Munsanamira za zitalizitali (kotero kuti sakatha kugwedezeka mmenemo kapena kupulumuka)

    Njobvu

    Surah 105

    [1] “Kodi sudaone momwe Mbuye wako adawachitira eni njovu

    [2] “Kodi sadachichite chiwembu chawo kukhala chosokera (chopanda phindu)

    [3] “Ndipo adawatumizira magulumagulu a mbalame otsatizana. (ndipo adawazungulira mbali zonse)

    [4] “Zimawagenda ndi miyala ya moto

    [5] “Choncho adawachita ngati m’mera wodyedwa (ndi nyama ndi kulavulidwa)

    Quraishi

    Surah 106

    [1] “Cholinga chakuwachita Maquraish kuti apitirize chizolowezi chawo

    [2] “Apitilize chizolowezi chawo choyenda nthawi ya dzinja (kunka ku Yemen) ndi nthawi yachirimwe (kunka ku Sham kukachita malonda, mosatekeseka ndi mopanda mantha)

    [3] “Choncho, amupembedze Mbuye wa Nyumba iyi (Al-Kaaba amene adachititsa kuti athe kuyenda maulendo awiriwo)

    [4] “Yemwe amawadyetsa (nthawi imene Arabu anzawo) ali m’njala, ndipo amawapatsa chitetezo (pomwe anzawo) ali ndi mantha

    Zokoma zazing'ono

    Surah 107

    [1] “Kodi wamuona yemwe akutsutsa za mphoto (ndi chiwerengero cha tsiku lachimaliziro)

    [2] “Iye ndi yemwe akukankha wamasiye (mwankhanza)

    [3] “Ndipo salimbikitsa (ena pamodzi ndi iye mwini) kudyetsa osauka

    [4] “Choncho kuonongeka kuli pa ena mwa opemphera swala (amene ali ndi mbiri izi)

    [5] “Omwe amachitira mphwayi mapemphero awo

    [6] “Amenenso (akamachita mapemphero awo) amadzionetsera (kwa anthu mwachipha maso kuti apeze ulemelero ndi kutamandidwa mmitima mwa anthu)

    [7] “Ndipo amamana ziwiya (zawo posabwereka anzawo zinthu zofunika pa moyo wa aliyense monga nkhwangwa, mpeni, mtondo ndi zina zotere)

    Kuchuluka

    Surah 108

    [1] “Ndithu takupatsa zabwino zambiri (zina mwa izo ndi mtsinje wotchedwa Kauthar)

    [2] “(Pakuti ndakupatsa zimenezo), pitiriza kupembedza Mbuye wako (moyera mtima) ndipo ipha nsembe yako (chifukwa chakuthokoza Allah pa zimene wakupatsa, monga ulemelero ndikukusankhira zabwino zambiri)

    [3] “Ndithu mdani wako ndiye ali wopanda mwawi

    Osakhulupirira

    Surah 109

    [1] “Nena (iwe Mtumiki) (s.a.w): E inu anthu osakhulupirira

    [2] “Sindipembedza chimene inu mukuchipembedza (kusiya Allah)

    [3] “Inunso simumpembedza amene ine ndikumpembedza (yemwe ndi Allah)

    [4] “Ndiponso ine sindidzapembedza chimene inu mwakhala mukuchipembedza (chifukwa inu ndinu ophatikiza Allah ndi zinthu zina)

    [5] “Ndipo inu simudzampembedza amene ine ndikumpembedza (yemwe ndi Allah)

    [6] “Inu muli ndi chipembedzo chanu (chimene mukuchikhulupirira), inenso ndili ndi chipembedzo changa (chimene Allah wandisankhira)

    Thandizo

    Surah 110

    [1] “Chikafika chipulumutso cha Allah ndi kugonjetsa (mzinda wa Makka kwa iwe ndi okutsatira)

    [2] “Ndikuwaona anthu akulowa m’chipembedzo cha Allah ali magulumagulu

    [3] “Pamenepo lemekeza Mbuye wako ndi kumtamanda ndiponso mpemphe chikhululuko, ndipo ndithu Iye ndiwolandira mochuluka kulapa (kwa anthu Ake)

    Lawi

    Surah 111

    [1] “Aonongeka manja a Abi Lahab (omwe adali kuwagwiritsa ntchito pozunza Asilamu). Nayenso wawonongeka

    [2] “Chuma chake ndi ulemelero wake (umene adaupeza) sizidamthandize ku chilango cha Allah

    [3] “Adzalowa ku Moto wa malawi

    [4] “Nayenso mkazi wake (adzalowa ku Moto) yemwe adali kusenza nkhuni (za minga pomutchera Mtumiki (s.a.w) komanso amanka nadanitsa pakati pa anthu

    [5] “Mkhosi mwake mdzamangidwa chingwe chopiringidwa bwino cha mlaza (chomlanga nacho)

    Kukhulupirika

    Surah 112

    [1] “Nena (iwe Mtumiki (s.a.w), kwa amene akukufunsa mwachipongwe, mbiri za Mulungu wako): “Iye ndi Allah Mmodzi, (alibe mnzake)

    [2] “Allah ndi Wokhala ndi zonse Wodaliridwa ndi zolengedwa Zake

    [3] “Sadabale (mwana) ndiponso sadaberekedwe

    [4] “Ndiponso palibe aliyense wofanana ndi Iye.”

    Kutuluka kwa mbanda

    Surah 113

    [1] “Nena: “Ndikudzitchinjiriza ndi Mbuye wam’bandakucha

    [2] “Kuchokera ku zoipa zimene Iye adazilenga

    [3] “Ndi ku zoipa za usiku pamene mdima ukulowa mwa mphamvu

    [4] “Ndi ku zoipa za afiti omwe amauzira mu mfundo

    [5] “Ndiponso ku zoipa za wansanje pamene akuchita nsanje.”

    Anthu

    Surah 114

    [1] “Nena: “Ndikudzitchinjiriza ndi Mbuye (Mleri) wa anthu (Yemwe akulinganiza zinthu zawo)

    [2] “Mfumu ya anthu ( Imene iri ndi mphamvu yochita chirichonse pa iwo)

    [3] “Wopembedzedwa wa anthu

    [4] “Kuzoipa za mnong’onezi (yemwe amathira unong’onezi wake m’mitimaya anthu) yemwenso amabisala (posiya unong’onezi wake ngati mwini mtimawo atankumbukira Allah)

    [5] “Yemwe amanong’oneza mzifuwa za anthu

    [6] “Wochokera m’ziwanda ndi mwa anthu.”