Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 89 - Al-Fajr
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Al-Fajr 89:1
“Ndikulumbilira kuyera kwa m’bandakucha; (pamene usiku uthawa)
Verse 2 — Surah Al-Fajr 89:2
“Ndi masiku khumi (a mwezi wa Dhul-Hijjah omwe ngopatulika kwa Allah)
Verse 3 — Surah Al-Fajr 89:3
“Ndi Shaf’i ndi Witri: (nambala yogawika ndi yosagawika)
Verse 4 — Surah Al-Fajr 89:4
“Ndi usiku pamene ukupita (chifukwa cha kuyenda kwa dziko kodabwitsa)
Verse 5 — Surah Al-Fajr 89:5
“Kodi m’zimene zatchulidwazi simuli kulumbira kokwanira, kwa munthu wa nzeru
Verse 6 — Surah Al-Fajr 89:6
“Kodi sudadziwe momwe Mbuye wako adawalangira Âdi (anthu a mneneri Hûd)
Verse 7 — Surah Al-Fajr 89:7
“Aku Irama; ataliatali ngati zipilala
Verse 8 — Surah Al-Fajr 89:8
“Omwe onga iwo sadalengedwe m’maiko ena
Verse 9 — Surah Al-Fajr 89:9
“Ndi Asamudu, (anthu a mneneri Swaleh) amene adali kudula matanthwe ku chigwa (chotchedwa Wadi Qura ndi kumamanga nyumba zikuluzikulu)
Verse 10 — Surah Al-Fajr 89:10
“Komanso Firiauna (Farawo) mwini magulu ankhondo (omwe amalimbikitsa ufumu wake monga momwe zichiri zimalimbikitsira tenti)
Verse 11 — Surah Al-Fajr 89:11
“Amene adaipitsa m’maiko mopyola malire
Verse 12 — Surah Al-Fajr 89:12
“Ndipo adachulukitsa m’menemo kuononga (pamwamba pa kuononga)
Verse 13 — Surah Al-Fajr 89:13
“Choncho Mbuye wako adawathira ndi mitundu ya zilango (zoopsa)
Verse 14 — Surah Al-Fajr 89:14
“Ndithu Mbuye wako ali tcheru (ndi zochita za anthu. Ndipo akuwasungira kuti adzawalipire)
Verse 15 — Surah Al-Fajr 89:15
“Pamene munthu Mbuye wake akumuyesa (mayeso) ndikumulemekeza ndi kumpatsa mtendere (wachuma, ulemelero ndi mphamvu) amanena monyada: Mbuye wanga wandilemekeza (chifukwa zimenezi nzondiyenera ine)
Verse 16 — Surah Al-Fajr 89:16
“Koma akamuyesa mayeso ndi kumchepetsera rizq lake, (chuma) amanena (motaya rntima): Mbuye wanga wandinyoza
Verse 17 — Surah Al-Fajr 89:17
“Sichoncho ayi, (monga momwe mukuganizira) koma inu simuchitira za ufulu ana amasiye
Verse 18 — Surah Al-Fajr 89:18
“Ndipo simulimbikitsana za kudyetsa osauka
Verse 19 — Surah Al-Fajr 89:19
“Ndipo mukudya chuma cha masiye; kudya kosusuka
Verse 20 — Surah Al-Fajr 89:20
“Ndiponso mukukonda chuma; kukonda kopyola muyeso
Verse 21 — Surah Al-Fajr 89:21
“Sichoncho! (Siyani machitidwe amenewa); nthaka ikadzapondedwa (ndikuifafaniza)
Verse 22 — Surah Al-Fajr 89:22
“Ndikubwera Mbuye wako (mmabweredwe omwe akuwadziwa Iye Mwini) ndi angelo ali mmizeremizere
Verse 23 — Surah Al-Fajr 89:23
“Ndi kubweretsedwa Jahannam pa tsikulo, basi tsiku limenelo munthu adzakumbukira, koma kukumbuka kumeneko kudzamthandiza chiyani
Verse 24 — Surah Al-Fajr 89:24
“Adzanena: Kalanga ine! Ndikadatsogoza zabwino pa za moyo wanga uno
Verse 25 — Surah Al-Fajr 89:25
“Motero patsikuli, palibe wina amene adzalange monga momwe (Allah) adzalangire
Verse 26 — Surah Al-Fajr 89:26
“Ndiponso sanganjate aliyense monga kunjata kwa iye (Allah)
Verse 27 — Surah Al-Fajr 89:27
“E iwe mzimu wokhazikika (ndi choona)
Verse 28 — Surah Al-Fajr 89:28
“Bwerera kwa Mbuye wako uli wokondwera (ndi zomwe wapatsidwa), ndipo uli woyanjidwa (ndi Allah pa zomwe udatsogoza)
Verse 29 — Surah Al-Fajr 89:29
“Lowa mgulu la akapolo anga abwino
Verse 30 — Surah Al-Fajr 89:30
“Ndipo lowa m’munda Wanga (mnyumba ya mtendere wa muyaya)