Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 91 - Ash-Shams
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Ash-Shams 91:1
“Ndikulumbilira dzuwa ndi dangalira lake
Verse 2 — Surah Ash-Shams 91:2
“Ndi mwezi pamene ukulitsatira (dzuwalo ndikulowa mmalo mwake powalitsa dziko dzuwalo litalowa)
Verse 3 — Surah Ash-Shams 91:3
“Ndi usana pamene ukulisonyeza poyera (kuti lisaphimbidwe)
Verse 4 — Surah Ash-Shams 91:4
“Ndi usiku pamene ukuliphimba
Verse 5 — Surah Ash-Shams 91:5
“Ndi thambo ndi (Mwini mphamvu zonse Wamkulu) Yemwe adalimanga ndi kulitukula (mwaluso)
Verse 6 — Surah Ash-Shams 91:6
“Ndi nthaka ndi (Mwini mphamvu zonse Wamkulu), Yemwe adaiyala (mbali zonse ndi kuichita kukhala ngati choyala)
Verse 7 — Surah Ash-Shams 91:7
“Ndi mzimu ndi Yemwe adawulinganiza (powupatsa mphamvu)
Verse 8 — Surah Ash-Shams 91:8
“Ndipo adaudziwitsa zoipa zake ndi zabwino zake; (ndi kuwupatsa ufulu ndi mphamvu zochitira zimene ukufuna)
Verse 9 — Surah Ash-Shams 91:9
“Ndithu wapambana amene wauyeretsa
Verse 10 — Surah Ash-Shams 91:10
“Ndipo ndithu wataika amene wauononga
Verse 11 — Surah Ash-Shams 91:11
“Thamud (Samudu) adakanira (Mneneri wawo) chifukwa cha kulumpha malire kwawo
Verse 12 — Surah Ash-Shams 91:12
“Pamene woipitsitsa wawo adadzipereka (kupha ngamira yozizwitsa)
Verse 13 — Surah Ash-Shams 91:13
“Pamenepo Mneneri wa Allah (Swaleh) adawauza: “Isiyeni ngamira ya Allah (idye mdziko la Allah). Musailetse kumwa madzi (pa tsiku lake).”
Verse 14 — Surah Ash-Shams 91:14
“Koma adamutsutsa ndikuipha; kwa chifukwa chimenecho Mbuye wawo (Allah) adawaononga chifukwa cha tchimo lawo; adangowafafaniza (onse mnthaka)
Verse 15 — Surah Ash-Shams 91:15
“Iye saopa zotsatira za chilangochi (chifukwa amenewa ndi malipiro a chilungamo pa zomwe adachita)