Back to LanguagesPrevious ChapterNext Chapter
Chichewa - Chapter 96 - Al-Alaq
Translation by Khaled Ibrahim Betala — Permalink
Verse 1 — Surah Al-Alaq 96:1
“Werenga! (Iwe Mneneri (s.a.w), zomwe zikuvumbulutsidwa) mdzina la Mbuye wako Yemwe adalenga (zolengedwa zonse)
Verse 2 — Surah Al-Alaq 96:2
“Adalenga munthu kuchokera ku magazi owundana
Verse 3 — Surah Al-Alaq 96:3
“Werenga! Ndipo Mbuye wako ndi Wopereka kwambiri
Verse 4 — Surah Al-Alaq 96:4
“Yemwe waphunzitsa (munthu kulemba) ndi cholembera
Verse 5 — Surah Al-Alaq 96:5
“Waphunzitsa munthu zinthu (zambiri) zomwe (iye) sadali kuzidziwa
Verse 6 — Surah Al-Alaq 96:6
“Zoona ndithu koma munthu akupyola malire (podzikweza)
Verse 7 — Surah Al-Alaq 96:7
“Chifukwa chodziona kuti walemera
Verse 8 — Surah Al-Alaq 96:8
“Palibe chikaiko, (iwe Mneneri (s.a.w) kobwerera (onse) nkwa Mbuye wako basi; (adzawaukitsa)
Verse 9 — Surah Al-Alaq 96:9
“Kodi wamuona yemwe akuletsa
Verse 10 — Surah Al-Alaq 96:10
“Kapolo (wa Allah) akamapemphera
Verse 11 — Surah Al-Alaq 96:11
“Tandiuza ngati ali pachiongoko
Verse 12 — Surah Al-Alaq 96:12
“Kapena kuti akulamulira zoopa Allah
Verse 13 — Surah Al-Alaq 96:13
“Tandiuza (za woletsayo) ngati akutsutsa (zimene wadza nazo Mneneri) ndikunyoza (chikhulupiliro ndi ntchito yabwino)
Verse 14 — Surah Al-Alaq 96:14
“Kodi sakudziwa kuti Allah akuona (machitidwe ake. Ndipo adzamlipira)
Verse 15 — Surah Al-Alaq 96:15
“Ayi ndithu ngati sasiya timukoka tsitsi lapatsumba (tiligwira mwamphamvu tsumba lake ndikukamponya ku Moto)
Verse 16 — Surah Al-Alaq 96:16
“Tsumba labodza (ndiponso) lamachimo
Verse 17 — Surah Al-Alaq 96:17
“Basi aliitane gulu lakelo, (la amene amakhala nawo pabwalo kuti amthandize pano pa dziko kapena tsiku lachimaliziro)
Verse 18 — Surah Al-Alaq 96:18
“Nafe tiitana azabaniya (angelo a ku Moto)
Verse 19 — Surah Al-Alaq 96:19
“Ayi ndithu usamumvere (pa zimene akukuletsazo); koma gwetsa nkhope yako pansi, ndipo dziyandikitse kwa Mbuye wako